Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • es22 tsamba 118-128
  • December

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • December
  • Kuphunzira Malemba Tsiku ndi Tsiku—2022
  • Timitu
  • Lachinayi, December 1
  • Lachisanu, December 2
  • Loweruka, December 3
  • Lamlungu, December 4
  • Lolemba, December 5
  • Lachiwiri, December 6
  • Lachitatu, December 7
  • Lachinayi, December 8
  • Lachisanu, December 9
  • Loweruka, December 10
  • Lamlungu, December 11
  • Lolemba, December 12
  • Lachiwiri, December 13
  • Lachitatu, December 14
  • Lachinayi, December 15
  • Lachisanu, December 16
  • Loweruka, December 17
  • Lamlungu, December 18
  • Lolemba, December 19
  • Lachiwiri, December 20
  • Lachitatu, December 21
  • Lachinayi, December 22
  • Lachisanu, December 23
  • Loweruka, December 24
  • Lamlungu, December 25
  • Lolemba, December 26
  • Lachiwiri, December 27
  • Lachitatu, December 28
  • Lachinayi, December 29
  • Lachisanu, December 30
  • Loweruka, December 31
Kuphunzira Malemba Tsiku ndi Tsiku—2022
es22 tsamba 118-128

December

Lachinayi, December 1

Wokayikira ali ngati funde lapanyanja lotengeka ndi mphepo ndi lowindukawinduka.​—Yak. 1:6.

Nthawi zina anthufe zingativute kumvetsa mfundo inayake ya m’Baibulo kapenanso Yehova sangayankhe mapemphero athu m’njira imene timayembekezera. Zikatere tingayambe kukayikira zimene timakhulupirira. Ngati sitingachitepo kanthu, kukayikira kumeneku kungawononge chikhulupiriro chathu komanso ubwenzi wathu ndi Yehova. (Yak. 1:7, 8) Zimenezi zingachititse kuti tisiye kukhulupirira zimene tikuyembekezera m’tsogolo. Mtumwi Paulo anayerekezera chiyembekezo chathu cham’tsogolo ndi nangula. (Aheb. 6:19) Nangula amathandiza kuti sitima iime malo amodzi panyanja pakachita mafunde komanso kuti isatengeke ndi mphepo n’kukaomba miyala. Komatu nangula amakhala wothandiza ngati tcheni chake chili cholimba. Mofanana ndi mmene dzimbiri limachititsira kuti tcheni cha nangula chikhale chosalimba, nakonso kukayikira kumachititsa kuti chikhulupiriro chathu chifooke. Choncho munthu amene amakayikira akakumana ndi mavuto amasiya kukhulupirira kuti Yehova adzakwaniritsa malonjezo ake. Ndiye munthu akasiya kukhulupirira sakhalanso ndi chiyembekezo. Munthu wotereyu sangakhale wosangalala ngakhale pang’ono. w21.02 30 ¶14-15

Lachisanu, December 2

Abulahamu anakhulupirira mwa Yehova.​—Yak. 2:23.

N’kutheka kuti Abulahamu anali ndi zaka 70 pamene ankachoka ku Uri. (Gen. 11:31–12:4) Ndipo kwa zaka pafupifupi 100, ankakhala moyo woyendayenda n’kumagona m’matenti m’dziko la Kanani. Abulahamu anamwalira ali ndi zaka 175. (Gen. 25:7) Koma sanaone Yehova akukwaniritsa lonjezo lake loti adzapereka dzikolo kwa ana ake. Ndiponso anamwalira mzinda kapena kuti Ufumu wa Mulungu usanakhazikitsidwe. Ngakhale zili choncho, Baibulo limati Abulahamu anamwalira atakhala ndi “moyo wabwino, wautali ndi wokhutira.” (Gen. 25:8) Abulahamu anafunika kupirira mavuto ambiri koma anapitiriza kukhala ndi chikhulupiriro cholimba ndipo ankasangalala pamene ankayembekezera malonjezo a Yehova. N’chiyani chinamuthandiza kupirira? Anapirira chifukwa Yehova ankamuteteza komanso ankachita naye zinthu ngati mnzake. (Gen. 15:1; Yes. 41:8; Yak. 2:22) Mofanana ndi Abulahamu nafenso tikuyembekezera mzinda wokhala ndi maziko enieni. (Aheb. 11:10) Komabe ifeyo sitikuyembekezera kuti mzindawu umangidwe. Tikutero chifukwa Ufumu wa Mulungu unakhazikitsidwa mu 1914 ndipo unayamba kale kulamulira kumwamba. (Chiv. 12:7-10) Tikungoyembekezera kuti uyambe kulamulira dziko lonse lapansi. w20.08 4-5 ¶11-12

Loweruka, December 3

Maganizo a mumtima mwa munthu ali ngati madzi akuya, koma munthu wozindikira ndi amene amawatunga.​—Miy. 20:5.

Kuti tizimvetsera anthu mwatcheru, tiyenera kukhala odzichepetsa komanso oleza mtima. Pali zifukwa zitatu zochitira zimenezi. Choyamba, zidzatithandiza kuti tisamaweruze anthu molakwika. Chachiwiri, tidzadziwa mmene m’bale kapena mlongo wathu akumvera komanso zolinga zake. Ndipo zimenezi zingatithandize kuti timumvetse n’kumuchitira chifundo. Chachitatu, tikhoza kumuthandiza kuti amvetse mmene akumvera mumtima mwake. Nthawi zina munthu amamvetsa mmene akumvera mumtima mwake pokhapokha atafotokoza maganizo ake kwa munthu wina. Abale ndi alongo athu ena amavutika kufotokoza maganizo awo chifukwa cha chikhalidwe chawo, mmene anakulira kapena mmene alili panopa. Zingatengenso nthawi kuti abale ndi alongo athu azimasuka nafe, koma akamatifotokozera maganizo awo m’pamene tingayambe kuwamvetsa. Tikamatsanzira Yehova pokhala oleza mtima, anthu akhoza kuyamba kumasuka nafe. Ndiyeno akayamba kutifotokozera maganizo awo, tizimvetsera mwatcheru. w20.04 15-16 ¶6-7

Lamlungu, December 4

Uzisodza anthu amoyo.​—Luka 5:10.

Nthawi zambiri nsomba zimapezeka malo amene kuli madzi abwino komanso zakudya zambiri. Koma kodi msodzi akhoza kupita nthawi iliyonse imene akufuna kuti akaphe nsomba? Mmishonale wina, yemwe amakhala pachilumba cha Pacific, anaphunzira kuti si nthawi iliyonse imene msodzi angapite kukapha nsomba. Tsiku lina m’bale wina wa kuderalo anam’pempha kuti apite kukapha nsomba. Ndiyeno mmishonaleyo anati, “tikumane mawa 9 koloko chakummawa.” Koma m’baleyo anayankha kuti, “Ayi, nsombatu sitipha choncho. Timapita nthawi imene nsombazo zingapezeke, osati nthawi imene ili yabwino kwa ifeyo.” Ndi zimenenso asodzi a anthu a munthawi ya atumwi ankachita. Iwo ankapita m’malo amene anthu ankapezeka komanso pa nthawi imene angawapeze. Mwachitsanzo, otsatira a Yesu ankalalikira kukachisi, m’masunagoge, kunyumba ndi nyumba komanso m’misika. (Mac. 5:42; 17:17; 18:4) Nafenso tiyenera kuwadziwa bwino kwambiri anthu a m’gawo lathu. Tizikhala okonzeka kusintha zinthu pa moyo wathu kuti tizitha kulalikira pa nthawi komanso malo amene anthu angapezeke.​—1 Akor. 9:19-23. w20.09 4 ¶8-9

Lolemba, December 5

Polankhula zoona, tiyeni tikule m’zinthu zonse, kudzera m’chikondi, pansi pa iye amene ndi mutu, Khristu.—Aef. 4:15.

Popeza Yesu ndi mutu wa mpingo, timakhalanso anzake tikamachita zinthu mogwirizana ndi anthu amene wawasankha kuti azitiyang’anira. (Aef. 4:16) Mwachitsanzo, masiku ano gulu lakonza zoti Nyumba za Ufumu zizigwiritsidwa ntchito mokwanira. Kuti zimenezi zitheke, mipingo ina inaphatikizidwa. Zimenezi zathandiza kuti ndalama zimene abale amapereka zizigwiritsidwa ntchito bwino. Koma zachititsanso kuti zinthu zisinthe pa moyo wa abale ndi alongo ena. Mwachitsanzo, ena anakhala mumpingo wina kwa nthawi yaitali ndipo ankagwirizana kwambiri ndi abale ndi alongo mumpingowo. Koma panopa apemphedwa kuti azitumikira mumpingo wina. Yesu ayenera kuti amasangalala kwambiri kuona Akhristu okhulupirikawa akutsatira bwinobwino malangizowa. w20.04 24 ¶14

Lachiwiri, December 6

Mfumu ya kum’mwera idzayamba kukankhana nayo.​—Dan. 11:40.

Mfumu ya kumpoto ndi mfumu ya kum’mwera, akulimbirana kukhala ulamuliro wamphamvu kwambiri padziko lonse lapansi. Chitsanzo ndi zimene zinachitika nkhondo yachiwiri yapadziko lonse itatha, boma la Soviet Union ndi mayiko ogwirizana nalo anayamba kulamulira madera ambiri a ku Europe. Zimenezi zinachititsa mfumu ya kum’mwera kupanga bungwe lotchedwa NATO, momwe muli mayiko ena a ku Europe omwe anagwirizana kuti azithandizana pankhondo. Komanso mafumuwa amawononga ndalama zambiri popanga zida zankhondo zamphamvu kwambiri. Mfumu iliyonse imathandiza adani a mfumu inzake pankhondo m’mayiko a ku Africa, Asia ndi Latin America. M’zaka zaposachedwapa, mphamvu za dziko la Russia ndi mayiko ogwirizana nalo, zakhala zikukulirakulira. Mfumuyi imapanganso uchigawenga wa pa intaneti polimbana ndi mfumu ya kum’mwera. Mfumu iliyonse imaloza chala inzake kuti imapanga mapulogalamu a pakompyuta ndi cholinga chofuna kusokoneza chuma ndi ulamuliro wa inzake. Komanso mogwirizana ndi ulosi wa Danieli, mfumu ya kumpoto ikupitiriza kuukira anthu a Mulungu.​—Dan. 11:41. w20.05 13 ¶5-6

Lachitatu, December 7

Inetu ndidzafunafuna nkhosa zanga ndi kuzisamalira.—Ezek. 34:11.

M’nthawi ya mneneri Yesaya, Yehova anafunsa kuti: “Kodi mayi angaiwale mwana wake woyamwa?” Poyankha, Yehova anauza anthu ake kuti: “Ngakhale amayi amenewa akhoza kuiwala, koma ine sindidzakuiwala.” (Yes. 49:15) Si nthawi zonse pamene Yehova amadziyerekezera ndi zimene mayi amachita ngati mmene anachitira pa nthawiyi. Iye anafotokoza zachikondi chimene chimakhalapo pakati pa mayi ndi mwana wake pofuna kusonyeza mmene amakondera atumiki ake. Azimayi ambiri angagwirizane ndi zimene mlongo wina dzina lake Jasmin ananena. Iye anati: “Mayi woyamwitsa amakondana kwambiri ndi mwana wake ndipo chikondi chimenechi sichitherapo.” Yehova amadziwa ngati mtumiki wake wina wasiya kulalikira kapena kusonkhana. Pakapita nthawi, abale ndi alongo ambiri omwe anafooka amayambiranso kutumikira Yehova ndipo timawalandira ndi manja awiri. Yehova amafunitsitsa kuti abwerere ndipo ifenso timalakalaka atabwerera.​—1 Pet. 2:25. w20.06 18 ¶1-3

Lachinayi, December 8

Ikani maso [anu] pa zinthu zosaoneka, . . . Pakuti zooneka n’zakanthawi, koma zosaoneka n’zamuyaya.—2 Akor. 4:18.

Zinthu zomwe ndi zamtengo wapatali kwambiri sizioneka ndi maso. Paulaliki wa paphiri, Yesu anatchula zinthu zakumwamba zomwe ndi zamtengo wapatali kuposa chuma. Anawonjezeranso kuti: “Kumene kuli chuma chako, mtima wako umakhalanso komweko.” (Mat. 6:19-21) Mtima wathu umatichititsa kuti tizifunafuna zinthu zomwe timaona kuti ndi zofunika kwambiri. Timasunga ‘chuma chathu kumwamba,’ ngati tili ndi mbiri yabwino kwa Mulungu. Ndipo Yesu anafotokoza kuti chuma chimenechi sichingawonongeke kapena kubedwa. Mtumwi Paulo anatilimbikitsa kuti ‘tiziika maso athu pa zinthu zosaoneka.’ (2 Akor. 4:17, 18) Zinthu zosaonekazi ndi zamtengo wapatali kwambiri ndipo zikuphatikizapo madalitso omwe tidzasangalale nawo m’dziko latsopano. Kodi timasonyeza kuti timayamikira chuma chosaoneka chimenechi? w20.05 26 ¶1-2

Lachisanu, December 9

Malangizo anga adzagwa ngati mvula.​—Deut. 32:2.

Zimene Mose anaphunzitsa Aisiraeli zinawalimbikitsa komanso kuwatsitsimula ngati mmene mvula imathandizira zomera. Kodi tingatani kuti nafenso tiziphunzitsa mwanjira imeneyi? Tikamalalikira kunyumba ndi nyumba kapena m’malo opezeka anthu ambiri, tizigwiritsa ntchito Baibulo posonyeza anthu dzina lenileni la Mulungu loti Yehova. Tingawapatse mabuku athu, mavidiyo komanso zinthu zina za pawebusaiti yathu zimene zimalemekeza Yehova. Tiziyesetsanso kupeza mwayi wouza ena za Mulungu wathu komanso makhalidwe ake tikakhala kuntchito, kusukulu kapena paulendo. Tingawauze zokhudza zinthu zodabwitsa zimene Yehova adzatichitire m’tsogolo. Akamva zimenezi akhoza kudziwa kuti Yehova amatikonda kwambiri, ndipo mwina aka kakhoza kukhala koyamba kumva zimenezi. Tikamauza ena choonadi chokhudza Atate wathu wachikondi, timathandiza kuyeretsa dzina la Mulungu. Timawathandiza kudziwa kuti zinthu zimene anaphunzitsidwa zokhudza Yehova ndi zabodza. Mfundo za m’Baibulo zimene timawaphunzitsazi zimawalimbikitsa komanso kuwatsitsimula.​—Yes. 65:13, 14. w20.06 10 ¶8-9

Loweruka, December 10

Bwererani kwa ine ndipo ine ndibwerera kwa inu.​—Mal. 3:7.

Kodi tiyenera kukhala ndi makhalidwe ati kuti tithandize anthu kubwerera kwa Yehova? Tiyeni tione zimene tikuphunzira mufanizo la Yesu la mwana wolowerera amene anachoka pakhomo pa makolo ake. (Luka 15:17-24) Mwanayo pambuyo pake anazindikira kuti sanaganize bwino ndipo anasankha zobwereranso kwawo. Bambo ataona mwana wawoyo anamuthamangira ndi kumukumbatira mwachikondi. Mwanayo ankadziimba mlandu ndipo ankaona kuti sakuyeneranso kutchedwa mwana wa bambowo. Koma atawafotokozera mmene ankamvera, anamumvera chisoni. Kenako anachita zinthu zimene zinatsimikizira mwanayo kuti amulandira ngati mwana wawo wokondedwa. Pofuna kusonyeza zimenezi, bambowo anakonza phwando komanso anapatsa mwana wawoyo zovala zabwino. Yehova ali ngati bambo a mufanizoli. Iye amakonda kwambiri abale ndi alongo athu amene anasiya kusonkhana ndipo amafuna kuti abwererenso kwa iye. Tikamatsanzira Yehova tingawathandize kuti abwerere. Kuti tichite zimenezi tiyenera kukhala oleza mtima, achifundo komanso achikondi. w20.06 25-26 ¶8-9

Lamlungu, December 11

Mukamasunga mawu anga nthawi zonse, ndiye kuti ndinudi ophunzira anga. Mudzadziwa choonadi, ndipo choonadi chidzakumasulani.—Yoh. 8:31, 32.

Yesu ananena kuti anthu ena amalandira choonadi “mwachimwemwe” koma akakumana ndi mavuto, chikhulupiriro chawo chimafooka. (Mat. 13:3-6, 20, 21) N’kutheka kuti anthuwa sadziwa kuti anthu amene amatsatira Yesu amakumana ndi mavuto. (Mat. 16:24) Mwinanso amaganiza kuti chifukwa choti ndi Akhristu ndiye kuti Mulungu aziwathetsera mavuto awo. Koma m’dzikoli n’zosatheka kumakhala osakumana ndi mavuto chifukwa zinthu zikhoza kusintha pa moyo wathu n’kuchititsa kuti tisamasangalale. (Sal. 6:6; Mlal. 9:11) Abale ndi alongo ambiri sakayikira kuti zomwe amakhulupirira ndi zoona. Tikutero chifukwa wokhulupirira mnzawo akachita zosayenera kapena akawakhumudwitsa, sasiya kutumikira Yehova. (Sal. 119:165) Akamakumana ndi mavuto safooka, m’malomwake chikhulupiriro chawo chimalimba. (Yak. 1:2-4) Tiyenera kuyesetsa kuti tikhale ndi chikhulupiriro cholimba ngati chimenechi. w20.07 8 ¶1; 9 ¶4-5

Lolemba, December 12

Ngati wina akusowa nzeru, azipempha kwa Mulungu.​—Yak. 1:5.

Musanayambe kuwerenga Baibulo, muzipempha Yehova kuti akuthandizeni kupindula ndi zimene mukufuna kuwerengazo. Mwachitsanzo, ngati mukufufuza malangizo amene angakuthandizeni pa vuto linalake, muzipempha Yehova kuti akuthandizeni kupeza mfundo za m’Mawu ake zimene zingakuthandizeni kudziwa zoyenera. (Afil. 4:6, 7) Yehova anatipatsa luso lodabwitsa lotha kuyerekezera. Kuti muziona nkhani imene mukuwerenga m’Baibulo kuti ndi yeniyeni, muziyesa kuyerekezera zimene zikuchitika ndipo muzidziyerekezera kuti ndinu munthu amene akutchulidwa munkhaniyo. Muziyesa kuona zimene munthuyo anaona komanso m’mene ankamvera. Kenako muziganizira mozama zimene mukuwerenga komanso kuona mmene mungagwiritsire ntchito mfundo zake pa moyo wanu. Kuchita zimenezi kungatithandize kumvetsa bwino nkhaniyo. Kuwerenga Baibulo popanda kuganizira mozama kuli ngati kumangoona zidutswa za chithunzi zomwe zamwazikana. Kuganizira mozama kumatithandiza kuti tione mmene chithunzi chonsecho chimaonekera. w21.03 15 ¶3-5

Lachiwiri, December 13

Ndikuyamika Mulungu, . . . sindiiwala za iwe m’mapembedzero anga, usana ndi usiku.​—2 Tim. 1:3.

Mtumwi Paulo akanatha kuyamba kuganizira zam’mbuyo n’kumaona kuti akanapanda kukhala Mkhristu wodzipereka, sakanamangidwa. Iye akanatha kukwiyira abale a ku Asia omwe anamusiya yekha ndipo mwina zimenezi zikanamuchititsa kuti asiye kukhulupirira anzake ena. Koma Paulo sanachite zimenezi. Ngakhale kuti iye ankadziwa kuti anali atatsala pang’ono kufa, sanasiye kuona kuti chinthu chofunika kwambiri ndi kulemekezedwa kwa Yehova. Komanso anapitiriza kuganizira mmene angalimbikitsire ena. Paulo ankadalira kwambiri Yehova ndipo ankapemphera kwa iye nthawi zonse. M’malo momangoganizira za abale omwe anali atamusiya, iye ananena kuti ankayamikira kwambiri anzake okhulupirika omwe ankamuthandiza m’njira zosiyanasiyana. Kuwonjezera pamenepo, Paulo anapitiriza kuphunzira Mawu a Mulungu. (2 Tim. 3:16, 17; 4:13) Koma chofunika kwambiri n’chakuti iye sankakayikira ngakhale pang’ono kuti Yehova ndi Yesu amamukonda. w21.03 18 ¶17-18

Lachitatu, December 14

Monga momwe amasonkhanitsira namsongole ndi kumutentha pamoto, zidzakhalanso choncho pa mapeto a nthawi ino.—Mat. 13:40.

M’zaka za m’ma 100 C.E., Akhristu onyenga omwe anatengera ziphunzitso zachikunja komanso omwe ankabisira anthu choonadi cha m’Mawu a Mulungu, anachuluka kwambiri kuposa Akhristu oona. Choncho kuchokera nthawi imeneyo kudzafika chakumapeto kwa zaka za m’ma 1800, padzikoli panalibe gulu lodziwika bwino la atumiki a Mulungu. Pa nthawiyi Akhristu onyenga okhala ngati namsongole anachuluka kwambiri ndipo zinali zovuta kudziwa Akhristu enieni. (Mat. 13:36-43) Kuzindikira mfundoyi n’kothandiza kwambiri chifukwa kumatithandiza kudziwa kuti zimene timawerenga mu Danieli chaputala 11 zonena za mfumu ya kumpoto ndi mfumu ya kum’mwera sizikhudza maulamuliro omwe analipo kuyambira m’zaka za m’ma 100 C.E., kudzafika chakumapeto kwa m’ma 1800. Tikutero chifukwa choti pa nthawiyi panalibe gulu lodziwika bwino la atumiki a Mulungu lomwe mafumuwa akanatha kuliukira. Komabe chitadutsa chaka cha 1870 zinali zotheka kudziwa mfumu ya kumpoto komanso mfumu ya kum’mwera. w20.05 3 ¶5

Lachinayi, December 15

Pali mtundu umene walowa m’dziko langa.​—Yow. 1:6.

Yoweli analosera kuti dzombe lidzasakaza dziko la Isiraeli, ananena kuti lidzadya chomera chilichonse. (Yow. 1:4) Kwa zaka zambiri, tinkafotokoza kuti ulosiwu unkanena za anthu a Yehova omwe amalalikira ngati dzombe lomwe silingaimitsidwe ndi chinthu chilichonse. Tinkaganiza kuti ntchito yolalikirayi imasakaza “dziko” kapena kuti anthu amene akulamuliridwa ndi atsogoleri achipembedzo. Koma tikaganizira mbali zonse za ulosi umenewu, tingaone kuti tiyenera kusintha kafotokozedwe kake. Taganizirani zimene Yehova analonjeza zokhudza dzombeli. Iye anati: “Ndidzakuchotserani mdani wa kumpoto [dzombe] kuti akhale kutali ndi inu.” (Yow. 2:20) Ngati dzombeli likuimira a Mboni za Yehova omwe amamvera lamulo la Yesu loti tizilalikira ndi kuphunzitsa anthu, n’chifukwa chiyani Yehova akulonjeza zolichotsa? (Ezek. 33:7-9; Mat. 28:19, 20) Apa n’zodziwikiratu kuti Yehova sakuchotsa atumiki ake okhulupirika koma chinthu china kapena munthu wina amene amadana ndi anthu ake. w20.04 3 ¶3-5

Lachisanu, December 16

Ngati wina akusowa nzeru, azipempha kwa Mulungu.​—Yak. 1:5.

Kodi tiyenera kutani ngati tikuona kuti Yehova sanayankhe pemphero lathu mwamsanga? Yakobo ananena kuti tiyenera ‘kumapemphabe’ kwa Mulungu. Yehova sakwiya nazo tikamapitirizabe kumupempha kuti atipatse nzeru ndipo samatinyoza. M’malomwake Atate wathu wakumwamba amatipatsa “mowolowa manja” tikamapempha kuti atipatse nzeru zimene zingatithandize kuti tipirire mayesero. (Sal. 25:12, 13) Yehova amaona mayesero amene tikukumana nawo, amakhudzidwa tikamavutika komanso ndi wokonzeka kutithandiza. Zimenezitu zimatithandiza kukhala osangalala. Koma kodi Yehova amatipatsa bwanji nzeru? Iye amachita zimenezi kudzera m’Mawu ake. (Miy. 2:6) Kuti tipeze nzeru zimenezi, tiyenera kumaphunzira Mawu a Mulungu komanso mabuku othandiza kuphunzira Baibulo. Koma kuphunzira kokha sikokwanira, tiyenera kugwiritsira ntchito nzeru za Mulungu pa moyo wathu potsatira malangizo ake. Yakobo analemba kuti: “Muzichita zimene mawu amanena, osati kungomva chabe.” (Yak. 1:22) Tikamatsatira malangizo a Mulungu timakhala anthu amtendere, ololera komanso achifundo. (Yak. 3:17) Makhalidwe amenewa amatithandiza kuti tizipirira mayesero aliwonse amene tingakumane nawo koma n’kumakhalabe osangalala. w21.02 29 ¶10-11

Loweruka, December 17

Thupi lonselo limakula . . . malinga ndi ntchito yoyenera ya chiwalo chilichonse.​—Aef. 4:16.

Wophunzira Baibulo angathe kupita patsogolo mpaka kubatizidwa akamathandizidwa ndi ena mumpingo. Wofalitsa aliyense angathandize kuti mpingo ukule. Mpainiya wina ananena kuti: “Pali mawu akuti udindo wolera mwana ndi wa mudzi wonse. Ndikuona kuti zimenezi n’zofanana ndi ntchito yothandiza anthu kuti akhale ophunzira a Yesu. Anthu onse mumpingo amathandiza nawo kuti munthu afike podziwa choonadi.” Kuti mwana akule bwino, makolo ake, anzawo a makolowo, achibale komanso aphunzitsi ake amathandizana. Iwo amachita zimenezi pomulimbikitsa komanso kumuphunzitsa zinthu zofunika. Mofanana ndi zimenezi, ofalitsa mumpingo angapereke chitsanzo chabwino, malangizo komanso kulimbikitsa ophunzira Baibulo zomwe zingawathandize kuti afike pobatizidwa. (Miy. 15:22) N’chifukwa chiyani wofalitsa amene akuchititsa phunziro la Baibulo ayenera kulola kuti ofalitsa ena azithandiza wophunzirayo? Chifukwa ofalitsawo angathandize kuti wophunzirayo apite patsogolo. w21.03 8 ¶1-3

Lamlungu, December 18

Tikanena kuti: “Tilibe uchimo,” ndiye kuti tikudzinamiza.​—1 Yoh. 1:8.

Akhristu onse, kaya ndi achinyamata kapena achikulire, ayenera kupewa moyo wachiphamaso. Mtumwi Yohane ananena kuti sizingatheke kuti tiziyenda m’choonadi kwinaku tikuchita makhalidwe oipa. (1 Yoh. 1:6) Ngati tikufuna kuti Yehova azisangalala nafe, tizikumbukira kuti iye amaona chilichonse chimene timachita. Ngakhale tibisire anthu zimene timachita mseri, Yehova amakhala akutiona. (Aheb. 4:13) Tiyenera kupewa maganizo a anthu a m’dzikoli pa nkhani ya tchimo. Munthawi ya Yohane, ampatuko ankanena kuti munthu akhoza kumachita machimo mwadala n’kukhalabe pa ubwenzi ndi Mulungu. Nafenso tikukhala pakati pa anthu omwe ali ndi maganizo ngati amenewa. Anthu ambiri amanena kuti amakhulupirira Mulungu, koma sagwirizana ndi zimene Yehova amanena pa nkhani ya tchimo, makamaka nkhani ya kugonana. Pali zinthu zina zomwe anthu amachita pa nkhaniyi zimene Yehova amati ndi zoipa. Koma anthuwa amaona kuti palibe vuto kuchita zimenezo ngati ukufuna. w20.07 22 ¶7-8

Lolemba, December 19

Tizisonyezana chikondi chenicheni m’zochita zathu.​—1 Yoh. 3:18.

Kodi nanunso mumathandiza alongo anu pakafunika kuti muwateteze? Taganizirani zinthu zotsatirazi. Ofalitsa ena amaona kuti mlongo wina yemwe mwamuna wake si wa Mboni, amafika mochedwa pamisonkhano komanso amachoka ikangotha. Amaonanso kuti sakonda kubwera ndi ana ake. Choncho amamunena kuti bwanji sakakamiza mwamuna wakeyo kuti azimulola kutenga ana popita kumisonkhano. Komabe chomwe anthuwo sakudziwa n’chakuti mlongoyo amayesetsa kuchita zomwe angathe. Mlongoyu amafika mochedwa kumisonkhano chifukwa amatanganidwa kwambiri komanso mwamuna wake ndi amene ali ndi mphamvu posankha zochita zokhudza ana awo. Ngati mutanena zomuyamikira komanso kuwauza anthuwo zinthu zimene mlongoyo amachita bwino, akhoza kusiya kumunena. Akulu amadziwa kuti Yehova amafuna kuti alongo azisamalidwa bwino. (Yak. 1:27) Choncho akulu amayesetsa kutengera chitsanzo cha Yesu ndipo amachita zinthu moganiza bwino. Iwo amachita zimenezi popewa kumangopanga malamulo pa nthawi yomwe zingakhale bwino kuchita zinthu mwachifundo komanso kumvetsa mavuto amene alongo amakumana nawo. (Mat. 15:22-28) Akulu akamayesetsa kuchita zimenezi, amathandiza alongo kudziwa kuti Yehova komanso gulu lake amawakonda. w20.09 24-25 ¶17-19

Lachiwiri, December 20

[Mulungu] wakudziwitsani, inu Mfumu Nebukadinezara, zimene zidzachitike.​—Dan. 2:28.

Mneneri Danieli anali wodzichepetsa ndipo nthawi zonse ankalola kuti Yehova azimutsogolera. Mwachitsanzo, pamene Yehova anamugwiritsa ntchito kumasulira loto la Nebukadinezara, Danieli sananene kuti anakwanitsa kuchita zimenezi ndi nzeru zake. M’malomwake, iye modzichepetsa anapereka ulemelero wonse kwa Yehova. (Dan. 2:26-28) Kodi tikuphunzirapo chiyani pamenepa? Ngati abale amasangalala ndi nkhani zathu kapena ngati zinthu zimatiyendera bwino mu utumiki, tizikumbukira kuti ulemerero wonse uyenera kupita kwa Yehova. Tiyenera kuzindikira kuti sitikanakwanitsa kuchita zinthuzo popanda kuthandizidwa ndi Yehova. (Afil. 4:13) Tikamachita zimenezi, timakhala tikutsanziranso Yesu. Iye ankadalira kwambiri Yehova. (Yoh. 5:19, 30) Iye sanayese kulanda udindo wa Atate wake wakumwamba. Lemba la Afilipi 2:6 limatiuza kuti kwa iye “kukhala wolingana ndi Mulungu sanakuganizirepo ngati chinthu choti angalande.” Monga Mwana wogonjera, Yesu ankadziwa malire ake ndipo ankalemekeza ulamuliro wa Atate wake. w20.08 11 ¶12-13

Lachitatu, December 21

Thamangani m’njira yoti mukalandire mphoto.​—1 Akor. 9:24.

Anthu ena amene akuthamanga pa mpikisano wokalandira moyowu amakhala ndi mavuto amene anthu ena sangawaone kapena kuwamvetsa. Ngati muli ndi vuto limene mukuona kuti anthu ena salimvetsa, mukhoza kulimbikitsidwa ndi chitsanzo cha Mefiboseti. (2 Sam. 4:4) Iye anali wolumala ndipo Mfumu Davide anamuganizira zolakwika. Koma m’malo mongokhalira kukhumudwa, iye ankayamikira zinthu zabwino zimene zinkachitika pa moyo wake. Mwachitsanzo, ankayamikira kukoma mtima kumene Davide anali atamusonyeza. (2 Sam. 9:6-10) Choncho pamene Davide anamuganizira zolakwika, maganizo ake sanali pa nkhani yokhayo. Iye sanalole kuti akhumudwe kwambiri ndi zimene Davide analakwitsazi. Komanso sanaimbe mlandu Yehova chifukwa cha zimene Davide anachita. Koma Mefiboseti ankaganizira kwambiri zimene akanatha kuchita pothandiza mfumu yosankhidwa ndi Yehova. (2 Sam. 16:1-4; 19:24-30) Ndipo Yehova anachititsa kuti chitsanzo chabwino cha Mefiboseti chilembedwe m’Mawu ake kuti chizitithandiza.​—Aroma 15:4. w20.04 26 ¶3; 30 ¶18-19

Lachinayi, December 22

Ndife antchito anzake a Mulungu.​—1 Akor. 3:9.

Ena amatha kusankhidwa kukhala amishonale, apainiya apadera kapena apainiya okhazikika. Ndipotu abale ndi alongo ena padziko lonse anasankha kuti nthawi zonse azigwira ntchito yolalikira ndi kuphunzitsa anthu. Chifukwa cha zimenezi athandiza anthu ambiri kuti akhale ophunzira a Khristu Yesu. Ngakhale kuti ambiri mwa anthu amenewa sakhala ndi ndalama kapena zinthu zambiri, Yehova wawadalitsa kwambiri. (Maliko 10:29, 30) Abale ndi alongo amenewa timawakonda kwambiri ndipo timayamikira kukhala nawo mumpingo. Kodi abale amene ali ndi udindo komanso amene ali mu utumiki wa nthawi zonse ndi okhawo amene ali ofunika mumpingo? Ayi. Wofalitsa aliyense ndi wofunika kwa Mulungu komanso mumpingo. (Aroma 10:15; 1 Akor. 3:6-8) Tikutero chifukwa ntchito yofunika kwambiri imene mpingo umagwira ndi kupanga ophunzira a ambuye wathu Yesu Khristu. (Mat. 28:19, 20; 1 Tim. 2:4) Ofalitsa onse, kaya obatizidwa kapena osabatizidwa, amaona ntchito yolalikira kukhala yofunika kwambiri pa moyo wawo.​—Mat. 24:14. w20.08 21 ¶7-8

Lachisanu, December 23

Ine ndili pamodzi ndi inu masiku onse mpaka m’nyengo ya mapeto a nthawi ino.​—Mat. 28:20.

Monga mmene mawu a mulemba lalerowa akusonyezera, Yesu amatithandiza tikakumana ndi mavuto. Mawu a Yesuwa ndi olimbikitsa kwambiri. Chifukwa chiyani tikutero? Chifukwa chakuti masiku ena timakumana ndi zinthu zovuta kupirira. Mwachitsanzo, munthu amene timam’konda akamwalira timakhala achisoni, osati kwa masiku ochepa, koma mwina kwa zaka zambiri. Enanso amavutika tsiku ndi tsiku chifukwa cha ukalamba. Ndipo ena amavutika chifukwa cha nkhawa. Ngakhale zili choncho, timapeza mphamvu kuti tithe kupirira chifukwa tikudziwa kuti Yesu alinafe “masiku onse” kuphatikizapo nthawi zovuta kwambiri pa moyo wathu.(Mat. 11:28-30) Mawu a Mulungu amatitsimikizira kuti Yehova amatithandiza pogwiritsa ntchito angelo. (Aheb. 1:7, 14) Mwachitsanzo, angelo amatithandiza ndi kutitsogolera tikamalalikira “uthenga wabwino wa Ufumu” kwa anthu ochokera “kudziko lililonse, fuko lililonse, chinenero chilichonse.”​—Mat. 24:13, 14; Chiv. 14:6. w20.11 13-14 ¶6-7

Loweruka, December 24

Maganizo a mumtima mwa munthu ali ngati madzi akuya, koma munthu wozindikira ndi amene amawatunga.​—Miy. 20:5.

Timafuna kuti wophunzira wathu azidziwa kuti zimene akuphunzirazo zikuchokera m’Mawu a Mulungu. (1 Ates. 2:13) Kodi tingamuthandize bwanji kudziwa zimenezi? Muzilimbikitsa wophunzirayo kuti azifotokoza zimene akuphunzira. M’malo moti nthawi zonse tizimufotokozera malemba, nthawi zina tizimupempha kuti atifotokozere malemba ena. Muzimuthandiza kuona mmene Mawu a Mulungu angamuthandizire pa moyo wake. Muzimufunsa mafunso amene angamuthandize kuti afotokoze mmene akuganizira komanso mmene akumvera pa malemba amene wawerengawo. (Luka 10:25-28) Mwachitsanzo, mungamufunse kuti: “Kodi palembali mwaonapo khalidwe liti limene Yehova ali nalo?” “Kodi mukuona kuti zinthu zimene mwaphunzira kuchokera m’Baibulozi zingakuthandizeni bwanji?” “Kodi mukumva bwanji ndi zimene mwaphunzirazi?” Tizikumbukira kuti chofunika kwambiri si kuchuluka kwa zimene wophunzirayo akudziwa, koma kuti azikonda ndi kugwiritsa ntchito zimene akudziwazo. Muzigwiritsa ntchito Baibulo pophunzitsa. Zimenezi n’zofunika chifukwa kuti mukhale mphunzitsi wabwino, muyenera kukhala wodzichepetsa. w20.10 15 ¶5-6

Lamlungu, December 25

Bzala mbewu zako m’mawa, ndipo dzanja lako lisapume mpaka madzulo.​—Mlal. 11:6.

Timadziwa kuti ntchito yolalikira idzatha pa nthawi yake. Taganizirani zimene zinachitika mu nthawi ya Nowa. Yehova anasonyeza kuti amachita zinthu pa nthawi yake. Zaka 120 chigumula chisanachitike, Yehova anaikiratu nthawi yakuti chidzayambe. Patadutsa zaka zambiri, Yehova anauza Nowa kuti amange chingalawa. Mwina kwa zaka 40 kapena 50 chigumula chisanachitike, Nowa anapitirizabe kugwira ntchito mwakhama. Ngakhale anthu sankamvetsera, iye anapitirizabe kuwachenjeza mpaka pamene Yehova anamuuza kuti alowe m’chingalawacho. Kenako nthawi yake itakwana “Yehova anatseka chitseko.” (Gen. 6:3; 7:1, 2, 16) Posachedwapa Yehova atiuza kuti ntchito yolalikira yafika pamapeto, kenako adzaononga dziko la Satanali n’kubweretsa dziko latsopano, lomwe mudzakhale anthu amene amamvera Mulungu. Kufikira nthawi imeneyo, tiyeni tipitirizebe kutsanzira Nowa ndi atumiki ena omwe sanapumitse manja awo. Choncho tiyeni tipitirize kumaona kuti ntchito yolalikira ndi yofunika kwambiri. Tipitirizenso kukhala oleza mtima komanso kulimbitsa chikhulupiriro chathu mwa Yehova ndi malonjezo ake. w20.09 13 ¶18-19

Lolemba, December 26

Zinthu zonse zizichitika moyenera ndi mwadongosolo.​—1 Akor. 14:40.

Zikanakhala kuti Yehova sanakonze kuti ena azitsogolera anzawo, m’banja lake mukanakhala chisokonezo ndipo zimenezi zikanachititsa kuti onse m’banjali asamasangalale. Mwachitsanzo, zikanakhala zovuta kudziwa amene ayenera kusankha zochita komanso amene angatsogolere pochita zimene asankhazo. Ngati zimene Mulungu anakonza kuti mwamuna azitsogolera m’banja zili zabwino, n’chifukwa chiyani akazi ambiri masiku ano amaona kuti amuna awo amawapondereza? Zimenezi zili choncho chifukwa amuna ambiri amanyalanyaza mfundo za Yehova zimene mabanja ayenera kutsatira, ndipo m’malomwake amasankha kutsatira mfundo zachikhalidwe komanso miyambo yawo. Nthawi zina chifukwa chodzikonda, iwo amachitira nkhanza akazi awo pofuna kungosangalala. Mwamuna akhoza kumazunza mkazi wake n’cholinga choti azidziona kuti ndi wofunika kwambiri kapenanso kuti anthu ena azimuona kuti ndi “mwamuna weniweni.” Iye akhoza kumaganiza kuti sangakakamize mkazi wake kuti azimukonda, koma akhoza kumuchititsa kuti azimuopa. Angamachite zimenezi n’cholinga choti mkaziyo azichita zilizonse zimene mwamunayo akufuna. Amuna amene amaganiza komanso kuchita zinthu zimenezi amalakwitsa chifukwa akazi ayenera kupatsidwa ulemu ndipo kulephera kuwalemekeza n’kosemphana ndi zimene Yehova amafuna.​—Aef. 5:25, 28. w21.02 3 ¶6-7

Lachiwiri, December 27

Chitani zimenezi pamene mukumutulira nkhawa zanu zonse, pakuti amakuderani nkhawa.​—1 Pet. 5:7.

Akhristu amene akumana ndi mavuto amene akuwachititsa kuda nkhawa angalimbikitsidwe ngati atapemphera kwa Yehova. Yehova adzayankha mapemphero athu potipatsa ‘mtendere umene umaposa kuganiza mozama kulikonse.’ (Afil. 4:6, 7) Iye adzatithandiza kuchepetsa nkhawa zathu potipatsa mzimu wake woyera womwe ndi wamphamvu. (Agal. 5:22) Mukamapemphera kwa Yehova muzimuuza momasuka zimene zili mumtima mwanu. Muzitchula zenizeni zimene mukufuna kuti akuchitireni. Muzimuuza mavuto anu ndipo muzimufotokozera mmene mukumvera. Ngati vuto limene mwakumana nalo ndi loti likhoza kuthetsedwa, muzimupempha kuti akupatseni nzeru kuti mudziwe zoyenera kuchita komanso mphamvu zimene zingakuthandizeni kuchita zimenezo. Koma ngati vutolo ndi loti silingathe, muzipempha Yehova kuti akuthandizeni kuti musade nkhawa kwambiri. Mukamatchula zenizeni zimene mukufuna popemphera, m’kupita kwa nthawi mudzaona mmene Yehova wayankhira mapemphero anuwo. Koma ngati Yehova sanayankhe nthawi yomweyo, musamagwe ulesi. Si kuti Yehova amangofuna kuti muzimuuza zimene mukufuna m’pemphero koma amafunanso kuti muzipemphera kwa iye mosalekeza.​—Luka 11:8-10. w21.01 3 ¶6-7

Lachitatu, December 28

[Yesu] anawauza kuti: “Si onse amene angathe kuchita zimenezi, koma okhawo amene ali ndi mphatso.”—Mat. 19:11.

Masiku ano m’mipingo muli anthu amene ali ndi mabanja komanso abale ndi alongo ena omwe sali pabanja. Ndiye kodi tiyenera kumawaona bwanji anthu amene sali pabanja? Tizitengera chitsanzo cha Yesu pankhani ya mmene ankaonera anthuwa. Pamene Yesu anali padzikoli, sanakwatire. Iye anagwiritsa ntchito nthawi yake yonse pochita utumiki wake. Yesu sananene kuti kukhala pabanja kapena ayi ndi kofunika kuti munthu akhale Mkhristu. Komabe ananena kuti Akhristu ena amasankha kuti asakhale pabanja. Yesu ankalemekeza anthu amene sanali pabanja ndipo sankawaona kuti ndi otsika kapena akusowa zinazake. Mofanana ndi Yesu, mtumwi Paulo anakhala wosakwatira pa nthawi yonse ya utumiki wake. Ngakhale zili choncho, iye sankaphunzitsa kuti n’kulakwa kuti Akhristu azikwatira. Paulo ankadziwa kuti munthu ayenera kusankha yekha kukhala pabanja kapena ayi. w20.08 28 ¶7-8

Lachinayi, December 29

Mulungu ndiye chikondi.​—1 Yoh. 4:16.

Mtumwi Yohane anakhala ndi moyo zaka zambiri ndipo pa moyo wake anakumana ndi zinthu zambiri zosangalatsa. Anakumananso ndi mavuto ambiri omwe akanatha kufooketsa chikhulupiriro chake. Koma nthawi zonse iye ankayesetsa kutsatira malamulo a Yesu kuphatikizapo lamulo loti azikonda abale ndi alongo ake. Chifukwa cha zimenezi, Yohane sankakayikira kuti Yehova komanso Yesu amamukonda ndiponso kuti azimupatsa mphamvu kuti athe kupirira mayesero aliwonse amene angakumane nawo. (Yoh. 14:15-17; 15:10) Palibe chimene Satana kapena dziko lakeli, akanachita chomwe chikanalepheretsa Yohane kusonyeza kuti amakonda abale ndi alongo ake mwa zochita ndi zolankhula zake. Mofanana ndi Yohane, ifenso tikukhala m’dziko limene wolamulira wake ndi Satana, yemwe alibe chikondi. (1 Yoh. 3:1, 10) Ngakhale kuti iye amafuna kuti tisiye kukonda abale ndi alongo athu, sizingatheke, pokhapokha ngati ifeyo titalola zimenezo. Tiyeni tipitirize kukonda abale ndi alongo athu ndipo tizisonyeza zimenezi mwa zolankhula komanso zochita zathu. Tikatero, tidzasangalala kukhala m’banja la Yehova ndipo moyo wathu udzakhala wabwino kwambiri.​—1 Yoh. 4:7. w21.01 13 ¶18-19

Lachisanu, December 30

Mulungu . . . amatipatsa mphamvu kuti tithe kupirira.​—Aroma 15:5.

Moyo m’dziko la Satanali ukhoza kukhala wovuta kwambiri mpaka kulephera kudziwa zoyenera kuchita. (2 Tim. 3:1) Koma sitiyenera kuda nkhawa mpaka kuchita mantha. Yehova amadziwa zimene tikukumana nazo. Tikagwa iye amatilonjeza kuti adzatigwira ndi dzanja lake lamanja lamphamvu. (Yes.  41:10, 13) Ndife otsimikiza kuti Yehova adzatithandiza ndipo kudzera m’Malemba tingapeze mphamvu zotithandiza kupirira mavuto ena alionse. Mavidiyo athu, masewero ongomvetsera komanso nkhani zakuti, “Tsanzirani Chikhulupiriro Chawo” zimathandiza kuti muziona kuti nkhani za m’Baibulo ndi zenizeni. Musanayambe kuonera, kumvetsera kapena kuwerenga nkhanizi, muzipempha Yehova kuti akuthandizeni kupeza mfundo zimene muyenera kutsatira. Muzidziyerekezera kuti ndinu munthu wotchulidwa munkhaniyo. Muziganizira mozama zimene atumiki okhulupirika a Yehovawo anachita komanso mmene Yehova anawathandizira kuti athe kulimbana ndi mavuto. Kenako muzigwiritsa ntchito mfundo zimene mwaphunzirazo pa zimene zikukuchitikirani. Muzithokoza Yehova pa zimene akukuchitirani. Ndipo mungasonyeze kuti mukuyamikira mukamalimbikitsa komanso kuthandiza anthu ena. w21.03 19 ¶22-23

Loweruka, December 31

Ana ndi cholowa chochokera kwa Yehova.​—Sal. 127:3.

Ngati muli pabanja ndipo mumafuna mutakhala ndi ana mungadzifunse kuti: ‘Kodi ndife anthu odzichepetsa komanso timakonda Yehova ndi Mawu ake? Kodi Yehova angatisankhe kuti tikhale makolo a ana omwe amawaona kuti ndi amtengo wapatali?’ (Sal. 127:4) Ngati ndinu kholo mungadzifunse kuti: ‘Kodi ndimaphunzitsa ana anga kuti aziona kufunika kogwira ntchito mwakhama?’ (Mlal. 3:12, 13) Kodi ndimayesetsa kuteteza ana anga ku zinthu zoopsa zimene angakumane nazo?’ (Miy. 22:3) Simungathe kuteteza ana anu ku mavuto onse koma mungawathandize kukonzekera mavuto amene angakumane nawo popitiriza kuwaphunzitsa mwachikondi kuti azidalira malangizo opezeka m’Mawu a Mulungu. (Miy. 2:1-6) Mwachitsanzo, ngati wachibale wanu wina wasiya kutumikira Yehova, muzithandiza ana anu pogwiritsira ntchito Baibulo kuti adziwe kufunika kopitirizabe kukhala okhulupirika kwa Yehova. (Sal. 31:23) Kapena ngati munthu wina amene mumamukonda wamwalira muzisonyeza ana anu mavesi a m’Baibulo amene angawathandize kupirira chisoni chimene ali nacho komanso kuti akhale ndi mtendere.​—2 Akor. 1:3, 4; 2 Tim. 3:16. w20.10 27 ¶7

    Mabuku a Chichewa (1974-2026)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena