Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • es24 tsamba 47-57
  • May

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • May
  • Kuphunzira Malemba Tsiku ndi Tsiku—2024
  • Timitu
  • Lachitatu, May 1
  • Lachinayi, May 2
  • Lachisanu, May 3
  • Loweruka, May 4
  • Lamlungu, May 5
  • Lolemba, May 6
  • Lachiwiri, May 7
  • Lachitatu, May 8
  • Lachinayi, May 9
  • Lachisanu, May 10
  • Loweruka, May 11
  • Lamlungu, May 12
  • Lolemba, May 13
  • Lachiwiri, May 14
  • Lachitatu, May 15
  • Lachinayi, May 16
  • Lachisanu, May 17
  • Loweruka, May 18
  • Lamlungu, May 19
  • Lolemba, May 20
  • Lachiwiri, May 21
  • Lachitatu, May 22
  • Lachinayi, May 23
  • Lachisanu, May 24
  • Loweruka, May 25
  • Lamlungu, May 26
  • Lolemba, May 27
  • Lachiwiri, May 28
  • Lachitatu, May 29
  • Lachinayi, May 30
  • Lachisanu, May 31
Kuphunzira Malemba Tsiku ndi Tsiku—2024
es24 tsamba 47-57

May

Lachitatu, May 1

Zimenezi zitatha . . . ndinaona khamu lalikulu la anthu, amene palibe munthu aliyense amene anatha kuwawerenga, ochokera m’dziko lililonse, fuko lililonse, mtundu uliwonse ndi chilankhulo chilichonse.—Chiv. 7:9.

Pambuyo poona gulu lopita kumwamba, Yohane anaona “khamu lalikulu.” Mosiyana ndi a 144,000, khamu lalikulu chiwerengero chake sichikudziwika. Kodi tikuuzidwa zotani zokhudza gulu limeneli? Yohane anauzidwa kuti: “Amenewa ndi amene atuluka m’chisautso chachikulu ndipo achapa mikanjo yawo n’kuiyeretsa m’magazi a Mwanawankhosa.” (Chiv. 7:14) “Khamu lalikulu” limeneli likadzapulumuka pa chisautso chachikulu, lidzakhala padzikoli ndipo lidzasangalala ndi madalitso ochuluka. (Sal. 37:​9-11, 27-29; Miy. 2:​21, 22; Chiv. 7:​16, 17) Kaya tasankhidwa kuti tidzapite kumwamba kapena tidzakhale padzikoli, kodi timadziona kuti tili m’gulu la anthu amene zomwe zafotokozedwa pa Chivumbulutso 7 zidzawachitikire? Tizidziona choncho. Imeneyitu idzakhala nthawi yosangalatsa kwambiri kwa magulu awiri a atumiki a Mulungu amenewa. Tidzakhala ndi chimwemwe chochuluka chifukwa choti tinasankha kukhala kumbali ya ulamuliro wa Yehova. w22.05 16 ¶6-7

Lachinayi, May 2

Yehova ndi amene amapereka nzeru.—Miy. 2:6.

Ngati pa nthawi ina munkafunika kusankha zinthu pa nkhani yofunika kwambiri, n’zosakayikitsa kuti munapempha nzeru kwa Mulungu chifukwa munkadziwa kuti nzeru zake zingakuthandizeni. (Yak. 1:5) Mfumu Solomo inalemba kuti: “Nzeru ndi chinthu chofunika kwambiri.” (Miy. 4:7) Koma sikuti iye ankangonena nzeru zilizonse. M’malomwake ankanena zokhudza nzeru zochokera kwa Yehova Mulungu. Koma kodi nzeru zochokera kwa Mulungu zingatithandize kulimbana ndi mavuto omwe timakumana nawo masiku ano? Inde zingatithandize. Chinthu chimodzi chomwe chingatithandize kukhala anzeru ndi kuphunzira komanso kutsatira mfundo zimene anthu awiri anzeru kwambiri anaphunzitsa. Choyamba, taganizirani za Solomo. Baibulo limafotokoza kuti “Mulungu anapatsa Solomo nzeru, luso lozindikira komanso mtima womvetsa zinthu zambirimbiri.” (1 Maf. 4:29) Kenako taganizirani za Yesu, yemwe nzeru zake zinali zoposa za munthu aliyense yemwe anakhalako. (Mat. 12:42) Ponena za Yesu, ulosi unanena kuti: “Mzimu wa Yehova udzakhazikika pa iye, mzimu wanzeru ndi womvetsa zinthu.”—Yes. 11:2. w22.05 20 ¶1-2

Lachisanu, May 3

Ndiloleni kuti ndiuze m’badwo wotsatira za mphamvu zanu.—Sal. 71:18.

Uchikulire sungalepheretse munthu kudziikira zolinga zauzimu n’kuzikwaniritsa. Taganizirani chitsanzo cha mlongo wina wa zaka 75 dzina lake Beverley. Iye anali ndi matenda ena ake aakulu omwe ankachititsa kuti azivutika kuyenda. Koma ankafuna atagwira nawo mokwanira ntchito yoitanira anthu ku Chikumbutso. Choncho anadziikira zolinga zimene ankafuna kuzikwaniritsa. Mlongoyo atakwaniritsa zolinga zakezo anasangalala kwambiri. Khama lake linalimbikitsa ena kuti adzipereke pa ntchito yolalikira. Yehova amayamikira ntchito imene abale ndi alongo athu achikulire amagwira, ngakhale kuti sangathe kuchita zambiri malinga ndi mmene zinthu zilili pa moyo wawo. (Sal. 71:17) Muzidziikira zolinga zimene mungazikwaniritse. Muziyesetsa kukhala ndi makhalidwe amene angachititse kuti Yehova azikukondani. Muziphunzira maluso amene angachititse kuti Mulungu ndi gulu lake azikugwiritsani ntchito kwambiri. Muzifunafuna njira zimene mungathandizire abale ndi alongo anu mokwanira. Mofanana ndi Timoteyo, Yehova adzakudalitsani ndipo ‘anthu onse adzaona kuti mukupita patsogolo.’—1 Tim. 4:15. w22.04 27 ¶18-19

Loweruka, May 4

Kuyambira pamene unali wakhanda, wadziwa malemba oyera.—2 Tim. 3:15.

Bwanji ngati pambuyo poyesetsa kumuthandiza, mmodzi wa ana anu wanena kuti sakufuna kutumikira Yehova? Zikatero musamaganize kuti mwalephera udindo wanu monga kholo. Yehova anapatsa tonsefe, kuphatikizapo mwana wanuyo, ufulu wosankha kumutumikira. Muziyembekezerabe kuti tsiku lina adzabwerera. Kumbukirani fanizo la mwana wolowerera. (Luka 15:​11-19, 22-24) Mnyamata ameneyu anachita zinthu zambiri zoipa, koma pamapeto pake anabwerera. Makolo, mwapatsidwa mwayi wapadera wolera ana omwe ndi m’badwo watsopano wa olambira Yehova. (Sal. 78:​4-6) Umenewu si udindo wophweka ndipo tikukuyamikirani mochokera pansi pamtima chifukwa choyesetsa kuthandiza ana anu kuti azikonda Yehova, ndi kuwalera m’malangizo ake ndiponso kuwaphunzitsa kaganizidwe kake. Mungakhale otsimikiza kuti Atate wathu wakumwamba adzasangalala nanu.—Aef. 6:4. w22.05 30-31 ¶16-18

Lamlungu, May 5

Ziwalo zonse za thupi . . . ndi zolumikizana bwino.—Aef. 4:16.

Tonsefe tiyenera kuyesetsa kuti tizilimbikitsa mtendere ndi mgwirizano mumpingo. Taganizirani chitsanzo cha Akhristu a m’nthawi ya atumwi. Iwo anali ndi mphatso komanso mautumiki osiyanasiyana. (1 Akor. 12:​4, 7-11) Koma zimenezi sizinawachititse kuti azipikisana ndi kugawikana. M’malomwake Paulo analimbikitsa aliyense kuchita zimene zikanathandiza kuti “amange mpingo umene uli ngati thupi la Khristu.” Paulo analembera Aefeso kuti: “Chiwalo chilichonse cha thupili chikamagwira ntchito yake, thupili limakula bwino ndipo tidzapitiriza kukondana.” (Aef. 4:​1-3, 11, 12,) Anthu omwe anatsatira malangizowa ankalimbikitsa mtendere ndi mgwirizano, makhalidwe omwe timawaonanso m’mipingo yathu masiku ano. Tiyenera kukhala otsimikiza mtima kuti tisamadziyerekezere ndi ena. M’malomwake, tiziphunzira kwa Yesu n’kumayesetsa kutsanzira makhalidwe ake. Mungakhale otsimikiza kuti Yehova “si wosalungama kuti angaiwale ntchito yanu.” (Aheb. 6:10) Iye amayamikira zonse zomwe mukuyesetsa kuchita pomusangalatsa. w22.04 14 ¶15-16

Lolemba, May 6

Khristu Yesu anabwera m’dziko kudzapulumutsa ochimwa. —1 Tim. 1:15.

N’zosangalatsa kudziwa kuti sitinapatsidwe udindo wosankha kuti Mulungu akhululukire munthu kapena ayi. Komabe pali chinthu china chimene timafunika kusankha. Kodi timafunika kusankha chiyani? Nthawi zina munthu angatilakwire, mwinanso kutilakwira kwambiri, kenako n’kupepesa komanso kutipempha kuti timukhululukire. Koma nthawi zina sangachite zimenezi. Ngakhale zili choncho, tingasankhe kumukhululukira posapitiriza kumusungira chakukhosi komanso kumukwiyira. Kunena zoona kuti tichite zimenezi pangafunike nthawi komanso khama, makamaka ngati munthuyo watilakwira kwambiri. Nsanja ya Olonda ya September 15, 1994 inanena kuti: “Tikakhululukira munthu sizitanthauza kuti tikusangalala ndi tchimo lomwe anachitalo. Kwa Mkhristu, kukhululuka kumatanthauza kusiya nkhaniyo m’manja mwa Yehova n’kumakhulupirira kuti achitapo kanthu. Iye ndi Woweruza wachilungamo m’chilengedwe chonse, ndipo adzaonetsetsa kuti chilungamo chachitika pa nthawi yake.” w22.06 9 ¶6-7

Lachiwiri, May 7

Yembekezera Yehova.—Sal. 27:14.

Yehova analonjeza kuti m’masiku athu ano adzachititsa kuti anthu a mitundu, zikhalidwe komanso zilankhulo zosiyanasiyana azimulambira mogwirizana. Masiku ano gulu la anthu lapaderali limadziwika kuti “khamu lalikulu.” (Chiv. 7:​9, 10) Ngakhale kuti m’gululi muli amuna, akazi komanso ana ochokera m’mitundu, zilankhulo komanso zikhalidwe zosiyanasiyana, iwo ali m’banja la padziko lonse logwirizana. (Sal. 133:1; Yoh. 10:16) Anthu a m’khamu lalikululi amagwiranso mwakhama ntchito yolalikira. Nthawi zonse amakhala okonzeka kuuza aliyense yemwe angamvetsere za chiyembekezo chawo chodzakhala m’dziko labwino. (Mat. 28:​19, 20; Chiv. 14:​6, 7; 22:17) Ngati inunso muli m’khamu lalikululi, n’zosakayikitsa kuti chiyembekezo choti zinthu zidzakhala bwino m’tsogolomu ndi chamtengo wapatali kwa inu. Mdyerekezi safuna kuti muziyembekezera zinthu za m’tsogolo. Amafuna muzikhulupirira kuti Yehova sakuganizirani ndipo sadzakwaniritsa zimene analonjeza. Ngati Satana angapambane, sitingakhalenso olimba mtima ndipo mwinanso tingasiye kutumikira Yehova. w22.06 20-21 ¶2-3

Lachitatu, May 8

Chiyembekezo chathuchi chili ngati nangula wa miyoyo yathu ndipo n’chotsimikizika komanso chokhazikika.—Aheb. 6:19.

Chiyembekezo chathu cholimba chimatithandiza kuti tipirire tikakumana ndi mayesero aakulu chifukwa sitikayikira kuti posachedwapa zinthu zikhalanso bwino. Kumbukirani kuti Yesu anachenjeza kuti tidzazunzidwa. (Yoh. 15:20) Choncho kuganizira za mphoto yam’tsogolo yomwe talonjezedwa, kumatithandiza kuti tisasunthike pa kulambira kwathu. Taganizirani mmene chiyembekezo chinathandizira Yesu kukhalabe wokhulupirika ngakhale kuti ankayembekezera kuphedwa mwankhanza. Pa tsiku la Pentekosite mu 33 C.E., mtumwi Petulo anatchula mawu opezeka m’buku la Masalimo, omwe amafotokoza bwino mmene Yesu analili wodekha kuti: “Ine ndidzakhala ndi chiyembekezo, chifukwa simudzandisiya m’Manda, ndipo simudzalola kuti thupi la wokhulupirika wanu livunde. . . . Mudzachititsa kuti ndizisangalala kwambiri ndikakhala nanu pafupi.” (Mac. 2:​25-28; Sal. 16:​8-11) Yesu anali ndi chiyembekezo champhamvu chakuti Mulungu adzamuukitsa ndipo adzasangalala kukumananso ndi Atate wake kumwamba.—Aheb. 12:​2, 3. w22.10 25 ¶4-5

Lachinayi, May 9

Tonsefe timapunthwa nthawi zambiri.—Yak. 3:2.

Pa nthawi ina atumwi ake awiri, Yakobo ndi Yohane, anauza mayi awo kuti akapemphe Yesu kuti adzawapatse malo apamwamba mu Ufumu wa Mulungu. (Mat. 20:​20, 21) Apatu Yakobo ndi Yohane anasonyeza kunyada ndi kudzikuza. (Miy. 16:18) Yakobo ndi Yohane si atumwi okhawo omwe anasonyeza makhalidwe oipa pa nthawiyi. Taonani zimene atumwi enawonso anachita: “Ophunzira 10 ena aja atamva zimenezi, anakwiya kwambiri ndi amuna awiri apachibalewo.” (Mat. 20:24) N’kutheka kuti atumwi enawo anakangana ndi Yakobo ndi Yohane. Ndiye kodi Yesu anatani pa nkhaniyi? Iye sanawakwiyire. Sananene kuti apeza atumwi ena abwino, odzichepetsa kwambiri ndiponso omwe akanamasonyezana chikondi nthawi zonse. M’malomwake, iye ankawathandiza moleza mtima chifukwa choti iwo ankafunitsitsa kuchita zoyenera. (Mat. 20:​25-28) Iye anapitiriza kuchita nawo zinthu mwachikondi. w23.03 28-29 ¶10-13

Lachisanu, May 10

Mwana wanga, khala wanzeru ndipo usangalatse mtima wanga, kuti ndimuyankhe amene amanditonza.—Miy. 27:11.

Pofika pano, mwakwanitsa kale kuchita zambiri. Mwakhala mukuphunzira Baibulo mwakhama mwina kwa zaka zingapo. Kuphunzirako kwakuthandizani kutsimikizira kuti Baibulo ndi Mawu a Mulungu. Kuposa pamenepo, munadziwa komanso kuyamba kukonda kwambiri mwiniwake wa buku lopatulikali. Chifukwa chokonda kwambiri Yehova, munafika podzipereka kwa iye n’kubatizidwa. Zimenezitu ndi zosangalatsa kwambiri. N’zosakayikitsa kuti chikhulupiriro chanu chinkayesedwa pamene munkayesetsa kuti mubatizidwe. Komabe pamene mukukula mwauzimu, muzikumana ndi mayesero ena. Satana ayesetsa kukuchititsani kuti musiye kukonda Yehova komanso kumutumikira. (Aef. 4:14) Musalole kuti zimenezi zikuchitikireni. Ndiye kodi n’chiyani chingakuthandizeni kuti mupitirize kukhalabe okhulupirika kwa Yehova n’kumakwaniritsa lonjezo lomwe munapanga podzipereka kwa iye? Muyenera kupitirizabe kupita patsogolo n’kumachita ‘khama’ kuti mukhale Mkhristu wolimba mwauzimu.—Aheb. 6:1. w22.08 2 ¶1-2

Loweruka, May 11

Muzilemekeza bambo anu ndi mayi anu mogwirizana ndi zimene Yehova Mulungu wanu anakulamulani, kuti mukhale ndi moyo nthawi yaitali komanso kuti zinthu zikuyendereni bwino.—Deut. 5:16.

M’banja, aliyense ali ndi udindo woonetsetsa kuti akusunga chinsinsi chokhudza banja lawo. Mwachitsanzo, tiyerekeze kuti m’bale wina mkazi wake ali ndi khalidwe limene silimusangalatsa. Kodi iye angamangouza ena za khalidwelo kuti amuchititse manyazi? Ayi sangatero. Amakonda mkazi wakeyo ndipo sangachite zinthu zimene zingamukhumudwitse. (Aef. 5:33) Nawonso achinyamata amafuna kulemekezedwa. Makolo angachite bwino kumakumbukira zimenezi. Sayenera kuchititsa manyazi anawo pouza anthu ena zimene amalakwitsa. (Akol. 3:21) Nawonso ana amafunika kuchita zinthu mozindikira kuti asamangoulula kwa anthu ena nkhani zomwe zingachititse manyazi anthu a m’banja lawo. Aliyense akamayesetsa kusunga chinsinsi pa nkhani zokhudza banja lawo, zimathandiza kuti onse m’banjamo azikhala mogwirizana. w22.09 10 ¶9

Lamlungu, May 12

Mvetserani izi inu a Yobu: Imani ndi kuganizira mozama.—Yobu 37:14.

Yehova analankhula ndi Yobu kumukumbutsa za nzeru zake zopanda malire komanso kuti amasamalira mwachikondi zinthu zimene analenga. Anafotokoza za nyama zambiri zomwe ndi zochititsa chidwi. (Yobu 38:​1, 2; 39:​9, 13, 19, 27; 40:15; 41:​1, 2) Iye anagwiritsanso ntchito wachinyamata wina wokhulupirika dzina lake Elihu kuti amulimbikitse komanso kumutonthoza. Elihu anamutsimikizira kuti Yehova nthawi zonse amapereka mphoto kwa atumiki ake omwe amapirira. Koma Yehova anathandizanso Elihu kuti amupatse Yobu malangizo mwachikondi. Elihu anathandiza Yobu kuti asamangoganizira kwambiri za iyeyo pomukumbutsa kuti anthufe ndi aang’ono kwambiri poyerekeza ndi Yehova, yemwe ndi Mlengi wa chilengedwe chonse. Yehova anapatsanso Yobu ntchito yoti agwire. Iye ankafunika kupempherera anzake atatu omwe anachimwa. (Yobu 42:​8-10) Kodi masiku ano Yehova amatithandiza bwanji tikakumana ndi mayesero aakulu? Yehova salankhula nafe mwachindunji ngati mmene anachitira ndi Yobu, koma amalankhula nafe kudzera m’Mawu ake Baibulo.—Aroma 15:4. w22.08 11 ¶10-11

Lolemba, May 13

Ndi bwino kusadya nyama kapena kusamwa vinyo kapena kusachita chilichonse chimene chimakhumudwitsa m’bale wako.—Aroma 14:21.

Mumpingo wa Chikhristu ku Roma munali Ayuda ndi anthu a mitundu ina. Kungochokera pamene Chilamulo cha Mose chinasiya kugwira ntchito, panalibenso malamulo oletsa kudya zakudya zina. (Maliko 7:19) Kuchokera nthawi imeneyo, Akhristu ena a Chiyuda ankaona kuti akhoza kudya zakudya za mtundu wina uliwonse. Komabe ena ankaona kuti si bwino kudya zakudya zina. Izi zinachititsa kuti mumpingo mukhale kugawikana. Mtumwi Paulo anatsindika kufunika kokhala mwamtendere. Choncho Paulo anathandiza Akhristu anzakewo kuona kuti kukangana pa nkhani zimenezi kukanabweretsa chisokonezo pakati pawo komanso mumpingo. (Aroma 14:​19-20) Iye anali wokonzekanso kusintha mmene ankachitira zinthu kuti asakhumudwitse ena. (1 Akor. 9:​19-22) Ifenso masiku ano tingalimbikitse ena komanso kukhala nawo pa mtendere, ngati timapewa kukangana pa nkhani zimene aliyense amafunika kusankha yekha. w22.08 22 ¶7

Lachiwiri, May 14

Yehova . . . amakonda munthu amene amachita chilungamo.—Miy. 15:9.

Tikamayesetsa kuti tikwaniritse cholinga china chake potumikira Yehova, pamafunika kuchita khama kuti tichikwaniritse. Zimenezi ndi zimenenso zimafunika tikamafuna kuchita chilungamo. Ndipo Yehova adzatithandiza moleza mtima kuti n’kupita kwa nthawi tizichita bwino pa nkhaniyi. (Sal. 84:​5, 7) Mwachikondi, Yehova amatikumbutsa kuti kuchita chilungamo si mtolo wolemetsa. (1 Yoh. 5:3) M’malomwake ndi chitetezo chomwe timafunikira tsiku lililonse. Kumbukirani zida zankhondo zimene mtumwi Paulo anafotokoza. (Aef. 6:​14-18) Kodi ndi chida chiti chimene chinkateteza mtima wa msilikali? Chinali “chodzitetezera pachifuwa chachilungamo,” chomwe chimaimira mfundo zolungama za Yehova. Mofanana ndi chodzitetezera pachifuwa chomwe chimateteza mtima, mfundo zolungama za Yehova zimateteza mtima wathu wophiphiritsa, womwe ndi umunthu wathu wamkati. Choncho nthawi zonse muzionetsetsa kuti pa zida zanu za nkhondo, palinso chodzitetezera pachifuwa cha chilungamo.—Miy. 4:23. w22.08 29 ¶13-14

Lachitatu, May 15

Mawu a Mulungu wathu adzakhalapo mpaka kalekale.—Yes. 40:8.

Kwa zaka zambiri, Mawu a Mulungu akhala akupereka malangizo abwino kwa amuna ndi akazi okhulupirika. Kodi zimenezi zatheka bwanji? Yehova anaonetsetsa kuti anthu akopera Malemba opatulika. Ngakhale kuti okoperawa sanali angwiro, anayesetsa kuchita zinthu mosamala kwambiri. Mwachitsanzo, ponena za Malemba a Chiheberi, katswiri wina analemba kuti: “Tinganene motsimikiza kuti palibe buku lina lakale lomwe linakoperedwa molondola kwambiri ngati Malembawa.” Choncho tingakhalebe otsimikiza kuti zimene timawerenga m’Baibulo masiku ano ndi maganizo a Mlembi wake, Yehova. Iye ndi amene amatipatsa “mphatso iliyonse yabwino ndi yangwiro.” (Yak. 1:17) Baibulo ndi imodzi mwa mphatso zabwino kwambiri zimene iye anatipatsa. Mphatso imatiuza zambiri zokhudza woperekayo kuti amatidziwa bwino komanso amadziwa zimene timafunikira. Ndi mmenenso zilili ndi Mulungu yemwe anatipatsa Baibulo. Timaphunzira zambiri zokhudza Yehova kudzera mu mphatsoyi. Timaphunziramonso kuti iye amatidziwa bwino kwambiri komanso amadziwa zimene timafunikira. w23.02 2-3 ¶3-4

Lachinayi, May 16

Dziko lapansi lidzadzaza ndi anthu odziwa Yehova.—Yes. 11:9.

Zidzakhalatu zosangalatsa kwambiri anthu akadzayamba kuukitsidwa padzikoli mu Ulamuliro wa Khristu wa Zaka 1,000. Anthu onse omwe okondedwa awo anamwalira amafunitsitsa kudzawaonanso. Umu ndi mmenenso Yehova amamvera. (Yobu 14:15) Tangoganizani mmene zidzakhalire zosangalatsa kuona anthu padziko lonse akukumananso ndi okondedwa awo omwe anamwalira. “Olungama” omwe mayina awo analembedwa m’buku la moyo, “adzauka kuti alandire moyo.” (Mac. 24:15; Yoh. 5:29) N’kutheka kuti ambiri mwa okondedwa athuwa adzakhala m’gulu la anthu oyambirira kuukitsidwa kuti akhale ndi moyo padzikoli Aramagedo ikadzangotha. Kuwonjezera pamenepo, “osalungama” omwe analibe mwayi wodziwa Yehova ndi kumutumikira mokhulupirika pa nthawi imene anali ndi moyo, “adzauka kuti aweruzidwe.” Anthu onse omwe adzaukitsidwe adzafunika kuphunzitsidwa. (Yes. 26:9; 61:11) Choncho padzafunika pakhale ntchito yaikulu yophunzitsa anthu yomwe sinachitikepo ndi kale lonse.—Yes. 11:10. w22.09 20 ¶1-2

Lachisanu, May 17

Iye ndi Mulungu wamoyo. —Dan. 6:26.

Yehova anasonyeza kuti ndi wamkulu kwambiri kuposa olamulira omwe anachita mgwirizano. Iye anamenyera nkhondo Aisiraeli ndipo anawathandiza kugonjetsa mbali yaikulu ya Dziko Lolonjezedwa. (Yos. 11:​4-6, 20; 12:​1, 7, 24) Mobwerezabwereza Yehova wakhala akusonyeza kuti iye ndi Wamkulukulu. Mfumu Nebukadinezara wa ku Babulo atadzikweza chifukwa chokhala ndi ‘mphamvu komanso ulemerero waukulu,’ m’malo movomereza kuti Yehova ndi woyenera kutamandidwa, Mulungu anamuchititsa misala. Atachira, Nebukadinezara ‘anatamanda Wam’mwambamwamba’ ndipo anavomereza kuti “ulamuliro wa [Yehova] udzakhalapo mpaka kalekale.” Anawonjezeranso kuti: “Palibe aliyense amene angaletse dzanja lake.” (Dan. 4:​30, 33-35) Wolemba masalimo anati: “Wosangalala ndi mtundu umene Mulungu wawo ndi Yehova, anthu amene iye wawasankha kuti akhale cholowa chake.” (Sal. 33:12) Tilitu ndi zifukwa zabwino kwambiri zotichititsa kukhalabe okhulupirika kwa Yehova. w22.10 15-16 ¶13-15

Loweruka, May 18

Mawu anu . . . ndi choonadi. —Sal. 119:160.

Maulosi ambiri a m’Baibulo omwe akwaniritsidwa kale amatithandiza kuti tizikhulupirira kwambiri kuti malonjezo a Mulungu adzakwaniritsidwa. Timamva ngati mmene anamvera wolemba masalimo wina yemwe anapemphera kwa Yehova kuti: “Ine ndikulakalaka chipulumutso chanu, Chifukwa mawu anu ndi chiyembekezo changa.” (Sal. 119:81) Kudzera m’Baibulo, mokoma mtima Yehova amatipatsa “tsogolo labwino ndi chiyembekezo chabwino “ (Yer. 29:11) Chiyembekezo chathu sichidalira pa zimene munthu angachite, koma pa malonjezo a Yehova. Tiyeni tipitirize kukhulupirira kwambiri Mawu a Mulungu pophunzira mwakhama maulosi a m’Baibulo. Umboni wina wotithandiza kuti tizikhulupirira kwambiri Baibulo ndi woti limathandiza kwambiri anthu omwe amatsatira malangizo ake. (Sal. 119:​66, 138) Mwachitsanzo, mabanja ena omwe anali atatsala pang’ono kutha panopa akukhalabe limodzi mosangalala. Ana awo amasangalala kuleredwa m’banja la Chikhristu momwe amadzimva kukhala otetezeka komanso okondedwa.—Aef. 5:​22-29. w23.01 5 ¶12-13

Lamlungu, May 19

Kondwerani chifukwa cha chiyembekezo.—Aroma 12:12.

Taganizirani mmene inuyo panokha mwapindulira chifukwa cha kukwaniritsidwa kwa malonjezo opezeka m’Mawu a Mulungu. Mwachitsanzo, Yesu analonjeza kuti Atate wake adzakupatsani zomwe mumafunikira pa moyo. (Mat. 6:​32, 33) Iye anakutsimikiziraninso kuti Yehova adzakupatsani mzimu wake woyera mukamupempha. (Luka 11:13) Yehova wakhala akukwaniritsa malonjezo amenewa. N’kutheka kuti pali malonjezo ena omwe inuyo mwaona akukwaniritsidwa pa inu. Mwachitsanzo, iye analonjeza kuti azikukhululukirani, kukutonthozani komanso kukudyetsani mwauzimu. (Mat. 6:14; 24:45; 2 Akor. 1:3) Mukamaganizira kwambiri zimene Mulungu wakuchitirani kale, mudzalimbitsa chiyembekezo chanu cha m’tsogolo. Sitimakayikira kuti Yehova adzakwaniritsa malonjezo ake. Wolemba masalimo anati: “Wosangalala ndi munthu amene . . . chiyembekezo chake chili mwa Yehova Mulungu wake, . . . amene amakhala wokhulupirika nthawi zonse.”—Sal. 146:​5, 6. w22.10 27 ¶15; 28 ¶17

Lolemba, May 20

Kuwala kwa Yehova kudzafika pa iwe.—Yes. 60:2.

Kodi ulosi wonena za kubwezeretsedwa kwa kulambira koona umatikhudzanso masiku ano? Inde. Motani? Kungoyambira mu 1919 C.E., anthu mamiliyoni ambiri amasulidwa ku ukapolo wa Babulo Wamkulu, yemwe ndi zipembedzo zonse zonyenga. Iwo atsogoleredwa kudziko labwino kwambiri kuposa Dziko Lolonjezedwa la Isiraeli. Dzikoli ndi paradaiso wauzimu. (Yes. 51:3; 66:8) Kungoyambira mu 1919 C.E., odzozedwa akhala akusangalala kukhala m’paradaiso wauzimu. Pamene nthawi ikupita, a “nkhosa zina” omwe ali ndi chiyembekezo chodzakhala padzikoli alowanso m’dziko lauzimuli ndipo akusangalala ndi madalitso a Yehova ochuluka. (Yoh. 10:16; Yes. 25:6; 65:13) Paradaiso wauzimu yemwe amakhalamo ali padziko lonse. Masiku ano, kaya timakhala kuti padzikoli, tingathe kukhala m’paradaiso wauzimu ngati timayesetsa kuchita zinthu zothandiza kulambira koona. w22.11 11-12 ¶12-15

Lachiwiri, May 21

Inu Yehova, mwakhala mulipo kuyambira kalekale. Inu Mulungu wanga, Mulungu wanga Woyera, inu simufa.—Hab. 1:12.

Kodi mumavutika kumvetsa mfundo yakuti Yehova wakhala alipo kuyambira “kalekale”? (Yes. 40:28) Anthu ambirinso zimawavuta kumvetsa. Ponena za Mulungu, Elihu anati: “Palibe amene angawerenge zaka zimene wakhala ndi moyo.” (Yobu 36:26) Koma ngati sitikumvetsa chinachake sizitanthauza kuti chinthucho si choona. Mwachitsanzo, ngakhale kuti sitingamvetse zonse zokhudza kuwala, kodi zimenezi zikutanthauza kuti kuwala kulibeko? Ayi ndithu. Mofanana ndi zimenezi, anthufe sitingathe kumvetsa bwinobwino mfundo yakuti Yehova alibe chiyambi komanso mapeto. Komatu zimenezi sizitanthauza kuti Mulungu sangakhale ndi moyo mpaka kalekale. Mlengi sangalephere kuchita zinthu chifukwa cha zimene tikumvetsa kapena ayi. (Aroma 11:​33-36) Ndipo iye anakhalapo zinthu zina zonse m’chilengedwechi, kuphatikizapo zomwe zimapereka kuwala monga dzuwa, zisanakhalepo. Iye anakhalako ‘asanayale kumwamba.’—Yer. 51:15. w22.12 2-3 ¶3-4

Lachitatu, May 22

Pemphero langa likhale ngati zofukiza zokonzedwa pamaso panu.—Sal. 141:2.

Nthawi zina tingapemphedwe kuti tipemphere m’malo mwa anthu ena. Mwachitsanzo, mlongo yemwe akuchititsa phunziro la Baibulo angapemphe mlongo wina yemwe wapita naye kuphunziroko kuti apemphere. Mlongo winayo angakhale kuti sakudziwa bwinobwino wophunzirayo. Choncho angakonde kupereka pemphero lomaliza. Zimenezi zingathandize kuti adziwe zomwe angatchule zokhudza wophunzirayo m’pempherolo. M’bale angauzidwe kuti apemphere pamsonkhano wampingo kapena wokonzekera utumiki. Abale amene apatsidwa mwayi umenewu ayenera kukumbukira cholinga cha misonkhanoyi. Pemphero si njira yoperekera malangizo kapena zilengezo. Pamisonkhano yampingo yambiri pamaperekedwa 5 minitsi ya nyimbo ndi pemphero. Choncho m’bale amene akupemphera sayenera kunena “mawu ambirimbiri” makamaka m’pemphero la koyambirira kwa misonkhano.—Mat. 6:7. w22.07 24 ¶17-18

Lachinayi, May 23

Mudzamva phokoso la nkhondo ndi malipoti a nkhondo. Izitu zisadzakuchititseni mantha, chifukwa zimenezi zikuyenera kuchitika ndithu, koma mapeto adzakhala asanafikebe.—Mat. 24:6.

Yesu ananeneratu kuti m’masiku otsiriza kudzakhala miliri, kapena kuti matenda omwe amafalikira kwambiri, “m’malo osiyanasiyana.” (Luka 21:11) Kodi kudziwa zimenezi kungatithandize bwanji kukhala ndi mtendere? Sitimadabwa tikaona miliri ikuchitika. Timadziwa kuti zimenezi zikuchitika monga mmene Yesu ananenera. Choncho tili ndi chifukwa chomveka chotsatirira malangizo ake omwe anapereka kwa anthu amene akukhala m’nthawi yamapeto, akuti: “Izitu zisadzakuchititseni mantha.” Mosakayikira mliri ungasokoneze pulogalamu yanu yochitira zinthu za tsiku ndi tsiku. Koma musalole kuti zimenezi zikuchititseni kulephera kuphunzira Baibulo panokha komanso kupezeka pamisonkhano. Zochitika pa moyo wa anthu ena zopezeka m’mabuku athu ndiponso m’mavidiyo, zingakukumbutseni kuti abale ndi alongo anu akupitirizabe kukhala okhulupirika ngakhale kuti akukumana ndi mavuto ngati omwewo. w22.12 17 ¶4, 6

Lachisanu, May 24

Zinthu zosayembekezereka zimagwera onsewo.—Mlal. 9:11.

Yakobo anasonyeza kuti ankakonda kwambiri Yosefe. (Gen. 37:​3, 4) Zimenezi zinachititsa kuti azichimwene ake azimuchitira nsanje. Pamene mpata unapezeka iwo anamugulitsa kwa amalonda a ku Midiyani. Amalondawa anamutengera kutali kwambiri ku Igupto kumene anakagulitsidwanso kwa Potifara, yemwe anali mkulu wa asilikali olondera Farao. Pamenepatu moyo wa Yosefe unasintha mofulumira kwambiri kuchoka pokhala mwana wokondedwa wa bambo ake, n’kukhala kapolo ku Iguputo. (Gen. 39:1) Nthawi zina timakumana ndi mavuto kapena mayesero omwe ndi ‘osiyana ndi amene anthu ena amakumana nawo.’ (1 Akor. 10:13) Kapenanso tingavutike chifukwa choti ndife ophunzira a Yesu. Mwachitsanzo, tikhoza kumanyozedwa, kutsutsidwa ngakhalenso kuzunzidwa chifukwa cha chikhulupiriro chathu. (2 Tim. 3:12) Kaya mukukumana ndi mayesero otani, Yehova angakuthandizeni kuti zinthu zikuyendereni bwino. w23.01 14-15 ¶3-4

Loweruka, May 25

Ngati palibe nkhuni moto umazima.—Miy. 26:20.

Nthawi zina tingaone kuti n’zofunika kuti tikambirane ndi Mkhristu mnzathu yemwe watilakwira. Koma choyamba tingachite bwino kudzifunsa mafunso monga: ‘Kodi ndikudziwa mfundo zonse zokhudza nkhaniyi?’ (Miy. 18:13) ‘Kodi n’kutheka kuti iye sanandilakwire mwadala?’ (Mlal. 7:20) ‘Kodi inenso ndinayamba ndalakwitsapo mwanjira imeneyi?’ (Mlal. 7:​21, 22) ‘Ngati nditakambirana naye, kodi ndichititsa kuti nkhaniyi ikule kwambiri m’malo moti ithe?’ Pambuyo poganizira mafunso amenewa, tingaone kuti chifukwa chokonda m’bale wathuyo tingonyalanyaza nkhaniyo. Komanso patokha timasonyeza kuti ndife wotsatira weniweni wa Yesu ngati timakonda abale ndi alongo athu ngakhale kuti amalakwitsa zinthu zina. Tikamachita zimenezi timathandiza kuti anthu ena azindikire chipembedzo choona komanso kuti nawonso ayambe kulambira Yehova. Choncho tiyeni tikhale otsimikiza kuti tipitiriza kusonyeza chikondi chomwe chimadziwikitsa Akhristu oona. w23.03 31 ¶18-19

Lamlungu, May 26

Mulungu ndi chikondi.—1 Yoh. 4:8.

Baibulo limatithandiza kumvetsa kuti khalidwe lalikulu la Mulungu ndi chikondi. Chifukwa choti Yehova amatikonda, sanatipatse malangizo ambirimbiri omwe ndi osafunika kwenikweni pa nkhani yomutumikira. (Yoh. 21:25) Yehova anasonyezanso kuti amatikonda polankhula nafe m’njira yotilemekeza. M’Baibulo, iye sanatipatse malamulo ambirimbiri otiuza zoyenera kuchita m’mbali iliyonse ya moyo wathu. M’malomwake, amatithandiza kuti tiziganiza komanso kusankha tokha zochita potifotokozera nkhani zochitikira anthu ena, maulosi ochititsa chidwi komanso malangizo othandiza. Mwa njira zimenezi, Mawu a Mulungu amatithandiza kuti tizimukonda komanso kumumvera kuchokera pansi pa mtima. Baibulo limasonyeza kuti Mulungu amachita nafe chidwi kwambiri. Motani? M’Mawu ake muli nkhani zambiri zosonyeza mmene anthu amamvera. Tingathe kumvetsa mmene anthu otchulidwa m’Baibulo ankamvera chifukwa iwo anali anthu “ngati ife tomwe.” (Yak. 5:17) Chofunika kwambiri n’chakuti tikamaganizira mmene Mulungu anachitira zinthu ndi anthu ngati ife, timafika pomvetsa bwino kuti “Yehova ndi wachikondi chachikulu komanso wachifundo.”—Yak. 5:11. w23.02 6 ¶13-15

Lolemba, May 27

Khalanibe oganiza bwino ndipo khalani tcheru.—1 Pet. 5:8.

Buku lomalizira la m’Baibulo limayamba ndi mawu akuti: “Chivumbulutso chimene Yesu Khristu anapereka. Mulungu anamupatsa Chivumbulutso chimenechi kuti aonetse akapolo ake zinthu zimene zikuyenera kuchitika posachedwapa.” (Chiv. 1:1) Choncho timachita chidwi kwambiri ndi zomwe zikuchitika m’dzikoli kuti tione mmene zikukwaniritsira maulosi a m’Baibulo. Ndipo timafunitsitsa kukambirana ndi ena zochitika zimenezi. Tikamakambirana maulosi a m’Baibulo tizipewa kufotokoza za m’maganizo mwathu. Chifukwa chiyani? Chifukwa sitimafuna kulankhula chilichonse chimene chingasokoneze mgwirizano mumpingo. Mwachitsanzo, mwina tingamve olamulira a mayiko akufotokoza zimene angachite kuti athetse vuto linalake komanso kubweretsa mtendere ndi chitetezo. M’malo mongofotokoza maganizo athu kuti zimenezi zikukwaniritsa ulosi wa pa 1 Atesalonika 5:3 tiyenera kufotokoza mogwirizana ndi mfundo zimene zafalitsidwa posachedwapa. Tikamanena zinthu mogwirizana ndi zimene zili m’mabuku a gulu la Yehova, timathandiza kuti mpingo upitirize kukhala wogwirizana komanso ukhale “ndi maganizo amodzi.”—1 Akor. 1:10; 4:6. w23.02 16 ¶4-5

Lachiwiri, May 28

Kwera pahatchi yako chifukwa cha choonadi, kudzichepetsa ndi chilungamo, ndipo dzanja lako lamanja lidzachita zinthu zochititsa mantha.—Sal. 45:4.

N’chifukwa chiyani mumakonda Yesu Khristu? Iye amakonda choonadi, kudzichepetsa komanso chilungamo. Ngati mumakonda choonadi ndi chilungamo, n’zomveka kuti mumakondanso Yesu Khristu. Taganizirani mmene iye anachitira zinthu molimba mtima pokhala kumbali ya choonadi ndi chilungamo. (Yoh. 18:37) Koma kodi Yesu amasonyeza bwanji kuti amalimbikitsa khalidwe la kudzichepetsa? Yesu amalimbikitsa khalidwe la kudzichepetsa mwa zochita zake. Mwachitsanzo, iye amaonetsetsa kuti ulemerero wonse ukupita kwa Atate wake osati kwa iyeyo. (Maliko 10:​17, 18; Yoh. 5:19) Kodi inuyo mumamva bwanji mukaganizira kudzichepetsa koteroko? Kodi sizimakuchititsani kuti muzikonda Mwana wa Mulungu komanso kumutsanzira? N’zosachita kufunsa. N’chifukwa chiyani Yesu ali wodzichepetsa? Chifukwa amakonda komanso kutsanzira Atate wake omwe ndi odzichepetsa. (Sal. 18:35; Aheb. 1:3) Kodi zimenezi sizikukuchititsani kuti muzikonda kwambiri Yesu yemwe amasonyeza bwino kwambiri makhalidwe a Yehova? w23.03 3-4 ¶6-7

Lachitatu, May 29

Mulungu adzaukitsa olungama ndi osalungama omwe.—Mac. 24:15.

Baibulo limatiuza za magulu awiri a anthu amene adzaukitsidwe kuti akhale ndi moyo wosatha padzikoli, omwe ndi “olungama” ndi “osalungama.” “Olungama” ndi anthu omwe anatumikira Yehova mokhulupirika pa nthawi yomwe anali ndi moyo. Pomwe anthu “osalungama” ndi omwe sanamutumikire. Popeza kuti anthu a m’magulu awiri onsewa adzaukitsidwa, kodi tinganene kuti mayina awo ali m’buku la moyo? “Olungama” asanamwalire, mayina awo anali atalembedwa m’buku la moyo. Ndiye kodi atamwalira, mayina awo anafufutidwa m’bukuli? Ayi, chifukwa kwa Yehova iwo ndi “amoyo.” Yehova “ndi Mulungu wa anthu amoyo, osati akufa, pakuti kwa iye onsewa ndi amoyo.” (Luka 20:38) Zimenezi zikutanthauza kuti olungama akadzaukitsidwa kuti akhale ndi moyo padzikoli, mayina awo adzakhala adakali m’buku la moyo, ngakhale kuti zidzakhala ngati alembedwa ndi pensulo.—Luka 14:14. w22.09 16 ¶9-10

Lachinayi, May 30

Tsopano Yehova Mulungu anatenga munthu uja n’kumuika m’munda wa Edeni kuti aziulima komanso kuusamalira.—Gen. 2:15.

Yehova ankafuna kuti munthu woyambirira azisangalala ndi zinthu zimene iye analenga. Mulungu atalenga Adamu anamuika m’malo abwino kwambiri oti azikhalamo n’kumaphunzira zinthu zimene zinali mmenemo. Anamupatsanso ntchito yoti azisamalira komanso kuwonjezera munda wokongolawo. (Gen. 2:​8, 9) Tangoganizani mmene Adamu ankasangalalira akamaona mbewu zikumera komanso zomera zina zikuchita maluwa. Iye analitu ndi mwayi waukulu wosamalira munda wa Edeni. Yehova anapemphanso Adamu kuti apereke mayina kwa nyama zosiyanasiyana. (Gen. 2:​19, 20) Yehova akanatha kuchita yekha zimenezi, koma anapereka ntchitoyi kwa Adamu. Mosakayikira, asanapereke mayina kwa nyamazo, Adamu ankaziyang’anitsitsa n’kumaona zimene zikuchita komanso makhalidwe awo. Iye ayenera kuti anasangalala kwambiri kugwira ntchitoyi. N’zoonekeratu kuti izi zinamuthandiza kumvetsa kuti Atate wake ndi wanzeru komanso kuti zinthu zimene analenga ndi zokongola ndi zosangalatsa. w23.03 15 ¶3

Lachisanu, May 31

Udzaphwanya n’kuthetsa maufumu ena onsewo, ndipo ndi ufumu wokhawu umene udzakhalapo mpaka kalekale.—Dan. 2:44.

Ulamuliro wa Britain ndi America womwe umaimiridwa ndi mapazi a chifaniziro, ndi ulamuliro wapadziko lonse womaliza womwe Baibulo linaneneratu. (Dan. 2:​31-33) Sudzalowedwa m’malo ndi ulamuliro wina wandale. M’malomwake, pa Aramagedo Ufumu wa Mulungu udzawononga mofulumira ulamulirowu pamodzi ndi maboma ena onse a anthu. (Chiv. 16:​13, 14, 16; 19:​19, 20) Kodi ulosiwu umatithandiza bwanji? Ulosi wa Danieli umatipatsa umboni wowonjezereka wosonyeza kuti tikukhala m’nthawi ya mapeto. Zaka pafupifupi 2,500 zapitazo, Danieli ananeneratu kuti pambuyo pa ulamuliro wa Babulo, padzabwera maulamuliro ena 4 omwe zochita zawo zidzakhudza kwambiri atumiki a Mulungu. Kuwonjezera pamenepo, iye anasonyeza kuti ulamuliro wamphamvu padziko lonse wa Britain ndi America udzakhala womaliza. Zimenezi zimatilimbikitsa komanso kutipatsa chiyembekezo choti posachedwapa, Ufumu wa Mulungu udzachotsa maboma onse a anthu n’kuyamba kulamulira dziko lonse. w22.07 4 ¶9; 5 ¶11-12

    Mabuku a Chichewa (1974-2026)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena