June
Loweruka, June 1
Mnofu wanga wakutidwa ndi mphutsi komanso fumbi, khungu langa lang’ambika n’kumatuluka mafinya.—Yobu 7:5.
Yobu anali pa ubwenzi ndi Yehova. Anali ndi banja lalikulu komanso logwirizana ndipo anali ndi chuma chambiri. (Yobu 1:1-5) Koma m’tsiku limodzi lokha iye anataya pafupifupi chilichonse. Choyamba, anataya chuma chake chonse. (Yobu 1:13-17) Kenako ana ake onse anafa. Taganizirani mmene Yobu ndi mkazi wake anamvera kupweteka atamva zoti ana awo onse 10 afa. Mpake kuti iye anang’amba zovala zake akulira n’kudzigwetsa pansi. (Yobu 1:18-20) Kenako Satana anadwalitsa Yobu matenda opweteka kwambiri komanso ochititsa manyazi. (Yobu 2:6-8) Pa nthawi ina anthu a m’dera lake ankamulemekeza kwambiri ndipo ankabwera kudzamupempha malangizo. (Yobu 31:18) Koma tsopano anayamba kumupewa. Iye anayamba kukanidwa ndi abale ake, anzake ngakhalenso antchito ake enieni.—Yobu 19:13, 14, 16. w22.06 21 ¶5-6
Lamlungu, June 2
Tikhale achikulire m’zinthu zonse, [kudzera m’chikondi].—Aef. 4:15.
Tonsefe tikabatizidwa timafunika kutsatira malangizo amene mtumwi Paulo anapereka kwa Akhristu a ku Efeso. Iye anawalimbikitsa kuti akhale ‘achikulire’ mwauzimu. (Aef. 4:13) Zinali ngati akuwauza kuti, ‘Pitirizani kupita patsogolo.’ Panopa mumakonda kale kwambiri Yehova. Koma mukhoza kuwonjezera chikondi chanucho. Motani? Mtumwi Paulo anatchula njira imodzi yochitira zimenezi pa Afilipi 1:9. Paulo anapemphera kuti chikondi cha Akhristu a ku Filipi “chipitirize kukula.” Choncho tikhoza kukulitsa chikondi chathu pa Yehova. Tingachite zimenezi popitirizabe “kudziwa zinthu molondola, komanso kuzindikira zinthu bwino kwambiri.” Tikamamudziwa bwino Yehova, m’pamenenso timayamba kumukonda kwambiri komanso kuyamikira makhalidwe ake ndiponso mmene amachitira zinthu. Timakhala ofunitsitsa kumusangalatsa n’kumapewa chilichonse chomwe chingamukhumudwitse. Timayesetsa kuzindikira chifuniro chake komanso mmene tingachitire zinthu mogwirizana ndi chifuniro chakecho. w22.08 2-3 ¶3-4
Lolemba, June 3
Chivumbulutso chimene Yesu Khristu anapereka. Mulungu anamupatsa Chivumbulutso chimenechi kuti aonetse akapolo ake zinthu zimene zikuyenera kuchitika posachedwapa.—Chiv. 1:1.
Zimene zinalembedwa m’buku la Chivumbulutso sikuti zinangolembedwera wina aliyense, koma ifeyo monga atumiki a Mulungu. Monga anthu a Mulungu, sitiyenera kudabwa kuti ifenso tikukwaniritsa nawo maulosi amene ali m’bukuli. Mtumwi Yohane, yemwe pa nthawiyi anali wokalamba anafotokoza za nthawi imene maulosiwa akuyenera kukwaniritsidwa. Iye anati: “[Mwa] mzimu woyera ndinapezeka kuti ndili m’tsiku la Ambuye.” (Chiv. 1:10) Pamene Yohane ankalemba mawuwa cha m’ma 96 C.E., n’kuti kutatsala zaka zambiri kuti ‘tsiku la Ambuye’ liyambe. (Mat. 25:14, 19; Luka 19:12) Koma mogwirizana ndi ulosi wa m’Baibulo, tsikuli linayamba mu 1914 pamene Yesu anaikidwa kukhala Mfumu kumwamba. Kungoyambira m’chaka chimenecho, maulosi a m’buku la Chivumbulutso omwe amakhudza anthu a Mulungu, anayamba kukwaniritsidwa. Panopa tikukhala “m’tsiku la Ambuye.”—Chiv. 1:3. w22.05 2 ¶2-3
Lachiwiri, June 4
Chilombocho chinagwidwa limodzi ndi mneneri wabodza uja.—Chiv. 19:20.
Adakali amoyo, onse awiri chilombo komanso mneneri wonyenga, anaponyedwa m’nyanja ya moto yoyaka ndi sulufule. Choncho pa nthawi imene adzakhale akulamulira, adani a Mulungu amenewa adzawonongedwa ndipo sadzakhalakonso mpaka kalekale. Kodi zimenezi zimatikhudza bwanji? Monga Akhristu, tiyenera kukhala okhulupirika kwa Mulungu ndi Ufumu wake. (Yoh. 18:36) Sitiyenera kulowerera ndale za m’dzikoli. Komabe kusalowerera ndale kungakhale kovuta kwambiri chifukwa maboma a m’dzikoli amafuna kuti tisonyeze kuti tili kumbali yawo mwa zolankhula ndi zochita zathu. Anthu amene amalolera zimenezi amalandira chizindikiro cha chilombo. (Chiv. 13:16, 17) Komatu anthu omwe alandira chizindikiro cha chilombochi, amakhala osavomerezeka kwa Yehova ndipo amataya mwayi wodzalandira moyo wosatha. (Chiv. 14:9, 10; 20:4) Choncho n’zofunika kwambiri kwa aliyense wa ife kuti asamalowerere ndale mpang’ono pomwe ngakhale maboma atatikakamiza chotani kuti tikhale kumbali yawo. w22.05 10-11 ¶12-13
Lachitatu, June 5
Kodi wamuona munthu waluso pa ntchito yake? Iye adzaima pamaso pa mafumu. Sadzaima pamaso pa anthu wamba.—Miy. 22:29.
Chimodzi mwa zolinga zimene mungadziikire ndi kuphunzira luso linalake lothandiza. Ngati titakulitsa maluso athu, tingamachite zambiri potumikira Yehova. Ganizirani za kuchuluka kwa anthu amene amafunika pomanga maofesi a nthambi, Malo a Msonkhano komanso Nyumba za Ufumu. Ambiri mwa iwo anapeza luso pogwira ntchito limodzi ndi abale ndi alongo omwe amadziwa bwino ntchitoyo. Masiku ano, abale ndi alongo akuphunzira luso lomwe lingawathandize pa ntchito yokonza Malo a Msonkhano ndi Nyumba za Ufumu. M’njira zimenezi komanso zina, Yehova Mulungu yemwe ndi “Mfumu yamuyaya,” ndi Yesu Khristu yemwe ndi “Mfumu ya mafumu,” akukwanitsa zinthu zazikulu pogwiritsa ntchito anthu aluso. (1 Tim. 1:17; 6:15) Timafuna kuti tizichita khama komanso kugwiritsa ntchito luso lathu polemekeza Yehova osati kudzilemekeza tokha.—Yoh. 8:54. w22.04 24 ¶7; 25 ¶11
Lachinayi, June 6
Ndalama [zimateteza].—Mlal. 7:12.
Solomo anali wolemera kwambiri ndipo ankakhala moyo wawofuwofu. (1 Maf. 10:7, 14, 15) Koma Yesu sanali ndi zinthu zambiri ndipo analibe nyumba yakeyake. (Mat. 8:20) Koma anthu onsewa ankaona zinthu moyenera chifukwa nzeru zawo zinkachokera kwa Yehova Mulungu. Solomo anavomereza kuti ndalama zimatithandiza kuti tipeze zinthu zofunika pa moyo komanso zinthu zina zomwe timafuna. Ngakhale kuti anali wolemera, Solomo anazindikira kuti palinso zinthu zina zofunika kwambiri kuposa ndalama. Mwachitsanzo iye analemba kuti: “Ndi bwino kusankha dzina labwino [kapena kuti, “mbiri yabwino,” mawu a m’munsi] kusiyana ndi chuma chochuluka.” (Miy. 22:1) Solomo anazindikiranso kuti anthu omwe amakonda ndalama sasangalala ndi zinthu zomwe ali nazo. (Mlal. 5:10, 12) Anatichenjezanso kuti tisamadalire kwambiri ndalama chifukwa zikhoza kutha m’kanthawi kochepa.—Miy. 23:4, 5. w22.05 21 ¶4-5
Lachisanu, June 7
Yehova akuyembekezera moleza mtima kuti akukomereni mtima, Ndipo adzanyamuka kuti akuchitireni chifundo, Chifukwa Yehova ndi Mulungu amene amaweruza mwachilungamo. Osangalala ndi anthu onse amene akumuyembekezera.—Yes. 30:18.
Tikamaganizira kwambiri madalitso omwe talandira panopa, timalimbitsa ubwenzi wathu ndi Yehova. Ndipo kuganizira kwambiri madalitso omwe Yehova watisungira m’tsogolomu, kungatichititse kuti tizikhulupirira kwambiri kuti tidzamutumikira mpaka kalekale. Zonsezi zingatithandize kuti tizimutumikira mosangalala panopa. Yehova “adzanyamuka” m’malo mwa ife pamene azidzawononga dziko loipali. Ndife otsimikiza kuti Yehova, yemwe ndi “Mulungu amene amaweruza mwachilungamo,” sadzalola kuti dziko lolamuliridwa ndi Satanali likhalepobe kuposa nthawi imene analiikira. (Yes. 25:9) Tikuyembekezera mwachidwi nthawi imene tsiku lachipulumutso la Yehova lidzafike. Koma panopa ndife otsimikiza kuti tipitiriza kuona kuti ndi mwayi wamtengo wapatali kupemphera, kuphunzira Mawu a Mulungu ndi kuwatsatira komanso kuganizira madalitso athu. Tikamachita zimenezi, Yehova adzatithandiza kuti tizipirira mosangalala pamene tikumulambira. w22.11 13 ¶18-19
Loweruka, June 8
Usasiye kutsatira malangizo a mayi ako.—Miy. 1:8.
Ngakhale kuti Baibulo silifotokoza mmene zinalili pa nthawi imene Timoteyo ankabatizidwa, n’zosavuta kuganizira chimwemwe chimene mayi ake, a Yunike anali nacho pa tsikulo. (Miy. 23:25) Apatu anakwanitsa kuthandiza mwana wawo kuti azikonda Yehova ndi Mwana wake Yesu Khristu, ngakhale kuti kuchita zimenezi kunali kovuta. Timoteyo analeredwa m’banja limene makolo ake anali osiyana zipembedzo. Bambo ake anali Mgiriki, pomwe mayi ake ndi agogo ake anali Ayuda. (Mac. 16:1) Iye ayenera kuti anali wachinyamata pomwe a Yunike ndi a Loisi anayamba Chikhristu. Koma bambo ake sanalowe nawo chipembedzochi. Ndiye kodi Timoteyo akanakhala mbali iti? Masiku anonso akazi a Chikhristu amakonda mabanja awo. Kuposa chilichonse, iwo amafunitsitsa kuthandiza ana awo kukhala pa ubwenzi wabwino ndi Yehova. Ndipo Mulungu wathu amayamikira kwambiri khama lawo. (Miy. 1:8, 9) Yehova wathandiza amayi ambiri kuphunzitsa ana awo choonadi. w22.04 16 ¶1-3
Lamlungu, June 9
Mulungu anaika pulani m’mitima yawo kuti [achite] mogwirizana ndi maganizo ake.—Chiv. 17:17.
Posachedwapa Yehova adzaika zofuna zake m’mitima ya olamulirawa kuti achite “monga mwa maganizo ake.” Kodi zotsatirapo zake zidzakhala zotani? Olamulirawa, kapena kuti “mafumu 10” adzaukira zipembedzo zonyenga n’kuziwononga. (Chiv. 17:1, 2, 12, 16) Kodi timadziwa bwanji kuti mapeto a Babulo Wamkulu ayandikira? Kuti tiyankhe funsoli, tiyenera kukumbukira kuti mzinda wakale wa Babulo unkatetezedwa ndi madzi a mtsinje waukulu wa Firate. Buku la Chivumbulutso limayerekezera anthu mamiliyoni omwe ali mu Babulo Wamkulu ndi “madzi” otetezawa. (Chiv. 17:15) Koma limasonyezanso kuti madziwa ‘adzauma,’ zomwe zikutanthauza kuti anthu a m’zipembedzo zonyenga adzatulukamo. (Chiv. 16:12) Pokwaniritsa ulosiwu, anthu ambiri masiku ano ayamba kutuluka m’zipembedzo zonyenga n’kuyamba kufufuza kwina mmene angathetsere mavuto awo. w22.07 5-6 ¶14-15
Lolemba, June 10
Munthu amene sasonyeza chifundo adzaweruzidwa mopanda chifundo. Chifundo n’chachikulu kuposa chiweruzo. —Yak. 2:13.
Kukhululuka kumasonyeza kuti ndife oyamikira. M’fanizo lina, Yesu anayerekezera Yehova ndi mbuye, yemwe anakhululukira kapolo wake ngongole yaikulu yomwe sakanatha kubweza. Komabe kapoloyo analephera kusonyeza chifundo kapolo mnzake amene anamukongoza ndalama zochepa kwambiri. (Mat. 18:23-35) Kodi Yesu ankafuna kutiphunzitsa chiyani pamenepa? Ngati timayamikiradi chifundo chachikulu chomwe Yehova amatisonyeza, tidzakhala ofunitsitsa kukhululukira ena. (Sal. 103:9) Zaka zambiri zapitazo, Nsanja ya Olonda ina inanena kuti: “Kaya takhala tikukhululukira anthu kambirimbiri bwanji, sitingafike pa mlingo umene Mulungu amatikhululukira komanso kutisonyeza chifundo kudzera mwa Khristu.” Okhululukira ena nawonso adzakhululukidwa. Yehova amachitira chifundo anthu omwenso ndi achifundo. (Mat. 5:7) Yesu anafotokoza mfundo imeneyi momveka bwino pamene ankaphunzitsa ophunzira ake kupemphera.—Mat. 6:14, 15. w22.06 10 ¶8-9
Lachiwiri, June 11
Kudzera mwa mbadwa yako, mitundu yonse ya padziko lapansi idzapeza madalitso.—Gen. 22:18.
Yesu anabwera padziko lapansi monga munthu. Iye anasonyeza bwino makhalidwe a Atate ake. (Yoh. 14:9) Choncho tikamaphunzira za Yesu timafika podziwa komanso kukonda Yehova Mulungu. Timapindulanso ndi zimene Yesu anaphunzitsa komanso malangizo amene amapereka akamatsogolera mpingo wa Chikhristu masiku ano. Watiphunzitsanso zimene tingachite kuti tizisangalatsa Mulungu. Tonsefe tingathe kupindula ndi imfa ya Yesu, yomwe ili ngati kuvulazidwa chidendene. Yesu ataukitsidwa anapereka mtengo wa magazi ake monga nsembe yangwiro yomwe ‘inatiyeretsa ku machimo wonse.’ (1 Yoh. 1:7) Panopa iye ndi Mfumu yaulemerero yomwe singafe. Posachedwapa, Yesu aphwanya mutu wa njoka. (Gen. 3:15) Anthu okhulupirika adzasangalalatu kwambiri Satana akadzawonongedwa. Mpaka pa nthawiyo, sitiyenera kufooka. Mulungu wathu ndi wodalirika. Iye adzapereka madalitso osaneneka kwa “mitundu yonse ya padziko lapansi.” w22.07 18 ¶13; 19 ¶19
Lachitatu, June 12
Sitingapewe kukumana ndi mavuto ngati amenewa.—1 Ates. 3:3.
Tiyenera kukhala okonzeka kusintha pa nkhani ya zolinga zimene timadziikira. Chifukwa chiyani? Chifukwa sitingathe kulamulira zinthu zonse zimene zimachitika pa moyo wathu. Mwachitsanzo, mtumwi Paulo anathandiza kukhazikitsa mpingo watsopano mumzinda wa Tesalonika. Koma otsutsa anamukakamiza kuti achoke mumzindawo. (Mac. 17:1-5, 10) Paulo akanakhalabe komweko, akanaika abale akewo pangozi. Komabe iye sanasiye kuwathandiza. M’malomwake anavomereza kusinthaku. Pambuyo pake anatumiza Timoteyo kuti akathandize Akhristu atsopanowo kukhala ndi chikhulupiriro cholimba. (1 Ates. 3:1, 2) Akhristu a ku Tesalonika anasangalala kwambiri. Tingaphunzire zambiri pa zimene zinachitikira Paulo ku Tesalonika. Tingamafune titachita utumiki winawake koma zinthu zina pa moyo wathu zingatilepheretse kukwaniritsa cholinga chathucho. (Mlal. 9:11) Ngati umu ndi mmene zilili ndi inu, muzikhala okonzeka kusankha cholinga china chimene mungachikwaniritse. w22.04 25-26 ¶14-15
Lachinayi, June 13
Wosangalala ndi munthu amene akupirira mayesero.—Yak. 1:12.
Yehova amatilimbikitsa potipatsa chiyembekezo cham’tsogolo. Taonani zina zomwe Baibulo limanena zomwe zingatilimbikitse tikamakumana ndi mayesero. M’Malemba, Yehova amatitsimikizira kuti china chilichonse kuphatikizapo mayesero aakulu sichidzatha “kutisiyanitsa ndi chikondi [chake].” (Aroma 8:38, 39) Amatitsimikiziranso kuti iye “ali pafupi ndi onse amene amamuitana” m’pemphero. (Sal. 145:18) Yehova amatiuza kuti tikamamudalira tingathe kupirira mayesero aliwonse ndipo tikhoza kumasangalalabe ngakhale kuti tikuvutika. (1 Akor. 10:13; Yak. 1:2) Mawu a Mulungu amatikumbutsanso kuti mayesero athu ndi a kanthawi poyerekeza ndi madalitso osatha omwe Mulungu amatipatsa. (2 Akor. 4:16-18) Yehova amatipatsa chiyembekezo chotsimikizika chakuti adzachotsa Satana Mdyerekezi, yemwe amayambitsa mavuto komanso onse amene amatsatira njira zake zoipa. (Sal. 37:10) Kodi mwaloweza mavesi ena a m’Baibulo omwe angadzakuthandizeni kupirira mayesero m’tsogolo? w22.08 11 ¶11
Lachisanu, June 14
Pitirizani kuganizira zinthu [zimenezi].—Afil. 4:8.
Kodi mumada nkhawa kuti mwina simungapitirize kutsatira mfundo za Yehova zachilungamo tsiku ndi tsiku komanso chaka chilichonse? Yehova amatitsimikizira kuti chilungamo chathu “chidzakhala ngati mafunde a m’nyanja.” (Yes. 48:18) Tayerekezani kuti mwaima mphepete mwa nyanja yaikulu ndipo mukuona mafunde akubwera mosalekeza. Kodi mungamadere nkhawa kuti mwina tsiku lina mafundewo adzasiya? Ayi. Chifukwa mukudziwa kuti mafundewo akhala akuchitika panyanjapo kwa zaka zambiri ndipo apitirizabe. Chilungamo chanu chingafanane ndi mafunde a nyanjayo. Mukafuna kusankha zochita pa nkhani ina yake, choyamba muziganizira kaye zimene Yehova angafune kuti muchite. Ndiyeno muzichita zimenezo. Kaya zimene mukufunika kusankha zitakhala zovuta bwanji, nthawi zonse Atate wanu yemwe ndi wachikondi adzakuthandizani kuti musatekeseke komanso kuti tsiku lililonse muzichita zinthu zogwirizana ndi mfundo zake zolungama.—Yes. 40:29-31. w22.08 30 ¶15-17
Loweruka, June 15
Zaka 1,000 zimenezi zikadzangotha, Satana adzamasulidwa m’ndende yake.—Chiv.20:7.
Zikadzatha zaka 1,000, Satana adzamasulidwa ndipo adzayesa kusocheretsa anthu angwiro. Pa nthawi ya mayeserowa, anthu onse angwiro adzakhala ndi mwayi wosonyeza mbali yomwe ali, pa nkhani ya dzina la Mulungu ndi ulamuliro wake. (Chiv. 20:8-10) Zimene aliyense adzachite pa nthawiyi, zidzasonyeza ngati ali woyenera kuti dzina lake lipitirizebe kukhala m’buku la moyo. Anthu ena omwe chiwerengero chawo sichikudziwika adzakhala ngati Adamu ndi Hava ndipo adzakana ulamuliro wa Yehova. Ndiye kodi n’chiyani chidzawachitikire? Lemba la Chivumbulutso 20:15, limatiuza kuti: “Aliyense amene sanapezeke atalembedwa m’buku la moyo anaponyedwa m’nyanja yamoto.” Choncho anthu osamverawa adzawonongedwa kuti asakhalekonso. Koma anthu ambiri angwiro adzapambana mayesero omalizawa. w22.09 23-24 ¶15-16
Lamlungu, June 16
Mukapanda kudulidwa mogwirizana ndi mwambo wa Mose, simungapulumuke.—Mac. 15:1.
Ena mumpingo wa m’nthawi ya atumwi ankafuna kuti Akhristu omwe sanali Ayuda azidulidwa, mwina poopa kutsutsidwa ndi Ayuda ena. (Agal. 6:12) Mtumwi Paulo sanagwirizane ndi maganizo amenewa koma m’malo moumirira kuti anthuwo atsatire maganizo ake, modzichepetsa, iye anapempha malangizo kwa atumwi ndi akulu ku Yerusalemu. (Mac. 15:2) Zimene anachitazi zinathandiza Akhristuwo kuti azisangalala ndipo mumpingo munali mtendere. (Mac. 15:30, 31) Ngati pabuka kusamvana pa nkhani inayake, timalimbikitsa mtendere popempha malangizo kwa abale amene Yehova wawasankha kuti azitsogolera mumpingo. Nthawi zambiri malangizo ochokera m’Baibulo tingawapeze m’mabuku athu kapena m’malangizo ena operekedwa ndi gulu. Tikamayesetsa kutsatira malangizowa, m’malo moumirira maganizo athu, timathandiza kuti mumpingo mukhale mtendere. w22.08 22 ¶8-9
Lolemba, June 17
Mnzako weniweni amakusonyeza chikondi nthawi zonse.—Miy. 17:17.
Tonsefe nthawi zina timafuna kuuza mnzathu wapamtima mmene tikumvera. Koma nthawi zina kuchita zimenezi kungakhale kovuta. N’kutheka kuti sitinazolowere kufotokozera ena mmene tikumvera ndipo tingakhumudwe ngati pambuyo pake titadziwa kuti mnzathu wafotokozera ena zomwe tinamuuza. Komabe timayamikira munthu wina akatisungira chinsinsi pa nkhani ina yake. Akulu omwe amadziwika kuti amasunga chinsinsi ali ngati “malo obisalirapo mphepo, malo obisalirapo mvula yamkuntho” kwa abale awo. (Yes. 32:2) Timadziwa kuti tingamasuke kuwafotokozera nkhani iliyonse ndipo timakhulupirira kuti sauza aliyense. Sitimawakakamiza kuti atifotokozere nkhani zachinsinsi. Kuwonjezera pamenepo timayamikira akazi a akulu chifukwa sakakamiza amuna awo kuti awauze nkhani zimene sakuyenera kuzidziwa. Kunena zoona zimakhala bwino ngati mkazi wa mkulu sanafotokozeredwe nkhani zachinsinsi zokhudza abale ndi alongo. w22.09 11 ¶10-11
Lachiwiri, June 18
Ine ndine Mulungu. Ndidzakwezedwa pakati pa mitundu ya anthu.—Sal. 46:10.
Sitikukayikira kuti Yehova adzapulumutsa atumiki ake okhulupirika pa nthawi ya “chisautso chachikulu.” (Mat. 24:21; Dan. 12:1) Iye adzachita zimenezi pamene mgwirizano wa mayiko wotchedwa Gogi wa ku Magogi udzaukire atumiki a Yehova okhulupirika padziko lonse. Ngakhale mgwirizanowo utadzaphatikizapo mayiko onse 193, omwe ali m’bungwe la United Nations, iwo sadzatha kulimbana ndi Wamkulukulu ndi gulu lake lakumwamba. Yehova akulonjeza kuti: “Ndidzasonyeza mphamvu zanga, komanso ndidzasonyeza kuti ndine Mulungu woyera ndipo ndidzachititsa kuti anthu ambiri a mitundu ina andidziwe. Iwo adzadziwa kuti ine ndine Yehova.” (Ezek. 38:14-16, 23) Kuukira kwa Gogi kudzayambitsa nkhondo ya Aramagedo, pomwe Yehova adzawononge “mafumu a dziko lonse lapansi.” (Chiv. 16:14, 16; 19:19-21) Mosiyana ndi zimenezi, “owongoka mtima okha ndi amene adzakhale padziko lapansi, ndipo opanda cholakwa ndi amene adzatsalemo.”—Miy. 2:21. w22.10 16-17 ¶16-17
Lachitatu, June 19
[Mulungu] amafuna kuti anthu osiyanasiyana apulumuke n’kukhala odziwa choonadi molondola.—1 Tim. 2:4.
Sitidziwa za mumtima mwa munthu koma Yehova yekha ndi amene “amafufuza zolinga zake.” (Miy. 16:2) Iye amakonda anthu onse posatengera chikhalidwe chawo kapena mmene anakulira. Ndipotu Yehova amatilimbikitsa kuti ‘titsegule kwambiri mitima yathu.’ (2 Akor. 6:13) Ifenso timafunitsitsa kuti tizikonda abale ndi alongo athu onse osati kuwaweruza. Zimenezi zikutanthauzanso kuti sitiyenera kuweruza anthu amene si abale ndi alongo. Kodi inuyo mungaweruze wachibale wanu yemwe si wa Mboni kuti, “Ameneyu sangayambe choonadi”? Ayi. Kuchita zimenezi kungakhale kudzikuza ndiponso kudziona kuti ndinu wabwino kuposa iyeyo. Yehova akupitirizabe kupereka mwayi kwa “anthu kwina kulikonse” woti alape. (Mac. 17:30) Nthawi zonse muzikumbukira kuti si chilungamo kumadziona kuti ndinu wolungama kwambiri kuposa ena. Tikamakonda mfundo za Yehova zachilungamo, timakhala osangalala ndipo timalimbikitsa ena kuti azitikonda komanso azikonda Mulungu wathu. w22.08 31 ¶20-22
Lachinayi, June 20
Adzadziwabe ndithu kuti pakati pawo panali mneneri.—Ezek. 2:5.
Tiziyembekezera kuti tingatsutsidwe pamene tikugwira ntchito yathu yolalikira. Ndipo m’tsogolomu tikhoza kudzatsutsidwa kwambiri. (Dan. 11:44; 2 Tim. 3:12; Chiv. 16:21) Komabe tingakhale otsimikiza kuti Yehova adzatithandiza. N’chifukwa chiyani tikutero? Nthawi zonse Yehova wakhala akuthandiza atumiki ake kukwaniritsa utumiki womwe apatsidwa, kaya utumikiwo ukhale wovuta bwanji. Taganizirani za mneneri Ezekieli, yemwe ankalalikira kwa Ayuda omwe anali ku ukapolo ku Babulo. Kodi anthu a m’gawo limene Ezekieli ankalalikira anali otani? Yehova anafotokoza kuti iwo anali “a nkhope zamwano,” “amakani” ndiponso ‘opanduka.’ Iwo anali ovulaza ngati minga komanso oopsa ngati zinkhanira. Mpake kuti Yehova anauza Ezekieli mobwerezabwereza kuti: “Usaope.” (Ezek. 2:3-6) Ezekieli anakwanitsa kugwira ntchito yolalikira imene anapatsidwa chifukwa (1) anatumidwa ndi Yehova, (2) ankathandizidwa ndi mzimu woyera ndipo (3) ankalimbikitsidwa ndi mawu a Mulungu. w22.11 2 ¶1-2
Lachisanu, June 21
Tsiku limene udzadye, udzafa ndithu.—Gen. 2:17.
Yehova analenga zamoyo zina zonse padzikoli kuti zizikhala ndi moyo kwa kanthawi, kupatulapo anthu. Iye anawapatsa chiyembekezo choti asadzafe. Yehova anatilenganso ndi mtima wofunitsitsa kuti tizikhala ndi moyo mpaka kalekale. Ponena za anthu, Baibulo limanena kuti Mulungu “anapatsa anthu mtima wofuna kukhala ndi moyo mpaka kalekale.” (Mlal. 3:11) Ichi ndi chifukwa chimodzi chomwe chimatichititsa kuti tiziona imfa monga mdani. (1 Akor. 15:26) Tikadwala kwambiri, kodi timangokhala n’kumadikira kuti tife? Ayi. Nthawi zambiri timapita kukaonana ndi dokotala kapenanso kumwa mankhwala kuti tichire. Ndipotu timachita zonse zomwe tingathe kuti tisafe. Komanso munthu yemwe timamukonda akamwalira, kaya wamkulu kapena wamng’ono, timamva kupweteka ndiponso chisoni kwa nthawi yaitali. (Yoh. 11:32, 33) N’zoonekeratu kuti Mlengi wathu wachikondi sakanatilenga kuti tizitha kuphunzira kapena kukhala ndi mtima wofunitsitsa kukhala ndi moyo mpaka kalekale, zikanakhala kuti si cholinga chake kuti anthu azikhala ndi moyo wosatha. w22.12 3 ¶5; 4 ¶7
Loweruka, June 22
Abale anu padziko lonse akukumananso ndi mavuto ngati omwewo.—1 Pet. 5:9.
Abale ndi alongo ambiri m’nthawi yovutayi akulimbana ndi mavuto monga kudwala, kuchita mantha kapenanso kumadziona kuti ali okhaokha. Muziyesetsa kulankhulana ndi abale ndi alongo anu. Mwina mliri ungachititse kuti tizikhala motalikirana ngakhalenso ndi Akhristu anzathu. Pa nthawi ngati imeneyi tingamamve ngati mmene mtumwi Yohane anamvera. Iye ankafuna kuonana ndi Gayo, yemwe anali mnzake komabe ankadziwa kuti kwa kanthawi sizikanatheka kuti aonane naye. (3 Yoh. 13, 14) Komabe anachita zomwe akanakwanitsa ndipo analembera Gayo kalata. Ngati inunso n’zosatheka kuti muonane ndi abale ndi alongo anu mungayese kulankhula nawo kudzera m’njira zina zosiyanasiyana. Mukamalankhula ndi Akhristu anzanu mungamamve kuti ndinu otetezeka komanso mudzakhala ndi mtendere. Mukakhala ndi nkhawa kwambiri muzilankhulana ndi akulu omwe angakulimbikitseni mwachikondi.—Yes. 32:1, 2. w22.12 17-18 ¶6-7
Lamlungu, June 23
Zitatero, mbuye wake wa Yosefe anamutenga n’kukamusiya kundende ya akaidi a mfumu kuti akamutsekere. —Gen. 39:20.
Baibulo limasonyeza kuti kwa kanthawi mapazi a Yosefe anali m’matangadza komanso khosi lake linamangidwa ndi unyolo. (Sal. 105:17, 18) Zinthu zinkangoipiraipira pa moyo wake. Anachoka pokhala kapolo wodalirika n’kufika pokhala mkaidi wamba. Kodi munakumanapo ndi mavuto omwe ankaipiraipira ngakhale kuti munapemphera mochokera pansi pa mtima? Zimenezi zingachitike. Yehova satiteteza kuti tisakumane ndi mavuto m’dziko lolamulidwa ndi Satanali. (1 Yoh. 5:19) Komabe mungakhale otsimikiza kuti Yehova akudziwa zimene mukukumana nazo ndipo amakuderani nkhawa. (Mat. 10:29-31; 1 Pet. 5:6, 7) Ndipotu iye amalonjeza kuti: “Sindidzakusiyani kapena kukutayani ngakhale pang’ono.” (Aheb. 13:5) Yehova angakuthandizeni kupirira ngakhale pamene zikuoneka kuti mwasowa mtengo wogwira. w23.01 16 ¶7-8
Lolemba, June 24
Mulungu wathu . . . [amakhululuka] ndi mtima wonse.—Yes. 55:7.
Malemba amatitsimikizira kuti Mulungu sadzatisiya ngakhale pamene talakwitsa zinthu. Aisiraeli ankachimwira Yehova mobwerezabwereza komabe akalapa kuchokera pansi pa mtima, iye ankawakhululukira. Akhristu a m’nthawi ya atumwi ankadziwanso kuti Yehova ankawakonda kwambiri. Mouziridwa, mtumwi Paulo analimbikitsa Akhristu anzake kuti ‘akhululukire ndi mtima wonse ndi kutonthoza’ munthu yemwe ankachita tchimo lalikulu koma kenako analapa. (2 Akor. 2:6, 7; 1 Akor. 5:1-5) N’zochititsa chidwi kuti Yehova sankasiya atumiki ake chifukwa choti amuchimwira. M’malomwake, ankawathandiza mwachikondi, kuwawongolera komanso kuwapempha kuti abwerere kwa iye. Masiku anonso iye amalonjeza kuti adzachita zimenezi kwa anthu onse omwe alapa. (Yak. 4:8-10) Baibulo limatiuza za nzeru, chilungamo komanso chikondi cha Mulungu. Bukuli limatitsimikizira kuti Yehova amafuna kuti timudziwe komanso tikhale anzake. w23.02 7 ¶16-17
Lachiwiri, June 25
Mukuchita bwino kuwaganizira mozama.—2 Pet. 1:19.
Pali zifukwa zabwino zotichititsa kukhala ndi chidwi ndi mmene zochitika za m’dzikoli zikukwaniritsira maulosi a m’Baibulo. Mwachitsanzo, Yesu anatchula zinthu zosiyanasiyana zomwe zimatithandiza kudziwa kuti mapeto a dziko la Satanali ali pafupi. (Mat. 24:3-14) Mtumwi Petulo anatilimbikitsa kuti tizichita chidwi ndi mmene maulosi akukwaniritsidwira n’cholinga choti chikhulupiriro chathu chikhale cholimba. (2 Pet. 1:20, 21) Iye amafuna kuti tizikhala ndi maganizo oyenera tikamawerenga maulosi a m’Baibulo. Anatilimbikitsa kuti ‘tizikumbukira nthawi zonse kubwera kwa tsiku la Yehova.’ (2 Pet. 3:11-13) Chifukwa chiyani? Osati chifukwa choti tikungofuna kudziwa “tsiku ndi ola” limene Yehova adzamenye nkhondo ya Aramagedo. Koma chifukwa chakuti tikufuna kugwiritsa ntchito nthawi yomwe yatsalayi kuti tikhale anthu ‘akhalidwe loyera ndipo tizichita ntchito zosonyeza kuti ndife odzipereka kwa Mulungu.’ (Mat. 24:36; Luka 12:40) Timafuna kuchita zoyenera komanso kuonetsetsa kuti tikuchita khama potumikira Yehova chifukwa chakuti timamukonda kwambiri. Kuti zimenezi zitheke, tiyenera kumasamala ndi zimene timachita. w23.02 16 ¶4, 6
Lachitatu, June 26
Ndili ndi nkhosa zina . . . , zimenezonso ndiyenera kuzibweretsa.—Yoh. 10:16.
Pali zimene a “nkhosa zina” ayenera kuchita panopa kuti adzakhale m’Paradaiso. Tiyenera kusonyeza kuti tili kumbali ya Yesu. Mwachitsanzo, timasonyeza kuti timamukonda pa zimene timachitira abale ake odzozedwa. Yesu ananena kuti adzaweruza anthu potengera mmene anachitira ndi abale akewa. (Mat. 25:31-40) Tingawathandize tikamagwira nawo mwakhama ntchito yolalikira ndi kuphunzitsa anthu. (Mat. 28:18-20) Sitikuyenera kuyembekezera mpaka tidzalowe m’Paradaiso kuti tidzayambe kukhala mtundu wa anthu amene Yehova akufuna kuti adzakhalemo. Panopa tiziyesetsa kukhala oona mtima mu zolankhula komanso zochita ndiponso tizikhala ndi makhalidwe abwino. Tiyeneranso kukhala okhulupirika kwa Yehova, mwamuna kapena mkazi wathu komanso Akhristu anzathu. Tikamayesetsa kutsatira mfundo za Mulungu panopa pomwe tili m’dziko loipali, zidzakhalanso zosavuta kuzitsatira tili m’Paradaiso. Tingayambiretu panopa kukulitsa luso komanso makhalidwe omwe adzafunike pa nthawiyo. w22.12 11-12 ¶14-16
Lachinayi, June 27
Amene amandikonda, Atate wanga adzamukondanso.—Yoh. 14:21.
Timakonda Yesu monga Mfumu yathu chifukwa ndi Wolamulira wabwino kwambiri. Yehova anaphunzitsa Mwana wakeyu ndipo anamuika kuti azilamulira. (Yes. 50:4, 5) Ganiziraninso chikondi chololera kuvutikira ena chimene Yesu anasonyeza. (Yoh. 13:1) Monga Mfumu yanu, Yesu ndi woyenerera kuti muzimukonda. Iye anafotokoza kuti anthu amene amamukondadi, omwe amawatchula kuti ndi anzake, amasonyeza chikondicho pomvera malamulo ake. (Yoh. 14:15; 15:14, 15) Ndi mwayitu waukulu kukhala anzake a Mwana wa Yehova. Timadziwa kuti Yesu ndi wodzichepetsa ndipo amatsanzira ndendende makhalidwe a Atate wake. Munaphunzira kuti anadyetsa anjala, analimbikitsa ofooka komanso anachiritsa odwala. (Mat. 14:14-21) Mwaonanso mmene amatsogolerera mpingo wake masiku ano. (Mat. 23:10) Ndipo mukudziwa kuti adzachita zambiri kuposa pamenepo m’tsogolomu monga Mfumu ya Ufumu wa Mulungu. Ndiye kodi mungasonyeze bwanji kuti mumamukonda? Mungachite zimenezo potengera chitsanzo chake. Mungayambe ndi kudzipereka kwa Yehova kenako n’kubatizidwa. w23.03 4 ¶8, 10
Lachisanu, June 28
Kwezani maso anu kumwamba ndipo muone. Kodi ndi ndani amene analenga zinthu zimenezi?—Yes. 40:26.
Yehova anadzaza kumwamba, dziko lapansi komanso nyanja ndi zinthu zambiri zomwe zingatiphunzitse zokhudza iye. (Sal. 104:24, 25) Ndipo tangoganizani mmene Mulungu anatilengera anthufe. Anatilenga m’njira yoti tizitha kusangalala ndi zinthu zokongola. Anatilenganso m’njira yoti tizitha kusangalala ndi zinthu zosiyanasiyana poona, kumva, kulawa, kununkhiza komanso kukhudza. Baibulo limatiuza chifukwa china chotichititsa kuti tizichita chidwi ndi chilengedwe. Chilengedwe chimatiphunzitsa zokhudza makhalidwe a Yehova. (Aroma 1:20) Mwachitsanzo, taganizirani zinthu zochititsa chidwi zomwe timaona m’chilengedwe. Kodi sizimatithandiza kudziwa kuti Mulungu ndi wanzeru? Taganiziraninso zakudya zosiyanasiyana zomwe timasangalala nazo. Umenewu ndi umboni woonekeratu woti Yehova amakonda anthu. Tikamamvetsa makhalidwe ake kudzera m’zinthu zimene anapanga timafika pomudziwa bwino kwambiri komanso timakhala naye pa ubwenzi wolimba. w23.03 16 ¶4-5
Loweruka, June 29
Mawu anu onse ndi choonadi chokhachokha.—Sal. 119:160.
Pamene zinthu m’dzikoli zikuipiraipira, kukhulupirira kwathu choonadi kudzayesedwa. Anthu ena adzayesa kutichititsa kuti tiyambe kukayikira ngati Baibulo lili loona kapenanso ngati Yehova anasankha anthu oti azitsogolera anthu ake masiku ano. Koma ngati timakhulupirira kuti Mawu a Yehova nthawi zonse ndi oona tidzatha kukana misampha yoyesa chikhulupiriro chathuyi. ‘Tidzatsimikiza mtima kumvera malamulo [a Yehova] nthawi zonse, mpaka tidzamwalire.’ (Sal. 119:112) ‘Sitidzachita manyazi’ kuuza ena zokhudza choonadi komanso kuwalimbikitsa kuti azichita zinthu mogwirizana ndi choonadicho. (Sal. 119:46) Tidzatha kupirira ‘moleza mtima ndiponso mwachimwemwe’ mavuto aakulu, kuphatikizapo kuzunzidwa. (Akol. 1:11; Sal. 119:143, 157) Choonadi chimatithandiza kukhala odekha ndiponso chimatiphunzitsa mmene tiyenera kukhalira m’dzikoli. Ndiponso chimatipatsa chiyembekezo cha tsogolo labwino mu Ufumu wa Mulungu. w23.01 7 ¶16-17
Lamlungu, June 30
Ndikukupatsani lamulo latsopano, kuti muzikondana. Mofanana ndi mmene ine ndakukonderani, inunso muzikondana choncho.—Yoh. 13:34.
Pa usiku wake womaliza, Yesu anapempherera ophunzira ake kwa nthawi yaitali, kupempha Atate wake kuti “muwateteze kwa woipayo.” (Yoh. 17:15) Apatu Yesu anasonyeza chikondi chachikulu. Iye ankayembekezera kukumana ndi mayesero aakulu, komabe ankadera nkhawa za atumwi ake. Potsanzira Yesu, ifenso sitimangoganizira zofuna zathu zokha. M’malomwake, nthawi zonse timapempherera abale ndi alongo athu. Tikamachita zimenezi timakhala tikumvera lamulo la Yesu lakuti tizikondana ndipo timamusonyeza Yehova kuti timakonda kwambiri Akhristu anzathu. Kupempherera abale ndi alongo athu n’kothandiza kwambiri. Mawu a Mulungu amatiuza kuti “pembedzero la munthu wolungama limagwira ntchito mwamphamvu kwambiri.” (Yak. 5:16) Timafunika kupempherera Akhristu anzathu chifukwa nawonso akukumana ndi mavuto ambiri. w22.07 23-24 ¶13-15