Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • es23 tsamba 108-118
  • November

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • November
  • Kuphunzira Malemba Tsiku ndi Tsiku—2023
  • Timitu
  • Lachitatu, November 1
  • Lachinayi, November 2
  • Lachisanu, November 3
  • Loweruka, November 4
  • Lamlungu, November 5
  • Lolemba, November 6
  • Lachiwiri, November 7
  • Lachitatu, November 8
  • Lachinayi, November 9
  • Lachisanu, November 10
  • Loweruka, November 11
  • Lamlungu, November 12
  • Lolemba, November 13
  • Lachiwiri, November 14
  • Lachitatu, November 15
  • Lachinayi, November 16
  • Lachisanu, November 17
  • Loweruka, November 18
  • Lamlungu, November 19
  • Lolemba, November 20
  • Lachiwiri, November 21
  • Lachitatu, November 22
  • Lachinayi, November 23
  • Lachisanu, November 24
  • Loweruka, November 25
  • Lamlungu, November 26
  • Lolemba, November 27
  • Lachiwiri, November 28
  • Lachitatu, November 29
  • Lachinayi, November 30
Kuphunzira Malemba Tsiku ndi Tsiku—2023
es23 tsamba 108-118

November

Lachitatu, November 1

Onse adzaphunzitsidwa ndi Yehova.​—Yoh. 6:45.

Yehova amatithandiza m’njira zosiyanasiyana. Angakuthandizeni kuti muziugwira mtima mukakumana ndi otsutsa, muzikumbukira lemba loyenera loti mukambirane ndi munthu amene wasonyeza chidwi komanso amakupatsani mphamvu kuti muzipitirizabe kulalikira, ngakhale pamene mwakumana ndi anthu amene sakufuna kumvetsera. (Yer. 20:7-9) Yehova amatisonyezanso ubwino wake potiphunzitsa mmene tingagwirire ntchito yolalikira. Pamisonkhano yamkati mwa mlungu, timamvetsera zitsanzo za ulaliki zokonzedwa bwino ndipo timalimbikitsidwa kuzigwiritsa ntchito tikamalalikira. Poyamba tikhoza kumachita mantha kuti tiyesere zinthu zatsopano. Koma tikamagwiritsa ntchito malangizo amene tapatsidwa, tingayambe kuona kuti uthenga wathu ukuwafika pamtima anthu a m’gawo lathu. Pamisonkhano yampingo komanso yachigawo, timalimbikitsidwanso kuti tiziyesa kugwiritsa ntchito njira zina zolalikirira zomwe sitinaziyesepo. Zimenezinso zingamatidetse nkhawa. Komabe tikamazichita, Yehova amatidalitsa. w21.08 27 ¶5-6

Lachinayi, November 2

Muzigwiritsa ntchito bwino nthawi yanu chifukwa masikuwa ndi oipa.​—Aef. 5:16.

M’kalata yake imene analembera Akhristu a ku Korinto, mtumwi Paulo anawapatsa malangizo amphamvu. Pambuyo powalembera kalatayi, anawatumiziranso Tito. Paulo anasangalalatu kwambiri atadziwa kuti anthuwo analandira malangizowo n’kuwatsatira. (2 Akor. 7:6, 7) Akulu angatsanzire Paulo popeza nthawi yomacheza ndi Akhristu anzawo. Njira ina imene angachitire zimenezi ndi kufika mofulumira pamisonkhano n’cholinga choti azicheza ndi kulimbikitsa ena. Nthawi zambiri pamangofunika maminitsi ochepa chabe kuti tilankhule zinthu zomwe zingalimbikitse m’bale kapena mlongo. (Aroma 1:12) Mkulu yemwe amatengera chitsanzo cha Paulo, amalimbitsanso chikhulupiriro cha Akhristu anzake pogwiritsa ntchito Baibulo komanso amawatsimikizira kuti Mulungu amawakonda. Amayesetsa kuwayamikira. Pamene mkuluyo akufunika kupereka malangizo, amaonetsetsa kuti achokera m’Mawu a Mulungu. Iye amapereka malangizo mosapita m’mbali koma mokoma mtima chifukwa amafuna kuti abale ndi alongowo awalandire.​—Agal. 6:1. w22.03 28-29 ¶11-12

Lachisanu, November 3

Tili ndi chuma chimenechi m’zonyamulira zoumbidwa ndi dothi, kuti mphamvu yoposa yachibadwa ichokere kwa Mulungu, osati kwa ife.​—2 Akor. 4:7.

Masiku ano Yehova amapatsa atumiki ake “mphamvu yoposa yachibadwa” kuti apitirize kumutumikira mokhulupirika. Njira imodzi imene Yehova amatipatsira mphamvu ndi kudzera m’pemphero. Pa Aefeso 6:18, mtumwi Paulo amatilimbikitsa kupemphera kwa Mulungu “pa chochitika chilichonse” ndipo iye amatiyankha potipatsa mphamvu. Nthawi zina tikhoza kupanikizika ndi mavuto mwinanso kufika posowa chonena m’pemphero. Komabe Yehova amatiuza kuti tizipemphera kwa iye pamene tikulephera kufotokoza bwinobwino mmene tikumvera. (Aroma 8:26, 27) Iye amatipatsanso mphamvu kudzera m’Baibulo. Paulo ankadalira Malemba kuti azimupatsa mphamvu komanso kumulimbikitsa ndipo ifenso tiyenera kuchita chimodzimodzi. (Aroma 15:4) Tikamawerenga komanso kuganizira mozama Mawu a Mulungu, Yehova angatithandize ndi mzimu wake kumvetsa mmene Malembawo angatithandizire pa zimene zikutichitikira.​—Aheb. 4:12. w21.05 22 ¶8-10

Loweruka, November 4

Mulungu . . . amalimbitsa zolakalaka zanu kuti muchite zinthu zonse zimene iye amakonda.​—Afil. 2:13.

Timaona kuti ntchito yophunzitsa ena ndi yofunika kwambiri ngakhale kuti timakumana ndi mavuto amene angatilepheretse kuchita zambiri pogwira ntchitoyi. Tikhoza kumaona kuti sitingachite zambiri. Mwachitsanzo, ofalitsa ena ndi achikulire kapena amadwaladwala. Kodi umu ndi mmene zilili ndi inu? Ngati ndi choncho, tikudziwa kuti n’zotheka kuchititsa maphunziro a Baibulo opita patsogolo pogwiritsa ntchito zipangizo zamakono. Choncho mukhoza kuyambitsa komanso kumachititsa phunziro la Baibulo muli kunyumba kwanu. Komanso pali ubwino wina. Anthu ena amafuna kuphunzira Baibulo koma sapezeka panyumba pa nthawi imene abale akulalikira. Komabe mwina akhoza kupezeka panyumba m’mawa kwambiri kapena usiku. Kodi mungasinthe zinthu kuti muziphunzira ndi anthu pa nthawi ngati imeneyi? Yesu anaphunzitsa Nikodemo usiku, nthawi imene Nikodemoyo anaona kuti ndi yabwino kwa iye.​—Yoh. 3:1, 2. w21.07 5 ¶10-11

Lamlungu, November 5

Anthu awa ayandikira kwa ine ndi pakamwa pawo pokha, ndipo andilemekeza ndi milomo yawo yokha koma mtima wawo auika kutali ndi ine.​—Yes. 29:13.

Ophunzira a Yohane M’batizi anadabwa kuti ophunzira a Yesu sankasala kudya. Koma Yesu anawauza kuti panalibe chifukwa choti azisalira kudya iye ali moyo. (Mat. 9:14-17) Ngakhale zinali choncho, Afarisi ndi anthu ena amene ankamutsutsa, anamudzudzula chifukwa choti sankachita nawo miyambo yawo. Iwo ankakwiya akaona kuti Yesu wachiritsa munthu patsiku la Sabata. (Maliko 3:1-6; Yoh. 9:16) Anthu amenewa ankanena kuti amasunga Sabata, koma sankaona vuto kuchita malonda m’kachisi. Ndipo anakwiya Yesu atawadzudzula chifukwa cha zimenezi. (Mat. 21:12, 13, 15) Ndiponso anthu amene Yesu anawalalikira m’sunagoge ku Nazareti, anakhumudwa chifukwa choti iye anawafotokozera nkhani za m’Malemba zimene zinasonyeza kuti iwo anali anthu odzikonda komanso opanda chikhulupiriro. (Luka 4:16, 25-30) Popeza Yesu ankachita zinthu zimene ambiri sankayembekezera, zimenezi zinawakhumudwitsa ndipo ambiri anasiya kumutsatira.​—Mat. 11:16-19. w21.05 5-6 ¶13-14

Lolemba, November 6

Tikudziwa bwino ziwembu zake.​—2 Akor. 2:11.

Yehova amatithandiza kupewa mtima wonyada komanso wadyera potilimbikitsa kuti tiziphunzirapo kanthu pa zimene zinachitikira anthu ena. Nthawi zambiri tikamva mawu akuti dyera timakumbukira zimene Satana Mdyerekezi anachita. Popeza kuti anali mngelo wa Yehova ayenera kuti anali ndi mwayi wochita zambiri. Komabe iye sankakhutira ndi zimenezi. Iye ankafuna kuti ena azimulambira ngakhale kuti ndi Yehova yekha amene ayenera kulambiridwa. Satana amafuna kuti tizikhala ngati iyeyo, choncho amatipangitsa kuti tisamakhutire ndi zimene tili nazo. Iye anayamba kuchita zimenezi pa nthawi imene analankhula ndi Hava. Mwachikondi Yehova anapatsa Hava ndi mwamuna wake zakudya zambiri zabwino kuchokera ‘mumtengo uliwonse wa m’mundamo’ kupatulapo mtengo umodzi wokha. (Gen. 2:16) Koma Satana ananamiza Hava pomupangitsa kuganiza kuti ankafunika kudya zipatso za mtengo umene anawaletsawo. Hava sanayamikire zimene anali nazo ndipo ankafunanso zina. Timadziwa bwino zimene zinachitika pambuyo pake. Hava anachimwa ndipo kenako anafa.​—Gen. 3:6, 19. w21.06 14 ¶2-3; 17 ¶9

Lachiwiri, November 7

Muberekane, muchuluke, mudzaze dziko lapansi, ndipo muliyang’anire.​—Gen. 1:28.

Adamu ndi Hava ankafunika kuti abereke ana ndiponso kusamalira dzikoli. Akanamvera n’kumachita zimene Mulungu amafuna, iwo komanso ana awo akanapitiriza kukhala m’banja la Mulungu mpaka kalekale. Adamu ndi Hava anali ndi malo abwino kwambiri m’banja la Yehova. Palemba la Salimo 8:5 komanso mawu a m’munsi palembali, pofotokoza mmene Yehova analengera munthu Davide anati: “Munamuchepetsa pang’ono poyerekeza ndi angelo kenako munamuveka ulemerero ndi ulemu monga chisoti chachifumu.” N’zoona kuti anthu sanapatsidwe mphamvu, nzeru kapena luso ngati angelo. (Sal. 103:20) Komabe munthu ‘anangomuchepetsa pang’ono’ kuyerekeza ndi angelo. N’zomvetsa chisoni kuti Adamu ndi Hava sanamvere Yehova ndipo sanapitirize kukhala m’banja lake. Zimenezi zinachititsa kuti ana awo akumane ndi mavuto aakulu. Koma cholinga cha Yehova sichinasinthe. Iye akufuna kuti anthu omvera adzakhale ana ake mpaka kalekale. w21.08 2-3 ¶2-4

Lachitatu, November 8

“Kuti zinthu zonsezi zichitike, sipakufunika gulu lankhondo, kapena mphamvu, koma mzimu wanga,” watero Yehova.​—Zek. 4:6.

Masiku ano atumiki a Yehova ambiri amatsutsidwa. Mwachitsanzo, ena amakhala m’mayiko amene ntchito yathu ndi yoletsedwa ndipo akhoza kumangidwa ‘n’kutengeredwa kwa abwanamkubwa ndi mafumu’ kuti ukhale umboni kwa iwo. (Mat. 10:17, 18) A Mboni ena amatsutsidwanso m’njira ina. Iwo amakhala m’mayiko amene kulambira Yehova si koletsedwa koma amatsutsidwa ndi achibale omwe amafunitsitsa kuti iwo asiye kulambira Mulungu. (Mat. 10:32-36) Nthawi zambiri, otsutsawo akazindikira kuti zomwe akuchita poyesetsa kufooketsa achibale awo omwe ndi a Mboni sizikuphula kanthu, amasiya. Ndipotu ena omwe ankatsutsidwa, pambuyo pake anakhala abale ndi alongo akhama kwambiri. Inunso mukamatsutsidwa musamafooke. Muzikhala olimba mtima. Yehova amakuthandizani ndi mzimu wake woyera womwe ndi wamphamvu. Choncho palibe choti muziopa. w22.03 16 ¶8

Lachinayi, November 9

Inu okonda Yehova danani nacho choipa.—Sal. 97:10.

Baibulo limasonyeza kuti Yehova amadana ndi ‘maso odzikweza, lilime lonama ndi manja okhetsa magazi a anthu osalakwa.’ (Miy. 6:16, 17) Komanso “munthu wokhetsa magazi ndi wachinyengo, Yehova amaipidwa naye.” (Sal. 5:6) Yehova amadana kwambiri ndi anthu a makhalidwe amenewa moti anawononga anthu onse oipa munthawi ya Nowa chifukwa anadzaza dzikoli ndi zinthu zachiwawa. (Gen. 6:13) Komanso kudzera mwa mneneri Malaki, Yehova ananena kuti amadana ndi anthu amene mwachinyengo amasiya akazi awo omwe ndi osalakwa. Iye savomereza kulambira kwa anthu otere, ndipo adzawaimba mlandu chifukwa cha makhalidwe awo. (Mal. 2:13-16; Aheb. 13:4) Yehova amafuna kuti ‘tizinyansidwa ndi choipa.’ (Aroma 12:9) Mawu akuti ‘kunyansidwa,’ amafotokoza za kuipidwa kwambiri ndi chinthu chinachake. Choncho ngakhale maganizo ofuna kuchita zinthu zimene Yehova amanena kuti n’zoipa, ayenera kukhala chinthu chonyansa kwa ife. w22.03 4-5 ¶11-12

Lachisanu, November 10

Odala ndi anthu onse amene amamuyembekezera.—Yes. 30:18.

Posachedwapa Atate wathu wakumwamba adzatipatsa madalitso ambiri pogwiritsa ntchito Ufumu wake. Anthu amene amayembekezera Yehova amapeza madalitso panopa komanso adzapeza madalitso ochuluka m’dziko limene likubweralo. Anthu a Mulungu akadzalowa m’dziko latsopano sadzafunikanso kupirira mavuto ndi zinthu zodetsa nkhawa zimene amakumana nazo masiku ano. Zinthu zopanda chilungamo zidzakhala mbiri yakale ndipo zopweteka sizidzakhalaponso. (Chiv. 21:4) Sitidzadandaulanso kuti tipeza bwanji zimene timafunikira chifukwa aliyense adzakhala ndi zinthu zochuluka. (Sal. 72:16; Yes. 54:13) Awatu adzakhala madalitso osaneneka. Panopa Yehova akutikonzekeretsa kuti tidzakhale mu Ufumu wake potithandiza kuthetsa makhalidwe amene sasangalala nawo, n’kumakhala ndi makhalidwe abwino. Choncho sitiyenera kutaya mtima kapena kufooka. Moyo wabwino ukubwera posachedwapa. Podikira tsogolo labwinoli, tiyeni tipitirize kuyembekezera moleza mtima kuti Yehova amalize kugwira ntchito yake. w21.08 13 ¶17-19

Loweruka, November 11

Musaiwale kuchita zabwino ndi kugawana zinthu ndi ena, pakuti nsembe zotero Mulungu amakondwera nazo.—Aheb. 13:16.

Pasanapite nthawi yayitali kuchokera pamene analandira kalata ya Paulo, Akhristu a ku Yudeya ankafunika kusiya nyumba, mabizinezi komanso achibale awo omwe sanali Akhristu, ‘n’kuyamba kuthawira kumapiri.’ (Mat. 24:16) N’zosachita kufunsa kuti panthawiyi iwo ankafunika kwambiri kuthandizana. Ngati Akhristuwa akanakhala kuti anali atayamba kale kutsatira malangizo a Paulo akuti azigawana zimene ali nazo, zikanakhala zosavuta kuzolowera moyo wawo watsopano kumene analowera. Si nthawi zonse pamene abale ndi alongo athu angatiuze zomwe akufunikira. Choncho muzikhala ofikirika. Mosakaikira mukudziwa abale ndi alongo mumpingo wanu amene amakhala okonzeka kuthandiza ena. Koma iwo samatichititsa kuti tiziona ngati tikuwavutitsa. Timadziwa kuti tingawadalire tikakumana ndi vuto ndipo timafuna kuwatsanzira. w22.02 23-24 ¶13-15

Lamlungu, November 12

[Tizisunga] umodzi wathu pokhala mwamtendere umene uli ngati chomangira chotigwirizanitsa. Umodziwo timaupeza mothandizidwa ndi mzimu woyera.​—Aef. 4:3.

M’zaka zaposachedwapa mipingo ndi madera ambiri zakonzedwanso. Ngati atatipempha kusamukira mumpingo wina, mwina tingaone kuti n’zovuta kusiyana ndi anzathu komanso achibale. Kodi akulu amauzidwa mwanjira inayake ndi Mulungu kuti asamutsire ofalitsa mumpingo winawake? Ayi. Choncho izi zingachititse kuti zizitivuta kutsatira malangizo omwe tapatsidwa. Koma Yehova amakhulupirira kuti akulu asankha bwino pa nkhani zimenezi ndipo ifenso tiyenera kuwakhulupirira. N’chifukwa chiyani tiyenera kuchita zinthu mogwirizana ndi zimene akulu asankha, ngakhale kuti zimene asankhazo si zimene tikanakonda? Chifukwa tikamachita zimenezi, timathandiza kuti anthu a Mulungu apitirize kukhala ogwirizana. Zinthu zimayenda bwino mumpingo, anthu onse akamatsatira modzichepetsa zimene bungwe la akulu lasankha. (Aheb. 13:17) Koma chofunika kwambiri n’chakuti timamusonyeza Yehova kuti timamukhulupirira tikamachita zinthu mogwirizana ndi anthu omwe wawapatsa udindo wotisamalira.​—Mac. 20:28. w22.02 4-5 ¶9-10

Lolemba, November 13

Pitiriza kukhala wodzipereka powerenga pamaso pa anthu, powadandaulira, ndi powaphunzitsa.​—1 Tim. 4:13.

Ngati ndinu m’bale wobatizidwa, mungamachite khama kuti muwonjezere luso lanu lokamba nkhani komanso kuphunzitsa. Chifukwa chiyani? Chifukwa ‘kudzipereka’ kwanu pa kuwerenga, luso lakulankhula komanso kuphunzitsa kungathandize kwambiri anthu okumvetserani. (1 Tim. 4:15) Mukhozanso kudziikira cholinga chakuti muziphunzira komanso kugwiritsa ntchito mfundo zamuphunziro lililonse m’kabuku kakuti Kuwerenga Komanso Kuphunzitsa Mwaluso. Muziyesa kuphunzira luso limodzi n’kuliyeserera muli kunyumba komanso kugwiritsa ntchito mfundo zake mukamakamba nkhani. Muzipemphanso malangizo kwa mlangizi wothandiza kapena akulu ena omwe “amachita khama kulankhula ndi kuphunzitsa.” (1 Tim. 5:17) Mukamakulitsa luso lomwe mwaphunzira mu phunziro linalake, muzithandizanso omvetsera anu kulimbitsa chikhulupiriro chawo kapenanso kuwalimbikitsa kuti azigwiritsa ntchito zimene aphunzira. Mukamachita zimenezi mudzawonjezera chimwemwe chanu komanso chawo. w21.08 24 ¶17

Lachiwiri, November 14

[Muzidzichepetsa,] ndi kuona ena kukhala okuposani.​—Afil. 2:3.

Ngati timaona ena kukhala otiposa sitidzayamba kuchita mpikisano ndi anthu amene amatha kuchita bwino zinthu zina, kapena ali ndi luso kuposa ifeyo. M’malomwake, tidzayamba kusangalala ndi zimene amakwanitsa kuchita. Ndipo tidzatero makamaka akamagwiritsa ntchito luso lawo potumikira Yehova ndi kumutamanda. Pamapeto pake tonse tidzalimbikitsa mtendere komanso mgwirizano mumpingo. Tingapewe chizolowezi chochitira ena nsanje pokhala odzichepetsa, kapena kuti kuzindikira zimene tingakwanitse kuchita ndi zimene sitingakwanitse. Ngati tili odzichepetsa sitingayambe kudzionetsera kuti tili ndi luso kapena timachita bwino zinthu kuposa wina aliyense. M’malomwake, tidzayamba kuganizira zimene tingaphunzire kwa ena amene ali ndi luso kuposa ifeyo. Tiyerekeze kuti mumpingo muli m’bale wina amene amakamba bwino nkhani, tingamufunse kuti amatani kuti akonzekere bwino nkhani. Ngati mlongo wina amaphika bwino chakudya, tingamufunse kuti atithandize kudziwa zimene tingachite kuti ifenso tiziphika bwino. w21.07 16 ¶8-9

Lachitatu, November 15

[Yehova] sachita chosalungama.​—Deut. 32:4.

