Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • es24 tsamba 78-88
  • August

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • August
  • Kuphunzira Malemba Tsiku ndi Tsiku—2024
  • Timitu
  • Lachinayi, August 1
  • Lachisanu, August 2
  • Loweruka, August 3
  • Lamlungu, August 4
  • Lolemba, August 5
  • Lachiwiri, August 6
  • Lachitatu, August 7
  • Lachinayi, August 8
  • Lachisanu, August 9
  • Loweruka, August 10
  • Lamlungu, August 11
  • Lolemba, August 12
  • Lachiwiri, August 13
  • Lachitatu, August 14
  • Lachinayi, August 15
  • Lachisanu, August 16
  • Loweruka, August 17
  • Lamlungu, August 18
  • Lolemba, August 19
  • Lachiwiri, August 20
  • Lachitatu, August 21
  • Lachinayi, August 22
  • Lachisanu, August 23
  • Loweruka, August 24
  • Lamlungu, August 25
  • Lolemba, August 26
  • Lachiwiri, August 27
  • Lachitatu, August 28
  • Lachinayi, August 29
  • Lachisanu, August 30
  • Loweruka, August 31
Kuphunzira Malemba Tsiku ndi Tsiku—2024
es24 tsamba 78-88

August

Lachinayi, August 1

Buku la chikumbutso linayamba kulembedwa pamaso pake. Buku limeneli linali lonena za anthu oopa Yehova ndi anthu amene anali kuganizira za dzina lake.—Mal. 3:16.

Kodi mukuganiza kuti n’chifukwa chiyani Yehova analemba ‘m’buku lake la chikumbutso’ mayina a anthu, omwe zolankhula zawo zinkasonyeza kuti ankamuopa komanso kuganizira za dzina lake? Zolankhula zathu zimasonyeza zomwe zili mumtima mwathu. Yesu anati: “Pakamwa pamalankhula zosefukira mumtima.” (Mat. 12:34) Yehova amafuna kuti anthu amene amamukonda adzasangalale ndi moyo mpaka kalekale m’dziko latsopano. Zolankhula zathu zingachititse kuti Yehova avomereze kulambira kwathu kapena ayi. (Yak. 1:26) Anthu ena omwe sakonda Mulungu, amalankhula mwaukali, mwamwano komanso modzikuza. (2 Tim. 3:​1-5) Ifeyo sitingakonde kukhala ngati anthu amenewa. Timafunitsitsa kuti Yehova azisangalala ndi zomwe timalankhula. Koma kodi Yehova angamasangalale nafe ngati timalankhula mokoma mtima kumisonkhano komanso mu utumiki, koma n’kumalankhula mwamwano komanso mopanda chikondi kwa anthu a m’banja lathu tikakhala kwatokha?—1 Pet. 3:7. w22.04 5 ¶4-5

Lachisanu, August 2

Zidzadana ndi hulelo. Zidzatenga zinthu zake zonse n’kulisiya lamaliseche ndipo zidzadya minofu yake n’kulipsereza ndi moto.—Chiv. 17:16.

Mulungu adzaika maganizo ake m’mitima ya nyanga 10 ndi chilombo kuti ziwononge Babulo Wamkulu. Choncho Yehova adzalimbikitsa maboma kuti agwiritse ntchito chilombo chofiira, chomwe ndi bungwe la United Nations, kuti chiukire zipembedzo zonse zonyenga n’kuziwonongeratu. (Chiv. 18:​21-24) Kodi zimenezi zikutikhudza bwanji? Kulambira kwathu kuyenera kukhala “kupembedza koyera ndi kosaipitsidwa kwa Mulungu ndi Atate wathu.” (Yak. 1:27) Sitiyenera kulola kuti tikhudzidwe ndi ziphunzitso zabodza, maholide a zipembedzo, makhalidwe oipa komanso zamizimu zomwe zimachokera ku Babulo Wamkulu. Tiyenera kupitiriza kuitana anthu kuti ‘atuluke mwa iye’ n’cholinga choti asagawane naye machimo ake.—Chiv. 18:4. w22.05 11 ¶17; 14 ¶18

Loweruka, August 3

Ndidzanena za ntchito za Yehova zosonyeza kukoma mtima kwake kosatha.—Yes. 63:7.

Makolo, muzikonza mipata yophunzitsira ana anu zokhudza Yehova komanso zinthu zabwino zambiri zimene wakuchitirani. (Deut. 6:​6, 7) Zimenezi n’zofunika makamaka ngati simungathe kuphunzira ndi ana anu pafupipafupi kunyumba chifukwa choti muli m’banja losiyana zipembedzo. Mlongo wina dzina lake Christine anati: “Panalibe mipata yambiri yokambirana ndi ana anga zokhudza Yehova, choncho ndinkagwiritsa ntchito mwayi uliwonse umene wapezeka.” Kuwonjezera pamenepo, muzilankhula zabwino zokhudza gulu la Yehova komanso abale ndi alongo. Musamalankhule zosonyeza kuti mukuimba mlandu akulu. Zimene mumalankhula zingachititse kuti ana anuwo akakumana ndi mavuto aziwadalira n’kuwapempha malangizo kapena ayi. Muzilimbikitsa mtendere m’banja mwanu. Nthawi zonse muzisonyeza kuti mumakonda mwamuna ndi ana anu. Muzilankhula mokoma mtima komanso mwaulemu zokhudza mwamuna wanu, ndipo muziphunzitsa ana anu kuchita zomwezo. Mukamatero mungathandize kuti m’banja mwanu mukhale mtendere ndipo zingakhale zosavuta kwa ana anu kuphunzira za Yehova.—Yak. 3:18. w22.04 18 ¶10-11

Lamlungu, August 4

Ndikudziwa ntchito zako.—Chiv. 3:1.

Uthenga umene Yesu anatumiza kumpingo wa ku Efeso umasonyeza kuti iwo ankapirira komanso kupitirizabe kutumikira Yehova ngakhale kuti ankakumana ndi mavuto osiyanasiyana. Ngakhale zinali choncho, iwo anali atasiya kukonda Yehova ngati mmene ankachitira poyamba. Ankafunika kuyambiranso kumukonda chifukwa kupanda kutero kulambira kwawo sikukanakhala kovomerezeka. Mofanana ndi zimenezi, masiku anonso timafunika kuchita zambiri kuposa pa kupirira. Tiyenera kupirira tili ndi zolinga zoyenera. Mulungu amachita chidwi osati ndi zimene tikuchita zokha, koma chifukwa chake tikuchitira zimenezo. Zolinga zathu ndi zofunika kwa iye popeza amafuna kuti tizimulambira chifukwa chomukonda kwambiri komanso kumuyamikira. (Miy. 16:2; Maliko 12:​29, 30) Tiyenera kupitiriza kukhala maso mwauzimu. Anthu a mumpingo wa ku Sade analinso ndi vuto. Ngakhale kuti poyamba ankachita khama potumikira Yehova, kenako anasiya. Yesu anawauza kuti ‘adzuke.’ (Chiv. 3:​1-3) N’zoona kuti Yehova sadzaiwala zimene tinachita pomutumikira.—Aheb. 6:10. w22.05 3 ¶6-7

Lolemba, August 5

Kugwira ntchito iliyonse mwakhama kumapindulitsa.—Miy. 14:23.

Solomo ananena kuti chisangalalo chomwe timapeza chifukwa chogwira ntchito mwakhama ndi “mphatso yochokera kwa Mulungu.” (Mlal. 5:​18, 19) Solomo ankadziwa kuti mfundo imene ananenayi ndi yoona. Tikutero chifukwa anali wakhama pantchito. Iye anamanga nyumba zambiri, analima minda ya mpesa komanso anali ndi minda ya maluwa ndiponso madamu a madzi. Anamanganso mizinda. (1 Maf. 9:19; Mlal. 2:​4-6) Anachitatu khama pogwira ntchitoyi ndipo n’zosakayikitsa kuti zinamuthandiza kukhala wosangalala. Koma sikuti Solomo ankangodalira zinthu zimenezi kuti azisangalala. M’malomwake ankagwiranso ntchito zokhudzana ndi kulambira Yehova. Mwachitsanzo, kwa zaka 7 iye anatsogolera pa ntchito yomanganso kachisi wokongola woti anthu azilambiriramo Yehova. (1 Maf. 6:38; 9:1) Komabe pambuyo pake Solomo anazindikira kuti kugwira ntchito zokhudzana ndi kulambira Yehova n’kofunika kwambiri kusiyana ndi kugwira ntchito zina zonse. Analemba kuti: “Poti zonse zanenedwa, mfundo yaikulu ndi yakuti: Opa Mulungu woona ndi kusunga malamulo ake.”—Mlal. 12:13. w22.05 22 ¶8

Lachiwiri, August 6

Mulungu anakukhululukirani ndi mtima wonse kudzera mwa Khristu.—Aef. 4:32.

M’Baibulo muli zitsanzo za anthu ambiri omwe Yehova anawakhululukira ndi mtima wonse. Kodi inuyo mukukumbukirako ndani? Mwina mukuganizira za Mfumu Manase. Munthu ameneyu anachita machimo akuluakulu komanso oipa kwambiri. Ankatsogolera anthu pa kulambira konyenga. Anapha ana ake powapereka nsembe kwa milungu yonyenga. Anafika mpaka popanga fano n’kukaliimika m’kachisi woyera wa Yehova. Ponena za Manase, Baibulo limati: “Iye anachita zinthu zoipa kwambiri pamaso pa Yehova ndipo anamukwiyitsa.” (2 Mbiri 33:​2-7) Komabe iye atalapa mochokera pansi pa mtima, Yehova anamukhululukira. (2 Mbiri 33:​12, 13) N’kutheka kuti mukuganiziranso za Mfumu Davide, yemwe anachita machimo akuluakulu kuphatikizapo chigololo komanso kupha munthu. Komabe iye atalapa mochokera pansi pa mtima n’kuvomereza machimo ake, Yehova anamukhululukiranso. (2 Sam. 12:​9, 10, 13, 14) Choncho tingakhale otsimikiza kuti Yehova ndi wofunitsitsa kukhululukira anthu omwe alapa. w22.06 3 ¶7

Lachitatu, August 7

Khalani oleza mtima. Limbitsani mitima yanu.—Yak. 5:8.

Sizophweka kupitiriza kulimbitsa chiyembekezo chathu. Nthawi zina tingasiye kuyembekezera moleza mtima kuti Mulungu akwaniritse malonjezo ake. Koma popeza Yehova ndi wamuyaya, nthawi yomwe imaoneka yaitali kwa ife, kwa iye ndi yaifupi. (2 Pet. 3:​8, 9) Iye adzakwanitsa cholinga chake pa nthawi yoyenera koma mwina sangachite zimenezi pa nthawi imene ifeyo tikuyembekezera. Kodi n’chiyani chingatithandize kupitiriza kulimbitsa chiyembekezo chathu, pamene moleza mtima tikudikira kuti Mulungu akwaniritse malonjezo ake? (Yak. 5:7) Tiyenera kupitiriza kukhala pa ubwenzi wolimba ndi Yehova, yemwe amatipatsa chiyembekezochi. Ndipotu Baibulo limasonyeza kuti pali kugwirizana pakati pa chiyembekezo ndi kukhulupirira kuti Yehova alipo komanso kuti “amapereka mphoto kwa anthu amene amamufunafuna ndi mtima wonse.” (Aheb. 11:​1, 6) Tikamakhulupirira kwambiri kuti Yehova alipo m’pamenenso timakhulupirira kwambiri kuti iye adzakwaniritsa zonse zimene analonjeza. Kuti tipitirize kukhala ndi chiyembekezo cholimba tizipemphera kwa Yehova komanso kuwerenga Mawu ake. Ngakhale kuti sitingathe kumuona Yehova, tingakhale naye pa ubwenzi. Tingalankhule naye m’pemphero ndipo sitikayikira kuti atimvetsera.—Yer. 29:​11, 12. w22.10 26-27 ¶11-13

Lachinayi, August 8

Yobu anayamba kulankhula ndi kutemberera tsiku limene anabadwa.—Yobu 3:1.

Yerekezani kuti mukuona zomwe zikuchitika. Yobu wakhala paphulusa ndipo akumva ululu kwambiri. (Yobu 2:8) Anzake akupitirizabe kunena kuti iye si munthu wabwino ndiponso kuti zonse zomwe anachita n’zopanda phindu. Mayesero ake akumulemera ngati miyala ikuluikulu pomwe akupitiriza kumva chisoni kwambiri chifukwa cha imfa ya ana ake. Poyamba Yobu sakulankhulapo chilichonse. (Yobu 2:13) Ngati anzake a Yobuwo akuganiza kuti iye wakhala chete posonyeza kuti wasiya Mlengi wake, akudzinamiza. Pa nthawi ina Yobu, mwina podzutsa mutu n’kuyang’ana anzake abodzawo, akunena kuti: “Mpaka ndidzamwalire, sindidzasiya kukhala wokhulupirika.” (Yobu 27:5) N’chiyani chinathandiza Yobu kupitirizabe kukhala wolimba pa mavuto onse omwe anakumana nawo? Ngakhale pamene zinthu zinafika povuta kwambiri sanasiye kuyembekezera kuti Mulungu wake wachikondi amuthandiza. Ankadziwa kuti ngakhale atamwalira, Yehova adzamuukitsa.—Yobu 14:​13-15. w22.06 22 ¶9

Lachisanu, August 9

Koma inu muzipemphera chonchi: “Atate wathu wakumwamba, dzina lanu liyeretsedwe. Ufumu wanu ubwere. Zofuna zanu zichitike.”—Mat. 6:​9, 10.

Tinapatsidwa mwayi wamtengo wapatali kwambiri wolankhulana m’pemphero ndi Mlengi wakumwamba ndi dziko lapansi. Tangoganizani, tingathe kumuuza Yehova zakukhosi kwathu nthawi ina iliyonse komanso m’chilankhulo chilichonse. Tikhoza kupemphera kwa iye kaya tili m’chipatala kapena m’ndende n’kumakhulupirira kuti Atate wathu wachikondiyu atimvetsera. Sitimaona mopepuka mwayi umenewu. Mfumu Davide inkayamikira mwayi wa pemphero. Iye anaimbira Yehova kuti: “Pemphero langa likhale ngati zofukiza zokonzedwa pamaso panu.” (Sal. 141:​1, 2) M’nthawi ya Davide, zofukiza zopatulika zomwe ansembe ankagwiritsa ntchito polambira zinkakonzedwa mosamala kwambiri. (Eks. 30:​34, 35) Potchula zofukiza, Davide ankatanthauza kuti ankaganizira bwino zomwe akufuna kulankhula m’pemphero kwa Atate wake wakumwamba. Zimenezi ndi zomwe ifenso timafuna, kuti mapemphero athu azikhala osangalatsa kwa Yehova. w22.07 20 ¶1-2; 21 ¶4

Loweruka, August 10

“Kubwezera ndi kwanga, ndidzawabwezera ndine,” watero Yehova.—Aroma 12:19.

Yehova ndi amene ali woyenera kubwezera. Yehova sanatipatse udindo wobwezera munthu wina akatilakwira. (Aroma 12:​20, 21) Popeza sitiona moyenera zinthu chifukwa choti si ife angwiro, sitingaweruze bwino nkhani ngati mmene Mulungu angachitire. (Aheb. 4:13) Ndipo nthawi zina tingalephere kuweruza bwino chifukwa chosokonezedwa ndi mmene tikumvera. Yehova anauzira Yakobo kulemba kuti: “Munthu amene wakwiya sachita zinthu mogwirizana ndi chilungamo cha Mulungu.” (Yak. 1:20) Tingakhale otsimikiza kuti Yehova adzachita zoyenera ndipo adzaonetsetsa kuti chilungamo chachitika. Kukhululuka kumasonyeza kuti timakhulupirira kuti Yehova adzachita chilungamo. Tikamasiya nkhani m’manja mwa Yehova, timasonyeza kuti tikukhulupirira kuti iye adzachotsa zoipa zonse zobwera chifukwa cha uchimo. M’dziko latsopano zinthu zopweteka “sizidzakumbukiridwanso, kapena kuvutitsa maganizo” ngakhale pang’ono.—Yes. 65:17. w22.06 10-11 ¶11-12

Lamlungu, August 11

Anthu a mitundu yonse adzadana nanu chifukwa cha dzina langa.—Mat. 24:9.

Zimene anthu amachita podana nafe ndi umboni wakuti Yehova akusangalala nafe. (Mat. 5:​11, 12) Mdyerekezi ndi amene amachititsa kuti tizitsutsidwa. Koma iye alibe mphamvu poyerekeza ndi Yesu. Chifukwa choti Yesu akutithandiza, uthenga wabwino ukulalikidwa kwa anthu a mitundu yonse. Tiyeni tione umboni wake. Monga olalikira za Ufumu, vuto linanso lomwe timakumana nalo ndi lakuti timafunika kulalikira kwa anthu azilankhulo zosiyanasiyana. M’masomphenya amene anaonetsa mtumwi Yohane, Yesu anasonyeza kuti uthenga wabwino udzalalikidwabe ngakhale pali mavuto ambiri. (Chiv. 14:​6, 7) Motani? Timayesetsa mmene tingathere kuuza anthu ambiri uthenga wa Ufumu. Masiku ano, anthu padziko lonse angathe kuwerenga mabuku ofotokoza Baibulo pawebusaiti yathu ya jw.org muzilankhulo zoposa 1,000. Bungwe Lolamulira linavomereza kuti buku la Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale, lomwe timagwiritsa ntchito pophunzira Baibulo ndi anthu, limasuliridwe m’zilankhulo zoposa 700. w22.07 9 ¶6-7

Lolemba, August 12

Zinthu zimayenda bwino ngati pali alangizi ambiri.—Miy. 11:14.

Yesu ankachitira chifundo anthu. Mtumwi Mateyu analemba kuti: “Ataona chigulu cha anthu, iye anawamvera chisoni, chifukwa anali onyukanyuka komanso opanda wowasamalira ngati nkhosa zimene zilibe m’busa.” (Mat. 9:36) Ndiye kodi nayenso Yehova amamva bwanji? Yesu anati: “Atate wanga wakumwamba sakufuna kuti ngakhale mmodzi wa tiana timeneti awonongeke.” (Mat. 18:14) Zimenezitu n’zolimbikitsa kwambiri. Choncho tikamudziwa bwino Yesu, timayambanso kukonda kwambiri Yehova. Mungaphunzirenso mmene mungakulitsire chikondi komanso mungapite patsogolo mukamacheza ndi abale ndi alongo olimba mwauzimu mumpingo mwanu. Muziona mmene akusangalalira. Iwo samanong’oneza bondo chifukwa chosankha kutumikira Yehova. Muziwapempha kuti akufotokozereni zimene zakhala zikuwachitikira pa utumiki wawo. Mukafuna kusankha zochita pa nkhani inayake yofunika, muziwapempha malangizo. Muzikumbukira kuti “zinthu zimayenda bwino ngati pali alangizi ambiri.” w22.08 3 ¶6-7

Lachiwiri, August 13

Maso a Yehova ali pa olungama. —1 Pet. 3:12.

Tonsefe tidzakumana ndi mayesero ena ake. Komabe, sikuti timakhala tokhatokha polimbana ndi mayeserowo. Monga Atate wachikondi, Yehova nthawi zonse amatiyang’anira. Iye amakhala nafe pafupi ndipo ndi wokonzeka kumvetsera mapemphero athu opempha kuti atithandize ndipo amakhala wofunitsitsa kutithandiza. (Yes. 43:2) Sitikayikira kuti tingathe kulimbana ndi mavuto chifukwa iye watipatsa chilichonse chomwe timafunikira kuti tipirire. Yehova watipatsa mwayi wa pemphero, Baibulo, chakudya chauzimu chochuluka komanso abale ndi alongo achikondi omwe amatithandiza pa nthawi ya mavuto. Timayamikira kwambiri kuti Atate wathu wakumwamba amatiyang’anira. Iye “amachititsa kuti mitima yathu isangalale” (Sal. 33:21) Tingasonyeze kuti timayamikira chikondi cha Yehova pogwiritsa ntchito bwino zinthu zonse zimene amatipatsa kuti atithandize. Timafunikanso kuchita mbali yathu kuti Mulungu apitirize kutikonda. M’mawu ena, tikamayesetsa kumvera Yehova komanso kuchita zinthu zimene amaziona kuti n’zoyenera, iye adzatiyang’anira mpaka kalekale. w22.08 13 ¶15-16

Lachitatu, August 14

Mawu anu onse ndi choonadi chokhachokha.—Sal. 119:160.

Anthu ambiri masiku ano sadziwa yemwe angamukhulupirire. Iwo amakayikira ngati anthu omwe amawalemekeza monga andale, asayansi ndi amalonda amafunadi kuwathandiza. Kuwonjezera pamenepo, iwo sakhulupirira atsogoleri a zipembedzo zomwe zimati ndi za Chikhristu. Choncho n’zosadabwitsa kuti sakhulupirira Baibulo, buku lomwe atsogoleriwo amati amatsatira mfundo zake. Monga atumiki a Yehova, sitikayikira kuti iye ndi “Mulungu wachoonadi” komanso kuti nthawi zonse amatifunira zabwino. (Sal. 31:5; Yes. 48:17) Timadziwa kuti tingakhulupirire zomwe timawerenga m’Baibulo. Timavomereza zimene katswiri wina wa Baibulo analemba kuti: “Pa zimene Mulungu ananena palibe chilichonse chabodza kapena zimene sizingachitike mpang’ono pomwe. Anthu a Mulungu amakhulupirira chilichonse chomwe iye wanena chifukwa samukayikira ngakhale pang’ono.” w23.01 2 ¶1-2

Lachinayi, August 15

Tiyeni tiganizirane.—Aheb. 10:24.

Timalimbikitsa abale ndi alongo athu tikamawathandiza kuti azikhulupirira kwambiri Yehova. Ena amanyozedwa ndi anthu omwe si a Mboni. Enanso akudwala matenda aakulu kapena akuvutika maganizo chifukwa chokhumudwa ndi zinazake. Palinso ena omwe akhala akutumikira Yehova kwa zaka zambiri ndipo kwa nthawi yaitali akhala akuyembekezera mapeto a dzikoli. Zinthu ngati zimenezi zingayese chikhulupiriro cha Akhristu masiku ano. Akhristu a mu nthawi ya atumwi ankakumananso ndi mavuto ngati amenewa. Mtumwi Paulo anagwiritsa ntchito Malemba pothandiza abale ndi alongo ake kulimbitsa chikhulupiriro chawo. Mwachitsanzo, n’kutheka kuti Akhristu omwe anali Ayuda ankavutika kuyankha achibale awo akamawanyoza ponena kuti Chiyuda ndiye chipembedzo choona osati Chikhristu. N’zodziwikiratu kuti kalata ya Paulo yopita kwa Aheberi inalimbikitsa kwambiri Akhristu amenewa. (Aheb. 1:​5, 6; 2:​2, 3; 9:​24, 25) Mfundo zokhutiritsa zomwe iye anawalembera zikanawathandiza kuti aziyankha anthu omwe ankawatsutsa. w22.08 23-24 ¶12-14

Lachisanu, August 16

Munthu amene amakhulupirira Yehova komanso amene amadalira Yehova, ndi amene amadalitsidwa.—Yer. 17:7.

Anthu m’dziko la Satanali sadziwa amene ayenera kumukhulupirira. Nthawi zambiri iwo amakhumudwitsidwa ndi amalonda, andale komanso atsogoleri azipembedzo. Zimenezi zimachititsa kuti asamakhulupirirenso anzawo, anthu oyandikana nawo ngakhalenso achibale awo. Izitu siziyenera kutidabwitsa. Baibulo linaneneratu kuti: “Masiku otsiriza . . . anthu adzakhala . . . osakhulupirika, . . . onenera ena zoipa, . . . [ndiponso] ochitira anzawo zoipa.” M’mawu ena, anthu amasonyeza makhalidwe a mulungu wa nthawi ino, yemwe ndi wosadalirika. (2 Tim. 3:​1-4; 2 Akor. 4:4) Monga Akhristu, timadziwa kuti tingakhulupirire kwambiri Yehova. Sitikayikira kuti iye amatikonda ndiponso kuti ‘sadzasiya’ anthu omwe ndi anzake. (Sal. 9:10) Tingakhulupirirenso Khristu Yesu chifukwa anapereka moyo wake kuti atiwombole. (1 Pet. 3:18) Ndiponso zimene zakhala zikuchitika pa moyo wathu zimatithandiza kukhulupirira kuti Baibulo limapereka malangizo odalirika.—2 Tim. 3:​16, 17. w22.09 2 ¶1-2

Loweruka, August 17

Wosangalala ndi aliyense amene amaopa Yehova, amene amayenda m’njira za Mulungu.—Sal. 128:1.

Chimwemwe chenicheni sichimangotanthauza kusangalala kwakanthawi, koma chimakhalapo nthawi zonse. N’chifukwa chiyani tikutero? Yesu anafotokoza pa ulaliki wake wapaphiri kuti: “Osangalala ndi anthu amene amazindikira zosowa zawo zauzimu.” (Mat. 5:3) Yesu ankadziwa kuti anthu analengedwa kuti azifunitsitsa kudziwa ndi kulambira Mlengi wawo Yehova. Chimenechi ndiye ‘chosowa chathu chauzimu.’ Popeza kuti Yehova ndi “Mulungu wachimwemwe,” anthu amene amamulambira angathenso kukhala osangalala. (1 Tim. 1:11) Kodi timafunikira kuti zinthu zizitiyendera bwino kuti tikhale osangalala? Ayi. Mu ulaliki wake, Yesu ananena kuti ngakhale anthu amene “akumva chisoni,” angathe kukhala osangalala. Iye ananenanso zomwezi ponena za ‘anthu amene akuzunzidwa chifukwa cha chilungamo.’ (Mat. 5:​4, 10, 11) Yesu anaphunzitsa kuti sikuti chimwemwe chenicheni chimabwera zinthu zikamatiyendera bwino pa moyo. M’malomwake, chimapezeka tikamazindikira zosowa zathu zauzimu komanso kukhala pa ubwenzi wabwino ndi Mulungu.—Yak. 4:8. w22.10 6 ¶1-3

Lamlungu, August 18

Munthu amene alidi wozindikira amakhala chete.—Miy. 11:12.

Kuzindikira kungamuthandize Mkhristu kudziwa “nthawi yokhala chete ndi nthawi yolankhula.” (Mlal. 3:7) M’zikhalidwe zina muli mawu odziwika bwino akuti, “kulankhula kuli ngati siliva koma kukhala chete kuli ngati golide.” M’mawu ena, pali nthawi imene zingakhale bwino kukhala chete m’malo molankhula. Taganizirani chitsanzo ichi: Mkulu wina wodziwa zambiri kawirikawiri amapemphedwa kukathandiza mipingo ina pa nkhani zovuta. Ponena za m’baleyu, mkulu mnzake ananena kuti, “Nthawi zonse amakhala wosamala kuti asamaulule nkhani zachinsinsi zokhudza mipingo ina.” Popeza kuti mkuluyu amachita zinthu mozindikira, akulu anzake mumpingo wawo amamulemekeza kwambiri. Iwo amamudalira kuti sangaulule nkhani zawo zachinsinsi kwa ena. Kuona mtima ndi khalidwe lina lofunika kuti tikhale odalirika. Timakhulupirira munthu woona mtima chifukwa timadziwa kuti nthawi zonse amalankhula zoona.—Aef. 4:25; Aheb. 13:18. w22.09 12 ¶14-15

Lolemba, August 19

Palibe nzeru kapena kuzindikira, kapena malangizo amene angalepheretse zimene Yehova amafuna.—Miy. 21:30.

Anthu ambiri safuna kumvetsera pamene nzeru yeniyeni “ikufuula mumsewu.” (Miy. 1:20) Baibulo limasonyeza kuti pali magulu atatu a anthu amene safuna kupeza nzeru: “osadziwa zinthu,” “onyoza,” ndi “opusa.” (Miy. 1:​22-25) Anthu “osadziwa zinthu” ndi amene amangokhulupirira zilizonse zimene amva ndiponso amapusitsidwa mosavuta. (Miy. 14:15) Mwachitsanzo, taganizirani za anthu mamiliyoni omwe amapusitsidwa ndi atsogoleri achipembedzo komanso andale. Anthu ena amakhumudwa akadziwa kuti apusitsidwa ndi atsogoleri ngati amenewa. Koma anthu otchulidwa pa Miyambo 1:​22, amasankha kukhala osadziwa chifukwa chakuti n’zimene amafuna. (Yer. 5:31) Iwo safuna kudziwa zimene Baibulo limanena kapena kutsatira malamulo ake. Ife sitikufuna kukhala ngati anthu amenewa omwe amasankha kukhala osadziwa.—Miy. 1:32; 27:12. w22.10 19 ¶5-7

Lachiwiri, August 20

[Muzigonjera] ulamuliro uliwonse wokhazikitsidwa ndi anthu.—1 Pet. 2:13.

Gulu la Mulungu limatipatsa malangizo pofuna kutiteteza. Nthawi zonse timalimbikitsidwa kuti tiyenera kupereka ma adiresi ndi manambala a foni amene tikugwiritsa ntchito panopa kwa akulu n’cholinga choti adzathe kulankhula nafe pakachitika ngozi. Mwina tingapatsidwenso malangizo oti tikhale malo otetezeka, tichoke m’deralo komanso okhudza mmene tingalandirire zinthu zofunika pa moyo kapenanso mmene tingathandizire ena. Ngati sitingamvere, tingaike pangozi moyo wathu komanso wa akuluwo omwe amatiyang’anira. (Aheb. 13:17) Abale ndi alongo omwe anathawa kwawo chifukwa cha ngozi zam’chilengedwe kapena zipolowe amayesetsa kusintha kuti azolowere moyo wawo watsopano ndipo amayambiranso mwamsanga kuchita zinthu zokhudza kulambira. Mofanana ndi Akhristu a mu nthawi ya atumwi omwe anabalalitsidwa chifukwa chozunzidwa, iwo amapitiriza ‘kulalikira uthenga wabwino wa mawu a Mulungu.’ (Mac. 8:4) Kulalikira kumawathandiza kuti aziganizira kwambiri za Ufumu osati mavuto awo, zomwe zachititsa kuti apitirizebe kukhala osangalala komanso ndi mtendere. w22.12 19 ¶12-13

Lachitatu, August 21

Yehova ali kumbali yanga, sindidzaopa.—Sal. 118:6.

Yehova amationa kuti aliyense payekha ndi wamtengo wapatali. Asanatume atumwi ake kuti akalalikire, Yesu anawathandiza kuti asamaope anthu otsutsa. (Mat. 10:​29-31) Iye anawauza za mpheta, zomwe zinali mbalame zodziwika kwambiri ku Isiraeli. Mbalame zimenezi zinali zotsika mtengo m’nthawi ya Yesu. Iye anauza ophunzira ake kuti: “Palibe ngakhale imodzi imene idzagwa pansi Atate wanu osadziwa.” Kenako anawonjezera kuti: “Ndinu ofunika kwambiri kuposa mpheta zambiri.” Apa Yesu anatsimikizira ophunzira akewo kuti Yehova amaona kuti aliyense payekha ndi wofunika kwambiri, choncho sankafunika kuopa kuzunzidwa. N’zosakayikitsa kuti ophunzirawo ankakumbukira mawu a Yesuwa akaona mpheta pamene ankagwira ntchito yolalikira m’matauni ndi m’midzi. Nthawi iliyonse yomwe mwaona mbalame yaing’ono, muzikumbukira kuti Yehova amakuonani kuti ndinu wamtengo wapatali panokha chifukwa inunso “ndinu ofunika kwambiri kuposa mpheta zambiri.” Mothandizidwa ndi iye, simungamaope anthu ena akamakutsutsani. w23.03 18 ¶12

Lachinayi, August 22

Mwachititsa kuti Farao ndi atumiki ake aipidwe nafe, moti mwawapatsa lupanga m’manja mwawo kuti atiphe.—Eks. 5:21.

Nthawi zina timakumana ndi mavuto monga kutsutsidwa ndi achibale kapena kutha kwa ntchito. Ngati tapirira vuto linalake kwa nthawi yaitali, tikhoza kufooka n’kuyamba kumaona kuti tilibe chiyembekezo. Satana amapezerapo mwayi wotichititsa kuti tizikayikira ngati Yehova amatikonda. Iye amafuna kuti tiziona kuti mavutowo akuchititsidwa ndi Yehova kapena gulu lake. Zofanana ndi zimenezi zinachitikirapo Aisiraeli ku Iguputo. Poyamba iwo ankakhulupirira kuti Yehova anatumiza Mose ndi Aroni kuti awalanditse ku ukapolo. (Eks. 4:​29-31) Koma Farao atachititsa kuti mavuto awo awonjezereke, iwo anayamba kuimba mlandu Mose ndi Aroni. (Eks. 5:​19, 20) Iwo ankaimba mlandu atumiki okhulupirika a Yehova. Zimenezitu zinali zomvetsa chisoni. Ngati mwakhala mukupirira mavuto enaake kwa nthawi yaitali, muzipemphera kwa Yehova ndi mtima wonse kuti akuthandizeni. w22.11 15 ¶5-6

Lachisanu, August 23

Ndithudi ndikukuuzani, nthawi ikubwera ndipo ndi inoyi, pamene akufa adzamva mawu a Mwana wa Mulungu ndipo amene akumvera adzakhala ndi moyo. —Yoh. 5:25.

Yehova ndi Wopatsa Moyo ndipo ali ndi mphamvu yobwezeretsa moyo kwa amene anamwalira. Iye anapatsa mphamvu Eliya kuti aukitse mwana wa mkazi wa ku Zarefati. (1 Maf. 17:​21-23) Patapita nthawi, mneneri Elisa mothandizidwa ndi Mulungu anaukitsa mwana wa mkazi wa Chisunemu. (2 Maf. 4:​18-20, 34-37) Kuukitsidwa kwa anthu amenewa ndi enanso kunasonyeza kuti Yehova ali ndi mphamvu yotha kubwezeretsa moyo. Yesu ali padzikoli anasonyeza kuti Atate wake anamupatsa mphamvu zimenezi. (Yoh. 11:​23-25, 43, 44) Panopa Yesu ali kumwamba, ndipo anapatsidwa “ulamuliro wonse . . . kumwamba ndi padziko lapansi.” Choncho iye angathe kukwaniritsa lonjezo lakuti “onse amene ali m’manda achikumbutso” adzaukitsidwa ndipo adzakhala ndi chiyembekezo chokhalabe ndi moyo mpaka kalekale.—Mat. 28:18; Yoh. 5:​26-29. w22.12 5 ¶10

Loweruka, August 24

A nyumba ya Isiraeli akakana kukumvera, chifukwa iwo sakufuna kundimvera.—Ezek. 3:7.

Pokana kumvera Ezekieli, anthuwo ankakana Yehova. Mawu a mulemba la lerowa anathandiza Ezekieli kudziwa kuti kukana kumvetsera kwa anthuwo, sikunkatanthauza kuti iye walephera utumiki wake wa uneneri. Yehova anatsimikiziranso Ezekieli kuti zinthu zimene ankalalikira zikadzakwaniritsidwa, iwo “adzadziwa kuti pakati pawo panali mneneri.” (Ezek. 2:5; 33:33) N’zosakayikitsa kuti mawu olimbikitsa amenewa anamuthandiza kukhala ndi mphamvu zoti akwaniritsire utumiki wake. Nafenso timapeza mphamvu chifukwa choti tinatumidwa ndi Yehova. Iye amatilemekeza potitchula kuti “mboni” zake. (Yes. 43:10) Umenewutu ndi mwayi waukulu kwambiri. Monga mmene Yehova anauzira Ezekieli kuti: “Usaope,” Yehova akutiuzanso kuti: ‘Musachite mantha.’ (Ezek. 2:6) N’chifukwa chiyani sitiyenera kuopa anthu amene amatitsutsa? Mofanana ndi Ezekieli, tatumidwa ndi Yehova ndipo iye amatithandiza.—Yes. 44:8. w22.11 3-4 ¶4-5

Lamlungu, August 25

Wokhulupirika amasunga chinsinsi.—Miy. 11:13.

Masiku ano timayamikira kwambiri kuti tili ndi akulu ndi atumiki othandiza odalirika. Abale okhulupirikawa amatisamalira bwino kwambiri ndipo timayamikira Yehova chifukwa cha zimenezi. Koma kodi ifeyo tingasonyeze m’njira ziti kuti ndife odalirika? Timakonda abale ndi alongo athu ndipo timachita chidwi ndi zimene zikuchitika pa moyo wawo. Komabe sitiyenera kupitirira malire ndipo tizilemekeza nkhani zawo zachinsinsi. Ena mumpingo wa munthawi ya atumwi ankakonda “miseche kulowerera nkhani za eni komanso kulankhula zinthu zimene sayenera kulankhula.” (1 Tim. 5:13) Ifeyo sitingafune kukhala ngati anthu amenewa. Koma tiyerekeze kuti wina watiuza nkhani yake yachinsinsi ndipo watipempha kuti tisauze aliyense. Mwina mlongo wina watifotokozera za matenda ena ake amene akudwala kapena mayesero ena ake amene akukumana nawo ndipo akufuna kuti tisauze anthu ena. Zikatero tiyenera kuchita zimene watipemphazo. w22.09 10 ¶7-8

Lolemba, August 26

Khalani munthu watsopano posintha kwambiri maganizo anu.—Aroma 12:2.

Mawu a Chigiriki omwe anamasuliridwa kuti “kusintha maganizo anu” angamasuliridwenso kuti “kukonzanso maganizo anu.” Choncho, zimenezi sizikutanthauza kuti tizingochita ntchito zabwino zochepa chabe. M’malomwake, tiyenera kumafufuza umunthu wathu wamkati komanso kumasintha pamene pakufunikira kutero, n’cholinga choti zochita zathu zizigwirizana kwambiri ndi mfundo za Yehova. Tiyenera kuchita zimenezi, osati kamodzi kokha koma nthawi zonse. Tikadzakhala angwiro, nthawi zonse tizidzachita zinthu zosangalatsa Yehova. Koma panopa tiyenera kuchita khama kuti tizichita zomusangalatsa. Taonani kugwirizana komwe kulipo pakati pa kusintha maganizo ndi kuzindikira chifuniro cha Mulungu, monga mmene Paulo analembera pa Aroma 12:2. M’malo mongotengera zochita ndi kaganizidwe ka anthu a m’dzikoli, choyamba tiyenera kudzifufuza ngati zolinga zathu komanso zimene timasankha zimatsogoleredwa ndi maganizo a Mulungu osati a dzikoli. w23.01 8-9 ¶3-4

Lachiwiri, August 27

Umutulire Yehova nkhawa zako, ndipo iye adzakuthandiza. Iye sadzalola kuti munthu wolungama agwe.—Sal. 55:22.

Kodi Yehova amalowererapo pa zilizonse zimene zimatichitikira? Kodi ndi amene amachititsa zilizonse zomwe zimachitika pa moyo wathu, moti zoipa zonse zimatichitikira pachifukwa chabwino? Ayi, Baibulo silifotokoza zimenezo. (Mlal. 8:9; 9:11) Komabe timadziwa kuti tikamakumana ndi mayesero, Yehova amadziwa ndipo amamvetsera kufuula kwathu kopempha thandizo. (Sal. 34:15; Yes. 59:1) Kuwonjezera pamenepo, Yehova amatithandiza kuti tipirire mavuto alionse. Motani? Njira imodzi imene Yehova amatithandizira ndi kutitonthoza komanso kutilimbikitsa, ndipo nthawi zambiri amachita zimenezo pa nthawi yoyenera. (2 Akor. 1:​3, 4) Kodi mukukumbukira nthawi yomwe Yehova anakuthandizani pokutonthozani komanso kukulimbikitsani pamene munkafunikira kwambiri zimenezi? Nthawi zambiri timazindikira mmene Yehova watithandizira kupirira mayesero enaake pambuyo poti mayeserowo atha. w23.01 17-18 ¶13-15

Lachitatu, August 28

Chilombo chimene chinalipo, koma panopa kulibe, . . . chikupita kuchiwonongeko.—Chiv. 17:11.

Chilombo chimenechi chimaoneka mofanana kwambiri ndi chilombo cha mitu 7, koma kusiyana kwake n’kwakuti chilombochi chimaoneka chofiira kwambiri. Chimatchulidwa kuti “chifaniziro cha chilombocho” ndipo chikufotokozedwa kuti ndi “mfumu ya 8.” (Chiv. 13:​14, 15; 17:​3, 8) ‘Mfumuyi’ imafotokozedwa kuti inalipo, kenako panalibe ndipo pambuyo pake inaonekeranso. Mfundo imeneyitu ikugwirizana kwambiri ndi zimene zinachitikira bungwe la United Nations, lomwe limalimbikitsa zolinga za maboma a padzikoli. Poyamba bungweli linkatchulidwa kuti League of Nations. Kenako linatha pa nthawi ya nkhondo yachiwiri ya padziko lonse ndipo pambuyo pake linakhazikitsidwanso n’kuyamba kudziwika kuti United Nations. Pogwiritsa ntchito mfundo zabodza, zilombozi zimalimbikitsa anthu kuti azitsutsa Yehova ndi anthu ake. Mophiphiritsa, zimasonkhanitsa “mafumu a dziko lonse lapansi” ku nkhondo ya Aramagedo, yomwe ndi “tsiku lalikulu la Mulungu Wamphamvuyonse.”—Chiv. 16:​13, 14, 16. w22.05 10 ¶10-11

Lachinayi, August 29

Umawerengamo zotani?—Luka 10:26.

Yesu ataphunzira kuwerenga payekha Malemba Opatulika, sikuti iye anangofika powadziwa bwino, koma ankawakondanso n’kumawalola kuti azimutsogolera. Mwachitsanzo, takumbukirani zimene zinachitika m’kachisi pamene Yesu anali ndi zaka 12 zokha. Aphunzitsi omwe anali odziwa bwino Chilamulo cha Mose, “anadabwa kwambiri ndi mayankho ake komanso poona kuti anali womvetsa zinthu kwambiri.” (Luka 2:​46, 47, 52) Ifenso tingafike podziwa komanso kukonda Mawu a Mulungu tikamawawerenga nthawi zonse. Tingaphunzirepo kanthu pa zimene Yesu anauza anthu odziwa Chilamulo omwe akuphatikizapo alembi, Afarisi komanso Asaduki. Nthawi zonse atsogoleri achipembedzo amenewa ankawerenga Malemba, koma sankapindula ndi zimene ankawerengazo. Yesu anatchula zinthu zitatu zimene zinkalepheretsa anthu amenewa kuti azipindula ndi Malemba. Zimene anawauza zingatithandize kuti tiwonjezere luso lathu n’cholinga choti (1) tizimvetsa zimene tikuwerenga, (2) tizipeza mfundo zothandiza za choonadi ndiponso (3) tizilola kuti Mawu a Mulungu azititsogolera. w23.02 8-9 ¶2-3

Lachisanu, August 30

Munthu wochenjera akaona tsoka amabisala.—Miy. 22:3.

Zinthu zina zimene tiyenera kupewa ndi monga kukopana, kuledzera, kudya kwambiri, kulankhula mawu omwe angakhumudwitse ena komanso kuonera zosangalatsa zachiwawa, zolaula ndi zinthu zina zotere. (Sal. 101:3) Mdyerekezi nthawi zonse amafunafuna mipata yoti awononge ubwenzi wathu ndi Yehova. (1 Pet. 5:8) Ngati sitingakhale maso, Satana angadzale m’mitima mwathu mbewu za nsanje, chinyengo, dyera, chidani, kudzikuza komanso mkwiyo. (Agal. 5:​19-21) Ngati sitingachitepo kanthu mwamsanga kuzizula mumtima mwathu, zingapitirize kukula ngati chomera chakupha ndipo zingayambitse mavuto. (Yak. 1:​14, 15) Vuto lina losaonekera ndi kugwirizana ndi anthu oipa. Tizikumbukira kuti timatengera zochita za anthu amene timacheza nawo kwambiri. (1 Akor. 15:33) Tikamasamala ndi mmene timachitira zinthu, tidzapewa kugwirizana ndi anthu amene satsatira mfundo za Yehova. (Luka 21:34; 2 Akor. 6:15) Tidzaona vuto lomwe lingakhalepo ndipo tidzalipewa. w23.02 16 ¶7; 17 ¶10-11

Loweruka, August 31

Kukonda Mulungu kumatanthauza kutsatira malamulo ake.—1 Yoh. 5:3.

Chikondi chanu kwa Yehova chakula pamene mwakhala mukuphunzira zambiri zokhudza iye. Mosakayikira mumafuna kukhala naye pa ubwenzi wolimba panopa komanso mpaka kalekale. Ndipo n’zotheka. Mokoma mtima iye amakulimbikitsani kuti muzichita zinthu zosangalatsa mtima wake. (Miy. 23:​15, 16) Mungachite zimenezi osati ndi mawu okha komanso ndi zochita zanu. Zimene mumachita pa moyo wanu zingasonyeze ngati mumakondadi Yehova. Chimenechi ndi cholinga chabwino kwambiri chimene mungasankhe pa moyo wanu. Kodi mungasonyeze bwanji kuti mumakonda Yehova? Choyamba muyenera kupereka pemphero panokha losonyeza kuti mukudzipereka kwa Mulungu woona yekha. (Sal. 40:8) Kenako muyenera kusonyeza poyera kudziperekako pobatizidwa. Nthawiyi imakhala yosangalatsa komanso yofunika kwambiri pa moyo wanu. Mumayamba moyo watsopano osati wongochita zofuna zanu zokha koma za Yehova. (Aroma 14:8; 1 Pet. 4:​1, 2) Imeneyitu ingaoneke ngati nkhani yaikulu ndipo ndi mmene ililidi. Komatu kuchita zimenezi kumakutsegulirani mwayi woti mukhale ndi moyo wabwino kwambiri. w23.03 5-6 ¶14-15

    Mabuku a Chichewa (1974-2026)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena