Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • es24 tsamba 27-37
  • March

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • March
  • Kuphunzira Malemba Tsiku ndi Tsiku—2024
  • Timitu
  • Lachisanu, March 1
  • Loweruka, March 2
  • Lamlungu, March 3
  • Lolemba, March 4
  • Lachiwiri, March 5
  • Lachitatu, March 6
  • Lachinayi, March 7
  • Lachisanu, March 8
  • Loweruka, March 9
  • Lamlungu, March 10
  • Lolemba, March 11
  • Lachiwiri, March 12
  • Lachitatu, March 13
  • Lachinayi, March 14
  • Lachisanu, March 15
  • Loweruka, March 16
  • Lamlungu, March 17
  • Lolemba, March 18
  • Lachiwiri, March 19
  • Lachitatu, March 20
  • Lachinayi, March 21
  • Lachisanu, March 22
  • Loweruka, March 23
  • TSIKU LA CHIKUMBUTSO
    Dzuwa Litalowa
    Lamlungu, March 24
  • Lolemba, March 25
  • Lachiwiri, March 26
  • Lachitatu, March 27
  • Lachinayi, March 28
  • Lachisanu, March 29
  • Loweruka, March 30
  • Lamlungu, March 31
Kuphunzira Malemba Tsiku ndi Tsiku—2024
es24 tsamba 27-37

March

Lachisanu, March 1

N’chifukwa chiyani ukudzitama? —1 Akor. 4:7.

Mtumwi Petulo analimbikitsa abale ake kugwiritsa ntchito mphatso zili zonse komanso luso limene anali nalo polimbikitsa Akhristu anzawo. Iye analemba kuti: “Aliyense wa inu analandira mphatso, choncho muzigwiritsa ntchito mphatso zanuzo potumikirana. Muzichita zimenezi monga atumiki amene amathandiza ena kuti apindule ndi kukoma mtima kwakukulu kwa Mulungu.” (1 Pet. 4:10) Sitiyenera kulephera kugwiritsira ntchito mokwanira mphatso zimene tili nazo poopa kuti ena achita nsanje kapena akhumudwa. Koma tizisamala kuti tisayambe kudzitama. (1 Akor. 4:6) Tizikumbukira kuti maluso aliwonse omwe tingakhale nawo, ndi mphatso zochokera kwa Mulungu. Tizigwiritsa ntchito mphatsozi polimbikitsa ena mumpingo osati pofuna kuti titchuke. (Afil. 2:3) Tikamagwiritsa ntchito mphamvu komanso luso lathu pochita zimene Mulungu amafuna, tidzakhala osangalala kwambiri osati chifukwa chakuti tikuposa ena kapena kuti tikuoneka apamwamba, koma chifukwa chakuti tikugwiritsa ntchito mphatso zathu potamanda Yehova. w22.04 11-12 ¶7-9

Loweruka, March 2

Tsegulani maso anga kuti ndione bwinobwino zinthu zodabwitsa zam’chilamulo chanu.—Sal. 119:18.

Yesu ankakonda Malemba Oyera ndipo lemba la Salimo 40:​8, limafotokoza mwaulosi mmene iye ankamvera, kuti: “Ndimasangalala kuchita zimene mumafuna, inu Mulungu wanga, Ndipo chilamulo chanu chili mumtima mwanga.” Zimenezi zinachititsa kuti azisangalala potumikira Yehova komanso kuti zinthu zizimuyendera bwino. Ifenso tingamasangalale ndipo zinthu zingamatiyendere bwino tikamayesetsa kuwerenga Mawu a Mulungu komanso kuwakonda. (Sal. 1:​1-3) Mogwirizana ndi Yesu komanso chitsanzo chake, tingamvetse zimene timawerenga m’Baibulo ngati timapemphera, kuwerenga mosathamanga, kufunsa mafunso komanso kulemba mfundo zachidule. Tingagwiritsenso ntchito luso la kuzindikira tikamafufuza zimene tawerenga pogwiritsa ntchito mabuku othandiza kuphunzira Baibulo. Ndipo tingalole kuti Mawu a Mulungu azitisintha tikamayesetsa kukhalabe ndi maganizo oyenera. Tikamachita khama, tidzapindula kwambiri tikamawerenga Baibulo ndipo tidzakhala pa ubwenzi wabwino ndi Yehova.—Sal. 119:17; Yak. 4:8. w23.02 13 ¶15-16

Lamlungu, March 3

Mapulani a munthu wakhama amamuthandiza kuti zinthu zimuyendere bwino.—Miy. 21:5.

Muzisankha cholinga chimene mukufuna kukwaniritsa ndipo kenako muzichita khama kuti muchikwaniritse. Kodi mungachite bwanji zimenezi? Tiyerekeze kuti mukufuna kukulitsa luso lanu lophunzitsa. Mukhoza kuphunzira mosamala kabuku ka Kuwerenga Komanso Kuphunzitsa Mwaluso. Mukapatsidwa nkhani pa misonkhano ya mkati mwa mlungu, mungapemphe m’bale waluso kuti aimvetsere pasadakhale komanso kukufotokozerani momwe mungafunike kukonza. Kuwonjezera pa kukhala waluso, muzikonzekera m’njira yoti anthu aone kuti ndinu wakhama komanso wodalirika. (2 Akor. 8:22) Bwanji ngati mukufuna kukulitsa luso linalake limene mwachibadwa ndi lovuta kwa inu? Musamataye mtima. Kodi Timoteyo anafika pokhala mphunzitsi wabwino kwambiri? Baibulo silinena. Koma n’zosakayikitsa kuti chifukwa chotsatira malangizo a Paulo, iye anapitiriza kuchita bwino kwambiri pa utumiki wake.—2 Tim. 3:10. w22.04 24-25 ¶8-11

Lolemba, March 4

Ndinaona chilombo chikutuluka m’nyanja. Chinali ndi nyanga 10 ndi mitu 7.—Chiv. 13:1.

Kodi chilombo cha mitu 7 chikuimira chiyani? Chilombochi ndi chooneka ngati kambuku, zala zake zooneka ngati za chimbalangondo, pakamwa pake ngati pa mkango ndipo chili ndi nyanga 10. Zilombo 4 zotchulidwa pa Danieli 7 zilinso ndi maonekedwe ngati amenewa. Koma m’buku la Chivumbulutso, ndi chilombo chimodzi chokha chomwe chili ndi maonekedwe onsewa. Chilombochi sichikuimira boma limodzi kapena ulamuliro umodzi wa padziko lonse. Chikufotokozedwa kuti chikulamulira “anthu a fuko lililonse, mtundu uliwonse, chilankhulo chilichonse ndi dziko lililonse.” Choncho chiyenera kukhala ulamuliro waukulu osati boma limodzi lokha. (Chiv. 13:7) Apa ndiye kuti chilombochi chiyenera kuti chikuimira maulamuliro onse omwe akhala akulamulira anthu mpaka pano. (Mlal. 8:9) Chinthu china chomwe chikusonyeza kuti chilombo cha mitu 7 chikuimira maulamuliro onse a padzikoli n’chakuti chili ndi “nyanga 10.” Nthawi zambiri nambala ya 10 m’Baibulo imaimira kukwanira kwa chinthu. w22.05 9 ¶6

Lachiwiri, March 5

Iye adzapukuta misozi yonse m’maso mwawo ndipo imfa sidzakhalaponso. Sipadzakhalanso kulira, kubuula, kapena kupweteka.—Chiv. 21:4.

Kodi ndi ndani adzasangalale ndi madalitso amenewa? Poyamba ndi khamu lalikulu lomwe lidzapulumuke pa Aramagedo komanso ana omwe angadzabadwe m’dziko latsopano. Koma pa Chivumbulutso 20 palinso lonjezo lakuti akufa adzaukitsidwa. (Chiv. 20:​11-13) “Olungama” okhulupirika omwe anamwalira limodzi ndi “osalungama” amene sanapatsidwe mwayi wophunzira za Yehova, adzaukitsidwa padzikoli. (Mac. 24:15; Yoh. 5:​28, 29) Kodi zimenezi zikutanthauza kuti aliyense adzaukitsidwa pa nthawi ya Ulamuliro wa Zaka 1000? Ayi. Anthu oipa omwe anakana mwayi wotumikira Yehova pa nthawi imene anali ndi moyo, sadzaukitsidwa. Iwo atapatsidwa mwayi anasonyeza kuti sanali oyenera kukhala ndi moyo m’Paradaiso.—Mat. 25:46; 2 Ates. 1:9; Chiv. 17:8; 20:15. w22.05 18 ¶16-17

Lachitatu, March 6

Tingapitenso kwa ndani? Inu ndi amene muli ndi mawu othandiza munthu kuti adzapeze moyo wosatha.—Yoh. 6:68.

Kudzera mwa “kapolo wokhulupirika komanso wanzeru,” Yesu anakhazikitsa gulu lochititsa chidwi padzikoli lomwe limalimbikitsa kulambira koyera. (Mat. 24:45) Kodi mumaliona bwanji gulu limeneli? Mwina mumamva ngati mmene mtumwi Petulo anamvera, yemwe anauza Yesu mawu a mu lemba lalerowa. Kodi bwenzi zinthu zili bwanji kwa aliyense wa ife zikanakhala kuti sitinalowe m’gulu la Yehova? Kudzera m’gululi, Khristu amaonetsetsa kuti tikudyetsedwa bwino mwauzimu. Amatiphunzitsanso mmene tingachitire utumiki wathu mwaluso. Kuwonjezera pamenepo, amatithandizanso kuvala “umunthu watsopano” n’cholinga choti tizisangalatsa Yehova. (Aef. 4:24) Yesu amatipatsa malangizo anzeru pa nthawi yamavuto. Tinaona umboni wa zimenezi pa nthawi ya mliri wa COVID-19. Pamene anthu ambiri m’dzikoli sankadziwa zoyenera kuchita, Yesu anaonetsetsa kuti tikulandira malangizo omveka bwino otithandiza kukhala otetezeka. w22.07 12 ¶13-14

Lachinayi, March 7

Muzitha kusankha zinthu zimene ndi zofunikadi kwambiri.—Afil. 1:10.

Yehova anauza Aisiraeli kuti nthawi zonse aziphunzitsa ana awo zokhudza iye. (Deut. 6:​6, 7) Makolo amenewa anali ndi mipata yambiri patsiku yocheza ndi ana awo komanso kuwathandiza kuti azikonda kwambiri Yehova. Mwachitsanzo, mnyamata Wachiisiraeli akanatha kukhala maola ambiri akuthandiza bambo ake kudzala mbewu kapena kukolola. Ndipo mchemwali wake akanatha kukhala nthawi yaitali akuthandiza mayi ake kusoka, kuluka komanso ntchito zina zapakhomo. Choncho makolo ndi ana awo akanatha kukambirana nkhani zambiri zofunika pamene akuchitira zinthu limodzi. Mwachitsanzo, iwo akanatha kukambirana za khalidwe la Yehova la ubwino komanso mmene iye akuthandizira banja lawo. M’mayiko ambiri, makolo sangakhale ali limodzi ndi ana awo kwa tsiku lonse. Mwina angakhale ali kuntchito ndipo anawo angakhale ali kusukulu. Choncho makolo amafunika kuyesetsa kuti azipeza nthawi yolankhula ndi ana awo.—Aef. 5:​15, 16. w22.05 28 ¶10-11

Lachisanu, March 8

Kodi zoonadi inu simukudziwa kuti anthu osalungama sadzalowa mu Ufumu wa Mulungu?—1 Akor. 6:9.

Munthu yemwe wachita tchimo lalikulu amakhala kuti wachita zoipa kwambiri zosemphana ndi malamulo a Mulungu. Zikatere munthuyo ayenera kupemphera kwa Yehova Mulungu komanso kukauza akulu. (Sal. 32:5; Yak. 5:14) Kodi akulu amakhala ndi udindo wotani? Yehova yekha ndiye ali ndi udindo wokhululukira machimo, ndipo amachita zimenezo pogwiritsa ntchito nsembe ya dipo. Komabe iye anapatsa akulu udindo wosankha pogwiritsa ntchito Malemba, ngati munthu wochimwa akufunika kukhalabe mumpingo. (1 Akor. 5:12) Mwa zina, akulu amafunika kupeza mayankho a mafunso awa: Kodi munthuyo anachita kukonzekera kuti achite tchimolo? Kodi ankabisira tchimolo anthu ena? Kodi wakhala akuchita tchimolo kwa nthawi yaitali? Ndipo funso lofunika kwambiri ndi lakuti, kodi pali umboni wosonyeza kuti walapa mochokera pansi pa mtima? Kodi pali umboni woti Yehova wamukhululukira?—Mac. 3:19. w22.06 9 ¶4

Loweruka, March 9

Muzikonda choonadi.—Zek. 8:19.

Yesu analimbikitsa otsatira ake kuti azifunafuna chilungamo. (Mat. 5:6) Zimenezi zikusonyeza kuti munthu ayenera kukhala wofunitsitsa kuchita zoyenera, zabwino komanso zoyera pamaso pa Mulungu. Kodi inuyo mumakonda choonadi ndi chilungamo? Sitikukayikira kuti mumatero. Mumadana ndi mabodza komanso zinthu zonse zoipa. (Sal. 119:​128, 163) Mabodza amasonyeza makhalidwe a Satana yemwe ndi wolamulira wa dzikoli. (Yoh. 8:44; 12:31) Chimodzi mwa zolinga za Satana ndi kudetsa dzina loyera la Yehova Mulungu. Iye wakhala akufalitsa mabodza okhudza Mulungu wathu kungochokera pamene anachimwitsa Adamu ndi Hava m’munda wa Edeni. Satana anachititsa kuti anthu aziona ngati Yehova ndi Wolamulira wodzikonda komanso wachinyengo yemwe amamana anthu zinthu zabwino. (Gen. 3:​1, 4, 5) Mabodza akewa akhala akuchititsa ambiri kuti azimuona molakwika Yehova. Anthu akasankha kuti ‘asamakonde choonadi,’ Satana angawachititse kuti azichita zosalungama zilizonse komanso makhalidwe oipa.—Aroma 1:​25-31. w23.03 2 ¶3

Lamlungu, March 10

Chikondi chokhulupirika [cha Yehova] chidzakhalapo mpaka kalekale. —Sal. 100:5.

N’kutheka kuti mukuyesetsa kuti musiye khalidwe linalake loipa koma nthawi zina mumapezeka kuti mwalichitanso. Kapena mwina mungayambe kutaya mtima komanso kukhumudwa chifukwa choti cholinga chanu sichikukwaniritsidwa msanga. Ndiye kodi n’chiyani chingakuthandizeni kuti mupirire? Ndi khalidwe lofunika kwambiri lomwe ndi kukonda Yehova. Kukonda Yehova ndi khalidwe lofunika kwambiri lomwe muyenera kukhala nalo. (Miy. 3:​3-6) Kukonda kwambiri Mulungu kungatithandize kuti tizipirira mavuto amene timakumana nawo. Nthawi zambiri Baibulo limafotokoza mmene Yehova amasonyezera chikondi chokhulupirika kwa atumiki ake. Chikondichi ndi champhamvu kwambiri moti sichitha zivute zitani. Inuyo munalengedwa m’chifaniziro cha Mulungu. (Gen. 1:26) Ndiye kodi mungasonyeze bwanji chikondi ngati chimenechi? Muziyamikira. (1 Ates. 5:18) Tsiku lililonse muzidzifunsa kuti, ‘Kodi Yehova wasonyeza bwanji kuti amandikonda?’ Kenako muzionetsetsa kuti mukumuthokoza m’mapemphero anu ndipo muzitchula zenizeni zimene wakuchitirani. Muziona kuti chikondicho akusonyeza inuyo panokha. w23.03 12 ¶17-19

Lolemba, March 11

[Yesu] ankadziwa zimene zili mumtima mwa munthu.—Yoh. 2:25.

Yesu ankachita zinthu mokoma mtima ndiponso mwachikondi ndi atumwi 12 onse. Kodi tikuphunzirapo chiyani? Sikuti nkhani imangogona pa zimene ena amachita, koma imaphatikizaponso zimene ifeyo timachita ena akalakwitsa zinthu. Tikakhumudwa chifukwa cha zimene Mkhristu wina wachita tingadzifunse kuti: ‘N’chifukwa chiyani ndikudandaula ndi zomwe wachita? Kodi izi zikusonyeza kuti ndili ndi khalidwe linalake lomwe ndikufunika kusintha? Kodi n’kutheka kuti munthu yemwe wandikhumudwitsayu akulimbana ndi vuto linalake? Ngakhale kuti pali zifukwa zomveka zokhumudwira, kodi ndingasonyeze chikondi chenicheni pongonyalanyaza nkhaniyo?’ Tikamayesetsa kuchita zinthu mwachikondi ndi anthu ena, m’pamenenso timasonyeza kwambiri kuti ndife otsatira oona a Yesu. Chitsanzo cha Yesu chikutiphunzitsanso kuti tiziyesetsa kuwamvetsa Akhristu anzathu. (Miy. 20:5) N’zoona kuti Yesu ankatha kudziwa zimene zili mumtima mwa munthu. Ifeyo sitingathe kutero. Komabe tingathe kuleza mtima abale ndi alongo athu akatikhumudwitsa. (Aef. 4:​1, 2; 1 Pet. 3:8) Kuchita zimenezi sikungakhale kovuta ngati titawadziwa bwino. w23.03 30 ¶14-16

Lachiwiri, March 12

Iye ndi Mulungu wa anthu amoyo, osati akufa.—Luka 20:38.

Pamene tikufunika thandizo lachipatala mwamsanga, nthawi zina Satana angapezerepo mwayi wotichititsa kusankha zinthu molakwika. Madokotala kapena achibale omwe si a Mboni angatikakamize kuti tivomere kuikidwa magazi zomwe zingachititse kuti tiphwanye malamulo a Mulungu. Kapenanso munthu wina angatilimbikitse kuti tipeze thandizo la mankhwala losemphana ndi mfundo za m’Malemba. Ngakhale kuti sitifuna kufa, timadziwa kuti Yehova sadzasiya kutikonda ngakhale titamwalira. (Aroma 8:​37-39) Anzake a Yehova akamwalira, iye amawakumbukirabe ndipo zimangokhala ngati adakali ndi moyo. (Luka 20:37) Amafunitsitsa kudzawaukitsa. (Yobu 14:15) Yehova anapereka malipiro okwera kwambiri n’cholinga choti ‘tidzapeze moyo wosatha.’ (Yoh. 3:16) Timadziwa kuti iye amatikonda kwambiri ndipo amatiganizira. Choncho m’malo mosiya Yehova tikakhala kuti tikudwala kapena tikhoza kufa, timamudalira kuti atilimbikitse, kutipatsa nzeru komanso kutipatsa mphamvu.—Sal. 41:3. w22.06 18 ¶16-17

Lachitatu, March 13

Nzeru yeniyeni ikufuula mumsewu. —Miy. 1:20.

Baibulo limati: “Kuopa Yehova ndi chiyambi cha nzeru, ndipo ngati ungadziwe Mulungu, yemwe ndi Woyera Koposa, udzakhala womvetsa zinthu.” (Miy. 9:10) Choncho tikafuna kusankha zochita pa nkhani yofunika kwambiri tiyenera kudziwa mmene Yehova amaganizira pa nkhaniyo, komwe ndi “kudziwa Woyera Koposa.” Tingachite zimenezo pofufuza m’Baibulo komanso m’mabuku athu. Tikamachita zimenezi timasonyeza kuti tili ndi nzeru yeniyeni. (Miy. 2:​5-7) Yehova yekha ndi amene angatipatse nzeru yeniyeni. (Aroma 16:27) N’chifukwa chiyani tikutero? Choyamba, iye pokhala Mlengi amadziwa chilichonse chokhudza zinthu zimene analenga. (Sal. 104:24) Chachiwiri, chilichonse chimene iye amachita chimasonyeza kuti iye ndi wanzeru. (Aroma 11:33) Chachitatu, onse amene amagwiritsa ntchito malangizo anzeru a Yehova zinthu zimawayendera bwino. (Miy. 2:​10-12) Choncho kuti tipeze nzeru yeniyeni tiyenera kulola kuti mfundo za choonadi zimenezi zizititsogolera tikamasankha zochita komanso tikamachita zimene tasankhazo. w22.10 19 ¶3-4

Lachinayi, March 14

Ndipo kumwamba kunabuka nkhondo: Mikayeli ndi angelo ake anamenyana ndi chinjoka. Chinjokacho ndi angelo ake chinamenya nkhondo, koma sanapambane ndipo malo awo sanapezekenso kumwamba.—Chiv. 12:​7, 8.

Satana sanapambane pa nkhondo yofotokozedwa pa Chivumbulutso 12, ndipo anaponyedwa padzikoli pamodzi ndi ziwanda zake. Chifukwa cha mkwiyo, iye anayamba kulimbana ndi anthu, zomwe zinachititsa ‘tsoka padziko lapansi.’ (Chiv. 12:​9-12) Kodi maulosiwa amatithandiza bwanji? Zochitika padzikoli komanso kuona mmene anthu asinthira makhalidwe awo zimatithandiza kudziwa kuti Yesu anakhala Mfumu. Choncho m’malo mokhumudwa chifukwa choona kuti anthu ndi odzikonda komanso amadana ndi anzawo, tizikumbukira kuti zochita zawo zikukwaniritsa maulosi a m’Baibulo. Apa n’zoonekeratu kuti Ufumu ukulamulira. (Sal. 37:1) Ndipo tiziyembekezera kuti mavuto awonjezeka makamaka pamene Aramagedo ikuyandikira. (Maliko 13:8; 2 Tim. 3:13) Kodi simukuthokoza Atate wathu wakumwamba chifukwa chotithandiza kumvetsa chifukwa chake padzikoli pali mavuto ambiri? w22.07 3-4 ¶7-8

Lachisanu, March 15

Pemphero lopembedzera la munthu wolungama limagwira ntchito mwamphamvu kwambiri.—Yak. 5:16.

Tingapemphe Yehova kuti athandize Akhristu anzathu kupirira matenda, ngozi zam’chilengedwe, nkhondo, kuzunzidwa kapenanso mavuto ena. Tingapemphererenso abale ndi alongo amene amagwira ntchito mwakhama pothandiza omwe akumana ndi mavuto. Mwina mukudziwa ena amene akukumana ndi mavuto ngati amenewa. Bwanji osatchula mayina awo mukamapemphera panokha? Timasonyeza kuti timawakonda tikamapempha Yehova kuti awathandize kupirira. Abale omwe amatsogolera mpingo amayamikira kwambiri tikamawapempherera ndipo mapempherowa amawathandiza. Ndi mmenenso zinalili ndi mtumwi Paulo. Iye analemba kuti: “Muzipemphereranso ineyo kuti ndikayamba kulankhula ndizipeza mawu oyenerera n’cholinga choti ndizitha kulankhula molimba mtima ndikamalalikira zokhudza chinsinsi chopatulika cha uthenga wabwino.” (Aef. 6:19) Masiku anonso pali abale ambiri omwe amagwira ntchito mwakhama potitsogolera. Timasonyeza kuti timawakonda tikamapempha Yehova kuti aziwathandiza pa ntchito yawo. w22.07 23-24 ¶14-16

Loweruka, March 16

Tivalenso chiyembekezo cha chipulumutso ngati chisoti.—1 Ates. 5:8.

Chisoti chimene msilikali amavala, chimamuteteza kuti adani asamuvulaze m’mutu. Pa nkhondo yathu yauzimu, timafunika kuteteza maganizo athu kuti Satana asawawononge. Iye amalimbana nafe pogwiritsa ntchito mayesero komanso mfundo zimene cholinga chake ndi kusokoneza maganizo athu. Monga mmene chisoti chimatetezera mutu wa msilikali, chiyembekezo chathu chimateteza maganizo athu kuti tipitirizebe kukhala okhulupirika kwa Yehova. Chiyembekezo chathu chikafooka, ndipo tikayamba kumangoganizira zofuna zathu, tingasiye kukhala ndi chiyembekezo cha moyo wosatha. Taganizirani zimene zinachitikira Akhristu ena a ku Korinto. Iwo anasiya kukhulupirira lonjezo lofunika kwambiri la Mulungu lakuti akufa adzauka. (1 Akor. 15:12) Paulo ananena kuti anthu omwe sankakhulupirira kuti akufa adzauka ankakhala moyo wongokhutiritsa zilakolako zawo. (1 Akor. 15:32) Masiku anonso anthu amene sayembekezera malonjezo a Mulungu, amachita china chilichonse chomwe angathe kuti akhale moyo wosangalala panopa. Koma ife timakhulupirira kwambiri malonjezo a Mulungu.—w22.10 25-26 ¶8-9

Lamlungu, March 17

Muzipemphera nthawi zonse. —1 Ates. 5:17.

Yehova amakuuzani kuti muzipemphera kwa iye. Iye amaona mavuto amene mukukumana nawo ndipo amakutsimikizirani kuti adzamvetsera mapemphero anu nthawi iliyonse. Amasangalala kumvetsera atumiki ake akamapemphera kwa iye. (Miy. 15:8) Kodi mungapempherere zinthu ziti mukamadzimva kuti muli nokhanokha? Muziuza Yehova zonse za mumtima mwanu. (Sal. 62:8) Muzimufotokozera zimene zikukudetsani nkhawa komanso mmene zimenezo zikukukhudzirani ndiponso kuti akuthandizeni kukhala olimba mtima. Mungamupemphenso kuti akupatseni nzeru kuti muthe kufotokoza mwaluso zimene mumakhulupirirazo. (Luka 21:​14, 15) Ngati mukuvutika ndi maganizo ena ake ofooketsa, mungapemphe Yehova kuti akuthandizeni kulankhula ndi Mkhristu wolimba mwauzimu. Mungamupemphenso kuti athandize munthu amene mukumufotokozerayo kuti amvetse mmene mukumvera. Muziona mmene Yehova akuyankhira mapemphero anu komanso kulola ena kuti akuthandizeni. Mukamachita zimenezi mudzayamba kuona kuti simuli nokhanokha. w22.08 10 ¶6

Lolemba, March 18

Anthu onsewa akuchita zotsutsana ndi malamulo a Kaisara.—Mac. 17:7.

Mpingo watsopano wa ku Tesalonika unayamba kutsutsidwa kwambiri. Anthu achiwawa anakokera “abale ena kwa olamulira a mzindawo.” (Mac. 17:6) Tangoganizani mmene Akhristu atsopanowo anachitira mantha, ataona kuti anthu amumzindawo awaukira. Iwo akanatha kusiya kuchita khama potumikira Yehova, koma mtumwi Paulo sankafuna kuti zimenezi ziwachitikire. Iye anaonetsetsa kuti mpingo watsopanowo ukusamalidwa moyenera. Paulo anakumbutsa Akhristu a ku Tesalonikawo kuti: “Tinatumiza Timoteyo m’bale wathu, . . . kuti adzakulimbikitseni ndi kukutonthozani n’cholinga choti chikhulupiriro chanu chikhale cholimba. Tinachita zimenezi kuti pasapezeke aliyense amene chikhulupiriro chake chafooka ndi masautso amenewa.” (1 Ates. 3:​2, 3) Timoteyo anaona mmene Paulo analimbikitsira abale a ku Lusitara. Pokumbukira mmene Yehova anawadalitsira, Timoteyo akanatha kutsimikizira abale ndi alongo atsopanowo kuti nawonso zinthu ziwayendera bwino.—Mac. 14:​8, 19-22; Aheb. 12:2. w22.08 21 ¶4

Lachiwiri, March 19

Tidzapeze moyo wosatha kudzera mwa iye.—1 Yoh. 4:9.

Chakumapeto kwa zaka za m’ma 1800, kagulu ka Ophunzira Baibulo kotsogoleredwa ndi Charles Taze Russell kanayamba kuphunzira Malemba mosamala kwambiri. Iwo ankafuna kudziwa zoona zenizeni zimene nsembe ya Yesu imatanthauza komanso mmene anthu ayenera kukumbukirira imfa yake. Zimene Akhristu oona mtimawa anafufuza zaka zambiri zapitazo, zimatithandizanso masiku ano. Motani? Timamvetsa choonadi chokhudza nsembe ya Yesu komanso zimene nsembeyo imakwaniritsa. (1 Yoh. 2:​1, 2) Taphunziranso zimene Baibulo limafotokoza zokhudza chiyembekezo chomwe anthu omwe amasangalatsa Mulungu ali nacho, kuti ena adzakhala ndi moyo wosafa kumwamba komanso ena adzakhala ndi moyo wosatha padziko lapansi. Timakhala pa ubwenzi wolimba ndi Yehova tikamaganizira chikondi chomwe amatisonyeza komanso mmene aliyense payekha amapindulira chifukwa cha nsembe ya Yesu. (1 Pet. 3:18) Choncho mofanana ndi abale athu okhulupirika akale, timaitanira ena kuti adzakhale nafe pamwambo wa Chikumbutso womwe umachitika mofanana ndi mmene Yesu anachitira. w23.01 21 ¶6-7

Kuwerenga Baibulo pa nyengo ya Chikumbutso: (Zochitika pa Nisani 9 dzuwa litalowa) Maliko 14:​3-9

Lachitatu, March 20

Iye anafera onse kuti amene ali moyo asakhale moyo wongodzisangalatsa okha, koma akhale moyo wosangalatsa amene anawafera n’kuukitsidwa.—2 Akor. 5:15.

Yesu ankaphunzitsa anthu zokhudza madalitso omwe Ufumu wa Mulungu udzabweretse. Timayamikiranso dipo chifukwa limatipatsa mwayi wokhala pa ubwenzi wabwino ndi Yehova ndi Yesu. Onse amene amakhulupirira Yesu alinso ndi chiyembekezo chodzakhala ndi moyo mpaka kalekale komanso kudzaona okondedwa awo omwe anamwalira. (Yoh. 5:​28, 29; Aroma 6:23) Palibe chomwe tinachita kuti tiyenerere madalitso amenewa, komanso sitingathe kubwezera Mulungu ndi Yesu pa zonse zomwe anatichitira. (Aroma 5:​8, 20, 21) Komabe tingathe kuwasonyeza kuti timayamikira kwambiri. Motani? Pogwiritsa ntchito zinthu zathu popititsa patsogolo ntchito ya Ufumu. Mwachitsanzo, tingathandize nawo pa ntchito yomanga ndi kukonza malo amene timagwiritsa ntchito pa kulambira koona. w23.01 26 ¶3; 28 ¶5

Kuwerenga Baibulo pa nyengo ya Chikumbutso: (Zochitika pa Nisani 9 kutacha) Maliko 11:​1-11

Lachinayi, March 21

Ndinaona Mwanawankhosa . . . limodzi ndi enanso 144,000.—Chiv. 14:1.

Olamulira a Ufumu wa Mulungu adzathandiza anthu mabiliyoni padziko lonse lapansi. Mofanana ndi Yesu, a 144,000 adzatumikira monga mafumu ndi ansembe. (Chiv. 5:10) Potsatira Chilamulo cha Mose, udindo waukulu wa ansembe unali woonetsetsa kuti anthu ali ndi thanzi labwino komanso ali pa ubwenzi wabwino ndi Yehova. Popeza Chilamulo chinkangochitira “chithunzi zinthu zabwino zimene zikubwera,” n’zomveka kunena kuti olamulira anzake a Yesu adzathandiza anthu kukhala ndi thanzi labwino komanso kukhala pa ubwenzi wabwino ndi Mulungu. (Aheb. 10:1) Tikungofunika kuyembekezera kuti tidzaone mmene mafumu ndi ansembewa adzathandizire nzika za Ufumu zomwe zidzakhale padziko lapansi. Ndife otsimikiza kuti m’Paradaiso akubwerayo, anthu omwe adzakhale padzikoli adzapatsidwa malangizo omwe adzafunikire.—Chiv. 21:​3, 4. w22.12 11 ¶11-13

Kuwerenga Baibulo pa nyengo ya Chikumbutso: (Zochitika pa Nisani 10 kutacha) Maliko 11:​12-19

Lachisanu, March 22

Mukulengeza imfa ya Ambuye, mpaka iye adzafike.—1 Akor. 11:26.

Chifukwa chimodzi chomwe chimatichititsa kuitanira ena ku Chikumbutso, ndi chakuti timafuna adzaphunzire zimene Yehova ndi Yesu atichitira. (Yoh. 3:16) Timayembekezera kuti zimene adzaone komanso kumva pamwambowu zidzawalimbikitsa kuti afune kudziwa zambiri komanso akhale atumiki a Yehova. Timaitaniranso anthu omwe anasiya kutumikira Yehova pofuna kuwakumbutsa kuti Mulungu amawakondabe. Ambiri amabwera tikawaitana ndipo timasangalala kwambiri kuwaona. Kupezeka pamwambowu kumawakumbutsa mmene ankasangalalira pamene ankatumikira Yehova. (Sal. 103:​1-4) Kaya anthu abwera ku Chikumbutso kapena ayi, timawaitanirabe mwakhama podziwa kuti Yehova amachita chidwi ndi munthu aliyense payekha.—Luka 15:7; 1 Tim. 2:​3, 4. w23.01 20 ¶1; 22-23 ¶9-11

Kuwerenga Baibulo pa nyengo ya Chikumbutso: (Zochitika pa Nisani 11 kutacha) Maliko 11:20–12:​27, 41-44

Loweruka, March 23

Diso la Yehova limayang’ana anthu amene amamuopa.—Sal. 33:18.

Pa usiku wake womaliza, Yesu anapereka pemphero lapadera kwa Atate wake wakumwamba, lopempha kuti aziyang’anira otsatira ake. (Yoh. 17:​15, 20) Yehova wakhala akuyang’anira, kusamalira komanso kuteteza anthu ake. Komabe Yesu ankadziwa kuti otsatira ake azidzatsutsidwa kwambiri ndi Satana. Yesu ankadziwanso kuti ophunzirawo adzafunika kuthandizidwa ndi Yehova kuti athe kupirira Mdyerekezi akamawaukira. Dziko lolamulidwa ndi Satanali limachititsa kuti Akhristu oona azikumana ndi mavuto ambiri. Timakumana ndi mavuto omwe angatifooketse komanso angayese kukhulupirika kwathu kwa Yehova. Koma sitiyenera kuopa. Yehova amatiyang’anira, amaona mavuto amene timakumana nawo ndipo nthawi zonse ndi wokonzeka kutithandiza. Inde, “diso la Yehova limayang’ana anthu amene amamuopa . . . kuti awapulumutse.”—Sal. 33:​18-20. w22.08 8 ¶1-2

Kuwerenga Baibulo pa nyengo ya Chikumbutso: (Zochitika pa Nisani 12 kutacha) Maliko 14:​1, 2, 10, 11; Mateyu 26:​1-5, 14-16

TSIKU LA CHIKUMBUTSO
Dzuwa Litalowa
Lamlungu, March 24

Muzichita zimenezi pondikumbukira.—Luka 22:19.

Chaka chilichonse pa nyengo ya Chikumbutso, timasonyeza kuyamikira zomwe anatichitira popemphera komanso kuganizira kwambiri tanthauzo la imfa ya Yesu. Timalimbikitsanso anthu ambiri kuti adzakhale nafe pamwambo wapaderawu. Timakhala otsimikiza kuti tisalole chilichonse kutilepheretsa kupezeka pa Chikumbutso. Pa Chikumbutso, timaphunzira chifukwa chake anthu amafunikira dipo komanso mmene limathandizira kuti machimo a anthu ambiri akhululukidwe. Timakumbutsidwa zimene mkate ndi vinyo zimaimira komanso amene ayenera kudya ndi kumwa. (Luka 22:​19, 20) Komanso timaganizira madalitso amene anthu omwe ali ndi chiyembekezo chodzakhala padzikoli adzapeze. (Yes. 35:​5, 6; 65:​17, 21-23) Tisamaone mopepuka mfundo za choonadizi. w23.01 20 ¶2; 21 ¶4

Kuwerenga Baibulo pa nyengo ya Chikumbutso: (Zochitika pa Nisani 13 kutacha) Maliko 14:​12-16; Mateyu 26:​17-19 (Zochitika pa Nisani 14 dzuwa litalowa) Maliko 14:​17-72

Lolemba, March 25

Mulungu anakonda kwambiri dziko moti anapereka Mwana wake wobadwa yekha, kuti aliyense womukhulupirira . . . akhale ndi moyo wosatha.—Yoh. 3:16.

Popereka Mwana wake monga dipo lophimba machimo athu, Mulungu anachititsa kuti zikhale zotheka kuti tidzapeze moyo wosatha. (Mat. 20:28) Mtumwi Paulo analemba kuti: “Imfa inabwera kudzera mwa munthu mmodzi, kuuka kwa akufa kunabweranso kudzera mwa munthu mmodzi. Monga zilili kuti anthu onse amafa chifukwa cha Adamu, anthu onse adzapatsidwanso moyo kudzera mwa Khristu.” (1 Akor. 15:​21, 22) Yesu anaphunzitsa otsatira ake kuti azipemphera kuti Ufumu wa Mulungu ubwere komanso chifuniro cha Mulungu chichitike padziko lapansi. (Mat. 6:​9, 10) Mbali ina ya cholinga cha Mulungu ndi yakuti anthu adzakhale padzikoli mpaka kalekale. Kuti zimenezi zitheke, Yehova wasankha Mwana wake kuti akhale Mfumu ya Ufumu wa Mesiya. Mulungu wakhala akusonkhanitsa anthu okwana 144,000 padzikoli kuti adzagwire ntchito ndi Yesu pokwaniritsa cholinga chake.—Chiv. 5:​9, 10. w22.12 5 ¶11-12

Kuwerenga Baibulo pa nyengo ya Chikumbutso: (Zochitika pa Nisani 14 kutacha) Maliko 15:​1-47

Lachiwiri, March 26

Chikondi chimene Khristu ali nacho chimatikakamiza . . . kuti amene ali moyo asakhale moyo wongodzisangalatsa okha.—2 Akor. 5:​14, 15.

Munthu yemwe timamukonda akamwalira timamusowa kwambiri. Poyamba tingamamve chisoni, makamaka ngati anavutika kwambiri asanamwalire. Komabe n’kupita kwa nthawi tingayambe kusangalala tikamaganizira zinazake zomwe anatiphunzitsa, zimene anachita kapenanso zimene analankhula n’cholinga choti atilimbikitse kapena tisekerere. Mofanana ndi zimenezi, timamva chisoni tikawerenga zokhudza kuvutika komanso imfa ya Yesu. Pa nyengo ya Chikumbutso timaganizira makamaka kufunika kwa nsembe yake ya dipo. (1 Akor. 11:​24, 25) Komabe timasangalala kwambiri tikaganizira zonse zimene ananena komanso kuchita ali padzikoli. Timalimbikitsidwanso tikaganizira zimene akuchita panopa ndiponso zimene adzatichitire m’tsogolo. w23.01 26 ¶1-2

Kuwerenga Baibulo pa nyengo ya Chikumbutso: (Zochitika pa Nisani 15 kutacha) Mateyu 27:​62-66 (Zochitika pa Nisani 16 dzuwa litalowa) Maliko 16:1

Lachitatu, March 27

Muziika Ufumu . . . pamalo oyamba.—Mat. 6:33.

Pamene Yesu anaphedwa, ophunzira ake anakhumudwa kwambiri. Sikuti iwo ankangoona kuti ataya mnzawo wapamtima koma ankaonanso kuti alibe chiyembekezo. (Luka 24:​17-21) Komabe ataonekera kwa iwo, Yesu anawathandiza kumvetsa mmene zomwe zinamuchitikira zinakwaniritsira ulosi wa m’Baibulo. Anawapatsanso ntchito yofunika kwambiri yoti agwire. (Luka 24:​26, 27, 45-48) Pamene Yesu ankakwera kumwamba, chisoni cha ophunzirawo chinasanduka chimwemwe chachikulu. Kudziwa kuti Mbuye wawo ali moyo komanso ndi wokonzeka kuwathandiza pantchito yatsopano imene anawapatsa, kunawathandiza kukhala osangalala. Chimwemwe chimene anali nacho chinawathandiza kuti azitamanda Yehova mwakhama. (Luka 24:​52, 53; Mac. 5:42) Kuti titsanzire ophunzira a Yesu, m’pofunika kuti tiziika Ufumu wa Mulungu pamalo oyamba. Ngakhale kuti timafunika kupirira kuti tipitirize kutumikira Yehova, iye amalonjeza kuti adzatidalitsa kwambiri tikamachita zimenezo.—Miy. 10:22. w23.01 30-31 ¶15-16

Kuwerenga Baibulo pa nyengo ya Chikumbutso: (Zochitika pa Nisani 16 kutacha) Maliko 16:​2-8

Lachinayi, March 28

Kufumbiko udzabwerera. —Gen. 3:19.

Ifeyo sitifuna kulakwitsa ngati mmene Adamu ndi Hava anachitira. Tingapewe zimenezi ngati titapitiriza kuphunzira zokhudza Yehova, kuyamikira makhalidwe ake komanso kuyesetsa kuti tizimvetsa mmene amaganizira. Tikatero tidzayamba kumukonda kwambiri. Taganizirani za Abulahamu. Iye ankakonda kwambiri Yehova. Ngakhale pamene zinkamuvuta kumvetsa zimene Yehova wasankha, iye ankamumverabe ndipo ankayesetsa kuti amudziwe bwino. Mwachitsanzo, atadziwa kuti Yehova akufuna kuwononga Sodomu ndi Gomora, poyamba Abulahamu ankaopa kuti mwina “Woweruza wa dziko lonse lapansi,” awononga oipa pamodzi ndi olungama omwe. Abulahamu ankaona kuti zimenezi ndi zosayenera choncho modzichepetsa anafunsa Yehova mafunso angapo. Yehova anamuyankha moleza mtima. Pamapeto pake Abulahamu anazindikira kuti Yehova amafufuza mtima wa munthu aliyense ndiponso kuti sapereka chilango kwa anthu oipa limodzi ndi osalakwa omwe.—Gen. 18:​20-32. w22.08 28 ¶9-10

Lachisanu, March 29

Munthu wokhulupirika amasunga chinsinsi.—Miy. 11:13.

Mu 455 B.C.E., Bwanamkubwa Nehemiya atamaliza kumanga mpanda wa Yerusalemu, anafufuza amuna odalirika omwe anawaika pa udindo woyang’anira mzindawo. Pa anthu omwe anawasankha panalinso Hananiya kalonga wa m’Nyumba Yachitetezo Champhamvu. Baibulo limanena kuti Hananiya “anali munthu wodalirika ndiponso woopa kwambiri Mulungu woona kuposa anthu ena ambiri.” (Neh. 7:2) Kukonda Yehova komanso kuopa kumukhumudwitsa kunachititsa Hananiya kuona kuti utumiki uliwonse umene anapatsidwa unali wofunika kwambiri. Makhalidwe amenewa angatithandizenso ifeyo kukhala odalirika tikamatumikira Mulungu. Taganizirani chitsanzo cha Tukiko yemwe anali mnzake wodalirika wa mtumwi Paulo. Paulo ankadalira Tukiko ndipo anamufotokoza kuti anali “mtumiki wokhulupirika.” (Aef. 6:​21, 22) Sikuti Paulo ankangomudalira pa nkhani yokapereka makalata ku Efeso ndi ku Kolose koma ankamudaliranso kuti akalimbikitsa ndi kutonthoza Akhristu kumeneko. Tukiko amatikumbutsa za abale okhulupirika komanso odalirika masiku ano, omwe amatithandiza kukhala pa ubwenzi wolimba ndi Yehova.—Akol. 4:​7-9. w22.09 9-10 ¶5-6

Loweruka, March 30

Chikondi chimakwirira machimo ochuluka.—1 Pet. 4:8.

Yosefe anakumana ndi mayesero aakulu kwambiri kwa zaka pafupifupi 13. Yosefe akanatha kukayikira ngati Yehova ankamukondadi. Akanathanso kumaona ngati Yehova wamusiya pamene akufunikira thandizo. Koma iye sanalole kuti zimenezi zimukhumudwitse. Anapitirizabe kukhala woganiza bwino pokhala wodekha. Pamene anali ndi mpata woti akanatha kuwabwezera abale akewo, iye sanatero koma anawasonyeza chikondi komanso anawakhululukira. (Gen. 45:​4, 5) Yosefe anakwanitsa kuchita zimenezi chifukwa ankaganiza bwino. M’malo moganizira mavuto omwe ankakumana nawo, iye ankaganizira nkhani yofunika kwambiri yokhudza cholinga cha Yehova. (Gen. 50:​19-21) Kodi tikuphunzirapo chiyani? Mukachitiridwa zinthu zopanda chilungamo, musamakwiyire Yehova kapena kuyamba kuona kuti wakutayani. M’malomwake, muziganizira mmene akukuthandizirani kupirira mayeserowo. Kuwonjezera pamenepo, ena akakulakwirani muziphimba zolakwa zawo ndi chikondi chanu. w22.11 21 ¶4

Lamlungu, March 31

Maulamuliro onse adzawatumikira ndi kuwamvera.—Dan. 7:27.

Mneneri Danieli anaona masomphenya omwe amasonyeza bwino kuti Yehova ndi wamkulu kwambiri kuposa olamulira onse. Choyamba Danieli anaona zilombo zazikulu 4, zomwe zikuimira maulamuliro omwe anali amphamvu padziko lonse monga Babulo, Mediya ndi Perisiya, Girisi, Roma komanso ulamuliro wa Britain ndi America, womwe ukulamulira panopa. (Dan. 7:​1-3, 17) Kenako Danieli anaona Yehova Mulungu atakhala pampando wachifumu mu khoti lake kumwamba. (Dan. 7:​9, 10) Mulungu anatenga mphamvu zonse ndi ulamuliro womwe maboma anali nawo n’kuzipereka kwa oyenerera komanso amphamvu kwambiri. Ndiye kodi anazipereka kwa ndani? Anazipereka kwa “winawake wooneka ngati mwana wa munthu,” Yesu Khristu komanso “oyera a Mulungu Wamkulu,” omwe ndi a 144, 000 amene adzalamulire “mpaka kalekale.” (Dan. 7:​13, 14, 18.) N’zoonekeratu kuti Yehova ndiye “Mulungu Wamkulu” amene akutchulidwayu. Zimene Danieli anaona m’masomphenya zikugwirizana kwambiri ndi zimene anali atanena kale. Danieli ananena kuti: “Mulungu wakumwamba amachotsa mafumu komanso kuika mafumu.”—Dan. 2:​19-21. w22.10 14-15 ¶9-11

    Mabuku a Chichewa (1974-2026)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena