Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • es24 tsamba 17-26
  • February

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • February
  • Kuphunzira Malemba Tsiku ndi Tsiku—2024
  • Timitu
  • Lachinayi, February 1
  • Lachisanu, February 2
  • Loweruka, February 3
  • Lamlungu, February 4
  • Lolemba, February 5
  • Lachiwiri, February 6
  • Lachitatu, February 7
  • Lachinayi, February 8
  • Lachisanu, February 9
  • Loweruka, February 10
  • Lamlungu, February 11
  • Lolemba, February 12
  • Lachiwiri, February 13
  • Lachitatu, February 14
  • Lachinayi, February 15
  • Lachisanu, February 16
  • Loweruka, February 17
  • Lamlungu, February 18
  • Lolemba, February 19
  • Lachiwiri, February 20
  • Lachitatu, February 21
  • Lachinayi, February 22
  • Lachisanu, February 23
  • Loweruka, February 24
  • Lamlungu, February 25
  • Lolemba, February 26
  • Lachiwiri, February 27
  • Lachitatu, February 28
  • Lachinayi, February 29
Kuphunzira Malemba Tsiku ndi Tsiku—2024
es24 tsamba 17-26

February

Lachinayi, February 1

Muzikondana mofanana ndi mmene ine ndimakukonderani.—Yoh. 15:12.

Kodi lemba laleroli likutanthauza chiyani? Monga mmene Yesu anafotokozera, ichi ndi chikondi chololera kuvutikira ena, chomwe chimachititsa Mkhristu kukhala wokonzeka ngakhale kufera Mkhristu mnzake ngati pakufunika kutero. Mawu a Mulungu amasonyeza kuti chikondi ndi chofunika kwambiri. Pa mavesi amene anthu ambiri amawakonda, pamakhalanso mavesi monga akuti: “Mulungu ndi chikondi.”(1 Yoh. 4:8) “Uzikonda mnzako mmene umadzikondera wekha.” (Mat. 22:39) “Chikondi chimakwirira machimo ochuluka.” (1 Pet. 4:8) “Chikondi sichitha.” (1 Akor. 13:8) Mavesi amenewa ndi ena ayenera kuthandiza aliyense kuona kufunika kokhala ndi khalidwe lochititsa chidwili ndiponso kulisonyeza. Chikondi chenicheni chimachokera kwa Yehova. Okhawo amene iye wawadalitsa komanso kuwapatsa mzimu wake ndi amene angakhale ndi chikondi chenicheni pakati pawo. (1 Yoh. 4:7) Ndiye kodi n’zodabwitsa kuti Yesu ananena kuti otsatira ake oona azidzadziwika ndi chikondi chopanda dyera? Monga mmene Yesu ananenera, anthu ambiri akwanitsa kuzindikira otsatira ake enieni poona chikondi chenicheni chimene amasonyezana. w23.03 27-28 ¶5-8

Lachisanu, February 2

Machimo ako akhululukidwa. —Luka 7:48.

Kodi mukufuna kuti muzikhululukira kwambiri ena? Mungayambe ndi kuwerenga komanso kuganizira mozama nkhani za anthu otchulidwa m’Baibulo omwe ankakhululuka ndi mtima wonse komanso amene sankakhululuka. Taganizirani chitsanzo cha Yesu. Iye ankakhululukira ena ndi mtima wonse. (Luka 7:47) Sankaganizira kwambiri zolakwa zawo ndipo ankawaona kuti angathe kusintha. Koma Afarisi a munthawi yake “ankaona anthu ena ngati opanda pake.” (Luka 18:9) Pambuyo poganizira zitsanzo zimenezi dzifunseni kuti: ‘Kodi ineyo ndimaona zotani mwa ena? Kodi ndimasankha kuganizira makhalidwe ati omwe ali nawo?’ Ngati zikukuvutani kukhululukira winawake, muziyesa kulemba penapake makhalidwe ambiri abwino a munthuyo. Kenako muzidzifunsa kuti: ‘Kodi Yesu amamuona bwanji munthuyu? Kodi akanasankha kumukhululukira?’ Kuphunzira mwa njira imeneyi kungatithandize kuti tisinthe mmene timaganizira. Poyamba tingamafunike kuyesetsa kuti tikhululukire munthu amene watilakwira. Koma tikapitiriza kuchita khama, m’kupita kwa nthawi zidzakhala zosavuta kuti tizikhululuka. w22.04 23 ¶6

Loweruka, February 3

Anatumiza mngelo wake kuti adzapereke Chivumbulutsocho . . . pogwiritsa ntchito zizindikiro.—Chiv. 1:1.

M’buku la Chivumbulutso, adani a Mulungu akufotokozedwa mophiphiritsa. Timawerenga zokhudza zilombo zingapo. Mwachitsanzo, akutchula za “chilombo chikutuluka m’nyanja” ndipo chili ndi “nyanga 10 ndi mitu 7.” (Chiv. 13:1) Kenako pakubwera “chilombo china chikutuluka pansi pa dziko lapansi.” Chilombochi chinayamba kulankhula ngati chinjoka ndipo chinachititsa kuti “moto ugwere padziko lapansi kuchokera kumwamba.” (Chiv. 13:​11-13) Kenako timawerenganso za “chilombo chofiira kwambiri,” chomwe pamsana pake pali hule. Zilombo zitatuzi zikuimira adani omwe akhala akulimbana ndi Yehova ndi Ufumu wake kwa nthawi yaitali. Choncho n’zofunika kuti tiwadziwe. (Chiv. 17:​1, 3) Chimene chingatithandize kumvetsa tanthauzo la zizindikirozi ndi kulola kuti Baibulo lidzifotokoze lokha. Zambiri mwa zizindikiro za m’buku la Chivumbulutsozi zinafotokozedwa kale m’mabuku ena a m’Baibulo. w22.05 8-9 ¶3-4

Lamlungu, February 4

Muzikonda Yehova Mulungu wanu ndi mtima wanu wonse.—Mat. 22:37.

Atumiki ena a Yehova zimawavuta kusintha akaona kuti akulephera kuchita zambiri chifukwa cha uchikulire kapena thanzi lawo. Ngati nthawi zina mumafooka chifukwa cholephera kuchita zina zake, muzidzifunsa kuti, ‘Kodi Yehova amafuna kuti ndichite chiyani?’ Iye amafuna kuti muzichita zimene mungathe malinga ndi mmene zinthu zilili pa nthawiyo. Mlongo wina yemwe ali ndi zaka za m’ma 80, amakhumudwa chifukwa sangathenso kuchita zambiri mu utumiki ngati mmene ankachitira ali ndi zaka za m’ma 40. Iye akuona kuti ngakhale kuti amayesetsa kuchita zonse zomwe angathe, Yehova sakusangalala nazo. Koma kodi zimenezi ndi zoona? Taganizirani izi. Ngati mlongoyo ankachita zonse zomwe akanatha m’zaka zake za m’ma 40, ndipo akuyesetsabe kuchita zimenezi m’zaka zake za m’ma 80, ndiye kuti sanasiye kuchita zonse zomwe angathe potumikira Yehova. Tikamachita zonse zomwe tingathe, Yehova adzasangalala nafe n’kutiuza kuti: “Wachita bwino kwambiri.” (Yerekezerani ndi Mateyu 25:​20-23.) Zingakhale zosavuta kuti tizisangalala ngati titamaganizira zimene tingakwanitse kuchita osati zimene sitingakwanitse. w22.04 10 ¶2; 11 ¶4-6

Lolemba, February 5

Ndinaonanso mzinda woyera, Yerusalemu Watsopano.—Chiv. 21:2.

Pa Chivumbulutso 21 amayerekezera a 144,000 ndi mzinda wokongola kwambiri womwe ukutchedwa “Yerusalemu Watsopano.” Mzindawu uli pa miyala 12 ya maziko yomwe yalembedwa “mayina 12 a atumwi 12 a Mwanawankhosa.” (Chiv. 21:​10-14; Aef. 2:20) Palibe mzinda wooneka ngati umenewu. Unali ndi msewu waukulu wopangidwa ndi golide woyenga bwino, mageti 12 a ngale, makoma ndi maziko okongoletsedwa ndi miyala yamtengo wapatali komanso mzindawu unayezedwa bwino kwambiri. (Chiv. 21:​15-21) Komabe pakuoneka kuti pakusowekera chinachake. Taonani zimene kenako Yohane akutiuza: “Sindinaonemo kachisi aliyense chifukwa kachisi wake ndi Yehova Mulungu Wamphamvuyonse komanso Mwanawankhosa. Mzindawo sunafunikirenso kuwala kwa dzuwa kapena kwa mwezi, chifukwa kuwala kwa ulemerero wa Mulungu kunkaunikira mzindawo ndipo Mwanawankhosa ndi amene anali nyale yake.” (Chiv. 21:​22, 23) Anthu omwe adzakhale mbali ya Yerusalemu Watsopano azidzakhala ndi Yehova.—Aheb. 7:27; Chiv. 22:​3, 4. w22.05 17-18 ¶14-15

Lachiwiri, February 6

Pitirizani kulolerana ndi kukhululukirana ndi mtima wonse . . . Mofanana ndi Yehova amene anakukhululukirani ndi mtima wonse, inunso muzichita chimodzimodzi.—Akol. 3:13.

Kuwonjezera pa kukhala Mlengi wathu, Wotipatsa malamulo komanso Woweruza wathu, Yehova ndi Atate wathu wachikondi. (Sal. 100:3; Yes. 33:22) Tikamuchimwira n’kulapa mochokera pansi pa mtima iye amatikhululukira, ndipo amachita zimenezi mofunitsitsa. (Sal. 86:5) Kudzera mwa mneneri Yesaya, Yehova amatitsimikizira mwachikondi kuti: “Ngakhale kuti machimo anu ndi ofiira kwambiri, adzayera kwambiri.” (Yes. 1:18) Chifukwa choti si ife angwiro, tonsefe nthawi zina timalankhula kapena kuchita zimene zingakhumudwitse ena. (Yak. 3:2) Komabe zimenezi sizikutanthauza kuti sitingathe kumagwirizana nawo. Titha kumagwirizana nawo ngati titayesetsa kukhala ndi mtima wokhululuka. (Miy. 17:9; 19:11; Mat. 18:​21, 22) Yehova amafuna kuti tizikhululukirana pa zinthu zing’onozing’ono zomwe timalakwirana. Tili ndi chifukwa chomveka chochitira zimenezi. Pajatu iye amatikhululukira “ndi mtima wonse.”—Yes. 55:7. w22.06 8 ¶1-2

Lachitatu, February 7

Muzitsanzira anthu amene, chifukwa cha chikhulupiriro ndiponso kuleza mtima, akulandira zinthu zimene Mulungu analonjeza.—Aheb. 6:12.

Ngakhale kuti sitiyenera kumadziyerekezera ndi ena, tingapindule pophunzira pa zitsanzo za atumiki okhulupirika a Yehova. Chitsanzo chabwino kwambiri ndi Yesu. Ngakhale kuti iye anali wangwiro, tingaphunzire zambiri pa makhalidwe ake abwino komanso mmene ankachitira zinthu. (1 Pet. 2:21) Tikamayesetsa kumutsanzira mosamala kwambiri, tingakhale atumiki abwino a Yehova. M’Mawu a Mulungu timapezamo zitsanzo zambiri za amuna ndi akazi okhulupirika omwe tingatengere chitsanzo chawo ngakhale kuti sanali angwiro. Taganizirani za Mfumu Davide, yemwe Yehova anamutchula kuti “munthu wapamtima panga.” (Mac. 13:22) Komatu Davide anachita machimo ena akuluakulu. Ngakhale zili choncho iye ndi chitsanzo chabwino kwa ife. N’chifukwa chiyani tikutero? Chifukwa sankayesa kudziikira kumbuyo. M’malomwake ankavomera malangizo amphamvu amene ankapatsidwa komanso kudzimvera chisoni chifukwa cha zimene anachita. Zimenezi zinachititsa kuti Yehova amukhululukire.—Sal. 51:​3, 4, 10-12. w22.04 13 ¶11-12

Lachinayi, February 8

Munthu angapereke chilichonse chimene ali nacho kuti apulumutse moyo wake.—Yobu 2:4.

Baibulo limavomereza kuti imfa ndi mdani. (1Akor. 15:​25, 26) Tikhoza kumada nkhawa tikaganizira za imfa makamaka ngati ifeyo kapena munthu amene timamukonda akudwala kwambiri. N’chifukwa chiyani timaopa imfa? Chifukwa Yehova anatilenga m’njira yoti tizilakalaka kukhala ndi moyo mpaka kalekale. (Mlal. 3:11) Ndipotu kuopa imfa moyenera kungatiteteze. Kungatithandize kuti tizisankha moyenera pa nkhani ya zakudya komanso masewera olimbitsa thupi, kupeza thandizo lachipatala pakafunika kutero komanso kupewa kuchita zinthu zimene zingaike moyo wathu pachiswe. Satana amadziwa kuti timaona kuti moyo wathu ndi wamtengo wapatali. Iye amanena kuti tikhoza kulolera kutaya chilichonse ngakhale ubwenzi wathu ndi Yehova, n’cholinga choti titeteze moyo wathu. (Yobu 2:5) Komatu iye amakhala akudzinamiza. Ngakhale zili choncho, popeza kuti iye “ali ndi njira yobweretsera imfa,” amayesa kugwiritsa ntchito mantha achibadwa omwe timakhala nawo pa nkhani ya imfa kuti atichititse kusamvera Yehova.—Aheb. 2:​14, 15. w22.06 18 ¶15-16

Lachisanu, February 9

Dzuwa lisalowe mudakali okwiya. —Aef. 4:26.

Pamene ntchito yathu yaletsedwa, tingafunike kumasonkhana m’timagulu ting’onoting’ono. Choncho n’zofunika kwambiri kuti panopa tizikhala mwamtendere. Tizilimbana ndi Satana osati tokhatokha. Tizinyalanyaza zimene abale athu amalakwitsa kapena tiziyesetsa kuthetsa mwamsanga kusemphana maganizo kulikonse. (Miy. 19:11) Tizikhala okonzeka kuthandizana. (Tito 3:14) Zimene woyang’anira kagulu ka utumiki wina anachita pothandiza mlongo yemwe ankafunika kuthandizidwa zinathandiza kwambiri onse m’kaguluko. Iwo anakhala ogwirizana kwambiri ngati anthu a m’banja limodzi. (Sal. 133:1) Abale ndi alongo athu ambiri akupitirizabe kutumikira Yehova ngakhale kuti ali m’mayiko amene boma linaletsa ntchito yathu. Ena anamangidwa chifukwa cha chikhulupiriro chawo. Tingapempherere abalewa, mabanja awo komanso anthu amene amaika moyo wawo pangozi kuti akalimbikitse abale ndi alongo amenewa ndi mfundo za m’Malemba, kuwapatsa zofunika pa moyo komanso kukawaimira m’makhoti. (Akol. 4:​3, 18) Musamaiwale kuti mapemphero anu angathandize kwambiri abale ndi alongo amenewa.—2 Ates. 3:​1, 2; 1 Tim. 2:​1, 2. w22.12 26-27 ¶15-16

Loweruka, February 10

Kodi iwe amene umaphunzitsa ena, bwanji sudziphunzitsa wekha?—Aroma 2:21.

Nthawi zambiri ana amatengera zimene makolo awo amachita. N’zoona kuti palibe kholo limene sililakwitsa zinthu. (Aroma 3:23) Ngakhale zili choncho, makolo anzeru amayesetsa kuti akhale chitsanzo chabwino kwa ana awo. Bambo wina anafotokoza kuti: “Iwo ali ngati thonje lomwe limangoyamwa chilichonse.” Anawonjezeranso kuti: “Zochita zawo zingasonyeze kuti tikuchita kapena sitikuchita zomwe timawaphunzitsa.” Choncho ngati tikufuna kuti ana athu azikonda Yehova, ifeyo tiyenera kusonyeza kuti timamukonda kwambiri. Pali njira zambiri zimene makolo angaphunzitsire ana awo kukonda Yehova. M’bale wina wachinyamata wazaka 17 dzina lake Andrew anati: “Nthawi zonse makolo anga akhala akundithandiza kuti ndiziona kufunika kwa pemphero. Madzulo alionse bambo anga ankapemphera nane ngakhale zitakhala kuti ndapemphera kale pandekha. . . . Panopa ndimapemphera kwa Yehova momasuka n’kumamuona monga Atate wanga wachikondi.” Makolo, musamakayikire kuti ana anu angayambe kukonda kwambiri Yehova chifukwa choona mmene inuyo mumamukondera. w22.05 28 ¶7-8

Lamlungu, February 11

Tsopano ubatizo . . . ukupulumutsanso inuyo.—1 Pet. 3:21.

Kuti tikhale okonzeka kubatizidwa, chimodzi mwa zinthu zoyambirira zomwe tiyenera kuchita ndi kulapa machimo athu mochokera pansi pa mtima. (Mac. 2:​37, 38) Kulapa kwenikweni kumatithandiza kuti tisinthe. Kodi munasiya makhalidwe amene Yehova amadana nawo monga chiwerewere, kusuta fodya, kulankhula mawu oipa kapena kutukwana? (1 Akor. 6:​9, 10; 2 Akor. 7:1; Aef. 4:29) Pitirizani kuyesetsa kuti musinthe. Mungapemphe amene amakuphunzitsani Baibulo kapena akulu kuti akuthandizeni komanso kukupatsani malangizo. Ngati ndinu wamng’ono ndipo mumakhala ndi makolo anu, pitirizani kuwapempha kuti akuthandizeni kusiya makhalidwe oipa omwe angakulepheretseni kubatizidwa. N’zofunikanso kuti nthawi zonse muzichita zinthu zokhudza kulambira. Zimenezi zikuphatikizapo kupezeka pamisonkhano, kukamba nkhani komanso kupereka ndemanga. (Aheb. 10:​24, 25) Ndipo akakuvomerezani kuti muyambe kulalikira, muzichitanso zimenezo nthawi zonse. w23.03 10-11 ¶14-16

Lolemba, February 12

Yehova Mulungu anauza njokayo kuti: “Chifukwa cha zimene wachitazi, ukhala wotembereredwa.”—Gen. 3:14.

Omwe akutchulidwa pa Genesis 3:​14, 15 akuphatikizapo “njoka.” Njoka yeniyeni sikanamva zomwe Yehova ananena m’munda wa Edeni. Choncho Yehova ankapereka chiweruzo chake kwa cholengedwa chanzeru. Kodi cholengedwachi ndi ndani? Lemba la Chivumbulutso 12:9 limatifotokozera momveka bwino za nkhaniyi. Lembali limati ‘njoka yakaleyi’ ndi Satana Mdyerekezi. Baibulo likamanena za mbewu, mophiphiritsa limanena za onse omwe amaganiza kapena kuchita zinthu ngati bambo wawo wophiphiritsayo. Choncho mbewu ya njoka ndi angelo osakhulupirika ndiponso anthu omwe mofanana ndi Satana, amakana Yehova Mulungu komanso kutsutsa anthu ake. Amenewa akuphatikizapo angelo omwe anasiya utumiki wawo kumwamba munthawi ya Nowa komanso anthu onse oipa omwe amachita zinthu ngati atate wawo Mdyerekezi.—Gen. 6:​1, 2; Yoh. 8:44; 1 Yoh. 5:19; Yuda 6. w22.07 14-15 ¶4-5

Lachiwiri, February 13

Muzitha kusankha zinthu zimene ndi zofunikadi kwambiri.—Afil. 1:10.

Mtumwi Paulo ankakonda kwambiri abale ndi alongo ake. Popeza kuti nayenso ankakumana ndi mavuto, ankatha kuchitira chifundo Akhristu anzake akamakumana ndi mayesero. Pa nthawi ina ndalama zinamuthera moti ankafunika kuti azigwira ntchito kuti azipeza zofunika pa moyo wa iyeyo ndi anzake omwe anali nawo. (Mac. 20:34) Paulo ankadziwa ntchito yokonza matenti. Choncho atafika ku Korinto, poyamba ankagwira ntchito imeneyi limodzi ndi Akula ndi Purisikila. Koma “tsiku la sabata lililonse,” ankalalikira kwa Ayuda ndi Agiriki. Kenako kutabwera Sila ndi Timoteyo, “Paulo anatanganidwa kwambiri ndi ntchito yolalikira mawu a Mulungu.” (Mac. 18:​2-5) Nthawi zonse iye ankakumbukira cholinga chake chachikulu pa moyo, chomwe chinali kutumikira Yehova. Popeza kuti ankachita khama pa nkhani yolalikira komanso kugwira ntchito, iye ankatha kulimbikitsa abale ndi alongo ake. Anawakumbutsa kuti asamalole mavuto komanso udindo wopezera banja zinthu zofunika kuwachititsa kuti azinyalanyaza “zinthu zofunika kwambiri,” zomwe ndi chilichonse chokhudza kulambira Yehova. w22.08 20 ¶3

Lachitatu, February 14

Uthenga wabwino ukuyenera kulalikidwa kwa anthu amitundu yonse.—Maliko 13:10.

Masiku ano, cholinga cha Mulungu ndi choti uthenga wabwino wa Ufumu ulalikidwe padziko lonse. (1 Tim. 2:​3, 4) Ntchitoyi ndi ya Yehova, choncho n’zosangalatsa kwambiri kuti wasankha Mwana wake wokondedwa kuti aziitsogolera. Tingakhale otsimikiza kuti popeza Yesu ndi amene akutsogolera ntchito yolalikirayi, tidzaimaliza monga mmene Yehova akufunira mapeto asanafike. (Mat. 24:14) Kodi tikudziwa bwanji zimenezi? Atangotsala pang’ono kupita kumwamba, Yesu anakumana ndi otsatira ake okhulupirika paphiri ku Galileya. Anawauza kuti: “Ulamuliro wonse waperekedwa kwa ine kumwamba ndi padziko lapansi.” Taonani zimene kenako ananena: “Choncho pitani mukaphunzitse anthu a mitundu yonse kuti akhale ophunzira anga.” (Mat. 28:​18, 19) Yesu anapatsidwanso udindo wotsogolera ntchito yolalikira ndipo inali kudzapitiriza mpaka m’masiku athu ano. w22.07 8 ¶1, 3; 9 ¶4

Lachinayi, February 15

Nthawi ikubwera imene onse amene ali m’manda achikumbutso adzamva mawu ake ndipo adzatuluka. Amene ankachita zabwino adzauka kuti alandire moyo.—Yoh. 5:​28, 29.

Olungama, omwe ndi anthu amene anachita zabwino, “adzauka kuti alandire moyo” chifukwa mayina awo analembedwa kale m’buku la moyo. Kuukitsidwa kwa anthu omwe “ankachita zabwino” kotchulidwa pa Yohane 5:​29, ndi kuuka kwa “olungama” komwe kwatchulidwanso pa Machitidwe 24:15. Mafotokozedwe amenewa ndi ogwirizana ndi zimene zili pa Aroma 6:​7, pomwe pamati: “Chifukwa munthu amene wafa sakhalanso ndi mlandu wa machimo ake.” Pa nthawi imene olungamawa anamwalira, Yehova anawakhululukira zolakwa zawo, koma amakumbukirabe zinthu zosonyeza chikhulupiriro zomwe anachita ali ndi moyo. (Aheb. 6:10) Komabe, olungama omwe adzaukitsidwewa, adzafunika kukhalabe okhulupirika kuti mayina awo apitirize kukhala m’buku la moyo. w22.09 18 ¶13, 15

Lachisanu, February 16

Chilichonse chimene [Yehova] amachita ndi chodalirika.—Sal 33:4.

Mneneri Danieli anasonyeza chitsanzo chabwino kwambiri pa nkhani yokhala wodalirika. Ngakhale kuti anali atatengedwa monga kapolo ku Babulo, posakhalitsa anayamba kudziwika monga munthu wodalirika. Anthu anayamba kumukhulupirira kwambiri pamene mothandizidwa ndi Yehova, anamasulira maloto a Nebukadinezara mfumu ya ku Babulo. (Dan. 4:​20-22, 25) Patapita zaka zambiri Danieli anasonyezanso kuti anali wodalirika pomwe molondola anamasulira uthenga wodabwitsa womwe unaonekera pakhoma la nyumba yachifumu ku Babulo. (Dan. 5:​5, 25-29) Nayenso Dariyo Mmedi ndi anthu audindo mu ufumu wake anaona kuti Danieli “anali ndi luso lodabwitsa.” Iwo anazindikira kuti iye ‘anali wokhulupirika ndipo iwo anapeza kuti sankanyalanyaza udindo wake kapena kuchita zachinyengo zilizonse.’ (Dan. 6:​3, 4) Tingachite bwino kudzifunsa kuti: ‘Kodi ndimadziwika monga munthu amene amakwaniritsa maudindo ake komanso yemwe anthu angamudalire?’ Tikakhala odalirika, anthu amalemekeza Yehova. w22.09 8-9 ¶2-4

Loweruka, February 17

Muzitsanzira Mulungu, monga ana ake okondedwa.—Aef. 5:1.

Timapindula chifukwa chotsatira mfundo za Yehova zokhudza chabwino ndi choipa. Kodi mukudziwa chifukwa chake tikutero? Taganizirani zimene zikanachitika ngati banki iliyonse ikanakhala ndi mfundo zakezake zokhudza mphamvu ya ndalama kapenanso ngati kampani iliyonse ya zomangamanga ikanakhala ndi mfundo zakezake pa nkhani ya miyezo. Bwenzitu kuli chisokonezo. Ndipo ngati azachipatala atalephera kutsatira mfundo zoyenera posamalira odwala, zingachititse kuti odwala ena amwalire. Choncho kutsatira mfundo zodalirika kumateteza. Mofanana ndi zimenezi, mfundo za Mulungu pa nkhani ya chabwino ndi choipa zimatiteteza. Yehova amadalitsa anthu amene amayesetsa kutsatira mfundo zake. Iye amalonjeza kuti: “Olungama adzalandira dziko lapansi, ndipo adzakhala mmenemo mpaka kalekale.” (Sal. 37:29) Taganizirani mmene anthu onse adzakhalire ogwirizana, amtendere komanso osangalala akamadzatsatira mfundo za Yehova. Yehova amafuna kuti mudzasangalale ndi moyo ngati umenewu. Kunena zoona, tonsefe tili ndi zifukwa zomveka zotichititsa kuti tizikonda chilungamo. w22.08 27-28 ¶6-8

Lamlungu, February 18

Ukhalebe woganiza bwino pa zinthu zonse.—2 Tim. 4:5.

Nthawi zina mavuto omwe timakumana nawo angatilepheretse kukhala okhulupirika kwa Yehova ndi gulu lake. Ndiye kodi tingatani kuti tithe kulimbana ndi mavutowa? Tiyenera kupitiriza kukhalabe oganiza bwino, kukhala maso komanso kukhala olimba m’chikhulupiriro. Timakhalabe oganiza bwino tikamakhala odekha komanso tikamaona zinthu mmene Yehova amazionera. Tikamachita zimenezi, maganizo athu sadzasokonekera chifukwa cha mmene tikumvera. Mwina tingaone kuti Mkhristu mnzathu sanatichitire zinthu mwachilungamo ndipo mwinanso ali ndi udindo. N’zodziwikiratu kuti m’baleyo sanali ndi cholinga chokukhumudwitsani. (Aroma 3:23; Yak. 3:2) Komabe mwina zomwe anachitazo zinakukwiyitsani. N’kutheka munadzifunsa kuti, ‘Ngati m’baleyu wachita zimenezi, kodi limenelidi ndi gulu la Mulungu?’ Izitu ndi zomwe Satana amafuna tiziganiza. (2 Akor. 2:11) Maganizo olakwikawa angachititse kuti tisiye Yehova ndi gulu lake. Choncho tiyenera kukhala osamala kuti tisamasunge chakukhosi. w22.11 20 ¶1, 3; 21 ¶4

Lolemba, February 19

Yembekezera Yehova.—Sal. 27:14.

Yehova watipatsa chiyembekezo chabwino kwambiri cha moyo wosatha. Ena akuyembekezera kukakhala kumwamba mpaka kalekale monga zolengedwa zauzimu zomwe sizingafe. (1 Akor. 15:​50, 53) Koma ambiri akuyembekezera kudzakhala mosangalala padzikoli mpaka kalekale komanso ali ndi thanzi labwino. (Chiv. 21:​3, 4) Kaya tikuyembekezera kudzakhala ndi moyo wosatha kumwamba kapena padzikoli, timaona kuti chiyembekezo chathu ndi chamtengo wapatali. Chiyembekezo chathu cha m’tsogolo ndi chotsimikizika chifukwa chimachokera kwa Yehova. (Aroma 15:13) Timadziwa zinthu zimene watilonjeza ndipo timadziwanso kuti nthawi zonse amakwaniritsa malonjezo ake. (Num. 23:19) Ndife otsimikiza kuti Yehova amalakalaka ndipo ali ndi mphamvu yokwaniritsa chilichonse chimene wanena kuti achita. Atate wathu wakumwamba amatikonda ndipo amafuna kuti tizimukhulupirira. Chiyembekezo chathu mwa Yehova chikakhala cholimba, tidzakwanitsa kupirira mayesero, tidzakhalabe olimba mtima ndiponso tidzakhala osangalala kaya tikumane ndi zotani m’tsogolo. w22.10 24 ¶1-3

Lachiwiri, February 20

Iwo ndi anthu opanduka, . . . amene safuna kumva malamulo a Yehova. —Yes. 30:9.

Popeza kuti iwo anakana kumvera, Yesaya ananeneratu kuti Yehova adzawalola kuti akumane ndi mavuto. (Yes. 30:​5, 17; Yer. 25:​8-11) Iwo anatengedwa kupita ku ukapolo ku Babulo. Komabe, panali Ayuda ena okhulupirika ndipo Yesaya anawauza kuti tsiku lina Yehova adzawakomera mtima. (Yes. 30:​18, 19) Ndipo izi ndi zomwe zinachitikadi. Yehova anawamasula ku ukapolo. Komabe, sikuti iye anawamasula nthawi yomweyo. Mawu akuti “Yehova akuyembekezera moleza mtima kuti akukomereni mtima” akusonyeza kuti panafunika kudutsa nthawi kuti Ayuda okhulupirika amasulidwe. Ndipotu Aisiraeli anakhala zaka 70 ku ukapolo ku Babulo asanamasulidwe kuti abwerere kwawo ku Yerusalemu. (Yes. 10:21; Yer. 29:10) Iwo atabwerera, chisoni chomwe anali nacho chinatha ndipo anayamba kukhala mosangalala. w22.11 9 ¶4

Lachitatu, February 21

Osangalala ndi anthu amene azunzidwa chifukwa cha chilungamo.—Mat. 5:10.

Masiku ano, abale ndi alongo athu m’mayiko ambiri akukumana ndi zimenenso atumwi anapirira pomwe ankazunzidwa chifukwa cholalikira za Yesu. Mobwerezabwereza, oweruza a khoti lalikulu la Ayuda ‘anawalamula kuti asiye kulankhula m’dzina la Yesu.’ (Mac. 4:​18-20; 5:​27, 28, 40) Koma iwo ankadziwa kuti yemwe ‘anawalamula kuti alalikire kwa anthu ndi kupereka umboni wokwanira’ wonena za Khristu ali ndi udindo waukulu kuposa oweruzawo. (Mac. 10:42) Choncho polankhula m’malo mwa atumwiwo, Petulo ndi Yohane molimba mtima ananena kuti apitiriza kumvera Mulungu osati oweruzawo ndipo sasiya kulankhula zokhudza Yesu. (Mac. 5:29) Atamenyedwa chifukwa chokhalabe okhulupirika, atumwiwo anachoka pamaso pakhoti lalikulu la Ayudawo “ali osangalala chifukwa Mulungu anawaona kuti ndi oyenera kuchitiridwa chipongwe chifukwa cha dzina la Yesu” ndipo anapitiriza kulalikira.—Mac. 5:​41, 42. w22.10 12-13 ¶2-4

Lachinayi, February 22

Kwa ine, kuyandikira kwa Mulungu ndi chinthu chabwino.—Sal. 73:28.

N’zomveka kuti kuphunzira zokhudza Yehova kumayamba ndi kuphunzira ziphunzitso zoyambirira za m’Baibulo. M’kalata imene analembera Aheberi, mtumwi Paulo anatchula ziphunzitsozi monga “mfundo zoyambirira” za m’Mawu a Mulungu. Iye sankasonyeza kuti ‘mfundo zoyambirirazi’ n’zosafunika, koma ankaziyerekezera ndi mkaka womwe umathandiza kuti mwana akhale wathanzi. (Aheb. 5:12; 6:1) Komabe iye analimbikitsa Akhristu onse kuti asamangokhutira ndi ziphunzitso zoyambirirazi ndipo azipitiriza kuphunzira mfundo zozama za m’Mawu a Mulungu. Kodi mumafunitsitsa kuphunzira mfundo zozama za m’Baibulo? Nanga mukufunitsitsa kupitiriza kuphunzira zokhudza Yehova ndi zolinga zake? Kwa ambirife kuphunzira si kophweka. Nanga bwanji inuyo? Muli kusukulu, kodi kuwerenga ndi kuphunzira sikunkakuvutani? Kodi munkaona kuti kuphunzira n’kosangalatsa komanso kopindulitsa? Kapena munkangoona kuti inuyo simungakwanitse kuphunzira pogwiritsa ntchito mabuku? Ngati ndi choncho, dziwani kuti si muli nokha. Yehova angakuthandizeni. Iye ndi wangwiro komanso Mphunzitsi wabwino kwambiri. w23.03 9-10 ¶8-10

Lachisanu, February 23

Vomerezani kuti mawu amene angathe kukupulumutsani adzalidwe mwa inu.—Yak. 1:21.

Tikakhala ofatsa, tidzalola kuti Mawu a Mulungu akhazikike mumtima mwathu. Tikamapewa kukhala ndi maganizo olakwika komanso mtima wonyada, mfundo za m’Baibulo zokhudza chifundo, kukoma mtima komanso chikondi zidzatithandiza kuti tisinthe. Mmene timachitira zinthu ndi ena zingasonyeze ngati timalola kuti Mawu a Mulungu azitisintha. Afarisi sanalole kuti Mawu a Mulungu aziwafika pamtima ndipo izi zinachititsa kuti ‘aziweruza anthu osalakwa.’ (Mat. 12:7) Mofanana ndi zimenezi mmene timaonera zinthu komanso mmene timachitira zinthu ndi ena, zingasonyeze ngati timalola Mawu a Mulungu kutisintha. Mwachitsanzo, kodi nthawi zambiri timaona zabwino zimene ena amachita kapena timangokhalira kuona zimene amalakwitsa? Kodi ndife achifundo ndiponso timakhala okonzeka kukhululuka kapena timakonda kuweruza ena ndiponso kusunga chakukhosi? Kudzifufuza mwanjira imeneyi kungatithandize kuona ngati timalola zimene timawerenga kuti zisinthe maganizo athu, mmene timamvera komanso zochita zathu.—1 Tim. 4:​12, 15; Aheb. 4:12. w23.02 12 ¶13-14

Loweruka, February 24

Ine, Yehova Mulungu wako, ndagwira dzanja lako lamanja, ine amene ndikukuuza kuti, “Usachite mantha. Ineyo ndikuthandiza.”—Yes. 41:13.

Taganizirani chitsanzo cha Yosefe wa ku Arimateya. Iye ankalemekezedwa kwambiri ndi Ayuda anzake. Yosefe anali mmodzi wa oweruza a Khoti Lalikulu la Ayuda lotchedwa Sanihedirini. Koma pamene Yesu ankachita utumiki wake padzikoli, Yosefe sanali wolimba mtima. Yohane ananena kuti iye anali “wophunzira wachinsinsi wa Yesu chifukwa ankaopa Ayuda.” (Yoh. 19:38) Ngakhale kuti Yosefe ankachita chidwi ndi uthenga wa Ufumu, sanauze ena kuti ankakhulupirira Yesu. Mosakayikira, iye ankaopa kuti ataya udindo wake wapamwamba. Koma Baibulo limatiuza kuti Yesu atafa, pamapeto pake Yosefe “anapita molimba mtima kwa Pilato kukapempha mtembo wa Yesu.” (Maliko 15:​42, 43) Apa Yosefe sanadzibisenso kuti anali wophunzira wa Yesu. Kodi nanunso munayamba mwachitapo mantha ngati mmene anachitira Yosefe? w23.01 30 ¶13-14

Lamlungu, February 25

Anthu anu komanso atumiki anu amene amatumikira pamaso panu nthawi zonse n’kumamva nzeru zanu, ndi osangalala.—1 Maf. 10:8.

Mfumukazi ya ku Seba inamva kuti anthu a ku Aisiraeli ankasangalala ndi mtendere komanso moyo wabwino mu ulamuliro wa Mfumu Solomo. Mfumukaziyo inayenda ulendo wautali kuchoka kwawo kupita ku Yerusalemu kuti ikadzionere yokha. (1 Maf. 10:1) Itayendera ufumu wa Solomo, mfumukaziyi inena mawu ali pamwambawa. Komatu mmene zinthu zinalili mu ufumu wa Solomo, zinkangosonyeza zimene Yehova adzachitire anthu mu ulamuliro wa Mwana wake Yesu. Yesu amaposa Solomo m’zinthu zonse. Solomo sanali wangwiro ndipo ankalakwitsa zinthu, zimene zinachititsa kuti anthu a Mulungu akumane ndi mavuto. Koma Yesu ndi Wolamulira wangwiro yemwe salakwitsa zinthu. (Luka 1:32; Aheb. 4:​14, 15) Khristu anasonyeza kuti sangachimwe kapena kuchita chilichonse chimene chingavulaze nzika zake zokhulupirika. Ndi mwayi wamtengo wapatali kukhala ndi Mfumu ngati imeneyi. w22.12 11 ¶9-10

Lolemba, February 26

Muzimvera amene akutsogolera ndipo muziwagonjera chifukwa iwo amayang’anira miyoyo yanu.—Aheb. 13:17.

Kodi tingatani ngati matenda opatsirana akufalikira m’dera lomwe timakhala? Tiyenera kumvera malangizo omwe angatiteteze monga kusamba m’manja, kukhala motalikirana, kuvala masiki, komanso kukhala kwatokha. Tikamayesetsa kutsatira malangizowa, timasonyeza kuti timayamikira mphatso ya moyo imene Mulungu anatipatsa. Pa nthawi ya ngozi zosiyanasiyana tingamve nkhani zabodza kuchokera kwa anzathu, anthu oyandikana nawo nyumba komanso kwa ofalitsa nkhani. M’malo mokhulupirira “mawu alionse” amene tamva, tingachite bwino kumvera malangizo odalirika ochokera kuboma komanso kwa a zaumoyo. (Miy. 14:15) Bungwe Lolamulira komanso maofesi a nthambi, amayesetsa kufufuza mfundo zolondola asanapereke malangizo okhudza misonkhano yampingo komanso ntchito yolalikira. Kutsatira malangizowa kumathandiza kuti ifeyo komanso anthu ena tikhale otetezeka. Timathandizanso kuti mpingo ukhale ndi mbiri yabwino m’dera lathu.—1 Pet. 2:12. w23.02 23 ¶11-12

Lachiwiri, February 27

Adzamvetsera ndipo adzaphunzira kuopa Yehova Mulungu wanu. —Deut. 31:13.

Pamene Aisiraeli analowa m’Dziko Lolonjezedwa, anakhazikika m’madera osiyanasiyana. Aisiraeli omwe ankakhala dera lina akanatha kusiya kuganizira za Aisiraeli anzawo omwe ankakhala mbali ina m’dzikolo. Koma Yehova anakonza zoti nthawi zambiri Aisiraeli azikumana pamodzi n’cholinga choti amvetsere Mawu ake akamawerengedwa ndiponso kufotokozedwa. (Deut. 31:​10-12; Neh. 8:​2, 8, 18) Tangoganizani mmene Mwisiraeli wokhulupirika ankamvera akafika ku Yerusalemu n’kuona mamiliyoni a olambira anzake ochokera m’madera onse. Mwanjira imeneyi, Yehova ankathandiza anthu ake kukhala ogwirizana. M’kupita kwa nthawi, mpingo wa Chikhristu unakhazikitsidwa ndipo munali amuna ndi akazi olankhula zilankhulo zambiri. Ena anali olemera ndi otchuka ndipo ena anali osauka. Koma onse anali ogwirizana polambira Mulungu woona. Anthu ena omwe anakhala okhulupirira akanatha kumvetsa Mawu a Mulungu pokhapokha ngati akanathandizidwa ndi olambira anzawo komanso kusonkhana nawo limodzi.—Mac. 2:42; 8:​30, 31. w23.02 3 ¶7

Lachitatu, February 28

Moyo wosatha adzaupeza. —Yoh. 17:3.

Yehova akulonjeza kuti anthu omwe amamumvera adzakhala ndi “moyo wosatha.” (Aroma 6:23) Tikamaganizira lonjezoli, timayamba kumukonda kwambiri. Taganizirani izi: Atate wathu wakumwamba amatikonda kwambiri moti palibe chomwe chingatilekanitse ndi iye. Lonjezo la Mulungu la moyo wosatha limatithandiza kupirira mayesero omwe tikukumana nawo panopa. Ngakhale adani athu atiopseze kuti atipha, sitimasiya kutumikira Yehova. Chifukwa chiyani? Chifukwa chimodzi n’chakuti timadziwa kuti ngati tingafe tili okhulupirika kwa Yehova, iye adzatiukitsa ndipo tidzakhala ndi chiyembekezo choti sitidzafanso. (Yoh. 5:​28, 29; 1 Akor. 15:​55-58; Aheb. 2:15) Timadziwa kuti Yehova angatithandize kukhala ndi moyo mpaka kalekale, chifukwa iye ndi Kasupe wa moyo komanso adzakhalapo mpaka kalekale. (Sal. 36:9) Baibulo limatsimikizira kuti Yehova anakhalapo kuyambira kalekale ndipo adzakhalapo mpaka kalekale.—Sal. 90:2; 102:​12, 24, 27. w22.12 2 ¶1-3

Lachinayi, February 29

Ndani adzatisiyanitsa ndi chikondi cha Khristu? Kodi ndi masautso, zowawa, kuzunzidwa?—Aroma 8:35.

Monga atumiki a Yehova sitimadabwa tikamakumana ndi mayesero. Timazindikira kuti monga mmene Baibulo limanenera, “tiyenera kukumana ndi mavuto ambiri kuti tikalowe mu Ufumu wa Mulungu.” (Mac. 14:22) Timadziwanso kuti mavuto athu ena sangatheretu mpaka nthawi imene tidzakhale m’dziko latsopano la Mulungu pamene “imfa sidzakhalaponso. Sipadzakhalanso kulira, kubuula, kapena kupweteka.” (Chiv. 21:4) Yehova samatiteteza kuti tisakumane ndi mayesero. Koma amatithandiza kuti tiziwapirira. Taonani zomwe mtumwi Paulo anauza Akhristu a ku Roma. Choyamba anatchula mayesero amene iye ndi abale ndi alongo ake ankakumana nawo. Kenako analemba kuti: “Tikugonjetsa zinthu zonsezi mothandizidwa ndi iye amene anatikonda.” (Aroma 8:​36, 37) Zimenezi zikutanthauza kuti Yehova angatithandize kuti zinthu zizitiyendera bwino ngakhale pa nthawi imene tikukumana ndi mayesero. w23.01 14 ¶1-2

    Mabuku a Chichewa (1974-2026)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena