June
Lachinayi, June 1
Panafika mkazi wamasiye wosauka ndipo anaponyamo timakobidi tiwiri tating’ono.—Maliko 12:42.
Mayiyu ndi wosauka kwambiri moti amavutika kupeza zinthu zofunika pa moyo. Komabe iye akupita pomwe pali choponyamo zopereka ndipo akuponya timakobidi tiwiri, tomwe mwina sitinamveke phokoso n’komwe. Yesu wadziwa kuti mayiyu waponya timalepitoni tiwiri, tomwe tinali timakobidi tochepa mphamvu kwambiri pa nthawiyo. Ndalamayi inali yosakwana kugula ngakhale mpheta imodzi, yomwe inali m’gulu la mbalame zotchipa kwambiri zimene anthu ankadya. Yesu wachita chidwi kwambiri ndi mayi wamasiyeyu. Choncho akuitana ophunzira ake n’kuwauza kuti: “Mkazi wamasiye wosaukayu waponya zochuluka kuposa onse.” Kenako akunena kuti: “Onsewo [makamaka anthu olemera] aponya zimene atapa pa zochuluka zimene ali nazo, koma mayiyu, mu umphawi wake, waponya zonse zimene anali nazo, inde zonse zochirikizira moyo wake.” (Maliko 12:43, 44) Popereka ndalama zonse zomwe anali nazo patsikulo, mayi wamasiyeyo ankakhulupirira kwambiri kuti Yehova amusamalira.—Sal. 26:3. w21.04 6 ¶17-18
Lachisanu, June 2
Taonani tsopano! Mwadzaza Yerusalemu yense ndi chiphunzitso chanuchi.—Mac. 5:28.
Yesu ali padziko lapansili, ankaona moyenera utumiki wake ndipo amafunanso otsatira ake aziona moyenera utumiki wawo. (Yoh. 4:35, 36) Ophunzira ake ankachita khama kugwira ntchito yolalikira pamene iye anali nawo limodzi. (Luka 10:1, 5-11, 17) Koma Yesu atagwidwa komanso kuphedwa, ophunzirawo kwa kanthawi kochepa anasiya kulalikira. (Yoh. 16:32) Ndiyeno ataukitsidwa iye analimbikitsa ophunzirawo kuti ayambirenso kugwira ntchito yolalikira mwakhama. Ndipo Yesu atakwera kumwamba iwo analalikira mwakhama kwambiri moti adani awo anafika podandaula monga taonera mulemba laleroli. Yesu ankatsogolera ntchito ya Akhristu oyambirira ndipo Yehova anawadalitsa moti anthu ambiri anakhala okhulupirira. Mwachitsanzo, pa Pentekosite mu 33 C.E., anthu pafupifupi 3,000 anabatizidwa. (Mac. 2:41) Ndipo chiwerengero cha ophunzira chinapitiriza kukula kwambiri. (Mac. 6:7) Komabe Yesu ananeneratu kuti ntchito yolalikira idzawonjezeka kwambiri m’masiku otsiriza.—Yoh. 14:12; Mac. 1:8. w21.05 14 ¶1-2
Loweruka, June 3
Wodala amene sapeza chokhumudwitsa mwa ine.—Mat. 11:6.
Kodi mukukumbukira mmene munamvera mutazindikira kuti mwapeza choonadi? Munkaona ngati aliyense avomereza zimene mwayamba kukhulupirirazo. Simunkakayikira kuti uthenga wa m’Baibulo ungawathandize kukhala ndi moyo wosangalala panopa komanso kuyembekezera zinthu zabwino m’tsogolo. (Sal. 119:105) Choncho ndi mtima wonse munayamba kuuza anzanu komanso achibale anu mfundo zomwe munkaphunzira. Koma kodi chinachitika n’chiyani? Muyenera kuti munadabwa kuona kuti ambiri anakana zimene munawauza. Sitiyenera kudabwa anthu ena akamakana uthenga umene timalalikira. Mu nthawi ya Yesu, anthu ambiri anamukana ngakhale kuti ankachita zozizwitsa posonyeza kuti anatumidwa ndi Mulungu. Mwachitsanzo, Yesu anaukitsa Lazaro, chomwe chinali chozizwitsa chimene ngakhale anthu amene ankamutsutsawo sakanachikana. Ngakhale zinali choncho, atsogoleri a Chiyuda sanakhulupirire kuti Yesu ndi Mesiya ndipo anayamba kufuna kumupha limodzi ndi Lazaro.—Yoh. 11:47, 48, 53; 12:9-11. w21.05 2 ¶1-2
Lamlungu, June 4
Tisaleke kusonkhana pamodzi, . . . Koma tiyeni [tizilimbikitsana].—Aheb. 10:25.
Muziyesetsa kuti muzisonkhana nthawi zonse. Mukamachita zimenezi muzilimbikitsidwa ndi mfundo zothandiza komanso mungadziwane ndi abale ndi alongo anu. Muzipeza anzanu mumpingo omwe mungaphunzire zinthu kwa iwo ngakhale mutakhala kuti mukusiyana msinkhu komanso kochokera. Baibulo limatikumbutsa kuti okalamba “amakhala ndi nzeru.” (Yobu 12:12) Achikulire angaphunzirenso zambiri kuchokera kwa achinyamata okhulupirika. Davide anali wamng’ono poyerekezera ndi Yonatani koma zimenezi sizinachititse kuti asakhale mabwenzi. (1 Sam. 18:1) Iwo ankathandizana potumikira Yehova ngakhale kuti ankakumana ndi mavuto aakulu. (1 Sam. 23:16-18) Mlongo wina dzina lake Irina, amene m’banja lawo alipo yekha wa Mboni ananena kuti: “Abale ndi alongo akhoza kukhala ngati makolo athu komanso achibale athu enieni. Yehova akhoza kuwagwiritsa ntchito kuti azitithandiza.” Anzanu amafuna kukulimbikitsani komanso kukuthandizani, koma mumafunika kuti muwafotokozere kuti adziwe mmene angakuthandizireni. w21.06 10-11 ¶9-11
Lolemba, June 5
Mofanana ndi zimenezi, Atate wanga wakumwamba adzathana ndi inu ngati aliyense wa inu sakhululukira m’bale wake ndi mtima wonse.—Mat. 18:35.
Yesu anafotokoza fanizo lonena za mfumu ndi kapolo wake. Mfumuyo inakhululukira kapoloyo ngongole yaikulu imene sakanatha kubweza. Koma kenako kapolo ameneyu sankafuna kukhululukira kapolo mnzake ngongole imene inali yochepa kwambiri. Pamapeto pake mfumuyo inamuika m’ndende kapolo wopanda chifundoyo. Zimene anachita kapoloyo sizinakhudze iye yekha, zinakhudzanso ena. Choyamba iye anachitira nkhanza kapolo mnzake ‘pokam’pereka kundende mpaka pamene adzabweze ngongoleyo.’ Chachiwiri iye anakhumudwitsa akapolo anzake. Iwo “ataona zimene zinachitikazo anamva chisoni kwambiri.” (Mat. 18:30, 31) Mofanana ndi zimenezi, zomwe timachita zimakhudzanso anthu ena. Ngati mnzathu watilakwira ndipo ife sitikufuna kumukhululukira, kodi chingachitike n’chiyani? Choyamba akhoza kukhumudwa chifukwa sitinamusonyeze chifundo komanso chikondi. Chachiwiri, tingakhumudwitsenso ena mumpingo ngati atazindikira kuti sitili pamtendere ndi m’bale wathuyo. w21.06 22 ¶11-12
Lachiwiri, June 6
[Iye] adzawononga amene akuwononga dziko lapansi.—Chiv. 11:18.
Anthu analengedwa m’chifanizo cha Mulungu, koma Satana amasangalala kuwasokoneza kuti azichita zoipa. Pamene Yehova “anaona kuti kuipa kwa anthu kwachuluka” m’nthawi ya Nowa, “anamva chisoni kuti anapanga anthu padziko lapansi, ndipo zinam’pweteka kwambiri mumtima.” (Gen. 6:5, 6, 11) Kodi zinthu zinasintha kuchokera nthawi imeneyo? Ayi ndithu. Satana akusangalala akamaona kuti khalidwe lachiwerewere likufala kwambiri, zomwe zikuphatikizapo kugonana kwamtundu uliwonse kwa anthu osakwatirana komanso kumene kumachitika pakati pa amuna kapena akazi okhaokha. (Aef. 4:18, 19) Ndipotu amasangalala kwambiri akachititsa anthu amene amatumikira Mulungu woona kuti achite tchimo. Motsogoleredwa ndi Satana, kuwonjezera pa kupweteka anthu anzawo powalamulira, anthu sakusamalira dziko ndi nyama zimene Yehova anawapatsa kuti azizisamalira. (Mlal. 8:9; Gen. 1:28) Kodi zotsatirapo zake n’zotani? Akatswiri ena akuchenjeza kuti zimene anthu akuchita zipangitsa kuti mitundu 1 miliyoni ya zomera komanso nyama itheretu padzikoli m’zaka zochepa zikubwerazi. w21.07 12 ¶13-14
Lachitatu, June 7
[Yehova] amakhululuka ndi mtima wonse.—Yes. 55:7.
Atumiki ena a Mulungu amadziimba mlandu kwambiri chifukwa cha zinthu zimene analakwitsa m’mbuyo. Iwo amaona kuti Mulungu sangawakhululukire ngakhale atalapa bwanji. Ngati inunso mukuvutika ndi maganizo oterewa, kudziwa kuti Yehova ndi wofunitsitsa kusonyeza chikondi chokhulupirika kwa atumiki ake kungakuthandizeni kuti muzitumikira Yehova mosangalala ndi chikumbumtima chabwino. Zimenezi n’zotheka chifukwa “magazi a Yesu Mwana wake akutiyeretsa ku uchimo wonse.” (1 Yoh. 1:7) Ngati mwafooka chifukwa cha zinthu zina zimene munalakwitsa, muzikumbukira kuti Yehova ndi wofunitsitsa kukhululukira munthu wochimwa amene walapa. Taonani zimene wolemba salimo Davide ananena zokhudza kugwirizana kumene kulipo pakati pa chikondi chokhulupirika ndi kukhululuka. Iye anati: “Monga mmene kumwamba kulili pamwamba kwambiri kuposa dziko lapansi, kukoma mtima kwake kosatha nakonso ndi kwapamwamba kwa onse omuopa. Monga mmene kum’mawa kwatalikirana ndi kumadzulo, momwemonso, watiikira kutali zolakwa zathu.”—Sal. 103:11, 12. w21.11 5-6 ¶12-13
Lachinayi, June 8
Ana ake amaimirira n’kumuuza kuti ndi wodala. Mwamuna wake amaimirira n’kumutamanda.—Miy. 31:28.
Mwamuna wa Chikhristu ayenera kumalemekeza mkazi wake. (1 Pet. 3:7) Kulemekeza munthu kumaphatikizapo kumuganizira komanso kumupatsa ulemu. Mwachitsanzo, mwamuna angasonyeze kuti amalemekeza mkazi wake akamamuona kuti ndi wofunika kwambiri. Iye samauza mkazi wake kuti achite zimene sangakwanitse ndipo samamuyerekezera ndi akazi ena. Kodi pangakhale mavuto otani ngati mwamuna amayerekezera mkazi wake ndi akazi ena? Mlongo wina dzina lake Rosa yemwe mwamuna wake si wa Mboni, nthawi zambiri amamuyerekezera ndi akazi ena. Mawu onyoza amene mwamuna wake amamulankhula amachititsa Rosa kuti asamamve bwino komanso azikayikira ngati pali anthu ena amene amamukonda. Iye ananena kuti: “Ndimafunika kuti pafupipafupi ena azindikumbutsa kuti Yehova amandikonda.” Mosiyana ndi zimenezi, mwamuna wa Chikhristu amalemekeza mkazi wake. Iye amadziwa kuti zimenezi zingathandize kuti azigwirizana ndi mkazi wake komanso akhale pa ubwenzi wabwino ndi Yehova. Mwamuna amene amalemekeza mkazi wake amalankhula zinthu zabwino zokhudza mkazi wakeyo, kumutsimikizira kuti amamukonda komanso kumuyamikira. w21.07 22 ¶7-8
Lachisanu, June 9
Ndidzayembekezera moleza mtima.—Mika 7:7.
Kodi mumakhumudwa ngati katundu amene mumafunika kulandira sanafike panthawi imene mumayembekezera? Koma kodi simungadikire moleza mtima mutadziwa kuti pali zifukwa zomveka zimene zachititsa kuti katunduyo asafike pa nthawi imene mumayembekezerayo? Pa Miyambo 13:11, pali chitsanzo chosonyeza kufunika kochita zinthu moleza mtima. Lembali limati: “Zinthu zamtengo wapatali zimene zimapezedwa m’njira yachinyengo zimacheperachepera, koma wozisonkhanitsa ndi dzanja lake ndi amene amazichulukitsa.” Kodi mfundo yake ndi yotani pamenepa? Munthu angasonyeze kuti ndi wanzeru ngati amachita zinthu moleza mtima komanso mwapang’onopang’ono. Lemba la Miyambo 4:18 limatiuza kuti: “Njira ya olungama ili ngati kuwala kwamphamvu kumene kumamka kuwonjezereka mpaka tsiku litakhazikika.” Mawuwa amatithandiza kumvetsa kuti Yehova amaulula cholinga chake kwa atumiki ake pang’onopang’ono. Koma mawu a palembali akutithandizanso kumvetsa mmene Mkhristu amasinthira zinthu pa moyo wake n’cholinga choti akhale pa ubwenzi ndi Yehova. Komabe pangatenge nthawi kuti Mkhristu akhale wolimba mwauzimu. w21.08 8 ¶1, 3-4
Loweruka, June 10
Ine ndilipo! Nditumizeni.—Yes. 6:8.
Tili ndi ntchito yambiri yoti tigwire pamene mapeto a dzikoli akuyandikira. (Mat. 24:14; Luka 10:2; 1 Pet. 5:2) Tonsefe timafunitsitsa kutumikira Yehova mmene tingathere. Ambiri akuwonjezera utumiki wawo. Ena amafuna atachita upainiya ndipo enanso amafuna kutumikira pa Beteli kapena kuchita utumiki wa zomangamanga. Komanso abale ambiri akuyesetsa kuti azitumikira monga atumiki othandiza kapena akulu. (1 Tim. 3:1, 8) Yehova amasangalala poona zimene atumiki ake akuyesetsa kuchita pomutumikira. (Sal. 110:3) Kodi ndinu wokhumudwa chifukwa chakuti simukukwaniritsa cholinga chinachake chauzimu? Ngati ndi choncho, muzifotokozera Yehova m’pemphero mmene mukumvera. (Sal. 37:5-7) Komanso muzipempha abale amene ndi olimba mwauzimu kuti akupatseni malangizo amene angakuthandizeni kuti muzichita bwino zinthu potumikira Mulungu, ndipo muziyesetsa kugwiritsa ntchito malangizo amene akupatsaniwo. Mukamachita zimenezi mungathe kupatsidwa utumiki umene mukufuna kapena kukwaniritsa cholinga chanu. w21.08 20 ¶1; 21 ¶4
Lamlungu, June 11
Yehova . . . sadzasiya anthu ake okhulupirika.—Sal. 37:28.
Mneneri wamkazi Anna, yemwenso anali wamasiye anali ndi zaka 84 koma “sanali kusowa pakachisi.” Popeza ankapezeka pakachisi nthawi zonse, iye anapatsidwa mwayi woona Yesu ali wakhanda. (Luka 2:36-38) Masiku ano, pali achikulire ambiri okhulupirika omwe amapereka chitsanzo chabwino kwa achinyamata. Tingapindule kwambiri ngati titawachititsa kuti akhale omasuka, n’kumamvetsera akamatifotokozera zinthu zosangalatsa zimene akumana nazo m’gulu la Yehova. Abale ndi alongo athu achikulire ndi ofunika kwambiri kwa Yehova komanso gulu lake. Iwo aona mmene Yehova wawadalitsira komanso mmene wakhala akudalitsira gulu lake m’njira zosiyanasiyana. Aphunziranso mfundo zofunika kuchokera pa zinthu zimene akhala akulakwitsa. Muziona kuti iwo ndi “chitsime cha nzeru” ndipo muziphunzirapo kanthu pa zimene zakhala zikuwachitikira. (Miy. 18:4) Mukamapeza nthawi yocheza nawo, mukhoza kulimbitsa chikhulupiriro chanu. w21.09 3 ¶4; 4 ¶7-8; 5 ¶11, 13
Lolemba, June 12
Wamng’ono adzasanduka anthu 1,000, ndipo wochepa adzasanduka mtundu wamphamvu.—Yes. 60:22.
Monga mmene Yesaya ananenera, anthu a Yehova akuyamwa “mkaka wa mitundu ya anthu.” (Yes. 60:5, 16) Popeza amuna komanso akazi amtengo wapataliwa amalowa m’gululi ali ndi maluso osiyanasiyana, tikulalikira uthenga wabwino m’mayiko okwana 240 komanso tikusindikiza mabuku athu m’zinenero zoposa 1,000. M’masiku a mapeto ano, ntchito yogwedeza mitundu ya anthu ikuwachititsa kuti asankhe zochita. Kodi iwo asankha kukhala kumbali ya Ufumu wa Mulungu, kapena azidalira maboma a anthu? Imeneyi ndi nkhani imene aliyense ayenera kusankha. Ngakhale kuti anthu a Yehova amamvera malamulo a boma la m’dziko limene akukhala, iwo salowerera ngakhale pang’ono ndale za m’dzikoli. (Aroma 13:1-7) Amadziwa kuti Ufumu wa Mulungu wokha ndi umene udzathetse mavuto onse a anthu. Ufumu umenewu suli mbali ya dzikoli.—Yoh. 18:36, 37. w21.09 17-18 ¶13-14
Lachiwiri, June 13
Mukhuthulireni za mumtima mwanu.—Sal. 62:8.
Munthu wina yemwe mumamukonda akasiya kutumikira Yehova, n’zofunika kwambiri kuti muzipitiriza kulimbitsa chikhulupiriro chanu komanso cha anthu ena m’banja lanu. Kodi mungachite bwanji zimenezi? Yehova angakupatseni mphamvu mukamawerenga Mawu ake nthawi zonse, kuwaganizira mozama komanso kupezeka pamisonkhano. Joanna, yemwe bambo ake komanso mchemwali wake anasiya choonadi, ananena kuti: “Mtima wanga umakhala m’malo ndikamawerenga za anthu otchulidwa m’Baibulo monga Abigayeli, Esitere, Yobu, Yosefe ndi Yesu. Zitsanzo za anthu amenewa zimanditsitsimula moti ndimayamba kuganiza bwino.” Mukakhala ndi nkhawa musamasiye kupemphera kwa Yehova. Muzipempha Mulungu wathu wachikondi kuti akuthandizeni kuona zinthu mmene iyeyo amazionera ndiponso ‘akupatseni nzeru ndi kukulangizani njira yoti muyendemo.’ (Sal. 32:6-8) N’zoona kuti nthawi zina zingakhale zovuta kuti mufotokozere Yehova mmene mukumveradi. Koma Yehova amamvetsa bwino mmene mukumvera mumtima. Iye akukulimbikitsani kuti muzimukhuthulira za mumtima mwanu.—Eks. 34:6; Sal. 62:7. w21.09 28 ¶9-10
Lachitatu, June 14
Uyu ndiye Mwana wanga wokondedwa, amene ndikukondwera naye, muzimumvera.—Mat. 17:5.
Pambuyo pa pasika wa mu 32 C.E., mtumwi Petulo, Yakobo ndi Yohane, anaona masomphenya ochititsa chidwi. Iwo anali paphiri, mwina mbali ina ya phiri la Herimoni pomwe Yesu anasandulika pamaso pawo. “Nkhope yake inawala ngati dzuwa. Malaya ake akunja anawala kwambiri.” (Mat. 17:1-4) Atumwiwo anamva Mulungu akunena kuti: “Uyu ndiye Mwana wanga wokondedwa, amene ndikukondwera naye, muzimumvera.” Zimene atumwiwa anachita pa moyo wawo zimasonyeza kuti ankamvera Yesu. Choncho timafunitsitsa kutengera chitsanzo chawo. Ndife osangalala kuti Yehova amatipatsa malangizo achikondi kudzera mwa Yesu Khristu yemwe ndi “mutu wampingo.” (Aef. 5:23) Mofanana ndi mtumwi Petulo, Yakobo ndi Yohane, tiyeni tikhale otsimikiza kuti ‘tizimumvera.’ Tikamachita zimenezi, tingapeze madalitso ambiri panopa komanso chimwemwe chosatha m’tsogolo. w21.12 22 ¶1; 27 ¶19
Lachinayi, June 15
Ndidzakuwongolera pa mlingo woyenera.—Yer. 30:11.
Mkhristu wina mumpingo wa ku Korinto ankachita zachiwerewere ndi mkazi wa bambo ake. Mtumwi Paulo anauza Akhristu a ku Korintoko kuti amuchotse mumpingo. Khalidwe loipa la munthuyo linkasokoneza anthu ena mumpingo moti anthu enanso sankaona kuti limeneli ndi tchimo lalikulu. (1 Akor. 5:1, 2, 13 ) Patapita nthawi, Paulo anamva zoti wochimwayo anali atalapa kuchokera pansi pa mtima. Ndiye anauza akulu kuti: “Mukhululukireni ndi mtima wonse ndi kumutonthoza.” Ndipo anapereka chifukwa chimene anawauzira zimenezi ponena kuti: “Kuopera kuti mwina wotereyu angamezedwe ndi chisoni chake chopitirira malire.” Paulo anamvera chisoni munthu amene analapayo. Iye sankafuna kuona munthuyo akuvutika kwambiri mumtima chifukwa cha zoipa zimene anachita mpaka kumaona kuti sangakhululukidwenso. (2 Akor. 2:5-8, 11) Mofanana ndi Yehova, akulu amakonda kuchitira ena chifundo. Iwo amapereka chilango chokhwima ngati pakufunika kutero koma amasonyezanso chifundo ngati n’zotheka ndiponso pakakhala zifukwa zomveka zochitira zimenezo. Koma ngati akulu atangomusiya munthu wochimwa osamupatsa chilango chilichonse, sichingakhale chifundo koma kulekerera zinthu. w21.10 11-12 ¶12-15
Lachisanu, June 16
Usabwezere choipa kapena kusunga chakukhosi.—Lev. 19:18.
Kukhumudwa tingakuyerekezere ndi bala. Mabala ena amakhala aang’ono, pomwe ena amakhala aakulu. Mwachitsanzo, potsegula envelopu, mwina pepala lingaticheke pachala. Tingamve kupweteka, koma pambuyo pa tsiku limodzi kapena awiri, sitingakumbukire pamene tinachekeka paja. Mofanana ndi zimenezi, zina mwa zimene ena atilakwira zingakhale zazing’ono. Mwachitsanzo, mnzathu angalankhule kapena kuchita zinthu mosaganizira ndipo zingatikhumudwitse. Komabe timamukhululukira mosavuta. Ngati tili ndi bala lalikulu, dokotala angafunike kulisoka kapenanso kulimanga ndi bandeji. Koma ngati tingamagwiregwire pabalapo, zingachititse kuti lisapole msanga. N’zomvetsa chisoni kuti nthawi zina munthu akakhumudwa kwambiri ndi zimene ena amuchitira, angamachite zofanana ndi zimenezi. Nthawi ndi nthawi angamaganizire zinthu zoipa zimene munthu wina anamuchitira komanso mmene anakhumudwira. Komatu anthu amene amasunga chakukhosi, amangodzivulaza okha. Choncho ndi bwino kutsatira malangizo a mulemba lalerowa. w21.12 12 ¶15
Loweruka, June 17
N’chifukwa chiyani umaweruza m’bale wako?—Aroma 14:10.
Tiyerekeze kuti mkulu akudera nkhawa ndi zimene Mkhristu wina amasankha pa nkhani ya kuvala ndi kudzikongoletsa. Mkuluyo angadzifunse kuti, ‘Kodi pali mfundo iliyonse ya m’Malemba imene ingandichititse kulankhulapo?’ Pofuna kupewa kulankhula za m’maganizo mwake, iye angafunse maganizo kwa mkulu wina kapena Mkhristu wolimba mwauzimu. Kenako angafufuzire limodzi malangizo a Paulo okhudza zovala ndi kudzikongoletsa. (1 Tim. 2:9, 10) Paulo anafotokoza mfundo zina zikuluzikulu zosonyeza kuti Mkhristu ayenera kuvala moyenera, mwaulemu komanso moganiza bwino. Koma sanatchule zimene munthu ayenera kuvala ndi zimene sayenera kuvala. Iye ankazindikira kuti Mkhristu aliyense payekha ali ndi ufulu wosankha zinthu zimene amakonda zomwe sizisemphana ndi mfundo za m’Malemba. Choncho akulu angachite bwino kuona ngati zimene munthu wasankha zikusonyeza kuti akuchita zinthu mwaulemu komanso moganiza bwino. Tingachite bwino kumakumbukira kuti Akhristu awiri olimba mwauzimu angasankhe zinthu ziwiri zosiyana koma zonsezo n’kukhala zovomerezeka. Sitiyenera kukakamiza Akhristu anzathu kuti azichita zimene ifeyo tikuona kuti n’zolondola. w22.02 16 ¶9-10
Lamlungu, June 18
Muzisonyezana kukoma mtima kosatha [chikondi chokhulupirika] ndi chifundo.—Zek. 7:9.
Tili ndi zifukwa zomveka zotichititsa kuti tizisonyezana chikondi chokhulupirika. Kodi zina mwa zifukwazi ndi ziti? Taonani mmene miyambi ya m’Baibulo yotsatirayi ikuyankhira funsoli: “Usasiye kukoma mtima kosatha ndi choonadi. . . . Ukachita zimenezi, Mulungu ndi anthu adzakukomera mtima ndipo adzakuona kuti ndiwe wozindikira.” “Munthu wosonyeza kukoma mtima kosatha amapindulitsa moyo wake.” “Amene akufunafuna chilungamo ndiponso kukoma mtima kosatha adzapeza moyo.” (Miy. 3:3, 4; 11:17; 21:21) Miyambiyi ikutchula zifukwa zitatu zotichititsa kuti tizisonyeza chikondi chokhulupirika. Choyamba, kusonyeza chikondi chokhulupirika kumatichititsa kukhala amtengo wapatali kwa Mulungu. Chachiwiri, zinthu zimatiyendera bwino tikamasonyeza chikondi chokhulupirika. Mwachitsanzo, timagwirizana kwambiri ndi anzathu. Ndipo chachitatu, tidzapeza madalitso m’tsogolo kuphatikizapo moyo wosatha. Choncho tili ndi zifukwa zomveka zotichititsa kutsatira malangizo a Yehova akuti: “Muzisonyezana kukoma mtima kosatha ndi chifundo.” w21.11 8 ¶1-2
Lolemba, June 19
Tiwonjezereni chikhulupiriro.—Luka 17:5.
Ngati mayesero omwe mwakumana nawo m’mbuyomu kapena panopa akusonyeza kuti chikhulupiriro chanu si cholimba kwenikweni, musataye mtima. Muziona kuti umenewo ndi mwayi woti mulimbitse chikhulupirirocho. Muzipemphera kwa Yehova mochokera pansi pa mtima, makamaka mukakumana ndi vuto lalikulu. Muzikumbukira kuti Yehova angakuthandizeni pogwiritsa ntchito achibale komanso anzanu. Mukamalola kuti Yehova akuthandizeni kupirira mayesero amene mukukumana nawo panopa, mungakhale otsimikiza kuti adzakuthandizaninso kupirira mayesero amene mungadzakumane nawo m’tsogolo. Yesu anathandiza ophunzira ake kuzindikira mbali zimene ankafunika kuwonjezera chikhulupiriro chawo koma sankakayikira kuti Yehova adzawathandiza kupirira mayesero alionse omwe angadzakumane nawo m’tsogolo. (Yoh. 14:1; 16:33) Iye ankakhulupirira kuti khamu lalikulu lidzapulumuka chisautso chachikulu chifukwa cha chikhulupiriro. (Chiv. 7:9, 14) Inuyo mudzakhala m’gulu la anthu opulumuka ngati panopa mumagwiritsa ntchito mpata uliwonse womwe wapezeka kuti mulimbitse chikhulupiriro chanu.—Aheb. 10:39. w21.11 25 ¶18-19
Lachiwiri, June 20
Mngelo wa Yehova amamanga msasa mozungulira onse oopa Mulungu.—Sal. 34:7.
Masiku ano sitiyembekezera kuti Yehova azititeteza modabwitsa. Koma tikudziwa kuti onse amene amadalira Yehova, ngakhale panopa atamwalira, adzalandira moyo wosatha. Posachedwapa m’tsogolomu tidzayesedwa ngati timakhulupirira kuti Yehova angatiteteze. Pamene Gogi wa ku Magogi, amene ndi mgwirizano wa mayiko, azidzaukira anthu a Mulungu, miyoyo yathu idzaoneka ngati ili pangozi. Tidzafunika kukhulupirira kuti Yehova angathe kutipulumutsa ndipo atipulumutsadi. Mitundu ya anthu izidzationa ngati nkhosa zosatetezeka. (Ezek. 38:10-12) Tidzakhala opanda zida komanso osadziwa nkhondo. Mayiko azidzaona kuti n’zosavuta kutigonjetsa. Iwo sadzadziwa kuti angelo a Mulungu atizungulira kuti atiteteze koma ife tidzadziwa zimenezi chifukwa cha chikhulupiriro. Mayiko amenewa sadzadziwa chifukwa sakhulupirira Mulungu. Iwotu adzadabwa kwambiri kuona magulu a angelo akumenya nkhondo kuti atipulumutse.—Chiv. 19:11, 14, 15. w22.01 6 ¶12-13
Lachitatu, June 21
Kondani gulu lonse la abale.—1 Pet. 2:17.
Abale ndi alongo athu onse ndi ofunika kwa Yehova choncho ayenera kukhalanso ofunika kwa ife. Timafunika ‘kukonda gulu lonse la abale,’ osati ochepa okha. Tiyenera kukhala ofunitsitsa kuchita chilichonse chomwe tingathe kuti tiziwateteza komanso kuwasamalira. Ngati tazindikira kuti takhumudwitsa winawake sitiyenera kuzisiya n’kumaona kuti munthuyo akukokomeza zinthu moti akungofunika kutikhululukira. Koma kodi anthu ena amakhumudwa chifukwa chiyani? Abale ndi alongo ena amadziona kuti ndi osafunika mwina chifukwa cha mmene anakulira. Enanso angoyamba kumene choonadi ndipo sanaphunzire mmene angachitire zinthu akalakwiridwa. Kaya zinthu zili bwanji, tizichita zimene tingathe kuti tikhalenso pamtendere ndi ena. Kuwonjezera pamenepa munthu amene amakonda kukhumudwa ndi zochita za ena, ayenera kuzindikira kuti limeneli si khalidwe labwino ndipo afunika kusintha. Kuchita izi kungawathandize kukhala ndi mtendere wamumtima komanso angamagwirizane ndi ena. w21.06 21 ¶7
Lachinayi, June 22
Yehova ali pafupi ndi onse oitanira pa iye. Iye ali pafupi ndi onse amene amamuitana m’choonadi.—Sal. 145:18.
Yesu amamvetsa mmene timamvera. Tikapanikizika ndi nkhawa, timayamikira mnzathu amene amatimvetsa akatitonthoza, makamaka ngati mnzathuyo anakumanapo ndi mavuto ngati amene ifenso takumana nawo. Yesu ndi mnzathu ameneyu. Iye amadziwa mmene zimakhalira ukafooka komanso ukamafuna kuti ena akuthandize. Amadziwa zofooka zathu ndipo adzaonetsetsa kuti tathandizidwa “pa nthawi imene tikufunika thandizo.” (Aheb. 4:15, 16) Mofanana ndi Yesu yemwe anavomera kuthandizidwa ndi mngelo m’munda wa Getsemane, ifenso tiyenera kukhala okonzeka kulandira thandizo lomwe Yehova angatipatse kudzera m’mabuku athu, mavidiyo, nkhani kapenanso kudzera mwa mkulu, m’bale kapena mlongo yemwe wabwera kudzatilimbikitsa. (Luka 22:39-44) Yehova adzatipatsa “mtendere” wake komanso kutilimbikitsa. Tikamapemphera, iye amatipatsa “mtendere [wake] umene umaposa kuganiza mozama kulikonse.”—Afil. 4:6, 7. w22.01 18-19 ¶17-19
Lachisanu, June 23
Anali kuwapatsa . . . malamulo oyenera kuwatsatira, malinga ndi zimene atumwi . . . anagamula.—Mac. 16:4.
Nthawi zonse zimene Yehova amachita zimakhala zoyenera. Komabe mwina tingamavutike kukhulupirira anthu amene iye akuwagwiritsa ntchito. Tingamakayikire ngati anthu amene ali ndi udindo m’gulu la Yehova akuchita zinthu mogwirizana ndi malangizo a Yehovayo kapena maganizo awo. Mfundo yosatsutsika ndi yakuti sitinganene kuti timakhulupirira Yehova pamene sitikhulupirira anthu omwe iye amawakhulupirira ndipo amawagwiritsa ntchito. Masiku ano Yehova amatsogolera mbali yapadziko lapansi ya gulu lake pogwiritsa ntchito “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru.” (Mat. 24:45) Mofanana ndi bungwe lolamulira la m’nthawi ya atumwi, kapoloyu amatsogolera anthu a Mulungu padziko lonse ndipo amapereka malangizo kwa akulu. Akulu nawonso amagwiritsa ntchito malangizowo m’mipingo. Timasonyeza kuti timakhulupirira mmene Yehova amachitira zinthu potsatira malangizo ochokera kugulu lake komanso kwa akulu. w22.02 4 ¶7-8
Loweruka, June 24
Tisaleke kuchita zabwino.—Agal. 6:9.
Timasangalala komanso timaona kuti ndi mwayi waukulu kukhala a Mboni za Yehova. Timasangalala tikathandiza munthu ‘amene ali ndi maganizo abwino omwe angamuthandize kukapeza moyo wosatha’ kuti akhale wokhulupirira. (Mac. 13:48) Timamva ngati mmene Yesu anamvera pamene “anakondwera kwambiri mwa mzimu woyera,” ophunzira ake atamufotokozera zinthu zosangalatsa zimene anakumana nazo polalikira. (Luka 10:1, 17, 21) Mtumwi Paulo analimbikitsa Timoteyo kuti: “Nthawi zonse uzisamala ndi zimene umachita komanso zimene umaphunzitsa.” Anawonjezeranso kuti: “Ukatero udzadzipulumutsa wekha komanso anthu okumvera.” (1 Tim. 4:16) Choncho ntchito yolalikira imapulumutsa miyoyo ya anthu. Timasamala ndi zimene timachita chifukwa ndife nzika za Ufumu wa Mulungu. Nthawi zonse timafuna kuchita zinthu m’njira imene imachititsa kuti Yehova alemekezedwe komanso mogwirizana ndi uthenga wabwino umene timalalikira. (Afil. 1:27) Timasonyeza kuti ‘timasamala ndi zimene timaphunzitsa’ tikamakonzekera bwino komanso tikamapempha Yehova kuti atithandize pamene tikukalalikira. w21.10 24 ¶1-2
Lamlungu, June 25
Muvale umunthu watsopano.—Akol. 3:10.
“Umunthu watsopano” umatanthauza kuganiza komanso kuchita zinthu motsanzira Yehova. Munthu amavala umunthu watsopano akamasonyeza makhalidwe amene mzimu woyera umatulutsa ndipo amalola kuti mzimuwo uzimutsogolera pa mmene amaganizira, mmene amamvera komanso zochita zake. Mwachitsanzo, iye amakonda Yehova komanso anthu ake. (Mat. 22:36-39) Amapitirizabe kukhala wosangalala ngakhale pamene akukumana ndi mayesero. (Yak. 1:2-4) Amakhala mwamtendere ndi ena. (Mat. 5:9) Amakhala woleza mtima komanso wokoma mtima akamachita zinthu ndi ena. (Akol. 3:13) Iye amakonda komanso kuchita zabwino. (Luka 6:35) Zochita zake zimasonyeza kuti amakhulupirira kwambiri Atate wake wakumwamba. (Yak. 2:18) Amakhalabe wofatsa anthu ena akamuputa komanso amakhala wodziletsa akakumana ndi mayesero. (1 Akor. 9:25, 27; Tito 3:2) Kuti tivale umunthu watsopano, tiyenera kukhala ndi makhalidwe otchulidwa pa Agalatiya 5:22, 23 komanso m’mavesi ena a m’Baibulo. w22.03 8-9 ¶3-4
Lolemba, June 26
Muzitsanzira ine.—1 Akor. 11:1.
Akulu angatsanzire mtumwi Paulo, osati pongolalikira kunyumba ndi nyumba, koma pokhala okonzeka kulalikiranso pa mpata uliwonse. (Aef. 6:14, 15) Mofanana ndi Paulo, akulu angagwiritse ntchito nthawi yomwe alowa mu utumiki pophunzitsa ena kuphatikizapo atumiki othandiza. (1 Pet. 5:1, 2) Komabe akulu ayenera kupewa kumatanganidwa kwambiri ndi utumiki womwe akuchita mpaka kufika pomasowa nthawi yolalikira. (Mat. 28:19, 20) Kuti azigawa bwino nthawi yawo, nthawi zina angafunike kukana kuchita mautumiki ena. Pambuyo poganizira komanso kupempherera utumiki womwe apatsidwawo, angazindikire kuti ngati atavomera utumikiwo sangakwanitse kusamalira zinthu zina zofunika kwambiri monga kuchita kulambira kwa pabanja, kugwira nawo mokwanira ntchito yolalikira komanso kuphunzitsa ana awo kulalikira. Iwo ayenera kukhala otsimikiza kuti Yehova amamvetsa kuti akufuna kugawa bwino nthawi yawo. w22.03 27 ¶4, 7; 28 ¶8
Lachiwiri, June 27
Musachite mantha ndi amene amapha thupi koma sangaphe moyo.—Mat. 10:28.
Kodi mumakumbukira nthawi imene munkachita mantha kuti mukhale wa Mboni za Yehova? Mwina munkaona kuti simungakwanitse kumagwira ntchito yolalikira. Mwinanso munkaopa kuti achibale komanso anzanu azikutsutsani. Ngati ndi choncho, ndiye kuti mungamvetse mmene wophunzira wanu angamvere. Yesu anavomereza kuti n’zotheka kuti munthu aziopa zimenezi. Komabe iye analimbikitsa otsatira ake kuti asamalole kuti mantha awalepheretse kutumikira Yehova. (Mat. 10:16, 17, 27) Nthawi zonse muziphunzitsa wophunzira wanu mmene angafotokozere kwa ena zimene amakhulupirira. Ophunzira a Yesu ayenera kuti ankachita mantha iye atawatumiza kuti akalalikire. Koma Yesu anawathandiza powauza uthenga komanso malo oti akalalikire. (Mat. 10:5-7) Ndiye kodi tingamutsanzire bwanji Yesu? Tizithandiza wophunzira wathu kudziwa anthu amene angawalalikire. Mwachitsanzo, mungamufunse ngati akudziwa munthu wina amene mfundo inayake ya m’Baibulo ingamuthandize. Kenako mungamuthandize kukonzekera komanso kumusonyeza mmene angafotokozere zimenezo mosavuta. w21.06 6 ¶15-16
Lachitatu, June 28
Ndigwedeza mitundu yonse ya anthu, ndipo zinthu zamtengo wapatali zochokera ku mitundu yonse ya anthu zidzalowa m’nyumba imeneyi.—Hag. 2:7.
“M’maminitsi ochepa, mashopu komanso nyumba zakale zinayamba kugwa.” “Aliyense ankachita mantha . . . Anthu ambiri amanena kuti kugwedezako kunachitika pafupifupi kwa 2 minitsi. Koma kwa ine ndinkangoona ngati kunachitika nthawi yaitali.” Zimenezi ndi zomwe ananena anthu ena omwe anapulumuka chivomerezi chomwe chinachitika ku Nepal mu 2015. Koma panopa tikukhala pa nthawi imene pakuchitika kugwedeza kwina kumene kukukhudza mitundu yonse ya anthu. Mneneri Hagai ananeneratu za kugwedeza kumeneku polemba kuti: “Yehova wa makamu wanena kuti, ‘Posachedwapa ndigwedezanso kumwamba [ndi] dziko lapansi.’” (Hag. 2:6) Kugwedeza kumene Hagai anakufotokoza n’kosiyana ndi kugwedeza kwa chivomerezi komwe kumangokhala kowononga. M’malomwake, kugwedeza uku kumakhala ndi zotsatirapo zabwino. Yehova amatiuza kuti: “Ndigwedeza mitundu yonse ya anthu, ndipo zinthu zamtengo wapatali zochokera ku mitundu yonse ya anthu zidzalowa m’nyumba imeneyi. Ine ndidzadzaza nyumbayi ndi ulemerero.” w21.09 14 ¶1-3
Lachinayi, June 29
Inu mwakhalabe ndi ine m’mayesero anga.—Luka 22:28.
Kuti anthu azigwirizana kwambiri amafunika azilankhulana nthawi zonse komanso momasuka. Zimenezi ndi zofanananso kwambiri ndi ubwenzi wathu ndi Yehova. Tikamamufotokozera m’pemphero mmene tikumvera, maganizo athu komanso zimene zikutidetsa nkhawa, timasonyeza kuti timamudalira ndipo timadziwa kuti amatikonda. (Sal. 94:17-19; 1 Yoh. 5:14, 15) Muzicheza ndi atumiki okhulupirika a Yehova chifukwa iwo ndi mphatso yochokera kwa iye. (Yak. 1:17) Atate wathu wakumwamba amasonyeza kuti amatiganizira potipatsa abale ndi alongo mumpingo omwe ‘amatikonda nthawi zonse.’ (Miy. 17:17) M’kalata imene analembera Akolose, mtumwi Paulo anatchula za Akhristu ena omwe ‘anamuthandiza ndi kumulimbikitsa.’ (Akol. 4:10, 11) Ngakhalenso Khristu Yesu ankafunikira kuti ena amuthandize, ndipo anayamikira kwambiri anzake omwe anamuthandiza kuphatikizapo angelo. (Luka 22:43) Kuuzako mnzathu wolimba mwauzimu zinthu zomwe zikutidetsa nkhawa sikusonyeza kuti ndife ofooka, koma kungatiteteze. w21.04 24-25 ¶14-16
Lachisanu, June 30
[Chikondi] chimakwirira zinthu zonse, chimakhulupirira zinthu zonse, chimayembekezera zinthu zonse, chimapirira zinthu zonse.—1 Akor. 13:7.
Kodi muyenera kuchita chiyani ngati Mkhristu mnzanu wachita zinthu zimene zakukhumudwitsani kwambiri? Muzichita zonse zimene mungathe kuti mukhale nayenso pamtendere. Muzimuuza Yehova m’pemphero mmene mukumvera. Muzimupempha kuti adalitse munthu amene wakukhumudwitsaniyo komanso akuthandizeni kuona makhalidwe abwino amene munthuyo ali nawo omwe amachititsa Yehova kumukonda. (Luka 6:28) Ngati simungathe kunyalanyaza zimene m’bale wanu wakuchitirani, muziganizira njira yabwino yoti mulankhule naye. (Mat. 5:23, 24) Nthawi zonse ndi bwino kumaganiza kuti m’bale wathuyo sanachite kufuna kuti atikhumudwitse. Mukamakambirana naye muzimuthandiza kuona kuti mukumvetsa kuti sanali ndi zolinga zolakwika. Nanga bwanji ngati sakufuna kuti mukambirane? Baibulo limati “pitirizani kulolerana,” choncho musasiye kumulezera mtima m’bale wanuyo. (Akol. 3:13) Koma chofunika kwambiri n’chakuti musamusungire chakukhosi chifukwa zimenezi zingasokoneze ubwenzi wanu ndi Yehova. Musalole kuti zochita za ena zikukhumudwitseni. Mukamachita zimenezi mudzasonyeza kuti mumakonda kwambiri Yehova kuposa china chilichonse.—Sal. 119:165. w21.06 23 ¶15