Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • es24 tsamba 98-108
  • October

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • October
  • Kuphunzira Malemba Tsiku ndi Tsiku—2024
  • Timitu
  • Lachiwiri, October 1
  • Lachitatu, October 2
  • Lachinayi, October 3
  • Lachisanu, October 4
  • Loweruka, October 5
  • Lamlungu, October 6
  • Lolemba, October 7
  • Lachiwiri, October 8
  • Lachitatu, October 9
  • Lachinayi, October 10
  • Lachisanu, October 11
  • Loweruka, October 12
  • Lamlungu, October 13
  • Lolemba, October 14
  • Lachiwiri, October 15
  • Lachitatu, October 16
  • Lachinayi, October 17
  • Lachisanu, October 18
  • Loweruka, October 19
  • Lamlungu, October 20
  • Lolemba, October 21
  • Lachiwiri, October 22
  • Lachitatu, October 23
  • Lachinayi, October 24
  • Lachisanu, October 25
  • Loweruka, October 26
  • Lamlungu, October 27
  • Lolemba, October 28
  • Lachiwiri, October 29
  • Lachitatu, October 30
  • Lachinayi, October 31
Kuphunzira Malemba Tsiku ndi Tsiku—2024
es24 tsamba 98-108

October

Lachiwiri, October 1

Ndidzakutamandani pakati pa mpingo.—Sal. 22:22.

Tonsefe tingathandize kuti misonkhano iziyenda bwino poimba nawo nyimbo mokweza komanso kupereka ndemanga zimene tazikonzekera bwino. Ena zimawavuta kuimba nyimbo kapena kupereka ndemanga pamisonkhano. Kodi inunso zimakuvutani? Ngati ndi choncho, muziganizira zimene ena achita kuti akwanitse kuthetsa mantha. Ponena za nyimbo, ena aona zimathandiza akamaimba ndi mtima wonse. Tikamaimba nyimbo za Ufumu, cholinga chathu chachikulu chizikhala kutamanda Yehova. Choncho muzikonzekera nyimbo ngati mmene mumachitira ndi mbali zina za pamisonkhano ndipo muziona mmene mawu ake akugwirizanira ndi zimene mukaphunzire kumisonkhanoko. Komanso muziganizira kwambiri mawu a nyimboyo, osati luso lanu loimba. Ena zimawavuta kupereka ndemanga. Ndiye kodi n’chiyani chingathandize. Muzipereka ndemanga pafupipafupi. Muzikumbukira kuti palibe vuto kupereka yankho lalifupi, losavuta komanso lachindunji. Dziwani kuti Yehova amayamikira tikamayesetsa kumutamanda pamisonkhano ya mpingo. w22.04 7-8 ¶12-15

Lachitatu, October 2

Yehova ndi amene amandithandiza. Sindidzaopa.—Aheb. 13:6.

Mawu akuti “amene amandithandiza,” akunena za munthu amene akuthamanga kuti akathandize winawake yemwe akufunika thandizo. Yerekezerani kuti mukuona Yehova akuthamangira kukapulumutsa winawake yemwe ali pamavuto. N’zosakayikitsa kuti mungavomereze kuti mafotokozedwe amenewa akusonyeza kuti Yehova ndi wofunitsitsa kutithandiza. Mothandizidwa ndi Yehova, tingathe kupirira mayesero aliwonse mosangalala. Kodi Yehova amatithandiza m’njira ngati ziti? Kuti tipeze yankho, tiyeni tiwerenge zimene zili m’buku la Yesaya. Chifukwa chiyani? Chifukwa maulosi ambiri amene Yesaya anauziridwa kulemba amakhudzanso atumiki a Mulungu masiku ano. Kuwonjezera pamenepo, nthawi zambiri Yesaya anamufotokoza Yehova m’mawu osavuta kumvetsa. Mu Yesaya chaputala 30, muli zitsanzo zangati zimenezo. Muchaputalachi, Yesaya anafotokoza pogwiritsa ntchito mawu amene amatithandiza kuona m’maganizo mwathu mmene Yehova amathandizira anthu ake (1) pomvetsera mwatcheru ndi kuyankha mapemphero athu, (2) potipatsa malangizo, komanso (3) potipatsa madalitso panopa ndiponso m’tsogolo. w22.11 8 ¶2-3

Lachinayi, October 3

Usachite mantha ndi mavuto amene ukumane nawo. . . . Sonyeza kukhulupirika kwako mpaka imfa, ndipo ndidzakupatsa mphoto ya moyo.—Chiv. 2:10.

M’mauthenga omwe Yesu anatumiza kumipingo ya ku Simuna ndi Filadefiya, iye anauza Akhristu a kumeneko kuti sankafunika kuopa kuzunzidwa popeza akanapeza mphoto chifukwa cha kukhulupirika kwawo. (Chiv. 3:10) Tiyenera kuyembekezera kuti tidzazunzidwa ndipo tizikhala okonzeka kupirira. (Mat. 24:​9, 13; 2 Akor. 12:10) Buku la Chivumbulutso limatiuza kuti anthu a Mulungu adzazunzidwa m’masiku athu ano, omwe ndi ‘tsiku la Ambuye.’ (Chiv. 1:10) Chaputala 12 chimafotokoza za nkhondo yomwe inayamba kumwamba Ufumu wa Mulungu utangokhazikitsidwa. Mikayeli, yemwe ndi Yesu Khristu, limodzi ndi angelo ake anamenyana ndi Satana ndi ziwanda. (Chiv. 12:​7, 8) Pamapeto pake adani a Mulungu amenewa, anagonjetsedwa ndi kuponyedwa padziko lapansi, zomwe zinachititsa kuti padzikoli pakhale mavuto aakulu.—Chiv. 12:​9, 12. w22.05 5 ¶12-13

Lachisanu, October 4

Yehova Mulungu wathu si wopanda chilungamo.—2 Mbiri 19:7.

Nthawi zonse Yehova amaweruza mwachilungamo ndipo sakondera ngakhale pang’ono. Kuti akhululukire munthu sizitengera mmene munthuyo akuonekera, chuma, kutchuka kapena luso lake. (1 Sam. 16:7; Yak. 2:​1-4) Palibe yemwe angamukakamize kuti achite zinazake kapena kumupatsa chiphuphu. Iye sasankha zinthu chifukwa cha mkwiyo kapena mmene akumvera. (Eks. 34:7) N’zosakayikitsa kuti kuzindikira komanso kumvetsa bwino zinthu kumachititsa Yehova kukhala Woweruza wabwino kwambiri. (Deut. 32:4) Anthu omwe ankalemba Malemba a Chiheberi ankazindikira kuti Yehova ndi wosiyana kwambiri ndi ena pa nkhani yokhululuka. Nthawi zina iwo ankagwiritsa ntchito mawu a Chiheberi omwe buku lina linafotokoza kuti “amanena makamaka zimene Mulungu amachita pokhululukira wochimwa, ndipo sanena za mlingo wakukhululuka umene munthu amachitira munthu mnzake, womwe ndi wochepa.” Yehova yekha ndi amene angathe kukhululukira kotheratu munthu yemwe walapa. w22.06 4 ¶10-11

Loweruka, October 5

Phunzitsa mwana kuti aziyenda m’njira imene akuyenera kuyendamo. Ngakhale akadzakalamba sadzachoka m’njira imeneyo.—Miy. 22:6.

Ngati mukulera nokha ana kapena muli m’banja losiyana zipembedzo, dziwani kuti kukhulupirika kwanu kumathandiza komanso kulimbikitsa ena. Koma bwanji ngati mutaona kuti zimene mukuchita pofuna kuthandiza mwana wanu sizikuphula kanthu? Muzikumbukira kuti kuphunzitsa mwana kumatenga nthawi yaitali. Mukadzala mbewu nthawi zina mungayambe kukayikira ngati idzakule n’kubereka zipatso. Ngakhale sikumudziwa ngati mbewuyo ingabereke zipatso, mumapitirizabe kuthirira kuti ikule. (Maliko 4:​26-29) Mofanana ndi zimenezi, monga mayi nthawi zina mungamakayikire ngati mukuwafika pamtima ana anu. N’zoona kuti simungawasankhire zochita. Koma mukamapitiriza kuchita zonse zimene mungathe powaphunzitsa, mumawapatsa mwayi woti akhale pa ubwenzi ndi Yehova. w22.04 19-20 ¶16-17

Lamlungu, October 6

Kunyada kumachititsa kuti munthu awonongeke, ndipo mtima wodzikuza umachititsa kuti munthu apunthwe. —Miy. 16:18.

Pa nthawi imene ankalambira Yehova mokhulupirika, Solomo ankadziona moyenera. Ali wachinyamata, iye anavomereza modzichepetsa zimene sangakwanitse ndipo anapempha Yehova kuti azimutsogolera. (1 Maf. 3:​7-9) Cha kumayambiriro kwa ulamuliro wake, Solomo ankadziwanso za kuopsa kwa kunyada. Koma n’zomvetsa chisoni kuti patapita nthawi, Solomo anakanika kutsatira malangizo ake omwe. Cha mkatikati mwa ulamuliro wake, modzikuza anayamba kunyalanyaza malamulo a Mulungu. Mwachitsanzo, lamulo lina linkanena kuti mfumu ya Chiheberi ‘isakhale ndi akazi ambiri kuti mtima wake usapatuke.’ (Deut. 17:17) Solomo sanamvere lamulo limeneli ndipo anakwatira akazi 700 komanso anali ndi akazi 300 a pambali, ndipo ambiri mwa iwo ankalambira milungu ina. (1 Maf. 11:​1-3) N’kutheka kuti iye ankaona kuti chilichonse chili m’chimake. Mulimonse mmene zinalili, patapita nthawi Solomo anakumana ndi zotsatirapo za kusamvera Yehova.—1 Maf. 11:​9-13. w22.05 23 ¶12

Lolemba, October 7

“Wolungama wanga adzakhala ndi moyo chifukwa cha chikhulupiriro chake,” ndipo “ngati angabwerere m’mbuyo, ine sindikondwera naye.”—Aheb. 10:38.

Masiku ano anthu akuyenera kusankha pa nkhani yofunika kwambiri. Kodi iwo adzasankha kukhala ku mbali ya Yehova Mulungu monga woyenera kulamulira chilengedwe chonse, kapena adzasankha kukhala ku mbali ya Satana Mdyerekezi, yemwe ndi mdani wake komanso wankhanza? Palibe amene anganene kuti sali kumbali iliyonse. Zimene aliyense angasankhe zidzakhudza tsogolo lake mpaka kalekale. (Mat. 25:​31-33, 46) Pa ‘chisautso chachikulu,’ adzaikidwa chizindikiro choti apulumutsidwe kapena kuwonongedwa. (Chiv. 7:14; 14:​9-11; Ezek. 9:​4, 6) Ngati mwasankha kukhala ku mbali ya ulamuliro wa Yehova, mwasankha bwino kwambiri. Tsopano ndinu ofunitsitsa kuthandiza ena kuti nawonso asankhe bwino. Yehova adzadalitsa anthu omwe ali kumbali yake ya Ufumu wake. Tingachite bwino kuganizira mfundo za choonadi zimenezi. Kuchita izi kudzatithandiza kukhala otsimikiza kuti tipitirizabe kutumikira Yehova. Kuwonjezera pamenepo, tingathe kugwiritsa ntchito mfundo zimene taphunzira kuthandiza ena kuti asankhe kutumikira Yehova ndiponso asasiye. w22.05 15 ¶1-2

Lachiwiri, October 8

Ndinu osangalala pamene anthu . . . akukunamizirani zoipa zilizonse. —Mat. 5:11.

Tiyenera kumvera Yehova osati adani athu. Yobu anamvetsera mwatcheru pamene Yehova ankamulankhula. Mulungu anamuthandiza kuganizira nkhaniyo, zomwe zinali ngati akumuuza kuti: ‘Ndikudziwa chilichonse chomwe chakuchitikira. Kodi ukuganiza kuti sindingathe kukusamalira?’ Yobu anayankha modzichepetsa komanso anayamikira kwambiri Yehova chifukwa cha ubwino wake. Iye anati: “Makutu anga anamva za inu, koma tsopano ndikukuonani ndi maso angawa.” (Yobu 42:5) Yobu ayenera kuti analankhula zimenezi adakali pa phulusa pompaja, thupi lake lili zilonda zokhazokha. Ngakhale zinali choncho Yehova anamutsimikizira kuti ankamukonda komanso ankamuonabe kuti ndi bwenzi lake. (Yobu 42:​7, 8) Masiku anonso anthu angatinyoze kapena kutichitira zinthu ngati kuti ndife opanda pake. Angayese kuipitsa mbiri yathu kapena ya gulu lathu. Pa zomwe zinachitikira Yobu, timaphunzira kuti Yehova sakayikira kuti tidzakhalebe okhulupirika tikakumana ndi mayesero. w22.06 24 ¶15-16

Lachitatu, October 9

Ukwati wa Mwanawankhosa wafika.—Chiv. 19:7.

Ngakhale kuti kumwamba kudzakhala chisangalalo Babulo Wamkulu akadzawonongedwa, pali chinthu chinanso chomwe chidzachititse kuti chisangalalocho chiwonjezereke kwambiri. (Chiv. 19:​1-3) Kudzakhala “ukwati wa Mwanawankhosa,” womwe udzakhala pachimake pa zochitika za m’buku la Chivumbulutso. A 144,000 onse adzakhala atapita kumwamba nkhondo ya Aramagedo isanayambe. Komatu iyi siidzakhala nthawi ya ukwati wa Mwanawankhosa. (Chiv. 21:​1, 2) Ukwatiwu udzachitika pambuyo poti nkhondo ya Aramagedo yamenyedwa ndipo adani onse a Mulungu awonongedwa. (Sal. 45:​3, 4, 13-17) Kodi ukwati wa Mwanawankhosa udzatanthauza chiyani kwa Yesu ndi odzozedwa? Mofanana ndi ukwati womwe umagwirizanitsa mwamuna ndi mkazi, ukwati wophiphiritsawu udzachititsa kuti Yesu Khristu, yemwe ndi Mfumu agwirizane ndi a 144,000, omwe ndi “mkwatibwi” wake. Kumeneku kudzakhala kukhazikitsidwa kwa boma latsopano lomwe lidzalamulira dzikoli kwa zaka 1,000.—Chiv. 20:6. w22.05 17 ¶11-13

Lachinayi, October 10

Kapolo ameneyo adzakhala wosangalala, ngati mbuye wake . . . adzamupeze akuchita zimenezo!—Mat. 24:46.

Yesu ananeneratu kuti munthawi yamapeto, adzasankha “kapolo wokhulupirika komanso wanzeru” kuti azipereka malangizo a m’Mawu a Mulungu. (Mat. 24:45) Izi ndi zimene zikuchitikadi. Mtsogoleri wathu wakhala akugwiritsa ntchito kagulu ka amuna odzozedwa popereka ‘chakudya chauzimu pa nthawi yoyenera’ kwa anthu ake komanso anthu omwe asonyeza chidwi. Amuna amenewa sadziona monga olamulira chikhulupiriro cha ena. (2 Akor. 1:24) M’malomwake iwo amazindikira kuti Yesu Khristu ndiye “mtsogoleri ndi wolamulira” wa anthu ake. (Yes. 55:4) Kungoyambira mu 1919, kapolo wokhulupirika wakhala akukonza mabuku osiyanasiyana omwe athandiza anthu achidwi kuphunzira mfundo za choonadi chopezeka m’Mawu a Mulungu. Mu 1921, kapoloyu anatulutsa buku lakuti Zeze wa Mulungu pofuna kuthandiza anthu omwe asonyeza chidwi kuphunzira mfundo zoyambirira za m’Baibulo. M’kupita kwa nthawi, mabuku enanso akhala akutulutsidwa. Ndi buku liti lomwe linakuthandizani inuyo kuti mudziwe komanso kuyamba kukonda Atate wathu wakumwamba? w22.07 10 ¶9-10

Lachisanu, October 11

Mudzasangalala nane mpaka kalekale.—Sal. 41:12.

Yehova ndi wowolowa manja kwambiri. Posatengera zimene inuyo mumamupatsa, nthawi zonse amakupatsani zinthu zambiri. (Maliko 10:​29, 30) Iye adzakupatsani moyo wosangalatsa, watanthauzo komanso wokhutiritsa ngakhale panopa m’dziko loipali. Ndipotu ichi n’chiyambi chabe. Mungapitirizebe kutumikira Atate wanu wokondedwa mpaka kalekale. Chikondi pakati pa inu ndi Atate wanu chidzapitiriza kukula. Ndipo pamapeto pake mudzakhala ndi moyo ngati iyeyo mpaka kalekale. Mukadzipereka komanso kubatizidwa mumakhala ndi mwayi wopereka kwa Atate wanu chinthu chamtengo wapatali kwambiri. Iye wakupatsani chilichonse chabwino chomwe mumasangalala nacho. Posonyeza kuyamikira inunso mungamupatse Mwiniwake wakumwamba ndi dzikoli chinachake chomwe alibe, chimene ndi kufunitsitsa kwanu kumutumikira modzipereka. (Yobu 1:8; 41:11; Miy. 27:11) Umenewu ndi moyo wabwino kwambiri womwe mungakhale nawo. w23.03 6 ¶16-17

Loweruka, October 12

Kodi wachinyamata angakhale bwanji woyera pa moyo wake? Akamadzifufuza nthawi zonse kuti aone ngati zochita zake zikugwirizana ndi mawu anu.—Sal. 119:9.

Pamene achinyamata akukula, chilakolako cha kugonana chimakhala champhamvu ndipo mwina ena angamawakakamize kuti achite chiwerewere. Satana amafuna kuti muzingochita zimene mumalakalaka. Ndiye kodi n’chiyani chingakuthandizeni kuti mupewe kuchita makhalidwe oipa? (1 Ates. 4:​3, 4) Mukamapemphera muzimufotokozera Yehova mmene mukumvera. Ndipo muzimupempha kuti akupatseni mphamvu. (Mat. 6:13) Kumbukirani kuti Yehova amafuna kukuthandizani, osati kukuweruzani. (Sal. 103:​13, 14) Musamayese kulimbana ndi mavuto anu panokha. Muzifotokozera makolo anu zimene mukulimbana nazo. N’zoona kuti kukambirana nkhani ngati zimenezi si kophweka koma n’kofunika kuti muzichita zimenezi. Mukamawerenga Baibulo komanso kuganizira mozama mfundo zake, zidzakhala zosavuta kuti muzisankha zochita zimene zingasangalatse Yehova. Mudzaona kuti simukufunikira malamulo pa nkhani iliyonse chifukwa mudzamvetsa mmene Yehova amaganizira pa nkhani zosiyanasiyana. w22.08 5 ¶10-12

Lamlungu, October 13

Ngati munthu sasamalira anthu amene ndi udindo wake kuwasamalira, . . . wakana chikhulupiriro.—1 Tim. 5:8.

Mkhristu yemwe ndi mutu wa banja saona mopepuka udindo wosamalira banja lake. Ngati ndinu mutu wa banja, n’kutheka kuti mungamade nkhawa kuti muzipeza bwanji chakudya komanso ndalama yolipirira nyumba. Mwinanso mungamaope kuti ngati ntchito itakutherani simukwanitsa kupezanso ina. Kapenanso mungazengereze kusintha zinthu zina pa nkhani ya ntchito chifukwa choopa kuti muzipeza ndalama zochepa. Satana wakwanitsa kuchititsa anthu ambiri kuti asiye kutumikira Yehova chifukwa chokhala ndi mantha ngati amenewa. Satana amayesetsa kutichititsa kuganiza kuti Yehova satiganizira ifeyo patokha ndipo satithandiza kupezera banja lathu zofunika. Choncho tingamaone kuti tiyenera kuchita chilichonse chomwe tingathe kuti titeteze ntchito yathu, ngakhale zitakhala kuti tikuphwanya mfundo za m’Malemba. w22.06 15 ¶5-6

Lolemba, October 14

Chiyembekezo chathuchi chili ngati nangula wa miyoyo yathu ndipo n’chotsimikizika komanso chokhazikika.—Aheb. 6:19.

Timadziwa kuti Mulungu wathu ndi “wachifundo ndi wokoma mtima, wosakwiya msanga ndiponso wachikondi chokhulupirika chochuluka komanso choonadi.” (Eks. 34:6) Yehova amakonda chilungamo. (Yes. 61:8) Zimamupweteka akamationa tikuvutika ndipo ndi wokonzeka komanso wofunitsitsa kudzathetsa mavuto onse pa nthawi yoyenera. (Yer. 29:11) Zimenezitu ndi zosangalatsa. Mpake kuti timakonda kwambiri Yehova. Kodi n’chifukwa chinanso chiti chomwe chimatichititsa kukonda choonadi? Choonadi chimatithandiza m’njira zambiri. Tiyeni tiganizire chitsanzo. Choonadi cha m’Baibulo chimaphatikizapo chiyembekezo chathu cham’tsogolo. Monga mmene nangula amachititsira kuti boti lisayendeyende, chiyembekezo chathu chingatithandize kuti tikhalebe olimba tikakumana ndi mayesero. Mulemba laleroli, Paulo ankafotokoza za chiyembekezo chopita kumwamba chomwe Akhristu odzozedwa ali nacho. Koma zimene ananenazi zikukhudzanso anthu amene ali ndi chiyembekezo chodzakhala m’paradaiso padzikoli. (Yoh. 3:16) Kunena zoona, kuphunzira za chiyembekezo cha moyo wosatha kwatithandiza kuti tikhale ndi moyo watanthauzo. w22.08 14-15 ¶3-5

Lachiwiri, October 15

Dzuwa lisalowe mudakali okwiya. —Aef 4:26.

Chikondi ndi chimene chimatithandiza kuti tizikhulupirira ena. Chaputala 13 cha 1 Akorinto chimafotokoza mbali zambiri za chikondi zomwe zingatithandize kuti tizikhulupirira kapena tiyambirenso kukhulupirira anthu ena. (1 Akor. 13:​4-8) Mwachitsanzo, vesi 4 limanena kuti “chikondi n’choleza mtima ndiponso n’chokoma mtima.” Yehova amaleza nafe mtima ngakhale pamene tamuchimwira. Choncho ifenso tingamalezere mtima abale athu ngati alankhula kapena kuchita zinthu zimene zatikhumudwitsa. Vesi 5 limawonjezera kuti: “[Chikondi] sichikwiya ndipo sichisunga zifukwa.” Choncho sitingafune kumangokumbukirabe zimene abale athu atilakwira. Lemba la Mlaliki 7:​9, limanena kuti ‘tisamafulumire kukwiya mumtima mwathu.’ Muziona abale ndi alongo anu mmene Yehova amawaonera. Mulungu amawakonda ndipo samangokhalira kufufuza zolakwa zawo. Ifenso tiyenera kumutsanzira. (Sal. 130:3) M’malo momangoganizira zolakwa zawo, muziona makhalidwe abwino amene ali nawo.—Mat. 7:​1-5. w22.09 3-4 ¶6-7

Lachitatu, October 16

Padzafika nthawi yamasautso. —Dan. 12:1.

Buku la Danieli limatiuza zinthu zosangalatsa zomwe zidzachitike m’nthawi ya mapeto. Mwachitsanzo, pa Danieli 12:1 amatiuza kuti Mikayeli, yemwe ndi Yesu Khristu, “waimirira kuti athandize anthu a [Mulungu].” Mbali ya ulosi imeneyi inayamba kukwaniritsidwa mu 1914, pamene Yesu anaikidwa kukhala Mfumu ya Ufumu wakumwamba. Komabe Danieli anauzidwanso kuti Yesu “adzaimirira” pa “nthawi yamasautso imene sinakhalepo kuyambira pamene mtundu woyambirira wa anthu unakhalapo kudzafika nthawi imeneyo.” Apatu “nthawi yamasautso” imeneyi, ndi “chisautso chachikulu” chotchulidwa pa Mateyu 24:21. Yesu adzaimirira kapena kuti adzachitapo kanthu kuti ateteze anthu a Mulungu kumapeto kwa nthawi yamasautsoyi yomwe ndi pa Aramagedo. Buku la Chivumbulutso limanena kuti anthuwa ndi khamu lalikulu lomwe ‘lidzatuluke m’chisautso chachikulu.’—Chiv. 7:​9, 14. w22.09 21 ¶4-5

Lachinayi, October 17

Amene wandichimwira ndi amene ndimufufute m’buku langa. —Eks. 32:33.

Mayina amene ali m’buku la moyo angathe kufufutidwamo. Zili ngati Yehova walemba kaye mayinawa pogwiritsa ntchito pensulo. (Chiv. 3:5.) Tiyenera kuyesetsa kuti dzina lathu likhalebe m’bukuli mpaka pa nthawi imene silingadzafufutidwenso ngati kuti lalembedwa ndi inki. Gulu limodzi lomwe mayina awo alembedwa m’buku la moyo ndi la anthu omwe asankhidwa kuti akalamulire ndi Yesu kumwamba. Mogwirizana ndi mawu a mtumwi Paulo opita kwa ‘antchito anzake’ ku Filipi, mayina a odzozedwa, omwe aitanidwa kuti akalamulire limodzi ndi Yesu, panopo ali m’buku la moyoli. (Afil. 4:3) Koma kuti mayina awo apitirize kukhala m’buku lophiphiritsali, iwo ayenera kukhalabe okhulupirika. Ndiyeno akadzaikidwa chidindo chomaliza, kaya atatsala pang’ono kumwalira kapena chisautso chachikulu chitatsala pang’ono kuyamba, mayina awo sadzafufutidwanso m’bukuli.—Chiv. 7:3. w22.09 14 ¶3; 15 ¶5-6

Lachisanu, October 18

Osangalala ndi anthu amene akumva mawu a Mulungu n’kuwasunga! —Luka 11:28.

Kodi zinthu ngati izi zinakuchitikiraponi? Munthu wina wakuphikirani chakudya chimene mumachikonda. Koma mwina chifukwa choti mulibe nthawi yokwanira kapena mwasokonezedwa chifukwa choganizira zinthu zina, mwangodya chakudyacho mofulumira osamvetsera kukoma kwake bwinobwino. Pamene mwamaliza kudya, mukuzindikira kuti mumadya mofulumira kwambiri ndipo mukulakalaka mukanachidya pang’onopang’ono kuti muchimve kukoma. Kodi munayamba mwawerengapo Baibulo mofulumira choncho, moti munalephera kumvetsa uthenga wake? Muzikhala ndi nthawi yokwanira kuti muzisangalala mukamawerenga Mawu a Mulungu. Muziyerekezera kuti mukuona zimene zikuchitikazo m’maganizo mwanu, kumva phokoso komanso zimene anthu akulankhula ndipo muziganizira zimene mwawerengazo. Zimenezi zingachititse kuti muzisangalala kwambiri. Yesu anasankha “kapolo wokhulupirika komanso wanzeru” kuti azitipatsa chakudya chauzimu pa nthawi yoyenera ndipo timadyetsedwa bwino mwauzimu. (Mat. 24:45) Malemba ouziridwa ndi mbali yaikulu ya chakudya chauzimu chomwe kapoloyu amatipatsa.—1 Ates. 2:13. w22.10 7-8 ¶6-8

Loweruka, October 19

Anthu odzikuza atinyoza kwambiri. —Sal. 123:4.

Baibulo linaneneratu kuti m’masiku otsiriza padzakhala anthu ambiri onyoza. (2 Pet. 3:​3, 4) Iwo amangochita “zinthu zoipa zimene amalakalaka.” (Yuda 7, 17, 18) Kodi tingatani kuti tisakhale m’gulu la anthu onyoza? Njira imodzi ndi kupewa kugwirizana ndi anthu omwe amangokhalira kudandaula zilizonse. (Sal. 1:1) Zimenezi zikutanthauza kuti sitikuyenera kumvetsera kapena kuwerenga chilichonse chochokera kwa ampatuko. Timazindikira kuti ngati sitingasamale, tikhoza kuyamba kumangodandaula zilizonse komanso kumakayikira Yehova ndi malangizo amene amatipatsa kudzera m’gulu lake. Kuti zimenezi zisatichitikire tiyenera kumadzifunsa kuti: ‘Kodi nthawi zambiri ndimakonda kudandaula tikalandira malangizo kapena mfundo zina zikafotokozedwa mwatsopano? Kodi ndimakonda kupezera zifukwa amene akutsogolera?’ Tikasiya kuchita zimenezi mwamsanga, Yehova adzasangalala nafe.—Miy. 3:​34, 35. w22.10 20 ¶9-10

Lamlungu, October 20

A nyumba ya Isiraeli akakana kukumvera.—Ezek. 3:7.

Mzimu wa Mulungu unapatsa mphamvu Ezekieli yoti athe kugwira ntchito yolalikira kwa anthu a m’gawo lake omwe anali “amakani komanso osamva.” Yehova anauza Ezekieli kuti: “Ndachititsa kuti nkhope yako ikhale yolimba mofanana ndi nkhope zawo, ndiponso chipumi chako kuti chikhale cholimba mofanana ndi zipumi zawo. Ndachititsa kuti chipumi chako chikhale ngati mwala wa dayamondi, cholimba kuposa mwala wa nsangalabwi. Usawaope kapena kuchita mantha ndi nkhope zawo.” (Ezek. 3:​8, 9) Apa zinali ngati Yehova akuuza Ezekieli kuti ‘usafooke chifukwa cha kuuma mitima kwawo, ineyo ndikulimbitsa.’ Pambuyo pake mzimu wa Mulungu unatengera Ezekieli kugawo limene ankafunika kukalalikira. Iye analemba kuti: “Dzanja la Yehova linandigwira mwamphamvu.” Mneneriyu zinamutengera mlungu wathunthu kuti amvetse uthenga umene ankafunika kukalalikira. (Ezek. 3:​14, 15) Kenako Yehova anamutsogolera kuchigwa komwe “mzimu unalowa mwa [iye].” (Ezek. 3:​23, 24) Tsopano Ezekieli anali wokonzeka kuyamba utumiki wake. w22.11 4-5 ¶8-9

Lolemba, October 21

Inu Yehova, kodi ndidzalirira thandizo koma inu osandimva mpaka liti? . . . N’chifukwa chiyani mukundichititsa kuona zinthu zoipa?—Hab. 1:​2, 3.

Mneneri Habakuku anakumana ndi mavuto ambiri. Pa nthawi ina, ankakayikira ngati Yehova ankamuganizira. Choncho anapemphera kwa iye mochokera pansi pa mtima. Yehova anayankha pemphero la mtumiki wake wokhulupirikayu. (Hab. 2:​2, 3) Ataganizira mmene Yehova anapulumutsira anthu ake m’mbuyomu, Habakuku anayambiranso kukhala wosangalala. Iye anatsimikiza kuti Yehova amamuganizira komanso kuti amuthandiza kupirira mayesero aliwonse. (Hab. 3:​17-19) Kodi tikuphunzirapo chiyani? Mukakumana ndi mavuto, muzipemphera kwa Yehova ndipo muzimuuza mmene mukumvera. Kenako muzimudalira kuti akuthandizani. Mukatero, mungakhale otsimikiza kuti Yehova akupatsani mphamvu zomwe mumafunikira kuti mupirire. Ndipo mukaona kuti wakuthandizani, mudzayamba kumukhulupirira kwambiri. Ngati nthawi zonse mumachita zinthu zokhudza kulambira, simudzalola kuti kukayikira kapena mavuto omwe mukukumana nawo, zikulekanitseni ndi Yehova.—1 Tim. 6:​6-8. w22.11 15 ¶6-7

Lachiwiri, October 22

Ndithu ndikukuuza lero, iwe udzakhala ndi ine m’Paradaiso.—Luka 23:43.

Yesu ndi achifwamba amene anapachikidwa naye limodzi ankamva ululu woopsa pomwe moyo wawo unkachoka pang’onopang’ono. (Luka 23:​32, 33) Achifwambawa ankamunyoza Yesu. (Mat. 27:44; Maliko 15:32) Koma mmodzi wa iwo anasintha maganizo. Iye anati: “Yesu, mukandikumbukire mukakalowa mu Ufumu wanu.” Yesu anayankha zimene zili mulemba laleroli. (Luka 23:​39-43) Mawu amene Yesu anauza wachifwambayu ayenera kutichititsa kuganizira mmene moyo udzakhalire m’Paradaiso. Ndipotu tingaphunzirepo kanthu zokhudza Paradaiso pa ulamuliro wa Mfumu Solomo womwe unali wamtendere. Tingayembekezere Yesu yemwe ndi woposa Solomo kuti adzagwira ntchito ndi olamulira anzake kukonza dzikoli kuti likhale malo abwino kwambiri. (Mat. 12:42) N’zomveka kuti a “nkhosa zina” angakhale ofunitsitsa kudziwa zomwe akuyenera kuchita kuti adzakhale ndi moyo mpaka kalekale m’Paradaiso.—Yoh. 10:16. w22.12 8 ¶1; 9 ¶4

Lachitatu, October 23

Mulungu adzakukomerani mtima akadzamva kulira kwanu kopempha thandizo.—Yes. 30:19.

Yesaya anatitsimikizira kuti Yehova adzamvetsera mwatcheru pamene tikupempha thandizo ndipo adzayankha mofulumira mapemphero athu. Iye anawonjezera kuti: “Akadzangomva kulira kwanu, nthawi yomweyo adzakuyankhani.” Mawu olimbikitsawa amatikumbutsa kuti Atate wathu ndi wofunitsitsa kuthandiza aliyense amene amapempha thandizo kwa iye. Kudziwa zimenezi kumatithandiza kuti tizipirira mosangalala. Yehova amamvetsera mapemphero athu aliyense payekha. N’chifukwa chiyani tikutero? Mumbali yoyamba ya Yesaya chaputala 30, Yehova anagwiritsa ntchito mawu akuti “inu” ponena za anthu ake monga gulu. Koma muvesi 19, mawu akuti “inu” amasonyeza kuti uthengawo ukupita kwa munthu aliyense payekha. Yesaya analemba kuti: “Inu simudzaliranso”; “Mulungu adzakukomerani mtima”; “adzakuyankhani.” Monga Tate wachikondi, Yehova amaganizira aliyense payekha ndipo amamvetsera pemphero la aliyense mwachidwi.—Sal. 116:1; Yes. 57:15. w22.11 9 ¶5-6

Lachinayi, October 24

Muzichita zinthu mochenjera ngati njoka koma moona mtima ngati nkhunda.—Mat. 10:16.

Kulalikira komanso kuphunzitsa anthu ngakhale pamene tikuzunzidwa, kumatipatsa chimwemwe komanso mtendere. M’mbuyomo olamulira a Chiyuda atalamula atumwi kuti asiye kulalikira, amuna okhulupirikawa anasankha kumvera Mulungu. Iwo anapitirizabe kulalikira ndipo zimenezi zinawathandiza kukhala osangalala. (Mac. 5:​27-29, 41, 42) N’zoona kuti pamene ntchito yathu yaletsedwa timayenera kulalikira mosamala. Koma ngati timachita zonse zomwe tingathe, tingapeze mtendere umene umabwera chifukwa chakuti tikusangalatsa Yehova komanso tikugwira ntchito yolengeza uthenga wopulumutsa moyo. Musamakayikire kuti ngakhale pa nthawi zovuta kwambiri mungathe kukhala ndi mtendere. Pa nthawi ngati zimenezi tizikumbukira kuti mtendere umene timafunika ndi mtendere umene Yehova yekha ndi amene angatipatse. Muzimudalira pa nthawi ya mliri, ngozi zam’chilengedwe komanso mukamazunzidwa. Tisamasiyane ndi gulu lake. Tiziganizira zinthu zabwino kwambiri zimene tikuyembekezera m’tsogolo. Tikamatero, ‘Mulungu wamtendere adzakhala nafe.’—Afil. 4:9. w22.12 21 ¶17-18

Lachisanu, October 25

Muvale umunthu watsopano. —Aef. 4:24.

Zimenezitu zimafunika kuchita khama. Mwa zina, tiyenera kuyesetsa kuti tisiye makhalidwe oipa monga kuwawidwa mtima kwa njiru, kupsa mtima komanso mkwiyo. (Aef. 4:​31, 32) N’chifukwa chiyani kuchita zimenezi kungakhale kovuta? Chifukwa makhalidwe ena oipa amakhala kuti anazika mizu. Mwachitsanzo, Baibulo limanena kuti anthu ena ‘sachedwa kukwiya’ komanso “sachedwa kupsa mtima.” (Miy. 29:22) Kusintha makhalidwe oipa omwe tinazolowera kumafuna kupitirizabe kuchita khama ngakhale pambuyo pobatizidwa. (Aroma 7:​21-23) Muzipemphera kwa Yehova za khalidwe loipa lomwe mukulimbana nalo ndipo muzikhulupirira kuti akuyankhani komanso kukuthandizani. (1 Yoh. 5:​14, 15) Ngakhale kuti Yehova sangachotse khalidwelo mozizwitsa, adzakupatsani mphamvu kuti mulisiye. (1 Pet. 5:10) Muzichita mogwirizana ndi mapemphero anu poyesetsa kusachita zinthu zomwe zingakupangitseni kuyambiranso kusonyeza umunthu wakale. Komanso musamangokhalira kuganizira zinthu zoipa.—Afil. 4:8; Akol. 3:2. w23.01 10 ¶7, 9-10

Loweruka, October 26

Munthu amene amakonda Mulungu azikondanso m’bale wake.—1 Yoh. 4:21.

Njira imodzi imene timasonyezera chikondi, ndi kugwira nawo mwakhama ntchito yolalikira. Timalalikira kwa aliyense amene takumana naye. Sitimasankha munthu chifukwa cha mtundu wake, chikhalidwe, kapezedwe kake ka zinthu kapenanso maphunziro ake. Tikamachita zimenezi timakhala tikuchita zinthu mogwirizana ndi chifuniro cha Yehova chakuti “anthu osiyanasiyana apulumuke n’kukhala odziwa choonadi molondola.” (1 Tim. 2:4) Timasonyezanso kuti timakonda Mulungu ndi Khristu tikamakonda abale ndi alongo athu. Timawaganizira ndipo timawathandiza akakumana ndi mayesero. Timawatonthoza akaferedwa, kukawaona akadwala komanso timachita zonse zomwe tingathe kuti tiwalimbikitse pamene afooka. (2 Akor. 1:​3-7; 1 Ates. 5:​11, 14) Timapitiriza kuwapempherera chifukwa timadziwa kuti “pemphero lopembedzera la munthu wolungama limagwira ntchito mwamphamvu kwambiri.”—Yak. 5:16. w23.01 28-29 ¶7-8

Lamlungu, October 27

Pitirizani kutonthozana ndi kulimbikitsana.—1 Ates. 5:11.

Mofanana ndi wogwira ntchito zomangamanga, yemwe luso lake limawonjezeka m’kupita kwa nthawi, ifenso tingawonjezere zomwe timachita polimbikitsana. Tingathandize ena kupirira mayesero amene akukumana nawo, powafotokozera zitsanzo za anthu akale omwe anapirira. (Aheb. 11:​32-35; 12:1) Tingalimbikitse mtendere potchula zabwino zimene ena amachita, kupewa zinthu zimene zingasokoneze mtendere, komanso kubwezeretsa mtendere pakakhala kusemphana maganizo. (Aef. 4:3) Ndiponso tingapitirize kulimbikitsa chikhulupiriro cha abale ndi alongo athu powafotokozera mfundo zofunika za choonadi, powathandiza kupeza zimene akufunikira komanso kulimbikitsa amene chikhulupiriro chawo chafooka. Tikhoza kumasangalala komanso kukhala okhutira tikamathandiza abale ndi alongo athu mumpingo kukhala ndi chikhulupiriro cholimba. Mosiyana ndi nyumba zimene m’kupita kwa nthawi zimawonongeka, zotsatirapo za zimene timachita polimbikitsa ena, zidzakhalapo mpaka kalekale. w22.08 22 ¶6; 25 ¶17-18

Lolemba, October 28

Yehova ndi amene amapereka nzeru. Kudziwa zinthu komanso kuzindikira zimatuluka m’kamwa mwake.—Miy. 2:6.

Yesu anatchula khalidwe lofunika kwambiri la kuzindikira lomwe lingatithandize kuti tizimvetsa zomwe timawerenga m’Mawu a Mulungu. (Mat. 24:15) Kodi kuzindikira n’kutani? Ndi luso lotha kudziwa kugwirizana pakati pa mfundo ina ndi mfundo ina kapena kusiyana komwe kulipo komanso kumvetsa bwino ngakhale zimene sizinafotokozedwe. Kuwonjezera pamenepo, Yesu anasonyeza kuti timafunika kukhala ozindikira kuti tithe kuona zinthu zimene zikukwaniritsa maulosi a m’Baibulo. Timafunikanso khalidweli kuti tizipindula ndi zonse zomwe timawerenga m’Baibulo. Yehova amathandiza atumiki ake kuti akhale ozindikira. Choncho muzipemphera kwa iye ndipo muzimupempha kuti akuthandizeni kukulitsa khalidweli. Kodi mungatani kuti muzichita zinthu mogwirizana ndi pemphero lanu? Mosamala kwambiri, muziganizira zimene mwawerenga ndipo muziona mmene zikugwirizanira ndi zomwe mukudziwa. Muzifufuza tanthauzo la zomwe mukuwerenga m’Baibulo komanso kuona mmene mungagwiritsire ntchito mfundo zake pa moyo wanu. (Aheb. 5:14) Luso lotha kuzindikira powerenga lidzakuthandizani kuti muzimvetsa bwino Malemba. w23.02 10 ¶7-8

Lachiwiri, October 29

Chifukwa cha iye tili ndi moyo, timayenda ndipo tilipo.—Mac. 17:28.

Tayerekezerani kuti mnzanu wakupatsani chithunzi chojambulidwa mwaluso chakale koma chamtengo wapatali. Chithunzicho chili ndi malo ena akuda komanso owonongeka. Ngakhale zili choncho chithunzicho ndi chodula moti chingagulitsidwe ndi ndalama za madola mamiliyoni. N’zoonekeratu kuti mungayamikire komanso kumachiteteza. Mofanana ndi zimenezi Yehova watipatsa mphatso yamtengo wapatali ya moyo. Ndipotu Yehova anasonyeza kuti amaona kuti moyo wathu ndi wamtengo wapatali popereka Mwana wake monga dipo. (Yoh. 3:16) Yehova ndi Mwiniwake wa moyo. (Sal. 36:9) Mtumwi Paulo anavomereza mfundo ya choonadi imeneyi pomwe anati: “Chifukwa cha iye tili ndi moyo, timayenda ndipo tilipo.” (Mac. 17:​25, 28) Choncho m’pomveka kunena kuti moyo ndi mphatso yochokera kwa Mulungu. Mwachikondi, iye amatipatsa zonse zomwe timafunikira kuti tikhale ndi moyo. (Mac. 14:​15-17) Koma panopa sikuti Yehova amateteza moyo wathu mozizwitsa. M’malomwake amayembekezera kuti tichita zonse zomwe tingathe kuti tikhale ndi thanzi labwino komanso tipitirize kumutumikira.—2 Akor. 7:1. w23.02 20 ¶1-2

Lachitatu, October 30

Lemba m’buku mawu onse amene ndikukuuza.—Yer. 30:2.

Timayamikira kwambiri Yehova chifukwa chotipatsa Baibulo. Kudzera m’bukuli, iye amatipatsa malangizo anzeru amene angatithandize kudziwa zomwe tingachite polimbana ndi mavuto omwe timakumana nawo masiku ano. Amatipatsanso chiyembekezo chosangalatsa cha m’tsogolo. Koposa zonse kudzera m’Baibulo, Yehova watidziwitsa zambiri zokhudza makhalidwe ake. Tikamaganizira makhalidwe ake abwinowa, timakhudzidwa mtima ndipo izi zimachititsa kuti tiyambe kukhala naye pa ubwenzi wolimba. (Sal. 25:14) Yehova amafuna kuti anthu amudziwe. M’mbuyomu, iye anadzidziwikitsa kwa anthu kudzera mwa angelo, m’maloto komanso m’masomphenya. (Num. 12:6; Mac. 10:​3, 4) Koma kodi tikanadziwa bwanji zokhudza maloto, masomphenya kapena mauthenga ochokera kwa angelowa zikanakhala kuti sizinalembedwe penapake? Choncho pachifukwa chabwino, Yehova anauza amuna kuti ‘alembe m’buku’ zimene ankafuna kuti tizidziwe. Popeza kuti “njira ya Mulungu woona ndi yangwiro,” sitikayikira kuti njira imene anagwiritsa ntchito polankhula nafeyi ndi yabwino kwambiri komanso yothandiza.—Sal. 18:30. w23.02 2 ¶1-2

Lachinayi, October 31

Kupatsa kumatichititsa kukhala osangalala kwambiri kuposa kulandira.—Mac. 20:35.

Muzikhala ndi zolinga zothandiza. Muzisankha zolinga zimene zingalimbitse chikhulupiriro chanu komanso kukuthandizani kuti mukhale Mkhristu wolimba. (Aef. 3:16) Mwachitsanzo, mungasankhe kuti muziphunzira panokha komanso kuwerenga Baibulo nthawi zonse. (Sal. 1:​2, 3) Kapenanso mungakonze zoti muzipemphera pafupipafupi komanso mochokera pansi pa mtima. Mwinanso mungaone kuti mukufunika kumadziletsa pa nkhani yosankha zosangalatsa komanso mmene mumagwiritsira ntchito nthawi yanu. (Aef. 5:​15, 16) Mungakhale Mkhristu wolimba mukamathandiza anthu ena. Mwachitsanzo, mungakhale ndi cholinga choti muzithandiza achikulire komanso odwala mumpingo mwanu. Mwina mungamakawagulire zinthu kapenanso kuwathandiza mmene angagwiritsire ntchito zipangizo zawo zamakono. Mungasonyezenso kuti mumakonda anthu omwe si a Mboni powalalikira uthenga wabwino wa Ufumu. (Mat. 9:​36, 37) Ngati n’zotheka, mungadziikire cholinga choti muchiteko utumiki winawake wa nthawi zonse. w22.08 6 ¶16-17

    Mabuku a Chichewa (1974-2026)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena