NYIMBO 162
Zosowa Zanga Zauzimu
1. Tonsefe tilitu ndi
Zosowa za uzimu.
Timafuna kudziwatu
Mulungu woona.
Anthu amafufuza,
Mayankho alipotu.
M’mawu ake, M’Baibulo.
Tiziwawerenga.
(KOLASI)
Ine ndimutamanda.
Ndizimvera mawu ake.
Ndipo ndim’tumikira.
Andisamalira.
Ndipitiliza
Kukhala mnzake.
2. Ndizipezabe nthawi
Yowerenga mawuwo,
N’kumapeza zinthu zomwe
Ndingamasinthebe.
Ena safuna kumva.
Ndiziwapempherera
Kuti nawo amudziwe,
N’kumuyandikira.
(KOLASI)
Ine ndimutamanda.
Ndizimvera mawu ake.
Ndipo ndim’tumikira.
Andisamalira.
Ndipitiliza
Kukhala mnzake.
Ine ndimutamanda.
Ndizimvera mawu ake.
Ndipo ndim’tumikira.
Andisamalira.
Ndipitiliza
Kukhala mnzake.
Ine ndimutamanda.
Ndizimvera mawu ake.
Ndipo ndim’tumikira.
Andisamalira.
Ndipitiliza
Kukhala mnzake.
(Onaninso Mat. 5:6; 16:24; Yes. 40:8; Sal. 1:1, 2; 112:1; 119:97; 2 Tim. 4:4.)