NYIMBO 161
“Ndimasangalala Kuchita Zimene Mumafuna”
1. Yesu atangobatizidwa
Munamulimbikitsatu.
Ankafunitsitsa kuchita
Zimene mumafuna.
Sanagonje mu mayesero.
Anadziperekadi.
Anayeretsa dzina lanu,
Nane ndimutsanzire.
(KOLASI)
Kuchita zofuna zanu
Kumandisangalatsadi.
N’kamamvera mawu anu,
Ndidzasangalalabe.
Kuchita zofuna zanu
Kumandisangalatsadi.
Ndimadziwa m’mandikonda.
Ndizichitabe zomwe
Mumafuna.
2. Kudziwa za inu Yehova
Kumandipatsa chimwemwe.
Ndizilalikira za inu
Monga mboni yanudi.
Kutumikira ndi abale
Kumandisangalatsa.
Ndimanyadira podziwika
Ndi dzina lanu M’lungu.
(KOLASI)
Kuchita zofuna zanu
Kumandisangalatsadi.
N’kamamvera mawu anu,
Ndidzasangalalabe.
Kuchita zofuna zanu
Kumandisangalatsadi.
Ndimadziwa m’mandikonda.
Ndizichitabe zomwe
Mumafuna.
Zomwe mumafuna.
(Onaninso Sal. 40:3, 10.)