Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • es24 tsamba 37-47
  • April

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • April
  • Kuphunzira Malemba Tsiku ndi Tsiku—2024
  • Timitu
  • Lolemba, April 1
  • Lachiwiri, April 2
  • Lachitatu, April 3
  • Lachinayi, April 4
  • Lachisanu, April 5
  • Loweruka, April 6
  • Lamlungu, April 7
  • Lolemba, April 8
  • Lachiwiri, April 9
  • Lachitatu, April 10
  • Lachinayi, April 11
  • Lachisanu, April 12
  • Loweruka, April 13
  • Lamlungu, April 14
  • Lolemba, April 15
  • Lachiwiri, April 16
  • Lachitatu, April 17
  • Lachinayi, April 18
  • Lachisanu, April 19
  • Loweruka, April 20
  • Lamlungu, April 21
  • Lolemba, April 22
  • Lachiwiri, April 23
  • Lachitatu, April 24
  • Lachinayi, April 25
  • Lachisanu, April 26
  • Loweruka, April 27
  • Lamlungu, April 28
  • Lolemba, April 29
  • Lachiwiri, April 30
Kuphunzira Malemba Tsiku ndi Tsiku—2024
es24 tsamba 37-47

April

Lolemba, April 1

Chikhulupiriro chanu chikakhalabe cholimba pamene mukuyesedwa, mumaphunzira kukhala opirira.—Yak. 1:3.

Dzifunseni kuti: ‘Kodi ndimatani ndikapatsidwa malangizo? Kodi ndimavomereza mwamsanga zimene ndalakwitsa kapena ndimadziikira kumbuyo? Kodi ndimafulumira kuimba ena mlandu?’ Mukamawerenga nkhani za amuna ndi akazi okhulupirika otchulidwa m’Baibulo, muziganizira zimene anachita atakumana ndi zoterezi. Pa nkhani iliyonse imene mwawerenga muzidzifunsa kuti: ‘Kodi ndingamutsanzire bwanji mtumiki wa Yehova wokhulupirikayu?’ Tingapindulenso poona zimene Akhristu anzathu amachita, kaya ndi achikulire kapena achinyamata. Mwachitsanzo, kodi pali winawake mumpingo wanu yemwe akupirira mokhulupirika mayesero monga matenda, kukakamizidwa ndi anzake kuti achite zosayenera kapena kutsutsidwa ndi anthu a m’banja lake? Kodi mumaona makhalidwe ena ake abwino mwa munthu ameneyo, omwe inunso mukufunitsitsa kukhala nawo? Kuganizira chitsanzo chake chabwino, kungakuthandizeni kudziwa zimene mungachite kuti muthe kupirira mayesero amene mukukumana nawo. Timayamikira komanso kusangalala kuti tili ndi abale ndi alongo okhulupirika omwe tingatengere chitsanzo chawo.—Aheb. 13:7. w22.04 13 ¶13-14

Lachiwiri, April 2

Kupatsa kumatichititsa kukhala osangalala kwambiri kuposa kulandira.—Mac. 20:35.

Tikakumana ndi mavuto enaake, timayamikira mkulu wachikondi akapatula nthawi yake kuti atimvetsere komanso kutilimbikitsa. Tikafuna thandizo pa nkhani ya mmene timachititsira phunziro la Baibulo, timasangalala mpainiya waluso akavomera kukhala nawo paphunzirolo komanso kutipatsa malangizo. Abale ndi alongo onsewo amasangalala kutithandiza. Ifenso tingamasangalale ngati titamadzipereka kuti tithandize abale athu. Ndiye ngati mukufuna kuchita zambiri pambali zimenezi komanso m’njira zina, n’chiyani chingakuthandizeni kukwaniritsa zolinga zanuzo? Muzidziikira cholinga chenicheni chimene mukufuna kuti muchikwaniritse. Mwachitsanzo, mwina mungaganize kuti, ‘Ndikufuna ndizichita zambiri mumpingo.’ Komatu zingakhale zovuta kudziwa mmene mungakwaniritsire cholinga ngati chimenecho ndipo mwina simungadziwe ngati mwachikwaniritsa. Choncho muzidziwa zenizeni zimene mukufuna kuchita. Mungathe kulemba penapake cholingacho komanso zimene mukufuna kuchita kuti muchikwaniritse. w22.04 25 ¶12-13

Lachitatu, April 3

Uzikonda mnzako mmene umadzikondera wekha.—Yak. 2:8.

Panopa Yehova akusonkhanitsa a “khamu lalikulu” komanso kuwaphunzitsa kuti akhale nzika za Ufumu wake. (Chiv. 7:​9, 10) Ngakhale kuti masiku ano anthu ambiri m’dzikoli ndi ogawikana chifukwa cha chidani komanso nkhondo, a khamu lalikuluwa amayesetsa kukhala mwamtendere posatengera kuti akuchokera m’mayiko kapena mitundu yosiyana. Mophiphiritsa iwo asula kale malupanga awo kuti akhale makasu a pulawo. (Mika 4:3) M’malo momenya nawo nkhondo zomwe zimaphetsa anthu ambiri, iwo amathandiza anthu kupeza “moyo weniweniwo” powaphunzitsa zokhudza Mulungu woona komanso zolinga zake. (1 Tim. 6:19) Achibale awo angamawatsutse kapena angamakumane ndi mavuto azachuma chifukwa chokhala kumbali ya Ufumu wa Mulungu, koma Yehova amaonetsetsa kuti iwo ali ndi zonse zimene akufunikira. (Mat. 6:​25, 30-33; Luka 18:​29, 30) Mfundo zimenezi zimatitsimikizira kuti Ufumu wa Mulungu ndi weniweni komanso kuti udzapitiriza kukwaniritsa cholinga cha Yehova. w22.12 5 ¶13

Lachinayi, April 4

Ame! Bwerani, Ambuye Yesu. —Chiv. 22:20.

Zaka 1000 zikamadzatha, anthu onse padzikoli adzakhala ali angwiro. Palibe munthu yemwe adzakhale ndi uchimo womwe tinatengera kwa Adamu. (Aroma 5:12) Temberero la uchimo wa Adamu lidzakhala litachotsedweratu. Zimenezi zikutanthauza kuti anthu onse padzikoli ‘adzakhalanso ndi moyo’ monga angwiro kumapeto kwa zaka 1,000. (Chiv. 20:5) Timadziwa kuti Yesu anakhalabe wangwiro pamene Satana ankamuyesa. Koma kodi anthu onse omwe adzakhale angwiro pa nthawiyo adzakhalabe okhulupirika Satana akadzapatsidwa mwayi wowayesa? Aliyense adzayankha yekha funso limeneli Satana akadzamasulidwa kuphompho pambuyo pa zaka 1000. (Chiv. 20:7) Anthu omwe adzakhale okhulupirika pa mayesero omalizawa adzalandira moyo wosatha komanso adzasangalala ndi ufulu weniweni. (Aroma 8:21) Anthu otsutsa adzawonongedwa mpaka kalekale.—Chiv. 20:​8-10. w22.05 19 ¶18-19

Lachisanu, April 5

Udzaivulaza chidendene. —Gen. 3:15.

Ulosiwu unakwaniritsidwa pamene Satana anachititsa Ayuda ndi Aroma kuti aphe Mwana wa Mulungu. (Luka 23:​13, 20-24) Mofanana ndi bala la chidendene lomwe lingachititse munthu kulephera kuyenda kwa kanthawi, imfa ya Yesu inachititsa kuti iye asiye kuchita zinthu kwa kanthawi pomwe anagona m’manda kwa masiku atatu. (Mat. 16:21) Kuti ulosi wa pa Genesis 3:15 ukwaniritsidwe, Yesu sankafunika kukhalabe m’manda mpaka kalekale. Chifukwa chiyani? Chifukwa malinga ndi ulosi, mbewu ya mkazi inkafunika kudzaphwanya mutu wa njoka. Zimenezi zinkatanthauza kuti Yesu ankafunika kuukitsidwa zomwe zinali ngati kuchira bala la chidendene. Ndipotu iye anaukitsidwadi. Pa tsiku lachitatu Yesu anaukitsidwa ndi moyo womwe sungafe. Pa nthawi ya Mulungu, Yesu adzawononga Satana n’kumuchotseratu. (Aheb. 2:14) Anthu omwe adzalamulire ndi Khristu adzathandiza nawo kuchotsa adani a Mulungu onse padzikoli, omwe ndi mbewu ya njoka.—Chiv. 17:14; 20:​4, 10. w22.07 16 ¶11-12

Loweruka, April 6

Munthu woyenda ndi anthu anzeru adzakhala wanzeru.—Miy. 13:20.

Makolo, muzithandiza ana anu kupeza anzawo abwino. Mawu a Mulungu amafotokoza momveka bwino kuti anzathu angatithandize kukhala ndi makhalidwe abwino kapena oipa. Kodi mumadziwa anzawo a ana anu? Kodi mungatani kuti muwathandize kuti azigwirizana ndi anthu omwe amakonda Yehova? (1 Akor. 15:33) Mungawathandize kusankha anzawo abwino poitanira kunyumba kwanu anthu omwe ndi olimba mwauzimu kuti mudzachitire limodzi zinthu zina. (Sal. 119:63) Bambo wina dzina lake Tony anati: “Kwa zaka zambiri, ine ndi mkazi wanga takhala tikuitanira kunyumba kwathu abale ndi alongo a misinkhu yosiyanasiyana. Timawaitanira chakudya komanso kuti adzapange nafe kulambira kwa pabanja. Imeneyi ndi njira yabwino yodziwira anthu omwe amakonda komanso kutumikira Yehova mosangalala. . . . Zinthu zomwe zakhala zikuwachitikira, khama lawo komanso kudzipereka kwawo zathandiza kwambiri ana athu kuti akhale pa ubwenzi wolimba ndi Yehova.” w22.05 29-30 ¶14-15

Lamlungu, April 7

Zilizonse zimene mudzamange padziko lapansi zidzakhala zoti zamangidwa kale kumwamba.—Mat. 18:18.

Akulu akakumana ndi munthu yemwe wachita tchimo amafuna asankhe zinthu mogwirizana ndi zomwe zasankhidwa kale kumwamba. Kodi kuchita zimenezi kumathandiza bwanji mpingo? Mpingo umakhala wotetezeka chifukwa anthu osalapa omwe angasokoneze nkhosa za Yehova za mtengo wapatali amachotsedwa. (1 Akor. 5:​6, 7, 11-13; Tito 3:​10, 11) Zingathandizenso wochimwa kuti alape ndiponso kuti Yehova amukhululukire. (Luka 5:32) Akulu amapempherera munthu yemwe walapa ndipo amapempha Yehova kuti amuthandize kuchira mwauzimu. (Yak. 5:15) Tiyerekeze kuti munthu sakusonyeza kulapa pamene wakumana ndi akulu, zikatero amachotsedwa mumpingo. Komabe ngati munthuyo nzeru zamubwerera, ndipo walapa kuchokera pansi pa mtima, Yehova amakhala wofunitsitsa kumukhululukira. (Luka 15:​17-24) Amamukhululukirabe ngakhale kuti anachita machimo akuluakulu kwambiri.—2 Mbiri 33:​9, 12, 13; 1 Tim. 1:15. w22.06 9 ¶5-6

Lolemba, April 8

Khalanibe oganiza bwino ndipo khalani tcheru chifukwa mdani wanu Mdyerekezi akuyendayenda ngati mkango wobangula, kuti ameze winawake.—1 Pet. 5:8.

Mothandizidwa ndi Yehova, Akhristu padziko lonse akwanitsa kulimbana ndi mavuto osiyanasiyana komanso kutsutsa Mdyerekezi. (1 Pet. 5:9) Inunso mungakwanitse. Posachedwapa Yehova adzauza Yesu ndi olamulira anzake kuti “awononge ntchito za Mdyerekezi.” (1 Yoh. 3:8) Zimenezi zikadzachitika, anthu amene azidzatumikira Mulungu padzikoli ‘sadzaopa kanthu ndipo palibe chimene chidzawachititse mantha.’ (Yes. 54:14; Mika 4:4) Komabe pamene tikuyembekezera zimenezi tiyenera kumayesetsa kuthetsa mantha omwe tingakhale nawo. Tiyenera kupitiriza kukhulupirira kwambiri kuti Yehova amakonda komanso kuteteza atumiki ake. Kuganizira ndiponso kukambirana mmene Yehova anatetezera atumiki ake mbuyomu kungatithandize kuchita zimenezi. Komanso tiziganizira mmene iye wakhala akutithandizira ifeyo patokha pa nthawi ya mavuto. Mothandizidwa ndi Yehova, tikhoza kusiya kuchita mantha.—Sal. 34:4. w22.06 19 ¶19-20

Lachiwiri, April 9

Mwalawo unamenya chifanizirocho kumapazi ake achitsulo chosakanikirana ndi dongo.—Dan. 2:34.

Ufumu wamphamvu padziko lonse womaliza womwe umene umaimiridwa ndi mapazi “achitsulo chosakanizika ndi dongo” ukulamulira panopa. Ufumuwu unakhazikitsidwa pa nthawi ya nkhondo yoyamba ya padziko lonse pomwe mayiko a Britain ndi America anachita mgwirizano wapadera. Maloto a Nebukadinezara anatchulanso zinthu zokhudza ufumuwo zomwe zimauchititsa kukhala wosiyana ndi maufumu ena a m’mbuyo mwake. Mosiyana ndi maulamuliro ena amphamvu padziko lonse otchulidwa m’masomphenyawa, ulamuliro wa Britain ndi America sukuimiridwa ndi zinthu zolimba ngati golide kapena siliva, koma chitsulo chosakanizika ndi dongo. Dongolo likuimira “ana a anthu” kapena kuti anthu wamba. (Dan. 2:​43, mawu a m’munsi.) Monga mmene timaonera masiku ano, zochita za anthu pa nkhani ya zisankho, ziwonetsero, kumenyera maufulu komanso kukhazikitsa mabungwe zimachititsa kuti ulamuliro womalizawu uzivutika kukwaniritsa zolinga zake. w22.07 4-5 ¶9-10

Lachitatu, April 10

Chakudya changa ndi kuchita zofuna za amene anandituma.—Yoh. 4:34.

Kodi mukuzengereza kubatizidwa? Mungachite bwino kudzifunsa kuti, ‘Kodi ndikudikira chiyani?’ (Mac. 8:36) Palemba laleroli Yesu anayerekezera kuchita chifuniro cha Atate wake ndi chakudya. Chifukwa chiyani? Chifukwa chakuti chakudya n’chabwino kwa tonsefe. Yesu amadziwa kuti zilizonse zimene Yehova amatiuza kuti tichite zimakhala zabwino kwa ifeyo. Yehova safuna kuti tichite chilichonse chomwe chingativulaze. Kodi zimene Yehova amafuna kuti inuyo muchite zimaphatikizapo kubatizidwa? Inde. (Mac. 2:38) Choncho mungakhale otsimikiza kuti kumvera lamulo lakuti mubatizidwe n’kothandiza kwa inuyo. Ngati simungazengereze kudya chakudya chabwino kwambiri, kodi pali chifukwa chilichonse chomwe chingakuchititseni kuti muzengereze kubatizidwa? Kodi mukudikira chiyani? Ambiri angayankhe kuti, “Panopa sindinakonzeke.” Mfundo ndi yakuti kusankha kuti mudzipereke kwa Yehova komanso kubatizidwa, ndi nkhani yofunika kwambiri pa moyo wanu. Choncho pamafunika nthawi, kuganizira mosamala komanso khama kuti mukhale okonzeka. w23.03 7 ¶18-20

Lachinayi, April 11

Akunena kuti, “kwa mbadwa yako,” kutanthauza kuti ndi imodzi, amene ndi Khristu.—Agal. 3:16.

Atadzozedwa, Yesu anakhala mbali yoyamba ya mbewu ya mkazi. Yesu ataphedwa n’kuukitsidwa, Mulungu anamuveka “ulemerero ndi ulemu ngati chisoti chachifumu” ndipo anamupatsa “ulamuliro wonse . . . kumwamba ndi padziko lapansi,” kuphatikizapo mphamvu zoti “awononge ntchito za Mdyerekezi.” (Aheb. 2:7; Mat. 28:18; 1 Yoh. 3:8) Palinso mbali yachiwiri ya mbewu ya mkazi. Mtumwi Paulo ananena za mbali ya mbewuyi pomwe anauza Akhristu odzozedwa a Chiyuda komanso mitundu ina kuti: “Ngati muli ophunzira a Khristu, ndinudi mbadwa za Abulahamu, olandira cholowa mogwirizana ndi lonjezolo .” (Agal. 3:​28, 29) Yehova akadzoza Mkhristu ndi mzimu wake woyera, munthuyo amakhala mbali ya mbewu ya mkazi. Choncho mbewu ya mkazi ndi Yesu Khristu ndi olamulira anzake okwana 144,000. (Chiv. 14:1) Onsewa amayesetsa kuti aziganiza ndi kuchita zinthu ngati Atate wawo Yehova Mulungu. w22.07 16 ¶8-9

Lachisanu, April 12

Moyo wanga ndikunyansidwa nawo, sindikufuna kupitirizanso kukhala ndi moyo.—Yobu 7:16.

Masiku otsiriza ano timayembekezera kukumana ndi mayesero. (2 Tim. 3:1) Komabe mayesero ena omwe sitimawaganizira angatipeze pa nthawi imene sitimayembekezera. Mwadzidzidzi tingakumane ndi mavuto azachuma, matenda aakulu komanso munthu amene timamukonda angamwalire. Pa nthawi ngati zimenezi tingakhumudwe kapena kufooka makamaka ngati mayeserowo abwera motsatizana kapena pa nthawi imodzi. Komabe tizikumbukira kuti Yehova amatiyang’anira ndipo angatithandize kupirira mayesero aliwonse amene tingakumane nawo. Taganizirani mmene Yehova anathandizira Yobu, yemwe anali munthu wokhulupirika. Iye anakumana ndi mayesero ambiri m’kanthawi kochepa. M’tsiku limodzi lokha, iye anamva zinthu zoopsa zokhudza kubedwa ndi kuphedwa kwa ziweto zake, kuphedwa kwa antchito ake ndipo chopweteka kwambiri chinali choti ana akenso okondedwa anaphedwa. (Yobu 1:​13-19) Patangopita nthawi yochepa adakali ndi chisoni chachikulu chonchi, Yobu anadwala matenda opweteka kwambiri. (Yobu 2:7) Yehova ankayang’anira Yobu. Chifukwa choti ankamukonda, iye anamupatsa zomwe ankafunikira kuti athe kupirira mayesero komanso kukhalabe wokhulupirika. w22.08 11 ¶8-10

Loweruka, April 13

Yehova amalanga aliyense amene iye amamukonda.—Aheb. 12:6.

Kupatsidwa malangizo kungakhale kowawa. Tingamaone kuti sitimayenera kupatsidwa kapenanso aperekedwa mopanda chifundo. Zotsatira zake zingakhale zakuti sitingamaone malangizowo ngati njira imene Yehova akutisonyezera chikondi. (Aheb. 12:​5, 11) Choncho muzivomereza malangizo ndipo muzisintha. Maulendo angapo, Yesu anadzudzula Petulo pamaso pa atumwi ena. (Maliko 8:33; Luka 22:​31-34) N’kutheka kuti Petulo ankachita manyazi. Komabe iye anakhalabe wokhulupirika kwa Yesu. Ankavomera malangizo ndipo ankaphunzirapo kanthu. M’kupita kwa nthawi, Yehova anadalitsa Petulo chifukwa chokhalabe wokhulupirika ndipo anamupatsa maudindo akuluakulu mumpingo. (Yoh. 21:​15-17; Mac. 10:​24-33; 1 Pet. 1:1) Tikamapewa kuganizira kwambiri kuti tachititsidwa manyazi n’kuvomera malangizo komanso kusintha, zinthu zimatiyendera bwino ifeyo komanso anthu ena. Tikatero timakhala ofunika kwambiri kwa Yehova komanso abale athu. w22.11 21-22 ¶6-7

Lamlungu, April 14

Kumeneko ukamupereke [Isaki] nsembe yopsereza.—Gen. 22:2.

Abulahamu ankadziwa kuti Yehova sangachite chilichonse mopanda chilungamo kapena mopanda chikondi. Mogwirizana ndi zimene mtumwi Paulo ananena, Abulahamu ankakhulupirira kuti Yehova aukitsa mwana wake Isaki. (Aheb. 11:​17-19) Ndipotu Yehova anali atalonjeza kuti Isaki adzakhala tate wa mtundu waukulu, koma pa nthawiyi iye analibe ana. Abulahamu ankakonda Yehova choncho ankakhulupirira kuti Atate ake nthawi zonse amachita zinthu mwachilungamo. Mwachikhulupiriro, iye anamvera ngakhale kuti zinali zovuta. (Gen. 22:​1-12) Kodi tingatsanzire bwanji Abulahamu? Mofanana ndi iye, tiyenera kupitiriza kuphunzira za Yehova. Tikamachita zimenezi tidzakhala naye pa ubwenzi ndipo tidzayamba kumukonda kwambiri. (Sal. 73:28) Tidzaphunzitsa chikumbumtima chathu kuti chizitithandiza kuganiza ngati mmene Mulungu amaganizira. (Aheb. 5:14) Zotsatira zake n’zakuti tidzakana munthu wina akatiyesa kuti tichite zoipa. Sitidzalola kuchita chilichonse chimene chingakhumudwitse Atate wathu kapena kuwononga ubwenzi wathu ndi iye. w22.08 28-29 ¶11-12

Lolemba, April 15

Nkhawa mumtima mwa munthu ndi imene imauweramitsa, koma mawu abwino ndi amene amausangalatsa.—Miy. 12:25.

Pa ulendo wawo wobwerera ku Lusitara, Ikoniyo ndi Antiokeya, mtumwi Paulo ndi Baranaba ‘anasankhanso akulu mumpingo uliwonse.’ (Mac. 14:​21-23) Mosakayikira amuna amene anasankhidwawo ankalimbikitsa mipingoyo monga mmenenso akulu masiku ano amachitira. Akulu, muzikhala tcheru kuti muthandize anthu omwe angafunike “mawu abwino” olimbikitsa. Paulo anakumbutsa Akhristu anzake kuti pali ‘gulu lalikulu la mboni,’ la amuna ndi akazi omwe anapirira mavuto chifukwa chothandizidwa ndi Yehova. (Aheb. 12:1) Paulo ankadziwa kuti nkhani za anthu akale omwe anakwanitsa kupirira mavuto osiyanasiyana, zikanathandiza abale ndi alongowo kukhala olimba mtima komanso kupitirizabe kuganizira za “mzinda wa Mulungu wamoyo.” (Aheb. 12:22) N’chimodzimodzinso masiku ano. Ndani salimbikitsidwa akamawerenga nkhani zokhudza mmene Yehova anathandizira Gidiyoni, Baraki, Davide, Samueli ndi enanso ambiri?—Aheb. 11:​32-35. w22.08 21-22 ¶5-6

Lachiwiri, April 16

Aliyense payekha anaweruzidwa mogwirizana ndi ntchito zake. —Chiv. 20:13.

Kodi oukitsidwawa adzaweruzidwa potengera “ntchito” ziti? Kodi zidzakhala ntchito zimene ankachita asanamwalire? Ayi. Kumbukirani kuti machimo omwe anachita poyamba anakhululukidwa pamene anamwalira. Choncho “ntchito zawo” zotchulidwa panozi, sizingakhale zomwe anachita asanamwalire. M’malomwake, ayenera akunena za ntchito zomwe adzachite pambuyo pophunzitsidwa m’dziko latsopano. Ngakhalenso anthu okhulupirika monga Nowa, Samueli, Davide ndi Danieli, adzafunika kuphunzitsidwa zokhudza Yesu Khristu komanso kukhulupirira nsembe yake. Ndiye kuli bwanji anthu osalungama? Kodi n’chiyani chomwe pamapeto pake chidzachitikire anthu omwe adzakane mwayi wamtengo wapataliwu? Lemba la Chivumbulutso 20:15 limatiuza kuti: “Aliyense amene dzina lake silinalembedwe m’buku la moyo anaponyedwa m’nyanja yamoto.” Anthu amenewa adzawonongedwa ndipo sadzakhalaponso. Choncho n’zofunika kwambiri kuti tiziyesetsa kuti dzina lathu lilembedwe m’buku la moyo ndipo lisadzafufutidwemo. w22.09 19 ¶17-19

Lachitatu, April 17

[Tikhale] ndi chikumbumtima chabwino kwa Mulungu ndiponso kwa anthu. —Mac. 24:16.

Nthawi zambiri zimene timasankha pa nkhani yokhudza thanzi lathu kapena thandizo lachipatala, zimakhala zogwirizana ndi chikumbumtima chathu chophunzitsidwa bwino Baibulo. (1 Tim. 3:9) Tikamasankha kapena kukambirana ndi ena nkhani zimenezi, tingachite bwino kumatsatira mfundo ya pa Afilipi 4:​5, yomwe imati: “Anthu onse adziwe kuti ndinu ololera.” Tikakhala ololera sitimadera nkhawa kwambiri zokhudza thanzi lathu. Timakonda komanso kulemekeza abale ndi alongo athu ngakhale zosankha zawo zitakhala zosiyana ndi zathu. (Aroma 14:​10-12) Tingasonyeze kuti timayamikira Yehova yemwe ndi Mwiniwake wa moyo, pouteteza komanso kumamutumikira ndi mtima wonse. (Chiv. 4:11) Panopa timalimbanabe ndi zinthu ngati matenda komanso mavuto ena. Koma Mlengi wathu sankafuna kuti tizikhala moyo woterowu. Posachedwapa atipatsa moyo wosatha wopanda imfa komanso zowawa. (Chiv. 21:4) Koma panopa timaona kuti ndi mwayi wamtengo wapatali kukhala ndi moyo komanso kumatumikira Atate wathu wachikondi Yehova. w23.02 25 ¶17-18

Lachinayi, April 18

Ufumu wanu wagawidwa ndipo waperekedwa kwa Amedi ndi Aperisiya. —Dan. 5:28.

Yehova wakhala akusonyeza kuti iye ndi wamkulu kwambiri kuposa “olamulira akuluakulu.” (Aroma 13:1) Taganizirani zitsanzo zitatu izi. Farao wa ku Iguputo ankagwiritsa ntchito yaukapolo anthu a Yehova ndipo mobwerezabwereza anakana kuwamasula. Koma Mulungu anawamasula ndipo anamiza Farao m’Nyanja Yofiira. (Eks. 14:​26-28; Sal. 136:15) Mfumu Belisazara wa ku Babulo anakonza phwando ndipo ‘anadzikweza pamaso pa Ambuye wakumwamba’ komanso ‘anatamanda milungu wamba yasiliva ndi yagolide’ m’malo motamanda Yehova. (Dan. 5:​22, 23) Koma Mulungu anatsitsa munthu wodzikwezayu. Iye anaphedwa “usiku womwewo” ndipo ufumu wake unaperekedwa kwa Amedi ndi Aperisiya. (Dan. 5:​30, 31) Mfumu Herode Agiripa I wa ku Palesitina anapha mtumwi Yakobo ndipo kenako anaika m’ndende mtumwi Petulo n’cholinga choti amuphenso. Koma Yehova anamulepheretsa kukwaniritsa zolinga zakezi. “Mngelo wa Yehova anamudwalitsa,” ndipo anafa.—Mac. 12:​1-5, 21-23. w22.10 15 ¶12

Lachisanu, April 19

Ine ndidzakumvetserani.—Yer. 29:12.

Tingamvetsere Mulungu tikamawerenga Mawu ake komanso kuwaganizira mozama. Tikamawerenga za mmene Yehova anasamalirira anthu omwe anakhalabe okhulupirika kwa iye m’mbuyomu, chiyembekezo chathu chimalimba kwambiri. Zonse zimene timawerenga m’Mawu a Mulungu, “zinalembedwa kuti zitilangize. Malembawa amatithandiza kupirira ndiponso amatilimbikitsa n’cholinga choti tikhale ndi chiyembekezo.” (Aroma 15:4) Muziganizira mmene Yehova wakhala akukwaniritsira malonjezo ake. Taganizirani zimene Yehova anachitira Abulahamu ndi Sara. Iwo anali atafika pamsinkhu woti sangakhale ndi ana. Komabe Mulungu anawalonjeza kuti adzakhala ndi mwana. (Gen. 18:10) Kodi Abulahamu anatani chifukwa cha zimenezi? Baibulo limati: “Anali ndi chiyembekezo ndiponso chikhulupiriro chakuti adzakhala bambo wa mitundu yambiri.” (Aroma 4:18) Ngakhale kuti kwa munthu zikanaoneka ngati zosatheka, Abulahamu anakhulupirira kuti Yehova akwaniritsa lonjezo lake. Munthu wokhulupirikayu sanagwiritsidwe fuwa lamoto. (Aroma 4:​19-21) Nkhani ngati zimenezi zimatiphunzitsa kuti tingamadalire kuti Mulungu akwaniritsa malonjezo ake. w22.10 27 ¶13-14

Loweruka, April 20

Maso anu adzaona Mlangizi wanu wamkulu.—Yes. 30:20.

Mawu amenewa anakwaniritsidwa pamene Ayuda anamasulidwa ku ukapolo. Yehova anasonyeza kuti analidi Mlangizi wawo Wamkulu, ndipo malangizo omwe ankawapatsa anathandiza kuti akwanitse kubwezeretsa kulambira koona. Ifenso masiku ano tili ndi mwayi kuti Yehova ndi Mlangizi wathu Wamkulu. Yesaya akutifotokoza monga ophunzira omwe akuphunzitsidwa ndi Yehova ponena kuti: “Maso anu adzaona Mlangizi wanu wamkulu.” Mufanizoli, Mlangizi waima kutsogolo kwa ophunzira ake. Masiku ano tili ndi mwayi waukulu kuti timalandira malangizo ake. Kodi Yehova amatiphunzitsa bwanji? Kudzera m’gulu lake. Timayamikira kwambiri chifukwa cha malangizo omveka bwino omwe amatipatsa kudzera m’gulu lakeli. Malangizo omwe timapatsidwa pamisonkhano komanso m’mabuku athu, pulogalamu ya JW Broadcasting ndi njira zina, amatithandiza kupirira mosangalala tikakumana ndi mavuto. w22.11 10 ¶8-9

Lamlungu, April 21

[Kodi] chizindikiro cha . . . mapeto a nthawi ino chidzakhala chiyani? —Mat. 24:3.

Ponena za kuwonongedwa kwa Yerusalemu ndi kachisi wake komanso zokhudza “mapeto a nthawi ino,” omwe ifeyo tikukhalamo,Yesu anati: “Kunena za tsikulo kapena ola lake, palibe amene akudziwa, ngakhale angelo kumwamba kapenanso Mwana, kupatulapo Atate wokha.” Kenako anachenjeza ophunzira ake onse kuti ‘akhale tcheru’ ndiponso ‘akhale maso.’ (Maliko 13:​32-37) Akhristu a Chiyuda m’nthawi ya atumwi ankafunika kukhala maso kuti apulumuke. Yesu anauza otsatira ake kuti: “Mukadzaona magulu ankhondo atazungulira Yerusalemu, mudzadziwe kuti mzindawu watsala pang’ono kuwonongedwa.” Pa nthawiyo iwo ankafunika kumvera chenjezo la Yesu loti “adzayambe kuthawira kumapiri.” (Luka 21:​20, 21) Amene anamvera chenjezoli anapulumuka pamene Aroma anawononga Yerusalemu. Panopa tikukhala m’nthawi ya mapeto a dziko loipali. Choncho nafenso tiyenera kukhalabe oganiza bwino komanso kukhala maso. w23.02 14 ¶1-2; 16 ¶3

Lolemba, April 22

Yehova, Mulungu wa choonadi. —Sal. 31:5.

Yehova amaphunzitsa atumiki ake kuti azikhala oona mtima komanso achilungamo. Zimenezi zimathandiza kuti ena aziwalemekeza ndiponso azikhala ndi mtendere wamumtima. (Miy. 13:​5, 6) Kodi inuyo mwaona akukuchitirani zimenezi pamene mumaphunzira Baibulo? Mwaphunzira kuti njira za Yehova ndi zabwino kwambiri kwa anthu onse kuphatikizaponso inuyo. (Sal. 77:13) Choncho mumafuna kuchita zimene Mulungu amaona kuti n’zachilungamo. (Mat. 6:33) Mumafuna kukhala kumbali ya choonadi komanso kutsimikizira kuti zimene Satana ananena zokhudza Mulungu wathu Yehova ndi zabodza. Kodi mungachite bwanji zimenezi? Zimene mumasankha pa moyo wanu zingakhale ngati mukunena kuti: “Ndimakana mabodza a Satana ndipo ndimakonda choonadi. Ndikufuna kuti Yehova akhale Wolamulira wanga ndipo ndikufuna kuti ndizichita zimene iye amanena kuti n’zoyenera.” Kodi mungachite bwanji zimenezi? Mungatero podzipereka kwa Yehova m’pemphero kenako n’kusonyeza poyera kudzipereka kwanuko pobatizidwa. Kukonda choonadi ndi chilungamo ndi chifukwa chachikulu chimene chingakuchititseni kuti musankhe kubatizidwa. w23.03 3 ¶4-5

Lachiwiri, April 23

Mitima yanu isavutike kapena kuchita mantha.—Yoh. 14:27.

Pali mtendere wina umene anthu ambiri m’dzikoli saudziwa. Umenewu ndi “mtendere wa Mulungu,” kapena kuti kukhazikika maganizo kumene timakhala nako chifukwa chokhala pa ubwenzi wabwino kwambiri ndi Atate wathu wakumwamba. Tikakhala ndi mtendere wa Mulungu timadzimva kukhala otetezeka. (Afil. 4:​6, 7) Timakhala pa ubwenzi wabwino ndi “Mulungu wamtendere” komanso anthu omwe amamukonda. (1 Ates. 5:23) Tikamadziwa, kukhulupirira komanso kumvera Atate wathu, mtendere wa Mulungu ungachititse kuti mitima yathu ikhale m’malo tikakumana ndi mavuto. Kodi n’zothekadi kukhala ndi mtendere wa Mulungu pa nthawi yamavuto monga ngozi zam’chilengedwe, nkhondo, kuzunzidwa kapenanso kukagwa mliri? Chilichonse mwa zinthu zimenezi chingatichititse mantha. N’zosangalatsa kuti abale ndi alongo akutsatira malangizo a Yesu a mulemba lalero. Mothandizidwa ndi Yehova, iwo akwanitsa kupeza mtendere ngakhale pamene akumana ndi mayesero aakulu. w22.12 16 ¶1-2

Lachitatu, April 24

Yakani ndi mzimu. Tumikirani Yehova monga akapolo.—Aroma 12:11.

Sitingathe kulamulira chilichonse chimene chimachitika pa moyo wathu. Choncho tisamaone kuti ndife ofunika kwa Yehova chifukwa cha utumiki umene tikuchita kapenanso kumayerekezera utumiki wathu ndi wa ena. (Agal. 6:4) Choncho n’zofunika kuti tizifufuza njira zimene tingathandizire ena komanso kutumikira Yehova. Mungathe kuchita zambiri potumikira Yehova ngati mumakhala moyo wosalira zambiri komanso ngati mumapewa ngongole. Mungadziikire zolinga zing’onozing’ono zomwe zingakuthandizeni kudzakwaniritsa zolinga zikuluzikulu m’tsogolo. Mwachitsanzo, ngati cholinga chanu chachikulu ndi kudzachita upainiya wokhazikika, bwanji osayamba panopa kuchita upainiya wothandiza mwezi uliwonse? Ngati cholinga chanu ndi kukhala mtumiki wothandiza, kodi mukhoza kuwonjezera nthawi imene mumalalikira? Zimene mungaphunzire panopa zingathandize kuti mudzachite mautumiki osiyanasiyana m’tsogolo. Muziyesetsa kuchita zonse zomwe mungathe pa utumiki uliwonse womwe mwapatsidwa. w22.04 26 ¶16-17

Lachinayi, April 25

Ndimakonda Yehova chifukwa amamva mawu anga komanso kuchonderera kwanga kopempha thandizo.—Sal. 116:1.

Yehova angatithandize kupirira mavuto athu ndiponso kuti tizisangalala pamene tikumutumikira. Tikapemphera kwa Mulungu pa nkhani yomwe ikutidetsa nkhawa, chinthu choyamba chomwe Yehova angatichitire ndi kutipatsa mphamvu kuti tipirire. Ndipo ngati mayeserowo sakutha msanga monga mmene timayembekezera, tingafunike kupitiriza kumupempha kuti atipatse mphamvu zoti tipirire. Iye amatilimbikitsa kuti tizichita zimenezi. Izi zikugwirizana ndi mawu a Yesaya akuti: “Pitirizani kupemphera kwa [Yehova].” (Yes. 62:7) Kodi zimenezi zimatanthauza chiyani? Tiyenera kupemphera kwa Yehova mobwerezabwereza komwe kungakhale ngati kumukumbutsa. Mawu a Yesayawa akutikumbutsa fanizo la Yesu lokhudza kupemphera lomwe limapezeka pa Luka 11:​8-10, 13. Palembali Yesu anatilimbikitsa kuti “tizipemphabe” mzimu woyera. Tingamupemphenso Yehova kuti atitsogolere kuti tisankhe bwino zinthu. w22.11 8 ¶1; 9 ¶6-7

Lachisanu, April 26

Tiyenera kukumana ndi mavuto ambiri kuti tikalowe mu Ufumu wa Mulungu.—Mac. 14:22.

Inuyo ndi banja lanu mungakonzekereretu panopa zimene mungachite pa nthawi imene mukuzunzidwa. Musamayese kuganizira zinthu zonse zoipa zomwe zingachitike. M’malomwake, muzilimbitsa ubwenzi wanu ndi Yehova ndipo muzithandizanso ana anu kuchita zomwezo. Ngati nthawi zina mumayamba kukhala ndi nkhawa, muzimuuza Mulungu za mumtima mwanu. (Sal. 62:​7, 8) Monga banja, muzikambirana zifukwa zomwe zingakuchititseni kuti muzimukhulupirira. Monga mmene mumakonzekerera ngozi zosiyanasiyana, kukonzekera zimene mungachite mukamazunzidwa komanso kukhulupirira Yehova, kungathandize ana anu kukhala ndi mtendere komanso olimba mtima. Mtendere wa Mulungu umatithandiza kudzimva kuti ndife otetezeka. (Afil. 4:​6, 7) Ngakhale kuti masiku ano tingakumane ndi mavuto monga matenda, ngozi zam’chilengedwe kapena kuzunzidwa, mtenderewu umathandiza kuti mitima yathu ikhale m’malo. Mulungu amagwiritsa ntchito akulu akhama kuti azitilimbikitsa. Watipatsanso mwayi tonsefe woti tizithandizana. Panopa pamene tili pa mtendere, ndi nthawi yabwino yomwe tingakonzekere mavuto aakulu omwe tingakumane nawo m’tsogolo, ngakhalenso “chisautso chachikulu.”—Mat. 24:21. w22.12 27 ¶17-18

Loweruka, April 27

Sindinabwere kudzaitana anthu olungama, koma ochimwa. —Mat. 9:13.

Sitikuyenera kumangodziimba mlandu chifukwa cha machimo akuluakulu omwe tinachita m’mbuyomo. N’zoona kuti sitiyenera kumaona nsembe ya dipo ngati chifukwa ‘chomachitira machimo mwadala.’ (Aheb. 10:​26-31) Koma tingakhale otsimikiza kuti ngati talapa mochokera pansi pamtima ndipo talandira thandizo lochokera kwa Yehova komanso tasintha khalidwe lathu, iye angatikhululukire ndi mtima wonse. (Yes. 55:7; Mac. 3:19) Nsembe ya dipo ndi yamphamvu kwambiri moti ingaphimbe machimo athu onse komanso ingachititse kuti zikhale zotheka kudzakhala ndi moyo m’Paradaiso. Pa nthawiyo moyo sudzakhala wotopetsa. Nthawi zonse tizidzakumana ndi anthu abwino komanso kugwira ntchito yosangalatsa. Koposa zonse, tsiku lililonse tizidzadziwa bwino Atate wathu wakumwamba komanso kusangalala ndi zinthu zimene watipatsa. Sitidzamaliza kuphunzira za iye ndipo padzakhala zambiri zoti tiphunzire zokhudza chilengedwe chake. w22.12 13 ¶17, 19

Lamlungu, April 28

Ndidzaika chidani pakati pa iwe ndi mkaziyo.—Gen. 3:15.

“Mkaziyo” sangakhale Hava. Ulosiwu unanena kuti mbewu ya mkaziyo “idzaphwanya” mutu wa njoka. Njoka ndi Satana yemwe ndi cholengedwa chauzimu choncho sizikanatheka kuti mwana wa Hava yemwe si wangwiro athe kumuwononga. Ndiye kodi Satana akanawonongedwa bwanji? Buku lomaliza la m’Baibulo limatiuza za mkazi wotchulidwa pa Genesis 3:15. (Chiv. 12:​1, 2, 5, 10) Mkaziyu si wapadzikoli. Iye ali ndi mwezi kumapazi kwake ndipo kumutu kwake kuli chisoti chachifumu chokhala ndi nyenyezi 12. Mkaziyu anabereka mwana wapadera kwambiri yemwe ndi Ufumu wa Mulungu. Ufumuwu ndi wakumwamba choncho mkaziyu ayeneranso kuti ndi wakumwamba. Iye amaimira mbali yakumwamba ya gulu la Yehova lopangidwa ndi angelo okhulupirika. (Agal. 4:26) Mawu a Mulungu amatithandizanso kudziwa mbali yoyamba ya mbewu ya mkazi. Mbewuyi inkayenera kukhala yochokera mu mzera wa Abulahamu.—Gen. 22:​15-18 w22.07 15-16 ¶6-8

Lolemba, April 29

Simunawalandire monga mawu a anthu, koma mmene alilidi, monga mawu a Mulungu. —1 Ates. 2:13.

Mphatso ya Yehova, Baibulo, imene anatipatsa ndi yodzaza ndi malangizo anzeru ndipo amathandiza kwambiri anthu. Baibulo limasintha anthu. Mabuku oyambirira a Baibulo atalembedwa, Mose anauza Aisiraeli kuti: “Amenewa si mawu opanda pake kwa inu, koma angakuthandizeni kukhala ndi moyo.” (Deut. 32:47) Anthu omwe ankatsatira malangizo a m’Malemba ankakhala moyo wabwino komanso wosangalala. (Sal. 1:​2, 3) Ngakhale kuti Mawu a Mulungu analembedwa kalekale, adakali ndi mphamvu yosintha moyo wa anthu. Malangizo anzeru a m’Baibulo amakhala othandiza nthawi zonse ndipo amathandiza anthu a mibadwo yonse. Tikamawerenga buku lopatulikali komanso kuganizira zimene tikuphunzirazo, Mlembi wake amagwiritsa ntchito mzimu wake woyera kutithandiza kuona mmene tingagwiritsire ntchito mfundo za m’Baibulo pa moyo wathu. (Sal. 119:27; Mal. 3:16; Aheb. 4:12) Choncho Mlembi wa Baibulo yemwe ndi wamoyo, ndi wofunitsitsa kutithandiza. Zimenezitu ziyenera kutilimbikitsa kuti tiziwerenga Baibulo nthawi zonse. w23.02 3 ¶5-6

Lachiwiri, April 30

Idzawononga zinthu zambiri.—Dan. 8:24.

Mu Chivumbulutso 13, timauzidwa kuti mutu wa nambala 7, womwe ndi ulamuliro wamphamvu padziko lonse wa United Kingdom ndi America, umachitanso zinthu ngati chilombo chomwe “chinali ndi nyanga ziwiri ngati mwana wa nkhosa, koma chinayamba kulankhula ngati chinjoka.” Chilombochi “chinachitanso zizindikiro zazikulu, moti chinapangitsa kuti moto ugwere padziko lapansi kuchokera kumwamba, anthu akuona.” (Chiv. 13:​11-15) Pa Chivumbulutso 16 ndi 19 amachifotokoza kuti ndi “mneneri wabodza.” (Chiv. 16:13; 19:20) Danieli anafotokoza zofanana ndi zimenezi, pomwe anasonyeza kuti ulamuliro wamphamvu padziko lonse wa United Kingdom ndi America, ‘udzaononga zinthu zambiri.’ (Dan. 8:​19, 23, 24) Zimenezi ndi zomwe zinachitikadi pa nthawi ya nkhondo yachiwiri ya padziko lonse. Mabomba awiri anyukiliya omwe anachititsa kuti nkhondoyo ithe anapangidwa ndi asayansi a ku Britain ndi America. Apa zinali ngati ulamuliro wa padziko lonse wa United Kingdom ndi America ‘wachititsa moto kugwera padziko lapansi kuchokera kumwamba.’ w22.05 10 ¶9

    Mabuku a Chichewa (1974-2026)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena