August
Lachiwiri, August 1
Atate, akhululukireni.—Luka 23:34.
Pamenepa Yesu ayenera kuti ankanena za asilikali a Chiroma omwe anakhomerera manja ndi mapazi ake ndi misomali. Yesu sanalole kuti zinthu zopanda chilungamo zomwe zinamuchitikira zimuchititse kukhala wokwiya komanso kulephera kukhululukira ena. (1 Pet. 2:23) Mofanana ndi Yesu, tiyenera kukhala okonzeka kukhululukira ena. (Akol. 3:13) Anthu ena kuphatikizapo achibale athu, angamatitsutse chifukwa samvetsa zimene timakhulupirira komanso mmene timachitira zinthu. Iwo akhoza kutinenera zabodza, kutichititsa manyazi pamaso pa anthu ena, kutiwonongera mabuku ngakhalenso kutiopseza kuti atichitira zinthu zankhanza. M’malo mosunga chakukhosi tingam’pemphe Yehova kuti awathandize kuti tsiku lina nawonso adzaphunzire choonadi. (Mat. 5:44, 45) Nthawi zina zingativute kukhululuka makamaka ngati anthu ena anatichitira zinthu zoipa kwambiri. Koma ngati sitingakhululuke n’kumangokhalabe okwiya, tingakhale tikudzivulaza tokha. (Sal. 37:8) Tikasankha kukhululuka, zimasonyeza kuti sitikufuna kumangopitirizabe kukhala okwiya chifukwa cha zinthu zoipa zimene ena anatichitira.—Aef. 4:31, 32. w21.04 8-9 ¶3-4
Lachitatu, August 2
Iwo analitu . . . kumukhumudwitsa.—Sal. 78:40.
Kodi munthu wina amene mumamukonda anachotsedwa mumpingo? Zimenezitu zimakhala zopweteka kwambiri. Taganizirani mmene Yehova zinamupwetekera kuona angelo ake ena akumupandukira. (Yuda 6) Ndiye taganiziraninso mmene ankamvera kuona anthu ake okondedwa Aisiraeli akumupandukira mobwerezabwereza. (Sal. 78:41) Musamakayikire kuti Atate wathu wachikondi zimamuwawanso munthu amene mumamukonda akasiya kumutumikira. Iye amamvetsa ululu umene mukumva mumtima mwanu. Mokoma mtima iye adzakulimbikitsani ndi kukuthandizani. Mwana akasiya kutumikira Yehova, kawirikawiri makolo amadziimba mlandu poganiza kuti pali zina zomwe akanachita kuti amuthandize kukhalabe m’choonadi. M’bale wina ananena kuti: “Ndinkaona kuti vuto ndi ineyo. Nthawi zina ndinkalota maloto oipa.” Mlongo wina yemwenso zimenezi zinamuchitikira ananena kuti: “Nthawi zina ndinkadzifunsa kuti, ‘kodi ndinalakwitsa chiyani monga mayi?’ Ndinkaona kuti ndinalephera kukhomereza choonadi mwa mwana wanga.” w21.09 26 ¶1-2, 4
Lachinayi, August 3
[Iwo] anazindikira kuti anali anthu osaphunzira ndiponso anthu wamba.—Mac. 4:13.
Ena amaona kuti anthu a Mulungu sangaphunzitse Baibulo chifukwa sanapite kumasukulu azachipembedzo. Komabe iwo ayenera kufufuza mfundo zoona. Zimenezi ndi zomwe wolemba Uthenga Wabwino Luka anachita. Iye anachita khama pofufuza “zinthu zonse mosamala kwambiri kuchokera pa chiyambi.” Ankafuna kuti anthu amene ankawerenga uthenga wake wonena za Yesu adziwe bwinobwino kuti zinthu zimene anaphunzitsidwa “n’zodalirika.” (Luka 1:1-4) Ayuda a ku Bereya nawonso anachita zofanana ndi zimene Luka anachita. Iwo atamva koyamba uthenga wonena za Yesu, anafufuza m’Malemba a Chiheberi kuti atsimikizire kuti zimene anauzidwazo zinali zoona. (Mac. 17:11) Mofanana ndi zimenezi, anthu masiku ano ayenera kufufuza kuti adziwe zoona. Afunika kumayerekezera zimene anthu a Mulungu amaphunzitsa ndi zimene Malemba amanena. Ayeneranso kufufuza zimene anthu a Yehova akuchita masiku ano. Ngati atafufuza bwinobwino, sangasokonezedwe ndi tsankho kapena nkhani zimene anthu ena amangonena, zomwe zilibe umboni. w21.05 3 ¶7-8
Lachisanu, August 4
Futukulani mtima wanu.—2 Akor. 6:13.
Kodi pali munthu wina mumpingo wanu yemwe mungamachite naye zinthu zina limodzi? Nthawi zina Akhristu anzathu akhoza kuyamikira kwambiri ngati titachita nawo zinthu limodzi. Ena zingawavute kukhala ndi achibale awo omwe si a Mboni pa nthawi ya zikondwerero zina. Enanso angamamve chisoni kwambiri pa masiku ena monga tsiku limene munthu amene ankamukonda anamwalira. Tikamapeza nthawi yocheza ndi abale ndi alongo amene akukumana ndi mavuto ngati amenewa, timawasonyeza kuti timawaganizira kapena kuti ‘timasamaladi za iwo.’ (Afil. 2:20) Pali zifukwa zambiri zimene zingachititse Mkhristu kuti nthawi zina azidziona ngati ali yekhayekha. Komabe tisamaiwale kuti Yehova amadziwa bwino mmene timamvera. Iye nthawi zambiri amagwiritsa ntchito abale ndi alongo athu potithandiza. (Mat. 12:48-50) Ifenso timasonyeza kuti timayamikira zimene Yehova watichitira tikamayesetsa kuthandiza abale ndi alongo athu. Ngakhale kuti nthawi zina tingamadzione kuti tili tokhatokha, nthawi zonse Yehova amakhala nafe. w21.06 13 ¶18-20
Loweruka, August 5
Khalani ndi khalidwe labwino pakati pa anthu a m’dzikoli, kuti pamene akukunenerani monga anthu ochita zoipa, pa mapeto pake iwo pokhala mboni zimene zikuona ndi maso zochita zanu zabwino, adzatamande Mulungu.—1 Pet. 2:12.
Yesu anapitirizabe kugwira ntchito yolalikira ngakhale kuti anthu ena sankafuna kumvetsera uthenga wake. Iye anachita zimenezi chifukwa ankadziwa kuti anthu afunika kudziwa choonadi ndipo anali wofunitsitsa kuthandiza anthu ambiri kuti amve uthenga wa Ufumu. Ankadziwanso kuti anthu ena omwe poyamba sankafuna kumvetsera adzasintha. Chitsanzo ndi zimene zinachitika ndi anthu a m’banja lake. Pa zaka zitatu zimene Yesu anachita utumiki wake, palibe m’bale wake aliyense amene anakhala wophunzira wake. (Yoh. 7:5) Koma iye ataukitsidwa abale akewo anakhala Akhristu. (Mac. 1:14) Sitingadziwiretu amene angadzakhale atumiki a Yehova. Anthu ena angatenge nthawi yaitali kuti aphunzire choonadi kusiyana ndi ena. Ngakhale anthu amene sakufuna kumvetsera uthenga wathu amaona zimene timachita komanso makhalidwe athu abwino, ndipo kenako angayambe “kutamanda Mulungu.” w21.05 18 ¶17-18
Lamlungu, August 6
Pitani ndi kulalikira kuti, “Ufumu wakumwamba wayandikira.”—Mat. 10:7.
Pamene Yesu anali padzikoli, anapatsa otsatira ake lamulo lomwe linali ndi mbali ziwiri. Iye anawauza kuti azilalikira uthenga wabwino wa Ufumu ndipo anawasonyeza mmene angachitire zimenezi. (Luka 8:1) Mwachitsanzo, Yesu anauza ophunzira ake zimene angachite ngati anthu atakana kapena kumvetsera uthenga wa Ufumu. (Luka 9:2-5) Yesu ananeneratunso kuchuluka kwa ntchitoyi pomwe anauza otsatira ake kuti adzachitira “umboni ku mitundu yonse.” (Mat. 24:14; Mac. 1:8) Iye anauzanso otsatira ake kuti aziphunzitsa anthu kusunga zinthu zonse zimene analamula. Koma kodi ntchito yolalikira komanso kuphunzitsa inaperekedwa kwa Akhristu oyambirira okha monga mmene ena amanenera? Ayi. Yesu anasonyeza kuti ntchito yofunikayi idzapitirizabe kuchitika mpaka mu nthawi yathu ino kapena kuti “mpaka m’nyengo ya mapeto a nthawi ino.” (Mat. 28:18-20) Komanso m’masomphenya amene anaonetsa Yohane, Yesu anasonyeza kuti amafuna kuti ophunzira ake onse azithandiza ena kudziwa zokhudza Yehova.—Chiv. 22:17. w21.07 2-3 ¶3-4
Lolemba, August 7
Tisakhale odzikuza, oyambitsa mpikisano pakati pathu, ndi ochitirana kaduka.—Agal. 5:26.
Masiku ano anthu ambiri m’dzikoli ndi odzikonda ndipo amalimbikitsa mtima wampikisano. Mwachitsanzo munthu wina wabizinezi angalolere kuchita zinthu zoipa n’cholinga choti bizinezi yake iziyenda bwino kuposa anzake. Wochita masewera angavulaze dala mnzake wa timu ina n’cholinga choti timu yake ipambane. Komanso mtima wampikisano ungalimbikitse mwana wasukulu kuti abere mayeso n’cholinga choti apeze malo kuyunivesite ina yotchuka. Monga Akhristu, timadziwa kuti zimenezi ndi zolakwika ndipo ndi “ntchito za thupi.” (Agal. 5:19-21) Komabe, kodi n’zotheka kuti mosadziwa mtumiki wa Yehova azilimbikitsa mtima wampikisano mumpingo? Limenelitu ndi funso lofunika chifukwa mtima umenewu ungachititse kuti abale ndi alongo asamagwirizane. Choncho, tingachite bwino kuganizira zitsanzo za amuna ndi akazi okhulupirika otchulidwa m’Baibulo amene anapewa mtima wampikisano. w21.07 14 ¶1-2
Lachiwiri, August 8
Wodala ndi munthu amene amachita zinthu moganizira munthu wonyozeka. Pa tsiku la tsoka, Yehova adzamupulumutsa.—Sal. 41:1.
Chikondi chokhulupirika chimatichititsa kuti tizithandiza anthu amene akumana ndi mavuto. Masiku ano abale ndi alongo okoma mtima amafunitsitsa kuthandiza ena mumpingo omwe akumana ndi mavuto. Iwo amakonda abale ndi alongo awo ndipo amafuna kuchita zonse zimene angathe kuti awathandize. (Miy. 12:25; 24:10) Izi ndi zogwirizana ndi zimene Paulo anatilimbikitsa pomwe anati: “Lankhulani molimbikitsa kwa amtima wachisoni, thandizani ofooka, khalani oleza mtima kwa onse.” (1 Ates. 5:14.) Nthawi zambiri njira yabwino imene tingathandizire m’bale kapena mlongo amene ali ndi nkhawa ndi kumumvetsera akamalankhula komanso kumutsimikizira kuti timamukonda. Mulungu amaona zimene mumachita pothandiza atumiki ake amtengo wapatali. Pa Miyambo 19:17 pamati: “Wokomera mtima munthu wonyozeka akukongoza Yehova, ndipo adzam’bwezera zimene anachitazo.” w21.11 10 ¶11-12
Lachitatu, August 9
Anthu inu, talawani ndipo muona kuti Yehova ndi wabwino. Wodala ndi munthu wamphamvu amene amathawira kwa iye.—Sal. 34:8.
Kodi tingatani kuti panopa tizikonzekera zam’tsogolo? Tiyenera kumakhala okhutira ndipo tizisangalala kwambiri chifukwa cha ubwenzi wabwino umene tili nawo ndi Yehova. Tikamamudziwa bwino Mulungu wathu, m’pamenenso tingadzakhulupirire kwambiri kuti adzatiteteza Gogi wa ku Magogi akamadzatiukira. Mawu a mulemba lalero akusonyeza chifukwa chake Davide ankakhulupirira kuti Yehova angamuthandize. Nthawi zonse ankadalira Yehova ndipo sanamugwiritsepo mwala. Iye ali mnyamata, atakumana ndi Goliyati yemwe anali Mfilisiti wodziwa kumenya nkhondo anamuuza kuti: “Lero Yehova akupereka m’manja mwanga.” (1 Sam. 17:46) Pa nthawi inanso Davide ankatumikira Mfumu Sauli, yemwe mobwerezabwereza ankafuna kumupha. Koma “Yehova anali ndi Davideyo.” (1 Sam. 18:12) Choncho popeza Davide anali ataona Yehova akumuthandiza m’mbuyomu, ankakhulupirira kuti amuthandizanso pa mavuto amene ankakumana nawo. w22.01 6 ¶14-15
Lachinayi, August 10
Ana onse a Mulungu anayamba kufuula ndi chisangalalo.—Yobu 38:7.
Pa zonse zimene amachita, Yehova amaleza mtima komanso amadzipatsa nthawi yokwanira kuti amalize ntchito imene akugwira. Iye amachita zimenezi kuti dzina lake lilemekezedwe komanso pofuna kuthandiza anthu ena. Mwachitsanzo taganizirani zimene anachita pokonza dziko lapansili pang’onopang’ono. Pofotokoza zimenezi, Baibulo limanena kuti iye “anaika miyezo yake,” anazika “maziko ake” komanso anaika “mwala wake wapakona.” (Yobu 38:5, 6) Iye ankapeza nthawi yoonanso mmene zinthu zimene analenga zinkaonekera. (Gen. 1:10, 12) Tangoganizani mmene angelo ankamvera akaona chinthu chatsopano chilichonse chimene Yehova walenga. Iwo ayenera kuti ankasangalala kwambiri. Tikutero chifukwa pa nthawi ina, “anayamba kufuula ndi chisangalalo.” Kodi tikuphunzirapo chiyani? Panatenga zaka zambiri kuti Yehova amalize ntchito yake yolenga zinthu, koma ataona zinthu zonse zimene analenga, iye ananena kuti “zinali zabwino kwambiri.”—Gen. 1:31. w21.08 9 ¶6-7
Lachisanu, August 11
Wachita bwino kwambiri, kapolo wabwino ndi wokhulupirika iwe!—Mat. 25:23.
Mufanizo lina, Yesu anatchula za munthu amene ankafuna kupita kudziko lina. Asananyamuke, iye anaitana akapolo ake n’kuwapatsa matalente kuti achite nawo malonda. Poganizira zimene kapolo aliyense angakwanitse, munthuyo anapereka matalente 5 kwa kapolo woyamba, matalente awiri kwa kapolo wina ndipo wachitatu anam’patsa talente imodzi. Akapolo awiri oyambawo, anagwiritsa ntchito bwino matalente amene anapatsidwa. Koma kapolo wachitatu uja sanachite chilichonse ndi talente imene anapatsidwa, ndipo mbuye wake anamuchotsa ntchito. Kapolo woyamba komanso wachiwiri anaona kuti apatsidwa udindo wofunika kwambiri ndipo anachita khama kutumikira mbuye wawo. Iwo anawonjezera matalente ena pa matalente amene mbuye wawo anawapatsa. Akapolowa anapatsidwa mphoto chifukwa cha khama komanso luso lawo. Kuwonjezera pa kusangalala ndi zimene anachita, mbuye wawo anawawonjezeranso zochita zina. w21.08 21 ¶7; 22 ¶9-10
Loweruka, August 12
Ndigwedezanso kumwamba [ndi] dziko lapansi.—Hag. 2:6.
Yehova wakhala akuleza mtima kwambiri m’masiku otsiriza ano. Iye safuna kuti aliyense adzawonongedwe. (2 Pet. 3:9) Yehova wapereka mwayi kwa anthu onse woti alape. Komabe, kuleza mtima kwake kuli ndi malire. Anthu amene amakana mwayi umenewu adzaona zimene Farao wa mu nthawi ya Mose anakumana nazo. Yehova anauza Farao kuti: “Pofika pano ndikanatambasula kale dzanja langa ndi kukupha ndi mliri, iweyo ndi anthu ako, kukufafanizani padziko lapansi. Koma ndakusiya ndi moyo kuti ndikusonyeze mphamvu zanga, ndi kuti dzina langa lilengezedwe padziko lonse lapansi.” (Eks. 9:15, 16) Pamapeto pake, mitundu yonse ya anthu idzadziwa kuti Yehova yekha ndiye Mulungu woona. (Ezek. 38:23) Kugwedeza kotchulidwa mulemba la lero, kudzachititsa kuwonongedwa kwa anthu onse okhala ngati Farao, omwe amakana kuti Yehova ndi woyenera kulamulira. w21.09 18-19 ¶17-18
Lamlungu, August 13
Sangalalani ndi anthu amene akusangalala. Lirani ndi anthu amene akulira.—Aroma 12:15.
Kodi mukumva kupweteka mumtima chifukwa choti munthu amene mumamukonda wachotsedwa? Nanga mungachite chiyani ngati mukuona kuti mumpingo ena alankhula zinthu zimene zachititsa kuti mumve kuwawa kwambiri? Sitingayembekezere kuti aliyense azilankhula zinthu zoyenera. (Yak. 3:2) Tonsefe si angwiro. Choncho musamadabwe ngati ena zikuwavuta kulankhula zinthu zoyenera, kapenanso ngati mosadziwa alankhula zinthu zimene zakukhumudwitsani. Muzikumbukira malangizo a mtumwi Paulo akuti: “Pitirizani kulolerana ndi kukhululukirana ndi mtima wonse, ngati wina ali ndi chifukwa chodandaulira.” (Akol. 3:13) Muzipitiriza kuthandiza achibale okhulupirika. Pa nthawiyi m’pamene amafunika kuwakonda komanso kuwalimbikitsa kuposa kale lonse. (Aheb. 10:24, 25) Nthawi zina achibale a munthu amene wachotsedwayo akhoza kumamva ngati akusalidwa mumpingo. Koma musamalole kuti azimva choncho. Achinyamata omwe makolo awo anasiya kutumikira Yehova amafunika kwambiri kuwayamikira komanso kuwalimbikitsa. w21.09 29 ¶13-14; 30 ¶16
Lolemba, August 14
Munthu wanzeru amamvetsera ndi kuphunzira malangizo owonjezereka.—Miy. 1:5.
Achikulire akamacheza ndi achinyamata, onse amalimbikitsana. (Aroma 1:12) Achinyamatanu, zimenezi zidzakuthandizani kutsimikiza kuti Yehova amasamalira atumiki ake okhulupirika, ndipo wachikulireyo adzaona kuti mumamukonda. Iye adzasangalala kukufotokozerani mmene Yehova wamudalitsira. Kukongola kumatha munthu akamakalamba. Koma kwa anthu amene amatumikira Yehova mokhulupirika, kukongola kwawo kumawonjezereka zaka zikamapita. (1 Ates. 1:2, 3) N’chifukwa chiyani zili choncho? Zili choncho chifukwa kwa zaka zambiri, iwo alola kuti mzimu wa Mulungu uziwaphunzitsa komanso kuwathandiza kukhala ndi makhalidwe abwino. Tikamayesetsa kuwadziwa bwino abale ndi alongo athu achikulire, kuwalemekeza komanso kuphunzira kuchokera kwa iwo, m’pamenenso timawaona kuti ndi chuma chamtengo wapatali. Mpingo umakhala wolimba kwambiri achinyamata akamaona kuti achikulire ndi ofunika komanso achikulirewo akamaona kuti achinyamata ndi ofunika. w21.09 7 ¶15-18
Lachiwiri, August 15
Lekani kuweruza ena kuti inunso musaweruzidwe, pakuti chiweruzo chimene mukuweruza nacho ena inunso mudzaweruzidwa nacho.—Mat. 7:1, 2.
Tiyenera kupewa kukhala ouma mtima n’kumayesetsa kukhala ‘achifundo chochuluka’ ngati Mulungu wathu. (Aef. 2:4) Chifundo sichitanthauza kungomvera anthu ena chisoni. M’malomwake anthu achifundo amachitapo kanthu pofuna kuthandiza ena. Choncho tonsefe tizikhala tcheru kuti tidziwe zimene anthu a m’banja lathu, mumpingo kapena m’dera lathu akufunikira. Kunena zoona, tili ndi mipata yambiri imene tingasonyezere ena chifundo. Kodi pali munthu wina amene akufunika kulimbikitsidwa? Kodi tingamuthandize mwina pomupatsa chakudya kapena kumuchitira zinthu zosonyeza kuti timamuganizira? Kodi pali Mkhristu amene wangobwezeretsedwa kumene yemwe angafunike kumutonthoza komanso kumulimbikitsa? Kodi tingauze ena uthenga wabwino wolimbikitsa? (Yobu 29:12, 13; Aroma 10:14, 15; Yak. 1:27) Ngati titakhala tcheru, tingaone kuti pali mipata yambiri imene tingasonyezere chifundo kwa ena. Tikamasonyeza chifundo, timasangalatsa kwambiri Atate wathu wakumwamba yemwe ndi Mulungu “wachifundo chochuluka.” w21.10 13 ¶20-22
Lachitatu, August 16
Yehova ndi M’busa wanga. Sindidzasowa kanthu.—Sal. 23:1.
Mu Salimo 23, Davide anatchula zinthu zimene ndi zofunika kwambiri monga madalitso amene Yehova ankamupatsa chifukwa anali M’busa wake. Iye ananena kuti Yehova ankamutsogolera “m’tinjira tachilungamo” ndiponso kumuthandiza mokhulupirika pa nthawi imene zinthu zinali bwino komanso pa mavuto. Iye ankadziwa kuti kukhala “m’mabusa a msipu wambiri” a Yehova, sikunkatanthauza kuti sazikumana ndi mavuto. Ankadziwanso kuti nthawi zina angakumane ndi zofooketsa, zomwe anaziyerekezera ndi kuyenda “m’chigwa cha mdima wandiweyani,” ndiponso kuti adzakhala ndi adani. Koma popeza Yehova anali M’busa wake, Davide ‘sakanaopa kanthu.’ Kodi Davide ‘sanasowe chilichonse’ m’njira yotani? Iye anali ndi chilichonse chimene chikanamuthandiza kukhala pa ubwenzi wabwino ndi Yehova. Kuti akhale wosangalala sizinkadalira kuti akhale ndi zinthu zambiri. Davide ankakhutira ndi zimene Yehova ankamupatsa. Chofunika kwambiri kwa iye chinali madalitso komanso chitetezo zochokera kwa Mulungu. Kuchokera pa mawu a Davidewa tingaone kufunika koona moyenera zinthu zimene tingakhale nazo. w22.01 3-4 ¶5-7
Lachinayi, August 17
Aliyense payekha adzalandira mphoto yake mogwirizana ndi ntchito yake.—1 Akor. 3:8.
Atumiki akale a Yehova ankakumananso ndi anthu omwe sankamvetsera uthenga wawo. Mwachitsanzo, Nowa anali “mlaliki wa chilungamo,” mwina kwa zaka pafupifupi 40 kapena 50. (2 Pet. 2:5) N’zosakayikitsa kuti iye ankayembekezera kuti anthu ambiri amvetsera uthenga wake, koma Yehova sanamuuze kuti zimenezi ndi zomwe zidzachitike. M’malomwake, pouza Nowa kuti amange chingalawa, Mulungu anati: “Iweyo udzalowe m’chingalawacho limodzi ndi ana ako, mkazi wako, ndi akazi a ana ako.” (Gen. 6:18) Komanso poganizira kukula kwa chingalawa chomwe Mulungu anamuuza kuti amange, Nowa ayenera kuti anazindikira kuti ndi anthu ochepa okha omwe adzamvetsere uthenga wake. (Gen. 6:15) Ndipotu n’zimene zinachitikadi. Palibe ngakhale munthu mmodzi amene anamvetsera uthenga wa Nowa. (Gen. 7:7) Ndiye kodi Yehova anaona kuti Nowa sanagwire bwino ntchito yolalikira? Ayi. Yehova anasangalala ndi Nowa chifukwa anachita mokhulupirika zimene anamuuza.—Gen. 6:22. w21.10 26 ¶10-11
Lachisanu, August 18
Ndinali ndi zonse pochoka kuno, koma Yehova wandibweza wopanda kanthu.—Rute 1:21.
Tangoganizani mmene Rute anamvera Naomi atalankhula zimenezi. Iye anali atachita zonse zimene akanatha kuti athandize Naomi. Ankalira naye, kumutonthoza komanso anali atayenda naye masiku ambiri. Koma ngakhale kuti iye anachita zonsezi, Naomi ananena kuti: “Yehova wandibweza wopanda kanthu.” Ngakhale kuti Rute anali naye nthawi zonse, zimene Naomi analankhulazi zinasonyeza ngati sankayamikira zonse zimene Rute anamuchitira. Zimenezitu ziyenera kuti zinali zopweteka kwambiri kwa Rute. Koma iye anapitirizabe kumuthandiza Naomi. (Rute 1:3-18) Masiku anonso mlongo amene wakhumudwa akhoza kutilankhula zinthu zimene zingatipweteke mumtima, ngakhale kuti tachita zonse zimene tingathe kuti timuthandize. Koma zikatero sitiyenera kukhumudwa. Tiyenera kupitirizabe kumuthandiza n’kumapempha Yehova kuti atithandize kupeza njira yabwino yomutonthozera. (Miy. 17:17) Poyamba mlongo yemwe akufunika kuthandizidwa akhoza kukana kuti timuthandize. Komabe, chikondi chokhulupirika chingapangitse kuti tiyesetsebe kumuthandiza.—Agal. 6:2. w21.11 11 ¶17-19
Loweruka, August 19
Inunso khalani oyera m’makhalidwe anu onse.—1 Pet. 1:15.
M’Baibulo mawu akuti “kukhala woyera” kapena “chiyero,” nthawi zambiri amanena za kukhala wosaipitsidwa kapena wopatulika m’makhalidwe komanso pa nkhani zachipembedzo. Mawu amenewa anganenenso za zinthu kapena munthu amene wapatulidwa kuti atumikire Mulungu. Tingaonedwe kuti ndife oyera ngati tili ndi makhalidwe abwino, timalambira Yehova movomerezeka komanso ngati tili pa ubwenzi wabwino ndi iye. Timasowa chonena tikaganizira mfundo yakuti tingathe kukhala pa ubwenzi wabwino ndi Yehova yemwe ndi woyera komanso tikaganizira zimene Baibulo limanena zokhudza chiyero chake. Yehova ndi woyera pa chilichonse. Timadziwa zimenezi chifukwa cha zimene ananena aserafi, amene ndi angelo ake omwe amakhala pafupi ndi mpando wake wachifumu. Pa nthawi ina, aserafi ena analengeza kuti: “Woyera, woyera, woyera ndiye Yehova wa makamu.” (Yes. 6:3) Ndipotu kuti akhale pa ubwenzi wabwino ndi Mulungu wawo yemwe ndi woyera, angelo amafunika kuti nawonso akhale oyera, ndipo ndi mmene alilidi. w21.12 3 ¶4-5
Lamlungu, August 20
Samalani kwambiri kuti mmene mukuyendera si monga anthu opanda nzeru, koma ngati anzeru. Muzigwiritsa ntchito bwino nthawi yanu.—Aef. 5:15, 16.
Nthawi zambiri achinyamata amaganizira zimene angachite kuti akhale ndi moyo wabwino. Aphunzitsi komanso achibale awo omwe si a Mboni, angamawalimbikitse kuti apite kuyunivesite n’cholinga choti adzagwire ntchito zapamwamba n’kumapeza ndalama zambiri. Komatu kuchita zimenezi kumafuna nthawi yochuluka. Makolo ndi anzawo mumpingo angamawalimbikitse kuti azichita zambiri potumikira Yehova. Ndiye kodi n’chiyani chingathandize wachinyamata yemwe amakonda Yehova kuti asankhe zochita mwanzeru? Iye angachite bwino kuwerenga komanso kuganizira mozama zimene zili pa Aefeso 5:15-17. Pambuyo powerenga mavesiwa, wachinyamatayo angachite bwino kudzifunsa kuti: ‘Kodi “chifuniro cha Yehova” n’chiyani? Kodi iye angasangalale kwambiri nditasankha ziti? Kodi ndi zosankha ziti zomwe zingachititse kuti ndizigwiritsa ntchito bwino nthawi?’ Kumbukirani kuti “masikuwa ndi oipa” ndipo dzikoli, lomwe wolamulira wake ndi Satana, liwonongedwa posachedwapa. w22.01 27 ¶5
Lolemba, August 21
Abale akewo sanali kumukhulupirira.—Yoh. 7:5.
Kodi ndi liti pamene Yakobo anakhala wotsatira wokhulupirika wa Yesu? Yesu ataukitsidwa “anaonekera kwa Yakobo, kenakonso kwa atumwi onse.”(1 Akor. 15:7) Kukumana kumeneku kunachititsa kuti Yakobo akhale wophunzira wa Yesu. Iye analipo pamene atumwi ankayembekezera kulandira mzimu woyera m’chipinda cha m’mwamba ku Yerusalemu. (Mac. 1:13, 14) Pambuyo pake iye anali ndi mwayi wotumikira m’bungwe lolamulira la mu nthawi ya atumwi. (Mac. 15:6, 13-22; Agal. 2:9) Ndipo pa nthawi ina chisanafike chaka cha 62 C.E., iye anauziridwa kulembera kalata Akhristu odzozedwa. Malangizo a m’kalatayo angatithandizenso masiku ano, kaya tikuyembekezera kudzapita kumwamba kapena kudzakhala padzikoli. (Yak. 1:1) Malinga ndi zimene ananena Josephus, wolemba mbiri wa mu nthawi ya atumwi, Yakobo anaphedwa Hananiya wamng’ono yemwe anali mkulu wa ansembe wa Chiyuda atalamula. Yakobo anakhalabe wokhulupirika, mpaka pamene anamaliza moyo wake wapadzikoli. w22.01 8 ¶3; 9 ¶5
Lachiwiri, August 22
Mulungu wanga, Mulungu wanga, mwandisiyiranji ine?—Mat. 27:46.
Chinthu chimodzi chimene tikuphunzira mulemba laleroli ndi chakuti sitimayembekezera kuti Yehova azititeteza kuti tisakumane ndi mavuto amene angayese chikhulupiriro chathu. Mofanana ndi Yesu, yemwe anayesedwa mokwanira ifenso tizikhala okonzeka kukhalabe okhulupirika ngakhale pamene anthu akufuna kutipha. (Mat. 16:24, 25) Komabe tiyenera kukhala otsimikiza kuti Mulungu sadzatisiya kuti tiyesedwe mpaka kufika poti sitingathenso kupirira. (1 Akor. 10:13) Chinthu china chimene tikuphunzirapo ndi chakuti mofanana ndi Yesu, ifenso tingachitiridwe zinthu zopanda chilungamo. (1 Pet. 2:19, 20) Anthu amene amatitsutsa angatichitire zinthu zopanda chilungamo osati chifukwa choti talakwitsa zinazake koma chifukwa chakuti sitili mbali ya dzikoli komanso timachitira umboni choonadi. (Yoh. 17:14; 1 Pet. 4:15, 16) Yesu ankamvetsa chifukwa chake Yehova analola kuti akumane ndi mavuto. Koma mosiyana ndi Yesu, atumiki ena okhulupirika a Yehova amadabwa kuti n’chifukwa chiyani iye amalola kuti iwo akumane ndi zinthu zina. (Hab. 1:3) Koma Mulungu wathu yemwe ndi wachifundo komanso woleza mtima amamvetsa ndipo saona kuti atumiki akewo alibe chikhulupiriro, koma amangofunika kuwalimbikitsa.—2 Akor. 1:3, 4. w21.04 11 ¶9-10
Lachitatu, August 23
Pemphero langa likhale lokonzedwa ngati zofukiza pamaso panu.—Sal. 141:2.
Yehova amavomereza zimene timachita pomulambira ngati zikugwirizana ndi cholinga chake ndipo tikuzichita chifukwa chomukonda komanso kumulemekeza. Timadziwa kuti Yehova ayenera kulambiridwa ndipo tiyenera kumulambira m’njira yabwino kwambiri. Njira imodzi yomwe timamulambirira ndi kupemphera kwa iye. Malemba amayerekezera mapemphero athu ndi zofukiza zomwe zinkakonzedwa bwino n’kukaperekedwa kuchihema. Zofukizazo zinkasangalatsa Mulungu. Mofanana ndi zimenezi mapemphero athu ochokera pansi pa mtima amakhala ‘osangalatsa’ kwa iye, ngakhale titagwiritsa ntchito mawu osavuta. (Miy. 15:8; Deut. 33:10) Yehova amasangalala kumvetsera mapemphero athu osonyeza kuti timamukonda komanso kumuyamikira. Iye amafuna kuti tizimufotokozera nkhawa zathu, chikhulupiriro chathu komanso zimene timalakalaka. Ndiye musanapemphere kwa Yehova, bwanji osaganizira kaye zimene mukufuna kunena m’pemphero? Mukamachita zimenezi mudzapereka “zofukiza” zabwino kwambiri kwa Atate wanu wakumwamba. w22.03 20 ¶2; 21 ¶7
Lachinayi, August 24
Pa nthawi imene Ambuye Yesu adzaonekere kuchokera kumwamba limodzi ndi angelo ake amphamvu . . . , inuyo amene panopo mukuvutika mudzapeza mpumulo pamodzi nafe.—2 Ates. 1:7.
Pa Aramagedo, si ife amene tidzasankhe anthu amene Yehova adzawachitire chifundo kapena ayi. (Mat. 25:34, 41, 46) Kodi tidzakhulupirira kuti Yehova waweruza moyenera kapena tidzakhumudwa? Kunena zoona, tiyenera kumakhulupirira Yehova panopa kuti tidzathe kumukhulupiriranso kwambiri m’tsogolo. Tangoganizani mmene tidzamvere m’dziko latsopano. Sipadzakhalanso chipembedzo chonyenga, amalonda adyera komanso maboma andale omwe akhala akupondereza anthu n’kubweretsa mavuto ochuluka kwa zaka zambiri. Matenda, ukalamba komanso imfa ya anthu amene timawakonda sizidzakhalanso mbali ya moyo wathu wa tsiku ndi tsiku. Satana ndi ziwanda adzamangidwa kwa zaka 1,000. Zoipa zomwe zinabwera chifukwa cha kusamvera kwawo zidzatha. (Chiv. 20:2, 3) Tidzasangalala kwambiri poona kuti tinakhulupirira mmene Yehova amachitira zinthu. w22.02 6-7 ¶16-17
Lachisanu, August 25
Odala ndi anthu amene amabweretsa mtendere.—Mat. 5:9.
Yesu ankayamba ndi iyeyo kuchita zinthu mwamtendere ndipo ankalimbikitsa ena kuti azithetsa kusamvana pakati pawo. Iye anaphunzitsa kuti munthu ayenera kukhazikitsa mtendere ndi m’bale wake kuti Mulungu azivomereza kulambira kwake. (Mat. 5:23, 24) Ndipo mobwerezabwereza anathandiza atumwi ake kuti asamakangane pa nkhani yakuti wamkulu ndani pakati pawo. (Luka 9:46-48; 22:24-27) Kuti tizikhala mwamtendere ndi ena, tiyenera kuchita zambiri osati kungopewa kuyambitsa mikangano. Tiyenera kuyesetsa kuti tizikhala mwamtendere komanso kulimbikitsa abale ndi alongo kuti azithetsa kusamvana pakati pawo. (Afil. 4:2, 3; Yak. 3:17, 18) Tingadzifunse kuti: ‘Kodi ndingalolere kudzimana zinthu zina kuti ndikhale pamtendere ndi ena? M’bale kapena mlongo akandikhumudwitsa, kodi ndimasunga chakukhosi? Kodi ndimadikira kuti ayambe ndi munthu winayo kukhazikitsa mtendere kapena ndimayamba ndi ineyo kuchitapo kanthu ngakhale zikuoneka kuti winayo ndi amene walakwitsa?’ w22.03 10 ¶10-11
Loweruka, August 26
Kupatsa kumabweretsa chimwemwe chochuluka kuposa kulandira.—Mac. 20:35.
Kalero, Baibulo linaneneratu kuti anthu a Mulungu “adzadzipereka mofunitsitsa” potumikira Yehova motsogoleredwa ndi Mwana wake. (Sal. 110:3) Ulosi umenewu ukukwaniritsidwa masiku ano. Chaka chilichonse atumiki akhama a Yehova, amalalikira kwa maola ambiri. Iwo amachita zimenezi mwakufuna kwawo ndipo amagwiritsa ntchito zinthu zawo. Amathandizanso abale ndi alongo awo kupeza zimene akufunikira, kuwalimbikitsa komanso kuwathandiza kukhala pa ubwenzi wabwino ndi Yehova. Abale audindo amakhala maola ambiri akukonzekera mbali zimene apatsidwa pamisonkhano komanso kuchita maulendo aubusa kwa abale ndi alongo awo. Koma kodi n’chifukwa chiyani anthu a Yehova amachita zinthu zonsezi? N’chifukwa chakuti iwo amakonda Yehova komanso anzawo. (Mat. 22:37-39) Yesu anapereka chitsanzo chabwino kwambiri poika patsogolo zofuna za ena m’malo mwa zofuna zake. Timachita zonse zomwe tingathe pomutsanzira. (Aroma 15:1-3) Anthu omwe amayesetsa kumutsanzira adzapeza madalitso. w22.02 20 ¶1-2
Lamlungu, August 27
Malipiro a munthu waganyu asagone m’nyumba mwako kufikira m’mawa.—Lev. 19:13.
Munthawi ya Aisiraeli, anthu omwe alembedwa ganyu yakumunda ankapatsidwa malipiro pakutha pa tsiku. Kusapatsa waganyu malipiro ake kukanachititsa kuti iye alephere kupezera chakudya banja lake pa tsikulo. Yehova anafotokoza kuti: ‘Iye ndi wovutika ndipo akuyembekezera malipiro akewo.’ (Deut. 24:14, 15; Mat. 20:8) Masiku ano, ogwira ntchito ambiri amapatsidwa malipiro awo kamodzi kapena kawiri pamwezi, osati tsiku lililonse. Komabe, mfundo ya pa Levitiko 19:13, imagwirabe ntchito. Mabwana ena amapondereza antchito awo powapatsa malipiro ochepa kwambiri. Iwo amadziwa kuti antchitowo palibe chomwe angachite koma kupitirizabe kugwira ntchitoyo ngakhale kuti amalandira malipiro ochepa. Akamachita zimenezi, zimakhala ngati malipiro a waganyu ‘akugona m’nyumba mwawo.’ Mkhristu yemwe amalemba ena ntchito, ayenera kuonetsetsa kuti akuwachitira zinthu mwachilungamo. w21.12 10 ¶9-10
Lolemba, August 28
Ndikumva ludzu.—Yoh. 19:28.
Pambuyo poti Yesu wakumana ndi mavuto osiyanasiyana kuphatikizaponso kumva ululu pamtengo wozunzikirapo, iye ayenera kuti analidi ndi ludzu choncho ankafunika munthu wina kuti amuthandize kuti athetse ludzu lakelo. Yesu sankaona kuti aoneka wofooka akafotokoza mmene ankamvera. Ifenso sitiyenera kuona choncho. N’kutheka kuti nthawi zambiri sitimakonda kuuza anthu ena zimene tikufunikira. Koma ngati pa nthawi ina titadzaona kuti tikufunika thandizo, tisadzanyalanyaze kupempha ena kuti atithandize. Mwachitsanzo, ngati ndife wachikulire kapena tikudwala, tingapemphe mnzathu kuti atiperekeze kukagula zinthu kapena kukaonana ndi adokotala. Ngati takhumudwa kapena kufooka ndi zinazake, tizifotokozera mkulu kapena Mkhristu wolimba mwauzimu n’cholinga choti atimvetsere komanso kutilimbikitsa ndi “mawu abwino.” (Miy. 12:25) Tizikumbukira kuti abale ndi alongo athu amatikonda ndipo amafuna kutithandiza tikakumana ndi mavuto. (Miy. 17:17) Koma si kuti iwo amadziwa zimene zili m’maganizo mwathu. Iwo sangadziwiretu ngati tikufunika kuti munthu winawake atithandize pokhapokha ngati tawafotokozera. w21.04 11-12 ¶11-12
Lachiwiri, August 29
Ukafooka pa tsiku la masautso, mphamvu zako zidzakhala zochepa.—Miy. 24:10.
Ambirife timavutika zinthu zikasintha. Ena omwe akhala akuchita utumiki wa nthawi zonse kwa nthawi yaitali, utumiki wawo unasintha. Chifukwa cha uchikulire, ena anafunika kusiya utumiki womwe ankaukonda. Si zachilendo kukhala wokhumudwa zinthu zikasintha chonchi pa moyo wathu. N’zosavuta kuvomereza zinthu zikasintha ngati tikuona zinthu mmene Yehova akuzionera. Iye akuchita zinthu zambiri masiku ano, ndipo tili ndi mwayi waukulu wokhala antchito anzake. (1 Akor. 3:9) Yehova sasiya kutikonda. Choncho ngati kusintha kwina m’gululi kwakukhudzani, musamachedwe n’kuganizira chifukwa chake zinthu zasintha choncho. M’malo momalakalaka ‘zinthu zakale’ muzipemphera kwa Yehova n’kumaona zabwino zomwe zachitika chifukwa cha kusinthako. (Mlal. 7:10) Tiyenera kukhalabe ndi maganizo oyenera. Tikamatero tidzapitiriza kukhala osangalala komanso okhulupirika ngakhale zinthu zitasintha pa moyo wathu. w22.03 17 ¶11-12
Lachitatu, August 30
Yehova, Yehova, Mulungu . . . . Wosungira mibadwo masauzande kukoma mtima kosatha.—Eks. 34:6, 7.
Kodi Yehova amasonyeza kwa ndani chikondi chokhulupirika? Baibulo limasonyeza kuti anthufe timakonda zinthu zosiyanasiyana monga “ulimi,” “vinyo ndi mafuta,” “malangizo,” “kudziwa zinthu,” “nzeru” komanso zinthu zina. (2 Mbiri 26:10; Miy. 12:1; 21:17; 29:3) Komabe chikondi chokhulupirika chimasonyezedwa kwa anthu okha osati ku zinthu zina. Ndipo sikuti Yehova amasonyeza chikondichi kwa wina aliyense. M’malomwake amachisonyeza kwa anthu okhawo amene ali pa ubwenzi wabwino ndi iye. Mulungu wathu ndi wokhulupirika kwa anthu amene ndi mabwenzi ake. Iye wawakonzera zinthu zabwino m’tsogolo ndipo sadzasiya kuwakonda. Yehova anasonyeza chikondi kwa anthu onse. Yesu anauza munthu wina dzina lake Nikodemo kuti: “Mulungu anakonda kwambiri dziko [kapena kuti anthu] mwakuti anapereka Mwana wake wobadwa yekha, kuti aliyense wokhulupirira iye asawonongeke, koma akhale ndi moyo wosatha.”—Yoh. 3:1, 16; Mat. 5:44, 45. w21.11 2 ¶3; 3 ¶6-7
Lachinayi, August 31
Ngati inu mudzapirire, mudzapeza moyo.—Luka 21:19.
Masiku ano moyo ndi wovuta ndiponso mwina tikhoza kukumana ndi mavuto aakulu m’tsogolomu. (Mat. 24:21) Tikuyembekezera mwachidwi nthawi imene zonsezi zidzatha, sizidzakumbukiridwanso ndipo sizidzachitikanso. (Yes. 65:16, 17) Choncho tiyenera kuphunzira zimene tingachite kuti tizipirira kwambiri. Chifukwa chiyani? Chifukwa Yesu ananena kuti: “Ngati inu mudzapirire, mudzapeza moyo.” (Luka 21:19) Kuganizira zimene zikuthandiza ena kupirira mavuto ofanana ndi amene ife tikukumana nawo, kungatithandize kuti tizipirira kwambiri. Kodi chitsanzo chabwino kwambiri pankhani ya kupirira ndi ndani? Yehova Mulungu. Kodi zimenezi zikukudabwitsani? Mwina n’kutheka. Koma mutaganizira nkhaniyi mungamvetse chifukwa chake tikutero. Mdyerekezi ndi amene akulamulira dzikoli, ndipo lili ndi mavuto adzaoneni. Yehova ali ndi mphamvu zoti akhoza kuthetsa mavutowa panopa, koma akudikira tsiku loti adzachite zimenezi. (Aroma 9:22) Mulungu wathu akupitirizabe kupirira mpaka nthawi imene anakhazikitsa itafika. w21.07 8 ¶2-4