January
Lamlungu, January 1
Iwo ndi atsogoleri akhungu.—Mat. 15:14.
Yesu ankadzudzula molimba mtima zochita zachinyengo za atsogoleri achipembedzo. Mwachitsanzo, iye anadzudzula chinyengo cha Afarisi omwe ankaona kuti kusamba m’manja n’kofunika kwambiri kuposa kusamalira makolo awo. (Mat. 15:1-11) Ngakhale kuti zomwe Yesu ananena zinakwiyitsa atsogoleriwo, zimenezi sizinamulepheretse kulankhula choonadi. Yesu anadzudzulanso zinthu zachinyengo zimene atsogoleri achipembedzo ankaphunzitsa. Iye sananene kuti Mulungu amavomereza zonse zimene zipembedzo zimaphunzitsa. M’malomwake, iye ananena kuti anthu ambiri adzayenda pamsewu waukulu ndi wotakasuka wopita kuchiwonongeko, pomwe ochepa adzayenda pamsewu wopanikiza wopita kumoyo. (Mat. 7:13, 14) Yesu ananena momveka bwino kuti ena adzaoneka ngati akutumikira Mulungu. Iye anachenjeza kuti: “Chenjerani ndi aneneri onyenga amene amabwera kwa inu atavala ngati nkhosa, koma mkati mwawo ali mimbulu yolusa. Mudzawazindikira ndi zipatso zawo.”—Mat. 7:15-20. w21.05 9 ¶7-8
Lolemba, January 2
Ndipo sanakhalenso ndi nkhawa.—1 Sam. 1:18.
Hana anakwatiwa ndi Mlevi wina dzina lake Elikana, yemwe ankamukonda kwambiri. Elikana anali ndi mkazi wina dzina lake Penina. Iye ankakonda kwambiri Hana kuposa Penina. Komabe, “Penina anabereka ana koma Hana analibe ana.” Chifukwa cha zimenezi, Penina ankanyoza Hana ndipo “anali kum’sautsa kwambiri n’cholinga choti amukhumudwitse.” Hana ankakhumudwa kwambiri chifukwa cha zimenezi, moti “anali kulira ndiponso sankadya.” Koma palibe paliponse m’Baibulo pamene timawerenga kuti Hana anabwezera zimene Penina ankachita. M’malomwake, iye anafotokozera Yehova mmene ankamvera ndipo ankakhulupirira kuti achitapo kanthu. (1 Sam. 1:2, 6, 7, 10) Kodi tikuphunzira chiyani pa chitsanzo cha Hana? Ngati munthu wina akufuna kuti muzipikisana, muzikumbukira kuti inuyo mukhoza kupewa zimenezi. Musamalole kuti muzikangana. M’malo mobwezera choipa muziyesetsa kukhala naye pa mtendere. (Aroma 12:17-21) Ngakhale zitaoneka kuti munthu winayo sakufuna kuti mukhazikitse mtendere, inuyo mungakhale ndi mtendere wamumtima. w21.07 17 ¶13-14
Lachiwiri, January 3
Khalani maso ndipo chenjerani ndi kusirira kwa nsanje kwamtundu uliwonse.—Luka 12:15.
Dyera linachititsa Yudasi Isikarioti kuchita zoipa kwambiri moti anapereka Yesu. Koma poyamba sanali munthu woipa. (Luka 6:13, 16) Iye anali wodalirika chifukwa anapatsidwa udindo woyang’anira bokosi la ndalama. Koma patapita nthawi Yudasi ankaba ndalamazi ngakhale kuti anali atamumva Yesu akuchenjeza mobwerezabwereza zokhudza dyera. (Maliko 7:22, 23; Luka 11:39) Dyera la Yudasi linaonekera kwambiri Yesu atatsala pang’ono kuphedwa. Yesu ndi ophunzira ake kuphatikizapo Mariya ndi mchemwali wake Marita anapita kunyumba kwa Simoni wakhate. Pa nthawi ya chakudya, Mariya anadzuka n’kuthira pamutu pa Yesu mafuta onunkhira omwe anali okwera mtengo. Yudasi ndi ophunzira ena anakwiya kwambiri ndi zimenezi. N’kutheka kuti ophunzira enawo anaona kuti mafutawo akanagulitsidwa, akanapeza ndalama zambiri zothandizira pa ntchito yolalikira. Koma izi si zimene Yudasi ankaganiza. Iye “anali wakuba” ndipo ankafuna kuti adzabe ndalamazo.—Yoh. 12:2-6; Mat. 26:6-16; Luka 22:3-6. w21.06 18 ¶12-13
Lachitatu, January 4
Munthu wovutika ine! Ndani adzandipulumutse?—Aroma 7:24.
Kodi nthawi zina mumapanikizika n’kumaona kuti pali zambiri zoti muchite koma simungakwanitse kuzichita? Ngati zili choncho ndiye kuti mungamvetse mmene Paulo ankamvera. Iye ankadera nkhawa osati mpingo umodzi wokha koma “mipingo yonse.” (2 Akor. 11:23-28) Kodi mukudwala matenda aakulu omwe nthawi zambiri amakuchititsani kukhala wosasangalala? Paulo ankalimbana ndi “munga m’thupi.” N’kutheka kuti mwina panali matenda enaake amene ankadwala ndipo ankafunitsitsa matendawo atatha. (2 Akor. 12:7-10) Kodi nthawi zina mumafooka chifukwa cha zinthu zimene mumalakwitsa? Nthawi zinanso Paulo ankamva choncho. Iye anafika ponena kuti “munthu wovutika ine,” chifukwa nthawi zambiri ankakhala pa nkhondo yofuna kuyesetsa kuti azichita zabwino. (Aroma 7:21-24) Ngakhale kuti ankakumana ndi mayesero komanso zinthu zambiri zofooketsa, Paulo anapitirizabe kutumikira Yehova. Kodi n’chiyani chinam’patsa mphamvu? Iye ankadziwa kuti si wangwiro koma ankakhulupirira kwambiri kuti nsembe ya dipo ingamuthandize. w21.04 22 ¶7-8
Lachinayi, January 5
Mwana wa munthu [anabwera] . . . kudzapereka moyo wake dipo kuwombola anthu ambiri.—Maliko 10:45.
Adamu yemwe anali wangwiro, atachimwa anataya mwayi wokhala ndi moyo wosatha. Zimene anachitazi sizinakhudze iye yekha koma zinakhudzanso ana ake onse. Adamu analibe chifukwa chomveka chodzikhululukira chifukwa anachimwa mwadala. Koma nanga bwanji ana ake? Iwo sanalakwe chilichonse. (Aroma 5:12, 14) Ndiye kodi pali chilichonse chomwe chikanachitika kuti apulumutsidwe ku chilango cha imfa chimene kholo lawo linkayenera kulandira? Inde, tikutero chifukwa Adamu atangochimwa, Yehova anayamba kuulula pang’onopang’ono zimene adzachite kuti apulumutse ana a Adamu ku uchimo ndi imfa. (Gen. 3:15) Chifukwa cha dipo, timatha kukhala pa ubwenzi ndi Yehova ngakhale kuti si ife angwiro. Dipo lidzatheketsanso kuti ntchito za Mdyerekezi ziwonongedwe kotheratu. (1 Yoh. 3:8) Komanso dipo lidzathandiza kuti cholinga chimene Mulungu anali nacho chokhudza dziko lapansi chikwaniritsidwe ndipo dziko lonseli lidzakhala paradaiso. w21.04 14 ¶1; 19 ¶17
Lachisanu, January 6
Aliyense wa inu abatizidwe.—Mac. 2:38.
Gulu lalikulu la amuna ndi akazi ochokera m’mayiko ambiri komanso olankhula zinenero zosiyanasiyana linasonkhana ku Yerusalemu. Pa tsiku limeneli panachitika chinthu china chapadera. Ayuda ena anayamba kulankhula zinenero za alendo ochokera m’mayiko enawo. Zimenezi zinali zodabwitsa, koma zimene Ayudawo komanso mtumwi Petulo analankhula ndi zomwe zinali zapadera kwambiri. Unali uthenga wonena kuti anthuwo angapulumutsidwe ngati atakhulupirira Yesu Khristu. Uthengawo unawafika pamtima anthuwo. Iwo anakhudzidwa kwambiri moti anafunsa kuti: “Tichite chiyani pamenepa?” Poyankha Petulo anawauza kuti: “Aliyense wa inu abatizidwe.” (Mac. 2:37, 38) Zimene zinachitika pambuyo pake zinali zodabwitsa. Anthu pafupifupi 3000 anabatizidwa tsiku limeneli n’kukhala ophunzira a Khristu. Ichi chinali chiyambi cha ntchito yaikulu yophunzitsa anthu imene Yesu analamula otsatira ake kuti azigwira. Ntchito imeneyi yakhala ikuchitika mpaka m’nthawi yathu ino. w21.06 2 ¶1-2
Loweruka, January 7
Ineyo ndinabzala, Apolo anathirira, koma Mulungu ndiye anakulitsa. Chotero wobzala kapena wothirira sali kanthu, koma Mulungu amene amakulitsa.—1 Akor. 3:6, 7.
Tikhoza kumakhala m’dera limene n’zovuta kuyambitsa maphunziro a Baibulo. Mwina anthu sangamachite chidwi ndi uthenga wathu ndipo akhoza kumatitsutsa. N’chiyani chingatithandize kuti tizipitirizabe kuona moyenera anthu a m’gawo ngati limeneli? Tizikumbukira kuti zinthu zikhoza kusintha mwadzidzidzi pa moyo wa anthu m’dziko loipali, ndipo anthu amene poyamba analibe chidwi akhoza kuzindikira kuti amafunika Mulungu kuti aziwatsogolera. (Mat. 5:3) Anthu ena omwe ankakana mabuku athu, patapita nthawi anavomera kuti aziphunzira Baibulo. Tizikumbukiranso kuti Yehova ndiye Mwiniwake wa zokolola. (Mat. 9:38) Amafuna kuti tizipitiriza kudzala komanso kuthirira koma iye ndi amene amakulitsa. Komanso ndi zolimbikitsa kudziwa kuti ngakhale kuti tilibe phunziro la Baibulo, Yehova amatidalitsa chifukwa cha khama lathu osati chifukwa cha kuchuluka kwa mabuku amene timagawira kapena maphunziro amene tili nawo. w21.07 6 ¶14
Lamlungu, January 8
Ana ndi cholowa chochokera kwa Yehova.—Sal. 127:3.
Yehova analenga anthu kuti azikhala ndi ana ndipo anawapatsa udindo wophunzitsa anawo kuti azimukonda komanso kumutumikira. Angelo sanapatsidwe mwayiwu ngakhale kuti anapatsidwa luso lochita zinthu zambiri. Poganizira mfundo imeneyi, makolo amene akulera ana ayenera kuona kuti umenewu ndi udindo wofunika kwambiri. Makolo apatsidwa udindo wolera ana awo “m’malangizo a Yehova ndikuwaphunzitsa kaganizidwe kake.” (Aef. 6:4; Deut. 6:5-7) Pofuna kuthandiza makolo, gulu la Yehova limapereka zinthu zothandiza pophunzira Baibulo monga mabuku, mavidiyo, nyimbo komanso zinthu zina kudzera pa webusaiti. N’zoonekeratu kuti Atate wathu wakumwamba komanso Mwana wake amakonda kwambiri ana. (Luka 18:15-17) Makolo akamadalira Yehova n’kumachita zonse zomwe angathe posamalira ana awo, omwe ndi amtengo wapatali, Yehova amasangalala. Ndipo makolo oterewa, amathandiza ana awo kukhala ndi chiyembekezo chodzakhala m’banja la Yehova mpaka kalekale. w21.08 5 ¶9
Lolemba, January 9
Chikhulupiriro ndicho . . . umboni wooneka wa zinthu zenizeni, ngakhale kuti n’zosaoneka.—Aheb. 11:1.
Anthu ena amaganiza kuti kukhala ndi chikhulupiriro kumatanthauza kukhulupirira zinthu zimene zilibe umboni. Koma malinga ndi zimene Baibulo limanena, chimenecho si chikhulupiriro chenicheni. Dziwani kuti munthu amakhulupirira zinthu zosaoneka zomwe ndi zenizeni monga Yehova, Yesu komanso Ufumu wakumwamba chifukwa choti ali ndi umboni wotsimikizirika. (Aheb. 11:3) Wa Mboni wina yemwe ndi katswiri wasayansi ananena kuti: “Zomwe timakhulupirira zili ndi umboni ndipo sizitsutsana ndi sayansi.” Mwina tingafunse kuti, ‘Ngati pali umboni wotsimikizirika woti kuli Mlengi, n’chifukwa chiyani anthu ambiri sakhulupirira kuti Mulungu ndi amene analenga zinthu zamoyo?’ Chifukwa china n’choti anthu ena sanafufuze paokha kuti apeze umboniwo. Robert yemwe panopa ndi wa Mboni za Yehova ananena kuti: “Popeza kusukulu sankaphunzitsa kuti zinthu zinachita kulengedwa, ndinkaganiza kuti zinangokhalako zokha. Ndinkakhulupirira zimenezi mpaka pamene ndinamva mfundo zomveka bwino za m’Baibulo zotsimikizira kuti zinthu zinachita kulengedwa. Pa nthawiyo n’kuti ndili ndi zaka za m’ma 20.” w21.08 15 ¶4-5
Lachiwiri, January 10
Talawani ndipo muona kuti Yehova ndi wabwino.—Sal. 34:8.
Tikhoza kuphunzira za ubwino wa Yehova powerenga Baibulo komanso pomvetsera pamene anthu ena akufotokoza madalitso amene apeza. Komabe, timamvetsa ubwino wa Yehova ‘tikalawa’ tokha ubwino wakewo. Tiyerekeze kuti tikufuna kuchita utumiki winawake wanthawi zonse, koma kuti tikwanitse cholinga chimenechi, tazindikira kuti tiyenera kusintha zinthu zina pa moyo wathu. Tikudziwa lonjezo la Yesu lakuti tikamayika zinthu zokhudza Ufumu pamalo oyamba, Yehova adzatipatsa zimene timafunikira. Koma ifeyo patokha, sitinaonepo kukwaniritsidwa kwa lonjezo limeneli. (Mat. 6:33) Ngakhale zili choncho, pokhulupirira lonjezo la Yesuli, tachepetsa zimene timagula komanso nthawi imene timagwira ntchito n’cholinga choti tizichita zambiri pa ntchito yolalikira. Pamene tikuchita zimenezi, tikufika podzionera tokha kuti Yehova amatipatsadi zinthu zimene timafunikira. Zikatero timakhala kuti ‘talawa’ tokha ubwino wa Yehova. w21.08 26 ¶2
Lachitatu, January 11
Anthu sadzafunanso chiphunzitso cholondola.—2 Tim. 4:3.
Kodi vuto limeneli liliponso masiku ano? Inde. Atsogoleri achipembedzo ambiri amasangalala kulandira m’mipingo mwawo anthu omwe ndi otchuka, olemera komanso amene amaonedwa ngati anzeru m’dzikoli. Iwo amalola anthuwa kukhala m’zipembedzo zawo ngakhale kuti makhalidwe komanso zochita zawo n’zosemphana ndi zimene Mulungu amafuna. Anthu m’dzikoli amaona kuti atumiki a Yehova omwe amatsatira mfundo zake zamakhalidwe abwino ndi osafunika, choncho atsogoleri achipembedzo amanyoza atumiki a Yehovawo. Mogwirizana ndi zimene mtumwi Paulo ananena, Mulungu anasankha anthu amene amaonedwa ngati ‘achabechabe.’ (1 Akor. 1:26-29) Komabe, Yehova amaona kuti atumiki ake onse okhulupirika ndi amtengo wapatali. Kodi tingatani kuti Tisasocheretsedwe ndi maganizo a anthu a m’dzikoli? (Mat. 11:25, 26) Musamaone anthu a Mulungu ngati mmene dzikoli limawaonera. Muzikumbukira kuti Yehova amagwiritsa ntchito anthu odzichepetsa okha kuti achite chifuniro chake. (Sal. 138:6) Ndiponso muziganizira zinthu zimene Yehova wakwanitsa kuchita pogwiritsa ntchito anthu amene dziko siliwaona kuti ndi anzeru kapena ophunzira. w21.05 8 ¶1; 9 ¶5-6
Lachinayi, January 12
Inu munanditumizira kenakake pa zosowa zanga.—Afil. 4:16.
Mtumwi Paulo ankayamikira kwambiri abale akamuthandiza. Iye anali wodzichepetsa ndipo ankalola kuti abale ndi alongo azimuthandiza. (Afil. 2:19-22) Achikulirenu, mungasonyeze kuti mumayamikira achinyamata mumpingo mwanu m’njira zosiyanasiyana. Ngati akufuna kukuthandizani pankhani ya mayendedwe, kukagula zinthu kapena kuchita zinthu zina zofunika, muzilola kuti akuthandizeni. Muziona kuti zimene akuchita pokuthandizani ndi umboni wakuti Yehova amakukondani. Mukhoza kudabwa kuona kuti mwayamba kugwirizana nawo kwambiri. Muzithandiza anzanu achinyamata kukhala pa ubwenzi wolimba ndi Yehova ndipo muziwauza mmene mukusangalalira chifukwa choona kuti akuchita zambiri pothandiza mumpingo. Muzikhala ofunitsitsa kucheza nawo komanso kuwafotokozera zimene mwakumana nazo pa moyo wanu. Mukamachita zimenezi ‘mungasonyeze kuyamikira’ Yehova chifukwa cha achinyamata amene iye wawakokera mumpingo.—Akol. 3:15; Yoh. 6:44; 1 Ates. 5:18. w21.09 11-12 ¶12-13
Lachisanu, January 13
Ndi chifundo chimenechi, kuwala kwa m’mawa kudzatifikira kuchokera kumwamba.—Luka 1:78.
Yehova amakonda abale ndi alongo athu. Koma mwina nthawi zina ifeyo zingamativute kuti tiziwakonda. Mwina izi zingachitike chifukwa chosiyana zikhalidwe komanso kochokera. Ndiponso tonsefe tingachite zinthu zina zimene zingakwiyitse kapena kukhumudwitsa anthu ena. Komabe tonsefe tingachite zinthu zomwe zingathandize kuti abale ndi alongo azikondana. Tingatero potsanzira Atate wathu n’kumakonda abale ndi alongo. (Aef. 5:1, 2; 1 Yoh. 4:19) Munthu wachifundo amafunafuna njira yoti athandize komanso kulimbikitsa ena. Mmene Yesu ankachitira zinthu ndi anthu, zinkasonyeza mmene Yehova amawakondera. (Yoh. 5:19) Pa nthawi ina Yesu ataona khamu la anthu, “anawamvera chisoni, chifukwa anali onyukanyuka ndi otayika ngati nkhosa zopanda m’busa.” (Mat. 9:36) Kuwonjezera powachitira chifundo, Yesu anachitanso zinthu zina powathandiza. Iye anachiritsa odwala komanso kuthandiza anthu “ogwira ntchito yolemetsa ndi olemedwa.”—Mat. 11:28-30; 14:14. w21.09 22 ¶10-11
Loweruka, January 14
[Mulungu] anawamvera chifundo. Anali kukhululukira machimo awo ndipo sanali kuwawononga.—Sal. 78:38.
Yehova amakonda kuchita zinthu mwachifundo. Mtumwi Paulo analemba kuti Mulungu ndi “wachifundo chochuluka.” Pamene ankalemba zimenezi, Paulo ankafotokoza mmene Mulungu anasonyezera chifundo popereka chiyembekezo choti atumiki ake odzozedwa, omwe si angwiro akakhale kumwamba. (Aef. 2:4-7) Koma sikuti Yehova anangosonyeza chifundo kwa atumiki ake odzozedwa okha. Wolemba masalimo Davide anati, “Yehova amakomera mtima aliyense, ndipo ntchito zake zonse amazichitira chifundo.” (Sal. 145:9) Chifukwa chakuti Yehova amakonda anthu, iye amawachitira chifundo pakakhala chifukwa chomveka chochitira zimenezo. Kuposa wina aliyense, Yesu amadziwa bwino mmene Yehova amakondera kusonyeza chifundo. Yehova ndi Yesu anakhala limodzi kumwamba kwa zaka zambiri Yesuyo asanabwere padzikoli. (Miy. 8:30, 31) Yesu ankaona mmene Atate wake ankasonyezera chifundo kambimbiri kwa anthu ochimwa. (Sal. 78:37-42) Akamaphunzitsa, iye nthawi zambiri ankafotokoza za khalidwe labwino la Atate wakeli. w21.10 8-9 ¶4-5
Lamlungu, January 15
Atate lemekezani dzina lanu.—Yoh. 12:28.
Yehova anayankha pemphero limeneli kuchokera kumwamba ndi mawu amphamvu ndipo analonjeza kuti adzalilemekeza. Pa utumiki wake wonse, Yesu ankalemekeza dzina la Atate wake. (Yoh. 17:26) Choncho n’zomveka kuti Akhristu oona amasangalala kugwiritsa ntchito dzina la Mulungu komanso kuuza ena za dzinali. Mpingo wa Chikhristu utangokhazikitsidwa kumene mu nthawi ya atumwi, Yehova “anacheukira anthu a mitundu ina . . . kuti mwa iwo atengemo anthu odziwika ndi dzina lake.” (Mac. 15:14) Akhristu oyambirira ankasangalala kugwiritsa ntchito dzina la Mulungu komanso kuuza ena zokhudza dzinali. Iwo ankaligwiritsa ntchito akamalalikira komanso akamalemba mabuku a m’Baibulo. Choncho anasonyezadi kuti anali anthu odziwika ndi dzina la Mulungu. (Mac. 2:14, 21) Masiku anonso a Mboni za Yehova ndi anthu odziwika ndi dzina la Mulungu. w21.10 20-21 ¶8-10
Lolemba, January 16
[Muzichita] chidwi ndi ntchito za Yehova zosonyeza kukoma mtima kwake kosatha.—Sal. 107:43.
Chikondi chokhulupirika cha Mulungu chidzakhalapobe mpaka kalekale. Mfundo imeneyi yokhudza chikondi chokhulupirika ikupezeka maulendo 26 mu Salimo 136. Muvesi loyambirira timawerenga kuti: “Yamikani Yehova anthu inu, pakuti iye ndi wabwino. Kukoma mtima kwake kosatha kudzakhalapobe mpaka kalekale.” (Sal. 136:1) Pavesi lililonse, kuyambira vesi 2 mpaka 26 timapezapo mawu akuti, “pakuti kukoma mtima kwake kosatha [chikondi chokhulupirika] kudzakhalapobe mpaka kalekale.” Tikamawerenga salimo limeneli timachita chidwi ndi njira zosiyanasiyana zimene Yehova amasonyezera chikondi chake chokhulupirika nthawi zonse. Mawu amene atchulidwa mobwerezabwereza akuti “pakuti kukoma mtima kwake kosatha kudzakhalapobe mpaka kalekale,” akutitsimikizira kuti chikondi cha Mulungu kwa anthu ake sichisintha. N’zolimbikitsa kudziwa kuti Yehova samafulumira kusiya kukonda atumiki ake. M’malomwake iye amakhala nawo pafupi ndipo sawasiya makamaka pamene akukumana ndi mavuto. Kudziwa kuti Yehova amapitirizabe kukhala nafe, kumatithandiza kukhala osangalala komanso kumatipatsa mphamvu kuti tithe kupirira mavuto amene tikukumana nawo n’kupitirizabe kuyenda pa njira ya kumoyo.—Sal. 31:7. w21.11 4 ¶9-10
Lachiwiri, January 17
Mitima yanu isavutike. Khulupirirani Mulungu.—Yoh. 14:1.
Kodi nthawi zina mumachita mantha mukaganizira zimene zichitike m’tsogolomu monga kuwonongedwa kwa chipembedzo chonyenga, kuukiridwa ndi Gogi wa ku Magogi komanso nkhondo ya Aramagedo? Kodi mwina mumadzifunsa kuti, ‘Zochitika zochititsa manthazi zikadzayamba, ndidzakhalabe wokhulupirika?’ Ngati mumada nkhawa ndi zimenezi, mawu a Yesu opezeka mulemba lalero, angakuthandizeni kwambiri. Yesu anauza ophunzira ake kuti: “Mitima yanu isavutike. Khulupirirani Mulungu.” Chikhulupiriro cholimba chidzathandiza kuti tikhale olimba mtima, kaya tidzakumana ndi zotani. Tingalimbitse chikhulupiriro chathu kuti tidzathe kupirira mayesero omwe tidzakumane nawo m’tsogolo tikaganizira zimene timachita panopa tikakumana ndi mayesero. Zimenezi zingatithandize kuona mbali zimene tiyenera kulimbitsa chikhulupiriro chathu. Nthawi iliyonse tikapirira mayesero enaake, chikhulupiriro chathu chimalimba kwambiri. Ndipo zimenezi zidzatithandiza kuti tidzapirire mayesero omwe tidzakumane nawo m’tsogolo. w21.11 20 ¶1-2
Lachitatu, January 18
Pamene ndili wofooka, m’pamene ndimakhala wamphamvu.—2 Akor. 12:10.
Mtumwi Paulo analimbikitsa Timoteyo komanso Akhristu onse kuti azichita zonse zomwe angathe pa utumiki wawo. (2 Tim. 4:5). Koma nthawi zina kuchita zimenezi kumakhala kovuta. Mwachitsanzo, taganizirani za abale athu amene akukhala m’mayiko omwe ntchito yathu ndi yoletsedwa. Atumiki a Yehova amakumana ndi mavuto osiyanasiyana omwe akhoza kuwafooketsa. Mwachitsanzo, ena amafunika kugwira ntchito maola ambiri kuti athe kupeza zinthu zofunika posamalira mabanja awo. Iwo amafunitsitsa atachita zambiri pa ntchito yolalikira koma pofika kumapeto kwa mlungu amakhala atatopa. Ndipo ena amalephera kuchita zambiri chifukwa akudwala matenda aakulu kapenanso chifukwa cha uchikulire moti sangathe kuchoka pakhomo. Ndiye pali enanso omwe amavutika ndi maganizo odziona ngati opanda pake. Kaya zinthu zili bwanji pa moyo wathu, Yehova angatipatse mphamvu kuti tithe kupirira mavuto athu n’kupitirizabe kumutumikira mmene tingathere. w21.05 20 ¶1-3
Lachinayi, January 19
[Musamaipitse] dzina la Mulungu wanu.—Lev. 19:12.
Nthawi zina ena angatilimbikitse kuchita zinthu zosemphana ndi kulambira kwathu. Zikatero timayenera kusankha zochita pa nkhani yofunikayi. Taganizirani mfundo yochititsa chidwi yomwe ili pa Levitiko 19:19, lomwe mbali ina limati: “musamavale chovala cha ulusi wa mitundu iwiri yosakaniza.” Lamuloli linkathandiza kuti Aisiraeli azioneka mosiyana ndi anthu a mitundu yoyandikana nawo. Popeza kuti masiku ano sititsatira Chilamulo, sizolakwika kuti Mkhristu avale chovala chopangidwa ndi mitundu yosiyanasiyana ya ulusi. Komabe n’zolakwika kuti tizichita zinthu ngati anthu omwe zikhulupiriro komanso zochita zawo n’zosemphana ndi zimene Baibulo limaphunzitsa. N’zoona kuti timakonda achibale athu komanso anthu ena komabe pa nkhani zofunika kwambiri zokhudza moyo, monga atumiki a Yehova timafunitsitsa kukhala osiyana ndi ena. Kuchita zimenezi n’kofunika kuti tikhale oyera.—2 Akor. 6:14-16; 1 Pet. 4:3, 4. w21.12 5 ¶14; 6 ¶16
Lachisanu, January 20
Chipata cholowera ku moyo n’chopapatiza komanso msewu wake ndi wopanikiza.—Mat. 7:14.
N’zotheka kupeza msewu wopita kumoyo. Yesu anati: “Mukamasunga mawu anga nthawi zonse, ndiye kuti ndinudi ophunzira anga. Mudzadziwa choonadi, ndipo choonadi chidzakumasulani.” (Yoh. 8:31, 32) Tikuyamikira kuti simunangotsatira chikhamu cha anthu, koma munafufuza choonadi. Munayamba kuphunzira mwakhama Mawu a Mulungu kuti mudziwe zimene iye amafuna ndipo munamvera zimene Yesu anaphunzitsa. Munaphunzira kuti Yehova amafuna kuti tizipewa ziphunzitso za zipembedzo zonyenga komanso kuti tisamachite nawo maholide achikunja. Munaphunziranso kuti sizophweka kusiya makhalidwe amene Yehova amadana nawo n’kumachita zimene amafuna. (Mat. 10:34-36) Mwina zinkakuvutani kuti musiye zinthu zina pa moyo wanu. Komabe munayesetsa kuti musinthe chifukwa mumakonda Atate wanu wakumwamba. Yehova anasangalalatu kwambiri ndi zimene munachita.—Miy. 27:11. w21.12 22 ¶3; 23 ¶5
Loweruka, January 21
Tamvera mwana wanga, ndipo utsatire mawu anga.—Miy. 4:10.
Mose ndi chitsanzo chabwino kwambiri cha munthu amene anavomera kuwongoleredwa atalakwitsa kwambiri zinthu. Pa nthawi ina, iye anakwiya kwambiri ndipo sanalemekeze Yehova. Chifukwa cha zimenezi anataya mwayi wolowa m’Dziko Lolonjezedwa. (Num. 20:1-13) Mose atapempha Yehova kuti asinthe maganizo ake pankhaniyi, iye anamuuza kuti: “Usatchulenso nkhani imeneyi kwa ine.” (Deut. 3:23-27) Mose sanakwiye nazo zimenezi. M’malomwake anavomereza zimene Yehova anasankha ndipo iye anapitiriza kumugwiritsa ntchito potsogolera Aisiraeli. (Deut. 4:1) Mose ndi chitsanzo chabwino kwambiri chimene tingatengere pa nkhani yovomera kupatsidwa malangizo. Anasonyeza kuti anavomera malangizo amene Yehova anamupatsa pokhalabe wokhulupirika ngakhale kuti anali atataya mwayi umene unali wamtengo wapatali kwa iye. Timapindula kwambiri tikamatsanzira anthu okhulupirika monga Mose. (Miy. 4:10-13) Abale ndi alongo athu ambiri akhala akumutsanzira polola kulangizidwa. w22.02 11 ¶9-10
Lamlungu, January 22
Yesu anagwetsa misozi.—Yoh. 11:35.
Cha munyengo yozizira mu 32 C.E., Lazaro yemwe anali mnzake wapamtima wa Yesu anadwala n’kumwalira. (Yoh. 11:3, 14) Iye anali ndi azichemwali ake awiri, Mariya ndi Marita, ndipo Yesu ankakonda kwambiri banja limeneli. Marita atamva kuti Yesu akubwera, anathamanga kuti akakumane naye. Tangoganizani mmene iye ankamvera pamene anati: “Ambuye, mukanakhala kuno mlongo wanga sakanamwalira.” (Yoh. 11:21, 32, 33) Yesu ayenera kuti anagwetsa misozi poona mmene Mariya ndi Marita anakhudzidwira chifukwa cha imfa ya mlongo wawo. Ngati wokondedwa wanu anamwalira, Yehova amamvetsa mmene mukumvera. Yesu ndi “chithunzi chenicheni” cha Atate wake. (Aheb. 1:3) Iye atagwetsa misozi, anasonyeza mmene Yehova amamvera. (Yoh. 14:9) Ngati muli ndi chisoni chifukwa cha imfa ya munthu amene munkamukonda, mungakhale otsimikiza kuti sikuti Yehova amangoona zimenezo, koma amakhudzidwanso chifukwa cha mmene mukumvera. Iye amafuna kukutonthozani.—Sal. 34:18; 147:3. w22.01 15 ¶5-7
Lolemba, January 23
Munthu amakhala ndi chikhulupiriro chifukwa cha zimene wamva.—Aroma 10:17.
Mungapindule kwambiri mukamapeza nthawi yoti muzilankhula, kumvetsera komanso kuganizira za Yehova. Choyamba, muzisankha zochita mwanzeru. Baibulo limatitsimikizira kuti “munthu woyenda ndi anthu anzeru adzakhala wanzeru.” (Miy. 13:20) Chachiwiri, mukhoza kukhala mphunzitsi wabwino. Tikamaphunzira Baibulo ndi munthu, chimodzi mwa zolinga zathu zikuluzikulu ndi kumuthandiza kukhala pa ubwenzi ndi Yehova. Tikamayesetsa kupemphera komanso kuphunzira za Atate wathu wakumwamba m’pamenenso timayamba kumukonda kwambiri. Izi zimachititsa kuti tikhale okonzeka mokwanira kuthandiza amene tikuphunzira naye Baibulo kuti nayenso ayambe kukonda Yehova. Chitsanzo pa nkhaniyi ndi Yesu. Iye ankafotokoza zokhudza Atate wake mokoma mtima komanso mwachikondi moti otsatira ake okhulupirika sakanachitira mwina koma nawonso kuyamba kukonda Yehova. (Yoh. 17:25, 26) Chachitatu, chikhulupiriro chanu chidzalimba kwambiri. Taganizirani zimene zimachitika mukapempha Mulungu kuti akutsogolereni, akulimbikitseni kapena akuthandizeni. Nthawi iliyonse imene Yehova wayankha pemphero lanu, mumayamba kumukhulupirira kwambiri.—1 Yoh. 5:15. w22.01 30 ¶15-17
Lachiwiri, January 24
Vulani umunthu wakale pamodzi ndi ntchito zake.—Akol. 3:9.
Yehova amatilimbikitsa kuti tisiye maganizo komanso makhalidwe oipa amene tinazolowera chifukwa choti amatikonda kwambiri ndipo amafuna kuti tizisangalala ndi moyo. (Yes. 48:17, 18) Iye amadziwa kuti anthu amene amangotsatira zinthu zoipa zomwe amalakalaka amadzivulaza okha komanso anthu ena. Zimam’pweteka kutiona tikuchita zinthu zimene zingativulaze komanso zimene zingavulaze anthu ena. Poyamba mwina anzathu kapena achibale angamatinyoze chifukwa choyesetsa kusintha makhalidwe athu. (1 Pet. 4:3, 4) Iwo angamatiuze kuti tili ndi ufulu wochita chilichonse chimene tikufuna komanso kuti sitiyenera kulola aliyense kutiuza zochita. Koma amene amakana mfundo za Yehova zokhudza chabwino ndi choipa sikuti amakhaladi pa ufulu. M’malomwake, iwo amakhala kuti akulola dziko lolamulidwa ndi Satanali liziwaumba. (Aroma 12:1, 2) Tonsefe tiyenera kusankha kuti kaya tipitirizabe kukhala ndi umunthu wathu wakale, womwe umatsogoleredwa ndi uchimo ndi dziko la Satanali, kapena kulola kuti Yehova atisinthe n’kukhala munthu wabwino kwambiri panopa.—Yes. 64:8. w22.03 3 ¶6-7
Lachitatu, January 25
Mawu a Mulungu ndi amoyo ndi amphamvu, ndipo ndi akuthwa kuposa lupanga lililonse lakuthwa konsekonse. . . . amathanso kuzindikira zimene munthu akuganiza komanso zolinga za mtima wake.—Aheb. 4:12.
Kuganizira mozama zimene tawerenga m’Mawu a Mulungu kungatithandize kukhala ndi maganizo oyenera pa mavuto amene takumana nawo. Tiyeni tione mmene Baibulo linathandizira mlongo wina wamasiye yemwe anali ndi chisoni chachikulu. Mkulu wina anamuuza kuti angapeze mfundo zothandiza ngati atawerenga buku la Yobu. Atangoyamba kuwerenga bukuli, mlongoyu ankaona kuti Yobu anali ndi maganizo olakwika ndipo mumtima mwake anayamba kumudzudzula kuti: “Yobu, amenewotu si maganizo abwino.” Koma kenako anazindikira kuti nayenso anali ndi maganizo olakwika ngati Yobu. Zimenezi zinamuthandiza kuti asinthe n’kuyamba kuona zinthu moyenera komanso zinamupatsa mphamvu kuti athe kupirira ululu umene ankamva chifukwa cha imfa ya mwamuna wake. Njira ina imene Yehova amatipatsira mphamvu ndi kudzera mwa olambira anzathu. Paulo analemba kuti ankalakalaka atakumana ndi abale ndi alongo n’cholinga choti ‘alimbikitsane.’—Aroma 1:11, 12. w21.05 22 ¶10-11; 24 ¶12
Lachinayi, January 26
Uzichitira Yehova Mulungu wako chikondwerero chimenecho masiku 7 pamalo amene Yehova adzasankhe.—Deut. 16:15.
Aisiraeli anauzidwa kuti: “Mwamuna aliyense pakati panu azikaonekera katatu pa chaka pamaso pa Yehova Mulungu wanu, pamalo amene Mulungu adzasankhe.” (Deut. 16:16) Iwo ankafunika kusiya nyumba ndi mbewu zawo popanda woziyang’anira. Yehova anawalonjeza kuti: “Palibe aliyense adzasirira dziko lanu pamene mwachoka kukaona nkhope ya Yehova Mulungu wanu.” (Eks. 34:24) Popeza kuti ankakhulupirira kwambiri Yehova, Aisiraeli oopa Mulunguwa ankapezeka pa zikondwererozi chaka chilichonse. Zimenezi zinkachititsa kuti azidalitsidwa kwambiri. Mwachitsanzo, ankamvetsa bwino Chilamulo cha Mulungu, kuganizira ubwino wake ndiponso ankalimbikitsidwa akasonkhana ndi olambira anzawo. Ifenso timapindula kwambiri ndi zinthu zimenezi tikamayesetsa kuti tikapezeke pamisonkhano. Komanso taganizirani mmene Yehova amasangalalira tikafika pamisonkhano titakonzekera kupereka ndemanga zachidule komanso zolimbikitsa. w22.03 22 ¶9
Lachisanu, January 27
Amatha kuthandiza anthu amene akuyesedwa.—Aheb. 2:18.
Yehova ankakonzekeretsa Yesu kuti adzakwaniritse udindo wake wam’tsogolo monga Mkulu wa Ansembe. Yesu anaona mmene zimakhalira zovuta kumvera Mulungu ukakumana ndi mayesero aakulu. Iye anapanikizika kwambiri mpaka anafika popempha Yehova kuti amuthandize, ‘akufuula komanso akugwetsa misozi.’ Popeza kuti anavutikapo kwambiri chonchi, Yesu amamvetsa mmene timamvera ndipo “amatha kuthandiza anthu amene akuyesedwa.” Timayamikira kwambiri kuti Yehova anatipatsa mkulu wa ansembe wachifundo, yemwe ‘amatimvera chisoni pa zofooka zathu.’ (Aheb. 2:17; 4:14-16; 5:7-10) Yehova analolera kuti Yesu avutike kwambiri chifukwa ankafuna kupereka yankho pa funso lofunika kwambiri, lakuti: Kodi anthu angakhalebe okhulupirika kwa Yehova ngakhale atakumana ndi mayesero aakulu? Satana amatsutsa zimenezi. Iye amanena kuti anthu amatumikira Mulungu ndi zolinga zadyera komanso kuti sakonda Yehova. (Yobu 1:9-11; 2:4, 5) Yesu anakhalabe wokhulupirika ndipo anasonyeza kuti Satana ndi wabodza. w21.04 16-17 ¶7-8
Loweruka, January 28
Choncho pitani mukaphunzitse anthu . . . kuti akhale ophunzira anga. . . . , ndi kuwaphunzitsa kusunga zinthu zonse zimene ndinakulamulirani.—Mat. 28:19, 20.
Wophunzira Baibulo asanabatizidwe, ayenera kumagwiritsa ntchito zimene amaphunzira. Akamachita zimenezi angafanane ndi “munthu wochenjera” wa m’fanizo la Yesu, yemwe anakumba kwambiri pansi kuti amange nyumba yake pathanthwe. (Mat. 7:24, 25; Luka 6:47, 48) Muzithandiza wophunzira wanu kusintha zinthu pa moyo wake. (Maliko 10:17-22) Yesu ankadziwa kuti zikanakhala zovuta kuti munthu wina wolemera agulitse zinthu zake zonse. (Maliko 10:23) Komabe iye anamuuza kuti achite zimenezi ngakhale kuti kunali kusintha kwakukulu pa moyo wake. Yesu anamuuza izi chifukwa ankamukonda kwambiri. Nthawi zina tingalephere kulimbikitsa wophunzira wathu kuti asinthe zinthu zina pa moyo wake poganiza kuti sanakonzeke kuchita zimenezi. (Akol. 3:9, 10) Koma mukakambirana naye mofulumira zinthu zimene afunika kusintha, wophunzirayo amayambanso kusintha mofulumira. Mukamakambirana naye nkhani ngati zimenezi mumasonyeza kuti mumamuganizira.—Sal. 141:5; Miy. 27:17. w21.06 3 ¶3, 5
Lamlungu, January 29
Khristu . . . anakusiyirani chitsanzo kuti mutsatire mapazi ake mosamala kwambiri.—1 Pet. 2:21.
Mtumwi Petulo kwenikweni ankafotokoza chitsanzo chabwino chimene Yesu anatipatsa pa nkhani yopirira. Komabe pali zinthu zambiri zimene Yesu anachita zomwe tiyenera kutsanzira. (1 Pet. 2:18-25) Ndipotu zonse zimene Yesu ankalankhula komanso kuchita pa moyo wake ndi chitsanzo chabwino chimene tiyenera kutengera. Popeza kuti si ife angwiro, kodi tingathedi kutengera chitsanzo cha Yesu? Inde n’zotheka. Kumbukirani kuti Petulo sananene kuti tizitsatira mapazi a Yesu ndendende, m’malomwake iye anati ‘tizitsatira mapazi a [Yesu] mosamala kwambiri.’ Tikamayesetsa kuchita zonse zomwe tingathe potsatira mapazi ake mosamala kwambiri, tidzakhala tikumvera mawu a mtumwi Yohane akuti: ‘Pitirizani kuyenda mmene iyeyo [Yesu] anayendera.’ (1 Yoh. 2:6) Tikamatsatira mapazi a Yesu tidzakhala pa ubwenzi wabwino ndi Yehova. N’chifukwa chiyani tikutero? Chifukwa choyamba n’chakuti Yesu anatisiyira chitsanzo chabwino cha zimene tiyenera kuchita kuti tizisangalatsa Mulungu. (Yoh. 8:29) Choncho tikamatsatira mapazi a Yesu, timasangalatsa Yehova. Ndipo tingakhale otsimikiza kuti Atate wathu wakumwamba adzakhala pa ubwenzi ndi onse amene amayesetsa kuti akhale anzake.—Yak. 4:8. w21.04 3 ¶4-6
Lolemba, January 30
Yehova amasangalala ndi anthu ake.—Sal. 149:4.
Yehova amaona makhalidwe athu abwino, amadziwa zimene tingakwanitse kuchita komanso amatithandiza kuti tikhale naye pa ubwenzi. Tikapitiriza kukhala okhulupirika, iyenso adzapitiriza kukhala nafe pa ubwenzi mpaka kalekale. (Yoh. 6: 44). Tikakhala kuti sitikukayikira kuti Yehova amatikonda timafunitsitsa kumutumikira ndi mtima wonse ngakhale tikumane ndi mavuto. Koma tikayamba kukayikira, ‘mphamvu zathu zimakhala zochepa.’ (Miy. 24:10) Ndipo tikafooka n’kusiya kukhulupirira kuti Mulungu amatikonda, Satana angatigonjetse mosavuta. (Aef. 6:16) Akhristu ena okhulupirika, chikhulupiriro chawo chafooka chifukwa chokayikira kuti Yehova amawakonda. Kodi tingatani ngati tayamba kukhala ndi maganizo amenewa? Tiyenera kuwachotsa mwamsanga. Tizipempha Yehova kuti atithandize kuchotsa ‘malingaliro amene akutisowetsa mtendere,’ n’kutipatsa ‘mtendere umene udzateteza mitima yathu ndi maganizo athu.’ (Sal. 139:23; Afil. 4:6, 7) Komanso muzikumbukira kuti simuli nokha. w21.04 20 ¶1; 21 ¶4-6
Lachiwiri, January 31
Mulungu . . . amalimbitsa zolakalaka zanu kuti muchite zinthu zonse zimene iye amakonda.—Afil. 2:13.
Kodi munayamba bwanji choonadi? Choyamba munamva uthenga wabwino mwina kwa makolo anu, mnzanu wakuntchito kapena wakusukulu kapenanso kwa a Mboni ena omwe ankalalikira khomo ndi khomo. (Maliko 13:10) Kenako wa Mboni wina anachita khama kumaphunzira nanu Baibulo. Pa nthawi imene ankaphunzira nanu, munayamba kukonda Yehova ndipo munadziwa kuti iyenso amakukondani. Yehova anakuthandizani kudziwa choonadi ndipo panopa ndinu wophunzira wa Yesu Khristu komanso mukuyembekezera kudzapeza moyo wosatha. (Yoh. 6:44) Mosakayikira, mumayamikira Yehova kuti analimbikitsa munthu wina kuti akuphunzitseni choonadi komanso analola kuti mukhale mtumiki wake. Tsopano popeza kuti tikudziwa choonadi, tili ndi mwayi wothandiza ena kuti nawonso aziyenda panjira yopita ku moyo wosatha. N’kutheka kuti sizimativuta kulalikira kunyumba ndi nyumba. Koma mwina zikhoza kumativuta kuti tiyambitse komanso kuchititsa maphunziro a m’Baibulo. w21.07 2 ¶1-2