Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • es23 tsamba 88-97
  • September

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • September
  • Kuphunzira Malemba Tsiku ndi Tsiku—2023
  • Timitu
  • Lachisanu, September 1
  • Loweruka, September 2
  • Lamlungu, September 3
  • Lolemba, September 4
  • Lachiwiri, September 5
  • Lachitatu, September 6
  • Lachinayi, September 7
  • Lachisanu, September 8
  • Loweruka, September 9
  • Lamlungu, September 10
  • Lolemba, September 11
  • Lachiwiri, September 12
  • Lachitatu, September 13
  • Lachinayi, September 14
  • Lachisanu, September 15
  • Loweruka, September 16
  • Lamlungu, September 17
  • Lolemba, September 18
  • Lachiwiri, September 19
  • Lachitatu, September 20
  • Lachinayi, September 21
  • Lachisanu, September 22
  • Loweruka, September 23
  • Lamlungu, September 24
  • Lolemba, September 25
  • Lachiwiri, September 26
  • Lachitatu, September 27
  • Lachinayi, September 28
  • Lachisanu, September 29
  • Loweruka, September 30
Kuphunzira Malemba Tsiku ndi Tsiku—2023
es23 tsamba 88-97

September

Lachisanu, September 1

Anam’pempha kuti awaonetse chizindikiro chochokera kumwamba.—Mat. 16:1.

Anthu ena m’nthawi ya Yesu sanakhutire ndi zimene iye ankaphunzitsa moti ankafuna kuti achitenso zinthu zina. Koma Yesu atakana kuwasonyeza chizindikiro chomwe ankafunacho, anakhumudwa ndipo anakana kumukhulupirira. (Mat. 16:4) Kodi Malemba amati chiyani? Ponena za Mesiya, mneneri Yesaya analemba kuti: “Iye sadzafuula kapena kukweza mawu ake, ndipo mawu ake sadzamvedwa mumsewu.” (Yes. 42:1, 2) Pa utumiki wake, Yesu ankachita zinthu modzichepetsa. Iye sanamange akachisi ogometsa, ndiponso sankavala zovala zapadera zachipembedzo kapena kufuna kuti anthu azimuitana ndi maina aulemu achipembedzo. Pa nthawi imene ankaimbidwa mlandu, Yesu anakana kuchita chozizwitsa pongofuna kusangalatsa Mfumu Herode. (Luka 23:8-11) N’zoona kuti Yesu ankachita zozizwitsa, koma cholinga chake chachikulu chinali kulengeza uthenga wabwino. Iye anauza ophunzira ake kuti chimenechi “ndicho cholinga chimene ndinabwerera.”​—Maliko 1:38. w21.05 4 ¶9-10

Loweruka, September 2

Pakuti moyo wosatha adzaupeza akamaphunzira ndi kudziwa za inu, Mulungu yekhayo amene ali woona, ndi za Yesu Khristu, amene inu munamutuma.​—Yoh. 17:3.

Timafufuza anthu ‘omwe ali ndi maganizo abwino amene angawathandize kukapeza moyo wosatha.’ (Mac. 13:48) Kuti anthu amenewa akhale ophunzira a Yesu, tiyenera kuwathandiza (1) kumvetsa, (2) kukhulupirira komanso (3) kugwiritsa ntchito zimene aphunzira m’Baibulo. (Akol. 2:6, 7; 1 Ates. 2:13) Aliyense mumpingo angathandize ophunzira Baibulo powasonyeza chikondi komanso kuwalandira ndi manja awiri akabwera kumisonkhano. (Yoh. 13:35) Mphunzitsiyo amafunika khama komanso nthawi yambiri kuti athandize wophunzirayo kusiya miyambo ndi zikhulupiriro zimene ‘zinazikika molimba’ mwa iye. (2 Akor. 10:4, 5) Pangadutse miyezi yambiri kuti munthu asinthe moyo wake n’kufika poyenerera kuti abatizidwe. Koma kusintha kumeneko n’kothandiza kwambiri. w21.07 3 ¶6

Lamlungu, September 3

Tsimikizirani zinthu zonse. Gwirani mwamphamvu chimene chili chabwino.​—1 Ates. 5:21.

Kodi ifeyo timakhulupirira ndi mtima wonse kuti zimene timaphunzitsa ndi choonadi, komanso kuti njira imene a Mboni za Yehova amalambirira Mulungu ndi imene ili yovomerezeka kwa Yehova? Mtumwi Paulo sankakayikira ngakhale pang’ono kuti zomwe ankakhulupirira ndi choonadi. (1 Ates. 1:5) Sikuti ankakhulupirira zimenezi chifukwa chakuti zinkangomusangalatsa. M’malomwake, iye ankaphunzira Mawu a Mulungu mwakhama kwambiri ndipo ankakhulupirira kuti “Malemba onse anauziridwa ndi Mulungu.” (2 Tim. 3:16) Ndiye kodi zimene ankaphunzira zinamuthandiza kuzindikira chiyani? M’Malemba, Paulo anapeza umboni wosatsutsika wakuti Yesu anali Mesiya yemwe Mulungu analonjeza, umboni womwe atsogoleri achipembedzo cha Chiyuda ankaukana. Atsogoleri achinyengowa ankanena kuti amaphunzitsa zoona zokhudza Mulungu koma ankamukana m’zochita zawo. (Tito 1:16) Mosiyana ndi anthuwa, Paulo sankachita kusankha mbali ya Mawu a Mulungu yoti azikhulupirira. Iye ankaphunzitsa komanso kutsatira “chifuniro chonse cha Mulungu.”​—Mac. 20:27. w21.10 18 ¶1-2

Lolemba, September 4

Palibe munthu angabwere kwa ine akapanda kukokedwa ndi Atate amene anandituma ine.​—Yoh. 6:44.

Tikamadzala komanso kuthirira mbewu za choonadi, tisamaiwale kuti Mulungu ndi amene amakulitsa. (1 Akor. 3:6, 7) Yehova amaona kuti moyo wa munthu aliyense ndi wamtengo wapatali. Iye watipatsa mwayi wogwira ntchito ndi Mwana wake posonkhanitsa anthu kuchokera m’mitundu yonse mapeto asanafike. (Hag. 2:7) Ntchito yathu yolalikira tingaiyerekezere ndi ntchito yopulumutsa anthu. Timakhala ngati tikugwira ntchito yopulumutsa anthu omwe akwiririka mumgodi. Ngakhale kuti pangapezeke opulumuka ochepa kwambiri, onse m’gulu la opulumutsa anthulo amakhala kuti agwira ntchito yofunika kwambiri. Zimenezi ndi zofanana ndi zimene timachita pa ntchito yathu yolalikira. Sitingadziwe kuti ndi anthu angati amene tingawapulumutse m’dziko loipa la Satanali, koma Yehova akhoza kugwiritsa ntchito aliyense wa ife powathandiza. Andreas yemwe amakhala ku Bolivia ananena kuti, “Ndimaona kuti munthu akaphunzira Baibulo mpaka kubatizidwa, zimakhala kuti ndi khama la anthu ambiri osati munthu mmodzi.” Choncho tiyeni ifenso tizikhala ndi maganizo ngati amenewa pa ntchito yathu yolalikira. Tikamachita zimenezi, Yehova adzatidalitsa ndipo tizisangalala kwambiri ndi ntchito yathu yolalikira. w21.05 19 ¶19-20

Lachiwiri, September 5

Kuti awonjoke mumsampha wa Mdyerekezi.​—2 Tim. 2:26.

Mlenje amakhala ndi cholinga chimodzi chomwe ndi kugwira kapena kupha nyama. Mogwirizana ndi zimene ananena mmodzi wa anzake a Yobu omwe anabwera kudzamufooketsa, mlenje amagwiritsa ntchito misampha yosiyanasiyana. (Yobu 18:8-10) Kodi iye amanyengerera bwanji nyama kuti igwidwe mumsampha wake? Amaiyang’anitsitsa kuti adziwe zimene imachita. Amaganizira kuti, ‘Kodi imakonda kupita kuti? Imakonda chiyani? Kodi ndi msampha uti umene ungaigwire mosavuta?’ Satana ali ngati mlenje ameneyu. Iye amatiyang’anitsitsa kuti adziwe zimene timachita, kumene timakonda kupita komanso zimene zimatisangalatsa. Kenako amatiikira msampha umene ungatigwire tisakudziwa. Komabe Baibulo limatitsimikizira kuti ngati tingagwidwe mumsampha wa Satana, tikhoza kupulumuka. Limatithandizanso kudziwa zimene tingachite kuti tipewe kukodwa m’misampha yakeyi. Misampha iwiri imene Satana amakonda kugwiritsa ntchito ndi kunyada komanso dyera kapena kuti kusirira kwa nsanje. Kwa zaka zambiri Satana wakhala akugwiritsa ntchito makhalidwe awiri amenewa posokoneza anthu. Iye ali ngati wosaka mbalame amene amazinyengerera kuti azigwire pamsampha kapena pogwiritsa ntchito ukonde. (Sal. 91:3) Koma ife sitiyenera kukodwa m’misampha ya Satana. N’chifukwa chiyani tikutero? Tikutero chifukwa Yehova watidziwitsa misampha imene Satana amagwiritsa ntchito.​—2 Akor. 2:11. w21.06 14 ¶1-2

Lachitatu, September 6

Imvi ndizo chisoti chachifumu cha ulemerero zikapezeka m’njira yachilungamo.​—Miy. 16:31.

Abale ndi alongo athu achikulire okhulupirika ndi chuma chamtengo wapatali. Mawu a Mulungu amayerekezera imvi zawo ndi chisoti chachifumu. (Miy. 20:29) Komabe mwina nthawi zina sitingazindikire chuma chimenechi. Achinyamata amene amazindikira kuti achikulire ndi ofunika, angapeze zinthu zamtengo wapatali kwambiri kuposa chuma chenicheni. Achikulire okhulupirika ndi amtengo wapatali kwa Yehova Mulungu. Iye amaona zimene zili mumtima mwawo komanso amadziwa makhalidwe awo abwino. Yehova amasangalala achikulirewa akamathandiza achinyamata ndi nzeru zimene apeza pa zaka zambiri zimene akhala akumutumikira mokhulupirika. (Yobu 12:12; Miy. 1:1-4) Iye amayamikiranso kupirira kwawo. (Mal. 3:16) Abale ndi alongo amenewa akhala akukumana ndi mavuto osiyanasiyana koma sanasiye kutumikira Yehova. Panopa chiyembekezo chawo ndi champhamvu kwambiri kuposa pa nthawi imene anayamba kuphunzira choonadi. Ndipo Yehova amawakonda chifukwa akupitirizabe kulalikira za dzina lake ‘ngakhale achita imvi,’ kapena kuti ndi achikulire.​—Sal. 92:12-15. w21.09 2 ¶2-3

Lachinayi, September 7

Aliyense payekha ayese ntchito yake, kuti aone kuti ndi yotani. Akatero adzakhala ndi chifukwa chosangalalira ndi ntchito yake.​—Agal. 6:4.

Nthawi ndi nthawi tingachite bwino kumafufuza zolinga zathu. Tingadzifunse kuti: ‘Kodi ndimamva bwino mumtima pokhapokha ndikaona kuti ndimaposa anthu ena pa zinthu zinazake? Kodi ndimachita khama mumpingo n’cholinga choti anthu andione kuti ndine wabwino kwambiri kuposa m’bale kapena mlongo winawake? Kapena ndimachita khama chifukwa chofuna kusangalatsa Yehova?’ Baibulo limatiuza kuti tisamadziyerekezere ndi ena. Chifukwa chiyani? Chifukwa tikayamba kuganiza kuti timaposa m’bale wathu tingayambe kunyada. Ndipo chifukwa china n’chakuti tikamadziona kuti ndife osafunika chifukwa choti ena akutiposa, tingafooke. (Aroma 12:3) Tizikumbukira kuti Yehova anatikokera kwa iye, osati chifukwa choti ndife okongola, odziwa kulankhula kapena ndife otchuka, koma chifukwa choti timafunitsitsa kumukonda komanso kumvera Mwana wake.​—Yoh. 6:44; 1 Akor. 1:26-31. w21.07 14-15 ¶3-4

Lachisanu, September 8

Munaphunzitsidwa kuti mukhale atsopano mu mphamvu yoyendetsa maganizo anu.​—Aef. 4:23.

Kuti tisinthe maganizo athu tiyenera kumapemphera, kuphunzira Mawu a Mulungu komanso kuganizira mozama zimene taphunzirazo. Nthawi zonse muzichita zimenezi ndipo muzipempha Yehova kuti akupatseni mphamvu. Mzimu wake woyera udzakuthandizani kuchotsa maganizo alionse odziyerekezera ndi ena. Iye adzakuthandizani kuti mudziwe ngati mwayamba kukhala ndi mtima wansanje kapena wonyada ndipo adzakuthandizani kuti musinthe mwamsanga. (2 Mbiri 6:29, 30) Yehova amadziwa mtima wathu. Iye amadziwanso mavuto amene timalimbana nawo monga zinthu zoipa za m’dzikoli zimene zingatisokoneze komanso zimene timalakwitsa chifukwa chakuti si ife angwiro. Yehova akamaona zimene timachita poyesetsa kulimbana ndi mavuto amenewa, amayamba kutikonda kwambiri. Pofuna kutithandiza kumvetsa kuti amatikonda kwambiri, Yehova anagwiritsa ntchito chitsanzo cha chikondi chimene chimakhalapo pakati pa mayi ndi mwana wake. (Yes. 49:15) N’zolimbikitsa kudziwa kuti Yehova amatikonda kwambiri chonchi akationa tikuyesetsa kulimbana ndi mavuto n’cholinga choti tizimutumikira ndi mtima wonse. w21.07 24-25 ¶17-19

Loweruka, September 9

Sangalalani ndi anthu amene akusangalala.​—Aroma 12:15.

Tingamasangalale kwambiri ngati titakhala akhama pa chilichonse chimene timachita potumikira Yehova. Nthawi zonse ‘tizitanganidwa kwambiri’ ndi ntchito yolalikira ndipo tizidzipereka ndi mtima wonse pogwira ntchito zamumpingo. (Mac. 18:5; Aheb. 10:24, 25) Muzikonzekera bwino misonkhano n’cholinga choti muzikapereka ndemanga zolimbikitsa. Muzikonzekeranso bwino mukapatsidwa nkhani za ophunzira pamisonkhano ya mkati mwa mlungu. Mukapemphedwa kuti mugwire ntchito inayake mumpingo, muzisunga nthawi komanso muzikhala odalirika. Musamaone kuti zimene mwapemphedwa n’zosafunika kapena kungotaya nthawi. Muziyesetsa kuwonjezera luso lanu. (Miy. 22:29) Mukamadzipereka kwambiri pa utumiki wanu, m’pamenenso mumapita patsogolo mofulumira ndipo mumasangalala. (Agal. 6:4) Zimenezi zingakuthandizeninso kuti muzisangalala ndi ena akapatsidwa utumiki umene inuyo mumaulakalaka.​—Agal. 5:26. w21.08 22 ¶11

Lamlungu, September 10

Nzeru yochokera kumwamba, choyamba, ndi yoyera, kenako yamtendere, yololera, yokonzeka kumvera, yodzaza ndi chifundo ndi zipatso zabwino, yopanda tsankho, ndiponso yopanda chinyengo.—Yak. 3:17.

Tizipewa kunyada ndipo tizikhala ophunzitsika. Mofanana ndi matenda ena omwe angachititse kuti mtima uzivutika kugwira bwino ntchito, kunyada kungachititsenso kuti tizivutika kumvera malangizo a Yehova. Afarisi anali onyada moti anakana kuvomereza umboni woonekeratu wakuti Yesu ankatsogoleredwa ndi mzimu woyera komanso kuti anali Mwana wa Mulungu. (Yoh. 12:37-40) Zimenezi zinali zoopsa chifukwa zinalepheretsa kuti adzapeze moyo wosatha. (Mat. 23:13, 33) Choncho n’zofunika kwambiri kuti tizilola Mawu a Mulungu ndi mzimu wake woyera kutithandiza kusintha makhalidwe athu, maganizo athu komanso zimene timasankha. Popeza kuti Yakobo anali wodzichepetsa, analola kuphunzitsidwa ndi Yehova. Ndipo chifukwa cha kudzichepetsa kwake, iye anakhala mphunzitsi waluso. w22.01 10 ¶7

Lolemba, September 11

Pemphanibe.​—Mat. 7:7.

‘Tikalimbikira kupemphera,’ tingakhale otsimikiza kuti Atate wathu wakumwamba adzamva komanso kuyankha mapemphero athu. (Akol. 4:2) Ngakhale tingaone ngati akuchedwa kuyankha, Yehova akulonjeza kuti adzatiyankha “pa nthawi imene tikufunika thandizo.” (Aheb. 4:16) N’chifukwa chake sitikuyenera kumuimba mlandu ngati zinazake sizinachitike msanga ngati mmene timaganizira. Mwachitsanzo anthu ambiri akhala akupemphera kuti Ufumu wa Mulungu ubwere kuti udzathetse dziko loipali. Ndipotu Yesu anatiuza kuti tizitchula zimenezi m’mapemphero athu. (Mat. 6:10) Choncho kungakhaletu kupusa kwambiri ngati munthu angalole kuti chikhulupiriro chake chichepe chifukwa chakuti mapeto sanafike pa nthawi imene anthu amayembekezera. (Hab. 2:3; Mat. 24:44) Tingasonyeze kuti ndife anzeru tikamayembekezera Yehova moleza mtima komanso kupemphera kwa iye n’kumakhulupirira kuti ayankha mapemphero athu. Mapeto adzafika pa nthawi yoyenera chifukwa Yehova anasankha kale ‘tsiku ndi ola’ limene mapetowa adzafike. Ndipo nthawi imeneyo idzakhala yabwino kwambiri kwa aliyense.​—Mat. 24:36; 2 Pet. 3:15. w21.08 10 ¶10-11

Lachiwiri, September 12

Modzichepetsa, [muziona] ena kukhala okuposani.—Afil. 2:3.

Akhristu odzichepetsa akamakula amazindikira kuti sangamachite zambiri ngati mmene ankachitira kale. Mwachitsanzo, taganizirani zimene zimachitikira oyang’anira madera. Iwo akafika zaka 70, amapemphedwa kuti ayambe utumiki wina. Zimenezi zingakhale zovuta. Iwo amakhala kuti ankasangalala kutumikira abale awo. Koma amamvetsa kuti zingakhale bwino achinyamata atapitiriza ntchitoyi. Akamachita zimenezi amasonyeza mtima umene Alevi ku Isiraeli anali nawo, omwe akafika zaka 50 ankafunika kusiya kutumikira pachihema. Sikuti chimwemwe cha Alevi achikulirewa chinkadalira utumiki umene ankachita. Ankachita zonse zimene angathe pa utumiki umene wapezeka komanso kuthandiza achinyamata. (Num. 8:25, 26) Masiku anonso abale amene anali oyang’anira madera ngakhale kuti sayenderanso mipingo, amathandiza komanso kulimbikitsa abale ndi alongo mumpingo wawo. w21.09 8-9 ¶3-4

Lachitatu, September 13

Bambo, ndachimwira kumwamba komanso ndachimwira inu. Sindilinso woyenera kutchedwa mwana wanu.​—Luka 15:21.

Yesu anafotokoza fanizo logwira mtima la mwana wolowerera lomwe lili pa Luka 15:11-32. Mnyamata wina anapandukira bambo ake n’kuchoka pakhomo ndipo anapita “kudziko lina lakutali.” Ali kumeneko analowerera m’makhalidwe oipa kwambiri. Koma atakumana ndi mavuto aakulu, anayamba kuganizira kwambiri za moyo wake. Anazindikira kuti ankakhala moyo wabwino kwambiri ali kunyumba ya bambo ake. Monga mmene Yesu ananenera, “nzeru zitam’bwerera” iye anaganiza zobwerera kwawo kukapempha bambo ake kuti amukhululukire. Chinthu chofunika kwambiri chimene anachita ndi kuzindikira kuti anachita zinthu zoipa kwambiri. Ankafunikanso kusintha khalidwe lake. Mwana wolowerera anasonyeza kulapa kochokera pansi pamtima pa zoipa zimene anachita. Nkhani imeneyi sikuti yangokhala yokhudza mtima basi. Koma mfundo zake zingathandizenso kwambiri akulu akamafuna kudziwa ngati munthu amene wachita tchimo lalikulu walapadi kuchokera pansi pamtima. w21.10 5 ¶14-15

Lachinayi, September 14

Ndigwedezanso kumwamba [ndi] dziko lapansi.​—Hag. 2:6.

Kodi n’chiyani chomwe sichidzagwedezeka kapena kuchotsedwa? Mtumwi Paulo analemba kuti: “Poona kuti tidzalandira ufumu umene sungagwedezeke, tiyeni . . . tichitire Mulungu utumiki wopatulika m’njira yovomerezeka, ndipo tiuchite moopa Mulungu komanso mwaulemu waukulu.” (Aheb. 12:28) Pambuyo pa kugwedeza komalizaku Ufumu wa Mulungu wokha ndi umene udzakhale wosagwedezeka. (Sal. 110:5, 6; Dan. 2:44) Panopa nthawi yatha. Anthu ayenera kusankha kuti, kodi apitiriza kuchita zinthu zimene dzikoli limalimbikitsa zomwe ndi zotsogolera kuchiwonongeko kapena asankha kumachita zinthu mogwirizana ndi zimene Mulungu amafuna zomwe zingachititse kuti adzapeze moyo wosatha? (Aheb. 12:25) Tikamagwira ntchito yolalikira, timathandiza anthu kuti asankhe zochita pa nkhani yofunika kwambiriyi. Tiyeninso tizikumbukira mawu a Ambuye wathu Yesu akuti: “Uthenga wabwino uwu wa ufumu udzalalikidwa padziko lonse lapansi kumene kuli anthu, kuti ukhale umboni ku mitundu yonse, kenako mapeto adzafika.”​—Mat. 24: 14. w21.09 19 ¶18-20

Lachisanu, September 15

Sindidzakusiyani kapena kukutayani ngakhale pang’ono.​—Aheb. 13:5.

Akulu, muli ndi udindo wapadera wotonthoza achibale a munthu amene wasiya kutumikira Yehova. (1 Ates. 5:14) Muziyesetsa kuwalimbikitsa misonkhano isanayambe komanso ikatha ndipo muziwayendera komanso kupemphera nawo limodzi. Muzilowa nawo mu utumiki kapenanso nthawi zina mungawaitane kuti adzakhale nawo pakulambira kwanu kwa pabanja. Akulu ayenera kusonyeza chikondi, chifundo ndiponso kusamalira nkhosa za Yehova zomwe zili ndi chisoni. (1 Ates. 2:7, 8) Yehova “safuna kuti wina aliyense adzawonongedwe, koma amafuna kuti anthu onse alape.” (2 Pet. 3:9) Ngakhale munthu atachita tchimo lalikulu, moyo wake umakhalabe wamtengo wapatali kwa Mulungu. Yehova anapereka nsembe ya dipo ya Mwana wake wokondedwa, yomwe ndi yokwera mtengo kwambiri kuti awombole anthu ochimwa. Mwachifundo iye amachita zonse zomwe angathe kuti athandize anthu ngati amenewa kubwerera kwa iye. Ndipo monga mmene fanizo la Yesu lonena za mwana wolowerera limasonyezera, Yehova amayembekezera kuti iwo achitadi zimenezo.​—Luka 15:11-32. w21.09 30-31 ¶17-19

Loweruka, September 16

Inu mwalowa kukapindula ndi ntchito imene iwo anaigwira mwamphamvu.​—Yoh. 4:38.

Bwanji ngati simungathe kuchita zambiri pa ntchito yolalikira ndi kuphunzitsa uthenga wabwino chifukwa cha kufooka kwa thanzi? Mukhoza kumasangalalabe ndi zimene mukukwanitsa kuchita pa ntchito yokolola. Taganizirani zimene zinachitika pamene Mfumu Davide ndi amuna omwe anali nawo anakapulumutsa mabanja awo ndi katundu wawo kwa Aamaleki. Amuna 200 anali atatopa kwambiri moti sakanatha kumenya nkhondo, choncho anatsala n’kumalondera katundu. Atapambana pa nkhondoyo, Davide analamula kuti onse agawane mofanana zinthu zomwe anafunkha kwa Aamaleki. (1 Sam. 30:21-25) Zimenezi ndi zofanana ndi zimene zimachitika pa ntchito yathu yophunzitsa anthu. Onse omwe achita zomwe angathe pa ntchitoyi amasangalala mofanana, munthu wina akayamba kuyenda panjira yopita kumoyo. Yehova amaona khama ndi zolinga zathu zabwino ndipo amadalitsa ntchito yathu. Amatiphunzitsanso zimene tingachite kuti tizisangalala ndi zomwe timachita pa ntchito yaikulu yokololayi. (Yoh. 14:12) Tingatsimikize kuti Yehova akusangalala ndi zomwe tikuchita ngati sitingafooke. w21.10 28 ¶15-17

Lamlungu, September 17

Kukongola kwa anyamata ndiko mphamvu zawo.​—Miy. 20:29.

Tikamakalamba mwina tingamade nkhawa kuti Yehova sangatigwiritsenso ntchito ngati kale. N’zoona kuti mphamvu zathu zingachepe koma tikhoza kugwiritsa ntchito nzeru ndi zimene tikudziwa pothandiza achinyamata kuti azichita zambiri potumikira Yehova komanso kutumikira m’maudindo osiyanasiyana. Achikulire ayenera kukhala odzichepetsa kuti azithandiza achinyamata. Munthu wodzichepetsa amaona ena kukhala omuposa. (Afil. 2:3, 4) Achikulire omwe ndi odzichepetsa amazindikira kuti pali njira zosiyanasiyana zochitira zinthu, zimene sizisemphana ndi mfundo za m’Malemba komanso zomwe zingakhale zothandiza. Choncho sayembekezera kuti aliyense azichita zinthu ngati mmene iwowo ankachitira kale. (Mlal. 7:10) Ngakhale kuti amadziwa zinthu zambiri zimene angathandize nazo achinyamata, amazindikira kuti “zochitika za padzikoli zikusintha.” Iwo angafunike kuphunzira njira zatsopano zochitira zinthu.​—1 Akor. 7:31. w21.09 8 ¶1, 3

Lolemba, September 18

Ndi mulungu wina uti amene angafanane nanu, inu Yehova? Ndinu woyera kopambana, ndani angafanane ndi inu?​—Eks. 15:11.

Yehova sakanalola kuti anthu amene amamulambira, azichita zinthu zimene zingawaipitse. Iye ndi woyera kwambiri. Zimenezi zinaonekera bwino pa zimene zinalembedwa pakachitsulo kagolide komwe mkulu wa ansembe ankavala pamphumi. Pakachitsulopo analembapo mochita kugoba kuti, “Chiyero n’cha Yehova.” (Eks. 28:36-38) Mawu amene analembedwa pakachitsuloko ankatsimikizira aliyense wowaona kuti Yehova ndi woyeradi. Nanga bwanji Aisiraeli omwe sakanatha kuona kachitsuloka chifukwa choti sakanatha kukumana ndi mkulu wa ansembe? Kodi ndiye kuti uthengawo sakanaumva? Ayi. Ku Isiraeli, aliyense ankamva uthengawu Chilamulo chikamawerengedwa pamaso pa amuna, akazi komanso ana. (Deut. 31:9-12) Mukanakhalapo pa nthawiyo, bwenzi mukumva mawu akuti: “Ine ndine Yehova Mulungu wanu. . . . Muzikhala oyera, chifukwa ine ndine woyera.” “Mukhale oyera kwa ine, chifukwa ine Yehova ndine woyera.”​—Lev. 11:44, 45; 20:7, 26. w21.12 3 ¶6-7

Lachiwiri, September 19

Siyani kuvutika mumtima.—Luka 12:29.

Ena akhoza kumada nkhawa kuti apeza bwanji zinthu zofunika. N’kutheka kuti iwo amakhala m’mayiko osauka. Choncho zingakhale zovuta kuti azipeza ndalama zokwanira zosamalira mabanja awo. Mwina munthu yemwe ankapezera zofunika banja lawo anamwalira, zimene zingachititse kuti anthu a m’banjalo azivutika kupeza ndalama zogulira zinthu zofunika. Zinthu zingatiyendere bwino ngati titasiya kuda nkhawa n’kumadalira Yehova. Kumbukirani kuti Atate wathu wachikondi Yehova, amatilonjeza kuti adzatipatsa zofunikira pa moyo ngati timaika pamalo oyamba zinthu zokhudza kulambira. (Mat. 6:32, 33) Nthawi zonse amakwaniritsa zomwe analonjezazi. (Deut. 8:4, 15, 16; Sal. 37:25) Ngati Yehova amasamalira mbalame komanso maluwa, sitiyenera kuda nkhawa kuti tidzapeza bwanji chakudya komanso zovala. (Mat. 6:26-30; Afil. 4:6, 7) Monga mmene chikondi chimachititsira makolo kuti azipezera ana awo zofunikira, chimachititsanso Atate wathu wakumwamba kuti azithandiza anthu ake kupeza zinthu zofunika. w21.12 17 ¶4-5; 18 ¶8

Lachitatu, September 20

Yehova anapitirizabe kukhala ndi Yosefe ndi kumusonyeza kukoma mtima kosatha.​—Gen. 39:21.

Kodi munthu wina kapena Mkhristu mnzanu anayamba wakukhumudwitsanipo kwambiri? Taganizirani chitsanzo cha Yosefe yemwe abale ake enieni anamuchitira zinthu zopanda chilungamo. Iye ankaganizira kwambiri zotumikira Yehova yemwe anamudalitsa chifukwa choyembekezerabe mopirira. N’kupita kwa nthawi Yosefe anakhululukira abale ake omwe anamulakwirawo ndipo anaona mmene Yehova anamudalitsira. (Gen. 45:5) Mofanana ndi Yosefe, timalimbikitsidwa tikakhala pa ubwenzi wabwino ndi Yehova n’kumayembekezera kuti akonze zinthu pa nthawi yake. (Sal. 7:17; 73:28) Ngati mukupirira zinthu zina zopanda chilungamo kapena zokhumudwitsa muzikumbukira kuti Yehova ali pafupi ndi anthu “a mtima wosweka.” (Sal. 34:18) Amakukondani chifukwa mumaleza mtima komanso kumutulira nkhawa zanu. (Sal. 55:22) Iye ndi Woweruza wa dziko lonse. Ndipo amaona zonse zimene zikuchitika. (1 Pet. 3:12) Ndiye ngati mukukumana ndi mavuto amene simungathe kuwathetsa, kodi mudzayembekezera Yehova kuti achitepo kanthu? w21.08 11 ¶14; 12 ¶16

Lachinayi, September 21

Pitirizani kuzindikira chifuniro cha Yehova.​—Aef. 5:17.

Ndi nzeru kugwiritsa ntchito moyo wathu m’njira imene ingatithandize kukhala pa ubwenzi wabwino ndi Yehova. Tiyenera kumaika zinthu zofunika kwambiri pamalo oyamba. Nthawi zina kuti tigwiritse ntchito nthawi yathu mwanzeru, timafunika kusankha pakati pa zinthu ziwiri zomwe si zolakwika pazokha. Timaona mfundo imeneyi tikaganizira zimene zinachitika Yesu atapita kunyumba kwa Mariya ndi Marita. N’zoonekeratu kuti posangalala kuti alandira Yesu monga mlendo wawo, Marita anaganiza zomuphikira chakudya chapamwamba. Koma pa nthawiyi, mchemwali wake Mariya anaona kuti ndi mwayi wake kuti akhale pafupi ndi Ambuye n’kumawamvetsera pamene ankaphunzitsa. N’zoona kuti Marita anali ndi zolinga zabwino pa zimene ankachitazi, koma Mariya anasankha “chinthu chabwino kwambiri.” (Luka 10:38-42) Ngakhale kuti patapita nthawi Mariya anaiwala chakudya chimene anadya pa tsikulo, tingakhale otsimikiza kuti iye sanaiwale zimene anaphunzira kwa Yesu. Mofanana ndi Mariya, yemwe anaona kuti nthawi yochepa yomwe ankamvetsera Yesu inali yamtengo wapatali, ifenso timaona kuti nthawi yomwe timachita zinthu zokhudza Yehova ndi yamtengo wapatali. w22.01 27 ¶5-6

Lachisanu, September 22

Kodi waona mmene Ahabu wadzichepetsera pamaso panga?​—1 Maf. 21:29.

Ngakhale kuti Ahabu anadzichepetsa pamaso pa Yehova, zimene anachita pambuyo pake zinasonyeza kuti sanalape kuchokera pansi pamtima. Iye sanathetse kulambira Baala mu ufumu wake komanso sanalimbikitse anthu kuti azilambira Yehova. Ahabu atamwalira, Yehova anasonyeza mmene ankaonera munthu ameneyu. Mneneri wa Mulungu dzina lake Yehu ananena kuti anali ‘woipa.’ (2 Mbiri 19:1, 2) Ndiye taganizirani izi: Ahabu akanasonyeza kulapa kwenikweni, mneneriyu sakanamufotokoza kuti anali munthu woipa yemwe ankadana ndi Yehova. Apa n’zoonekeratu kuti, ngakhale kuti Ahabu anasonyeza kulapa pamlingo winawake, iye sanalape kuchokera pansi pamtima. Kodi tingaphunzire chiyani pa zimene Ahabu anachita? Eliya atauza Ahabu kuti banja lake lidzapatsidwa chilango, poyamba iye anadzichepetsa. Chimenechitu chinali chiyambi chabwino. Koma zimene anachita pambuyo pake zinasonyeza kuti sanalape kuchokera pansi pamtima. Choncho kulapa kumaphatikizapo zambiri osati kungodzimvera chisoni pa zimene wachita. w21.10 3 ¶4-5, 7-8

Loweruka, September 23

Uthenga wabwino uwu wa ufumu udzalalikidwa.​—Mat. 24:14.

Mneneri Yesaya ndi mkazi wake ankaona kuti kutumikira Yehova ndi kofunika kwambiri. Yesaya anali mneneri ndipo zikuoneka kuti mkazi wake ankachita zinthu zina zokhudzana ndi uneneri chifukwa amatchulidwa kuti “mneneri wamkazi.” (Yes. 8:1-4) Monga banja, n’zoonekeratu kuti Yesaya ndi mkazi wake ankaika patsogolo kulambira Yehova pa moyo wawo. Anthu okwatirana masiku anonso, angaike kutumikira Yehova pamalo oyamba poyesetsa kuchita zonse zomwe angathe pomutumikira. Iwo angamadalire kwambiri Yehova akamaphunzira limodzi maulosi a m’Baibulo komanso kuona mmene nthawi zonse akukwaniritsidwira. (Tito 1:2) Angaganizire zimene angachite kuti azikwaniritsa nawo maulosi ena a m’Baibulo. Mwachitsanzo, akhoza kuthandiza kukwaniritsa nawo ulosi wa Yesu wonena kuti uthenga wabwino udzalalikidwa padziko lonse mapeto asanafike. Anthu okwatirana akamazindikira kwambiri kuti maulosi a m’Baibulo akukwaniritsidwa, m’pamenenso amafunitsitsa kwambiri kuti azichita zonse zomwe angathe potumikira Yehova. w21.11 16 ¶9-10

Lamlungu, September 24

Anauza wophunzirayo kuti: “Kuyambira lero awa akhala mayi ako.”​—Yoh. 19:27.

Yesu ankadera nkhawa mayi ake omwe ayenera kuti pa nthawiyi anali amasiye. Chifukwa chakuti iye ankawakonda kwambiri, anapereka udindo wowasamalira kwa Yohane chifukwa ankadziwa kuti iye angawathandize kupitirizabe kutumikira Yehova. Kuyambira tsiku limenelo, Yohane anakhala ngati mwana wa Mariya ndipo ankawasamalira ngati mayi ake enieni. Yesu anasonyeza chikondi chachikulu kwa mayi ake okondedwawa, omwe anamusamalira kuchokera pa nthawi imene anabadwa ndiponso amene anaima chapafupi pa nthawi imene ankaphedwa. Kodi tikuphunzira chiyani pa mawu a Yesu? Ubwenzi wathu ndi Akhristu anzathu ungathe kukhala wolimba kwambiri kuposa ubwenzi umene tingakhale nawo ndi achibale athu. Achibale athu angamatitsutse kapena kutikana koma Yesu analonjeza kuti tikapitiriza kukhala pa ubwenzi ndi Yehova komanso kukhalabe m’gulu lake tidzapeza zochuluka “kuwirikiza maulendo 100” kuposa zimene tingataye. Tingapeze ambiri omwe angakhale ngati ana athu, mayi athu komanso bambo athu. (Maliko 10:29, 30) Kodi mumamva bwanji chifukwa chokhala m’banja la Yehova limene anthu ake amagwirizana chifukwa choti amakhulupirira komanso amakonda Yehova ndi anthu anzawo?​—Akol. 3:14; 1 Pet. 2:17. w21.04 9-11 ¶7-8

Lolemba, September 25

Musaiwale kuchita zabwino ndi kugawana zinthu ndi ena.​—Aheb. 13:16.

Chikondi chokhulupirika chimapangitsa munthu kuchita zoposa zimene zimayembekezeredwa. Masiku ano abale ndi alongo ambiri amasankha kusonyeza chikondi chokhulupirika kwa Akhristu anzawo ngakhale amene sakuwadziwa. Mwachitsanzo, pakachitika ngozi za m’chilengedwe, mwansanga iwo amafunitsitsa kudziwa zimene angachite kuti athandizepo. Ngati wina mumpingo wakumana ndi vuto lobwera chifukwa cha mavuto azachuma, iwo amachitapo kathu mwansanga kuti amuthandize kupeza zimene akufunikira. Mofanana ndi Akhristu a ku Makedoniya a m’nthawi ya atumwi, iwo amachita zoposa zimene zikuyembekezeredwa. Amagwiritsa ntchito nthawi komanso zinthu zawo ndipo amachita “ngakhale zoposa pamenepo,” kuti athandize abale awo amene akumana ndi mavuto. (2 Akor. 8:3) Akulu atcheru masiku ano amayamikira thandizo limene abale ndi alongo amapereka. Kuyamikira abale ndi alongo amenewa pa nthawi yake kungawathandize kukhala ndi mphamvu zoti apitirize kuchita zabwino.​—Yes. 32:1, 2. w21.11 11 ¶14; 12 ¶21

Lachiwiri, September 26

Tchera khutu lako ndi kumva mawu a anthu anzeru.​—Miy. 22:17.

Tonsefe timafunika kupatsidwa malangizo nthawi ndi nthawi. Nthawi zina tingapemphe munthu amene timamulemekeza kuti atipatse malangizo. Nthawi zinanso m’bale angabwere kudzatiuza kuti tayamba kuyenda “njira yolakwika” imene tingadzanong’oneze nayo bondo. (Agal. 6:1) Komanso tingapatsidwe malangizo podzudzulidwa chifukwa cholakwitsa zina zake. Kaya tapatsidwa malangizo m’njira yotani, tiyenera kumvera. Zimenezi zingachititse kuti zinthu zitiyendere bwino komanso kuti tipulumutse moyo wathu. (Miy. 6:23) Lemba laleroli likutilimbikitsa kumvera “mawu a anthu anzeru.” Palibe munthu amene amadziwa chilichonse ndipo nthawi zonse pamakhala munthu amene akudziwa zambiri kuposa ifeyo. (Miy. 12:15) Choncho tikamamvera malangizo timasonyeza kuti ndife odzichepetsa. Zimasonyezanso kuti timazindikira zimene sitingakwanitse komanso kuti timafunika kuthandizidwa kuti tikwaniritse zolinga zathu. Mfumu yanzeru Solomo inalemba kuti: ‘Aphungu akachuluka zolingalira zimakwaniritsidwa.’​—Miy. 15:22. w22.02 8 ¶1-2

Lachitatu, September 27

Wobisa machimo ake zinthu sizidzamuyendera bwino, koma woulula n’kuwasiya adzachitiridwa chifundo.—Miy. 28:13.

Kulapa kwenikweni kumaphatikizapo zambiri osati kungonena kuti tikudzimvera chisoni chifukwa cha zimene tachita. Koma kumaphatikizapo kusintha maganizo ndi mtima wathu. Zimenezi zikuphatikizapo kusiya zoipazo, kutembenuka n’kuyambiranso kutsatira mfundo za Yehova. (Ezek. 33:14-16) Chofunika kwambiri kwa munthu amene wachita tchimo ndi kukonzanso ubwenzi wake ndi Yehova. Kodi tiyenera kuchita chiyani ngati mnzathu wa pamtima wachita tchimo lalikulu? Sitingasonyeze kuti timamukonda mnzathuyo ngati tikuyesa kubisira akulu tchimo lakelo. Kubisa tchimolo n’kudzinamiza chifukwa Yehova amaona zonse. (Miy. 5:21, 22) Mungathandize mnzanuyo pomukumbutsa kuti akulu angamuthandize. Ngati akukana kukafotokozera akulu, inuyo muyenera kukawafotokozera za nkhaniyo. Mukatero mungasonyeze kuti mukufunitsitsa kumuthandiza. w21.10 7 ¶19-21

Lachinayi, September 28

Musamaganizire zofuna zanu zokha, koma muziganiziranso zofuna za ena.​—Afil. 2:4.

Tonsefe tingathe kutsanzira mtima wa Yesu wofunitsitsa kuthandiza ena. Baibulo limati iye anakhala “ngati kapolo.” (Afil. 2:7) Kapolo wabwino ankayesetsa kuchita zimene angathe kuti azisangalatsa mbuye wake. Monga kapolo wa Yehova komanso munthu amene amatumikira abale ake, n’zosakaikitsa kuti mumafuna kuchita zambiri potumikira Yehova komanso Akhristu anzanu. Muzidzifunsa kuti: ‘Kodi ndine wofunitsitsa kuika zofuna za ena patsogolo kuti ndiwathandize? Kodi ndimafulumira kudzipereka pakafunika anthu oti akathandize kuyeretsa malo a msonkhano kapena kukonza Nyumba ya Ufumu?’ Tiyerekeze kuti mwazindikira kuti mukufunika kukonza zinthu zina, koma mukuona kuti mulibe mtima wofuna kuchita zimenezo. Ngati zili choncho, muzipemphera kwa Yehova kuchokera pansi pa mtima. Muzimuuza mmene mukumvera. Ndipo muzimupempha kuti ‘alimbitse zolakalaka zanu,’ kuti muchite zinthu zonse zimene iye amakonda.​—Afil. 2:13. w22.02 22-23 ¶9-11

Lachisanu, September 29

Ndidzakutsitsimutsani.​—Mat. 11:28.

Yesu anasonyeza khalidweli pokhala wodekha komanso wololera ngakhale pa nthawi zovuta kwambiri. (Mat. 11:29, 30) Mwachitsanzo, mayi wa ku Foinike atamupempha kuti amuchiritsire mwana wake, poyamba iye anakana, koma mayiyo atasonyeza chikhulupiriro chachikulu, mokoma mtima anamuchiritsira mwana wakeyo. (Mat. 15:22-28) Ngakhale kuti anali wokoma mtima Yesu sankalekerera zinthu. Nthawi zina Yesu ankasonyeza kukoma mtima popereka malangizo amphamvu kwa anthu amene ankawakonda. Mwachitsanzo, pamene Petulo ankayesa kumuletsa kuti asachite chifuniro cha Yehova, Yesu anamudzudzula pamaso pa ophunzira ena. (Maliko 8:32, 33) Iye anachita zimenezi osati pofuna kumuchititsa manyazi, koma pofuna kumuphunzitsa komanso kuchenjeza ophunzira enawo kuti asakhale odzikuza. N’zosakayikitsa kuti Petulo anachita manyazi komabe malangizowo anamuthandiza. Kuti tisonyeze ena kukoma mtima, nthawi zina timafunika kuwapatsa malangizo mosapita mbali. Tikamachita zimenezi, tizitsanzira Yesu popereka malangizo ochokera m’Mawu a Mulungu. w22.03 11 ¶12-13

Loweruka, September 30

Tiyeni nthawi zonse tizitamanda Mulungu. Tizichita zimenezi monga nsembe imene tikupereka kwa Mulungu, yomwe ndi chipatso cha milomo yathu. Timagwiritsa ntchito milomo imeneyi polengeza dzina lake kwa anthu ena.​—Aheb. 13:15.

Timalambira Yehova tikamamutamanda. (Sal. 34:1) Timamutamanda tikamauza ena monyadira za makhalidwe ake odabwitsa komanso ntchito zake. Tingakhale ndi zabwino zambiri zolankhula zokhudza Yehova ngati timamuyamikira. Tikamapeza nthawi yoganizira ubwino wa Yehova pa zabwino zonse zimene amatichitira tingakhale ndi zifukwa zambiri zomutamandira. Ntchito yolalikira imatipatsa mwayi wabwino woti tizitamanda Mulungu ‘monga nsembe imene tikupereka kwa iye, yomwe ndi chipatso cha milomo yathu.’ Mofanana ndi zimene timayenera kuchita poganizira kaye zimene tinganene popemphera kwa Yehova, tingachitenso bwino kuganizira zimene tinganene kwa anthu amene timawalalikira. Timafuna kuti “nsembe imene tikupereka” izikhala yabwino kwambiri. Choncho timalankhula ndi mtima wonse tikamauza ena mfundo za choonadi. w22.03 21 ¶8

    Mabuku a Chichewa (1974-2026)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena