Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • es23 tsamba 17-26
  • February

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • February
  • Kuphunzira Malemba Tsiku ndi Tsiku—2023
  • Timitu
  • Lachitatu, February 1
  • Lachinayi, February 2
  • Lachisanu, February 3
  • Loweruka, February 4
  • Lamlungu, February 5
  • Lolemba, February 6
  • Lachiwiri, February 7
  • Lachitatu, February 8
  • Lachinayi, February 9
  • Lachisanu, February 10
  • Loweruka, February 11
  • Lamlungu, February 12
  • Lolemba, February 13
  • Lachiwiri, February 14
  • Lachitatu, February 15
  • Lachinayi, February 16
  • Lachisanu, February 17
  • Loweruka, February 18
  • Lamlungu, February 19
  • Lolemba, February 20
  • Lachiwiri, February 21
  • Lachitatu, February 22
  • Lachinayi, February 23
  • Lachisanu, February 24
  • Loweruka, February 25
  • Lamlungu, February 26
  • Lolemba, February 27
  • Lachiwiri, February 28
Kuphunzira Malemba Tsiku ndi Tsiku—2023
es23 tsamba 17-26

February

Lachitatu, February 1

Yehova ali pafupi ndi onse oitanira pa iye.​—Sal. 145:18.

Yehova amachita chidwi kwambiri ndi zimene zimachitikira anthu amene amamulambira. Iye ali pafupi ndi aliyense wa ife ndipo amaona tikakhumudwa kapena kufooka ndi zinazake. (Sal. 145:18, 19) Taganizirani mmene anasonyezera kuti anakhudzidwa chifukwa cha mmene mneneri wake Eliya ankamvera. Munthu wokhulupirikayu anakhala ndi moyo pa nthawi imene zinthu sizinali bwino ku Isiraeli. Olambira Yehova ankazunzidwa kwambiri ndipo Eliya anali mdani wamkulu wa anthu amene ankatsutsa Mulungu. (1 Maf. 19:1, 2) N’kuthekanso kuti Eliya ankavutika maganizo chifukwa ankadziona kuti anali mneneri wa Yehova yekhayo amene anatsala. (1 Maf. 19:10) Mulungu anazindikira mwansanga mmene Eliya ankamvera. Choncho anatumiza mngelo kuti akamutsimikizire mneneri wakeyu kuti sanali yekha koma panali Aisiraeli enanso ambiri oopa Mulungu. (1 Maf. 19:5, 18) Mokoma mtima, Yesu anatsimikizira ophunzira ake kuti adzapeza abale ndi alongo ambiri omwe adzakhale ngati anthu a m’banja lawo. (Maliko 10:29, 30) Ndipo Yehova, yemwe ndi Atate wathu wakumwamba, akulonjeza kuti adzapitiriza kuthandiza aliyense amene wasankha kumutumikira.—Sal. 9:10. w21.06 8-9 ¶3-4

Lachinayi, February 2

Wochokera kwa Mulungu amamvetsera mawu a Mulungu.​—Yoh. 8:47.

Anthu ambiri amakana kumvetsera uthenga wathu chifukwa timagwiritsa ntchito mfundo za m’Baibulo pothandiza ena kudziwa zinthu zabodza zomwe zipembedzo zimaphunzitsa. Atsogoleri achipembedzo amaphunzitsa anthu awo kuti Mulungu amalanga anthu oipa kumoto. Iwo amaphunzitsa zimenezi pofuna kuti anthu asamachite zoipa. Monga atumiki a Yehova omwe amalambira Mulungu yemwe ndi wachikondi, timathandiza anthu kudziwa kuti zimenezi ndi zabodza. Atsogoleriwo amaphunzitsanso kuti mzimu wa munthu suufa. Zimenezi zikanakhala zoona, sipakanafunikanso kuti anthu adzaukitsidwe. Choncho timathandiza anthu kudziwa kuti izi si zomwe Baibulo limaphunzitsa. Komanso, mosiyana ndi zipembedzo zambiri zomwe zimaphunzitsa kuti Mulungu kapena mphamvu inayake yosaoneka ndi zimene zimachititsa zonse zomwe zimachitika pa moyo wathu, timaphunzitsa kuti aliyense ali ndi ufulu wosankha kutumikira Mulungu kapena ayi. Ndiye kodi atsogoleri achipembedzo amatani chifukwa cha zimene timachitazi? Nthawi zambiri, iwo amakwiya. Ngati timakonda choonadi, tiyenera kukhulupirira komanso kumvera zimene Mulungu amanena. (Yoh. 8:45, 46) Mosiyana ndi Satana Mdyerekezi, ndife okhazikika m’choonadi. Timachita zinthu mogwirizana ndi zimene timakhulupirira. (Yoh. 8:44) Mulungu amafuna kuti anthu ake ‘azinyansidwa ndi choipa’ ndipo ‘azigwiritsitsa chabwino,’ ngati mmene Yesu anachitira.​—Aroma 12:9; Aheb. 1:9. w21.05 10 ¶10-11

Lachisanu, February 3

Tsutsani Mdyerekezi ndipo adzakuthawani.​—Yak. 4:7.

Kodi tiyenera kuchita chiyani ngati tazindikira kuti tayamba kukhala ndi mtima wonyada kapena wadyera? Tikhoza kusintha. Mtumwi Paulo ananena kuti anthu amene Mdyerekezi “wawagwira amoyo” mu msampha wake, akhoza kupulumuka. (2 Tim. 2:26) Tizikumbukira kuti Yehova ndi wamphamvu kuposa Satana. Choncho tikamavomera kuti Yehova atithandize tikhoza kupulumuka ku msampha uliwonse umene Mdyerekezi angatitchere. N’zoona kuti tikhoza kupulumuka ngati titagwidwa ku misampha ya Satana, koma zingakhale bwino ngati titapeweratu misampha yakeyi ndipo Mulungu ndi amene angatithandize. Choncho tsiku lililonse muzipempha Yehova kuti akuthandizeni kuzindikira ngati zoganiza komanso zochita zanu zikusonyeza kuti mwayamba kukhala ndi makhalidwe oipawa. (Sal. 139:23, 24) Muziyesetsa kuti musakhale onyada kapena adyera. Satana wakhala ali mlenje kwa zaka zambiri. Koma posachedwapa iye adzamangidwa ndipo kenako adzawonongedwa. (Chiv. 20:1-3, 10) Tikuyembekezera mwachidwi nthawi imeneyi. Koma panopa tiyenera kukhala tcheru kuti tisakodwe m’misampha yakeyi. Muziyesetsa kupewa mtima wonyada kapena wadyera. Ndipo khalani wotsimikiza ‘kutsutsa Mdyerekezi ndipo adzakuthawani.’ w21.06 19 ¶15-17

Loweruka, February 4

Pemphani Mwini zokolola kuti atumize antchito kukakolola.​—Mat. 9:38.

Yehova amasangalala munthu akaphunzira choonadi cha m’Baibulo n’kumauzako ena zimene waphunzirazo. (Miy. 23:15, 16) Iye ayenera kuti amasangalala kwambiri akaona zimene zikuchitika masiku ano. Mwachitsanzo, ngakhale kuti m’chaka chautumiki cha 2020 padziko lonse panali mliri, tinachititsa maphunziro a Baibulo 7,705,765 zomwe zinathandiza kuti anthu 241,994 adzipereke kwa Yehova n’kubatizidwa. Ophunzira atsopanowa, nawonso azichititsa maphunziro a Baibulo kuti anthu enanso ambiri akhale ophunzira a Yesu. (Luka 6:40) N’zosakayikitsa kuti timasangalatsa mtima wa Yehova tikamagwira nawo ntchito yothandiza anthu kuti akhale ophunzira. Kuthandiza anthu kuti akhale ophunzira kumafuna khama. Koma Yehova angatithandize kuphunzitsa atsopano amenewa kuti azikonda Atate wathu wakumwamba. Bwanji osakhala ndi cholinga choyambitsa komanso kuchititsa phunziro la Baibulo, ngakhale limodzi lokha? Tikhoza kudabwa ndi zimene zingachitike ngati titamagwiritsa ntchito mpata uliwonse umene wapezeka kupempha munthu kuti tiziphunzira naye Baibulo. w21.07 6-7 ¶14-16

Lamlungu, February 5

Chifukwa chakuti ndikusangalala ndi nyumba ya Mulungu wanga, ndili ndi chuma chapadera chomwe ndi golide ndi siliva. Ndikupereka chuma chimenechi kunyumba ya Mulungu wanga.​—1 Mbiri 29:3.

Mfumu Davide anapereka zinthu zake zochuluka zothandiza pantchito yomanga kachisi. (1 Mbiri 22:11-16) Ngati tilibenso mphamvu moti sitingagwire nawo ntchito ya zomangamanga, tingathandize pa ntchitoyi popereka ndalama zathu mogwirizana ndi mmene zinthu zilili pa moyo wathu. Tingathandizenso achinyamata ndi luso limene tapeza. Pa nkhani ya kuwolowa manja, taganizirani chitsanzo cha mtumwi Paulo. Iye anapempha Timoteyo kuti aziyenda naye pa maulendo a umishonale ndipo anaphunzitsa wachinyamatayu zimene angachite kuti azilalikira komanso kuphunzitsa bwino. (Mac. 16:1-3) Zimenezi zinathandiza kuti Timoteyo azilalikira komanso kuphunzitsa mwaluso uthenga wabwino. (1 Akor. 4:17) Pamapeto pake nayenso Timoteyo ankaphunzitsa ena zimene anaphunzira kwa Paulo. w21.09 12 ¶14-15

Lolemba, February 6

Mukuchitirana nsanje ndi kukangana nokhanokha.​—1 Akor. 3:3.

Kodi tingaphunzirepo chiyani pa chitsanzo cha Apolo ndi mtumwi Paulo? Anthu awiri onsewa ankadziwa bwino Malemba. Onse anali aphunzitsi abwino komanso odziwika. Ndiponso onse anali atathandiza anthu ambiri kukhala ophunzira. Koma palibe amene ankaona mnzake ngati wopikisana naye. (Mac. 18:24) Ndipotu patapita nthawi Apolo atachoka ku Korinto, Paulo anamulimbikitsa kuti abwererekonso. (1 Akor. 16:12) N’zoonekeratu kuti Apolo ankagwiritsa bwino ntchito luso lake polalikira uthenga wabwino komanso kulimbikitsa abale. Tingathenso kunena motsimikiza kuti Apolo anali wodzichepetsa. Mwachitsanzo, palibe paliponse m’Baibulo pamene pamasonyeza kuti iye anakhumudwa pamene Akula ndi Purisikila anamutenga ndi “kumufotokozera njira ya Mulungu molondola.” (Mac. 18:24-28) Mtumwi Paulo ankadziwa ntchito yabwino imene Apolo ankagwira. Koma iye sankadera nkhawa kuti anthu ena aziona kuti Apolo akumuposa. Malangizo amene Paulo anapereka kumpingo wa ku Korinto anasonyeza kuti iye anali wodzichepetsa komanso woganiza bwino.​—1 Akor. 3:4-6. w21.07 18-19 ¶15-17

Lachiwiri, February 7

Ambiri adzakhala olungama.—Aroma 5:19.

Mwadala Adamu ndi Hava sanamvere Mulungu, choncho m’pomveka kuti iye anawachotsa m’banja lake. Koma bwanji ponena za ana awo? Mwachikondi Yehova anakonza zoti adzatenge ana omvera a Adamu n’kuwaikanso m’banja lake. Iye anachita zimenezi pogwiritsa ntchito nsembe ya Mwana wake wokondedwa. (Yoh. 3:16) Chifukwa cha nsembe imeneyi anthu okwana 144,000 okhulupirika amaonedwa ngati ana a Mulungu. (Aroma 8:15-17; Chiv. 14:1) Kuwonjezera pamenepo, anthu mamiliyoni ambiri omwe ndi okhulupirika amamvera ndiponso kuchita zimene Mulungu amafuna. Iwo ali ndi chiyembekezo chodzakhala m’banja la Mulungu pambuyo pa mayesero omaliza, zikadzatha zaka 1,000. (Sal. 25:14; Aroma 8:20, 21) Ngakhale panopa anthu amenewa amatchula Yehova yemwe ndi Mlengi wawo kuti “Atate.” (Mat. 6:9) Komanso anthu amene adzaukitsidwe, adzapatsidwa mwayi woti aphunzire zimene Yehova amafuna kuti iwo azichita. Ndipo amene adzasankhe kumvera, nawonso adzapatsidwa mwayi woti akhale m’banja lake. w21.08 5 ¶10-11

Lachitatu, February 8

Muzitsimikizira kuti zinthu zofunika kwambiri ndi ziti.​—Afil. 1:10.

Mtumwi Paulo anali atapatsidwa utumiki woti achite ndipo kwa zaka zambiri ankaona utumikiwo monga chinthu chofunika kwambiri. Ankalalikira “poyera komanso kunyumba ndi nyumba.” (Mac. 20:20) Ndipotu ankalalikira pa mpata uliwonse umene wapezeka. Mwachitsanzo, pamene ankayembekezera anzake ku Atene, iye analalikira uthenga wabwino kwa anthu ena otchuka ndipo ena mwa anthuwo anamvetsera uthenga wake. (Mac. 17:16, 17, 34) Ngakhale pamene ‘anamangidwa,’ Paulo ankalalikira kwa anthu amene ankakhala pafupi naye. (Afil. 1:13, 14; Mac. 28:16-24) Paulo ankagwiritsa ntchito bwino nthawi yake. Iye nthawi zambiri ankapempha ena kuti azilalikira naye limodzi. Mwachitsanzo, pa ulendo wake woyamba waumishonale anatenga Yohane Maliko, ndipo pa ulendo wachiwiri anatenga Timoteyo. (Mac. 12:25; 16:1-4) N’zosakayikitsa kuti Paulo anayesetsa kuphunzitsa amunawa mmene angayendetsere zinthu mumpingo, kuchita maulendo aubusa komanso kukhala aphunzitsi abwino.​—1 Akor. 4:17. w22.03 27 ¶5-6

Lachinayi, February 9

[Mulungu] sali kutali ndi aliyense wa ife.—Mac. 17:27.

Anthu ena sakhulupirira kuti kuli Mlengi chifukwa amanena kuti amakhulupirira zinthu zokhazo zimene amaona. Komabe anthu amenewa amakhulupirira zinthu zina zosaoneka monga mphamvu yokoka, yomwe pali umboni woti ilipodi. Mtundu wa chikhulupiriro chomwe chatchulidwa m’Baibulo, umakhalanso ndi umboni wa “zinthu zenizeni, ngakhale kuti n’zosaoneka.” (Aheb. 11:1) Timafunika khama komanso nthawi yophunzira kuti tipeze umboni umenewu patokha. Koma anthu ambiri safuna kuchita zimenezi. Munthu amene safufuza kuti apeze umboni angamanene kuti kulibe Mulungu. Pambuyo pofufuza umboni, asayansi ena atsimikizira kuti Mulungu analenga zinthu zonse. Poyamba ankangoganiza kuti kulibe Mlengi chifukwa choti ali kuyunivesite sanaphunzitsidwe kuti zinthu zinachita kulengedwa. Komabe, iwo aphunzira zokhudza Yehova ndipo amamukonda. Tonsefe tiyenera kuyesetsa kuti tizilimbitsa chikhulupiriro chathu, kaya tinaphunzira kwambiri kapena ayi. w21.08 14 ¶1; 15-16 ¶6-7

Lachisanu, February 10

Yehova amakomera mtima aliyense, ndipo ntchito zake zonse amazichitira chifundo.—Sal. 145:9.

Yesu anagwiritsa ntchito fanizo la mwana wolowerera pofuna kutithandiza kumvetsa kuti Yehova amakonda kwambiri kusonyeza chifundo. Mwana ameneyu anachoka kwawo ndipo “anasakaza chuma chake chonse mwa kulowerera m’makhalidwe oipa.” (Luka 15:13) Kenako analapa n’kusiya makhalidwe ake oipawo, anadzichepetsa ndipo anabwerera kwawo. Ndiye kodi bambo ake anachita chiyani? Yesu anati: “Ali chapatali ndithu, bambo akewo anamuona ndipo anagwidwa chifundo. Pamenepo anamuthamangira ndi kumukumbatira ndipo anamupsompsona mwachikondi.” Bambowo sanachititse manyazi mwana wawoyo. M’malomwake, iwo anamukhululukira mwachifundo ndipo anamulandiranso m’banja lawo. Mwana wolowererayo anali atachita zoipa kwambiri koma chifukwa choti analapa, bambo akewo anamukhululukira. Bambo achifundowo mu fanizoli akuimira Yehova. Pofotokoza fanizoli, Yesu anasonyeza kuti Atate wake ndi wofunitsitsa kukhululukira ochimwa omwe alapa ndi mtima wonse.​—Luka 15:17-24. w21.10 8 ¶4; 9 ¶6

Loweruka, February 11

Mulungu anacheukira anthu a mitundu ina kwa nthawi yoyamba, kuti mwa iwo atengemo anthu odziwika ndi dzina lake.—Mac. 15:14.

Masiku ano atsogoleri ambiri azipembedzo amayesetsa kubisa zoti Mulungu ali ndi dzina. Iwo akhala akuchotsa dzinali m’Mabaibulo awo ndipo nthawi zinanso amaletsa kuligwiritsira ntchito m’matchalitchi awo. Ndiye kodi pali amene angatsutse kuti ndi a Mboni za Yehova okha omwe amalemekeza dzina la Yehova? Kuposa chipembedzo chilichonse, ifeyo ndi amene tikuthandiza kwambiri anthu kuti adziwe dzina la Mulungu. Pa nkhani imeneyi, tikuyesetsa kuchita zinthu mogwirizana ndi dzina lathu lakuti Mboni za Yehova. (Yes. 43:10-12) Tatulutsa Mabaibulo oposa 240 miliyoni a Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika, lomwe linabwezeretsa dzina la Yehova m’malo amene omasulira Mabaibulo ena anachotsamo. Ndipo timatulutsa mabuku othandiza pophunzira Baibulo omwe amagwiritsa ntchito dzina la Yehova m’zilankhulo zoposa 1,000. w21.10 20-21 ¶9-10

Lamlungu, February 12

Wina mwa abale ako akasauka pakati panu . . . , usamuumire mtima kapena kumuumitsira dzanja lako.​—Deut. 15:7.

Timalambira Yehova tikamathandiza Akhristu anzathu omwe akufunika kuthandizidwa. Yehova analonjeza kuti adzadalitsa Aisiraeli omwe ankathandiza osauka. (Deut. 15:10) Ifenso tikamathandiza olambira anzathu Yehova amaona kuti tikupereka mphatso kwa iyeyo. (Miy. 19:17) Mwachitsanzo, pamene Akhristu a ku Filipi anatumiza mphatso kwa Paulo yemwe anali mkaidi, iye ananena kuti imeneyo inali “nsembe yovomerezeka yosangalatsa kwa Mulungu.” (Afil. 4:18) Mukaona abale ndi alongo a mumpingo mwanu muzidzifunsa kuti, ‘Kodi pali wina amene ndingamuthandize?’ Yehova amasangalala akaona kuti tikugwiritsa ntchito nthawi, mphamvu, luso ndi zinthu zathu pothandiza ena. Amaona kuti imeneyi ndi mbali ya kulambira kwathu. (Yak. 1:27) Kulambira koona kumafuna nthawi komanso khama koma si chinthu cholemetsa. (1 Yoh. 5:3) N’chifukwa chiyani tikutero? Timalambira chifukwa chokonda Yehova komanso abale ndi alongo athu. w22.03 24 ¶14-15

Lolemba, February 13

Iye amawalitsira dzuwa lake pa anthu oipa ndi abwino.​—Mat. 5:45.

Tiyenera kuganizira kaye mavuto amene abale ndi alongo athu akukumana nawo kuti tikwanitse kuwachitira chifundo. Mwachitsanzo, mlongo wina akhoza kukhala akuvutika ndi matenda aakulu. Mwina sangamalankhulelankhule za vuto lakelo koma angayamikire kwambiri ngati ena atamuthandiza. Tingadzifunse kuti: Kodi tingamuthandize kuphika chakudya kapena kukonza m’nyumba? Kapenanso m’bale wina ntchito yamuthera. Kodi tingamupatse mphatso ya ndalama, mwinanso osamuuza kuti yachokera kwa ife, n’cholinga chofuna kumuthandiza mpaka atapezanso ntchito ina? Mofanana ndi Yehova tizithandiza ena ngakhale asanatipemphe. Tisamachite kudikira kuti abale ndi alongo athu atipemphe kaye kuti tiwasonyeze chifundo. Yehova amatiwalitsira dzuwa lake tsiku lililonse ndipo sitimachita kumupempha. Komanso kutentha kwa dzuwalo kumathandiza aliyense, osati anthu amene amayamikira okha. Kodi simukuvomereza kuti Yehova amasonyeza kuti amatikonda potipatsa zimene timafunikira? Timakonda kwambiri Yehova chifukwa ndi wokoma mtima komanso wowolowa manja. w21.09 22-23 ¶12-13

Lachiwiri, February 14

Inu Yehova ndinu Mulungu wabwino ndipo ndinu wokonzeka kukhululuka. Kukoma mtima kosatha kumene mumawasonyeza onse oitana pa inu ndi kwakukulu.​—Sal. 86:5.

Chikondi chokhulupirika chimamuchititsa Mulungu kuti azikhululuka. Yehova akaona kuti munthu wochimwa walapa ndipo wasintha, chikondi chokhulupirika chimamuchititsa kuti amukhululukire. Ponena za Yehova, wolemba masalimo Davide anati: “Sanatichitire mogwirizana ndi machimo athu, kapena kutipatsa chilango chogwirizana ndi zolakwa zathu.” (Sal. 103:8-11) Chifukwa cha zinthu zopweteka zimene zinamuchitikira pa moyo wake, Davide ankamvetsa bwino mmene munthu amamvera akakhala kuti akuvutika ndi chikumbumtima. Koma iye anaphunzirapo kuti Yehova ndi “wokonzeka kukhululuka.” Kodi n’chiyani chimachititsa kuti Yehova azikhululuka? Yankho likupezeka mulemba la tsiku lalero. Mogwirizana ndi mfundo yomwe Davide anatchula m’pemphero lake, Yehova amakhululuka chifukwa chikondi chokhulupirika chomwe amasonyeza n’chachikulu. Kumva chisoni chifukwa cha zoipa zimene tachita n’koyenera komanso ndi kwabwino. Kungatithandize kuti tilape n’kusiya zoipa zimene timachitazo. w21.11 5 ¶11-12

Lachitatu, February 15

Atate wathu wakumwamba, dzina lanu liyeretsedwe.​—Mat. 6:9.

Yehova amakonda dzina lake ndipo amafuna kuti aliyense azililemekeza. (Yes. 42:8) Koma kwa zaka 6000, dzina lake labwinoli lakhala likunyozedwa. (Sal. 74:10, 18, 23) Zimenezi zinayamba pamene Mdyerekezi (kutanthauza “Woneneza”) anaimba Mulungu mlandu woti ankamana Adamu ndi Hava zinthu zimene ankafunikira. (Gen. 3:1-5) Kuchokera nthawi imeneyo, Yehova wakhala akuimbidwa mlandu wabodza wakuti amamana anthu zinthu zimene amafunikira. Zinkamukhudza kwambiri Yesu kuona dzina la Atate wake likunyozedwa. Yehova yekha ndi amene ali ndi ufulu wonse wolamulira kumwamba ndi dziko lapansi ndipo ulamuliro wake ndi wabwino kwambiri. (Chiv. 4:11) Koma Mdyerekezi wakhala akusocheretsa angelo komanso anthu powachititsa kuganiza kuti Mulungu si woyenera kulamulira. Posachedwapa, nkhani imeneyi idzathetsedwa m’njira yabwino kwambiri ndipo siidzachitikanso. Yehova adzalemekezedwa pamene adzasonyeze kuti Ufumu wake wokha ndi umene ungabweretse mtendere weniweni komanso chitetezo padzikoli. w21.07 9 ¶5-6

Lachinayi, February 16

Ine ndidzakondwerabe mwa Yehova ndipo ndidzasangalala mwa Mulungu wachipulumutso changa.—Hab. 3:18.

Si zachilendo kuti mwamuna amafuna kupezera ana ndi mkazi wake chakudya chokwanira, zovala komanso malo okhala. Kodi mukukumana ndi mavuto azachuma? Ngati ndi choncho, imeneyi ndi nthawi yovuta kwa inu. Komabe mungagwiritse ntchito nthawi imeneyi kuti mulimbitse chikhulupiriro chanu. Mungapemphere kwa Yehova n’kuwerenga mawu a Yesu opezeka pa Mateyu 6:25-34 komanso kuwaganizira kwambiri. Muziganizira zitsanzo za masiku ano zosonyeza mmene Yehova amathandizira anthu omwe amatanganidwa ndi zinthu za Ufumu. (1 Akor. 15:58) Kuchita zimenezi kungakuthandizeni kuti muzikhulupirira kwambiri kuti Atate wanu wakumwamba adzakuthandizani ngati mmene anathandiziranso ena omwe anakumana ndi zomwe inu mukukumana nazo. Yehova amadziwa zomwe mumafunikira komanso mmene angakupatsireni zimenezo. Mukamaona kuti iye akukuthandizani pa moyo wanu, chikhulupiriro chanu chidzalimba kwambiri moti mudzakwanitsa kupirira mayesero aakulu omwe mudzakumane nawo m’tsogolo. w21.11 20 ¶3; 21 ¶6

Lachisanu, February 17

Wina akachita tchimo, tili ndi mthandizi wolungama, Yesu Khristu, amene ali ndi Atate.—1 Yoh. 2:1.

Kuphunzira za dipo kwathandiza Akhristu ambiri kukhala ndi chikhulupiriro cholimba. Iwo amapitirizabe kulalikira ngakhale kuti amatsutsidwa komanso akhala akupirira mayesero osiyanasiyana pa moyo wawo. Taganizirani chitsanzo cha mtumwi Yohane. Iye ankalalikira mokhulupirika choonadi chonena za Khristu komanso dipo mwina kwa zaka zoposa 60. Ali ndi zaka za m’ma 90, ulamuliro wa Roma unamuika m’ndende pachilumba cha Patimo chifukwa chomuganizira kuti anali munthu woopsa. Koma kodi iye analakwa chiyani? Iwo anamumanga chifukwa “cholankhula za Mulungu ndi kuchitira umboni za Yesu.” (Chiv. 1:9) Yohane anapereka chitsanzo chabwino pa nkhani yokhala ndi chikhulupiriro komanso kupirira. Mabuku a m’Baibulo omwe Yohane analemba, amasonyeza kuti ankakonda kwambiri Yesu ndipo ankayamikira dipo. Iye analemba zokhudza dipo kapena madalitso amene timapeza chifukwa cha dipolo, maulendo oposa 100. (1 Yoh. 2:2) N’zoonekeratu kuti Yohane ankayamikira kwambiri dipo. w21.04 17 ¶9-10

Loweruka, February 18

Usatemberere munthu wogontha, ndipo usaikire munthu wakhungu chinthu chopunthwitsa.​—Lev. 19:14.

Yehova ankayembekezera kuti atumiki ake azichita zinthu moganizira anthu omwe ali ndi mavuto pathupi lawo. Mwachitsanzo, Aisiraeli sankayenera kutemberera munthu amene ali ndi vuto losamva. Kutemberera kumeneku kunkaphatikizapo kumuopseza kapena kulankhula mawu omufunira zoipa. Kumenekutu kunali kumuchitira zinthu zoipa kwambiri munthu ameneyu. Iye sakanamva zinthu zomwe zanenedwa zokhudza iyeyo ndipo sakanatha kudziteteza. Kuwonjezera pamenepo, pa Levitiko 19:14 timaphunzira kuti atumiki a Mulungu sankafunika ‘kuikira munthu wakhungu chinthu chopunthwitsa.’ Ponena za anthu omwe ali ndi mavuto ena pathupi lawo, buku lina linanena kuti: “Kalelo ku Middle East, nthawi zina anthu amenewa ankachitidwa zachipongwe.” Munthu ankatha kuika chinthu patsogolo pa munthu wosaona n’cholinga choti akapunthwa azimuseka. Izitu zinali nkhanza. Choncho popereka lamulo limeneli, Yehova anathandiza anthu ake kuti azichitira chifundo anthu amene ali ndi mavuto ena. w21.12 8-9 ¶3-4

Lamlungu, February 19

Yakobo anachita mantha ndi kuda nkhawa kwambiri.​—Gen. 32:7.

Yakobo ankada nkhawa kwambiri poganiza kuti mwina m’bale wake adakamusungirabe chakukhosi. Ndiye anapemphera kwa Yehova za nkhaniyi mochokera pansi pa mtima. Kenako anatumiza mphatso kwa Esau. (Gen. 32:9-15) Pamapeto pake atakumana pamasom’pamaso, anayamba ndi iye kuchitapo kanthu posonyeza kuti amamulemekeza m’bale wakeyo. Iye anagwada pamaso pa Esau osati kamodzi kokha kapena kawiri, koma nthawi 7. Mwaulemu komanso modzichepetsa, Yakobo anakhazikitsa mtendere ndi m’bale wakeyo. (Gen. 33:3, 4) Tikuphunzirapo kanthu pa zimene Yakobo anachita pokonzekera kukumana ndi m’bale wake komanso zimene anachita atakumana naye. Modzichepetsa iye anapempha Yehova kuti amuthandize. Kenako anachita zinthu mogwirizana ndi pemphero lake poyesetsa kuti akhalenso pamtendere ndi Esau. Anthu awiriwa atakumana, Yakobo sanakangane ndi Esau kuti adziwe amene anali wolakwa. Cholinga cha Yakobo chinali kukhazikitsa mtendere ndi m’bale wake. Kodi mungatsanzire bwanji Yakobo?​—Mat. 5:23, 24. w21.12 25 ¶11-12

Lolemba, February 20

Mulungu ndi wamkulu kuposa mitima yathu ndipo amadziwa zonse.—1 Yoh. 3:20.

Mwina mukaganizira kuti Yesu anafa chifukwa cha machimo anu munganene kuti, ‘Koma ine sindikuyenera kulandira mphatso yamtengo wapatali imeneyi.’ N’chifukwa chiyani nthawi zina mukhoza kumva choncho? Popeza kuti si ife angwiro mtima wathu ukhoza kutinamiza n’kumaona ngati ndife opanda pake komanso sitimakondedwa. (1 Yoh. 3:19) Tikayamba kukhala ndi maganizo amenewa tizikumbukira kuti “Mulungu ndi wamkulu kuposa mitima yathu.” Ngakhale titamaganiza kuti Yehova samatikonda ndiponso sangatikhululukire tiyenera kukhala otsimikiza kuti Atate wathu wakumwamba amatikonda kwambiri ndipo amatikhululukira. Kuti tikwanitse kuchita zimenezi, tiziwerenga Mawu ake pafupipafupi, tizipemphera mobwerezabwereza komanso nthawi zonse tizicheza ndi anthu amene amamulambira. Koma kodi n’chifukwa chiyani kuchita zimenezi kuli kofunika kwambiri? Mukatero mudzayamba kumvetsa bwino kwambiri makhalidwe amene Yehova ali nawo ndipo mudzamvetsa mmene amakukonderani. Kuganizira mozama zimene mwawerenga m’Mawu a Mulungu tsiku lililonse kungakuthandizeni kuti muziganiza bwino, kapena kuti “kuwongola zinthu” m’maganizo ndi mumtima mwanu.​—2 Tim. 3:16. w21.04 23-24 ¶12-13

Lachiwiri, February 21

Ndithu, ndidzafuulira Mulungu, ndipo iye adzatchera khutu lake kwa ine.​—Sal. 77:1.

Kuti tilimbitse chikhulupiriro chathu, pamafunika zambiri osati kungophunzira chabe. Tiyenera kumaganizira mozama zimene tikuphunzira. Taganizirani zimene zinachitikira yemwe analemba Salimo 77. Wolemba salimoyu ankada nkhawa chifukwa choganiza kuti iyeyo limodzi ndi Aisiraeli anzake sankakondedwanso ndi Yehova. Maganizo amenewa anamuchititsa kuti azilephera kugona usiku. (Vesi 2-8) Ndiye kodi anatani? Iye anauza Yehova kuti: “Ndidzasinkhasinkha za ntchito zanu zonse, ndipo ndiziganizira zochita zanu.” (Vesi 12) N’zoona kuti wolemba salimoyu ankadziwa zinthu zimene Yehova anali atachitira anthu ake m’mbuyomo. Komabe anadzifunsa kuti: “Kodi Mulungu waiwala kukhala wokoma mtima, kapena watsekereza chifundo chake mwaukali?” (Vesi 9) Iye anaganizira ntchito za Yehova komanso mfundo yakuti Mulungu anali atasonyeza chifundo ndiponso kukoma mtima kwa anthu ake m’mbuyomo. (Vesi 11) Ndiye kodi zotsatirapo zake zinali zotani? Wolemba masalimoyo anakhala wotsimikiza kuti Yehova sangasiye anthu ake. (Vesi 15) w22.01 30-31 ¶17-18

Lachitatu, February 22

Kwa iye onsewa ndi amoyo.—Luka 20:38.

Kodi Yehova amamva bwanji chifukwa cha amuna ndi akazi okhulupirika omwe anamwalira? Iye amafunitsitsa kudzawaonanso. (Yobu 14:15) Tangoganizani mmene Yehova amamusowera mnzake Abulahamu. (Yak. 2:23) Taganiziraninso za Mose yemwe ankalankhula naye “pamasom’pamaso.” (Eks. 33:11) Yehova ayenera kuti amalakalaka kudzamvanso Davide ndi anthu ena omwe analemba nawo masalimo akuimba nyimbo zosangalatsa zomutamanda. (Sal. 104:33) Ngakhale kuti anzake a Mulungu amenewa anamwalira, Yehova sanawaiwale. (Yes. 49:15) Tsiku lina iye adzawaukitsa ndipo adzayambiranso kumvetsera mapemphero awo ochokera pansi pamtima komanso kuvomereza kuti azimulambira. Ngati munthu amene munkamukonda anamwalira ndiye kuti mfundo zimenezi zingakutonthozeni komanso kukulimbikitsani. Kusamvera kutayamba m’munda wa Edeni, Yehova anadziwa kuti zinthu zidzaipa kwambiri zisanakhalenso bwino. Iye amadana ndi zinthu zoipa, zachiwawa komanso zopanda chilungamo zomwe zimachitika m’dzikoli masiku ano. w21.07 10 ¶11; 12 ¶12

Lachinayi, February 23

[Tizikondana] ndi . . . chikondi chenicheni m’zochita zathu.​—1 Yoh. 3:18.

Tikamakonda abale ndi alongo athu, timasonyezanso kuti timayamikira dipo. N’chifukwa chiyani tikutero? Tikutero chifukwa Yesu sanafere ife tokha koma anaferanso abale ndi alongo athuwo. Ndiye ngati Yesu anali wofunitsitsa kuwafera, n’zoonekeratu kuti amawakonda kwambiri. (1 Yoh. 3:16-18) Timasonyeza kuti timakonda abale ndi alongo athu kudzera m’zochita zathu. (Aef. 4:29, 31–5:2) Mwachitsanzo, timawathandiza akadwala kapena akakumana ndi mavuto aakulu kuphatikizapo ngozi zam’chilengedwe. Koma kodi tiyenera kuchita chiyani Mkhristu mnzathu akalankhula kapena kuchita zinthu zimene zatikhumudwitsa? Kodi nthawi zina zimakuvutani kukhululuka? (Lev. 19:18) Ngati ndi choncho, muzitsatira malangizo akuti: “Pitirizani kulolerana ndi kukhululukirana ndi mtima wonse, ngati wina ali ndi chifukwa chodandaulira za mnzake. Monga Yehova anakukhululukirani ndi mtima wonse, inunso teroni.” (Akol. 3:13) Nthawi iliyonse imene takhululukira m’bale kapena mlongo, timasonyeza Atate wathu wakumwamba kuti timayamikira kwambiri dipo. w21.04 18 ¶12-13

Lachisanu, February 24

[Mphatso imene aliyense walandira,] igwiritseni ntchito potumikirana.​—1 Pet. 4:10.

Tikhoza kumachita khama kutumikira Yehova komanso tingathandize anthu ambiri kuti afike pobatizidwa. Koma timazindikira kuti zimenezi zimatheka chifukwa chakuti Yehova akutithandiza. Pa chitsanzo cha Apolo komanso mtumwi Paulo tikupezapo phunziro lakuti ngati tili ndi maudindo mumpingo tingachitenso zambiri polimbikitsa mtendere. Timayamikira kwambiri abale audindo akamalimbikitsa mtendere komanso mgwirizano. Iwo amachita zimenezi popereka malangizo a m’Mawu a Mulungu komanso pothandiza onse kuti asamaganizire kwambiri za iwowo, koma za Yesu Khristu yemwe ndi chitsanzo chathu. (1 Akor. 4:6, 7) Aliyense ali ndi mphatso kapena luso limene Mulungu anamupatsa. Mwina tingamaone kuti zimene timachita mumpingo ndi zazing’ono. Koma zinthu zing’onozing’ono zimene timachita polimbikitsa mgwirizano zili ngati ulusi wosokera umene umathandiza kuti chovala chilumikizane. Choncho tiyeni tonse tizichita khama kuchotsa maganizo alionse a mpikisano amene tingakhale nawo. Tiyeninso titsimikize mtima kuchita zonse zomwe tingathe polimbikitsa mtendere komanso mgwirizano mumpingo.​—Aef. 4:3. w21.07 19 ¶18-19

Loweruka, February 25

Mlongo wako adzauka.—Yoh. 11:23.

Mungakhale otsimikiza kuti mudzaonanso okondedwa anu amene anamwalira. Kulira kwa Yesu pamene ankatonthoza anzake omwe anali ndi chisoni ndi umboni woti Yesu amafunitsitsa kudzaukitsa akufa. (Yoh. 11:35) Mungathe kuthandiza amene aferedwa. Kuwonjezera pa kulira ndi Marita ndi Mariya, Yesu ankawamvetsera komanso kuwatonthoza. (Yoh. 11:25-27) Ifenso tingachite zimenezi kwa amene ali ndi chisoni chifukwa choferedwa. Dan, yemwe amakhala ku Australia, ananena kuti: “Mkazi wanga atamwalira, ndinkafunika kuthandizidwa. Mabanja angapo ankakhala nane nthawi zonse ndipo ankandimvetsera ndikamalankhula. Iwo sankandiletsa kusonyeza chisoni changa ndipo sankakhumudwa ndikamalira. Ankandithandizanso m’njira zina monga kunditsukira galimoto, kukandigulira zinthu komanso kundiphikira ngati ndikulephera kuchita zinthu zimenezi ndekha. Ankapempheranso nane pafupipafupi. Iwo anasonyeza kuti anali anzanga enieni ndiponso m’bale amene ‘anabadwira kuti akuthandize pakagwa mavuto.’”​—Miy. 17:17. w22.01 16 ¶8-9

Lamlungu, February 26

Munthu amene khutu lake limamvetsera chidzudzulo chopatsa moyo, amakhala pakati pa anthu anzeru.—Miy. 15:31.

Yehova amatifunira zabwino. (Miy. 4:20-22) Iye akatipatsa malangizo kudzera m’Mawu ake, m’mabuku ofotokoza Baibulo kapena kudzera mwa Mkhristu mnzathu, amakhala akutisonyeza chikondi chake. (Aheb. 12:9, 10) Tiziganizira kwambiri malangizowo osati mmene aperekedwera. Nthawi zina tingaone ngati munthu sanatipatse malangizo m’njira yoyenera. N’zoona kuti aliyense amene akufuna kupereka malangizo ayenera kuyesetsa kuchita zimenezo m’njira yabwino. (Agal. 6:1) Ngati ndife amene tikulangizidwa, tingachite bwino kuganizira malangizo amene tapatsidwa, ngakhale titaona kuti munthu amene watipatsa malangizoyo akanatha kuchita zimenezo m’njira yabwino. Mwina tingadzifunse kuti: ‘Ngakhale kuti sindinakonde njira imene wandipatsira malangizowo kodi pali zimene ndingaphunzirepo? Kodi ndinganyalanyaze zimene amene wandipatsa malangizoyo amalakwitsa, n’kugwiritsa ntchito malangizo amene waperekawo?’ Tingakhale anzeru ngati nthawi zonse timayesetsa kuti tizipindula ndi malangizo amene tapatsidwa. w22.02 12 ¶13-14

Lolemba, February 27

Zikumbutso za Yehova ndi zodalirika, zimapatsa nzeru munthu wosadziwa zinthu.—Sal. 19:7.

Yehova amadziwa kuti pamafunika nthawi komanso khama kuti tizipewa maganizo ndi makhalidwe oipa. (Sal. 103:13, 14) Komabe pogwiritsa ntchito Mawu ake, mzimu wake ndi gulu lake, Yehova amatipatsa nzeru, mphamvu komanso kutithandiza kuti tisinthe. Muzigwiritsa ntchito Baibulo podzifufuza. Mawu a Mulungu ali ngati galasi. Angakuthandizeni kuti mudziwe mmene mumaganizira, mmene mumalankhulira komanso mmene mumachitira zinthu. (Yak. 1:22-25) Ndipo nthawi zonse Yehova ndi wokonzeka kukuthandizani. Iye amadziwa bwino mmene angakuthandizireni chifukwa amadziwa zimene zili mumtima mwanu. (Miy. 14:10; 15:11) Choncho muzikhala ndi chizolowezi chopemphera kwa iye komanso kuphunzira Mawu ake tsiku lililonse. Musamakayikire kuti mfundo za Yehova ndi zabwino kwambiri. Tikhoza kupindula ndi zonse zimene Yehova amatiuza kuti tizichita. Anthu amene amatsatira mfundo zake amalemekezedwa, amakhala ndi moyo watanthauzo komanso amapeza chimwemwe chenicheni.​—Sal. 19:8-11. w22.03 4 ¶8-10

Lachiwiri, February 28

Ganizirani mofatsa za khoma lake lolimba. Yenderani nsanja zake zokhalamo, kuti mudzasimbire m’badwo wam’tsogolo.—Sal. 48:13.

Timalambira Yehova tikamakonza komanso kumanga malo olambirira. Baibulo limanena kuti ntchito yokonza chihema ndi zonse zokhudza chihemacho zinali “zopatulika.” (Eks. 36:1, 4) Masiku anonso Yehova amaona kuti ntchito yomanga Nyumba za Ufumu ndi nyumba zina za gulu ndi yopatulika. Abale ndi alongo ena amakhala akugwira ntchito zimenezi kwa nthawi yayitali. Kodi sitikuyenera kuyamikira zimene amachitazi zomwe ndi zofunika kwambiri pa ntchito ya Ufumu? Komabe iwo amagwiranso ntchito yolalikira. Enanso amafuna atachita upainiya. Akulu angasonyeze kuti akuthandiza pantchito ya zomangamanga, povomereza kuti abale ndi alongo akhamawa achite upainiya ngati akuyenerera. Kaya tili ndi luso la zomangamanga kapena ayi, tonsefe tingathandize pantchito yomanga ndi kukonza nyumba zolambirirazi. w22.03 22 ¶11-12

    Mabuku a Chichewa (1974-2026)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena