Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • es23 tsamba 98-108
  • October

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • October
  • Kuphunzira Malemba Tsiku ndi Tsiku—2023
  • Timitu
  • Lamlungu, October 1
  • Lolemba, October 2
  • Lachiwiri, October 3
  • Lachitatu, October 4
  • Lachinayi, October 5
  • Lachisanu, October 6
  • Loweruka, October 7
  • Lamlungu, October 8
  • Lolemba, October 9
  • Lachiwiri, October 10
  • Lachitatu, October 11
  • Lachinayi, October 12
  • Lachisanu, October 13
  • Loweruka, October 14
  • Lamlungu, October 15
  • Lolemba, October 16
  • Lachiwiri, October 17
  • Lachitatu, October 18
  • Lachinayi, October 19
  • Lachisanu, October 20
  • Loweruka, October 21
  • Lamlungu, October 22
  • Lolemba, October 23
  • Lachiwiri, October 24
  • Lachitatu, October 25
  • Lachinayi, October 26
  • Lachisanu, October 27
  • Loweruka, October 28
  • Lamlungu, October 29
  • Lolemba, October 30
  • Lachiwiri, October 31
Kuphunzira Malemba Tsiku ndi Tsiku—2023
es23 tsamba 98-108

October

Lamlungu, October 1

Wodala amene sapeza chokhumudwitsa mwa ine.​—Mat. 11:6.

Zonse zomwe timaphunzitsa komanso kukhulupirira zimachokera m’Mawu a Mulungu. Koma ngakhale zili choncho, anthu ambiri amakana uthenga wathu chifukwa amaona kuti zimene timachita polambira Mulungu ndi zosasangalatsa ndiponso zimene timaphunzitsa sizigwirizana ndi zimene amafuna kumva. Kodi tingatani kuti tisakhumudwe n’kusiya kutsatira Yesu? Mtumwi Paulo anauza Akhristu a ku Roma kuti: “Munthu amakhala ndi chikhulupiriro chifukwa cha zimene wamva. Ndipo zimene wamvazo zimachokera m’mawu onena za Khristu.” (Aroma 10:17) Choncho timakhala ndi chikhulupiriro chifukwa chophunzira Baibulo, osati pochita nawo miyambo yosemphana ndi Malemba, ngakhale itaoneka kuti ndi yosangalatsa. Tiyenera kuphunzira Malemba kuti tikhale ndi chikhulupiriro cholimba chifukwa “popanda chikhulupiriro n’zosatheka kukondweretsa Mulungu.” (Aheb. 11:1, 6) Pamenepa zikusonyeza kuti sitikuchita kufunikira kuona chizindikiro chochokera kumwamba kuti tidziwe kuti tapeza choonadi. Kuphunzira mosamala mfundo za m’Baibulo zolimbitsa chikhulupiriro, kungatithandize kuti tisamakaikire ngakhale pang’ono kuti tapeza choonadi. w21.05 4-5 ¶11-12

Lolemba, October 2

Zondichitikira zija, zathandiza kupititsa patsogolo uthenga wabwino m’malo moulepheretsa.—Afil. 1:12.

Mtumwi Paulo ankakumana ndi mavuto ambiri. Iye ankafunika kuti Yehova amuthandize makamaka pa nthawi imene anamenyedwa, kuponyedwa miyala komanso kutsekeredwa m’ndende. (2 Akor. 11:23-25) Paulo anavomerezanso kuti ankalimbana ndi maganizo ofooketsa. (Aroma 7:18, 19, 24) Ankapiriranso vuto lina lomwe analitchula kuti “munga m’thupi,” limene ankafunitsitsa kuti Mulungu alichotse. (2 Akor. 12:7, 8) Ngakhale kuti Paulo ankakumana ndi mavuto, Yehova anamupatsa mphamvu kuti akwanitse kuchita utumiki wake. Mwachitsanzo, taganizirani zimene Paulo anakwanitsa kuchita. Pa nthawi imene anali pa ukaidi wosachoka panyumba ku Roma, iye ankachita khama kuteteza uthenga wabwino polankhula ndi atsogoleri a Chiyuda komanso akuluakulu a boma. (Mac. 28:17; Afil. 4:21, 22) Iye analalikiranso Asilikali Oteteza Mfumu komanso anthu omwe ankabwera kudzamuona. (Mac. 28:30, 31; Afil. 1:13) Pa nthawiyi, Paulo analembanso makalata amene akuthandiza Akhristu oona mpaka pano. w21.05 21 ¶4-5

Lachiwiri, October 3

“Musapitirire zinthu zolembedwa,” kuti aliyense wa inu asadzitukumule.​—1 Akor. 4:6.

Kunyada kunachititsa kuti Mfumu Uziya ya ku Yuda ikane malangizo komanso kuchita zinthu modzikuza. Uziya ankachita bwino pa zinthu zambiri. Iye anapambana pankhondo zambiri, anamanga mizinda yambiri komanso anali ndi minda yochuluka. Baibulo limati: “Mulungu woonayo anachititsa kuti zinthu zizimuyendera bwino.” (2 Mbiri 26:3-7, 10) Limanenanso kuti: “Koma atangokhala wamphamvu mtima wake unadzikuza mpaka kufika pom’pweteketsa.” Yehova anali atalamula kuti ndi ansembe okha amene azipereka nsembe zofukiza kukachisi. Koma Mfumu Uziya anadzikweza n’kuchita zimenezi. Yehova sanasangalale nazo ndipo anakantha munthu wonyadayu ndi khate. (2 Mbiri 26:16-21) Kodi kunyada kungachititse kuti ifenso tikodwe mumsampha ngati mmene zinakhalira ndi Uziya? Inde, zimenezi zingachitike ngati timadziganizira kuposa mmene tiyenera kudziganizira. Tizikumbukira kuti luso lililonse limene tingakhale nalo komanso utumiki uliwonse umene tingapatsidwe mumpingo zimachokera kwa Yehova. (1 Akor. 4:7) Yehova sangatigwiritse ntchito ngati tili ndi mtima wonyada. w21.06 16 ¶7-8

Lachitatu, October 4

Musakondwere ndi zimenezi, kuti mizimu yakugonjerani, koma kondwerani chifukwa mayina anu alembedwa kumwamba.​—Luka 10:20.

Yesu ankadziwa kuti si nthawi zonse pamene ophunzira ake azidzakumana ndi zosangalatsa mu utumiki. Ndipotu sitikudziwa kuti ndi anthu angati amene anamvetsera ophunzirawo omwe anakhala okhulupirira. Sikuti ophunzirawo ankangofunika kukhala osangalala chifukwa cha zimene akwanitsa kuchita, koma makamaka chifukwa choti Yehova ankasangalala ndi khama lawo. Tikamapirira pa ntchito yathu yolalikira, tidzapeza moyo wosatha. Tikamachita zonse zomwe tingathe pofesa komanso kusamalira mbewu za choonadi cha Ufumu, timakhalanso kuti ‘tikutsatira mzimu wa Mulungu’ polola kuti mzimuwo uzigwira ntchito mwaufulu pa moyo wathu. Ngati sitingafooke kapena “kutopa,” Yehova akulonjeza kuti adzatipatsa moyo wosatha ngakhale ngati sitinathandizepo munthu wina mpaka kufika pobatizidwa.​—Agal. 6:7-9. w21.10 26 ¶8-9

Lachinayi, October 5

Anawamvera chifundo, . . . Choncho anayamba kuwaphunzitsa zinthu zambiri.​—Maliko 6:34.

Pa nthawi ina Yesu ndi ophunzira ake anatopa kwambiri chifukwa choti analalikira kwa nthawi yaitali. Iwo ankafunika kupeza malo oti akapume, koma khamu la anthu linawatsatira komweko. Powamvera chifundo, Yesu anayamba kuwaphunzitsa “zinthu zambiri.” Iye ankaganizira mmene anthuwo ankamvera. Ankafunitsitsa kuwathandiza chifukwa ankadziwa mavuto amene ankakumana nawo komanso kuti analibe chiyembekezo. Umunso ndi mmene anthu alili masiku ano. Sitiyenera kupusitsika ndi mmene amaonekera. Iwo ali ngati nkhosa zosochera zimene zilibe m’busa. Mtumwi Paulo anafotokoza kuti anthu ngati amenewa sadziwa Mulungu ndipo alibe chiyembekezo. (Aef. 2:12) Choncho tikamaganizira kuti umu ndi mmene anthu a m’gawo lathu alili, chikondi ndi chifundo zimatilimbikitsa kuti tiwathandize. Ndipo njira yabwino kwambiri imene tingawathandizire ndi kuphunzira nawo Baibulo. w21.07 5 ¶8

Lachisanu, October 6

Tisakhale odzikuza, . . . ndi ochitirana kaduka.​—Agal. 5:26.

Munthu wodzikuza amakhala wonyada komanso wodzikonda. Munthu wakaduka kapena kuti wansanje, sikuti amangosirira zimene ena ali nazo koma amalakalakanso atazitenga kuti zikhale zake. Choncho munthu amene ali ndi nsanje amadana kwambiri ndi munthu amene akumuchitira nsanjeyo. Tingayerekezere kudzikuza komanso nsanje ndi tizitsotso timene tili m’mafuta a ndege. Ndegeyo ikhoza kunyamuka koma tizitsotsoto tikhoza kutseka mapaipi ndipo ndegeyo ingagwe. Mofanana ndi zimenezi, munthu akhoza kutumikira Yehova kwa kanthawi ndithu koma ngati ali wodzikuza komanso wansanje, sangapite patali. (Miy. 16:18) Akhoza kusiya kutumikira Yehova ndipo zimenezi zingavulaze iyeyo komanso anthu ena. Tingathe kupewa kudzikuza potsatira malangizo a Paulo amene analembera Afilipi akuti: “Musachite chilichonse ndi mtima wokonda mikangano kapena wodzikuza, koma modzichepetsa, ndi kuona ena kukhala okuposani.”​—Afil. 2:3. w21.07 15-16 ¶6-8

Loweruka, October 7

Pamene tinali kulalikira uthenga wabwino kwa inu, sitinali kungolankhula basi, koma uthengawo unakukhudzani kwambiri, komanso unabwera limodzi ndi mphamvu ya mzimu woyera, ndipo unachititsa kuti mukhale otsimikiza mtima kwambiri.​—1 Ates. 1:5.

Anthu ena amaona kuti chipembedzo choona chiyenera kukhala ndi yankho la funso lililonse, ngakhale mafunso amene m’Baibulo mulibe mayankho ake. Koma kodi zimenezi n’zomveka? Taganizirani chitsanzo cha mtumwi Paulo. Iye analimbikitsa Akhristu anzake kuti ‘azitsimikizira zinthu zonse,’ koma anavomerezanso kuti panali zambiri zomwe sankazimvetsa. (1 Ates. 5:21) Iye analemba kuti: “Tikudziwa moperewera” komanso anawonjezera kuti, “sitikuona bwinobwino chifukwa tikugwiritsa ntchito galasi losaoneka bwinobwino.” (1 Akor. 13:9, 12) Paulo sankamvetsa zinthu zonse, chimodzimodzinso ifeyo. Komabe iye ankamvetsa zinthu zikuluzikulu zokhudza Yehova. Zimene ankadziwazo zinali zokwanira kumutsimikizira kuti zomwe ankakhulupirirazo ndi choonadi. Chimodzi mwa zinthu zomwe zingatithandize kukhulupirira kwambiri kuti tinapeza choonadi ndi kuyerekezera njira yolambirira imene Yesu anayambitsa ndi zimene a Mboni za Yehova amachita masiku ano. w21.10 18-19 ¶2-4

Lamlungu, October 8

Akakwanitsa zaka 50 atuluke m’gululo.​—Num. 8:25.

Achikulirenu, kaya mukuchita utumiki wa nthawi zonse kapena ayi, mukhoza kuchita zambiri pothandiza ena. Kodi mungachite bwanji zimenezi? Muzisangalala ndi mmene zinthu zilili pa moyo wanu panopa, muzikhala ndi zolinga zatsopano komanso muziganizira kwambiri zimene mungakwanitse kuchita, osati zimene simungakwanitse. Mfumu Davide ankafunitsitsa kumanga nyumba ya Yehova. Koma atauzidwa kuti mwayi umenewu udzaperekedwa kwa Solomo yemwe anali wachinyamata, Davide anavomereza zimene Yehova anasankha ndipo anachita zonse zimene akanatha pothandiza kukonzekera ntchitoyo. (1 Mbiri 17:4; 22:5) Davide sankaona kuti iye ndi amene angagwire bwino ntchitoyo chifukwa chakuti Solomo anali “wamng’ono ndi wosakhwima.” (1 Mbiri 29:1) Iye ankadziwa kuti ntchitoyo ingayende bwino ngati Yehova akuidalitsa, osati chifukwa cha kudziwa zinthu kapena msinkhu wa amene ankatsogolera. Mofanana ndi Davide, masiku ano achikulire amapitirizabe kuchita khama ngakhale pamene utumiki wawo wasintha. Ndipo amadziwa kuti Yehova adzadalitsa achinyamata amene akugwira ntchito imene iwowo ankagwira. w21.09 9 ¶4; 10 ¶5, 8

Lolemba, October 9

Adzachititsa ofatsa kutsatira zigamulo zake, ndipo adzaphunzitsa ofatsa kuyenda m’njira yake.​—Sal. 25:9.

Kukhala ndi zolinga potumikira Yehova kungatithandize kukhala ndi moyo wokhutiritsa komanso watanthauzo. Chinsinsi chagona pa kukhala ndi zolinga zimene tingazikwaniritse malinga ndi luso komanso mmene zinthu zilili pa moyo wathu, osati mmene zilili pa moyo wa anthu ena. Zimenezi zingathandize kuti tisadzakhumudwe kapena kufooka. (Luka 14:28) Monga mtumiki wa Yehova, dziwani kuti iye amakuonani kuti ndinu wamtengo wapatali komanso wapadera m’banja lake. Sikuti Yehova anakukokerani kwa iye chifukwa choti anaona kuti ndinu wabwino kwambiri kuposa ena. Iye anakukokani chifukwa anaona mtima wanu kuti ndinu munthu wofatsa komanso wophunzitsika, yemwe akhoza kumuumba. Dziwani kuti iye amayamikira mukamachita zonse zomwe mungathe pomutumikira. Kupirira komanso kukhulupirika kwanu, ndi umboni wakuti muli ndi “mtima woona komanso wabwino.” (Luka 8:15) Choncho pitirizani kutumikira Yehova ndi mtima wanu wonse. Mukatero mudzakhala ndi chifukwa chosangalalira ‘ndi ntchito yanu.’​—Agal. 6:4. w21.07 24 ¶15; 25 ¶20

Lachiwiri, October 10

Amene wabweza wochimwa panjira yake yoipa, adzapulumutsa moyo wa wochimwayo.​—Yak. 5:20.

Timafunika kukhala oleza mtima pamene tikuyembekezera kuti chilungamo chichitike. Mwachitsanzo, akulu akazindikira kuti wina mumpingo wachita tchimo lalikulu, amapempha “nzeru yochokera kumwamba” n’cholinga choti adziwe maganizo a Yehova pa nkhaniyo. (Yak. 3:17) Cholinga chawo chimakhala chakuti ngati n’kotheka, ‘abweze wochimwa panjira yake yoipa.’ (Yak. 5:19, 20) Komanso amayesetsa kuchita zonse zomwe angathe kuti ateteze mpingo komanso kulimbikitsa amene alakwiridwa. (2 Akor. 1:3, 4) Akulu akamaweruza nkhani yokhudza munthu amene wachita tchimo lalikulu, amafunika kufufuza zimene zachitika ndipo pangafunike nthawi yokwanira kuti achite zimenezi. Kenako iwo amapemphera, kupereka mosamala malangizo a m’Malemba komanso kuwongolera wochimwayo “pa mlingo woyenera.” (Yer. 30:11) Akulu samangothamangira kupereka chiweruzo. Iwo akatsatira malangizo a Yehova, anthu onse mumpingo amapindula. w21.08 11 ¶12-13

Lachitatu, October 11

Kumene inu mupite inenso ndipita komweko . . . Anthu a mtundu wanu adzakhala anthu a mtundu wanga, ndipo Mulungu wanu adzakhala Mulungu wanga.​—Rute 1:16.

Chifukwa chakuti ku Isiraeli kunali njala, Naomi, mwamuna wake komanso ana awo amuna awiri anasamukira ku Mowabu. Ali kumeneko mwamuna wake wa Naomi anamwalira. Ana ake awiri aja anakwatira koma n’zomvetsa chisoni kuti nawonso anamwalira. (Rute 1:3-5) Zomwe zinachitikazi zinachititsa kuti Naomi afooke kwambiri. Zimenezi zinamusokoneza kwambiri maganizo mpaka anafika poyamba kuona kuti Yehova sakusangalala naye. Taonani mmene anafotokozerera momwe ankamvera zokhudza Mulungu: “Dzanja la Yehova landiukira.” “Wamphamvuyonse wachititsa moyo wanga kukhala wowawa kwambiri.” “Ndi Yehova amene wandichititsa kukhala wonyozeka, ndipo ndi Wamphamvuyonseyo amene wandigwetsera tsokali.” (Rute 1:13, 20, 21) Yehova amadziwa kuti “kuponderezedwa kumapangitsa munthu wanzeru kuchita zinthu zopanda nzeru.” (Mlal. 7:7) Iye anachititsa kuti Rute amuthandize komanso kumusonyeza chikondi chokhulupirika. Mofunitsitsa komanso mokoma mtima, Rute anathandiza apongozi akewo kuti ayambirenso kuona kuti Yehova sanawasiye ndipo ankawakonda. w21.11 9 ¶9; 10 ¶10, 13

Lachinayi, October 12

Azipempha kwa Mulungu.​—Yak. 1:5.

Kodi kukhala wokhutira ndi utumiki umene tikuchita panopa kukutanthauza kuti sitiyenera kuganizira njira zina zowonjezera utumiki wathu kwa Yehova? Ayi si choncho. Tingathe kuchita zambiri ndipo tikhoza kudziikira zolinga zimene zingathandize kuti tizilalikira mwaluso komanso tizithandiza abale ndi alongo athu. Tingakwaniritse zolinga zimenezi tikamachita zinthu mwanzeru komanso modzichepetsa pothandiza ena m’malo momangoganizira zofuna zathu. (Miy. 11:2; Mac. 20:35) Kodi ndi zolinga ziti zimene mungadziikire? Muzipempha Yehova kuti akuthandizeni kudziwa zolinga zimene mungazikwaniritse. (Miy. 16:3) Kodi n’zotheka kuti mukhale ndi zolinga monga kuchita upainiya wothandiza, kapena wokhazikika, kutumikira pa Beteli kapenanso kuchita nawo utumiki wa zomangamanga? Mukhozanso kuphunzira chinenero china n’cholinga choti muzilalikira uthenga wabwino m’gawo limene amalankhula chinenerocho. w21.08 23 ¶14-15

Lachisanu, October 13

Kukoma mtima [kwa Yehova] kosatha kudzakhalapobe mpaka kalekale.​—Sal. 136:1.

Yehova amaona kuti khalidwe la kukoma mtima, kapena kuti chikondi chokhulupirika, ndi lofunika kwambiri. (Hos. 6:6) Kudzera mwa mneneri Mika, Mulungu wathu amatilimbikitsa kuti tizikhala ndi chikondi chokhulupirika. (Mika 6:8) Komabe choyamba tiyenera kudziwa kaye zimene khalidweli limatanthauza. Kodi munthu amene ali ndi chikondi chokhulupirika amatani? Mawu akuti “chikondi chokhulupirika” amapezeka nthawi pafupifupi 230 mu Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika lokonzedwanso. Ndiye kodi amatanthauza chiyani? Munthu amene ali ndi chikondi chimenechi amakonda kwambiri munthu wina n’kupitirizabe kukhala wokhulupirika kwa iye zivute zitani. Chimenechi ndi chikondi chomwe nthawi zambiri Mulungu amasonyeza anthu. Komabe anthu amasonyezananso chikondichi. Yehova ndi chitsanzo chabwino kwambiri pa nkhani yosonyeza chikondi chokhulupirika. Mpake kuti Mfumu Davide anafuula kuti: “Inu Yehova, kukoma mtima kwanu kosatha kuli kumwamba . . . Inu Mulungu, kukoma mtima kwanu kosatha ndi kwamtengo wapatali!” (Sal. 36:5, 7) Mofanana ndi Davide, kodi ifenso timayamikira chikondi chokhulupirika cha Mulungu? w21.11 2 ¶1-2; 3 ¶4

Loweruka, October 14

Koma inu muzipemphera motere: “Atate wathu wakumwamba.”—Mat. 6:9.

M’banja la Yehova muli Yesu, yemwe ndi “woyamba kubadwa wa chilengedwe chonse,” komanso angelo ambirimbiri. (Akol. 1:15; Sal. 103:20) Ali padzikoli, Yesu anasonyeza kuti anthu okhulupirika akhoza kumaona Yehova ngati Atate wawo. Ponena za Yehova pamene ankalankhula ndi ophunzira ake, iye ananena kuti “Atate wanga ndi Atate wanu.” (Yoh. 20:17) Ndipo tikadzipereka kwa Yehova n’kubatizidwa, timakhala m’banja la abale ndi alongo omwe amakondana. (Maliko 10:29, 30) Yehova ndi Atate wachikondi. Yesu amafuna kuti tiziona Yehova ngati mmene iye amamuonera. Iye amamuona monga kholo lachikondi komanso lokoma mtima lomwe tikhoza kulankhula nalo nthawi iliyonse, osati ngati munthu waudindo wouma mtima amene amangouza ena zochita. Yesu anayamba pemphero lachitsanzo ndi mawu akuti: “Atate wathu.” Iye akanatha kunena kuti tizitchula Yehova kuti “Wamphamvuyonse,” “Mlengi” kapena “Mfumu yamuyaya.” Ndipotu amenewa ndi mayina audindo oyenera opezeka m’Malemba. (Gen. 49:25; Yes. 40:28; 1 Tim. 1:17) M’malomwake Yesu anatiuza kuti tizitchula Yehova kuti “Atate.” w21.09 20 ¶1, 3

Lamlungu, October 15

Manase anadziwa kuti Yehova ndiye Mulungu woona.​—2 Mbiri 33:13.

Mfumu Manase anakana machenjezo omwe Yehova anamupatsa kudzera mwa aneneri ake. Pomalizira pake, “Yehova anawabweretsera [Ayuda] akuluakulu a asilikali a mfumu ya Asuri. Iwo anagwira Manase akubisala m’dzenje. Atatero anam’manga ndi zomangira ziwiri zamkuwa n’kupita naye ku Babulo.” Ali kundende ku Babulo, zikuoneka kuti Manase anaganizira kwambiri zimene ankachita. Iye “anadzichepetsa kwambiri pamaso pa Mulungu wa makolo ake.” Anachitanso zambiri kuposa pamenepo moti “anakhazikitsa pansi mtima wa Yehova Mulungu wake.” Ndipotu mobwerezabwereza Manase “anayamba kupemphera kwa Mulungu.” (2 Mbiri 33:10-12) Patapita nthawi Yehova anayankha mapemphero a Manase ndipo anaona kuti wasinthadi chifukwa cha zinthu zimene ankatchula m’mapemphero ake. Choncho anamukhululukira ndipo anamubwezeretsa pa ufumu wake. Manase anachita zonse zimene akanatha posonyeza kuti anali atalapadi kuchokera pansi pamtima. w21.10 4 ¶10-11

Lolemba, October 16

Awiri amaposa mmodzi, chifukwa amapeza mphoto yabwino pa ntchito yawo imene amaigwira mwakhama.​—Mlal. 4:9.

Akula ndi Purisikila ankafunika kusamuka dera lomwe anazolowera n’kukhala ndi nyumba yatsopano komanso kumachita bizinezi yawo yopanga matenti kudera latsopano. Atayamba kukhala ku Korinto, Akula ndi Purisikila anayamba kuthandiza abale mumpingo wakumeneko ndipo ankagwira ntchito limodzi ndi mtumwi Paulo powalimbikitsa. Patapita nthawi, anasamukira kumadera ena komwe kunkafunikira olalikira ambiri. (Mac. 18:18-21; Aroma 16:3-5) Anthu awiriwa ankakhala moyo wabwino ndipo ayenera kuti ankasangalala kwambiri. Anthu okwatirana masiku ano, angatsanzire Purisikila ndi Akula pomaika pamalo oyamba zinthu zokhudza Ufumu pa moyo wawo. Nthawi yabwino kwambiri yokambirana zimene adzachite pa moyo wawo, ndi pamene ali pachibwenzi. Iwo akasankhira limodzi zomwe akufuna kuchita potumikira Yehova n’kumayesetsa kukwaniritsa zomwe asankhazo, amakhala ndi mwayi waukulu woona mmene Yehova akuwathandizira pa moyo wawo.​—Mlal. 4:12. w21.11 17 ¶11-12

Lachiwiri, October 17

Aliyense wa inu aziopa mayi ndi bambo ake, . . . Ine ndine Yehova Mulungu wanu.​—Lev. 19:3.

N’zoonekeratu kuti n’zofunika kwambiri kutsatira malangizo a Mulungu okhudza kulemekeza makolo athu. Kumbukirani kuti malangizo a pa Levitiko 19:3, akuti munthu azilemekeza mayi ndi bambo ake, amabwera pambuyo pa mawu akuti, “Mukhale oyera, chifukwa ine Yehova Mulungu wanu ndine woyera.” (Lev. 19:2) Mogwirizana ndi malangizo a Yehova akuti tizilemekeza makolo athu, tingachite bwino kudzifunsa kuti, ‘Kodi ineyo ndikuchita bwanji pa nkhani imeneyi?’ Ngati mukuona kuti munkafunika kuchita zambiri m’mbuyomu, mungasankhe kuti muyambe kuchita bwino panopa. Simungathe kusintha kale lanu, koma mungakhale otsimikiza kuti kuyambira panopa muzichita zambiri pothandiza makolo anu. Mungakonze zoti muzikhala ndi nthawi yambiri yocheza nawo. Mwina mungawagulire zinthu, kuwathandiza kuti akhale pa ubwenzi wabwino ndi Yehova kapenanso kuwalimbikitsa. Kuchita zimenezi ndi kogwirizana ndi zimene lemba la Levitiko 19:3 limanena. w21.12 4-5 ¶10-12

Lachitatu, October 18

Lekani kuweruza ena.​—Mat. 7:1.

Mfumu Davide anachita machimo akuluakulu. Mwachitsanzo, iye anachita chigololo ndi Bati-seba komanso anaphetsa mwamuna wake. (2 Sam. 11:2-4, 14, 15, 24) Chifukwa cha zimenezi, iye ndi anthu a m’banja lake kuphatikizapo akazi ake ena, anakumana ndi mavuto aakulu. (2 Sam. 12:10, 11) Pa nthawi ina, Davide analephera kudalira Yehova polamula kuti asilikali a Isiraeli awerengedwe, zomwe Yehovayo sanamulamule. Kodi zotsatira zake zinali zotani? Aisiraeli pafupifupi 70,000 anafa ndi mliri. (2 Sam. 24:1-4, 10-15) Kodi mukanamuona Davide kuti si woyenera kuti Yehova amuchitire chifundo? Yehova sankaona choncho. M’malomwake, iye ankaganizira zinthu zabwino zimene Davide anachita komanso kuti analapa kuchokera pansi pa mtima. Choncho anamukhululukira machimo akuluakulu amene anachitawa. Yehova ankadziwa kuti Davide ankamukonda ndipo ankafuna kuchita zinthu zoyenera. Kodi sitiyenera kuthokoza kuti Mulungu amaona zabwino mwa ife?​—1 Maf. 9:4; 1 Mbiri 29:10, 17. w21.12 19 ¶11-13

Lachinayi, October 19

Nthawi yomweyo anayamba kuona, ndipo anayamba kumutsatira akulemekeza Mulungu.​—Luka 18:43.

Yesu ankasonyeza chifundo kwa anthu omwe anali ndi mavuto pathupi lawo. Takumbukirani uthenga umene anatumiza kwa Yohane M’batizi. Iye anati: “Akhungu akuona, olumala akuyenda, akhate akuyeretsedwa, ogontha akumva, [ndipo] akufa akuukitsidwa.” Poona zozizwitsa zimene Yesu ankachita, “anthu onse . . . anatamanda Mulungu.” (Luka 7:20-22) Akhristu amasangalala kutsanzira Yesu pochitira chifundo anthu omwe ali ndi mavuto pathupi lawo. Choncho timayesetsa kuwakomera mtima, kuwaganizira komanso kuwachitira zinthu moleza mtima. N’zoona kuti Yehova sanatipatse mphamvu yochita zozizwitsa. Koma tili ndi mwayi wouza anthu osaona mwakuthupi komanso mwauzimu uthenga wabwino wonena za dziko latsopano, mmene anthu adzakhala athanzi komanso adzakhala pa ubwenzi wabwino ndi Yehova. (Luka 4:18) Uthenga wabwino umenewu, ukuthandiza kale anthu ambiri kuti azitamanda Mulungu. w21.12 9 ¶5

Lachisanu, October 20

Munamva za kupirira kwa Yobu ndipo mwaona zimene Yehova anamupatsa.​—Yak. 5:11.

Yakobo akamaphunzitsa ankagwiritsa ntchito Malemba. Anagwiritsa ntchito Mawu a Mulungu pothandiza omvera ake kudziwa kuti Yehova nthawi zonse amapereka mphoto kwa anthu amene mofanana ndi Yobu amakhala okhulupirika kwa iye. Yakobo anaphunzitsa mfundo imeneyi pogwiritsa ntchito mawu osavuta kumva komanso motsatirika. Pochita zimenezi iye anathandiza anthu kuti aziganizira kwambiri za Yehova osati iyeyo. Zimene tikuphunzirapo: Uthenga wathu uzikhala wosavuta kumva ndipo tiziphunzitsa pogwiritsa ntchito Mawu a Mulungu. Cholinga chathu chisamakhale kugometsa anthu ndi zimene tikudziwa, koma kuwathandiza kudziwa zimene Yehova amadziwa komanso mmene amawasamalirira. (Aroma 11:33) Tingathe kukwaniritsa cholinga chathuchi ngati nthawi zonse zomwe timanena zimachokera m’Malemba. Mwachitsanzo, m’malo mouza ophunzira Baibulo zimene ifeyo tikanachita tikanakhala iwowo, tiziwathandiza kuganizira zitsanzo za m’Baibulo ndiponso kumvetsa mmene Yehova amaganizira komanso mmene amamvera. Tikatero tidzawathandiza kuti azifunitsitsa kusangalatsa Yehova osati ifeyo. w22.01 11 ¶9-10

Loweruka, October 21

Uzikonda mnzako mmene umadzikondera wekha.​—Lev. 19:18.

Kuwonjezera pa kusachita zinthu zopweteka ena, Mulungu amayembekezeranso kuti tizichita zina zambiri. Mkhristu yemwe amafuna kusangalatsa Mulungu, amayenera kukonda mnzake ngati mmene amadzikondera yekha. Taganizirani mmene Yesu anatsindikira kufunika kwa lamulo lopezeka pa Levitiko 19:18. Mfarisi wina anamufunsa kuti: “Kodi lamulo lalikulu kwambiri m’Chilamulo ndi liti?” Yesu anamuyankha kuti “lamulo lalikulu kwambiri komanso loyamba” ndi lakuti, uzikonda Yehova Mulungu wako ndi mtima wako wonse, moyo wako wonse ndi maganizo ako onse. Kenako, Yesu anatchula mawu a pa Levitiko 19:18, ponena kuti: “Lachiwiri lofanana nalo ndi ili, ‘Uzikonda mnzako mmene umadzikondera wekha.’” (Mat. 22:35-40) Pali njira zambiri zosonyezera chikondi kwa ena. Njira imodzi imene tingasonyezere kuti timakonda anzathu ndi kutsatira malangizo a pa Levitiko 19:18. Lembali limati: ‘Usabwezere choipa kapena kusunga chakukhosi.’ w21.12 10-11 ¶11-13

Lamlungu, October 22

Ataona mphepo yamkuntho, anachita mantha, ndipo atayamba kumira anafuula kuti: “Ambuye, ndipulumutseni!”​—Mat. 14:30.

Yesu anatambasula dzanja lake ndi kum’pulumutsa mtumwi Petulo. Onani kuti Petulo anakwanitsa kuyenda pamadzi pa nthawi yonse imene ankayang’ana Yesu. Koma atangoyang’ana mphepo yamkunthoyo, anachita mantha kwambiri komanso kukayikira moti anayamba kumira. (Mat. 14:24-31) Tingaphuzirepo kanthu pa zimene zinachitikira Petulo. Pamene iye ankatsika m’ngalawa, n’kuyamba kuyenda pamadzi, sankaganiza kuti angachite mantha ndi mphepoyo n’kuyamba kumira. Ankafuna kuyendabe pamadziwo mpaka atafika kumene kunali Mbuye wake. Koma m’malo moyang’ana Yesu iye anayamba kuchita mantha ndi mphepo yamphamvuyo. N’zoona kuti sitingayende pamadzi, koma chikhulupiriro chathu chikhoza kuyesedwa. Ngati titasiya kuganizira kwambiri za Yehova komanso malonjezo ake, chikhulupiriro chathu chikhoza kuchepa chifukwa cha nkhawa ndipo tingayambe kumira mwauzimu. Ndiye kaya takumana ndi mavuto aakulu bwanji pa moyo wathu, tiyenera kupitiriza kuganizira za Yehova komanso kumudalira kuti atithandiza. w21.12 17-18 ¶6-7

Lolemba, October 23

Ndidzalowa m’nyumba yanu chifukwa cha kuchuluka kwa kukoma mtima kwanu kosatha.​—Sal. 5:7.

Pemphero, kuphunzira komanso kuganizira za Yehova ndi mbali ya kulambira kwathu. Tikamapemphera, timakhala tikulankhula ndi Atate wathu wakumwamba yemwe amatikonda kwambiri. Tikamaphunzira Baibulo ‘timamudziwadi Mulungu,’ yemwe ndi mwiniwake wa nzeru zonse. (Miy. 2:1-5) Kuganizira mozama kumatithandiza kuona makhalidwe ochititsa chidwi amene Yehova ali nawo komanso kumatikumbutsa zinthu zabwino zimene iye wakonzera anthu onse. Imeneyi ndi njira yabwino kwambiri yogwiritsira ntchito nthawi yathu. Ndiye kodi n’chiyani chingatithandize kuchita zimenezi? Ngati n’zotheka, muzikhala pamalo opanda phokoso. Asanayambe utumiki wake wapadzikoli, Yesu anakhala m’chipululu masiku 40. (Luka 4:1, 2) Kumalo opanda phokoso amenewa anapemphera kwa Yehova komanso kuganizira mozama zimene Atate wake ankafuna kuti iye achite. Mosakayikira, kuchita zimenezi kunamuthandiza kukonzekera mayesero amene anakumana nawo pambuyo pake. w22.01 27-28 ¶7-8

Lachiwiri, October 24

Aphungu akachuluka [zolingalira] zimakwaniritsidwa.​—Miy. 15:22.

Mkulu kapena m’bale wina angatiuze zinthu zimene tikufunika kukonza. Ngati munthu wina amatikonda kwambiri mpaka kufika potipatsa malangizo ochokera m’Baibulo, tiyenera kutsatira malangizo amene watipatsa. Kunena zoona zingakhale zovuta kuvomereza malangizo amene tikupatsidwa mwachindunji. Mwinanso tikhoza kukhumudwa. Chifukwa chiyani? Ngakhale kuti timavomereza kuti si ife angwiro, komabe zingativute kuvomereza malangizo, munthu wina akatiuza zenizeni zimene talakwitsa. (Mlal. 7:9) Tikhoza kumadziikira kumbuyo. Mwinanso tingamakaikire zolinga za munthu amene watipatsa malangizoyo kapenanso kukhumudwa ndi mmene watipatsira. Tikhozanso kuyamba kumupezera zifukwa n’kumanena kuti: ‘Kodi iyeyu ndi ndani kuti andipatse malangizo? Nayenso amalakwitsa zinthu.’ Komanso ngati malangizo amene tapatsidwa sanatisangalatse, sitingawamvere komanso mwina tikhoza kukafunsa kwa munthu wina amene angatipatse malangizo amene angatikomere. w22.02 8-9 ¶2-4

Lachitatu, October 25

Mudzakhala amphamvu mukakhala osatekeseka ndi achikhulupiriro.—Yes. 30:15.

Kodi m’dziko latsopano tingadzayesedwenso pa nkhani yokhulupirira mmene Yehova amachitira zinthu? Mwachitsanzo, taganizirani zimene zinachitika Aisiraeli atangomasulidwa kumene ku ukapolo ku Iguputo. Ena anayamba kudandaula chifukwa choti sankadyanso zakudya zabwino zimene ankadya ku Iguputo ndipo sankayamikira mana amene Yehova anawapatsa. (Num. 11:4-6; 21:5) Kodi ifenso tingadzakhale ndi maganizo ngati amenewa pambuyo pa chisautso chachikulu? Sitikudziwa kuchuluka kwa ntchito yomwe idzakhalepo yoti tichotse zinthu zomwe zawonongedwa n’kuyamba kukonza dzikoli pang’onopang’ono kuti likhale Paradaiso. N’zodziwikiratu kuti tidzakhala ndi ntchito yambiri komanso mavuto ena chakumayambiriro. Kodi tidzadandaula ndi zimene Yehova adzatipatse pa nthawi imeneyo? Mfundo yosatsutsika ndi yakuti: Tikamayamikira zimene Yehova akutipatsa panopa, n’zosakayikitsa kuti tidzayamikiranso zimene adzatipatse pa nthawiyo. w22.02 7 ¶18-19

Lachinayi, October 26

Adzagwira chovala cha munthu amene ndi Myuda ndi kunena kuti: “Anthu inu tipita nanu limodzi.”—Zek. 8:23.

Mu ulosi wopezeka pa Zekariya 8:23, mawu akuti “Myuda” komanso “anthu inu,” akunena za gulu limodzi la anthu lomwe ndi odzozedwa omwe adakali padzikoli. (Aroma 2:28, 29) “Amuna 10 ochokera m’zilankhulo zonse za anthu a mitundu ina” akuimira a nkhosa zina. Iwo “adzagwira,” kapena kuti kukhalabe okhulupirika kwa odzozedwa, n’kumalambira limodzi Yehova movomerezeka. Pokwaniritsa ulosi wa pa Ezekieli 37:15-19, 24, 25, Yehova wathandiza kuti odzozedwa ndi a nkhosa zina azigwira ntchito limodzi mogwirizana kwambiri. Ulosiwu umatchula za ndodo ziwiri. Amene ali ndi chiyembekezo chodzapita kumwamba, ali ngati ndodo “ya Yuda,” fuko limene munkachokera mafumu a Isiraeli. Ndipo amene ali ndi chiyembekezo chodzakhala padzikoli ali ngati ndodo “ya Efuraimu.” Yehova anati adzagwirizanitsa magulu awiriwa kuti akhale “ndodo imodzi.” Zimenezi zikutanthauza kuti iwo amatumikira mogwirizana motsogoleredwa ndi Mfumu imodzi, Khristu Yesu.​—Yoh. 10:16. w22.01 22 ¶9-10

Lachisanu, October 27

Samalani kuti musamachite chilungamo chanu pamaso pa anthu ndi cholinga chakuti akuoneni.—Mat. 6:1.

Yesu ananena za anthu ena omwe ankathandiza osauka, n’kumafunitsitsa kuti anthu ena adziwe za mphatso zimene apereka. Ngakhale kuti anthuwa ankachita ntchito zabwino, Yehova sankasangalala nazo. (Mat. 6:2-4) Tingasonyeze kuti ndifedi munthu wabwino ngati timachita zoyenera tili ndi zolinga zabwino. Tingadzifunse kuti: ‘Kuwonjezera pakudziwa zoyenera kuchita, kodi ndimayesetsanso kuti ndizizichita? Kodi cholinga changa pochita zabwino chimakhala chiyani?’ Yehova ndi Mulungu amene amachita zinthu ndipo mzimu wake ndi mphamvu yogwira ntchito. (Gen. 1:2) Choncho khalidwe lililonse limene mzimu woyera umatulutsa lizitichititsa kuchitapo kathu. Mwachitsanzo, Yakobo analemba kuti: “Chikhulupiriro chopanda ntchito zake ndi chakufa.” (Yak. 2:26) N’chimodzimodzinso ndi makhalidwe ena amene mzimu wa Mulungu umatulutsa. Nthawi iliyonse imene tasonyeza makhalidwewa, timasonyeza kuti mzimuwo ukugwira ntchito mwa ife. w22.03 11-12 ¶14-16

Loweruka, October 28

Khalani motsanzira Woyera amene anakuitanani. Inunso khalani oyera m’makhalidwe anu onse.​—1 Pet. 1:15.

Tikhoza kumachita zambiri polambira Mulungu ndiponso kumachita ntchito zabwino zambiri. Koma mtumwi Petulo analimbikitsa Akhristu kuchita chinthu china chofunika kwambiri. Iye asanauze Akhristu kuti akhale oyera m’makhalidwe awo onse, anawalimbikitsa kuti: “Konzekeretsani maganizo anu kuti mugwire ntchito mwamphamvu.” (1 Pet. 1:13) Kodi iye ankanena ntchito yotani? Petulo ananena kuti abale ake a Khristu odzozedwa ‘adzalengeza makhalidwe abwino kwambiri a amene anawaitana.’ (1 Pet. 2:9) Ndipotu Akhristu onse masiku ano, ali ndi mwayi wogwira nawo ntchito yofunikayi yomwe imathandiza kwambiri anthu. Monga anthu oyera, tili ndi mwayi waukulu wogwira nawo ntchito yolalikira ndi kuphunzitsa anthu nthawi zonse komanso mwakhama. (Maliko 13:10) Tikamayesetsa kuchita zimenezi, timasonyeza kuti timakonda Mulungu komanso anthu ena. Timasonyezanso kuti tikufuna ‘kukhala oyera’ m’makhalidwe athu onse. w21.12 13 ¶18

Lamlungu, October 29

Chilichonse chimene mwakhululukira munthu ndi mtima wonse, inenso ndimukhululukira chimodzimodzi.​—2 Akor. 2:10.

Nthawi zonse mtumwi Paulo ankaona moyenera abale ndi alongo ake. Ankadziwa kuti munthu akalakwitsa zina zake sizitanthauza kuti ndi woipa. Iye ankawakonda abale ake ndipo ankaganizira kwambiri makhalidwe awo abwino. Iwo akamavutika kuchita zoyenera, iye ankaona kuti zolinga zawo ndi zabwino koma kuti ankangofunika kuthandizidwa. Taganizirani mmene Paulo anathandizira alongo awiri a mumpingo wa ku Filipi. (Afil. 4:1-3) Zikuoneka kuti Eodiya ndi Suntuke, analola kuti kusiyana maganizo pa zinthu zina kuwagawanitse. Paulo sanawachitire zinthu mopanda chifundo kapena kuwaweruza. M’malomwake ankaganizira kwambiri makhalidwe awo abwino. Iwo anali alongo okhulupirika omwe anatumikira Yehova kwa nthawi yaitali. Paulo ankadziwa kuti Yehova ankawakonda. Popeza kuti ankawaona moyenera, iye analimbikitsa alongowa kuti athetse kusamvana kwawo. Kuganizira kwambiri makhalidwe abwino a ena, kunamuthandiza kuti azikhala wosangalala komanso azigwirizana kwambiri ndi anthu a mumpingowo. w22.03 30 ¶16-18

Lolemba, October 30

Yehova ali pafupi ndi anthu a mtima wosweka. Ndipo odzimvera chisoni mumtima mwawo amawapulumutsa.​—Sal. 34:18.

Mtendere umene Yehova amatipatsa umatithandiza kuti mtima wathu ukhale pansi komanso kuti tiziganiza bwino. Zimenezi ndi zomwe zinachitikira mlongo wina dzina lake Luz. Iye anati: “Nthawi zambiri ndimavutika ndi maganizo odziona kuti ndili ndekhandekha. Nthawi zina maganizo amenewa amandichititsa kuona ngati Yehova sandikonda. Koma ndikangoyamba kukhala ndi maganizo amenewa, nthawi yomweyo ndimafotokozera Yehova mmene ndikumvera. Pemphero limandithandiza kuti ndiyambenso kuganiza bwino.” Zimene zinachitikira mlongoyu zikusonyeza kuti tingapeze mtendere tikamapemphera. (Afil. 4:6, 7) Tikudziwa kuti Yehova ndi Yesu angatithandize ngati munthu amene timamukonda wamwalira. Chifundo chizitichititsa kulalikira ndi kuphunzitsa anthu chifukwa Mulungu ndi Yesu Khristu amasonyeza khalidwe labwinoli. Timalimbikitsidwanso kudziwa kuti Yehova ndi Mwana wake wokondedwa amatichitira chifundo pa zofooka zathu komanso amafuna kutithandiza kuti tipirire. Tikuyembekezera tsiku limene Yehova ‘adzapukute misozi yonse m’maso [mwathu].’​—Chiv. 21:4. w22.01 15 ¶7; 19 ¶19-20

Lachiwiri, October 31

Lowani pachipata chopapatiza. Pakuti msewu waukulu ndi wotakasuka ukupita kuchiwonongeko, ndipo anthu ambiri akuyenda mmenemo.​—Mat. 7:13.

Yesu anatchula zipata ziwiri zomwe misewu yake ikulowera kosiyana. Msewu wina ndi “wotakasuka” pomwe winawo ndi “wopanikiza” ndipo palibe msewu wachitatu. (Mat. 7:14) Tiyenera kusankha tokha msewu umene tikufuna kuyendamo. Zimene tingasankhe pankhani yofunika kwambiri imeneyi, n’zomwe zingathandize kuti tidzapeze moyo wosatha. Anthu ambiri akuyenda mumsewu “wotakasuka” chifukwa chakuti ndi wosavuta kuyendamo. N’zomvetsa chisoni kuti anthu ambiri asankha kupitiriza kuyenda mumsewu umenewu n’kumangotsatira chikhamu cha anthu omwe akuyendamo. Iwo sazindikira kuti Satana Mdyerekezi ndi amene amalimbikitsa anthu kuti aziyenda mumsewu umenewu, womwe mathero ake ndi kuchiwonongeko. (1 Akor. 6:9, 10; 1 Yoh. 5:19) Mosiyana ndi msewu ‘wotakasukawu,’ msewu winawu ndi “wopanikiza” ndipo Yesu ananena kuti ndi ochepa amene akuupeza. N’chifukwa chiyani? Onani kuti muvesi lotsatira, Yesu anachenjeza otsatira ake za aneneri onyenga.​—Mat. 7:15. w21.12 22-23 ¶3-5

    Mabuku a Chichewa (1974-2026)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena