September
Lamlungu, September 1
Ngati munthu akuganiza kuti amalambira Mulungu, koma satha kulamulira lilime lake, akudzipusitsa ndipo kulambira kwake n’kopanda phindu.—Yak. 1:26.
Tikamagwiritsa ntchito bwino mphatso yakulankhula timasonyeza kuti ndife atumiki a Yehova. Timathandiza ena kuona kusiyana kumene kulipo “pakati pa munthu amene akutumikira Mulungu ndi amene sakumutumikira.” (Mal. 3:18) Zimenezi ndi zimene zinachitikira mlongo wina dzina lake Kimberly. Iye anapatsidwa zoti achite limodzi ndi mnzake wa m’kalasi. Atamaliza, mnzakeyo anaona kuti Kimberly anali wosiyana kwambiri ndi ana ena pasukulupo. Iye sankanenera anzake zoipa koma ankalankhula mokoma mtima ndipo sankagwiritsa ntchito mawu oipa. Mnzake wa Kimberly anachita chidwi ndi zimenezi ndipo anavomera kuti aziphunzira Baibulo. Yehovatu amasangalala kwambiri tikamalankhula m’njira imene ingachititse kuti anthu ena aphunzire choonadi. Tonsefe tikufuna kuti tizilankhula m’njira imene imamulemekeza. w22.04 5-6 ¶5-7
Lolemba, September 2
Azimayi . . . ankatumikira Yesu ndi atumwiwo pogwiritsa ntchito chuma chawo.—Luka 8:3.
Yesu anathandiza Mariya Mmagadala, yemwe ankazunzidwa ndi ziwanda 7. Kuyamikira kunachititsa kuti iye akhale wotsatira wa Yesu komanso kuti azithandiza Yesu pa ntchito yolalikira. (Luka 8:1-3) Ngakhale kuti Mariya ankayamikira mochokera pansi pa mtima zimene Yesu anamuchitira, n’kutheka kuti sankadziwa kuti iye adzamupatsanso mphatso yaikulu m’tsogolo. Yesu anali kudzapereka moyo wake “kuti aliyense womukhulupirira” adzapeze moyo wosatha. (Yoh. 3:16) Komabe, Mariya anasonyezanso kuti ankayamikira Yesu pokhala wokhulupirika. Pamene Yesu ankavutika ndi ululu pamtengo wozunzikirapo, Mariya anaima chapafupi kuti alimbikitse Yesuyo ndi anthu ena. (Yoh. 19:25) Yesu atafa, Mariya ndi amayi ena awiri anabweretsa zonunkhira zoti apake thupi lake asanaliike m’manda. (Maliko 16:1, 2) Iye anali ndi mwayi wokumana ndi Yesu komanso kulankhula naye ataukitsidwa, mwayi womwe ophunzira ambiri analibe.—Yoh. 20:11-18. w23.01 27 ¶4
Lachiwiri, September 3
Ndikanakonda ukanakhala wozizira kapena wotentha.—Chiv. 3:15.
Sitiyenera kumangodalira zimene tinachita potumikira Yehova m’mbuyomu. Ngakhale kuti tingalephere kuchita zambiri ngati mmene tinkachitira kale, tiyenera kutanganidwa kwambiri mu “ntchito ya Ambuye” komanso kukhalabe maso mpaka pamapeto. (1 Akor. 15:58; Mat. 24:13; Maliko 13:33) Tiyenera kukhala akhama komanso odzipereka pa kulambira kwathu. Uthenga umene Yesu anatumiza kumpingo wa ku Laodikaya unasonyeza kuti kumeneko kunali vuto lina. Iwo anali ‘ofunda’ pa kulambira kwawo. Chifukwa choti sankachita khama, Yesu anawauza kuti anali ‘ovutika komanso omvetsa chisoni.’ Iwo ankafunika kumachita khama kwambiri polambira Yehova. (Chiv. 3:16, 17, 19) Kodi ifeyo tikuphunzirapo chiyani? Ngati khama lathu layamba kuchepa, tiyenera kuganizira ndiponso kuyamikira kwambiri zinthu zabwino zimene Yehova watipatsa kudzera m’gulu lake. (Chiv. 3:18) Sitiyenera kulola kuti kufunafuna moyo wapamwamba kutisokoneze mpaka kuyamba kuika zinthu zokhudza Yehova pamalo achiwiri pa moyo wathu. w22.05 3-4 ¶7-8
Lachitatu, September 4
Buku la chikumbutso linayamba kulembedwa pamaso pake. Buku limeneli linali lonena za anthu oopa Yehova.—Mal. 3:16.
Kwa zaka masauzande ambiri, Yehova wakhala akulemba buku lapadera. M’bukuli muli mayina ambiri ndipo dzina loyamba ndi la mboni yokhulupirika yoyamba, Abele. (Luka 11:50, 51) Kuchokera nthawi imeneyo, Yehova wakhala akuwonjezera mayina m’bukuli ndipo panopa muli mayina mamiliyoni. M’Baibulo, bukuli limatchulidwa kuti “buku la chikumbutso,” ‘buku la moyo’ ndiponso ‘mpukutu wa moyo.’ (Mal 3:16; Chiv. 3:5; 17:8) M’bukuli muli mayina a anthu omwe amalambira Yehova komanso kulemekeza dzina lake. Iwo akuyembekezera kudzalandira moyo wosatha. Masiku anonso dzina lathu lingalembedwe m’bukuli ngati titayesetsa kukhala pa ubwenzi wabwino ndi Yehova, zomwe zimatheka chifukwa cha nsembe ya dipo ya Mwana wake Yesu Khristu. (Yoh. 3:16, 36) Tonsefe, kaya tikuyembekera kukakhala kumwamba kapena kudzakhala padzikoli, timafunitsitsa dzina lathu litalembedwa m’bukuli. w22.09 14 ¶1-2
Lachinayi, September 5
Mdyerekezi, amene ankawasocheretsa, adzaponyedwa m’nyanja yamoto ndi sulufule.—Chiv. 20:10.
Buku la Chivumbulutso limafotokozanso za “chinjoka chachikulu chofiira.” (Chiv. 12:3) Chinjokachi chinamenyana ndi Yesu ndi angelo ake. (Chiv. 12:7-9) Chinapita kukaukira anthu a Mulungu komanso chinapereka ulamuliro kwa zilombo, kapena kuti maboma a anthu. (Chiv. 12:17; 13:4) Kodi chinjoka chimenechi ndi ndani? Ndi “njoka yakale ija, amene ndi Mdyerekezi ndiponso Satana.” (Chiv. 12:9; 20:2) Iye ndi amene amatsogolera adani onse a Yehova. Kodi n’chiyani chidzachitikire chinjoka? Lemba la Chivumbulutso 20:1-3 limafotokoza kuti mngelo adzaponyera Satana kuphompho, zomwe zidzakhale ngati waikidwa m’ndende. Akadzamangidwa, iye ‘sadzatha kusocheretsanso mitundu ya anthu kufikira zitatha zaka 1000.’ Pamapeto pake Satana ndi ziwanda zake adzawonongedwa, zomwe zili ngati kuponyedwa “m’nyanja yamoto ndi sulufule.” Tangoganizani mmene zinthu zidzakhalire padzikoli popanda Satana ndi ziwanda zake. Imeneyitu idzakhala nthawi yosangalatsa kwambiri. w22.05 14 ¶19-20
Lachisanu, September 6
Azigwira ntchito molimbikira. Azigwira ntchito yabwino ndi manja ake kuti azitha kupeza zinthu zimene angathe kugawana ndi munthu wosowa.—Aef. 4:28.
Yesu anali wakhama pantchito. Ali wachinyamata ankagwira ntchito ya ukalipentala. (Maliko 6:3) N’zosakayikitsa kuti makolo ake ankayamikira powathandiza kupeza zofunikira zothandiza banja lawo lomwe linali lalikulu. Ndipo popeza anali wangwiro, ziyenera kuti zinthu zinkamuyendera bwino kwambiri pa ntchito yake ya ukalipentala. N’zosakayikitsa kuti iye ankasangalala ndi ntchitoyi. Ngakhale kuti ankachita khama kwambiri pa ntchito yakeyi, Yesu ankapeza nthawi yotumikira Yehova. (Yoh. 7:15) Pambuyo pake atayamba utumiki wa nthawi zonse, analangiza omvetsera ake kuti: “Musamagwire ntchito kuti mungopeza chakudya chimene chimawonongeka, koma kuti mupeze chakudya chokhalitsa, chimene chimabweretsa moyo wosatha.” (Yoh. 6:27) Ndipo pa ulaliki wake wa paphiri, Yesu ananena kuti: “Unjikani chuma chanu kumwamba.” (Mat. 6:20) Nzeru za Mulungu zimatithandiza kuti tiziona ntchito moyenera. Monga Akhristu, timalimbikitsidwa kuti tizigwira “ntchito molimbikira . . . , ntchito yabwino.” w22.05 22 ¶9-10.
Loweruka, September 7
Mayi ako adzasangalala.—Miy. 23:25.
A Yunike ankapereka chitsanzo chabwino kwa Timoteyo. Mosakayikira, iye ankaona kuti zochita za mayi ake zinkasonyeza kuti ankakonda kwambiri Yehova ndiponso kuti kutumikira Yehova kunkawathandiza kukhala osangalala. Mofanana ndi zimenezi, masiku ano alongo ambiri athandiza anthu a m’banja mwawo kuyamba kutumikira Yehova, “osati ndi mawu” koma zochita. (1 Pet. 3:1, 2) Inunso mungachite zimenezi. Motani? Muziona kuti ubwenzi wanu ndi Yehova ndi chinthu chofunika kwambiri. (Deut. 6:5, 6) Mofanana ndi azimayi ambiri, mumalolera kudzimana zinthu zambiri. Mumasala tulo ndipo mumagwiritsa ntchito nthawi, ndalama ndi zinthu zina kuti muzipezera ana anu zinthu zofunika pa moyo. Koma simuyenera kutanganidwa kwambiri ndi zinthu zimenezi mpaka kusoweratu nthawi yolimbitsa ubwenzi wanu ndi Yehova. Nthawi zonse muzipeza nthawi yopemphera panokha, kuphunzira Baibulo komanso kusonkhana. Mukamachita zimenezi, mudzalimbitsa ubwenzi wanu ndi Yehova komanso kupereka chitsanzo chabwino kwa anthu a m’banja lanu ndi ena. w22.04 16 ¶1; 19 ¶12-13
Lamlungu, September 8
Muchitepo kanthu posonyeza amene ali wolakwa n’kumubwezera mogwirizana ndi zochita zake komanso musonyeze amene ali wosalakwa n’kumupatsa mphoto.—1 Maf. 8:32.
Timapepukidwa mumtima chifukwa chodziwa kuti sitinapatsidwe udindo wovuta wosankha mmene anthu ayenera kuweruzidwira. Monga Woweruza Wamkulu, Yehova ndi amene adzagwire ntchito yofunikayi. (Aroma 14:10-12) Timakhala otsimikiza kuti iye nthawi zonse adzaweruza mogwirizana ndi mfundo zake zokhudza chabwino ndi choipa. (Gen. 18:25) Iye sadzachita zinthu zopanda chilungamo ngakhale pang’ono. Tikuyembekezera mwachidwi nthawi imene Yehova adzathetse mavuto obwera chifukwa chakuti anthufe ndi ochimwa. Pa nthawiyo, mavuto onse omwe anakhudza thanzi lathu komanso maganizo adzathetsedwa. (Sal. 72:12-14; Chiv. 21:3, 4) Sitidzakumbukiranso mavuto amenewa. Pamene tikuyembekezera kuti nthawi yosangalatsayi ifike, timathokoza kwambiri Yehova chifukwa amatithandiza kuti tizimutsanzira pa nkhani yokhululuka. w22.06 13 ¶18-19
Lolemba, September 9
Ndinu Woweruza wa dziko lonse lapansi. Ndiye kodi simuchita chilungamo? —Gen. 18:25.
Woweruza wabwino amafunika kudziwa bwino malamulo komanso kumvetsa bwino pa nkhani ya chabwino ndi choipa. Kodi woweruza wabwino amafunikiranso kukhala wotani? Amafunikanso azimvetsa bwino mfundo zonse za nkhani asanaweruze. Choncho Yehova ndi Woweruza wabwino chifukwa amadziwa chilichonse. Mosiyana ndi anthu oweruza, nthawi zonse Yehova amadziwa bwino mfundo za nkhani yomwe akufunika kuweruza. (Gen. 18:20, 21; Sal. 90:8) Iye amadziwa zoposa zimene anthu angaone kapena kumva. Amamvetsa bwino mmene munthu wachitira zinthu chifukwa cha chibadwa chake, mmene analeredwera, kumene amakhala, mmene amamvera komanso mmene amaganizira. Yehova amadziwanso zimene zili mumtima. Iye amamvetsa bwino zolinga, zolakalaka komanso zimene zimachititsa munthu aliyense kuchita zinazake. Palibe chomwe Yehova sachiona. (Aheb. 4:13) Choncho Yehova akamakhululuka, amakhala kuti akudziwa chilichonse chokhudza nkhaniyo. w22.06 4 ¶8-9
Lachiwiri, September 10
Munthu angapereke chilichonse chimene ali nacho kuti apulumutse moyo wake.—Yobu 2:4.
Tiyenera kukhala tcheru ndi njira zomwe Satana anagwiritsa ntchito poyesa Yobu chifukwa amazigwiritsanso ntchito masiku ano. Satana amanena kuti sititumikira Mulungu mochokera pansi pa mtima, ndipo tikhoza kulolera kusiya kumutumikira kuti tipulumutse moyo wathu. Iye amanenanso kuti Mulungu satikonda ndipo zonse zomwe timachita kuti timusangalatse alibe nazo ntchito. Popeza tinachenjezedwa, ife amene timayembekezera Yehova sitimapusitsidwa ndi mabodza a Satanawa. Tiziona mayesero omwe takumana nawo monga mwayi wathu wodziwira mmene tilili. Mayesero omwe Yobu anakumana nawo anamuthandiza kudziwa zinthu zomwe ankafunika kukonza pa moyo wake. Mwachitsanzo iye anazindikira kuti ankafunika kukulitsa khalidwe la kudzichepetsa. (Yobu 42:3) Ifenso tikakumana ndi mayesero tingadziwe zambiri zokhudza mmene tilili. Tikadziwa zofooka zathu tikhoza kuzikonza. w22.06 23 ¶13-14
Lachitatu, September 11
“Inu ndinu mboni zanga,” akutero Yehova. “Inde mtumiki wanga amene ndamusankha.”—Yes. 43:10.
Yehova amatitsimikizira kuti adzatithandiza. Mwachitsanzo, iye asananene kuti “Inu ndinu mboni zanga,” ananena kuti: “Ukamadzadutsa pamadzi, ine ndidzakhala nawe. Ukamadzawoloka mitsinje, madzi sadzakukokolola. Ukamadzayenda pamoto sudzapsa ndipo ngakhale lawi la moto silidzakuwaula.” (Yes. 43:2) Tikamachita utumiki wathu, nthawi zina timakumana ndi mavuto omwe ali ngati madzi osefukira komanso mayesero omwe ali ngati moto. Ngakhale zili choncho, Yehova amatithandiza kuti tipitirizebe kulalikira. (Yes. 41:13) Anthu ambiri masiku ano amakananso uthenga wathu. Timazindikira kuti kukana kwawo kumvetsera, sizitanthauza kuti talephera kugwira bwino ntchito yathu yolalikira. Timalimbikitsidwa komanso kupeza mphamvu podziwa kuti Yehova amasangalala tikapitiriza kulengeza uthenga wake mokhulupirika. Mtumwi Paulo ananena kuti: “Aliyense adzalandira mphoto mogwirizana ndi ntchito yake.”—1 Akor. 3:8; 4:1, 2. w22.11 4 ¶5-6
Lachinayi, September 12
Mukhale ndi khalidwe labwino pakati pa anthu am’dzikoli.—1 Pet. 2:12.
Masiku ano tikuona maulosi a m’Baibulo akukwaniritsidwa. Anthu “ochokera m’zilankhulo zonse za anthu a mitundu ina” akuphunzira kulankhula “chilankhulo choyera,” chomwe ndi mfundo za choonadi cha m’Baibulo. (Zek. 8:23; Zef. 3:9) Anthu oposa 8 miliyoni omwe ali m’mayiko 240, ali m’gulu la Yehova ndipo chaka chilichonse anthu ambiri amabatizidwa. N’zoona kuti anthuwo alipo ambiri, komabe chofunika kwambiri n’chakuti anthu amenewa asintha makhalidwe awo ndipo avala “umunthu watsopano.” (Akol. 3:8-10) Ambiri anasiya chiwerewere, chiwawa, tsankho komanso kukonda kwambiri dziko lawo. Ulosi wa pa Yesaya 2:4, ukukwaniritsidwa womwe umati, “sadzaphunziranso nkhondo.” Tikamayesetsa kuvala umunthu watsopano, timathandiza anthu kuti alowe m’gulu la Mulungu ndipo timasonyeza kuti tikutsatira mtsogoleri wathu Khristu Yesu. (Yoh. 13:35) Komatu zimenezi sikuti zimangochitika mwangozi. Yesu ndi amene amatithandiza. w22.07 9 ¶7-8
Lachisanu, September 13
Pemphero langa likhale ngati zofukiza zokonzedwa pamaso panu.—Sal. 141:2.
Tikamapemphera kwa Yehova tiyenera kuchita zinthu mwaulemu kwambiri. Taganizirani masomphenya ochititsa chidwi omwe Yesaya, Ezekieli, Danieli ndi Yohane anaonetsedwa. Ngakhale kuti masomphenyawo anali osiyana, panali chinthu china chofanana. Onsewa amasonyeza kuti Yehova ndi Mfumu yolemekezeka. Yesaya ‘anaona Yehova atakhala pampando wachifumu wolemekezeka umene unali pamalo wokwezeka.’ (Yes. 6:1-3) Ezekieli anaona Yehova atakhala pagaleta lake lakumwamba ndipo “pamalo onse omuzungulira panali powala ngati utawaleza.” (Ezek. 1:26-28) Danieli anaona “Wamasiku Ambiri” atavala zovala zoyera ndipo kumpando wake wachifumu kunkayaka moto. (Dan. 7:9, 10) Ndipo Yohane anaona Yehova atakhala pampando wake wachifumu utazunguliridwa ndi utawaleza wooneka ngati mwala wa emarodi. (Chiv. 4:2-4) Tikamaganizira ulemerero waukulu womwe Yehova ali nawo, timakumbutsidwa za mwayi wamtengo wapatali wolankhula naye m’pemphero komanso kufunika kochita zimenezo mwaulemu. w22.07 20 ¶3
Loweruka, September 14
[Samalani] ndi zachinyengo zimene anthu amaphunzitsa.—Aef. 4:14.
Achinyamata, Satana amayesetsa kuti akulepheretseni kupita patsogolo mwauzimu. Njira ina imene angachitire zimenezo ndi kukuchititsani kuti muzikayikira zinthu zina zimene Baibulo limaphunzitsa. Mwachitsanzo, mwina mukhoza kumva mfundo yosalemekeza Mulungu yakuti zinthu zinachita kusintha kuchokera ku zinthu zina. N’kutheka kuti muli wamng’ono munali musanaganizirepo kwambiri nkhani imeneyi. Koma pamene mukukula, mwayamba kuphunzira zimenezi kusukulu. Zimene aphunzitsi anu amanena polimbikitsa mfundoyi, zingaoneke ngati zomveka. Komabe n’kutheka kuti iwo sanafufuze kuti apeze umboni wotsimikizira kuti kuli Mlengi. Kumbukirani mfundo ya pa Miyambo 18:17, yomwe imati: “Woyamba kufotokoza mbali yake pa mlandu amaoneka ngati wolondola, mpaka mnzake atabwera n’kudzamufunsa mafunso.” M’malo momangokhulupirira zilizonse zimene mwamva kusukulu, muzifufuza mosamala mfundo za choonadi za m’Mawu a Mulungu komanso m’mabuku athu. w22.08 2 ¶2; 4 ¶8
Lamlungu, September 15
Uzitsatira bwinobwino zonse zimene zalembedwamo. Ukamatero, zizikuyendera bwino ndipo uzichita zinthu mwanzeru.—Yos. 1:8.
Timafuna kumvetsa tanthauzo la zimene tikuwerenga m’Mawu a Mulungu. Ngati sitingatero sitingapindule mokwanira. Mwachitsanzo, taganizirani zimene Yesu anakambirana ndi “munthu wina wodziwa Chilamulo.” (Luka 10:25-29) Pamene munthuyo anamufunsa zimene angachite kuti adzapeze moyo wosatha, Yesu anamuthandiza kupeza yankho m’Mawu a Mulungu pofunsa kuti: “Kodi m’Chilamulo analembamo chiyani? Umawerengamo zotani?” Munthuyo anayankha molondola potchula mawu a m’Malemba omwe amanena za kukonda Mulungu ndi anzathu. (Lev. 19:18; Deut. 6:5) Koma taonani zimene kenako ananena, iye anati: “Nanga mnzanga amene ndikuyenera kumukonda ndi ndani kwenikweni?” Munthuyo anasonyeza kuti sankamvetsa tanthauzo la zimene anawerenga. Choncho sankadziwa mmene angagwiritsire ntchito moyenera mfundo za m’Malemba amenewa pa moyo wake. Timafunika kuthandizidwa ndi Yehova kuti timvetse Malemba. Choncho muzimupempha mzimu woyera kuti ukuthandizeni kuika maganizo anu pa zimene mukuwerenga, ndipo muzimupemphanso kuti akuthandizeni kugwiritsa ntchito zomwe mwawerengazo. w23.02 9 ¶4-5
Lolemba, September 16
Akuyendabe m’choonadi.—3 Yoh. 4.
“Kodi munayamba bwanji choonadi?” N’zosakayikitsa kuti mwakhala mukufunsidwa funso limeneli kambirimbiri. Limeneli ndi limodzi mwa mafunso amene Mkhristu mnzathu angatifunse tikamafuna kudziwana. Timafuna kudziwa mmene abale ndi alongo athu anayambira kudziwa komanso kukonda Yehova ndipo ifenso timasangalala kuwafotokozera mmene timasangalalira chifukwa chodziwa choonadi. (Aroma 1:11) Kukambirana zimenezi kumatithandiza kupitiriza kumaona kuti choonadi ndi chamtengo wapatali. Ndipo zikatere timakhala otsimikiza mtima kuti tipitirize ‘kuyendabe m’choonadi,’ zomwe zikutanthauza kupitirizabe kuchita zinthu zimene zingachititse kuti Yehova azisangalala nafe komanso kutidalitsa. Pali zifukwa zambiri zimene zimatichititsa kukonda choonadi. Chifukwa chachikulu ndi chakuti timakonda Yehova Mulungu, yemwe ndi mwiniwake wa choonadicho. Kudzera m’Mawu ake Baibulo, tinafika pomudziwa monga Atate wathu wakumwamba yemwe amatisamalira mwachikondi, osati kungomudziwa monga Mlengi wamphamvuyonse yemwe analenga kumwamba ndi dziko lapansi.—1 Pet. 5:7. w22.08 14 ¶1, 3
Lachiwiri, September 17
Tizikumbukira osauka.—Agal. 2:10.
Mtumwi Paulo analimbikitsa abale ndi alongo ake kuti azisonyeza chikondi ndiponso “kuchita zabwino.” (Aheb. 10:24) Iye anathandiza abale ndi alongo akewa osati ndi mawu okha komanso ndi zochita. Mwachitsanzo, Akhristu a ku Yudeya atavutika ndi njala, Paulo anathandiza nawo powapatsa zinthu zofunika. (Mac. 11:27-30) Ndipotu ngakhale kuti Paulo ankatanganidwa ndi ntchito yolalikira ndi kuphunzitsa, nthawi zonse ankafunafuna njira zothandizira ena pa zimene ankafunikira. Pochita zimenezi, iye analimbikitsa Akhristu anzakewo kuti azidalira kuti Yehova adzawathandiza. Ifenso masiku ano tikamadzipereka kugwiritsa ntchito nthawi, mphamvu komanso luso lathu pothandiza ena pa nthawi ya ngozi zam’chilengedwe, timathandiza abale ndi alongo kulimbitsa chikhulupiriro chawo. Zimenezi n’zimene zimachitikanso ngati nthawi zonse timathandiza pa ntchito ya padziko lonse ndi ndalama zathu. Tikamathandiza m’njira zimenezi komanso zina, timachititsa abale ndi alongo athu kuti azikhulupirira kuti Yehova sadzawataya ngakhale pang’ono. w22.08 24 ¶14
Lachitatu, September 18
Ulosi sunachokere kwa anthu, koma anthuwo analankhula mawu ochokera kwa Mulungu motsogoleredwa ndi mzimu woyera.—2 Pet. 1:21.
M’Baibulo muli maulosi ambiri amene anakwaniritsidwa, ndipo ena anakwaniritsidwa patapita zaka mahandiredi kuchokera pamene analembedwa. Mbiri imatitsimikizira kuti maulosiwa anakwaniritsidwadi. Izi sizimatidabwitsa chifukwa timadziwa kuti maulosi a m’Baibulo anauziridwa ndi Yehova. Taganizirani za maulosi onena za kugonjetsedwa kwa mzinda wa Babulo. Cha m’ma 700 B.C.E., mneneri Yesaya anauziridwa kulosera kuti mzindawu womwe unali wamphamvu, udzagonjetsedwa. Ananena ngakhale dzina la yemwe adzaugonjetse kuti ndi Koresi ndipo ananeneratu mwatsatanetsatane mmene mzindawo udzagonjetsedwere. (Yes. 44:27–45:2) Yesaya ananeneratunso kuti mzindawo ukadzawonongedwa simudzakhalanso anthu. (Yes. 13:19, 20) Amedi ndi Aperisiya anagonjetsa Babulo mu 539 B.C.E., ndipo panopa pamalo omwe panali mzinda wamphamvuwu, ndi milu ya miyala yokhayokha. w23.01 4 ¶10
Lachinayi, September 19
Pitirizani kutonthozana. —1 Ates. 5:11.
Yehova anatisankha kuti tikhale m’banja la anthu ake, omwe amamutumikira padziko lonse. Umenewutu ndi mwayi waukulu umene umachititsa kuti tipeze madalitso ambiri. (Maliko 10:29, 30) Mofanana ndi ifeyo, padziko lonse pali abale ndi alongo omwenso amakonda Yehova ndipo amayesetsa kutsatira mfundo zake. Tingasiyane nawo chilankhulo, chikhalidwe komanso mmene timavalira. Komabe timawakonda ngakhale pamene takumana nawo kwa nthawi yoyamba. Timasangalala tikamatamanda komanso kulambira limodzi Atate wathu wakumwamba yemwe ndi wachikondi, ndipo tiyenera kukhala ogwirizana nawo kwambiri. (Sal. 133:1) Nthawi zambiri amatithandiza polimbana ndi mavuto athu. (Aroma 15:1; Agal. 6:2) Iwo amatilimbikitsanso kuti tipitirizebe kukhala akhama pa utumiki wathu komanso kukhalabe pa ubwenzi wolimba ndi Yehova. (Aheb. 10:23-25) Tangoganizani mmene tikanamvera zikanakhala kuti panalibe mpingo woti uzitithandiza kulimbana ndi adani athu, omwe ndi Satana Mdyerekezi ndi dziko lake loipali. w22.09 2-3 ¶3-4
Lachisanu, September 20
Amene amalamulira milomo yake amachita zinthu mwanzeru. —Miy. 10:19.
Nthawi zina kudziletsa kungakhale kovuta pamene tikugwiritsa ntchito malo ochezera a pa intaneti. Ngati sitingasamale, mosadziwa tingaulule nkhani zachinsinsi kwa anthu ambiri. Tikangotumiza uthenga pamalo ochezera a pa intaneti, sitingadziwe mmene anthu amene alandira uthengawo angaugwiritsire ntchito komanso sitingachitepo kathu pa mavuto amene angatsatirepo. Komanso kudziletsa kungatithandize kuti tikhale chete otsutsa akamatinyengerera kuti tiulule zinthu zimene zingaike pangozi moyo wa abale ndi alongo athu. Zimenezi zingachitike tikamafunsidwa mafunso ndi apolisi m’dziko limene ntchito yathu ndi yoletsedwa. Tingatsatire mfundo yakuti ‘timange pakamwa pathu kuti patetezeke’ pazochitika ngati zimenezi komanso zina. (Sal. 39:1) Timafunika kukhala odalirika kaya tikuchita zinthu ndi anthu a m’banja lathu, anzathu, abale ndi alongo kapena wina aliyense. Ndipo kuti tikhale odalirika tiyenera kukhala odziletsa. w22.09 13 ¶16
Loweruka, September 21
Wosangalala ndi munthu . . . [yemwe] amakonda kwambiri chilamulo cha Yehova, ndipo amawerenga ndi kuganizira mozama chilamulocho masana ndi usiku.—Sal. 1:1, 2.
Kuti tikhaledi osangalala tiyenera kumadya chakudya chauzimu. Ndipo chakudya chauzimuchi n’chofunikadi. N’chifukwa chake Yesu anati: “Munthu sangakhale ndi moyo ndi chakudya chokha, koma ndi mawu alionse ochokera m’kamwa mwa Yehova.” (Mat. 4:4) Choncho tisamalole kuti tsiku lizidutsa tisanawerenge Mawu amtengo wapatali a Mulungu. M’Baibulo, Yehova anatipatsa malangizo amene angatithandize kukhala ndi moyo wosangalala. Timaphunziramo za cholinga chimene anatilengera, zimene tingachite kuti tikhale naye pa ubwenzi komanso azitikhululukira machimo athu. Timaphunziramonso za chiyembekezo chosangalatsa ndi malonjezo a m’tsogolo. (Yer. 29:11) Mfundo za choonadi zimene timaphunzira m’Baibulozi zimachititsa mitima yathu kukhala yosangalala. Mukakhumudwa chifukwa cha mavuto amene mukukumana nawo, muzipeza nthawi yambiri yowerenga komanso kuganizira mozama Mawu a Yehova. w22.10 7 ¶4-6
Lamlungu, September 22
Pa nkhani yomvetsa zinthu khalani anthu akuluakulu.—1 Akor. 14:20.
Potifunira zabwino, Baibulo limatilimbikitsa kuti tisapitirize kukhala osadziwa. Kugwiritsa ntchito mfundo za m’Baibulo pa moyo wathu kumatithandiza kukhala odziwa zinthu. Pang’ono ndi pang’ono timadzionera tokha mmene mfundozi zimatithandizira kupewa mavuto komanso kusankha zochita mwanzeru. Tingachite bwino kudzifufuza mmene tikuchitira pa nkhaniyi. Ngati takhala tikuphunzira Baibulo komanso kupezeka pamisonkhano kwa kanthawi, tingadzifunse chifukwa chake sitinadzipereke komanso kubatizidwa mpaka pano. Ngati tinabatizidwa, kodi tikupita patsogolo pa nkhani yophunzitsa komanso kulalikira uthenga wabwino? Kodi zosankha zathu zimasonyeza kuti tikutsogoleredwa ndi mfundo za m’Baibulo? Kodi timasonyeza makhalidwe abwino tikamachita zinthu ndi ena? Ngati taona kuti pali zimene tifunika kukonza, tiyenera kumvetsera zikumbutso za Yehova zomwe “zimapatsa nzeru munthu wosadziwa zinthu.”—Sal. 19:7. w22.10 20 ¶8
Lolemba, September 23
Ankapita kulikonse kumene mzimu ukufuna kuti apite.—Ezek. 1:20.
Ezekieli anaona mmene mzimu wa Mulungu ulili wamphamvu. M’masomphenya, iye anaona mzimu woyera ukuthandiza angelo amphamvu komanso ukuyendetsa mawilo akuluakulu a galeta lakumwamba. (Ezek. 1:21) Kodi Ezekieli anatani ataona zimenezi? Iye analemba zomwe zinachitika kuti: “Nditaona zimenezo, ndinagwada n’kuwerama mpaka nkhope yanga pansi.” Chifukwa cha mantha, Ezekieli anagwa pansi. (Ezek. 1:28) Nthawi zonse Ezekieli akaganizira masomphenya ochititsa chidwiwa ankalimbikitsidwa ndipo ankakhulupirira kuti mothandizidwa ndi mzimu wa Mulungu, angathe kukwaniritsa utumiki wake. Yehova analamula Ezekieli kuti: “Iwe mwana wa munthu, imirira kuti ndikulankhule.” Mawu amenewa komanso mzimu wa Mulungu zinapatsa mphamvu Ezekieli zoti athe kudzuka. (Ezek. 2:1, 2) Pambuyo pa zimenezi komanso pautumiki wake wonse, Ezekieli ankatsogoleredwa ndi “dzanja” la Mulungu, kapena kuti mzimu wake woyera.—Ezek. 3:22; 8:1; 33:22; 37:1; 40:1. w22.11 4 ¶7-8
Lachiwiri, September 24
Makutu anu adzamva mawu kumbuyo kwanu.—Yes.30:21.
Apa mneneri Yesaya anafotokoza Yehova monga mlangizi watcheru yemwe akuyenda kumbuyo kwa ophunzira ake n’kumawalozera njira patsogolo pawo komanso kuwapatsa malangizo. Masiku ano timamva mawu a Mulungu kuchokera kumbuyo kwathu. Motani? Mawu a Mulungu analembedwa m’Baibulo kalekale ife tisanabadwe, choncho tikamawawerenga zimakhala ngati tikumva mawu a Mulungu kumbuyo kwathu. (Yes. 51:4) Kodi tingatani kuti tizipindula ndi malangizo omwe Yehova amatipatsa? Onani kuti Yesaya anatchula zinthu ziwiri. Choyamba iye anati, “njira ndi iyi.” Chachiwiri anati, “yendani m’njira imeneyi.” Si zokwanira kungodziwa “njira,” timafunikanso ‘kuyendamo.’ Kudzera m’Mawu a Yehova, monga mmene gulu lake limawafotokozera, timadziwa zomwe Mulungu amafuna kuti tizichita. Timaphunziranso mmene tingagwiritsire ntchito zomwe timaphunzirazo. Kuti tizipirira mosangalala potumikira Yehova, timafunika kuchita zinthu ziwiri zonsezi. Tikamachita zimenezo m’pamene tingakhale otsimikiza kuti Yehova adzatidalitsa. w22.11 11 ¶10-11
Lachitatu, September 25
Ine ndikachoka, mimbulu yopondereza idzafika pakati panu.—Mac. 20:29.
Patangopita kanthawi kuchokera pamene atumwi ambiri a Yesu anamwalira, Akhristu onyenga analowa mumpingo. (Mat. 13:24-27, 37-39) Iwo ankalankhula “zinthu zopotoka kuti apatutse ophunzira aziwatsatira.” (Mac. 20:30) Chimodzi mwa “zinthu zopotoka” zomwe anayamba kuphunzitsa, chinali chakuti Yesu sanapereke thupi lake “kamodzi kokha kuti anyamule machimo a anthu ambiri,” monga mmene Baibulo limanenera, koma kuti nsembe yake iyenera kumaperekedwa mobwerezabwereza. (Aheb. 9:27, 28) Masiku ano anthu ambiri oona mtima amakhulupirira chiphunzitso chabodzachi. Iwo amasonkhana m’matchalitchi pafupipafupi, nthawi zinanso tsiku lililonse, kuti achite mwambo umene amautchula kuti “Nsembe ya Misa.” Zipembedzo zina zimachitanso mwambo wokumbukira imfa ya Yesu mwa apo ndi apo koma anthu ambiri m’zipembedzozo sadziwa tanthauzo la nsembe ya Yesu. w23.01 21 ¶5
Lachinayi, September 26
Musaiwale kuchita zabwino ndi kugawira ena zomwe muli nazo.—Aheb. 13:16.
Mu Ulamuliro wa Zaka 1,000 wa Yesu, anthu omwe anamwalira adzaukitsidwa ndipo omvera adzathandizidwa kuti akhale angwiro. Anthu omwe Yehova adzawaweruze kuti ndi olungama “adzalandira dziko lapansi, ndipo adzakhala mmenemo mpaka kalekale.” (Sal. 37:10, 11, 29) N’zosangalatsa kuti “imfa nayonso, yomwe ndi mdani womaliza, idzawonongedwa.” (1 Akor. 15:26) Chiyembekezo chathu chodzakhala ndi moyo mpaka kalekale n’chochokera m’Mawu a Mulungu. Chiyembekezochi chingatithandize kukhalabe okhulupirika m’masiku otsiriza ovutawa. Koma kuti tizisangalatsa Yehova, tiyenera kumamutumikira osati chabe chifukwa chakuti tikufunitsitsa kudzapeza moyo. Chifukwa chachikulu chokhalirabe okhulupirika kwa Yehova ndi Yesu ndi chakuti timawakonda kwambiri. (2 Akor. 5:14, 15) Chikondichi chimatilimbikitsa kuti tiziwatsanzira komanso kuuza ena za chiyembekezo chathu. (Aroma 10:13-15) Tikamayesetsa kukhala owolowa manja komanso kupewa kukhala odzikonda timakhala anthu amene Yehova akufuna kuti akhale anzake mpaka kalekale. w22.12 6-7 ¶15-16
Lachisanu, September 27
Onse ofuna kukhala ndi moyo wodzipereka kwa Mulungu mogwirizana ndi Khristu Yesu, nawonso adzazunzidwa.—2 Tim. 3:12.
Kuzunzidwa kungachititse kuti tisakhale ndi zinthu zambiri zomwe zimachititsa kuti tikhale ndi mtendere. Tingamade nkhawa posadziwa chimene chitichitikire. Si zachilendo kumva choncho. Komabe tiyenera kukhala osamala. Yesu ananena kuti kuzunzidwa kudzachititsa kuti otsatira ake afooke. (Yoh. 16:1, 2) Ngakhale kuti Yesu anafotokoza kuti tiziyembekezera kuzunzidwa, anatitsimikiziranso kuti tingathe kukhalabe okhulupirika. (Yoh. 15:20; 16:33) Ngati akuluakulu a boma atiletsa kuchita zinthu zina kapena aletseratu ntchito yathu, tingalandire malangizo kuchokera ku ofesi ya nthambi komanso kwa akulu. Cholinga cha malangizowo n’kutiteteza kuti tipitirizebe kulandira chakudya chauzimu komanso kugwira ntchito yolalikira mmene tingathere. Tiziyesetsa kuwatsatira. (Yak. 3:17) Komanso tisamaulule nkhani zokhudza abale ndi alongo athu kwa anthu amene sakufunika kuzidziwa.—Mlal. 3:7. w22.12 20-21 ¶14-16
Loweruka, September 28
Mupitirize kusonyeza khama limene munali nalo poyamba.—Aheb. 6:11.
Masiku ano, Yesu akupitiriza kutsogolera ophunzira ake pamene akulalikira za Ufumu wa Mulungu padziko lonse. Iye akukwaniritsa zomwe analonjeza. Kudzera m’gulu la Yehova, Yesu amatiphunzitsa mmene tingamalalikirire komanso amatipatsa zonse zotithandiza pogwira ntchitoyi. (Mat. 28:18-20) Timachita mbali yathu tikamagwira mwakhama ntchito yolalikira ndi kuphunzitsa anthu komanso kukhalabe maso pamene tikuyembekezera kuti Yehova awononge dziko loipali. Tikamatsatira malangizo a pa Aheberi 6:11, 12, chiyembekezo chathu chidzakhala chotsimikizika “mpaka mapeto.” Yehova anakhazikitsa tsiku ndi nthawi yomwe adzawononge dziko lolamuliridwa ndi Satanali. Tsikulo likadzafika, Yehova sadzalephera kukwaniritsa maulosi onse omwe analemba m’Mawu ake. Nthawi zina tingamaone ngati mapeto akuchedwa. Komabe tsiku la Yehova ‘silidzachedwa.’ (Hab. 2:3) Choncho tiyeni tikhale otsimikiza mtima kuti ‘tidzadikirira Yehova’ komanso kusonyeza kuti ‘tikuyembekezera moleza mtima Mulungu wa chipulumutso chathu.’—Mika 7:7. w23.02 19 ¶15-16
Lamlungu, September 29
Palibe angafanane ndi inu.—Sal. 40:5.
Munthu amene akukwera phiri cholinga chake chimakhala kukafika pamwamba penipeni pa phirilo. Komabe akafika pamalo ena amaima n’kusangalala ndi zomwe akuona. Mofanana ndi zimenezi nthawi zina muziima kaye n’kuganizira mmene Yehova akukuthandizirani kuti zinthu zikuyendereni bwino ngakhale pamene mukukumana ndi mavuto. Kumapeto kwa tsiku lililonse muzidzifunsa kuti: ‘Kodi Yehova wandipatsa madalitso ati lero? Ngakhale kuti ndikukumanabe ndi mayesero, kodi Yehova akundithandiza bwanji kuwapirira?’ Muzipeza ngakhale dalitso limodzi lochokera kwa Yehova lomwe lakuthandizani kuti zinthu zikuyendereni bwino. N’zoona kuti mungapemphere kuti mayeserowo athe. (Afil. 4:6) Koma tiyeneranso kumaganizira madalitso amene tikupeza panopa. Ndipotu Yehova akulonjeza kuti adzatilimbitsa komanso kutithandiza kuti tipirire. Choncho nthawi zonse muziyamikira kuti Yehova akukuthandizani. Mukatero mudzaona mmene akukuthandizirani kuti zinthu zizikuyenderani bwino, ngakhale pa nthawi ya mayesero.—Gen. 41:51, 52. w23.01 19 ¶17-18
Lolemba, September 30
[Tizikumbukira] nthawi zonse kubwera kwa tsiku la Yehova.—2 Pet. 3:12.
Dzifunseni kuti: ‘Kodi zochita zanga zimasonyeza kuti ndikuzindikira kuti dziko loipali liwonongedwa posachedwapa? Kodi zimene ndimasankha pa nkhani ya maphunziro komanso ntchito zimasonyeza kuti ndimaona kutumikira Yehova kukhala kofunika kwambiri pa moyo wanga? Kodi ndimakhulupirira kuti Yehova adzandipatsa zofunikira ineyo ndi banja langa kapena nthawi zonse ndimadera nkhawa za zinthu zakuthupi?’ Taganizirani mmene Yehova amasangalalira akationa tikuyesetsa kuchita zinthu mogwirizana ndi chifuniro chake. (Mat. 6:25-27, 33; Afil. 4:12, 13) Nthawi ndi nthawi, tiyenera kumafufuza zimene timaganiza kenako n’kumasintha pamene pakufunikira kutero. Paulo anauza Akhristu a ku Korinto kuti: “Pitirizani kudziyesa kuti muone ngati mukadali ndi chikhulupiriro. Pitirizani kudziyesa kuti mudziwe kuti ndinu munthu wotani.” (2 Akor. 13:5) Choncho tiyenera kupitiriza kusintha maganizo athu powerenga Mawu a Mulungu kuti tiziphunzira mmene iye amaganizira, kenako n’kumachita zomwe tingathe kuti zochita zathu zizigwirizana ndi chifuniro cha Yehova.—1 Akor. 2:14-16. w23.01 9 ¶5-6