Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • es24 tsamba 67-77
  • July

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • July
  • Kuphunzira Malemba Tsiku ndi Tsiku—2024
  • Timitu
  • Lolemba, July 1
  • Lachiwiri, July 2
  • Lachitatu, July 3
  • Lachinayi, July 4
  • Lachisanu, July 5
  • Loweruka, July 6
  • Lamlungu, July 7
  • Lolemba, July 8
  • Lachiwiri, July 9
  • Lachitatu, July 10
  • Lachinayi, July 11
  • Lachisanu, July 12
  • Loweruka, July 13
  • Lamlungu, July 14
  • Lolemba, July 15
  • Lachiwiri, July 16
  • Lachitatu, July 17
  • Lachinayi, July 18
  • Lachisanu, July 19
  • Loweruka, July 20
  • Lamlungu, July 21
  • Lolemba, July 22
  • Lachiwiri, July 23
  • Lachitatu, July 24
  • Lachinayi, July 25
  • Lachisanu, July 26
  • Loweruka, July 27
  • Lamlungu, July 28
  • Lolemba, July 29
  • Lachiwiri, July 30
  • Lachitatu, July 31
Kuphunzira Malemba Tsiku ndi Tsiku—2024
es24 tsamba 67-77

July

Lolemba, July 1

Ukhale chitsanzo kwa okhulupirika pa zimene umalankhula.—1 Tim. 4:12.

Kulankhula ndi mphatso imene Mulungu wathu wachikondi anatipatsa. Komabe, mphatso yakulankhula inagwiritsidwa ntchito molakwika. Satana Mdyerekezi ananamiza Hava ndipo zimenezi zinachititsa kuti anthu achimwe komanso asakhale angwiro. (Gen. 3:​1-4) Atalakwitsa zinthu, Adamu anagwiritsa ntchito molakwika lilime lake pamene anaimba mlandu Hava komanso Yehova. (Gen. 3:12) Kaini anauza Yehova zabodza atapha m’bale wake Abele. (Gen. 4:9) Masiku ano n’zovuta kupeza mafilimu amene alibe mawu oipa. Ana amamva mawuwa akakhala kusukulu ndipo akuluakulu amawamva akakhala kuntchito. Ngati sitingasamale tingayambe kuzolowera kumva mawu oipa mpaka nafenso kuyamba kuwagwiritsa ntchito. N’zoona kuti monga Akhristu, timafuna kusangalatsa Yehova ndipo zimenezi zimaphatikizapo kupewa mawu alionse oipa. Timafuna kugwiritsa ntchito mphatso yamtengo wapatali yakulankhula m’njira yabwino kwambiri polemekeza Mulungu. w22.04 4 ¶1-3

Lachiwiri, July 2

Simungathe kutumikira Mulungu ndi Chuma nthawi imodzi.—Mat. 6:24.

Yesu ankaona moyenera nkhani yokhala ndi zinthu. Ankasangalala ndi zakudya komanso zakumwa. (Luka 19:​2, 6, 7) Pa nthawi ina iye anasandutsa madzi kukhala vinyo wabwino kwambiri ndipo ichi chinali chozizwitsa chake choyamba. (Yoh. 2:​10, 11) Ndipo pa tsiku lomwe anafa anavala chovala chamtengo wapatali. (Yoh. 19:​23, 24) Komabe Yesu sanalole kuti kukhala ndi zinthu kukhale chinthu chofunika kwambiri pa moyo wake. Yesu anaphunzitsa kuti tikamafunafuna Ufumu choyamba, Yehova adzaonetsetsa kuti tili ndi zonse zimene timafunikira. (Mat. 6:​31-33) Abale ndi alongo athu ambiri zinthu zawayendera bwino chifukwa chogwiritsa ntchito nzeru zochokera kwa Mulungu pa nkhani ya ndalama. Taganizirani chitsanzo cha m’bale wina yemwe sali pabanja dzina lake Daniel. Iye anati: “Ndili wachinyamata, ndinasankha kuti zinthu zofunika kwambiri kwa ine zikhale zokhudza kulambira.” Popeza kuti amakhala moyo wosalira zambiri, Daniel wakhala akugwiritsa ntchito nthawi ndi luso lake pochita zambiri m’gulu la Yehova. Iye anawonjezera kuti: “Yehova wandipatsa chimwemwe chochuluka kuposa chomwe ndikanakhala nacho chifukwa chokhala ndi ndalama zambiri.” w22.05 21-22 ¶6-7

Lachitatu, July 3

[Yehova] anakuitanani kuti muchoke mumdima ndipo anakulandirani m’kuwala kwake kodabwitsa.—1 Pet. 2:9.

Tingasonyeze kuti timakonda choonadi pophunzira Baibulo nthawi zonse komanso mabuku othandiza kuphunzira Baibulo. Ndipotu kaya takhala m’choonadi kwa nthawi yaitali bwanji, nthawi zonse pamakhala zambiri zoti tiphunzire. Kuphunzira kumafuna khama, koma n’kothandiza kwambiri. Si tonse amene timakonda kuwerenga ndi kuphunzira. Koma Yehova amatilimbikitsa kuti ‘tizifunafuna’ komanso ‘kufufuza’ kuti timvetse bwino mfundo zozama za choonadi. (Miy. 2:​4-6) Tikamachita zimenezi, nthawi zonse timapindula. Pofotokoza zimene amachita akamawerenga Baibulo, Corey ananena kuti amaganizira zimene zili pavesi lililonse palokha. Iye anafotokoza kuti: “Ndimawerenga mawu a m’munsi aliwonse komanso kufufuza mavesi ena ofotokoza mfundo yofanana ndi ya vesilo ndiponso zinthu zina zowonjezereka. . . . Kugwiritsa ntchito njira imeneyi kumandithandiza kuti ndiphunzire zambiri.” Kaya timagwiritsa ntchito njira imeneyi kapena ina, timasonyeza kuti timakonda choonadi tikamapatula nthawi yathu komanso kuchita khama kuti tichiphunzire.—Sal. 1:​1-3. w22.08 17 ¶13; 18 ¶15-16

Lachinayi, July 4

Ndinali pambali pake monga mmisiri waluso. Iye ankasangalala kwambiri ndi ine tsiku ndi tsiku. Ndinkakhala wosangalala pamaso pake nthawi zonse.—Miy. 8:30.

Ali padzikoli, Yesu anagwiritsa ntchito chilengedwe pophunzitsa ophunzira ake zokhudza Atate wake. Taganizirani mfundo imodzi yomwe anaphunzitsa. Yehova amakonda aliyense. Mu ulaliki wake wapaphiri, Yesu anafotokozera ophunzira ake zokhudza dzuwa ndi mvula, zinthu zimene anthu ambiri saziganizira kwenikweni. Zinthu ziwirizi ndi zofunika kwambiri kuti padzikoli pakhale zamoyo. Yehova akanatha kusankha kuti asamapereke zinthuzi kwa anthu omwe samutumikira. M’malomwake, mwachikondi, iye amapereka dzuwa komanso mvula kwa anthu onse. (Mat. 5:​43-45) Yesu anagwiritsa ntchito mfundo imeneyi pophunzitsa ophunzira ake kuti Yehova amafuna kuti tizikonda anthu onse. Nthawi zonse tikaona kuwala kwa dzuwa kosangalatsa komanso kamvula kotsitsimula tizikumbukira kuti Yehova amakonda anthu onse. Chitsanzo chake chizitilimbikitsa kuti ifenso tizisonyeza chikondi ngati chimenechi polalikira kwa anthu onse. w23.03 17 ¶9-10

Lachisanu, July 5

Ndinadabwa kwambiri.—Chiv. 17:6.

Kodi mtumwi Yohane anadabwa ndi chiyani? Iye anaona mkazi atakwera pachilombo chofiira kwambiri. Mkaziyu akufotokozedwa kuti ndi “hule lalikulu” ndipo akutchedwa kuti “Babulo Wamkulu.” Iye anachita “chiwerewere” ndi “mafumu a dziko lapansi.” (Chiv. 17:​1-5) Kodi “Babulo Wamkulu” ndi ndani? Mkaziyu sangaimire ulamuliro wina wake wapadzikoli chifukwa akufokozedwa kuti anachita dama ndi olamulira a m’dzikoli. (Chiv. 18:9) Ndipotu amayesetsa kuwalamulira, zomwe zili ngati kukwera pamsana pawo. Kuwonjezera pamenepa, sangaimire amalonda adyera a m’dziko la Satanali. Iwo amafotokozedwa kale kuti ndi “amalonda oyendayenda.” (Chiv. 18:​11, 15, 16) Mzinda wakale wa Babulo unali likulu la kulambira konyenga. Choncho Babulo Wamkulu ayenera kuimira kulambira konyenga kulikonse. Ndipotu iye akuimira zipembedzo zonse zonyenga.—Chiv. 17:​5, 18. w22.05 11 ¶14-16

Loweruka, July 6

Mdani wanu Mdyerekezi akuyendayenda ngati mkango wobangula, kuti ameze winawake.—1 Pet. 5:8.

Nthawi zina mayi angamadzifunse ngati ana ake adzasankhe kutumikira Yehova. Ndipotu makolo amadziwa mavuto amene ana amakumana nawo m’dziko la Satanali. Kuwonjezera pamenepo, vuto lina ndi lakuti azimayi ambiri amalera okha ana kapenanso amuna awo salambira Yehova. Sikuti ndi anthu a m’banja losiyana zipembedzo okha omwe amakumana ndi mavuto pothandiza ana kuti azikonda Yehova. Ngakhale pamene makolo onse ali m’choonadi, zikhoza kukhala zovuta kuphunzitsa ana mowafika pa mtima kuti akhale atumiki a Yehova okhulupirika. Komabe kaya zinthu zili bwanji, musamade nkhawa kwambiri. Yehova adzakuthandizani. Bwanji osafunsa makolo ena odziwa zambiri kuti akuthandizeni kudziwa mmene mungagwiritsire ntchito zinthu zophunzitsira zomwe tili nazo pa Kulambira kwa Pabanja? (Miy. 11:14) Yehova angakuthandizeninso kuti muzilankhulana bwino ndi ana anu. Muzimupempha kuti akuthandizeni kudziwa zimene zili mumtima ndi m’maganizo mwawo.—Miy. 20:5. w22.04 17 ¶4, 7; 18 ¶9

Lamlungu, July 7

Ine ndikupitiriza kupemphera kuti chikondi chanu chipitirize kukula kwambiri, limodzi ndi kudziwa zinthu molondola komanso kuzindikira zinthu bwino kwambiri.—Afil. 1:9.

Tingayambe kukonda kwambiri Yehova ngati titadziwa bwino Mwana wake, yemwe ankasonyeza bwino kwambiri makhalidwe a Atate wake. (Aheb. 1:3) Njira yabwino imene tingadziwire Yesu, ndi kuphunzira mabuku 4 a Uthenga Wabwino. Ngati mulibe chizolowezi chowerenga Baibulo tsiku lililonse, bwanji osayamba panopa? Mukamawerenga nkhani zokhudza Yesu, muziganizira kwambiri makhalidwe ake. Iye anali wofikirika moti nthawi ina ananyamula ana m’manja mwake. (Maliko 10:​13-16) Ankachititsa ophunzira ake kukhala omasuka moti akamacheza nawo, iwo sankaopa kufotokoza mmene ankamvera. (Mat. 16:22) Pochita zimenezi, Yesu ankatsanzira Atate wake wakumwamba. Yehova nayenso ndi wofikirika. Tikhoza kupemphera kwa iye ndipo tikamapemphera tingamuuze zonse zamumtima mwathu. Ndife otsimikiza kuti sangatiweruze chifukwa cha zimenezo. Iye amatikonda komanso amatidera nkhawa.—1 Pet. 5:7. w22.08 3 ¶4-5

Lolemba, July 8

Inu Yehova ndinu wabwino ndipo ndinu wokonzeka kukhululuka.—Sal. 86:5.

Monga Mlengi wathu, Yehova amadziwa chilichonse chokhudza anthufe. Ndiye tangoganizani, amadziwa chilichonse chokhudza munthu aliyense padzikoli. (Sal. 139:​15-17) Choncho angathe kuona uchimo wonse womwe tinatengera kwa makolo athu. Kuwonjezera pamenepa, iye amadziwa zinthu zomwe zakhala zikutichitikira, zimene zimaumba umunthu wathu. Ndiye popeza kuti Yehova amadziwa kwambiri anthu, kodi zimenezi zimamuchititsa kutani? Zimamuchititsa kuti azitichitira chifundo. (Sal. 78:39; 103:​13, 14) Yehova anasonyeza kuti ndi wofunitsitsa kutikhululukira. Iye amamvetsa kuti chifukwa cha zochita za munthu woyambirira Adamu, tonsefe ndi ochimwa ndipo timafa. (Aroma 5:12) Palibe chomwe tikanachita kuti tidzipulumutse kapena kupulumutsa ena ku temberero limeneli. (Sal. 49:​7-9) Komabe Mulungu wathu wachikondi anatisonyeza chifundo ndipo anakonza zoti tipulumutsidwe. Monga mmene lemba la Yohane 3:16 limanenera, Yehova anatumiza Mwana wake wobadwa yekha kuti adzatifere.—Mat. 20:28; Aroma 5:19. w22.06 3 ¶5-6

Lachiwiri, July 9

Munthu wokoma mtima zinthu zimamuyendera bwino.—Miy. 11:17.

Mfundo yakuti okhululukira ena nawonso adzakhululukidwa imaonekera pa zimene Yehova anauza mtumiki wake Yobu. Munthu wokhulupirikayu anali atakhumudwa kwambiri ndi mawu opweteka omwe Elifazi, Bilidadi ndi Zofari anamulankhula. Yehova anumuuza Yobu kuti awapempherere. Iye atachita zimenezi Yehova anamudalitsa. (Yobu 42:​8-10) Timadzivulaza tokha tikamasunga chakukhosi. Yehova amafuna tizisangalala komanso kupepukidwa mumtima chifukwa chosasunga chakukhosi. (Aef. 4:​31, 32) Iye amatilimbikitsa kuti ‘tisamapse mtima ndipo tizipewa kukwiya.’ (Sal. 37:8) Kutsatira malangizo amenewa n’kothandiza kwambiri. Kusunga chakukhosi kungawononge thanzi lathu komanso maganizo athu. (Miy. 14:30) Kusunga chakukhosi sikuvulaza munthu yemwe watilakwirayo, ngati mmene zingakhalire titamwa poizoni n’kumayembekezera kuti avulale ndi mnzathuyo. Choncho tikakhululukira ena zimakhala ngati tadzipatsa mphatso. Timakhala ndi mtendere wa mumtima ndi m’maganizo ndipo timapitirizabe kutumikira Yehova. w22.06 10 ¶9-10

Lachitatu, July 10

Tivale chodzitetezera pachifuwa chachikhulupiriro ndi chikondi. Tivalenso chiyembekezo chachipulumutso ngati chipewa.—1 Ates. 5:8.

Chiyembekezo chathu chili ngati chisoti chimene chimateteza maganizo athu ndipo chimatithandiza kuti tisasankhe moyo wongodzisangalatsa tokha, womwe ungawononge ubwenzi wathu ndi Yehova. (1 Akor. 15:​33, 34) Chisoti chathu cha chiyembekezo chingatiteteze kuti tisamaganize kuti zimene timayesetsa kuchita posangalatsa Yehova n’zopanda phindu. Kumbukirani kuti Elifazi yemwe ankanamizira kudzatonthoza Yobu anagwiritsanso ntchito maganizo ngati omwewa. Iye anati: “Kodi munthu ndi ndani kuti akhale woyera?” Pofotokoza za Mulungu iye anatinso: “Iyetu sakhulupirira angelo ake, ndipo ngakhale kumwamba si koyera m’maso mwake.” (Yobu 15:​14, 15) Ilitu linali bodza lankunkhuniza. Kumbukirani kuti Satana ndi amene amalimbikitsa maganizo amenewa. Iye amadziwa kuti mukamaganizira kwambiri zinthu ngati zimenezi, mungasiye kukhala ndi chiyembekezo. Choncho muzikana mabodza amenewa. Musamakayikire kuti Yehova amafuna kuti mudzakhale ndi moyo mpaka kalekale ndipo adzakuthandizani kuti mukwanitse zimenezi.—1 Tim. 2:​3, 4. w22.10 25-26 ¶8-10

Lachinayi, July 11

Yobu sananene chilichonse cholakwika.—Yobu 2:10.

Satana ankafuna kuti Yobu azikhulupirira kuti akukumana ndi mavuto chifukwa choti Yehova sakumukondanso. Mwachitsanzo, Satana anachititsa mphepo ya mphamvu kuomba nyumba imene ana onse 10 a Yobu ankachitiramo phwando. (Yobu 1:​18, 19) Anachititsanso moto kutsika kuchoka kumwamba nkuwononga, osati ziweto zokha, koma ngakhalenso antchito omwe ankazisamalira. (Yobu 1:16) Popeza kuti mphepoyo komanso motowo zinachokera kumwamba, Yobu ankaona ngati Yehova ndi amene akuchititsa ndipo ankaganiza kuti mwina wamukhumudwitsa mwa njira ina yake. Ngakhale zinali choncho, iye anakana kutukwana Atate wake wakumwamba. Yobu ankadziwa kuti kwa zaka zambiri anakhala akulandira zinthu zabwino kuchokera kwa Yehova. Choncho ankaganiza kuti ngati ankasangalala kulandira zinthu zabwino, ankayeneranso kukhala wokonzeka kulandira zinthu zoipa. Ndiye anati: “Dzina la Yehova lipitirize kutamandidwa.”—Yobu 1:​20, 21. w22.06 21 ¶7

Lachisanu, July 12

Anthu onse adzadana nanu chifukwa cha dzina langa. Koma amene adzapirire mpaka mapeto ndi amene adzapulumuke.—Maliko 13:13.

Yesu anachenjeza ophunzira ake za nkhani yomweyi zomwe timazipeza pa Yohane 17:14. Taona kukwaniritsidwa kwa ulosi umenewu makamaka m’zaka 100 zapitazi. Motani? Atangoikidwa kukhala mfumu mu 1914, Yesu yemwe ndi Mesiya anachotsa Satana kumwamba. Satana anaponyedwa padzikoli ndipo akuyembekezera kuwonongedwa. (Chiv. 12:​9, 12) Koma sikuti iye wangokhala podikira kuti adzawonongedwe. Posowa mtengo wogwira, panopa Satana ndi wokwiya kwambiri ndipo amasonyeza mkwiyo wakewo poukira anthu a Mulungu. (Chiv. 12:​13, 17) Pa chifukwa chimenechi dzikoli likudana kwambiri ndi anthu a Mulungu. Komabe sitiyenera kuopa Satana ndi otsatira ake. Tingakhale otsimikiza ngati mtumwi Paulo amene analemba kuti: “Ngati Mulungu ali kumbali yathu, ndani adzatsutsana nafe?” (Aroma 8:31) Tikhoza kumakhulupirira kwambiri Yehova. w22.07 18 ¶14-15

Loweruka, July 13

Uthenga wabwino uwu wa Ufumu udzalalikidwa padziko lonse lapansi kumene kuli anthu.—Mat. 24:14.

Yesu sankada nkhawa kuti kudzakhala anthu ochepa ogwira ntchito yolalikira munthawi ya mapeto. Iye ankadziwa kuti ulosi womwe wolemba masalimo ananena udzakwaniritsidwa, wakuti: “Anthu ako adzadzipereka mofunitsitsa pa tsiku limene udzatsogolera asilikali ako kunkhondo.” (Sal. 110:3) Ngati mukugwira nawo ntchito yolalikira, mukuthandiza Yesu ndi kapolo wokhulupirika komanso mukukwaniritsa nawo ulosiwu. Ntchitoyi ikupita patsogolo, komabe pali mavuto ena. Vuto limodzi lomwe olalikira za Ufumu amakumana nalo ndi kutsutsidwa. Ampatuko, atsogoleri azipembedzo komanso andale achititsa anthu ambiri kuti aziona molakwika ntchito yathu. Ngati achibale athu, anthu odziwana nawo komanso amene timagwira nawo ntchito asokonezedwa ndi zimenezi, angatikakamize kuti tisiye kutumikira Yehova komanso kulalikira. Pofuna kutsutsa ntchito yathu, m’mayiko ena abale ndi alongo amaukiridwa, kuopsezedwa ngakhalenso kutsekeredwa m’ndende. w22.07 8 ¶1; 9 ¶5-6

Lamlungu, July 14

Tiyenera kukumana ndi mavuto ambiri kuti tikalowe mu Ufumu wa Mulungu.—Mac. 14:22.

Yehova amayembekezera kuti tiziwerenga Baibulo nthawi zonse komanso kuganizira mozama zomwe tawerengazo. Tikamagwiritsa ntchito zomwe tikuphunzira, chikhulupiriro chathu chimalimba ndipo timakhala pa ubwenzi wabwino ndi Atate wathu wakumwamba. Zotsatira zake n’zakuti timakhala olimba ndipo tingathe kupirira mayesero. Yehova amaperekanso mzimu wake woyera kwa omwe amadalira Mawu ake. Ndipo mzimuwo umatipatsa “mphamvu yoposa yachibadwa” kuti tithe kupirira mayesero aliwonse. (2 Akor. 4:​7-10) Mothandizidwa ndi Yehova “kapolo wokhulupirika komanso wanzeru” amakonza nkhani, mavidiyo komanso nyimbo zomwe zingatithandize kukhala ndi chikhulupiriro cholimba ndiponso kuti tikhale pa ubwenzi wabwino ndi iye. (Mat. 24:45) Yehova waphunzitsa anthu ake kuti azikondana komanso kulimbikitsana pa nthawi yovuta. (2 Akor. 1:​3, 4; 1 Ates. 4:9) Abale ndi alongo athu amafunitsitsa kutithandiza kuti tikhalebe okhulupirika tikamakumana ndi mavuto. w22.08 12 ¶12-14

Lolemba, July 15

Muziyesetsa . . . kusunga umodzi umene timaupeza mothandizidwa ndi mzimu woyera, pokhala mwamtendere umene uli ngati chomangira chimene chimatigwirizanitsa.—Aef. 4:3.

Tikamayamikira kuchokera pansi pa mtima makhalidwe abwino amene abale ndi alongo athu ali nawo, zingathandize kuti onse mumpingo azigwirizana komanso azikondana kwambiri. Nthawi zina ngakhalenso Akhristu olimba mwauzimu angasemphane maganizo kapena kukangana kumene. Zimenezi zinachitikirapo mtumwi Paulo ndi mnzake wapamtima Baranaba. Amuna awiriwa anasemphana maganizo pa nkhani yoti atenge Maliko pa ulendo wawo wotsatira waumishonale. Iwo “anakangana koopsa” moti mpaka anasiyana. (Mac. 15:​37-39) Koma pambuyo pake amuna atatuwa anagwirizana. Patapita nthawi, Paulo anafotokoza zinthu zabwino zokhudza Baranaba ndi Maliko. (1 Akor. 9:6; Akol. 4:10) Ifenso tiyenera kuthetsa kusamvana kulikonse komwe tingakhale nako ndi ena mumpingo n’kupitiriza kumaona makhalidwe abwino amene ali nawo. Tikatero tidzalimbikitsa mtendere ndi mgwirizano. w22.08 23 ¶10-11

Lachiwiri, July 16

Siyani kuweruza ena kuti inunso musaweruzidwe.—Mat. 7:1.

Pamene tikuyesetsa kuti tizitsatira mfundo za Yehova zolungama, tiyenera kupewa kuweruza anzathu kapenanso kumadziona kuti ndife olungama kuposa anthu ena. Timakumbukira kuti Yehova ndi “Woweruza wa dziko lonse lapansi.” (Gen. 18:25) Yehova sanatipatse udindo woweruza. Taganizirani chitsanzo cha Yosefe, yemwe anali munthu wolungama. Iye anapewa kuweruza ena ngakhalenso amene anamuchitira zoipa. Azichimwene ake enieni anamuzunza, kumugulitsa ku ukapolo ndipo anatsimikizira bambo awo kuti anali ataphedwa. Patapita zaka, Yosefe anakumananso ndi anthu a m’banja lake. Popeza kuti pa nthawiyi anali wolamulira wamphamvu, iye akanatha kuweruza abale ake mwankhanza komanso kuwabwezera. Abale akewo ankaopa kuti mwina zimenezi ndi zimene angachite ngakhale kuti ankadzimvera chisoni chifukwa cha zimene anamuchitira. Koma Yosefe analankhula mowalimbikitsa kuti: “Musaope. Kodi ine ndatenga malo a Mulungu?” (Gen. 37:​18-20, 27, 28, 31-35; 50:​15-21) Modzichepetsa Yosefe anazindikira kuti ndi Yehova yekha, yemwe anali ndi udindo woweruza abale akewo. w22.08 30 ¶18-19

Lachitatu, July 17

Usalephere kuchitira zabwino anthu amene ukuyenera kuwachitira zabwinozo, ngati ungathe kuwathandiza.—Miy. 3:27.

Kodi mukudziwa kuti Yehova akhoza kugwiritsa ntchito inuyo poyankha pemphero lochokera pansi pa mtima la munthu wina? Iye angakugwiritseni ntchito kaya ndinu mkulu, mtumiki wothandiza, mpainiya kapenanso wofalitsa. Angakugwiritseni ntchito kaya ndinu wamng’ono kapena wamkulu ndiponso kaya ndinu m’bale kapena mlongo. Munthu amene amakonda Yehova akamupempha kuti amuthandize, Mulungu angagwiritse ntchito mkulu kapena mtumiki wake wokhulupirika aliyense kuti ‘amulimbikitse.’ (Akol. 4:11) Ndi mwayitu waukulu kutumikira Yehova komanso abale athu m’njira imeneyi. Tingathe kuchita zimenezi pa nthawi imene kwagwa mliri, kwachitika ngozi yam’chilengedwe kapenanso pamene tikuzunzidwa. Tingafune kuthandiza ena koma zingakhale zovuta ngati anthu a m’banja lathunso akuvutika. Komabe timafuna kuthandiza abale athu chifukwa Yehova amasangalala tikachita zomwe tingathe powathandiza.—Miy. 19:17. w22.12 22 ¶1-2

Lachinayi, July 18

Ndikukulamulani kuti muzikondana mofanana ndi mmene ine ndimakukonderani.—Yoh. 15:12.

Chikondi ndi khalidwe lofunika kwambiri lomwe limachititsa kuti anthu azikhulupirirana. Yesu ananena kuti malamulo awiri akuluakulu ndi akuti tizikonda Yehova komanso tizikonda anzathu. (Mat. 22:​37-39) Chikondi chathu pa Yehova chimatichititsa kuti tizimutsanzira pa nkhani yokhala odalirika. Mwachitsanzo, kukonda abale ndi alongo athu kumachititsa kuti tiziwasungira chinsinsi. Sitingafune kuulula nkhani zomwe zingawachititse kuti agwere m’mavuto, achite manyazi kapena amve kupweteka. Kudzichepetsa kungatithandizenso kuti tikhale odalirika. Mkhristu wodzichepetsa safuna kugometsa ena pokhala woyamba kuwauza nkhani inayake. (Afil. 2:3) Iye sadzionetsa kuti ndi wofunika kwambiri pouza ena kuti akudziwa nkhani inayake yomwe sakufunika kuulula. Kudzichepetsa kungatithandizenso kuti tizipewa kufalitsa nkhani zimene sizinafotokozedwe m’Baibulo kapena m’mabuku athu. w22.09 12 ¶12-13

Lachisanu, July 19

Adzadziwa zinthu zambiri zoona. —Dan. 12:4.

Mngelo anauza Danieli kuti anthu a Mulungu anali kudzamvetsa bwino maulosi opezeka m’buku lake, komanso kuti “palibe munthu woipa aliyense amene adzamvetsetse mawu amenewa.” (Dan. 12:10) Panopa ndi nthawi yoti tizisonyeza kuti sitili m’gulu la anthu oipa. (Mal. 3:​16-18) Yehova akusonkhanitsa anthu omwe amawaona kuti ndi “chuma chapadera,” kapena kuti anthu ake amtengo wapatali. N’zosakayikitsa kuti tikufuna kukhala m’gulu la anthu amenewa. Kunena zoona, panopa tikukhala munthawi yosangalatsa kwambiri. Koma zina zosangalatsanso kwambiri zatsala pang’ono kuchitika. Posachedwapa tiona zinthu zonse zoipa zikuthetsedwa. Pambuyo pa zimenezi tidzaona kukwaniritsidwa kwa zomwe Yehova analonjeza Danieli kuti: “Pamapeto amasikuwo udzauka kuti ulandire gawo lako.” (Dan. 12:13) Kodi mukuyembekezera mwachidwi nthawi imene Danieli limodzi ndi okondedwa anu ‘adzaukitsidwe’? Ngati zili choncho, panopa muzichita zonse zomwe mungathe kuti mukhalebe okhulupirika. Mukatero mungakhale otsimikiza kuti dzina lanu lidzapitirizabe kukhala m’buku la moyo la Yehova. w22.09 24 ¶17; 25 ¶19-20

Loweruka, July 20

Ndikukutumiza.—Ezek. 2:3.

Mawu amenewa ayenera kuti anamulimbikitsa Ezekieli. Chifukwa chiyani? N’zosakayikitsa kuti iye anakumbukira kuti Yehova anagwiritsanso ntchito mawu ngati omwewa pomwe ankatuma Mose ndi Yesaya monga aneneri ake. (Eks. 3:10; Yes. 6:8) Ankadziwanso mmene Yehova anathandizira aneneri awiriwa kulimbana ndi mavuto. Choncho pamene Yehova anamuuza kawiri kuti: “Ndikukutumiza,” mneneriyu anali ndi zifukwa zabwino zokhulupirira kuti Yehova amuthandiza. Kuwonjezera pamenepo, m’buku la Ezekieli timapezamo kambirimbiri mawu akuti: “Yehova anandiuza kuti.” (Ezek. 3:16) Ndipo mobwerezabwereza iye analemba kuti, “Yehova anandiuzanso kuti.” (Ezek. 6:1) Apatu Ezekieli sankakayikira kuti anatumidwa ndi Yehova. Komanso popeza anali mwana wa wansembe, bambo ake ayenera kuti anamuphunzitsa mmene Yehova nthawi zonse ankatsimikizira aneneri ake kuti awathandiza. Mwachitsanzo, Yehova anauza Isaki, Yakobo ndi Yeremiya kuti: “Ine ndili ndi iwe.”—Gen. 26:24; 28:15; Yer. 1:8. w22.11 2 ¶3

Lamlungu, July 21

Moyo wosatha adzaupeza. —Yoh. 17:3.

Ngakhale kuti Adamu ndi Hava anachimwa ndipo zinachititsa kuti ana awo azifa, Yehova sanasinthe maganizo ake okhudza cholinga chake. (Yes. 55:11) Iye amafunabe kuti anthu okhulupirika adzakhale ndi moyo mpaka kalekale. Taganizira zimene Yehova wakhala akunena komanso kuchita kuti akwaniritse cholinga chake. Yehova akulonjeza kuti adzaukitsa akufa n’kuwapatsa moyo wosatha. (Mac. 24:15; Tito 1:​1, 2) Munthu wokhulupirika Yobu sankakayikira kuti Yehova amafunitsitsa kudzaukitsa omwe anamwalira. (Yobu 14:​14, 15) Mneneri Danieli ankadziwa kuti anthu ali ndi chiyembekezo chodzaukitsidwa n’kukhala ndi mwayi wokhala ndi moyo mpaka kalekale. (Sal. 37:29; Dan. 12:​2, 13) Ayuda a munthawi ya Yesu ankadziwanso kuti Yehova angathe kupereka “moyo wosatha” kwa atumiki ake okhulupirika. (Luka 10:25; 18:18) Mobwerezabwereza, Yesu ankalankhula za lonjezoli ndipo iye anaukitsidwa ndi Atate wake.—Mat. 19:29; 22:​31, 32; Luka 18:30; Yoh. 11:25. w22.12 4-5 ¶8-9

Lolemba, July 22

Ine ndimakhulupirira inu Yehova. —Sal. 31:14.

Yehova amatiuza kuti timuyandikire. (Yak. 4:8) Iye amafuna kukhala Mulungu wathu, Atate wathu komanso mnzathu. Amayankha mapemphero athu komanso amatithandiza pa nthawi yovuta. Amatiphunzitsanso pogwiritsa ntchito gulu lake ndiponso amatiteteza. Tingakhale pa ubwenzi ndi Yehova popemphera kwa iye komanso kuwerenga ndi kuganizira Mawu ake. Tikamachita zimenezi, timayamba kumukonda kwambiri komanso kumuyamikira. Timafunitsitsa kumumvera komanso kumutamanda monga mmene kumafunikira. (Chiv. 4:11) Tikamamudziwa kwambiri Yehova m’pamene timadaliranso kwambiri iyeyo ndi gulu limene watipatsa kuti lizitithandiza. Komabe mwapang’onopang’ono, Mdyerekezi amafuna kutichititsa kuti tisamadalire Yehova ndi gulu lake. Koma tingathe kupewa misampha yake. Tikamakhulupirira komanso kudalira kwambiri Yehova, sitingasiye Mulungu wathu ndi gulu lake.—Sal. 31:​13, 14. w22.11 14 ¶1-3

Lachiwiri, July 23

Anali okonzeka kufa m’malo motumikira kapena kulambira mulungu wina aliyense kupatulapo Mulungu wawo.—Dan. 3:28.

Akhristu oona ambiri akhala akulolera kuvutika komanso kuika moyo wawo pangozi chifukwa chokonda Yehova monga Wolamulira wawo wamkulu. Iwo ndi okhulupirika ngati Aheberi atatu omwe anapulumutsidwa mung’anjo yoyaka moto chifukwa chokhala okhulupirika kwa Wolamulira Wamkulukulu. Posonyeza kufunika kokhalabe wokhulupirika kwa Mulungu, wolemba masalimo Davide anati: “Yehova adzapereka chigamulo kwa mitundu ya anthu. Ndiweruzeni inu Yehova, mogwirizana ndi chilungamo changa komanso mogwirizana ndi kukhulupirika kwanga.” (Sal. 7:8.) Iye analembanso kuti: “Kukhala wokhulupirika komanso kuchita zinthu zoyenera kunditeteze.” (Sal. 25:21.) Chinthu chofunika kwambiri ndi kupitirizabe kukhala okhulupirika kwa Yehova. Tikatero, tidzamva ngati mmene anamvera wolemba masalimo yemwe analemba kuti: “Osangalala ndi anthu amene salakwitsa kanthu, . . . amene amatsatira chilamulo cha Yehova.”—Sal. 119:1. w22.10 17 ¶18-19

Lachitatu, July 24

Makhalidwe a Mulungu osaoneka ndi maso akuonekera bwino . . . m’zinthu zimene anapanga.—Aroma 1:20.

Pa makambirano onse omwe Yobu anakhala nawo pa moyo wake, makambirano apadera kwambiri anali amene anakhala nawo ndi Yehova Mulungu. Pofuna kumuthandiza Yobu kuti azikhulupirira kwambiri nzeru za Mulungu komanso kuti amasamalira atumiki ake, Yehova anatchula zinthu zina zodabwitsa zam’chilengedwe. Mwachitsanzo, Mulungu anakumbutsa Yobu kuti iye amasamalira nyama, choncho akanatha kumusamaliranso iyeyo. (Yobu 38:​39-41; 39:​1, 5, 13-16) Poganizira zinthu zam’chilengedwe, Yobu anaphunzira makhalidwe ambiri a Mulungu wake. Ifenso tingaphunzire zokhudza Mulungu wathu tikamachita chidwi ndi zinthu zimene analenga. Komabe si nthawi zonse pamene kuchita zimenezi kumakhala kophweka. Ngati timakhala m’mizinda ikuluikulu, sitingamaone zinthu zambiri zimene Mulungu analenga. Mwina ngakhale pamene tikukhala m’dera limene kuli zachilengedwe zambiri, tingamaone kuti tilibe nthawi yokwanira yoziphunzira, koma ndi zofunika kuti tizipeza nthawi komanso kumachita khama kuphunzira zinthu zachilengedwe. w23.03 15 ¶1-2

Lachinayi, July 25

Munthu wochenjera akaona tsoka amabisala.—Miy. 22:3.

Yesu ananena kuti “zivomezi zamphamvu” ndi ngozi zina zam’chilengedwe zidzachitika mapeto asanafike. (Luka 21:11) Ananenanso za “kuwonjezeka kwa kusamvera malamulo,” ndipo timaonadi zinthu monga kuphwanya malamulo, chiwawa komanso za uchigawenga zikuchitika. (Mat. 24:12) Yesu sananene kuti zinthu zimenezi zidzachitikira anthu okhawo amene Yehova sasangalala nawo. Ndipotu atumiki okhulupirika ambiri a Yehova amakumana ndi ngozi zam’chilengedwe. (Yes. 57:1; 2 Akor. 11:25) Yehova sangatiteteze mozizwitsa ku ngozi zonse zam’chilengedwe, koma angatipatse zonse zomwe tikufunikira kuti mtima wathu ukhale m’malo komanso tikhale ndi mtendere. Zingakhale zosavuta kuti mtima wathu ukhale m’malo ngati takonzekereratu pasadakhale. Koma kodi kukonzekera kumasonyeza kuti sitikukhulupirira Yehova? Ayi si choncho. Ndipotu kukonzekerako kumasonyeza kuti timakhulupirira kuti iye adzatisamalira. N’chifukwa chiyani tikutero? Mawu a Mulungu amatilangiza kuti tizikonzekera ngozi zomwe zingachitike. w22.12 18 ¶9-10

Lachisanu, July 26

Mulungu ndi amene ananditumiza kuno kuti tikhalebe ndi moyo.—Gen. 45:5.

Yosefe adakali m’ndende, Yehova anachititsa mfumu ya Iguputo kulota maloto awiri osautsa. Atamva kuti Yosefe amatha kumasulira maloto, iye anamuitanitsa. Mothandizidwa ndi Yehova, Yosefe anamasulira malotowo ndipo Farao anakhutira ndi malangizo othandiza omwe iye anamupatsa. Poona kuti Yehova anali ndi mnyamatayu, Farao anamuika kukhala woyang’anira chakudya m’dziko lonse la Iguputo. (Gen. 41:​38, 41-44) Kenako kunagwa njala yoopsa yomwe inakhudza ku Iguputo komanso ku Kanani komwe kunkakhala abale ake a Yosefe. Apa Yosefe anali ndi mwayi wopulumutsa banja lakwawo lomwe linali mzere wodzabadwira Mesiya. N’zodziwikiratu kuti Yehova ndi amene ankachititsa kuti zonse zimene Yosefe ankachita zizimuyendera bwino. Pamapeto pake Yehova anagwiritsa ntchito chiwembu chimene abale ake a Yosefe anamuchitira kukhala ngati njira yokwaniritsira chifuniro chake. w23.01 17 ¶11-12

Loweruka, July 27

Samalani.—Luka 21:34.

Munthu amene akusamala, amakhala tcheru ndi zinthu zomwe zingasokoneze ubwenzi wake ndi Yehova ndipo amayesetsa kuzipewa. Akamachita zimenezi amapitiriza kuchita zinthu zimene zingachititse Mulungu kumukonda. (Miy. 22:3; Yuda 20, 21) Mtumwi Paulo analangiza Akhristu kuti azisamala ndi zimene amachita. Mwachitsanzo, anauza Akhristu a ku Efeso kuti: “Samalani kwambiri kuti mukamayenda, musamayende ngati anthu opanda nzeru koma ngati anthu anzeru.” (Aef. 5:​15, 16) Nthawi zonse Satana amayesetsa kuti awononge ubwenzi wathu ndi Yehova. Choncho Baibulo limatilangiza kuti tipitirize “kuzindikira chifuniro cha Yehova” n’cholinga choti tidziteteze ku misampha yake. (Aef. 5:17) Kuti tisankhe zinthu mwanzeru, timafunika kudziwa kapena kuti kuzindikira “chifuniro cha Yehova.” Tingachite zimenezo ngati nthawi zonse timaphunzira komanso kuganizira mozama Mawu a Mulungu. Tikamayesetsa kumvetsa chifuniro cha Yehova komanso kukhala ndi “maganizo a Khristu,” m’pamenenso timayenda “ngati anthu anzeru” ngakhale kuti tilibe malamulo otiuza zochita pa nkhani iliyonse.—1 Akor. 2:​14-16. w23.02 16-17 ¶7-9

Lamlungu, July 28

Khalani munthu watsopano posintha kwambiri maganizo anu, kuti muzindikire chifuniro cha Mulungu, chabwino, chovomerezeka ndi changwiro.—Aroma 12:2.

Kodi mumakonza kangati m’nyumba mwanu? N’kutheka kuti pa nthawi yoyamba pamene munkasamukiramo, munakonza bwino paliponse. Koma kodi n’chiyani chingachitike pambuyo pake ngati mutasiya kukonzamo? Monga mukudziwira, mungadenso mwamsanga ndi fumbi. Kuti m’nyumbamo muzikhalabe mwaukhondo, mumafunika kukonzamo pafupipafupi. Pamafunikanso khama lofanana ndi limeneli pa zimene timaganiza komanso khalidwe lathu. N’zoona kuti tisanabatizidwe, tinayesetsa kusintha moyo wathu kuti “tidziyeretse ndipo tichotse chinthu chilichonse choipitsa thupi ndi mzimu.” (2 Akor. 7:1) Komabe panopa tifunika kutsatira malangizo a mtumwi Paulo akuti tipitirize ‘kukhala atsopano.’ (Aef. 4:23) Kaganizidwe ndi zochita za anthu a m’dzikoli zingatidetse mofulumira. Kuti zimenezi zisatichitikire komanso kuti tipitirize kukhala ovomerezeka pamaso pa Yehova, nthawi zonse tiyenera kumafufuza zimene timaganiza, khalidwe lathu komanso zimene timalakalaka. w23.01 8 ¶1-2

Lolemba, July 29

Yohane anaona mzimu wa Mulungu ukutsika ngati nkhunda n’kudzamutera.—Mat. 3:16.

Taganizirani mmene anthu ankamvera kumva Yesu akuphunzitsa. Nthawi zonse iye ankaphunzitsa kuchokera m’Malemba ndipo ankachita zimenezi kuchokera mumtima. Pa nthawi imene anabatizidwa komanso kudzozedwa ndi mzimu woyera, zikuoneka kuti Yesu anakumbukira mmene analili poyamba asanabwere padzikoli. Mawu a Yesu oyambirira kulembedwa omwe analankhula atangobatizidwa komanso mawu ake ena omaliza omwe analankhula asanafe, anali ochokera m’Malemba. (Deut. 8:3; Sal. 31:5; Luka 4:4; 23:46) Ndipo pa zaka zitatu ndi hafu za utumiki wake, nthawi zonse Yesu ankawerenga komanso kufotokoza Malemba.(Mat. 5:​17, 18, 21, 22, 27, 28; Luka 4:​16-20) Kwa zaka zambiri asanayambe utumiki wake, Yesu ankawerenga komanso kumva Mawu a Mulungu kambirimbiri. Akakhala panyumba, mosakayikira ankamva Mariya ndi Yosefe akutchula Malemba. (Deut. 6:​6, 7) Komanso Sabata lililonse Yesu ankapita ku sunagoge ndi banja lawo. (Luka 4:16) Kumeneko ayenera kuti ankamvetsera mwatcheru Malemba akamawerengedwa. w23.02 8 ¶1-2

Lachiwiri, July 30

Muzikonda Yehova Mulungu wanu. —Maliko 12:30.

Pali zifukwa zambiri zokuchititsani kukonda Yehova. Mwachitsanzo, mwafika pomvetsa bwino kuti iye ndi “kasupe wa moyo” komanso kuti ndi amene amatipatsa “mphatso iliyonse yabwino ndi yangwiro.” (Sal. 36:9; Yak. 1:17) Chilichonse chabwino chomwe mumasangalala nacho chimachokera kwa Mulungu wathu wowolowa manja komanso wachikondi. Dipo ndi mphatso yamtengo wapatali imene Yehova anatipatsa. N’chifukwa chiyani tikutero? Taganizirani za ubwenzi wabwino kwambiri wa Yehova ndi Mwana wake. Yesu anati: “Atate amandikonda” komanso “ndimakonda Atate.” (Yoh. 10:17; 14:31) Ubwenziwu unalimba kwambiri chifukwa anakhala limodzi kwa zaka mabiliyoni. (Miy. 8:​22, 23, 30) Ndiye taganizani mmene zinamupwetekera Mulungu polola kuti Mwana wakeyu avutike komanso kufa. Yehova amakonda kwambiri anthu kuphatikizapo inuyo moti mpaka analolera kupereka Mwana wake wokondedwa monga nsembe n’cholinga choti inuyo komanso anthu ena mudzakhale ndi moyo mpaka kalekale. (Yoh. 3:16; Agal. 2:20) Chimenechitu ndi chifukwa chachikulu kwambiri chotichititsa kukonda Mulungu. w23.03 4-5 ¶11-13

Lachitatu, July 31

Gwirani mwamphamvu . . . zimene muli nazo.—Chiv. 2:25.

Tiyenera kumapewa ziphunzitso za ampatuko. Yesu anadzudzula ena ku Pegamo chifukwa cholimbikitsa magawano komanso mpatuko. (Chiv. 2:​14-16) Iye anayamikira Akhristu a ku Tiyatira omwe anakana “zinthu zozama za Satana” ndipo anawalimbikitsa kuti ‘agwire mwamphamvu’ choonadi. (Chiv. 2:​24-26) Akhristu ofooka kumeneko omwe anasocheretsedwa ndi ziphunzitso zabodzazi ankafunika kulapa. Nanga bwanji ifeyo masiku ano? Tiyenera kukana chiphunzitso chilichonse chomwe chimasemphana ndi zimene Yehova amafuna. Anthu ampatuko amakhala “ooneka ngati odzipereka kwa Mulungu” koma “amakana kuti mphamvu ya kudziperekako iwasinthe.” (2 Tim. 3:5) Zingakhaletu zosavuta kudziwa komanso kukana ziphunzitso zonyenga ngati timaphunzira mwakhama Mawu a Mulungu. (2 Tim. 3:​14-17; Yuda 3, 4) Tiyenera kuonetsetsa kuti kulambira kwathu kukhale kovomerezeka kwa Yehova. Ngati tikuchita zinazake zomwe zingachititse kuti kulambira kwathu kukhale kosavomerezeka, tiyenera kuchitapo kanthu mwamsanga kuti tikonze zinthu.—Chiv. 2:​5, 16; 3:​3, 16. w22.05 4 ¶9; 5 ¶11

    Mabuku a Chichewa (1974-2026)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena