Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • es23 tsamba 67-77
  • July

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • July
  • Kuphunzira Malemba Tsiku ndi Tsiku—2023
  • Timitu
  • Loweruka, July 1
  • Lamlungu, July 2
  • Lolemba, July 3
  • Lachiwiri, July 4
  • Lachitatu, July 5
  • Lachinayi, July 6
  • Lachisanu, July 7
  • Loweruka, July 8
  • Lamlungu, July 9
  • Lolemba, July 10
  • Lachiwiri, July 11
  • Lachitatu, July 12
  • Lachinayi, July 13
  • Lachisanu, July 14
  • Loweruka, July 15
  • Lamlungu, July 16
  • Lolemba, July 17
  • Lachiwiri, July 18
  • Lachitatu, July 19
  • Lachinayi, July 20
  • Lachisanu, July 21
  • Loweruka, July 22
  • Lamlungu, July 23
  • Lolemba, July 24
  • Lachiwiri, July 25
  • Lachitatu, July 26
  • Lachinayi, July 27
  • Lachisanu, July 28
  • Loweruka, July 29
  • Lamlungu, July 30
  • Lolemba, July 31
Kuphunzira Malemba Tsiku ndi Tsiku—2023
es23 tsamba 67-77

July

Loweruka, July 1

Pambuyo pake, kwa anthu amene aphunzirapo kanthu pa [chilango], chimabala chipatso chamtendere, chomwe ndi chilungamo.​—Aheb. 12:11.

Yehova ndi amene anakonza zoti anthu osalapa azichotsedwa mumpingo. Chilangochi chimathandiza anthu onse kuphatikizapo wolakwayo. Anthu ena mumpingo angamanene kuti sanaweruze bwino kuti munthu achotsedwe. Koma kumbukirani kuti anthu amene amanena zimenezi amakhala kuti sankafuna kuulula zinthu zoipa zimene munthu wolakwayo ankachita. Nthawi zambiri sitidziwa zonse zomwe zachitika. Choncho ndi nzeru kukhulupirira kuti akulu omwe anaweruza nkhaniyo anachita zonse zomwe angathe potsatira mfundo za m’Malemba komanso ‘kuweruzira Yehova.’ (2 Mbiri 19:6) Mukamagwirizana ndi zimene akulu asankha zoti wachibale wanu achotsedwe, mukhoza kumuthandiza kuti abwerere kwa Yehova. Elizabeth anavomereza kuti: “Zinali zovuta kwambiri kuti tisamalankhulane ndi mwana wathu wamkulu. Koma iye atabwerera kwa Yehova, anavomereza kuti ankafunikadi kuchotsedwa. Pamapeto pake iye ananena kuti amayamikira chifukwa cha zinthu zambiri zimene anaphunzirapo.” w21.09 28-29 ¶11-12

Lamlungu, July 2

Anaona mkazi wina wamasiye wosauka akuponya timakobidi tiwiri tating’ono mmenemo.​—Luka 21:2.

Taganizirani za mkazi wamasiyeyu. Mosakayikira iye ankafunitsitsa atapereka zambiri kwa Yehova. Komabe, iye anachita zonse zomwe angathe popereka kwa Yehova zinthu zabwino kwambiri. Ndipo Yesu ankadziwa kuti zimene mayiyu anapereka zinali zamtengo wapatali kwambiri kwa Yehova. Pamenepatu pali phunziro labwino kwambiri kwa ife. Yehova amayamikira tikamamupatsa zinthu zabwino kwambiri kapena kuti tikamamutumikira ndi mtima wonse. (Mat. 22:37; Akol. 3:23) Iye amasangalala akaona kuti tikuchita zonse zomwe tingathe. Zimenezi zikusonyeza kuti Yehova amayamikira kwambiri tikamagwiritsa ntchito nthawi ndi mphamvu zathu pomulambira, kaya mu utumiki kapena pamisonkhano. Kodi tingagwiritse ntchito bwanji mfundo zimene taphunzira pa nkhani ya mayi wamasiye? Tayesani kuganizira za winawake amene angafunike kumutsimikizira kuti Yehova amasangalala ndi zimene akuchita pomutumikira. Angakhale mlongo wachikulire amene mumamudziwa, yemwe amadziimba mlandu kapena kudziona kuti ndi wosafunika chifukwa choti alibenso thanzi labwino komanso mphamvu zotha kuchitira zambiri mu utumiki ngati mmene ankachitira poyamba. w21.04 6 ¶17, 19-20

Lolemba, July 3

Wodala ndi munthu wopirira mayesero, chifukwa akadzavomerezedwa, adzalandira mphoto ya moyo.—Yak. 1:12.

Yehova akudziwa nthawi yabwino imene adzawononge dziko loipali. Kuleza mtima kwake kwathandiza kuti anthu mamiliyoni ambiri omwe ndi akhamu lalikulu asonkhanitsidwe ndipo amamulambira komanso kumutamanda. Anthu onsewa amasangalala kuti iye analeza mtima kwa nthawi yaitali kuti iwo abadwe, aphunzire kumukonda komanso adzipereke kwa iye. Yehova akadzapereka mphoto kwa anthu omwe adzapirire mpaka pamapeto, zidzasonyeza kuti iye anachita bwino kusankha kuti aleze mtima. Ngakhale kuti Satana akuchititsa mavuto ambiri padzikoli, Yehova akupitirizabe kukhala “Mulungu wachimwemwe.” (1 Tim. 1:11) Nafenso tikhoza kumasangalala pamene tikuyembekezera moleza mtima kuti Yehova ayeretse dzina lake, asonyeze kuti ndi woyenera kulamulira komanso athetse zoipa ndi mavuto onse amene anthu akukumana nawo. Choncho tiyeni titsimikize mtima kuti tizipirira komanso kulimbikitsidwa podziwa kuti Atate wathu wakumwamba nawonso akupirira. w21.07 13 ¶18-19

Lachiwiri, July 4

Kodi mu Nazareti mungatuluke kanthu kabwino?​—Yoh. 1:46.

Anthu ambiri mu nthawi ya atumwi sanakhulupirire Yesu. Iwo ankangomuona kuti anali mwana wa kalipentala wosauka. Ndiponso Yesu anali wochokera ku Nazareti, mzinda umene n’kutheka kuti anthu ambiri ankauona kuti ndi wosafunika. Ngakhalenso Natanayeli, yemwe anadzakhala wophunzira wa Yesu, poyamba anati: “Kodi mu Nazareti mungatuluke kanthu kabwino?” Mwina iye ankaganizira ulosi wopezeka pa Mika 5:2, umene unaneneratu kuti Mesiya adzabadwira ku Betelehemu, osati ku Nazareti. Mneneri Yesaya ananeneratu kuti adani a Yesu sadzaganizira “tsatanetsane wa mibadwo ya makolo ake [a Mesiya].” (Yes. 53:8) Anthu amenewa akanafufuza mokwanira, akanadziwa kuti Yesu anabadwira ku Betelehemu, komanso anali wochokera mumzere wa Mfumu Davide. (Luka 2:4-7) Choncho malo omwe Yesu anabadwira ndi amene ananenedweratu mu ulosi wa pa Mika 5:2. Ndiyeno kodi vuto linali pati? Anthuwo ankangofulumira kumuweruza. Popeza kuti sankadziwa zinthu zonse, anakana kukhulupirira Yesu. w21.05 2-3 ¶4-6

Lachitatu, July 5

Wolungama . . . akandidzudzula ndiye kuti wandidzoza mafuta pamutu panga.​—Sal. 141:5.

M’Baibulo muli zitsanzo zabwino za anthu amene anadalitsidwa chifukwa chomvera malangizo. Taganizirani za Yobu. Ngakhale kuti anali woopa Mulungu sanali wangwiro. Chifukwa chopanikizika iye analankhula zinthu zina zolakwika. Choncho analandira malangizo osapita m’mbali kuchokera kwa Elihu komanso Yehova. Kodi Yobu anatani? Iye anati: “Ndinalankhula, koma sindinali kuzindikira . . . ndikubweza mawu anga, ndipo ndikulapa m’fumbi ndi m’phulusa.” (Yobu 42:3-6, 12-17) Iye anasonyeza kuti analidi wodzichepetsa povomera malangizo amene Elihu anamupatsa, ngakhale kuti Elihuyo anali wamng’ono kwa iye. (Yobu 32:6, 7) Kudzichepetsa kudzatithandiza kuti tigwiritse ntchito malangizo amene tapatsidwa ngakhale pamene tikuona kuti sitimayenera kupatsidwa malangizowo, kapenanso ngati amene watipatsa malangizoyo ndi wamng’ono kwa ife. Ndi ndani wa ife amene safuna kupita patsogolo pokulitsa makhalidwe amene mzimu woyera umatulutsa kapenanso pa ntchito yathu yolalikira? w22.02 11 ¶8; 12 ¶12

Lachinayi, July 6

Mwakutero, onse adzadziwa kuti ndinu ophunzira anga, ngati mukukondana.​—Yoh. 13:35.

Abale ndi alongo onse ali ndi udindo woonetsetsa kuti mumpingo muli mtendere komanso kuti aliyense aziona kuti amakondedwa. Zimene timachita komanso kulankhula zingalimbikitse kwambiri ena. Kodi mungathandize bwanji Akhristu amene achibale awo si a Mboni kuti aziona kuti abale ndi alongo mumpingo amawakonda? Muziyamba ndinu kukhala anzawo. Tingayambe ndi kulandira ndi manja awiri atsopano omwe abwera mumpingo. (Aroma 15:7) Komabe timafunikanso kuchita zina osati kungowapatsa moni mwansangala. Timafuna kuti pakapita nthawi akhale anzathu apamtima. Choncho tizichita nawo zinthu mokoma mtima komanso kusonyeza kuti timawaganizira. Popanda kuwafunsa mafunso amene angawachititse manyazi, muziyesetsa kumvetsa mavuto amene akukumana nawo. Ena angamavutike kufotokoza mmene akumvera, choncho muzikhala osamala kuti musamawakakamize kulankhula. M’malomwake muziwafunsa mokoma mtima komanso mwanzeru ndipo muzimvetsera moleza mtima akamayankha. Mwachitsanzo, mukhoza kuwafunsa mmene anaphunzirira choonadi. w21.06 11 ¶13-14

Lachisanu, July 7

Zidzamva mawu anga, ndipo zidzakhala gulu limodzi ndi m’busa mmodzi.​—Yoh. 10:16.

Timaona kuti ndi mwayi wamtengo wapatali kutumikira Yehova mogwirizana monga “gulu” limodzi la nkhosa lotsogoleredwa ndi “m’busa mmodzi.” Buku la Gulu Lochita Chifuniro cha Mulungu pa tsamba 165 limati: “Pamene mukusangalala ndi mgwirizano umenewu, muyenera kukumbukiranso kuti muli ndi udindo wothandiza kuti mgwirizanowu usathe.” Choncho ‘tiziyesetsa kuona abale ndi alongo athu mmene Yehova amawaonera.’ Yehova amationa kuti tonsefe ndife ‘tiana’ tamtengo wapatali. Kodi umu ndi mmene inunso mumaonera abale ndi alongo anu? Yehova amaona komanso amayamikira zonse zimene mumachita powathandiza komanso kuwasamalira. (Mat. 10:42) Timakonda Akhristu anzathu ndipo ndife ‘otsimikiza mtima kuti tisaikire m’bale wathu chokhumudwitsa kapena chopunthwitsa.’ (Aroma 14:13) Timaona abale ndi alongo athu kukhala otiposa ndipo timafunitsitsa kuwakhululukira ndi mtima wonse. Choncho sitiyenera kulola zochita za ena kutikhumudwitsa. M’malomwake tiyeni ‘tizitsatira zinthu zobweretsa mtendere ndiponso zolimbikitsana.”​—Aroma 14:19. w21.06 24 ¶16-17

Loweruka, July 8

Mulungu . . . amakulitsa.​—1 Akor. 3:7.

Ngati timachita khama kuphunzira ndi kugwiritsa ntchito malangizo amene timapeza m’Mawu a Mulungu komanso m’gulu lake, pang’ono ndi pang’ono tidzayamba kukhala ndi makhalidwe ofanana ndi a Khristu ndipo tingamudziwe bwino Mulungu. Yesu anagwiritsa ntchito fanizo pofotokoza mmene uthenga wa Ufumu umene timalalikira ulili ngati kambewu kamene kamakula pang’onopang’ono m’mitima ya anthu abwino. Iye anati: “Mbewuzo zimamera ndi kukula. Koma mmene zimenezi zimachitikira, mwiniwakeyo sadziwa ayi. Pang’onopang’ono, payokha nthaka ija imabala zipatso. Choyamba mmera umabiriwira, kenako umatulutsa ngala, pamapeto pake maso okhwima a tirigu amaonekera m’ngalamo.” (Maliko 4:27, 28) Yesu ankatanthauza kuti mofanana ndi mbewu imene imakula pang’onopang’ono, pamatenga nthawi kuti munthu amene wamva uthenga wa Ufumu asinthe zinthu pa moyo wake. Mwachitsanzo, anthu amene timaphunzira nawo Baibulo akayamba kukhala pa ubwenzi ndi Yehova timaona mmene asinthira zinthu zambiri pa moyo wawo. (Aef. 4:22-24) Koma tizikumbukira kuti Yehova ndi amene amachititsa kuti mbewu ya choonadi ikule mumtima mwa munthu. w21.08 8-9 ¶4-5

Lamlungu, July 9

Kuona ndi maso kuli bwino kuposa kulakalaka ndi mtima.​—Mlal. 6:9.

Tikamafufuza chimwemwe m’malo oyenera, tingathe kukhala osangalala. Munthu amene amasangalala ndi zimene ‘waona ndi maso ake,’ amayamikira zimene ali nazo ndipo amakhala wokhutira ndi mmene zinthu zilili pa moyo wake. Koma mosiyana ndi zimenezi, munthu amene amalakalaka ndi mtima wake, amafunitsitsa kukhala ndi zinthu zimene sangathe kuzipeza. Ndiye kodi tikuphunzirapo chiyani pamenepa? Kuti tizisangalala, tiziganizira kwambiri zimene tili nazo komanso tizikhala ndi zolinga zimene tingazikwaniritse. Mwachibadwa, anthufe timafuna kuchita zinthu zina zatsopano. Ndiye kodi n’zothekadi kumakhutira ndi zimene tili nazo? Inde n’zotheka. Tikhoza kumasangalala ndi zinthu zimene tili nazo panopa, zimene ‘tikuona ndi maso’ athu. Kodi tingachite bwanji zimenezi? Kuti tipeze yankho, taganizirani zimene Yesu ananena mufanizo lake la matalente, lomwe lili pa Mateyu 25:14-30, ndipo onani mmene fanizoli lingatithandizire kuti tizisangalala komanso zimene tingachite kuti tiwonjezere chimwemwe chathucho mogwirizana ndi mmene zinthu zilili pa moyo wathu. w21.08 21 ¶5-6

Lolemba, July 10

Ine ndimakhala kumwamba pamalo oyera. Ndimakhalanso ndi munthu wopsinjika ndi wa mtima wodzichepetsa.​—Yes. 57:15.

Yehova amakonda kwambiri anthu ‘opsinjika ndi a mtima wodzichepetsa.’ Tonsefe, osati akulu okha, tingalimbikitse abale ndi alongo okondedwa amenewa. Njira imodzi imene tingawalimbikitsire ndi kuwasonyeza kuti timawaganizira. Yehova amafuna kuti tiziwasonyeza kuti iye amawakonda komanso kuti ndi nkhosa zake zamtengo wapatali. (Miy. 19:17) Tingalimbikitsenso abale ndi alongowa tikamachita zinthu modzichepetsa. Sitiyenera kuchititsa ena kuti azingoganizira za ifeyo, zomwe zingachititse kuti ayambe kukhala ndi mtima wansanje. M’malomwake tiyenera kugwiritsa ntchito luso limene tili nalo komanso zimene timadziwa polimbikitsa abale athu. (1 Pet. 4:10, 11) Kuganizira mmene Yesu ankachitira zinthu ndi otsatira ake kungatithandize kudziwa mmene tingachitire zinthu ndi anthu ena. Iye anali munthu wamkulu woposa onse amene anakhalako. Koma anali “wofatsa ndi wodzichepetsa.” (Mat. 11:28-30) Pophunzitsa, ankagwiritsa ntchito mawu komanso zitsanzo zosavuta.​—Luka 10:21. w21.07 23 ¶11-12

Lachiwiri, July 11

Funsa . . . amuna achikulire pakati panu, ndipo akufotokozera.—Deut. 32:7.

Muziyesetsa kuyamba ndinu kucheza ndi achikulire. N’zoona kuti mwina panopa maso awo saona bwino, amayenda pang’onopang’ono komanso mawu awo samveka kwambiri. Koma iwo amafunitsitsa atamachita zambiri ndipo apanga “mbiri yabwino” pamaso pa Yehova. (Mlal. 7:1) Muzikumbukira chifukwa chake Yehova amawaona kuti ndi amtengo wapatali. Pitirizani kuwalemekeza. Muzikhala ngati Elisa, yemwe anafunitsitsa kukhalabe ndi Eliya pa tsiku lawo lomaliza kuchitira zinthu limodzi. Katatu konse Elisa ananena kuti “sindikusiyani.” (2 Maf. 2:2, 4, 6) Tingasonyeze chidwi kwa achikulire powafunsa mafunso mwaulemu. (Miy. 1:5; 20:5; 1 Tim. 5:1, 2) Mungawafunse mafunso ngati akuti: “Kodi muli wachinyamata, n’chiyani chinakutsimikizirani kuti mwapeza choonadi?” “Kodi zinthu zimene zakuchitikirani pa moyo wanu zakuthandizani bwanji kukhala pa ubwenzi wolimba ndi Yehova?” “Kodi mwapeza kuti chinsinsi chokhalira osangalala potumikira Yehova ndi chiyani?” (1 Tim. 6:6-8) Ndiyeno muzimvetsera akamakufotokozerani. w21.09 5 ¶14; 7 ¶15

Lachitatu, July 12

Pakuti Mulungu amachita zinthu m’njira imene imamusangalatsa. Iye amalimbitsa zolakalaka zanu kuti muchite zinthu zonse zimene iye amakonda.​—Afil. 2:13.

Tikamayesetsa kumvera lamulo lakuti tizilalikira komanso kuthandiza ena kukhala ophunzira, timasonyeza kuti timakonda Mulungu. (1 Yoh. 5:3) Taganizirani izi: Chifukwa chakuti mumakonda Yehova, munayamba kugwira nawo ntchito yolalikira kunyumba ndi nyumba. Kodi zinali zophweka kumvera lamulo limeneli? Osati kwenikweni. Kodi mutafika kwa nthawi yoyamba pakhomo la munthu munkachita mantha? N’zosakayikitsa. Komabe munkadziwa kuti imeneyi ndi ntchito imene Yesu akufuna kuti muzigwira ndipo munamvera lamuloli. M’kupita kwa nthawi zinakhala zosavuta kuti muzigwira ntchito yolalikira. Koma kodi mumamva bwanji mukaganiza zochititsa phunziro la Baibulo? Kodi mumachita mantha? Mwina ndi choncho. Komabe mukam’pempha Yehova kuti akuthandizeni kuthetsa mantha, komanso kukulimbitsani mtima kuti muyambitse phunziro la Baibulo, iye adzachititsa kuti mukhale ndi mtima wofuna kuthandiza ena kuti akhale ophunzira a Yesu. w21.07 3 ¶7

Lachinayi, July 13

Apatsidwe chizindikiro padzanja lawo lamanja kapena pamphumi pawo.​—Chiv. 13:16.

Kale akapolo ankadindidwa chizindikiro chowazindikiritsa kuti ali ndi mbuye wawo. Mofanana ndi zimenezi, masiku anonso anthu azidzayembekezera kuti aliyense akhale ndi chizindikiro chophiphiritsa padzanja kapena pamphumi. Zochita komanso maganizo awo zidzasonyeza kuti ali kumbali ya maboma a m’dzikoli. Kodi ifeyo tidzalola kulandira chizindikiro chophiphiritsachi n’kukhala kumbali ya maboma a m’dzikoli? Amene adzakane kulandira chizindikirocho adzakumana ndi mavuto aakulu komanso zinthu zoopsa. Buku la Chivumbulutso limanena kuti: “Aliyense asathe kugula kapena kugulitsa, kupatulapo ngati ali ndi chizindikirocho.” (Chiv. 13:17) Koma anthu a Mulungu amadziwa zimene iye adzachite ndi anthu omwe adzakhale ndi chizindikiro chotchulidwa pa Chivumbulutso 14:9, 10. Ndiye m’malo mokhala ndi chizindikiro chimenecho, iwo adzalemba padzanja lawo kuti: “Wa Yehova.” (Yes. 44:5) Inoyo ndi nthawi yoti tiziyesetsa kukhala okhulupirika kwambiri kwa Yehova. Tikamachita zimenezi, iye adzasangalala kutitchula kuti ndife anthu ake. w21.09 18 ¶15-16

Lachisanu, July 14

Chitsulo chimanola chitsulo chinzake. Momwemonso munthu amanola munthu mnzake.​—Miy. 27:17.

Kuti tikwanitse kuchita bwino utumiki wathu, tiyenera kulola kuti ena azitithandiza. Mtumwi Paulo anaphunzitsa Timoteyo mmene angalalikirire komanso kuphunzitsa ndipo anamulimbikitsa kuti aziphunzitsanso ena zimenezo. (1 Akor. 4:17) Mofanana ndi Timoteyo, ifenso tingaphunzire zambiri kwa ena amene ali ndi luso mumpingo. Komanso muzipempha Yehova kuti akuthandizeni pa nthawi iliyonse imene mukugwira ntchito yolalikira. Tikutero chifukwa popanda kuthandizidwa ndi mzimu wake womwe ndi wamphamvu, sitingakwanitse kugwira ntchitoyi. (Sal. 127:1; Luka 11:13) Mukamapemphera kwa Yehova, muzitchula zenizeni zimene mukufuna kuti akuthandizeni. Mwachitsanzo, mungamupemphe kuti akutsogolereni kwa anthu oyenerera omwe akufuna kumvetsera. Tiyeneranso kumapeza nthawi yophunzira Baibulo patokha. Mawu a Mulungu amati: “Muzindikire chimene chili chifuniro cha Mulungu, chabwino, chovomerezeka ndi changwiro.” (Aroma 12:2) Tikamaphunzira m’pamene timamudziwa bwino Mulungu, ndipo tikamauza ena zokhudza Mulunguyo, iwo amatha kuoneratu kuti tikukhulupirira kwambiri zimene tikuwauza. w21.05 18 ¶14-16

Loweruka, July 15

Zonse zimene mukuchita mu ntchito ya Ambuye sizidzapita pachabe.​—1 Akor. 15:58.

Bwanji ngati mumayesetsa kuthandiza munthu amene mukuphunzira naye Baibulo komanso kumupempherera koma iye sakupita patsogolo ndipo mukufunika kusiya kuphunzira naye? Kapenanso bwanji ngati simunaphunzirepo ndi munthu wina mpaka kufika pobatizidwa? Kodi muyenera kumadziimba mlandu, mwina n’kumaganiza kuti Yehova sakudalitsa utumiki wanu? Taonani zimene zimachititsa Yehova kuona kuti utumiki wathu ukuyenda bwino. Iye amaona khama komanso kupirira kwathu. Ngakhale ena asamvetsere uthenga wathu, Yehova amasangalala tikamagwira ntchito yolalikira mwakhama komanso chifukwa chomukonda. Paulo analemba kuti: “Mulungu si wosalungama woti angaiwale ntchito yanu ndi chikondi chimene munachisonyeza pa dzina lake, mwa kutumikira oyera ndipo mukupitiriza kuwatumikira.” (Aheb. 6:10) Iye amakumbukira khama lathu komanso chikondi chathu ngakhale sitinapeze munthu yemwe taphunzira naye Baibulo mpaka kubatizidwa. Choncho zimene Paulo ananena mulemba lalero zingagwirenso ntchito kwa inu. w21.10 25 ¶4-6

Lamlungu, July 16

Chilichonse chimene Atate adzandipatse chidzabwera kwa ine, ndipo wobwera kwa ine sindidzamukana.—Yoh. 6:37.

Mmene Yesu ankachitira zinthu ndi ophunzira ake, zinkasonyeza kuti ndi wokoma mtima komanso wachikondi. Iye ankadziwa kuti ophunzirawo anali ndi luso losiyana komanso zinthu pa moyo wawo zinali zosiyana. Choncho sizikanatheka kuti akhale ndi maudindo ofanana komanso azichita zofanana pa ntchito yolalikira. Komabe Yesu ankayamikira ophunzirawo chifukwa aliyense ankachita zinthu ndi mtima wake wonse. Yesu anasonyeza kuti ankamvetsa ophunzira ake pamene anafotokoza fanizo la matalente. M’fanizoli, mbuye anapereka ntchito kwa kapolo aliyense “malinga ndi luso lake.” Mmodzi wa akapolo awiri akhama, anapeza phindu lalikulu kuposa mnzake. Koma mbuyeyo anayamikira onsewa ndi mawu ofanana akuti: “Wachita bwino kwambiri, kapolo wabwino ndi wokhulupirika iwe!” (Mat. 25:14-23) Yesu amachita nafe zinthu mokoma mtima komanso mwachikondi. Iye amadziwa kuti tili ndi maluso osiyana komanso zinthu ndi zosiyana pa moyo. Ndipo amasangalala ndi zimene timayesetsa kuchita potumikira Mulungu. Tingachite bwino kutengera chitsanzo cha Yesu tikamachita zinthu ndi ena. w21.07 23 ¶12-14

Lolemba, July 17

Sindingatambasule dzanja langa ndi kuukira mbuyanga.​—1 Sam. 24:10.

Si nthawi zonse pamene Mfumu Davide ankasonyeza chifundo. Mwachitsanzo, Nabala, yemwe anali wouma mtima atalankhula zamwano komanso kukana kupatsa chakudya Davide ndi amuna amene anali naye, iye anakwiya ndipo anaganiza zokapha Nabalayo ndi amuna onse a m’nyumba yake. Koma mkazi wa Nabala, Abigayeli yemwe anali wokoma mtima, anachita zinthu mofulumira ndipo anathandiza Davide kuti asapalamule mlandu wa magazi. (1 Sam. 25:9-22, 32-35) Onani kuti Davide atakwiya kwambiri, anaganiza kuti Nabala ndi amuna omwe anali naye ankayenera kuphedwa. Ndipo patapita nthawi Davide anaweruza kuti munthu wa m’fanizo la Natani ankayeneranso kuphedwa. Koma Davide anali munthu wachikondi. Ndiye n’chifukwa chiyani anaweruza munthu wakuba nkhosa uja mwankhanza choncho? Taganizirani zimene zinali zitangomuchitikira kumene. Pa nthawiyo Davide sanali ndi chikumbumtima chabwino. Munthu akamachita nkhanza komanso kumangoweruza ena, amasonyeza kuti moyo wake wauzimu suli bwino. w21.10 12 ¶17-18; 13 ¶20

Lachiwiri, July 18

Mukhale oyera, chifukwa ine ndine woyera.​—1 Pet. 1:16.

Mawu a mulemba lalerowa akusonyeza kuti ndi zotheka kutsanzira Yehova yemwe ndi chitsanzo chabwino kwambiri pa nkhani yokhala oyera. Tiyenera kukhala oyera m’zochita zathu. Zimenezi zingaoneke ngati zosatheka chifukwa si ife angwiro. Mtumwi Petulo nayenso analakwitsapo zinthu zina, koma chitsanzo chake chimasonyeza kuti tingathe ‘kukhala oyera.’ Anthu ambiri akaganizira za munthu amene ndi woyera, amaona kuti ndi munthu amene amavala zovala zachipembedzo yemwe nthawi zonse nkhope yake sisekerera. Koma zimenezi si zolondola. Baibulo limati Yehova yemwe ndi woyera ndi “Mulungu wachimwemwe.” (1 Tim. 1:11) Ndipo munthu amene amamulambira amatchulidwa kuti ndi “wodala” kapena kuti wosangalala. (Sal. 144:15) Yesu anadzudzula anthu amene ankavala zovala zapadera n’kumadzionetsera kwa anthu kuti ndi olungama. (Mat. 6:1; Maliko 12:38) Monga Akhristu, mmene timaonera nkhani yokhala oyera, zimagwirizana ndi zimene timaphunzira m’Baibulo. Ndife otsimikiza kuti Mulungu wathu yemwe ndi wachikondi, sangatipatse malamulo omwe ndi zosatheka kuti tiwatsatire. w21.12 2 ¶1, 3

Lachitatu, July 19

Uzikonda Yehova Mulungu wako ndi mtima wako wonse.—Maliko 12:30.

Pali mphatso zambiri zimene Mulungu watipatsa mokoma mtima. Imodzi mwa mphatsozi ndi mwayi woti tizimulambira. Timasonyeza kuti timakonda Yehova ‘tikamasunga malamulo ake.’ (1 Yoh. 5:3) Polankhula m’malo mwa Atate wake, Yesu anatilamula kuti tizithandiza anthu kukhala ophunzira ake komanso kuwabatiza. (Mat. 28:19) Iye anatilamulanso kuti tizikondana. (Yoh. 13:35) Yehova adzalandira onse omvera m’banja lake lapadziko lonse la anthu amene amamulambira. (Sal. 15:1, 2) Tizikonda anthu ena. Chikondi ndi khalidwe lalikulu la Yehova. (1 Yoh. 4:8) Iye anasonyeza kuti amatikonda tisanamudziwe n’komwe. (1 Yoh. 4:9, 10) Timamutsanzira tikamakonda anthu ena. (Aef. 5:1) Njira imodzi imene tingasonyezere kuti timakonda anthu ndi kuwathandiza kudziwa za Yehova nthawi idakalipo. (Mat. 9:36-38) Tikamachita zimenezi, timakhala tikuwapatsa mwayi woti akhale ndi chiyembekezo chodzakhala m’banja la Mulungu. w21.08 5-6 ¶13-14

Lachinayi, July 20

Palibe amene ali ndi chikondi chachikulu kuposa [ichi.]—Yoh. 15:13.

Popeza amakonda kwambiri Yehova, Yesu anachita zinthu modzimana chifukwa cha Atate wakewo komanso ifeyo. (Yoh. 14:31) Ndipotu zimene Yesu anachita ali padzikoli zinasonyeza kuti amakonda kwambiri anthu. Tsiku lililonse iye ankasonyeza chikondi komanso chifundo, ngakhale pamene anthu ena ankamutsutsa. Njira yaikulu imene anasonyezera kuti amakonda anthu, ndi kuwaphunzitsa zokhudza Ufumu wa Mulungu. (Luka 4:43, 44) Yesu anasonyezanso Mulungu ndi anthu chikondi chovutikira ena pololera kuti azunzidwe komanso kuphedwa ndi anthu ochimwa. Zimene anachitazi zinatipatsa mwayi woti tidzapeze moyo wosatha. Tinadzipereka kwa Yehova komanso kubatizidwa chifukwa chakuti timakonda Atate wathu wakumwamba. Choncho mofanana ndi Yesu, mmene timachitira zinthu ndi anthu ziyenera kusonyeza kuti timakonda Yehova. Mtumwi Yohane analemba kuti: “Amene sakonda m’bale wake amene amamuona, sangakonde Mulungu amene sanamuonepo.”​—1 Yoh. 4:20. w22.03 10 ¶8-9

Lachisanu, July 21

Samalani kwambiri kuti mmene mukuyendera si monga anthu opanda nzeru, koma ngati anzeru. Muzigwiritsa ntchito bwino nthawi yanu.—Aef. 5:15, 16.

Ngakhale kuti timasangalala kupeza nthawi yochita zinthu ndi Yehova, pali vuto lina limene timakumana nalo. Timakhala otanganidwa, zomwe zimachititsa kuti zizikhala zovuta kupeza nthawi yochita zinthu zokhudza kulambira. Ntchito, udindo wathu wosamalira banja komanso zinthu zina zofunika zimafuna nthawi yambiri moti tikhoza kumaona kuti sitingapeze nthawi yopemphera, kuphunzira komanso kuganizira za Yehova. Palinso vuto lina losaonekera lomwe lingachititse kuti tiziwononga nthawi yathu. Ngati sitingasamale, zinthu zina zomwe timachita zomwe pazokha si zolakwika, zikhoza kuwononga nthawi yathu yoti tizilimbitsa ubwenzi wathu ndi Yehova. Mwachitsanzo, timafunika kupeza nthawi yopuma kapena kuchita zinthu zina zosangalatsa. Komatu ngakhale zosangalatsa zomwe si zolakwika zikhoza kuwononga nthawi yathu n’kufika poti sitingakhale ndi nthawi yokwanira yochita zinthu zokhudza kulambira. Choncho tizikumbukira kuti zosangalatsa siziyenera kukhala chinthu chofunika kwambiri.​—Miy. 25:27; 1 Tim. 4:8. w22.01 26 ¶2-3

Loweruka, July 22

Mlendo wokhala pakati panu muzimuona ngati mbadwa. Muzim’konda mmene mumadzikondera nokha.—Lev. 19:34.

Pamene Yehova analamula Aisiraeli kuti azikonda anzawo, sanatanthauze kuti azingokonda anthu a mtundu wawo okha. Iye anawauza kuti azikondanso alendo okhala pakati pawo. Umenewu ndi uthenga womveka bwino womwe uli pa Levitiko 19:33, 34. Mlendoyo ankayenera kumaonedwa ngati “mbadwa,” ndipo Aisiraeli ankafunika ‘kumamukonda’ ngati mmene amadzikondera okha. Aisiraeli ankayenera kulola alendo komanso osauka kuti azikunkha m’minda yawo. (Lev. 19:9, 10) Mfundo yokhudza kukonda alendo, imagwiranso ntchito kwa Akhristu masiku ano. (Luka 10:30-37) Motani? Pali anthu ambiri omwe anachoka m’mayiko awo kupita mayiko ena ndipo n’kutheka kuti ena amakhala pafupi ndi kumene timakhala. Choncho n’zofunika kuti tizilemekeza amuna, akazi ndi ana amenewa. w21.12 12 ¶16

Lamlungu, July 23

Ofunafuna Yehova sadzasowa chilichonse chabwino.—Sal. 34:10.

Tikamadalira kwambiri Yehova kuti azititsogolera panopa, tidzamudaliranso kwambiri m’tsogolo kuti adzatipulumutsa. Pamafunika chikhulupiriro komanso mtima wofunitsitsa kuti tidalire Yehova kuti tipemphe abwana athu kuti atilole kukapezeka kumsonkhano wadera kapena wachigawo, kapenanso kuwapempha kuti atichepetsere nthawi yogwira ntchito n’cholinga choti tizipezeka pamisonkhano komanso kumagwira nawo mokwanira ntchito yolalikira. Tiyerekeze kuti abwana athuwo akana zimene tawapempha ndipo atichotsa ntchito, kodi timakhulupirira kuti Yehova sangatisiye ndiponso kuti nthawi zonse azitipatsa zimene timafunikira? (Aheb. 13:5) Atumiki a nthawi zonse ambiri angatifotokozere zimene zinawachitikira, zomwe zimasonyeza mmene Yehova anawathandizira pa nthawi imene ankafunika kwambiri kuthandizidwa. Yehova ndi wokhulupirika. Popeza Yehova ali kumbali yathu, palibe chifukwa choopera zimene tikumane nazo m’tsogolo. Ngati timaika zimene Mulungu amafuna pamalo oyamba pa moyo wathu, iye sadzatisiya. w22.01 7 ¶16-17

Lolemba, July 24

Simukuweruzira munthu koma mukuweruzira Yehova.​—2 Mbiri 19:6.

Kodi chikhulupiriro chathu mwa akulu chingayesedwe bwanji? Tiyerekezere kuti munthu yemwe wachotsedwa ndi mnzathu wapamtima? Mwina tingamaone kuti akulu sanaganizire mfundo zonse za nkhaniyo kapena tingamakayikire ngati aweruza mogwirizana ndi zimene Yehova akufuna. Ndiye n’chiyani chingatithandize kuti tiziona moyenera zimene akulu asankha? Tiyenera kukumbukira kuti Yehova ndi amene anakonza zoti munthu wosalapa azichotsedwa mumpingo ndipo zimenezi zimapindulitsa mpingo komanso kuthandiza munthu wochimwayo. Ngati munthu wosalapayo atapitiriza kukhala mumpingo, angalimbikitse anthu ena kuti azichita zoipa. (Agal. 5:9) Kuwonjezera pamenepo, iye sangazindikire kukula kwa tchimo lake ndipo sangaone kufunika koti asinthe mmene amaganizira komanso zochita zake n’cholinga choti akhalenso pa ubwenzi ndi Yehova. (Mlal. 8:11) Tingakhale otsimikiza kuti akulu akafuna kusankha ngati munthu akufunika kuchotsedwa, saona udindo wawo mopepuka. w22.02 5-6 ¶13-14

Lachiwiri, July 25

Bango lophwanyika sadzalisansantha ndipo nyale yofuka sadzaizimitsa.​—Mat. 12:20.

Kuleza mtima ndiponso kukoma mtima n’kofunika kwambiri makamaka ngati munthu akukana kulandira malangizo a m’Baibulo. Mkulu ayenera kuyesetsa kuti asamakwiye ngati malangizo amene wapereka sakutsatiridwa nthawi yomweyo. Choncho akamapemphera payekha, mkulu angapemphe Yehova kuti adalitse munthu amene akufunika kupatsidwa malangizoyo komanso kuti amuthandize kumvetsa chifukwa chake akufunikira malangizowo ndi kuwatsatira. Nthawi zina m’bale amene akupatsidwa malangizoyo angafunike nthawi yokwanira kuti aganizire zimene wauzidwa. Ngati mkulu ali woleza mtima komanso wokoma mtima, munthu amene akumuthandizayo sadzasokonedwa ndi mmene malangizowo akuperekedwera, m’malomwake adzaganizira kwambiri malangizo amene akupatsidwawo. Komabe nthawi zonse malangizowo ayenera kukhala ochokera m’Mawu a Mulungu. Cholinga chathu sikungopereka malangizo amene ndi othandiza koma amenenso ‘angasangalatse mtima.’​—Miy. 27:9. w22.02 18 ¶17; 19 ¶19

Lachitatu, July 26

Chinthu chimene unali kuyembekeza chikalephereka, chimadwalitsa mtima.​—Miy. 13:12.

Nthawi zina tikapempha Yehova kuti atithandize kulimbana ndi mayesero amene takumana nawo, kapena kusiya khalidwe linalake limene iye sasangalala nalo, tingaone kuti akuchedwa kuyankha mapemphero athu. N’chifukwa chiyani Yehova sayankha mapemphero athu onse nthawi yomweyo? Amaona mapemphero athu ochokera pansi pamtima ngati umboni wosonyeza kuti timamukhulupirira. (Aheb. 11:6) Iye amafuna aone ngati tatsimikiza mtima kuchita zinthu mogwirizana ndi mapemphero athu komanso zimene amafuna. (1 Yoh. 3:22) Choncho tiyenera kuyembekezera moleza mtima komanso kuchita zonse zomwe tingathe kuti tisiye khalidwe limene iye sasangalala nalo. Yesu anasonyeza kuti mapemphero athu ena sangayankhidwe nthawi yomweyo. Iye anati: “Pemphanibe, ndipo adzakupatsani. Pitirizani kufunafuna, ndipo mudzapeza. Gogodanibe, ndipo adzakutsegulirani. Pakuti aliyense wopempha amalandira, aliyense wofunafuna amapeza, ndipo aliyense wogogoda adzamutsegulira.”​—Mat. 7:7, 8. w21.08 8 ¶1; 10 ¶9-10

Lachinayi, July 27

Ndimakonda kwambiri chilamulo chanu! Ndimasinkhasinkha chilamulocho tsiku lonse.​—Sal. 119:97.

Kuti muzikhulupirira kwambiri Mlengi, muyenera kupitiriza kuphunzira Mawu a Mulungu. (Yos. 1:8) Muziganiziranso maulosi komanso kugwirizana kwa nkhani zake. Kuchita zimenezi kungathandize kuti muzikhulupirira kwambiri kuti tinalengedwa ndi Mlengi wachikondi komanso wanzeru, yemwenso anachititsa kuti Baibulo lilembedwe. (2 Tim. 3:14; 2 Pet. 1:21) Mukamaphunzira Mawu a Mulungu mudzaona kuti malangizo ake ndi othandiza kwambiri. Mwachitsanzo, kale kwambiri Baibulo linachenjeza kuti kukonda ndalama n’koopsa ndipo kumabweretsera munthu “zopweteka zambiri.” (1 Tim. 6:9, 10; Miy. 28:20; Mat. 6:24) Pamenepatu tingaone kuti zimene Baibulo limatichenjeza kuti tisamakonde ndalama n’zothandiza. Kodi ndi mfundo zina ziti za m’Baibulo zomwe mwaona kuti ndi zothandiza? Tikamayamikira kwambiri malangizo a m’Baibulo, m’pamenenso timadalira kwambiri nzeru za Mlengi wathu wachikondi zomwe zimakhala zothandiza nthawi zonse. (Yak. 1:5) Tikamachita zimenezi, tidzakhala osangalala kwambiri.​—Yes. 48:17, 18. w21.08 17-18 ¶12-13

Lachisanu, July 28

Pakuti Mulungu si wosalungama woti angaiwale ntchito yanu ndi chikondi chimene munachisonyeza pa dzina lake.​—Aheb. 6:10.

Ngati mukukalamba, dziwani kuti Yehova amakumbukira zimene mwachita m’mbuyomu. Mwakhala mukugwira nawo ntchito yolalikira mwakhama. Mwapirira mayesero osiyanasiyana ngakhalenso ovuta kwambiri. Mwakhala mukutsatira mokhulupirika mfundo zolungama za m’Baibulo, kutumikira pa maudindo akuluakulu, kuphunzitsa ena ndiponso kuchita zinthu mogwirizana ndi kusintha kumene kwakhala kukuchitika m’gulu la Yehova. Mwakhalanso mukuthandiza komanso kulimbikitsa anthu amene akuchita utumiki wa nthawi zonse. Yehova Mulungu amakukondani kwambiri chifukwa chokhalabe okhulupirika. Iye amalonjeza kuti “sadzasiya anthu ake okhulupirika.” (Sal. 37:28) Akukutsimikizirani kuti: “Munthu wa imvi ndimamunyamula nthawi zonse.” (Yes. 46:4) Choncho musamaganize kuti si inunso ofunika m’gulu la Yehova chifukwa choti tsopano mwakalamba. Ndinu ofunika kwambiri. w21.09 3 ¶4

Loweruka, July 29

Yehova wasonyezanso chifundo kwa onse omuopa.​—Sal. 103:13.

Yehova amasonyeza chifundo chifukwa cha nzeru zake zopanda malire. Baibulo limati: “Nzeru yochokera kumwamba” ndi “yodzaza ndi chifundo ndi zipatso zabwino.” (Yak. 3:17) Mofanana ndi kholo lachikondi, Yehova amadziwa kuti chifundo chake chimathandiza kwambiri ana ake. (Yes. 49:15) Popeza Yehova amasonyeza chifundo anthu ake, iwo akuyembekezera zinthu zabwino m’tsogolo ngakhale kuti si angwiro. Choncho nzeru zopanda malire za Yehova, zimamuchititsa kuti azisonyeza chifundo pakakhala chifukwa chochitira zimenezo. Koma iye amadziwanso nthawi imene sayenera kusonyeza chifundo. Popeza ndi wanzeru, iye salekerera zoipa pongofuna kusonyeza chifundo. Tiyerekeze kuti mtumiki wa Mulungu mwadala wasankha kuti azichita machimo. Kodi tiyenera kuchita chiyani? Yehova anauzira Paulo kulemba kuti: “Muleke kuyanjana” naye. (1 Akor. 5:11) Anthu amene achita machimo koma osalapa amachotsedwa mumpingo. Kuchita zimenezi n’kofunika chifukwa kumateteza abale ndi alongo athu okhulupirika komanso kumasonyeza kuti Yehova ndi woyera. w21.10 9-10 ¶7-8

Lamlungu, July 30

Mulungu amakonda munthu wopereka mokondwera.​—2 Akor. 9:7.

Timalambira Yehova tikamathandiza pantchito ya Ufumu ndi zopereka zathu. Aisiraeli sankafunika kukaonekera pamaso pa Yehova chimanjamanja. (Deut. 16:16) Iwo ankafunika kubweretsa mphatso ina yake mogwirizana ndi mmene zinthu zinalili pa moyo wawo. Zimenezi zinkasonyeza kuti ankayamikira zonse zimene zinkakonzedwa kuti apindule mwauzimu. Kodi tingasonyeze bwanji kuti timakonda Yehova komanso kuti timayamikira zonse zimene akutichitira? Njira imodzi ndi kupereka ndalama zothandizira mpingo umene tikusonkhana komanso ntchito ya padziko lonse mogwirizana ndi mmene zinthu zilili pa moyo wathu. Pa nkhaniyi mtumwi Paulo anafotokoza kuti: “Mphatso yochokera pansi pa mtima ndi imene Mulungu amakondwera nayo, chifukwa Mulungu amafuna kuti munthu apereke zimene angathe, osati zimene sangathe.” (2 Akor. 8:4, 12) Yehova amasangalala ndi ndalama zimene timapereka mochokera pansi pa mtima, ngakhale zitakhala zochepa bwanji.​—Maliko 12:42-44. w22.03 24 ¶13

Lolemba, July 31

Lankhulani molimbikitsa kwa amtima wachisoni, thandizani ofooka, khalani oleza mtima kwa onse.​—1 Ates. 5:14.

Akulu sangathetse mavuto onse amene anthu a Yehova amakumana nawo. Ngakhale zili choncho, Yehova amafuna kuti akulu aziyesetsa kulimbikitsa komanso kuteteza nkhosa zake. Ndiye kodi akulu omwe amakhala kale ndi zochita zambiri angapeze bwanji nthawi yothandiza abale ndi alongo? Muzitengera Chitsanzo cha Paulo. Nthawi zonse Paulo ankayesetsa kuyamikira abale ake komanso kuwalimbikitsa. Akulunso angachite bwino kutengera chitsanzo chake pokonda abale komanso kuwakomera mtima. (1 Ates. 2:7) Paulo anatsimikizira Akhristu anzake kuti amawakonda komanso kuti Yehova amawakondanso. (2 Akor. 2:4; Aef. 2:4, 5) Ankaona anthu a mumpingo ngati anzake ndipo ankapeza nthawi yocheza nawo. Iye anasonyeza kuti ankawadalira powauza momasuka zimene zinkamudetsa nkhawa komanso zofooka zake. (2 Akor. 7:5; 1 Tim. 1:15) Komabe iye sankangokhalira kuganizira za mavuto ake. M’malomwake ankafuna kuthandiza abale ake. w22.03 28 ¶9-10

    Mabuku a Chichewa (1974-2026)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena