January
Lolemba, January 1
Ndikukutumizirani Timoteyo, popeza iye ndi mwana wanga wokondedwa ndi wokhulupirika mwa Ambuye. —1 Akor. 4:17.
Kodi n’chiyani chinathandiza Timoteyo kukhala mtumiki wabwino wa Yehova? Ndi makhalidwe abwino amene anali nawo. (Afil. 2:19-22) Tikaona mmene mtumwi Paulo anafotokozera zokhudza Timoteyo, tinganene kuti iye anali wodzichepetsa, wokhulupirika, wakhama komanso wodalirika. Iye ankadera nkhawa kwambiri abale. Zimenezi zinachititsa kuti Paulo azimukonda ndipo sankakayikira kuti akwanitsa mautumiki ovuta omwe anam’patsa. Mofanana ndi zimenezi, ifenso Yehova angamatikonde ndipo tingakhale othandiza kwambiri mumpingo tikakhala ndi makhalidwe omwe amamusangalatsa. (Sal. 25:9; 138:6) Choncho muzipemphera n’kuganizira mbali ya umunthu wanu imene muyenera kusintha. Muzisankha khalidwe linalake limene mukufuna kukulitsa. Kodi mukufunitsitsa kuti muzisonyeza kwambiri ena chifundo? Kodi mukufunitsitsa kuti muzikhala mwamtendere ndi ena komanso muzikhululuka? Mungachite bwino kufunsa mnzanu wodalirika kuti akuthandizeni kudziwa zimene mungachite kuti mupite patsogolo.—Miy. 27:6. w22.04 23 ¶4-5
Lachiwiri, January 2
Aliyense payekha ayese zochita zake.—Agal. 6:4.
Yehova amafuna kuti tizisangalala. Tikudziwa zimenezi chifukwa chimwemwe ndi limodzi mwa makhalidwe omwe mzimu woyera umatulutsa. (Agal. 5:22) Popeza kuti kupatsa kumabweretsa chimwemwe chochuluka kuposa kulandira, timasangalala kwambiri tikamagwira nawo mwakhama ntchito yolalikira komanso kuthandiza abale athu m’njira zosiyanasiyana. (Mac. 20:35) Monga mmene lemba lalero likusonyezera, mtumwi Paulo anatchula zinthu ziwiri zimene zingatithandize kupitirizabe kukhala osangalala. Choyamba, cholinga chathu chiyenera kukhala kupatsa Yehova zinthu zabwino koposa zomwe tingathe. Tikamamupatsa zonse zomwe tingathe, tingamakhale osangalala. (Mat. 22:36-38) Chachiwiri, tizipewa kudziyerekezera ndi ena. Tiyenera kuyamikira Yehova pa zilizonse zimene timakwanitsa kuchita chifukwa cha thanzi, maphunziro kapena luso limene tili nalo. Komanso ngati ena ali ndi luso pambali zina za utumiki kuposa ifeyo, tiyenera kumasangalala kuti akugwiritsa ntchito luso lawo potamanda Yehova. w22.04 10 ¶1-2
Lachitatu, January 3
Chipulumutso chanu chikuyandikira.—Luka 21:28.
Mapeto a zipembedzo zonyenga adzabwera modzidzimutsa, zomwe zidzadabwitse anthu ambiri. (Chiv. 18:8-10) Kuwonongedwa kwa Babulo Wamkulu kudzagwedeza dziko lonse ndipo mwina kudzachititsa kuti pakhale mavuto. Komabe anthu a Mulungu adzakhala ndi zifukwa ziwiri zosangalalira. Mdani wa Yehova ameneyu, yemwe wakhalako kwa nthawi yaitali sadzakhalakonso. Komanso tidzakhala titatsala pang’ono kuti tipulumutsidwe ku dziko loipali. Danieli analosera kuti anthu “adzadziwa zinthu zambiri zoona.” Ndipo n’zimene zakhala zikuchitikadi. Panopa timamvetsa maulosi okhudza nthawi yathu ino. (Dan. 12:4, 9, 10) Timagoma kwambiri ndi Yehova komanso Mawu ake tikaona mmene maulosiwa akukwaniritsidwira. (Yes. 46:10; 55:11) Choncho pitirizani kulimbitsa chikhulupiriro chanu pophunzira Malemba mwakhama komanso pothandiza ena kuti akhale pa ubwenzi wabwino ndi Yehova. Iye adzateteza onse omwe amamudalira ndipo adzapitiriza kuwapatsa “mtendere wosatha.”—Yes. 26:3. w22.07 6-7 ¶16-17
Lachinayi, January 4
Anawasonkhanitsa pamodzi, kumalo amene m’Chiheberi amatchulidwa kuti Aramagedo.—Chiv. 16:16.
Buku la Chivumbulutso limafotokoza kuti Ufumu wa Mulungu unakhazikitsidwa kumwamba ndipo Satana anathamangitsidwako. (Chiv. 12:1-9) Zimenezi zinachititsa kuti kumwamba zinthu ziziyenda bwino, koma zinabweretsa mavuto padzikoli. Chifukwa chiyani? Chifukwa Satana ndi wokwiya ndipo akulimbana ndi anthu omwe akutumikira Yehova mokhulupirika. (Chiv. 12:12, 15, 17) Kodi n’chiyani chingatithandize kukhalabe okhulupirika kwa Yehova ngakhale kuti Satana akulimbana nafe? (Chiv. 13:10) Chinthu chimodzi ndi kudziwa zomwe zichitike m’tsogolomu. Mwachitsanzo, m’buku la Chivumbulutso mtumwi Yohane anafotokoza ena mwa madalitso omwe tidzasangalale nawo posachedwapa, monga kuwonongedwa kwa adani a Mulungu. Muvesi loyambirira, buku la Chivumbulutso likutiuza kuti zimene timawerenga m’bukuli zikufotokozedwa “pogwiritsa ntchito zizindikiro.”—Chiv. 1:1. w22.05 8 ¶1-3
Lachisanu, January 5
M’masiku otsiriza, ine ndidzakubweretsa kuti uukire dziko langa n’cholinga choti anthu a mitundu ina adzandidziwe ndikamadzadziyeretsa pamaso pawo, kudzera mwa iwe Gogi.—Ezek. 38:16.
Zimene atumiki a Mulungu okhulupirika adzachite pokhalabe okhulupirika zidzakwiyitsa kwambiri anthu omwe amatsutsa Yehova. Zotsatira zake n’zakuti mgwirizano wa mayiko udzaukira anthu a Mulungu padziko lonse. Baibulo linaneneratu kuti zimene mayiko adzachitezi ndi kuukira kwa Gogi wa ku Magogi. (Ezek. 38:14, 15) Kodi Yehova adzatani ndi kuukira kwankhanza kumeneku? Iye amatiuza kuti: “Ndidzakhala ndi mkwiyo waukulu.” (Ezek. 38:18, 21-23) Pa Chivumbulutso 19 amafotokoza zimene zidzachitike pambuyo pake. Yehova adzatumiza Mwana wake kuti akateteze anthu ake komanso kugonjetsa adani awo. Yesu adzamenya nkhondoyi pamodzi ndi “magulu a nkhondo akumwamba,” omwe ndi angelo okhulupirika komanso a 144,000. (Chiv. 17:14; 19:11-15) Kodi zotsatirapo za nkhondoyi zidzakhala zotani? Anthu komanso mabungwe omwe amatsutsa Yehova adzawonongedweratu.—Chiv. 19:19-21. w22.05 17 ¶9-10
Loweruka, January 6
Ndidzaika chidani pakati pa iwe ndi mkaziyo.—Gen. 3:15.
Adamu ndi Hava atangochimwa, Yehova ananena ulosi wofunika womwe unapereka chiyembekezo kwa ana awo. Ulosi wake uli pa Genesis 3:15 ndipo umati: “Ndidzaika chidani pakati pa iwe ndi mkaziyo, komanso pakati pa mbadwa yako ndi mbadwa yake. Mbadwa ya mkaziyo idzaphwanya mutu wako, ndipo iwe udzaivulaza chidendene.” Ulosiwu umapezeka m’buku loyamba la Baibulo. Komabe mwa njira ina yake mabuku onse a m’Baibulo amagwirizana ndi ulosiwu. Mofanana ndi simenti yomwe imagwirizanitsa njerwa za khoma la nyumba, mawu a pa Genesis 3:15 amathandiza kuti uthenga wa m’mabuku onse a m’Baibulo ukhale wogwirizana. Uthenga wake ndi wakuti Mulungu adzatumiza Mpulumutsi yemwe adzawononge Mdyerekezi ndi oipa onse omwe amamutsatira. Amenewatu ndi madalitso aakulu kwa omwe amakonda Yehova. Kuphunzira Baibulo kumatithandiza kuona mmene ulosiwu ukukwaniritsidwira ndiponso mmene ifeyo tingapindulire ndi zimenezi. w22.07 14 ¶1-3
Lamlungu, January 7
Yehova ndi amene amapereka nzeru.—Miy. 2:6.
Muzipempha Yehova kuti akupatseni nzeru zomwe mukufunikira kuti muthandize ana anu kuyamba kumukonda. (Yak. 1:5) Iye ndi amene angakupatseni malangizo abwino kwambiri. Tikutero pazifukwa zingapo. Taganizirani zifukwa ziwiri izi. Choyamba, Yehova ndi amene wakhala kholo kwa nthawi yaitali. (Sal. 36:9) Ndipo chachiwiri, nthawi zonse malangizo anzeru omwe amapereka amakhala othandiza. (Yes. 48:17) Pogwiritsa ntchito Mawu ake komanso gulu lake, Yehova amapereka chakudya chauzimu chochuluka chomwe chingakuthandizeni kuphunzitsa ana anu kuti azimukonda. (Mat. 24:45) Mwachitsanzo, mungathe kupeza malangizo ambiri othandiza munkhani zakuti “Malangizo Othandiza Mabanja,” zomwe zinkapezeka m’magazini a Galamukani! kwa zaka zingapo ndipo pano zikupezeka pawebusaiti yathu. Komanso, mavidiyo ambiri opezeka pa jw.org amakhala ndi mbali yocheza ndi ena komanso zitsanzo zomwe zingathandize makolo kugwiritsa ntchito malangizo a Yehova akamalera ana awo.—Miy. 2:4, 5. w22.05 27 ¶4-5
Lolemba, January 8
Mukanakhala kuti mumayang’anitsitsa zolakwa, ndi ndani akanaima pamaso panu, inu Yehova?—Sal. 130:3.
Yehova ndi amene amakhululuka kwambiri m’chilengedwe chonse. Choyamba, nthawi zonse iye amakhala wokonzeka kukhululuka. Chachiwiri, amatidziwa bwino kwambiri. Amadziwa chilichonse chokhudza ife ndipo ndi amene angadziwe bwino ngati talapadi. Ndipo chachitatu, amatikhululukira kotheratu moti zimangokhala ngati kuti sitinachimwe n’komwe. Zimenezi zimatithandiza kuti tikhale ndi chikumbumtima choyera komanso kukhala naye pa ubwenzi wabwino. N’zoona kuti panopa tizipitirizabe kuchimwa popeza kuti si ife angwiro. Komabe tingalimbikitsidwe ndi mawu opezeka m’buku la Chingelezi la Insight, Voliyumu 2, tsamba 771, omwe amati: “Popeza mwachifundo Yehova amaganizira zofooka za atumiki ake, iwo sayenera kumangokhalira kudziimba mlandu chifukwa cha zimene amalakwitsa popeza si angwiro. (Sal. 103:8-14; 130:3) Ngati nthawi zonse amayesetsa kuchita zomwe Mulungu amafuna, angakhale osangalala. (Afil. 4:4-6; 1 Yoh. 3:19-22).” w22.06 7 ¶18-19
Lachiwiri, January 9
Adzakupititsani kwa mafumu ndi abwanamkubwa chifukwa cha dzina langa.—Luka 21:12.
Sikuti kuopa kutsutsidwa ndi boma ndi chida chokhacho chimene Satana amagwiritsa ntchito. Ena amaopa kwambiri zimene achibale awo angachite chifukwa choti akhala a Mboni za Yehova, kuposa mmene angaopere kuchitiridwa nkhanza. Amakonda kwambiri achibale awowo ndipo amafuna kuti adziwe komanso kukonda Yehova. Zimawapweteka akamamva akulankhula zinthu zosalemekeza Mulungu woona komanso atumiki ake. Komabe nthawi zina achibale omwe poyamba anali otsutsa nawonso amayamba kuphunzira Baibulo. Koma kodi tingatani ngati anthu a m’banja lathu asiya kuchita nafe zinthu chifukwa cha zimene tayamba kukhulupirira? Tingalimbikitsidwe kwambiri ndi mfundo ya choonadi yopezeka pa Salimo 27:10. Tikamakumbukira mmene Yehova amatikondera, timamva kuti ndife otetezeka pamene tikutsutsidwa. Timakhulupirira kuti iye adzatipatsa mphoto chifukwa chopirira. Kuposa aliyense, Yehova adzatipatsa zonse zimene timafunikira kuti tikhale ndi moyo, tizisangalala komanso tikhale naye pa ubwenzi wabwino. w22.06 16-17 ¶11-13
Lachitatu, January 10
Khristu anavutika chifukwa cha inu, ndipo anakusiyirani chitsanzo kuti mutsatire mapazi ake mosamala kwambiri.—1 Pet. 2:21.
Pa utumiki wake, Yesu ankanamiziridwa kuti anali munthu wokonda kwambiri vinyo, wosusuka, mtumiki wa Mdyerekezi, wosasunga Sabata ngakhalenso wonyoza Mulungu. (Mat. 11:19; 26:65; Luka 11:15; Yoh. 9:16) Komabe iye sankayankha ndi mawu aukali. Mofanana ndi Yesu, ifenso sitiyenera kubwezera ngakhale anthu atatilankhula mwamwano. (1 Pet. 2:22, 23) Komatu kudziletsa mwa njira imeneyi sikophweka. (Yak. 3:2) Ndiye n’chiyani chingatithandize? Muziyesa kuganizira zimene zachititsa mwininyumba kulankhula mawu osayenera. M’bale wina dzina lake Sam ananena kuti: “Ndimayesa kuganizira mfundo yakuti munthuyo ayenera kumva choonadi komanso kuti angathe kusintha.” Nthawi zina mwininyumba angakwiye chifukwa choti tamupeza pa nthawi yolakwika. Tikakumana ndi munthu yemwe wakwiya, tikhoza kupemphera mwachidule, kum’pempha Yehova kuti atithandize kukhala wodekha komanso kuti tisalankhule mawu oipa kapena opanda ulemu. w22.04 6 ¶8-9
Lachinayi, January 11
Yandikirani Mulungu.—Yak. 4:8.
Njira yofunika kwambiri yothandizira ana anu kuti akhale pa ubwenzi ndi Yehova ndi kuphunzira nawo Baibulo. (2 Tim. 3:14-17) Koma Baibulo limatchulanso njira ina imene angaphunzirire zokhudza Yehova. M’buku la Miyambo, zikuoneka kuti bambo akukumbutsa mwana wake wamwamuna kuti asasiye kuganizira makhalidwe a Yehova omwe amasonyezedwa m’chilengedwe. (Miy. 3:19-21) Makolo, n’zosachita kufunsa kuti mumasangalala kupita koyenda ndi ana anu. Muzigwiritsa ntchito mpata umenewu powathandiza kuona kugwirizana pakati pa “zimene [Yehova] anapanga” ndi makhalidwe ake ochititsa chidwi. (Aroma 1:20) Taonani mmene Yesu anagwiritsira ntchito chilengedwe pophunzitsa. Pa nthawi ina iye anauza ophunzira ake kuti aonetsetse makwangwala komanso maluwa. (Luka 12:24, 27-30) Iye anaphunzitsa ophunzirawo mfundo yofunika kwambiri yokhudza kukoma mtima komanso kuwolowa manja kwa Atate wawo wakumwamba. Yehova adzaonetsetsa kuti atumiki ake okhulupirika ali ndi chakudya komanso zovala monga mmene amasamalirira makwangwala ndi maluwa. w23.03 20-21 ¶1-4
Lachisanu, January 12
Chilichonse chimene mudzapemphe m’dzina langa, ine ndidzachichita, kuti Atate alemekezedwe mwa Mwana wake.—Yoh. 14:13.
Timathokoza Yehova chifukwa tingathe kupemphera kwa iye kudzera mwa Mwana wake. Yehova amagwiritsa ntchito Yesu poyankha mapemphero athu. Iye amamvetsera komanso kuyankha tikapemphera kudzera m’dzina la Yesu ndipo amatikhululukira machimo athu chifukwa cha nsembe ya Yesu. (Aroma 5:1) Malemba amafotokoza Yesu monga ‘mkulu wa ansembe amene wakhala kudzanja lamanja la mpando wachifumu wa Wolemekezeka kumwamba.’ (Aheb. 8:1) Iye ndi “wotithandiza . . . amene ali ndi Atate.” (1 Yoh. 2:1) Timathokoza Yehova chifukwa chotipatsa Mkulu wa Ansembe yemwe amamvetsa zofooka zathu ndipo “amatilankhulira mochonderera” kwa Mulungu. (Aroma 8:34; Aheb. 4:15) Sitikanatha kumalankhula ndi Yehova m’pemphero popanda nsembe ya Yesu. Kunena zoona, sitingathe kumuyamikira mokwanira chifukwa chotipatsa mphatso yamtengo wapatali yomwe ndi Mwana wake wokondedwa. w22.07 23 ¶10-12
Loweruka, January 13
Munthu wokhulupirika amasunga chinsinsi.—Miy. 11:13.
Munthu wodalirika amayesetsa kuti azisunga malonjezo ake komanso amalankhula zoona. (Sal. 15:4) Munthu woteroyo anthu amamudalira. Timafuna kuti abale ndi alongo athu azitiona choncho. Sitingakakamize ena kuti azitikhulupirira. M’malomwake tiyenera kuchita zinthu zimene zingachititse kuti azitidalira. Pali mawu akuti kudalirika kuli ngati ndalama. Kuti anthu azitiona kuti ndife odalirika pamafunika khama. Koma zimakhalanso zosavuta kuti asiye kutiona choncho. Yehova wakhala akusonyeza kuti ndi wodalirika. “Chilichonse chimene amachita ndi chodalirika.” (Sal. 33:4) Ndipo amayembekezera kuti tizimutsanzira. (Aef. 5:1) Timayamikira kwambiri Yehova chifukwa chotikokera m’banja lake lomwe muli anthu achikondi komanso odalirika. Tonsefe tili ndi udindo woonetsetsa kuti ndife odalirika kwa abale ndi alongo athu. Aliyense payekha akamayesetsa kusonyeza chikondi, kudzichepetsa, kuzindikira, kuona mtima komanso kudziletsa, timathandiza kuti mumpingo anthu azidalirana. Tiyeni tizitsanzira Mulungu wathu Yehova n’kumapitirizabe kusonyeza kuti ndife odalirika. w22.09 8 ¶1-2; 13 ¶17
Lamlungu, January 14
Diso la Yehova limayang’ana anthu amene amamuopa.—Sal. 33:18.
Ngakhale kuti tili ndi abale ndi alongo ambiri, nthawi zina tingamadzimve kuti tili tokhatokha ndipo tingavutike kapena kufooka poganiza kuti timafunika kulimbana ndi maganizo ofooketsawa patokha. Komatu Yehova safuna kuti tizimva choncho. Taganizirani mmene anachitira ndi mneneri Eliya. Yehova analimbikitsa Eliya kuti afotokoze mmene ankamvera. Kawiri konse anamufunsa Eliya kuti: “Ukudzatani kuno?” (1 Maf. 19:9, 13) Pa ulendo uliwonse Yehova ankamvetsera pamene Eliya ankafotokoza za mumtima mwake. Kenako Yehova anamusonyeza kuti anali naye komanso ndi wamphamvu kwambiri. Anatsimikizira Eliya kuti panalinso anthu ambiri omwe ankamulambira. (1 Maf. 19:11, 12, 18) N’zosakayikitsa kuti Eliya anamva bwino atafotokozera Yehova za mumtima mwake komanso kuona mmene anamuyankhira. Yehova anapatsa Eliya ntchito zofunika zingapo kuti agwire. Anamuuza kuti akadzoze Hazaeli kuti akhale mfumu ya Siriya, Yehu akhale mfumu ya Isiraeli komanso Elisa akhale mneneri. (1 Maf. 19:15, 16) Pom’patsa zochita zimenezi, Yehova anathandiza Eliya kuti aziganizira kwambiri zinthu zolimbikitsa. Mulungu anamupatsanso Elisa kuti akhale mnzake woti azimuthandiza. w22.08 8 ¶3; 9 ¶5
Lolemba, January 15
Pitirizani kutonthozana ndi kulimbikitsana.—1 Ates. 5:11.
Kodi mpingo wanu unagwirapo ntchito yomanga kapena kukonza Nyumba ya Ufumu? Ngati ndi choncho, muyenera kuti mukukumbukira nthawi yoyamba imene munasonkhana m’Nyumba ya Ufumu yatsopanoyo. Muyeneranso kuti munathokoza kwambiri Yehova. Mwinanso munakhudzidwa kwambiri moti munalephera kuimba bwino nyimbo yoyamba. Nyumba zathu za Ufumu zomangidwa bwino zimachititsa kuti Yehova atamandike. Komatu pali ntchito inanso yomanga imene tikamagwira nawo timachititsa kuti iye atamandike kwambiri. Ndipo ndi yamtengo wapatali kuposa nyumba zonse zimene tingamange. Ntchito imeneyi ndi yolimbikitsa anthu omwe amabwera kunyumba zolambirirazi. Mtumwi Paulo ankaganizira za ntchito imeneyi pomwe analemba mawu a mulemba laleroli. Mtumwi Paulo ndi chitsanzo chabwino cha munthu yemwe ankadziwa kulimbikitsa Akhristu anzake. Iye ankawachitira chifundo. Tingamutsanzire tikamalimbikitsa abale ndi alongo athu masiku ano.—1 Akor. 11:1. w22.08 20 ¶1-2
Lachiwiri, January 16
Mukhale ndi khalidwe logwirizana ndi zimene Yehova amafuna.—Akol. 1:10.
Mkhristu amene akufuna kukhala wolungama pamaso pa Mulungu amachita zinthu zonse moona mtima pa nkhani za malonda. Munthu amene amakonda chilungamo, amadana ndi kuona wina akuchitiridwa zopanda chilungamo. Ndipo ‘pofuna kuti azikondweretsa [Yehova] pa chilichonse,’ munthu wolungama amaganizira mmene Yehovayo amaonera zimene amasankha. Baibulo limafotokoza kuti Yehova ndi mwiniwake wa chilungamo. Pa chifukwa chimenechi iye amatchedwa “malo amene chilungamo chimakhalamo.” (Yer. 50:7) Monga Mlengi, ndi Yehova yekha amene angathe kukhazikitsa mfundo zokhudza chabwino ndi choipa. Popeza iye ndi wangwiro, maganizo ake pa nkhani yokhudza chabwino ndi choipa ndi apamwamba kwambiri kuposa maganizo athu, omwe nthawi zambiri amasokonezedwa chifukwa choti ndife ochimwa. (Miy. 14:12; Yes. 55:8, 9) Komabe popeza tinalengedwa m’chifaniziro cha Mulungu, timakwanitsa kuyendera mfundo zake zachilungamo. (Gen. 1:27) Ndipo timasangalala tikamachita zimenezi. Kukonda Atate wathu kumatichititsa kuti tizimutsanzira mmene tingathere.—Aef. 5:1. w22.08 27 ¶5-6
Lachitatu, January 17
Pitirizani kuzindikira chifuniro cha Yehova.—Aef. 5:17.
Tikamada nkhawa kapena tikafooka, tingamafune kuchita zinthu zina zomwe zingatithandize kuti tisiye kuda nkhawa. Zimenezitu n’zomveka. Komabe tiyenera kukhala osamala kuti tisachite zinthu zimene Yehova amadana nazo. (Aef. 5:10-12, 15, 16) M’kalata imene analembera Akhristu a ku Filipi, mtumwi Paulo anawalimbikitsa kupitiriza kuganizira zinthu zimene ndi “zolungama, . . . zoyera, . . . zolimbikitsa chikondi, [komanso] khalidwe labwino lililonse.” (Afil. 4:8) Ngakhale kuti Paulo sankanena mwachindunji zokhudza zinthu zosangalatsa, zimene ananenazi ziyenera kutithandiza kuganizira zosangalatsa zimene timasankha. Tayesani izi: Paliponse pamene pali mawu akuti “zilizonse” palembali, yesani kuikapo mawu akuti “nyimbo,” “mafilimu,” “mabuku,” kapena “magemu.” Kuchita zimenezi kungakuthandizeni kudziwa zosangalatsa zomwe zingakhale zovomerezeka kapena zosavomerezeka kwa Mulungu. Timafuna kuti tizichita zinthu mogwirizana ndi mfundo zapamwamba za Yehova.—Sal. 119:1-3. w22.10 9 ¶11-12
Lachinayi, January 18
Ankadziwa zimene zili mumtima mwa munthu.—Yoh. 2:25.
Anthu “osalungama” akadzaukitsidwa adzafunika kuthandizidwa kwambiri chifukwa asanamwalire, ena mwa iwo ankachita zinthu zoipa kwambiri. Choncho iwo adzafunika kuphunzitsidwa kuti azitsatira mfundo zolungama za Yehova. Kuti zimenezi zidzatheke, Ufumu wa Mulungu udzatsogolera pa ntchito yaikulu yophunzitsa anthu yomwe sinachitikeponso. Kodi ndi ndani amene adzaphunzitse anthu osalungama? Ndi a khamu lalikulu komanso olungama omwe adzaukitsidwe. Kuti mayina awo adzalembedwe m’buku la moyo, osalungama adzafunika kukhala pa ubwenzi wabwino ndi Yehova komanso kudzipereka kwa iye. Yesu Khristu limodzi ndi oweruza anzake, azidzachita chidwi ndi mmene osalungamawa akuchitira ndi zimene akuphunzitsidwa. (Chiv. 20:4) Aliyense amene adzakane kutsatira zimene akuphunzitsidwa, sadzaloledwa kuti apitirize kukhala ndi moyo ngakhale atakhala ndi zaka 100. (Yes. 65:20) Yehova ndi Yesu amafufuza mitima ndipo sadzalola kuti wina aliyense azidzasokoneza m’dziko latsopano.—Yes. 11:9; 60:18; 65:25. w22.09 17 ¶11-12
Lachisanu, January 19
Munthu aliyense azimvera olamulira akuluakulu.—Aroma 13:1.
Pavesili mawu akuti “olamulira akuluakulu” akunena za anthu omwe amalamulira maboma. Akhristu amayenera kumvera olamulira amenewa. Iwo amathandiza kuti m’dziko musakhale chisokonezo, amaonetsetsa kuti anthu akutsatira malamulo komanso nthawi zina amateteza anthu a Yehova. (Chiv. 12:16) Choncho timalamulidwa kuti tizipereka misonkho, tiziwaopa komanso tiziwapatsa ulemu umene amafuna. (Aroma 13:7) Komabe olamulirawa ali ndi mphamvu chifukwa chakuti Yehova wawalola kuti akhale nazo. Yesu anamveketsa bwino mfundo imeneyi pamene ankafunsidwa mafunso ndi bwanamkubwa wa Chiroma, Pontiyo Pilato. Pamene Pilato ananena kuti ali ndi mphamvu zotha kumumasula kapena kumupereka kuti aphedwe, Yesu anamuuza kuti: “Simukanakhala ndi mphamvu iliyonse pa ine mukanapanda kupatsidwa kuchokera kumwamba.” (Yoh. 19:11) Monga mmene zinalili ndi Pilato, mphamvu za olamulira komanso andale onse masiku ano zili ndi malire. w22.10 14 ¶6
Loweruka, January 20
Oipa sadzakhalaponso.—Sal. 37:10.
Mfumu Davide inauziridwa kulemba mmene moyo udzakhalire, mfumu yanzeru ndi yokhulupirika ikadzayamba kulamulira. (Sal. 37:10, 11, 29) Nthawi zambiri timawerengera ena Salimo 37:11 tikamanena za Paradaiso amene akubwerayo. Tili ndi zifukwa zabwino zochitira zimenezi chifukwa Yesu anatchulanso mawu a palembali pa ulaliki wake wa paphiri, posonyeza kuti zimenezi zidzakwaniritsidwanso m’tsogolo. (Mat. 5:5) Koma mawu a Davidewa anasonyezanso mmene moyo udzakhalire pa nthawi ya ufumu wa Solomo. Pa nthawi imene Solomo ankalamulira ku Isiraeli, anthu a Mulungu ankasangalala ndi mtendere ndipo sankasowa chilichonse m’dziko “loyenda mkaka ndi uchi.” Mulungu anati: “Mukapitiriza kutsatira malangizo anga . . . , ndidzakupatsani mtendere m’dzikolo, moti mudzagona pansi popanda wokuopsezani.” (Lev. 20:24; 26:3, 6) Malonjezo amenewo anakwaniritsidwa mu ulamuliro wa Solomo. (1 Mbiri 22:9; 29:26-28) Mawu opezeka pa Salimo 37:10, 11, 29, anakwaniritsidwapo m’mbuyomo ndipo adzakwaniritsidwanso m’tsogolo. w22.12 10 ¶8
Lamlungu, January 21
Amene amazigwiritsitsa [nzeru] adzatchedwa odala.—Miy. 3:18.
Monga Akhristu oona, tiyenera kumatsatira malangizo. Pofuna kuti zinthu zitiyendere bwino, Baibulo limatilangiza kuti: “Ukamatsatira malangizo anzeru udzatha kumenya nkhondo yako, ndipo pakakhala alangizi ambiri udzapambana.” (Miy. 24:6) Taganizirani mmene kutsatira mfundo imeneyi kungathandizire kuti zinthu zitiyendere bwino pa ntchito yathu yolalikira ndi kuphunzitsa. M’malo momagwira ntchitoyi m’njira yathuyathu, timatsatira malangizo omwe timapatsidwa. Timalandira malangizo anzeru kumisonkhano yathu, komwe aphungu anzeru amakamba nkhani za m’Baibulo komanso kuchita zitsanzo zotithandiza. Kuwonjezera pamenepo gulu la Yehova limatipatsa zinthu monga mavidiyo ndi mabuku zomwe zimathandiza anthu kumvetsa Baibulo. Timayamikira chifukwa cha malangizo abwino kwambiri amene timawapeza m’Mawu a Mulungu. Kodi zinthu zikanakhala bwanji pa moyo wathu pakanapanda malangizowa? Tiyeni nthawi zonse tizigwiritsa ntchito nzeru zimene Yehova amatipatsa.—Miy. 3:13-17. w22.10 23 ¶18-19
Lolemba, January 22
Mawu anu amatsekemera kwambiri m’kamwa mwanga, kuposa mmene uchi umakomera!—Sal. 119:103.
Mofanana ndi chakudya chimene tikadya chimagayika n’kutipatsa mphamvu, kuphunzira ndi kuganizira mozama Mawu a Mulungu kumatipatsanso mphamvu mwauzimu. Ponena za Mawu ake, Yehova amafuna kuti tiwamvetse bwino. Tingachite zimenezo popemphera, kuwawerenga komanso kuwaganizira mozama. Choyamba timapemphera pokonzekeretsa mtima wathu kuti tilandire maganizo a Mulungu. Kenako timawerenga Baibulo n’kuima kaye kuti tiganizire mozama zimene tawerengazo. Kodi zotsatirapo zake zimakhala zotani? Tikamaganizira kwambiri zimene tawerenga, m’pamenenso mtima wathu wophiphiritsa umamvetsa kwambiri Mawu a Mulungu. N’chifukwa chiyani zili zofunika kuwerenga Baibulo komanso kuganizira mozama zomwe tawerengazo? Kuchita zimenezi kumatipatsa mphamvu zomwe timafunikira kuti tizitha kulalikira uthenga wa Ufumu panopa ndiponso kuti tidzathe kulengeza uthenga wamphamvu wachiweruzo m’tsogolo. Komanso kuganizira makhalidwe abwino amene Yehova ali nawo kumathandiza kuti ubwenzi wathu ndi iye ukhale wolimba kwambiri. w22.11 6-7 ¶16-17
Lachiwiri, January 23
Onse adzadziwa kuti ndinu ophunzira anga, ngati mukukondana.—Yoh. 13:35.
Yesu anasonyeza kuti ngakhale anthu omwe sali mumpingo wa Chikhristu adzazindikira otsatira ake chifukwa amasonyezana chikondi chopanda dyera. Ndipo chikondi chimene chili pakati pa Akhristu oona n’chochititsa chidwi kwambiri. Komabe a Mboni za Yehova si anthu angwiro. (1 Yoh. 1:8) Choncho pamene tikuyamba kuwadziwa bwino abale ndi alongo, m’pamenenso timadziwa kwambiri zofooka zawo. (Aroma 3:23) N’zomvetsa chisoni kuti ena anakhumudwa chifukwa cha zolakwa za anzawo. Kodi Yesu anawasonyeza bwanji chikondi atumwi ake? Nanga kodi zingatheke bwanji kuti tizitsanzira Yesu masiku ano?’ A Mbonife tingachitenso bwino kuganizira mayankho a mafunso amenewa. Kuchita zimenezi kungathandize kuti tizikondana kwambiri makamaka pamene talakwirana.—Aef. 5:2. w23.03 26-27 ¶2-4
Lachitatu, January 24
Munthu wokhulupirika, mumamuchitira zinthu mokhulupirika.—Sal. 18:25.
Pamene tikuyandikira mapeto a dzikoli, tiziyembekezera kuti tingakumane ndi mavuto mumpingo. Mavuto amenewa angayese kukhulupirika kwathu kwa Yehova. Choncho tiyenera kukhalabe oganiza bwino. Ngati Mkhristu mnzanu wakuchitirani zinthu zopanda chilungamo, muzipewa kukwiya. Mukapatsidwa malangizo kapena chilango musamaganizire kwambiri zoti muchita manyazi. Muzingomvera malangizowo ndipo muzisintha. Ngati kusintha komwe kwachitika m’gululi kwakukhudzani, muzivomereza ndi mtima wonse ndipo muzitsatira malangizo omwe aperekedwa. Ngati kukhulupirika kwanu kwayesedwa, muzipitirizabe kukhala okhulupirika kwa Yehova ndi gulu lake. Muzikhala odekha, kuona zinthu moyenera komanso kumaziona mmene Yehova amaonera. Muzipemphera kwa Yehova kuti akuthandizeni ndipo musamasiye kuchita zinthu ndi mpingo. Ndiye kaya mukumana ndi zotani, Satana sadzatha kukulekanitsani ndi Yehova kapena gulu lake.—Yak. 4:7. w22.11 24-25 ¶14-16
Lachinayi, January 25
Muzikonda gulu lonse la abale. —1 Pet. 2:17.
Akulu amathandiza abale kukhala okonzeka ngozi isanachitike. Amaonetsetsa kuti onse mumpingo akudziwa zomwe angachite kuti akhale otetezeka komanso kuti azilankhulana ndi akuluwo. Kodi inuyo muyenera kuchita zotani? Ngati ngozi yachitika pafupi ndi dera lanu, muzifunsa akulu mmene mungathandizire. Mwina mungalandire m’nyumba yanu anthu omwe alibe pokhala kapenanso amene adzipereka kugwira ntchito zomangamanga. Mungathandizenso pokapereka chakudya ndi zinthu zina zofunika kwa ofalitsa omwe akufunika thandizo. Mungathenso kuthandiza ngakhale ngozi itachitika kutali ndi kumene mumakhala. Motani? Popempherera amene akhudzidwa. (2 Akor. 1:8-11) Mungathandizenso popereka ndalama zothandiza pa ntchito ya padziko lonse. (2 Akor. 8:2-5) Ngati mungakwanitse kupita kumene kwachitika ngozi, mungafunse akulu kuti akuuzeni zimene mungachite kuti mukathandize nawo. Ngati mwaitanidwa kuti mukathandize, mudzapatsidwa maphunziro amene angakuthandizeni kuti mukhale oyenerera kukathandiza. w22.12 24 ¶8; 25 ¶11-12
Lachisanu, January 26
Palibe mayesero amene mwakumana nawo osiyana ndi amene anthu ena amakumana nawo.—1 Akor. 10:13.
Baibulo lina linamasulira mawu a lemba la leroli kuti: “Palibe mayesero amene mwakumana nawo omwe ndi achilendo.” Mawuwa ankapita kwa Akhristu a ku Korinto, amuna ndi akazi omwe. Ena mwa iwo poyamba anali achigololo, ogonana ndi amuna kapena akazi anzawo ndiponso zidakwa. (1 Akor. 6:9-11) Kodi mukuganiza kuti pambuyo pobatizidwa, iwo sankavutikanso ndi zilakolako zoipa? Ayi, ndithu. N’zoona kuti anali odzozedwa koma sanali angwiro. N’zosakayikitsa kuti nthawi ndi nthawi ankalimbanabe ndi zilakolako zoipazi. Izitu ziyenera kutilimbikitsa chifukwa zikusonyeza kuti chilakolako choipa chilichonse chimene mukulimbana nacho, winawake anakwanitsa kuchigonjetsa. Choncho mungathe kukhalabe “ndi chikhulupiriro cholimba . . . podziwa kuti abale anu padziko lonse akukumananso ndi mavuto ngati omwewo.”—1 Pet. 5:9. w23.01 12 ¶15
Loweruka, January 27
M’dzikomu mukumana ndi mavuto aakulu, koma limbani mtima. Ine ndaligonjetsa dziko.—Yoh. 16:32, 33.
Yesu anapempha Yehova kuti aziyang’anira otsatira ake. (Yoh. 17:11) N’chifukwa chiyani zimenezi zimatithandiza kukhala olimba mtima? Chifukwa Yehova ndi wamphamvu kuposa adani athu. (1 Yoh. 4:4) Iye amaona chilichonse. Timakhulupirira kuti tikamamudalira, angatithandize kuti tisamaope ndiponso tikhale olimba mtima. Kodi nthawi zina mumachita manyazi kuuza ena kuti ndinu wa Mboni za Yehova? Kodi mumazengereza kukhala wofalitsa kapena kubatizidwa chifukwa choopa zimene ena aziganiza zokhudza inuyo? Musamalole zimenezi kukulepheretsani kuchita zimene mukudziwa kuti n’zoyenera. Muzipemphera kwa Yehova mochokera pansi pa mtima. Muzimupempha kuti akuthandizeni kukhala olimba mtima kuti muchite chifuniro chake. Mukamaona mmene Yehova akuyankhira mapemphero anu, mudzakhala amphamvu komanso olimba mtima kwambiri.—Yes. 41:10, 13. w23.01 29 ¶12; 30 ¶14
Lamlungu, January 28
Kodi simunawerenge?—Mat. 12:3.
Yesu anafunsa funso lakuti “Kodi simunawerenge?” pofuna kusonyeza kuti Afarisi anali ndi maganizo olakwika okhudza zimene ankawerenga m’Malemba. (Mat. 12:1-7) Pa nthawiyi Afarisi ankanena kuti ophunzira a Yesu sankasunga Sabata. Poyankha, Yesu anatchula zitsanzo ziwiri za m’Malemba komanso anatchula mawu a m’vesi lina m’buku la Hoseya pofuna kusonyeza kuti Afarisi sankamvetsa bwino lamulo lokhudza Sabata komanso ankalephera kusonyeza chifundo. N’chifukwa chiyani kuwerenga Mawu a Mulungu sikunkawathandiza kusintha? Chifukwa chakuti ankawawerenga ali ndi zolinga zolakwika komanso anali ndi mtima wonyada. Zimenezi zinawalepheretsa kumvetsa zimene ankawerenga. (Mat. 23:23; Yoh. 5:39, 40) Onaninso kuti pa lemba la Mateyu 19:4-6, Yesu anafunsa Afarisi funso lomweli lakuti: “Kodi simunawerenge?” Ngakhale kuti iwo anali atawerenga nkhani yokhudza mmene Yehova analengera zinthu, ankanyalanyaza zomwe imaphunzitsa pankhani ya mmene Mulungu amaonera ukwati. Timaphunzira kuchokera pa mawu a Yesu kuti tiyenera kumawerenga Baibulo tili ndi maganizo oyenera. Mosiyana ndi Afarisi, tiyenera kukhala odzichepetsa komanso ophunzitsika. w23.02 12 ¶12-13
Lolemba, January 29
Kuganiza bwino kudzakuyang’anira.—Miy. 2:11.
Chilamulo chomwe Yehova anapatsa Aisiraeli chinali ndi malangizo omwe akanawathandiza kupewa ngozi zoopsa zomwe zikanatha kuchitikira kunyumba kapena kumalo antchito. (Eks. 21:28, 29; Deut. 22:8) Ngati munthu wapha mnzake mwangozi ankakumana ndi mavuto aakulu. (Deut. 19:4, 5) Chilamulo chinkanena kuti ngakhale anthu omwe mwangozi avulaza mwana wosabadwa, ankayenera kulangidwa. (Eks. 21:22, 23) Malemba amafotokoza momveka bwino kuti Yehova amafuna kuti tiziyesetsa kupewa ngozi. Tingasonyeze kuti timayamikira mphatso yamoyo imene Mulungu anatipatsa, potsatira njira zopewera ngozi kunyumba komanso kuntchito. Timachita zinthu mosamala tikamataya zinthu zakuthwa, zapoizoni kapena mankhwala komanso timaika kutali ndi ana zinthu ngati zimenezi. Timakhalanso osamala ndi moto, zinthu zowira, zipangizo zamagetsi ndipo timaonetsetsa kuti sitinazisiye popanda oziyang’anira. Sitiyendetsa galimoto pamene maganizo athu asokonezedwa chifukwa choti tamwa mankhwala ena ake, mowa kapena kusagona mokwanira. Ndipo timaonetsetsa kuti sitikugwiritsa ntchito zipangizo zamakono poyendetsa galimoto. w23.02 21-22 ¶7-9
Lachiwiri, January 30
Maso anu adzaona Mlangizi wanu wamkulu.—Yes. 30:20.
Yehova ndi Mphunzitsi woleza mtima, wokoma mtima komanso womvetsetsa. Amaona zabwino mwa ophunzira ake. (Sal. 130:3) Sayembekezera kuti tichita zimene sitingakwanitse. Kumbukirani kuti iye ndi amene anapanga ubongo wanu womwe ndi mphatso yodabwitsa. (Sal. 139:14) Mlengi wathu amafuna kuti tipitirize kuphunzira mpaka kalekale komanso tizisangalala nako. Choncho ndi nzeru kuti ‘tizilakalaka’ kuphunzira choonadi cha m’Baibulo panopa. (1 Pet. 2:2) Muzidziikira cholinga chomwe mungachikwaniritse ndipo nthawi zonse muzitsatira ndandanda yanu yowerengera ndi kuphunzirira Baibulo. (Yos. 1:8) Mothandizidwa ndi Yehova, mudzayamba kusangalala kwambiri ndi kuwerenga komanso kuphunzira za iye. Kungodziwa zinthu pakokha si kokwanira. Cholinga chachikulu ndi kukuthandizani kuphunzira zambiri zokhudza Yehova, komanso kukhala ndi makhalidwe monga kukonda Mulungu ndi kumukhulupirira. (1 Akor. 8:1-3) Pamene mukupitiriza kuphunzira, muzipempha Yehova kuti akuthandizeni kuwonjezera chikhulupiriro chanu. (Luka 17:5) Iye amayankha mofunitsitsa mapemphero ngati amenewo. w23.03 10 ¶11, 13
Lachitatu, January 31
Muzigwiritsa ntchito bwino nthawi yanu.—Akol. 4:5.
Ophunzira a Yesu sankafunika kumangokhala pamene ankayembekezera kuti mapeto afike. Iye anawapatsa ntchito yoti azigwira. Anawalamula kuti azilalikira uthenga wabwino “mu Yerusalemu, ku Yudeya konse ndi ku Samariya, mpaka kumalekezero a dziko lapansi.” (Mac. 1:6-8) Imeneyitu inali ntchito yaikulu kwambiri. Iwo ankagwiritsa ntchito bwino nthawi yawo pamene ankadzipereka pogwira ntchitoyi. Kuti tizisamala ndi mmene timachitira zinthu, tiyenera kuganizira mmene timagwiritsira ntchito nthawi yathu. “Zinthu zosayembekezereka” zingagwere tonsefe. (Mlal. 9:11) Mwachitsanzo tingathe kumwalira mosayembekezereka. Tingagwiritse ntchito bwino nthawi yathu pomachita chifuniro cha Yehova, komanso kulimbitsa ubwenzi wathu ndi iye. (Yoh. 14:21) Tiyenera kukhala “olimba ndiponso osasunthika. Nthawi zonse tizikhala ndi zochita zambiri pa ntchito ya Ambuye.” (1 Akor. 15:58) Tikamachita zimenezi, mapeto akafika, kaya ndi mapeto a moyo wathu kapena a dziko loipali, sitidzanong’oneza bondo kuti sitinachite zambiri potumikira Yehova.—Mat. 24:13; Aroma 14:8. w23.02 18 ¶12-14