M’buku la Numeri timawerenga kuti Yehova anaweruza kuti Mwisiraeli wina aphedwe chifukwa chotola nkhuni pa tsiku la Sabata. Patapita zaka zambiri, malinga ndi zimene zili m’buku la 2 Samueli, Yehova anakhululukira Mfumu Davide atachita tchimo lachigololo komanso kupha munthu. (Num. 15:32, 35; 2 Sam. 12:9, 13) Ndiye mwina tingadabwe kuti: ‘N’chifukwa chiyani Yehova anakhululukira Davide, yemwe anapha munthu komanso kuchita chigololo, koma n’kuweruza kuti munthu amene anachita tchimo looneka ngati laling’ono aphedwe?’ Nthawi zina Baibulo silifotokoza mfundo zonse zokhudza nkhani inayake. Mwachitsanzo, timadziwa kuti Davide analapa mochokera pansi pa mtima pa zimene anachita. (Sal. 51:2-4) Koma bwanji za munthu yemwe anaphwanya lamulo la Sabata uja? Kodi anadzimvera chisoni chifukwa cha zimene anachita? Kodi analepherapo kumvera malamulo ena a Yehova m’mbuyomo? Kodi ananyalanyaza kapena kukana kumvera machenjezo omwe anapatsidwapo? Baibulo silinena. Komabe zochuluka zomwe timadziwa zokhudza Mulungu wathu zimatitsimikizira kuti iye “ndi wolungama m’njira zake zonse.”​—Sal. 145:17. w22.02 2-3 ¶3-4

Lachinayi, November 16

Nzeru zimakhala ndi anthu odzichepetsa.​—Miy. 11:2.

Mukamazindikira zimene mungakwanitse kuchita zingakuthandizeni kuti musamayembekezere kuchita zambiri kuposa zimene simungakwanitse. Mukamatero muzikhalabe osangalala komanso muzichita khama. Tingayerekezere zimenezi ndi munthu amene akuyendetsa galimoto pamalo okwera. Woyendetsa galimotoyo amafunika kuika giya yochepa yomwe imakhala yamphamvu, n’cholinga choti ipitirizebe kukwera mtundawo. N’zoona kuti galimotoyo imayenda pang’onopang’ono komabe ulendowo umapitirira. Mofanana ndi zimenezi, munthu amene amazindikira zimene sangakwanitse kuchita, amadziwa nthawi imene ayenera “kubweza magiya” n’cholinga choti apitirize kutumikira Yehova komanso kuthandiza ena. (Afil. 4:5) Taganizirani chitsanzo cha Barizilai yemwe anali ndi zaka 80 pamene Mfumu Davide inamuitana kuti azikakhala kunyumba yachifumu. Barizilai anakana mwayi umene mfumu inamupatsa. Poganizira zimene sakanatha kuchita, iye anapempha kuti Chimamu yemwe anali wachinyamata apite m’malomwake. (2 Sam. 19:35-37) Mofanana ndi Barizilai, abale achikulire amasangalala kupereka mwayi wa utumiki kwa achinyamata. w21.09 10 ¶6-7

Lachisanu, November 17

Atatewo palibe amene akuwadziwa bwino koma Mwana yekha ndiponso amene Mwanayo wakonda kuwaululira za Atatewo.​—Luka 10:22.

Kodi zimakuvutani kuti muziona Yehova ngati Atate wachikondi? Ena zimawavuta. Mwina chifukwa cha mmene tinaleredwera zingativute kumvetsa kuti pali makolo achikondi. N’zolimbikitsa kudziwa kuti Yehova amamvetsa mmene timamvera. Iye amafuna kukhala nafe pa ubwenzi. N’chifukwa chake Mawu ake amatilimbikitsa kuti: “Yandikirani Mulungu, ndipo iyenso adzakuyandikirani.” (Yak. 4:8) Yehova amatikonda ndipo amatiuza kuti adzakhala Atate wathu wabwino kwambiri. Yesu angatithandize kuti tikhale pa ubwenzi ndi Yehova. Iye amamudziwa bwino Yehova ndipo amatsanzira kwambiri makhalidwe ake moti ananena kuti: “Amene waona ine waonanso Atate.” (Yoh. 14:9) Mofanana ndi mwana wamkulu m’banja, Yesu amatiphunzitsa zimene tingachite kuti tizilemekeza komanso kumvera Atate wathu, kupewa kuwakhumudwitsa komanso kuti azisangalala nafe. Zimene Yesu anachita ali padzikoli, zimatithandizanso kwambiri kumvetsa kuti Yehova ndi wokoma mtima komanso wachikondi. w21.09 21 ¶4-5

Loweruka, November 18

Wetani gulu la nkhosa za Mulungu lomwe analisiya m’manja mwanu.​—1 Pet. 5:2.

Anthu a Yehova amakhala ogwirizana polambira Mulungu woona yekha. Yehova anapatsa akulu udindo waukulu woonetsetsa kuti mpingo ukhale woyera. Ngati Mkhristu wachita tchimo lalikulu, Yehova amayembekezera kuti akulu aone ngati munthuyo akufunika kupitiriza kukhala mumpingo. Mwa zina, iwo amafunika kufufuza kuti adziwe ngati munthuyo akudzimveradi chisoni chifukwa cha tchimo lakelo. Munthu angamanene kuti walapa, koma kodi akudanadi ndi zimene anachita? Kodi watsimikiza kuti sadzabwerezanso tchimolo? Ngati anachita tchimolo chifukwa chogwirizana ndi anthu oipa, kodi iye ndi wofunitsitsa kusiya kugwirizana nawo? Akulu amapempherera nkhaniyo, kufufuza mfundo za m’Malemba komanso kuona mmene munthuyo akuganizira. Akatero amaona ngati wochimwayo angapitirize kukhala mumpingo. Nthawi zina wochimwayo amafunika kuchotsedwa.​—1 Akor. 5:11-13. w22.02 5 ¶11-12

Lamlungu, November 19

Muvale umunthu watsopano.—Akol. 3:10.

Kaya tangobatizidwa kumene kapena tinabatizidwa zaka zambiri m’mbuyomu, tonsefe timafuna kukhala ndi makhalidwe amene Yehova amasangalala nawo. Kuti zimenezi zitheke tiyenera kulamulira maganizo athu chifukwa nthawi zambiri, zimene timaganiza ndi zomwe zimachititsa kuti tikhale ndi makhalidwe amene tili nawo. Ngati nthawi zambiri timaganizira zimene thupi lathu limalakalaka, tikhoza kulankhula kapena kuchita zoipa. (Aef. 4:17-19) Koma ngati nthawi zambiri timaganizira zinthu zabwino, tikhoza kumalankhula kapena kuchita zinthu zimene zingasangalatse Atate wathu Yehova. (Agal. 5:16) Komabe sitingapeweretu maganizo onse oipa. Koma tikhoza kusankha kuti tisamachite zimene timaganizazo. Tisanabatizidwe tiyenera kusiya kulankhula kapena kuchita zinthu zimene Yehova amadana nazo. Chimenechi ndi chinthu choyamba komanso chofunika kwambiri kuchita kuti tivule umunthu wakale. Komanso kuti tizisangalatsa kwambiri Yehova tiyenera kuvala umunthu watsopano. w22.03 8 ¶1-2

Lolemba, November 20

Mwanjira ina iliyonse, munasonyeza kuti ndinu oyera pa nkhani imeneyi.​—2 Akor. 7:11.

Si zophweka kuti akulu adziwe ngati munthu amene wachita tchimo walapadi zenizeni. N’chifukwa chiyani tikutero? Akulu sangadziwe zimene zili mumtima mwa munthu. Choncho amayesetsa kupeza umboni wosonyeza kuti m’bale wawoyo akudana ndi zimene anachitazo. Iwo angafunike kuona umboni wosonyeza kuti munthuyo wasintha kuchokera pansi pamtima mmene amaganizira, mmene amaonera zinthu komanso zochita zake. Zingamutengere nthawi yaitali munthu ameneyo kuti asinthe. Posonyeza kuti walapa kuchokera pansi pamtima, munthu amene wachotsedwa amafika pamisonkhano mokhazikika, ndipo amatsatira malangizo a akulu oti azipemphera nthawi zonse komanso kuphunzira Baibulo. Iye amayesetsanso kupewa zinthu zimene zinamuchititsa kuti achite tchimo. Ngati atayesetsa kukonza ubwenzi wake ndi Yehova sangakayikire kuti iye amukhululukira ndi mtima wonse komanso akulu angamubwezeretse mumpingo. w21.10 6 ¶16-18

Lachiwiri, November 21

Usadzipangire fano kapena chifaniziro cha chinthu chilichonse chakumwamba, kapena chapadziko lapansi, . . . Usaziweramire.​—Eks. 20:4, 5.

Ali kumwamba komanso padzikoli, Yesu ankalambira Yehova yekha chifukwa chomukonda kwambiri. (Luka 4:8) Iye anaphunzitsanso ophunzira ake kuti azilambira Yehova yekha. Yesu ngakhalenso ophunzira ake okhulupirika sanagwiritsirepo ntchito zifaniziro polambira. Mulungu ndi mzimu, choncho palibe munthu amene angapange chinthu chooneka ngati iye. (Yes. 46:5) Nanga bwanji pa nkhani yopanga komanso kupemphera kwa zifaniziro za anthu omwe ena amati ndi oyera? Mulamulo lachiwiri pa Malamulo Khumi, Yehova ananena mawu a mulemba la lero. Mawu amenewa ndi omveka bwino kwa anthu amene amafuna kusangalatsa Mulungu. Olemba mbiri amavomereza kuti Akhristu oyambirira ankalambira Mulungu yekha. Masiku ano a Mboni za Yehova amatsatira njira yolambirira imene Akhristu oyambirira ankagwiritsa ntchito. w21.10 19-20 ¶5-6

Lachitatu, November 22

Munthu amene ali padenga la nyumba asadzatsike kukatenga katundu m’nyumba mwake.—Mat. 24:17.

Yesu anachenjeza Akhristu a ku Yudeya kuti pa nthawi ina ‘magulu a nkhondo adzazungulira’ Yerusalemu. (Luka 21:20-24) Iwo ankafunika kuti akadzaona zimenezi “adzayambe kuthawira kumapiri.” Kuthawako kukanachititsa kuti apulumuke, komabe ankafunika kusiya zinthu zambiri. Nsanja ya Olonda ina m’mbuyomu inanena kuti: “Iwo anasiya minda, nyumba ndipo sanatenge ngakhale katundu wa m’nyumba zawo. Ankakhulupirira kuti Yehova adzawateteza komanso kuwathandiza ndipo ankaona kuti kumulambira n’kofunika kwambiri kuposa china chilichonse.” Nsanjayo inawonjezeranso kuti: “M’tsogolomu tingadzakumane ndi mayesero okhudza mmene timaonera zinthu zimene tili nazo. Kodi timaona kuti zinthu zimenezi ndi zofunika kwambiri? Kapena timaona kuti chofunika kwambiri ndi kupulumuka kwa anthu onse omwe ali kumbali ya Mulungu? Mapeto akadzafika tingadzakumane ndi mavuto ndipo mwinanso tingadzafunike kusiya zinthu zina. Tidzayenera kukhala okonzeka kuchita chilichonse chimene chingafunike kuti tipulumuke.” w22.01 4 ¶7-8

Lachinayi, November 23

Inu Mulungu, kukoma mtima kwanu kosatha ndi kwamtengo wapatali!—Sal. 36:7.

Pasanapite nthawi yaitali kuchokera pamene Aisiraeli anachoka ku Iguputo, Yehova anadziulula yekha kwa Mose pamene ankalengeza dzina lake ndi makhalidwe ake. Iye anati: “Yehova, Yehova, Mulungu wachifundo ndi wachisomo, wosakwiya msanga ndiponso wodzaza ndi kukoma mtima kosatha [chikondi chokhulupirika] ndi choonadi. Wosungira mibadwo masauzande kukoma mtima kosatha, wokhululukira zolakwa ndi machimo.” (Eks. 34:6, 7) M’mawu okhudza mtima amenewa onena za makhalidwe ake, Yehova anaulula kwa Mose kanthu kena kapadera kokhudza chikondi chake chokhulupirika. Kodi iye anati chiyani? Yehova sanangodzifotokoza kuti ali ndi chikondi chokhulupirika, iye anati ndi “wodzaza” ndi chikondi chokhulupirika. Ndipotu mawu amenewa amapezekanso m’malo ena 6 m’Baibulo. (Num. 14:18; Neh. 9:17; Sal. 86:15; 103:8; Yow. 2:13; Yona 4:2) M’malo onsewa, mawuwa amanena za Yehova yekha osati anthu. Kodi sizochititsa chidwi kuona kuti Yehova mwiniwakeyo amatsindika kwambiri za chikondi chake chokhulupirika? w21.11 2-3 ¶3-4

Lachisanu, November 24

Lekani kudera nkhawa moyo wanu.​—Mat. 6:25.

Anthu omwe ali pabanja angaphunzirepo kanthu pa chitsanzo cha mtumwi Petulo ndi mkazi wake. Patapita pafupifupi miyezi 6 kapena chaka kuchokera pa nthawi yoyamba imene anakumana ndi Yesu, mtumwi Petulo ankafunika kusankha zochita pa nkhani yofunika kwambiri. Petulo ankapeza zofunika pa moyo kudzera muntchito yausodzi. Choncho pamene Yesu anamuitana kuti amutsatire, iye ankafunika kuganiziranso za banja lake. (Luka 5:1-11) Petulo anasankha kuti aziyenda limodzi ndi Yesu pa ntchito yolalikira. Ndipo mkazi wake ayenera kuti anagwirizana ndi zomwe iye anasankhazi. Baibulo limasonyeza kuti Yesu ataukitsidwa, mkazi wa Petulo ankayenda limodzi ndi mwamuna wake pa maulendo ena. (1 Akor. 9:5) N’zosakayikitsa kuti chitsanzo chake chinathandiza kuti Petulo akhale ndi ufulu wolankhula n’kulemba malangizo ouziridwa othandiza mabanja a Chikhristu. (1 Pet. 3:1-7) N’zodziwikiratunso kuti Petulo ndi mkazi wake ankakhulupirira lonjezo la Yehova loti adzawasamalira akamaika zinthu zokhudza Ufumu pamalo oyamba pa moyo wawo.​—Mat. 6:31-34. w21.11 18 ¶14

Loweruka, November 25

Muzitsanzira ine.​—1 Akor. 11:1.

Mtumwi Paulo ankakonda abale ake ndipo ankagwira ntchito mwakhama kuti awathandize. (Mac. 20:31) Zimenezi zinachititsa kuti abale ndi alongo ake nawonso azimukonda kwambiri. Pa nthawi ina akulu a ku Efeso “analira kwambiri” atamva kuti sadzaonana nayenso. (Mac. 20:37) Akulu odzipereka nawonso amakonda abale ndi alongo awo ndipo amachita zonse zomwe angathe powathandiza. (Afil. 2:16, 17) Koma nthawi zina akulu amakumana ndi mavuto ena. Ndiye kodi n’chiyani chingawathandize kulimbana ndi mavuto amenewa? Akulu akhamawa ayenera kuganizira chitsanzo cha Paulo. Iye sanali munthu wapadera, chifukwa sanali wangwiro ndipo nthawi zina ankavutika kuchita zabwino. (Aroma 7:18-20) Nthawi zinanso ankafunika kulimbana ndi mavuto osiyanasiyana. Koma zimenezi sizinamuchititse kutaya mtima kapenanso kuti asamasangalale. Akulu akamatsanzira Paulo, angathe kulimbana ndi mavuto amene amakumana nawo n’kupitirizabe kukhala osangalala akamatumikira Yehova. w22.03 26 ¶1-2

Lamlungu, November 26

Muzisunga masabata anga. Ine ndine Yehova Mulungu wanu.​—Lev. 19:3.

Lemba la Levitiko 19:3, limanena za kusunga Sabata. Akhristu satsatiranso Chilamulo, choncho sitimasunga Sabata. Komabe tingaphunzire zambiri pa zimene Aisiraeli ankachita posunga Sabata komanso mmene kuchita zimenezi kunkawathandizira. Tsiku la Sabata linali nthawi imene ankapuma pa ntchito zimene ankagwira ndipo linkawapatsa mwayi wolambira Yehova. N’chifukwa chake pa tsikuli, Yesu ankapita ku sunagoge m’tauni yakwawo kukawerenga Mawu a Mulungu. (Eks. 31:12-15; Luka 4:16-18) Lamulo la Mulungu lopezeka pa Levitiko 19:3 lakuti, “muzisunga masabata anga,” likutiphunzitsa kuti tsiku lililonse tiyenera kumapeza nthawi yochita zinthu zokhudza kulambira. Kodi inuyo mukuona kuti pali zina zimene muyenera kusintha pa nkhani imeneyi? Ngati nthawi zonse mumapeza nthawi yochita zinthu zokhudza kulambira, mudzakhala pa ubwenzi wabwino ndi Yehova zomwe ndi zofunika kwambiri kuti mukhale woyera. w21.12 5 ¶13

Lolemba, November 27

Ine sindinabwere kudzaitana anthu olungama, koma ochimwa kuti alape.​—Luka 5:32.

Pamene Yesu anali padzikoli, ankachita zinthu ndi aliyense. Mwachitsanzo, iye ankadya ndi anthu olemera komanso audindo koma nthawi zambiri ankachitanso zinthu ndi osauka ndiponso oponderezedwa. Kuwonjezera apo, ankachitiranso chifundo anthu omwe ambiri ankawaona ngati “ochimwa.” Koma anthu ena odziona ngati olungama anakhumudwa ndi zimene Yesu ankachitazi. Iwo anafunsa ophunzira ake kuti: “N’chifukwa chiyani inu mumadya ndi kumwa limodzi ndi okhometsa msonkho ndi anthu ochimwa?” Poyankha, Yesu anawauza mawu a mulemba lalerowa. (Luka 5:29-31) Kudakali zaka zambiri kuti Mesiya abwere, mneneri Yesaya ananeneratu kuti anthu adzamukana. Ulosiwo unanena kuti: “Iye ananyozedwa ndipo anthu anali kumupewa. . . . Ife tinali kuyang’ana kumbali kuti tisaone nkhope yake. Ananyozedwa ndipo tinamuona ngati wopanda pake.” (Yes. 53:3) Popeza Mesiya anali woti “anthu” azidzamupewa, Ayuda a m’nthawi ya Yesu ankayenera kuyembekezera kuti iye azikanidwa. w21.05 8-9 ¶3-4

Lachiwiri, November 28

Yehova adzamulimbitsa.​—Yak. 5:15.

Akhristu ena a m’nthawi ya atumwi ankachedwa kutsatira malangizo. (Yak. 1:22) Ena ankakondera anthu olemera. (Yak. 2:1-3) Ndiye panalinso ena omwe ankavutika kulamulira lilime lawo. (Yak. 3:8-10) Akhristuwa anali ndi mavuto akulu koma Yakobo ankakhulupirira kuti iwo akhoza kusintha. Iye anawapatsa malangizo mokoma mtima koma mosapita m’mbali ndipo analimbikitsa Akhristu omwe ankakumana ndi mavutowo kuti azipempha akulu kuti awathandize. (Yak. 5:13, 14) Zimene tikuphunzirapo: Tizipereka malangizo mosapita m’mbali ndipo tiziona ena moyenera. N’kutheka kuti ambiri amene tikuphunzira nawo Baibulo zingamawavute kutsatira malangizo ake. (Yak. 4:1-4) Mwina zingawatengere nthawi kuti asiye makhalidwe oipa n’kuyamba kukhala ndi makhalidwe ngati a Khristu. Tiyenera kukhala olimba mtima kuti tizitha kuuza ophunzira Baibulo zimene ayenera kusintha. Tiyeneranso kukhala ndi maganizo oyenera n’kumakhulupirira kuti Yehova adzakokera kwa iye anthu amene ndi odzichepetsa ndipo adzawapatsa mphamvu zowathandiza kusintha zinthu pa moyo wawo.​—Yak. 4:10. w22.01 11 ¶11-12

Lachitatu, November 29

Aliyense wotseka khutu lake kuti asamve kudandaula kwa munthu wonyozeka, nayenso adzaitana koma sadzayankhidwa.​—Miy. 21:13.

Akhristu onse amayesetsa kutsanzira chifundo cha Yehova. N’chifukwa chiyani? Chifukwa chimodzi n’chakuti Yehova samvetsera mapemphero a anthu amene sachitira chifundo anzawo. Palibe yemwe angafune kuti Yehova asamamvetsere mapemphero ake. Choncho tizipewa kukhala anthu ouma mtima. M’malo mokana kumvetsera Mkhristu mnzathu akamatifotokozera mavuto ake, nthawi zonse tiyenera kukhala okonzeka kumvetsera “kudandaula kwa munthu wonyozeka.” Choncho tiziyesetsa kukumbukira mfundo yakuti: “Wosachita chifundo adzaweruzidwa mopanda chifundo.” (Yak. 2:13) Tikamazindikira kuti ifenso tikufunikira kusonyezedwa chifundo ndi pamenenso zimakhala zosavuta kusonyeza ena chifundo. Tiyenera kusonyeza chifundo makamaka pamene munthu walapa n’kubwerera mumpingo. Zitsanzo za m’Baibulo za anthu omwe anali okoma mtima komanso achifundo zingatithandize kuti tizichitira ena chifundo nkumapewa kukhala anthu ouma mtima. w21.10 12 ¶16-17

Lachinayi, November 30

Khalani pansi pompano, ine ndikupita uko kukapemphera.​—Mat. 26:36.

Pa usiku wake womaliza padzikoli, pamene utumiki wake unkapita kumapeto, Yesu anapita kumalo opanda phokoso kuti akaganizire kwambiri za Yehova komanso kupemphera. Malo opanda phokosowa anawapeza m’munda wa Getsemane. Pa nthawiyi, Yesu anapatsa ophunzira ake malangizo a panthawi yake okhudza kupemphera. Pamene ankafika m’munda wa Getsemane, unali usiku kwambiri, mwinanso kudutsa pakati pa usiku. Iye anauza atumwi kuti ‘akhale maso’ ndipo kenako anapita kukapemphera. (Mat. 26:37-39) Koma pamene iye ankapemphera, atumwiwo anagona. Atawapeza akugona, Yesu anawauzanso kachiwiri kuti ‘akhale maso ndi kupemphera mosalekeza.’ (Mat. 26:40, 41) Iye anadziwa kuti iwo anali ndi nkhawa kwambiri ndiponso anali atatopa. Mwachifundo Yesu anavomereza kuti “thupi ndi lofooka.” Ngakhale zinali choncho, Yesu anapita maulendo ena awiri kukapemphera ndipo ulendo uliwonse akabwera ankapeza ophunzirawo akugona m’malo mopemphera.​—Mat. 26:42-45. w22.01 28 ¶10-11

    Mabuku a Chichewa (1974-2026)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena