Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • es24 tsamba 108-118
  • November

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • November
  • Kuphunzira Malemba Tsiku ndi Tsiku—2024
  • Timitu
  • Lachisanu, November 1
  • Loweruka, November 2
  • Lamlungu, November 3
  • Lolemba, November 4
  • Lachiwiri, November 5
  • Lachitatu, November 6
  • Lachinayi, November 7
  • Lachisanu, November 8
  • Loweruka, November 9
  • Lamlungu, November 10
  • Lolemba, November 11
  • Lachiwiri, November 12
  • Lachitatu, November 13
  • Lachinayi, November 14
  • Lachisanu, November 15
  • Loweruka, November 16
  • Lamlungu, November 17
  • Lolemba, November 18
  • Lachiwiri, November 19
  • Lachitatu, November 20
  • Lachinayi, November 21
  • Lachisanu, November 22
  • Loweruka, November 23
  • Lamlungu, November 24
  • Lolemba, November 25
  • Lachiwiri, November 26
  • Lachitatu, November 27
  • Lachinayi, November 28
  • Lachisanu, November 29
  • Loweruka, November 30
Kuphunzira Malemba Tsiku ndi Tsiku—2024
es24 tsamba 108-118

November

Lachisanu, November 1

Mawu owola asamatuluke pakamwa panu, koma pazituluka mawu abwino okha kuti alimbikitse ena.—Aef. 4:29.

Mawu alionse oipa sayenera kutuluka pakamwa pa Mkhristu. Koma pali mawu ena amene sangaonekeretu kuti ndi oipa omwe tiyenera kusamala nawo. Mwachitsanzo, tiyenera kukhala osamala kuti tisamalankhule zoipa zokhudza anthu ena omwe timasiyana nawo chikhalidwe, mtundu kapena mayiko. Kuwonjezera pamenepo, sitiyenera kukhumudwitsa ena powalankhula mawu achipongwe. Muzilankhula zimene zingalimbikitse ena. Muziyamikira ena m’malo mofulumira kuwadzudzula kapena kudandaula. Aisiraeli anali ndi zinthu zambiri zomwe zikanawachititsa kukhala oyamikira, koma nthawi zambiri iwo ankangodandaula. Tisamaiwale kuti ngati timakonda kudandaula zingachititse kuti enanso azidandaula. Mwina mungakumbukire kuti zinthu zosalimbikitsa zimene azondi 10 ananena zinachititsa kuti ‘ana onse a Isiraeli ayambe kudandaula za Mose.’ (Num. 13:31–14:4) Koma kuyamikira ena, kungathandize kuti aliyense azisangalala. Choncho muziyesetsa kupeza mipata yoyamikira ena mochokera pansi pa mtima. w22.04 8 ¶16-17

Loweruka, November 2

Ndinaperekedwa kwa inu kuti muzindisamalira kuyambira pamene ndinabadwa. Kuyambira ndili m’mimba mwa mayi anga, inu mwakhala Mulungu wanga.—Sal. 22:10.

Kuyambira kale, Yehova wakhala akuthandiza achinyamata ambiri kuti akhale mabwenzi ake. Iye angathandizenso ana anu kukhala naye pa ubwenzi ngati iwowo akufuna. (1 Akor. 3:​6, 7) Ngakhale zitaoneka kuti sakumutumikira ndi mtima wonse, iye adzapitiriza kuwakonda. (Sal. 11:4) Akadzangosonyeza ngakhale pang’ono “maganizo abwino” iye adzawathandiza. (Mac. 13:48; 2 Mbiri 16:9) Adzakuthandizani kulankhula zoyenera pa nthawinso yoyenera pamene ana anu akufunikira kwambiri kumva zimenezo. (Miy. 15:23) Kapenanso angalimbikitse m’bale kapena mlongo wina mumpingo kuti awasonyeze chidwi. Ngakhale anawo atakula, Yehova angawathandize kukumbukira zimene munawaphunzitsa m’mbuyomu. (Yoh. 14:26) Yehova adzakudalitsani kwambiri mukamapitiriza kuphunzitsa ana anu mwa zolankhula ndi zochita zanu. w22.04 21 ¶18

Lamlungu, November 3

Chinjokacho chinakwiya. —Chiv. 12:17.

Popeza kuti Satana sangapitenso kumwamba, iye amalimbana ndi odzozedwa a padzikoli omwe amaimira Ufumu wa Mulungu ndipo “ali ndi ntchito yochitira umboni za Yesu.” (2 Akor. 5:20; Aef. 6:​19, 20) Mu 1918, 8 mwa abale audindo anaweruzidwa kuti ndi olakwa pa milandu yabodza ndipo anagamulidwa kuti akakhale kundende kwa nthawi yaitali. Zinkangooneka ngati ntchito ya abalewa yatheratu. (Chiv. 11:​3, 7-11) Koma chakumayambiriro kwa chaka cha 1919, abale odzozedwa aja anatulutsidwa m’ndende ndipo milandu yawo inathetsedwa. Nthawi yomweyo abalewo anayambiranso ntchito yawo ya Ufumu. Koma zimenezi sizinachititse kuti Satana asiye kuukira anthu a Mulungu. Kungochokera nthawi imeneyo, iye wakhala akuchititsa “mtsinje” wamazunzo polimbana ndi anthu onse a Mulungu. (Chiv. 12:15) Kunena zoona, apa ndi pamene aliyense “akufunika kupirira ndiponso kukhala ndi chikhulupiriro.”—Chiv. 13:10. w22.05 5-6 ¶14-16

Lolemba, November 4

Ndinamva chiwerengero cha amene anadindidwa chidindo. Anthu okwana 144,000.—Chiv. 7:4.

M’masomphenya, mtumwi Yohane anaona magulu awiri a anthu omwe ali kumbali ya ulamuliro wa Yehova ndipo adzalandira moyo wosatha. M’gulu loyamba muli anthu 144,000. Iwo anatengedwa padziko lapansi kuti akakhale ndi Yesu mu Ufumu wake kumwamba. Limodzi ndi iye adzalamulira dziko lonse lapansi. (Chiv. 5:​9, 10; 14:​3, 4) Yohane anawaona m’masomphenya ataimirira ndi Yesu pa Phiri la Ziyoni kumwamba. (Chiv. 14:1) Kwa zaka zambiri, anthu ochuluka akhala akusankhidwa kuti akhale m’gulu la a 144,000. (Luka 12:32; Aroma 8:17) Koma Yohane anauzidwa kuti ochepa mwa anthu amenewa adzakhala adakali ndi moyo padzikoli m’masiku otsiriza. (Chiv. 12:17) Kenako mkatikati mwa chisautso chachikulu adzatengedwa kupita kumwamba kuti akakumane ndi anzawo a 144,000, omwe anamwalira ali okhulupirika. Kumeneko iwo azikalamulira limodzi ndi Yesu mu Ufumu wa Mulungu.—Mat. 24:31; Chiv. 5:​9, 10. w22.05 16 ¶4-5

Lachiwiri, November 5

[Muzimvera] malamulo anga. —Yes. 48:18.

Yesu anaphunzitsa otsatira ake kuti azidziona moyenera. Iye anawalimbikitsa kuti: “Tsitsi lonse lam’mutu mwanu amaliwerenga.” (Mat. 10:30) Mawu amenewa ndi olimbikitsa kwambiri makamaka ngati nthawi zina timadziona molakwika. Amasonyeza kuti Atate wathu wakumwamba amachita nafe chidwi ndipo ndife ofunika kwambiri kwa iye. Sitiyenera kuganiza kuti iye akulakwitsa potilola kuti tizimulambira komanso kutiona kuti ndife oyenera kudzalandira moyo wosatha. Zaka 15 zapitazo, Nsanja ya Olonda ina inatilimbikitsa kuti tizidziona moyenera. Inanena kuti: ‘Indedi, sitiyenera kuganiza kuti ndife ofunika kwambiri mpaka kuyamba kunyada. Komanso tisamachite kudzitsitsa monyanyira n’kumadziona ngati ndife opanda ntchito. Cholinga chathu chiyenera kukhala kumadziona m’njira yoyenera n’kumadziwa zimene tingakwanitse ndi zomwe sitingakwanitse.’ w22.05 24-25 ¶14-16

Lachitatu, November 6

[Ndikupempha] . . . kuti onsewa akhale amodzi.—Yoh. 17:​20, 21.

Kodi ifeyo patokha tingatani kuti tizilimbikitsa mgwirizano mumpingo? Tizikhala anthu obweretsa mtendere. (Mat. 5:9; Aroma 12:18) Nthawi iliyonse yomwe tachita zinthu zolimbikitsa mtendere mumpingo, timawonjezera kukongola kwa paradaiso wauzimu. Timakumbukira kuti Yehova ndi amene wakokera kwa iye aliyense yemwe ali m’paradaisoyu. (Yoh. 6:44) Tangoganizani mmene Yehova amasangalalira akationa kuti tikuyesetsa kulimbikitsa mtendere ndi mgwirizano pakati pa atumiki ake, omwe amawaona kuti ndi amtengo wapatali. (Yes. 26:3; Hag. 2:7) Kodi tingatani kuti tizipindula mokwanira ndi madalitso omwe timalandira monga atumiki a Mulungu? Tiziganizira kwambiri zomwe timaphunzira m’Mawu a Mulungu. Kuchita zimenezi kungatithandize kuti tikhale ndi makhalidwe omwe angachititse kuti ‘tizikonda abale’ komanso ‘tikhale ndi chikondi chenicheni pakati pathu.’—Aroma 12:10. w22.11 12-13 ¶16-18

Lachinayi, November 7

Ndidzawakhululukira zolakwa zawo ndipo machimo awo sindidzawakumbukiranso.—Yer. 31:34.

Tikavomereza kuti Yehova watikhululukira timasangalala ndi “nyengo zotsitsimutsa,” zomwe zikuphatikizapo kukhala ndi mtendere wa m’maganizo komanso chikumbumtima choyera. Yehova yekha ndi amene angatikhululukire choncho osati anthu. (Mac. 3:19) Iye akatikhululukira, timakhala nayenso pa ubwenzi wabwino ngati kuti sitinachimwe n’komwe. Yehova akatikhululukira satiimbanso mlandu kapena kutilanga chifukwa cha tchimo lomwe tinachitalo. (Yes. 43:25) Iye amaika machimo athu kutali, “mofanana ndi mmene kotulukira dzuwa kwatalikirana ndi kolowera dzuwa.” (Sal. 103:12) Tikaganizira zimene Yehova amachita potikhululukira timasowa chonena ndipo timamuyamikira kwambiri. (Sal. 130:4) Sikuti Yehova amasankha kutikhululukira potengera kukula kapena kuchepa kwa tchimo lomwe tachita. Yehova amagwiritsa ntchito zomwe amadziwa monga Mlengi wathu, Wotipatsa malamulo komanso Woweruza wathu posankha kuti akhululuke. w22.06 5 ¶12-14

Lachisanu, November 8

Aliyense wofuna kulambira Mulungu ayenera kukhulupirira kuti iye alikodi ndipo amapereka mphoto kwa anthu amene amamufunafuna ndi mtima wonse.—Aheb. 11:6.

Yehova wapereka chiyembekezo chabwino kwambiri kwa onse omwe amamukonda. Posachedwapa athetsa matenda, zopweteka komanso imfa. (Chiv. 21:​3, 4) Iye adzathandiza “ofatsa” omwe akumuyembekezera kukonza dzikoli kukhala paradaiso. (Sal. 37:​9-11) Adzathandizanso aliyense wa ife kukhala naye pa ubwenzi wabwino kuposa panopa. Chimenechitu ndi chiyembekezo chabwino kwambiri. Koma kodi n’chifukwa chiyani timakhulupirira kuti malonjezo a Mulungu adzakwaniritsidwadi? Nthawi zonse iye amakwaniritsa malonjezo ake. Choncho tili ndi chifukwa chomveka chotichititsa ‘kuyembekezera Yehova.’ (Sal. 27:14) Timachita zimenezi poyembekezera moleza mtima komanso mosangalala kuti Mulungu akwaniritse cholinga chake. (Yes. 55:​10, 11) Tiyeni tipitirize kukhala okhulupirika kwa Yehova ndipo tisamakayikire kuti adzapereka mphoto kwa “anthu amene amamufunafuna ndi mtima wonse.” w22.06 20 ¶1; 25 ¶18

Loweruka, November 9

Atate wanu amadziwa zimene mukufunikira musanapemphe n’komwe.—Mat. 6:8.

Tingakhale otsimikiza kuti monga Mutu wa banja, Yehova adzachita zomwe anauza mitu ya mabanja pa 1 Timoteyo 5:8. Tikamakhulupirira kuti Yehova amatikonda komanso amakonda banja lathu, sitingakayikire kuti tidzapeza zomwe timafunikira. (Mat. 6:​31-33) Iye amafunitsitsa kutipatsa zimene timafunikira, ndipo ndi wowolowa manja. Pamene ankalenga dzikoli, sikuti anangotipatsa zinthu zimene zingatithandize kukhala ndi moyo. Mwachikondi, iye anadzaza dzikoli ndi zinthu zomwe zikanachititsa kuti tizisangalala kwambiri. (Gen. 2:9) Ngakhale kuti nthawi zina tingakhale ndi zinthu zofunika zokha tingachite bwino kumakumbukira kuti Yehova ndi amene watipatsa zimenezo. (Mat. 6:11) Tisamaiwale kuti zilizonse zimene tingadzimane sizingafanane ndi zimene Mulungu wathu wachikondi angatipatse panopa kapenanso m’tsogolo.—Yes. 65:​21, 22. w22.06 15 ¶7-8

Lamlungu, November 10

Chakudya chotafuna ndi cha anthu aakulu mwauzimu.—Aheb. 5:14.

Si anthu amene angoyamba kuphunzira Baibulo okha omwe amafunika kudziwa mfundo zozama zokhudza Yehova ndiponso Mawu ake. Tonsefe timafunikira mfundozi. Mtumwi Paulo analemba kuti kugwiritsa ntchito mfundo zotere kungatithandize kuti ‘tizisiyanitsa choyenera ndi chosayenera.’ M’masiku ovuta ano, pomwe makhalidwe a anthu aipa kwambiri, si zophweka kutsatira mfundo za Yehova. Koma Yesu amaonetsetsa kuti tapeza mphamvu zomwe timafunikira potipatsa malangizo abwino omwe angalimbitse chikhulupiriro chathu. Malangizo amenewa amachokera m’Mawu a Mulungu, Baibulo. Mofanana ndi Yesu, dzina la Mulungu timalipatsa ulemu umene limafunikira. (Yoh. 17:​6, 26) Mwachitsanzo, mu 1931 tinayamba kudziwika ndi dzina la m’Malemba lakuti Mboni za Yehova. Zimenezi zinasonyeza kuti timaona kuti dzina la Atate wathu wakumwambali ndi lofunika kwambiri kwa ife. (Yes. 43:​10-12) Kuwonjezera pamenepo, Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika linabwezeretsa dzina la Mulungu m’malo ake oyenerera. w22.07 11 ¶11-12

Lolemba, November 11

Mawu anu ndi nyale younikira kumapazi anga, komanso kuwala kounikira njira yanga.—Sal. 119:105.

Choonadi cha m’Baibulo chimaphatikizaponso uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu. Yesu anayerekezera choonadi cha Ufumuwo ndi chuma chobisika. Pa Mateyu 13:​44, iye anati: “Ufumu wakumwamba uli ngati chuma chobisika m’munda, chimene munthu anachipeza n’kuchibisa. Chifukwa cha chimwemwe chimene anali nacho, anapita kukagulitsa zinthu zonse zimene anali nazo n’kukagula mundawo.” Onani kuti munthu wotchulidwa palembali sikuti ankafunafuna chumacho. Koma atachipeza analolera kusiya zinthu zambiri kuti akhale nacho. Ndipotu anagulitsa chilichonse chimene anali nacho. Chifukwa chiyani? Ankadziwa kuti chumacho chinali chamtengo wapatali kwambiri. Timadziwa kuti palibe chimene dzikoli lingatipatse, chomwe tingayerekezere ndi chimwemwe chimene timapeza chifukwa chotumikira Yehova panopa poyembekezera kudzakhala ndi moyo wosatha mu Ufumu wa Mulungu. Mwayi wokhala naye pa ubwenzi ndi wamtengo wapatali kuposa chilichonse chomwe tingafunike kusiya. Timasangalala kwambiri ‘tikamamusangalatsa pa chilichonse.’—Akol. 1:10. w22.08 15 ¶8-9; 17 ¶12

Lachiwiri, November 12

Ndingachitirenji choipa chachikulu chonchi n’kuchimwira Mulungu? —Gen. 39:9.

Kodi Yosefe anadziwa bwanji kuti Mulungu wake amaona kuti chigololo ndi “choipa chachikulu”? Lamulo la m’Chilamulo cha Mose lakuti, “Usachite chigololo,” linalembedwa patapita zaka 200 kuchokera pa nthawiyo. (Eks. 20:14) Komabe Yosefe ankadziwa bwino Yehova ndipo anazindikira mmene angamvere ngati iye atachita chiwerewere. Mwachitsanzo, n’zosakayikitsa kuti Yosefe ankadziwa zimene Yehova anakonza pa nkhani ya ukwati kuti mwamuna azikhala ndi mkazi mmodzi. Ayeneranso kuti anamva mmene Yehova kawiri konse anatetezera agogo ake a Sara, pamene anakumana ndi zinthu zomwe zikanachititsa kuti asakhale wokhulupirika kwa mwamuna wawo. Mulungu anachitanso chimodzimodzi poteteza Rabeka mkazi wa Isaki. (Gen. 2:24; 12:​14-20; 20:​2-7) Kuganizira nkhani zimenezi kunathandiza Yosefe kuzindikira zoyenera ndi zosayenera pamaso pa Mulungu. Chifukwa chakuti Yosefe ankakonda Mulungu, ankakondanso mfundo zake zolungama ndipo anatsimikiza mtima kuzitsatira. w22.08 26 ¶1-2

Lachitatu, November 13

Ambiri amene agona munthaka adzadzuka. Ena adzalandira moyo wosatha.—Dan. 12:2.

Ulosiwu sukunena za kuukitsidwa kophiphiritsa kapena kwauzimu komwe kukuchitika masiku otsiriza ano, monga mmene tinkakhulupirira m’mbuyomu. M’malomwake, mawuwa akunena za kuukitsidwa kwa anthu komwe kudzachitike m’dziko latsopano. N’chifukwa chiyani tikutero? Mawu akuti “munthaka,” kapena kuti m’fumbi, omwe agwiritsidwanso ntchito pa Yobu 17:​16, ndi ofanana ndi mawu akuti “manda.” Choncho lemba la Danieli 12:​2, likunena za kuukitsidwa kumanda komwe kudzachitike masiku otsiriza akadzatha komanso pambuyo pa nkhondo ya Aramagedo. Kodi lemba la Danieli 12:​2, limatanthauza chiyani likamati ena adzaukitsidwa kuti alandire “moyo wosatha”? Limatanthauza kuti pa nthawi ya zaka 1,000 anthu oukitsidwa omwe adzadziwe kapena kupitiriza kudziwa ndi kumvera Yehova ndi Yesu, adzapatsidwa moyo wosatha.—Yoh. 17:3. w22.09 21 ¶6-7

Lachinayi, November 14

[Chikondi] chimakhulupirira zinthu zonse.—1 Akor. 13:7.

Koma zimenezi sizikutanthauza kuti Yehova amayembekezera kuti tizikhulupirira ena popanda zifukwa zomveka. M’malomwake amafuna tiziwakhulupirira chifukwa choti asonyeza kuti ndi odalirika. Mofanana ndi kulemekeza ena, pamatenga nthawi kuti tiyambe kukhulupirira munthu. Ndiye kodi mungatani kuti muzikhulupirira abale anu? Muyenera kuwadziwa bwino. Muzilankhula nawo kumisonkhano ya mpingo, muzilowa nawo mu utumiki, muzileza nawo mtima komanso muziwapatsa mpata woti asonyeze kuti ndi odalirika. Mwina poyamba mungafunike kusankha nkhani zimene mungauze munthu amene mukumudziwa kumene. Mukayamba kudziwana kwambiri, mwina mungamasuke n’kuyamba kumufotokozera mmene mukumvera. (Luka 16:10) Koma kodi mungatani ngati m’bale wachita zinthu zosonyeza kuti si wodalirika? Musamafulumire kusiya kugwirizana naye. Musamalole kuti zochita za ena zikuchititseni kuti musamakhulupirire abale ndi alongo onse. w22.09 4 ¶7-8

Lachisanu, November 15

Maso a Yehova akuyendayenda padziko lonse lapansi.—2 Mbiri 16:9.

Mkulu wina dzina lake Miqueas pa nthawi ina ankaona kuti abale ena audindo amuchitira zinthu mopanda chifundo. Koma iye anapitirizabe kukhala woganiza bwino ndipo sanalole kusokonezedwa ndi mmene ankamvera. Ankapemphera pafupipafupi, kupempha Yehova kuti amupatse mzimu wake woyera ndiponso mphamvu kuti apirire. Anafufuzanso m’mabuku athu mfundo zomwe zikanamuthandiza. Kodi tikuphunzirapo chiyani? Ngati mukuona kuti m’bale kapena mlongo wina sanakuchitireni zinthu mwachilungamo, muzikhala odekha ndipo muziyesetsa kuchotsa maganizo olakwika aliwonse omwe mungakhale nawo. N’kutheka kuti simungadziwe zomwe zinamuchititsa kulankhula kapena kuchita zimene anachitazo. Choncho muzipemphera kwa Yehova, kumupempha kuti akuthandizeni kuti muziona zinthu mmene munthu winayo akuzionera. Muzichita zinthu zosonyeza kuti mukuona kuti m’bale kapena mlongo wanuyo sanali ndi cholinga choti akuchitireni zoipa ndipo muziyesetsa kunyalanyaza cholakwacho. (Miy. 19:11) Muzikumbukira kuti Yehova akudziwa zomwe zakuchitikirani ndipo adzakupatsani mphamvu zimene mukufunikira kuti mupirire.—Mlal. 5:8. w22.11 21 ¶5

Loweruka, November 16

Ndimapewa anthu amene amabisa umunthu wawo.—Sal. 26:4.

Muzisankha anzanu omwe amakonda Yehova. Kusankha anzanu abwino kungakuthandizeni kuti mukhale Mkhristu wolimba mwauzimu. (Miy. 13:20) Julien yemwe panopa ndi mkulu anati: “Ndili wamng’ono, ndinkapeza anzanga abwino ndikamagwira ntchito yolalikira. Anzangawa anali akhama, ndipo anandithandiza kuona kuti munthu angamasangalale ndi utumiki. . . . Ndinazindikiranso kuti ndinkataya mwayi wokhala ndi anzanga abwino chifukwa chongofuna kukhala ndi anzanga a msinkhu wanga okha.” Bwanji ngati mwazindikira kuti winawake mumpingo sangakhale munthu wabwino kucheza naye? Paulo ankadziwa kuti ena mumpingo wa Chikhristu woyambirira sankakonda zinthu zauzimu. Choncho anachenjeza Timoteyo kuti aziwapewa. (2 Tim. 2:​20-22) Timaona kuti ubwenzi wathu ndi Atate wathu Yehova ndi wamtengo wapatali. Choncho sitiyenera kulola kuti aliyense asokoneze ubwenziwu, umene takhala tikuyesetsa mwakhama kuti tikhale nawo. w22.08 5-6 ¶13-15

Lamlungu, November 17

Usayandikire munthu wopusa.—Miy. 14:7.

Mosiyana ndi anthu amene amadana ndi malamulo a Mulungu, ifeyo timakonda malamulo ake kuphatikizaponso mfundo zake za makhalidwe abwino. Tikhoza kumakonda kwambiri mfundozi tikayerekezera zotsatirapo za kumvera ndi kusamvera. Taganizirani mavuto osiyanasiyana, omwe anthu amadzibweretsera chifukwa chochita zinthu mopusa pokana malangizo anzeru a Yehova. Ndiyeno ganizirani mmene zinthu zikukuyenderani bwino pa moyo wanu chifukwa chakuti mumamvera Mulungu. (Sal. 32:​8, 10) Yehova amapereka malangizo anzeru kwa wina aliyense koma sakakamiza anthu kuti awatsatire. Komabe amafotokoza zimene zimachitikira anthu amene samvera malangizo ake anzeru. (Miy. 1:​29-32) Iwo adzakolola “zipatso za njira yawo.” N’kupita kwa nthawi zochita zawo zidzawabweretsera mavuto okhaokha ndipo pamapeto pake adzawonongedwa. Koma amene amamvetsera malangizo anzeru a Yehova komanso kuwagwiritsa ntchito, amalonjezedwa kuti: “Munthu wondimvera adzakhala motetezeka ndipo sadzasokonezeka chifukwa choopa tsoka.”—Miy. 1:33. w22.10 21 ¶11-13

Lolemba, November 18

Wosangalala ndi aliyense amene amaopa Yehova, Amene amayenda m’njira za Mulungu.—Sal. 128:1.

Kuopa Yehova kumatanthauza kumulemekeza kwambiri komanso kupewa kuchita chilichonse chomwe sichingamusangalatse. (Miy. 16:6) Choncho timayesetsa kuti tizitsatira mfundo za Mulungu zokhudza chabwino ndi choipa monga mmene Baibulo limafotokozera. (2 Akor. 7:1) Tidzakhala osangalala tikamachita zimene Yehova amakonda komanso kupewa zimene amadana nazo. (Sal. 37:27; 97:10; Aroma 12:9) Munthu angathe kudziwa kuti Yehova ali ndi mphamvu zonena kuti ichi n’chabwino kapena choipa koma ayeneranso kuvomereza mfundo za Mulungu payekha. (Aroma 12:2) Zochita zathu zimasonyeza ngati timavomereza kuti kutsatira mfundo za Yehova n’kothandiza kwambiri. (Miy. 12:28) Davide ankaonanso choncho chifukwa ponena za Yehova, iye anati: “Mumandidziwitsa njira ya moyo. Ndikakhala nanu pafupi, ndimasangalala kwambiri. Kudzanja lanu lamanja kuli chimwemwe mpaka kalekale.”—Sal. 16:11. w22.10 8 ¶9-10

Lachiwiri, November 19

Mwana sangachite chilichonse chimene wangoganiza payekha, koma chokhacho chimene waona Atate wake akuchita.—Yoh. 5:19.

Yesu anapitirizabe kudziona moyenera komanso kukhala wodzichepetsa. Asanabwere padzikoli, iye anachita zinthu zambiri potumikira Yehova. Kudzera mwa Yesu, “Mulungu analenga zinthu zina zonse kumwamba ndi padziko lapansi.” (Akol. 1:16) Pa nthawi imene ankabatizidwa, zikuoneka kuti Yesu anakumbukira zinthu zimene anakwanitsa kuchita ali limodzi ndi Atate wake. (Mat. 3:16; Yoh. 17:5) Koma zimenezi sizinamuchititse kuti ayambe kunyada. Ndipotu iye sanadzionepo ngati woposa ena. Anauza ophunzira ake kuti sanabwere padzikoli “kudzatumikiridwa, koma kudzatumikira ndi kudzapereka moyo wake dipo kuti awombole anthu ambiri.” (Mat. 20:28) Komanso modzichepetsa, Yesu anavomereza kuti sakanachita chilichonse mongoganiza payekha. Kumenekutu kunali kudzichepetsa kwakukulu. Apa iye anasonyeza chitsanzo chabwino kwambiri chimene tiyenera kutengera. w22.05 24 ¶13

Lachitatu, November 20

Abwerere kwa Yehova.—Yes. 55:7.

Akamasankha kuti akhululuke, Yehova amaganizira ngati munthu yemwe wachita tchimoyo amadziwa kuti zomwe akuchitazo ndi zolakwika. Yesu anafotokoza momveka bwino mfundo imeneyi pa Luka 12:​47, 48. Munthu yemwe amachita kukonzekera kuti achite zinthu zoipa koma akudziwa bwino kuti zomwe akufuna kuchitazo Yehova amadana nazo, amakhala kuti akuchita tchimo lalikulu. Munthu wotereyu amakhala pa chiopsezo choti sangakhululukidwe. (Maliko 3:29; Yoh. 9:41). Ndiye zikatere, kodi pakhoza kukhala chiyembekezo choti angakhululukidwe? Inde. Chinthu china chomwe Yehova amaganizira ndi kuona ngati munthu wochimwayo walapa mochokera pansi pa mtima. Kulapa kumatanthauza “kusintha maganizo, mmene timaonera zinthu komanso zolinga zathu.” Kumaphatikizapo kudzimvera chisoni kwambiri chifukwa cha zinthu zoipa zomwe tachita kapena chifukwa chosachita zinthu zoyenera. Sikuti munthu wolapa amangomva chisoni chifukwa cha zoipa zomwe wachita koma chifukwa cholepheranso kulimbitsa ubwenzi wake ndi Yehova zomwe zachititsa kuti achite tchimolo. w22.06 5-6 ¶15-17

Lachinayi, November 21

Onse ofuna kukhala ndi moyo wodzipereka kwa Mulungu mogwirizana ndi Khristu Yesu, nawonso adzazunzidwa.—2 Tim. 3:12.

Adani athu amafalitsa nkhani zabodza zokhudza abale omwe akutsogolera m’gulu la Yehova. (Sal. 31:13) Abale ena amangidwa komanso kuimbidwa milandu ngati zigawenga. Zimenezi ndi zomwe zinachitikiranso Akhristu oyambirira, pamene mtumwi Paulo anaimbidwa milandu yabodza komanso kumangidwa. Ena anasiya kuthandiza Paulo pamene anatsekeredwa m’ndende ku Roma. (2 Tim. 1:​8, 15; 2:​8, 9) Tangoganizani mmene Paulo anamvera. Iye anali atapirira mavuto ambiri ngakhalenso kuika moyo wake pangozi chifukwa cha iwo. (Mac. 20:​18-21; 2 Akor. 1:8) Tiyeni tisamakhale ngati anthu amene anamutaya Paulo. Tisamadabwe kuona kuti Satana amalimbana kwambiri ndi abale omwe akutsogolera. Cholinga chake n’kuwachititsa kuti asiye kukhala okhulupirika komanso kuti ifeyo tichite mantha. (1 Pet. 5:8) Muzipitiriza kuthandiza abale anu ndipo muzikhala okhulupirika kwa iwo.—2 Tim. 1:​16-18. w22.11 16-17 ¶8-11

Lachisanu, November 22

Kodi iwe sukuopa Mulungu?—Luka 23:40.

N’kutheka kuti wachifwamba amene anapachikidwa pambali pa Yesu anali Myuda. Ayuda ankalambira Mulungu mmodzi pomwe anthu a mitundu ina ankalambira milungu yambiri. (Eks. 20:​2, 3; 1 Akor. 8:​5, 6) Zikanakhala kuti wachifwambayu sanali Myuda, funso limene akanafunsa mogwirizana ndi mawu a mulemba laleroli likanakhala lakuti, “Kodi iwe sukuopa milungu?” Kuwonjezera pamenepo Yesu sanatumidwe kwa anthu a mitundu ina koma “kwa nkhosa zotayika za nyumba ya Isiraeli.” (Mat. 15:24) Mulungu anali atadziwitsa Aisiraeli kuti adzaukitsa anthu amene anamwalira. Wachifwambayu ayenera kuti ankadziwa zimenezi, ndipo mawu ake akusonyeza kuti ankayembekezera kuti Yehova adzaukitsa Yesu kuti alamulire mu Ufumu wa Mulungu. N’zoonekeratu kuti munthuyu nayenso ankakhulupirira kuti Mulungu adzamuukitsa. Monga Myuda, wachifwamba amene analapayu ayenera kuti ankadziwa zokhudza Adamu ndi Hava. Choncho iye ayenera kuti ankakhulupirira kuti Paradaiso yemwe Yesu anatchula pa Luka 23:​43, adzakhala munda wokongola padziko lapansi pompano.—Gen. 2:15. w22.12 8-9 ¶2-3

Loweruka, November 23

Mogwirizana, onsewa ankalimbikira kupemphera.—Mac. 1:14.

Tingathe kugwira ntchito yolalikirayi pokhapokha ngati tikuthandizidwa ndi mzimu wa Mulungu. Chifukwa chiyani? Chifukwa Satana ali pa nkhondo yolimbana nafe n’cholinga chofuna kutilepheretsa kugwira ntchito yolalikirayi. (Chiv. 12:17) N’kuona kwa anthu, zingaoneke ngati sitingapambane pa nkhondo yolimbana ndi Satanayi. Koma kudzera muntchitoyi, timamugonjetsa. (Chiv. 12:​9-11) Motani? Tikamagwira nawo ntchitoyi timasonyeza kuti sitimaopa njira zimene Satana amagwiritsa ntchito potiopseza. Nthawi iliyonse imene talalikira timakhala kuti tagonjetsa Satana. Choncho tinganene kuti mzimu woyera umatipatsa mphamvu ndipo Yehova amasangalala nafe. (Mat. 5:​10-12; 1 Pet. 4:14) Mzimu wa Mulungu ungatipatse mphamvu kuti tithe kulimbana ndi vuto lililonse lomwe tingakumane nalo pa utumiki wathu. (2 Akor. 4:​7-9) Ndiye kodi tingatani kuti nthawi zonse tizilandira mzimu wa Mulungu? Tiyenera kupemphera kwa Mulungu mosalekeza tili ndi chikhulupiriro kuti iye amva mapemphero athu. w22.11 5 ¶10-11

Lamlungu, November 24

Tikukulimbikitsani abale, kuti muzichenjeza anthu ochita zosalongosoka, muzilankhula molimbikitsa kwa anthu amene ali ndi nkhawa, muzithandiza ofooka, muzikhala oleza mtima kwa onse.—1 Ates. 5:14.

Timasonyeza kuti timakonda abale ndi alongo athu tikamayesetsa kukhala nawo mwamtendere. Timayesetsa kutengera chitsanzo cha Yehova pa nkhani yokhululukira ena. Ngati Yehova analolera kuti Mwana wake afe chifukwa cha machimo athu, kodi ifenso sitiyenera kukhala okonzeka kukhululukira abale ndi alongo athu akatilakwira? Sitingafune kukhala ngati kapolo woipa yemwe anatchulidwa m’fanizo lina la Yesu. Ngakhale kuti mbuye wake anamukhululukira ngongole yaikulu, iye analephera kukhululukira kapolo mnzake ngongole yaing’ono. (Mat. 18:​23-35) Ngati munasemphana maganizo ndi munthu wina mumpingo, kodi mungayambepo kukhazikitsa mtendere isanafike nthawi ya Chikumbutso? (Mat. 5:​23, 24) Kuchita zimenezo kungasonyeze kuti mumakonda kwambiri Yehova ndi Yesu. w23.01 29 ¶8-9

Lolemba, November 25

Amene amakomera mtima munthu wonyozeka akukongoza Yehova. —Miy. 19:17.

Njira imodzi imene mungadziwire zimene abale ndi alongo anu akufunikira ndi kuwafunsa mafunso mwanzeru. (Miy. 20:5) Kodi ali ndi chakudya chokwanira, mankhwala kapena zinthu zina zofunika? Kodi akhoza kuchotsedwa ntchito kapenanso kutulutsidwa m’nyumba imene akukhala? Kodi akufunika kuwathandiza mmene angapemphere thandizo ku boma? Yehova amatipempha kuti tonsefe tizilimbikitsa komanso kuthandiza ena. (Agal. 6:10) Ngakhale zochepa zomwe tingachite posonyeza chikondi kwa munthu yemwe akudwala, zingamulimbikitse kwambiri. Mwana akhoza kutumiza khadi kapena kujambula chithunzi pofuna kulimbikitsa m’bale. Wachinyamata angathandize pa ntchito zina kapena kukagulira zinthu mlongo. Tingathenso kukonzera chakudya munthu yemwe akudwala. A Mboni ena amatumiza kakhadi kothokoza kwa akulu omwe amakhala otanganidwa kwambiri pa nthawi ya mliri. Ndi bwinotu kuti tizichita mbali yathu popitiriza “kutonthozana ndi kulimbikitsana.”—1 Ates. 5:11. w22.12 22 ¶2; 23 ¶5, 6

Lachiwiri, November 26

Mukulakwitsa kwambiri anthu inu. —Maliko 12:27.

Asaduki ankadziwa bwino mabuku 5 oyambirira a Malemba a Chiheberi koma sankavomereza mfundo za choonadi zofunika za m’mabuku ouziridwawa. Mwachitsanzo, taganizirani mmene Yesu anayankhira Asaduki pamene anamufunsa nkhani yokhudza kuukitsidwa. Yesu anawafunsa kuti: “Kodi inu simunawerenge m’buku la Mose munkhani yokhudza chitsamba chaminga, kuti Mulungu anamuuza kuti: ‘Ine ndine Mulungu wa Abulahamu, Mulungu wa Isaki ndi Mulungu wa Yakobo’?” (Maliko 12:​18, 26) Ngakhale kuti Asaduki ayenera kuti anawerengapo nkhaniyi maulendo ambiri, funso la Yesu linasonyeza kuti iwo sankavomereza mfundo yofunika ya choonadi yonena za kuuka. (Luka 20:38) Kodi tikuphunzirapo chiyani? Tiziyesa kuona zimene tikuphunzira pa mbali zonse za vesi kapena nkhani imene tikuwerengayo. Sitikuyenera kumangoganizira mfundo zokhazo zomwe ndi zosavuta kumvetsa koma tiziganiziranso mfundo zozama za choonadi zomwe zili ngati chuma chobisika. w23.02 11 ¶9-10

Lachitatu, November 27

Tazunguliridwa ndi gulu lalikulu chonchi la mboni.—Aheb. 12:1.

A Mboni onse omwe akufotokozedwa mulemba lalerowa anakumana ndi mayesero akuluakulu, koma anakhalabe okhulupirika kwa Yehova. (Aheb. 11:​36-40) Ndiye kodi kupirira komanso khama lawo zinapita pachabe? Ayi ndithu. Ngakhale kuti munthawi yawo sanaone kukwaniritsidwa kwa malonjezo a Yehova, anapitirizabe kumuyembekezera. Ndipo popeza ankakhulupirira kuti Yehova akusangalala nawo, sankakayikira kuti adzaona malonjezowo akukwaniritsidwa. (Aheb. 11:​4, 5) Chitsanzo chawo chingatithandize kukhala otsimikiza kwambiri kuti tiziyembekezera Yehova. Panopa tikukhala m’dziko limene likuipiraipirabe. (2 Tim. 3:13) Satana sanasiye kuyesa anthu a Mulungu. Kaya tikumana ndi mavuto otani m’tsogolomu, tiyeni titsimikize mtima kuti tizichita khama potumikira Yehova, n’kumakhulupirira kuti “chiyembekezo chathu chili mwa Mulungu wamoyo.”—1 Tim. 4:10. w22.06 25 ¶17-18

Lachinayi, November 28

Kodi imfa yanga ili ndi phindu lanji? . . . Kodi fumbi lingakutamandeni? —Sal. 30:9.

Chifukwa chimodzi chomwe chimatichititsa kuti tizisamalira thanzi lathu, ndi chakuti timafuna kutumikira Yehova mmene tingathere. (Maliko 12:30) Choncho timapewa kuchita zinthu zimene tikudziwa kuti zingawononge thanzi lathu. (Aroma 12:1) N’zoona kuti ngakhale titayesetsa tikhoza kudwalabe, koma timachita zomwe tingathe kuti tikhale ndi thanzi labwino chifukwa timafuna kusonyeza Atate wathu wakumwamba kuti timayamikira mphatso yamoyo. Matenda komanso ukalamba zingatilepheretse kuchita zambiri ngati mmene tinkachitira poyamba. Zikatere tingafooke ndiponso kukhumudwa. Komabe sitiyenera kunyalanyaza nkhani yosamalira thanzi lathu. N’chifukwa chiyani tikutero? Chifukwa kaya takalamba kwambiri kapena tadwala chotani, tingathe kutamandabe Yehova ngati mmene inachitira Mfumu Davide. N’zolimbikitsatu kwambiri kudziwa kuti Mulungu wathu amationa kuti ndife amtengo wapatali kaya tikudwala kapena takalamba. (Mat. 10:​29-31) Ngakhale titamwalira, iye amafunitsitsa kutiukitsa. (Yobu 14:​14, 15) Panopo pamene tili ndi moyo timafuna kuchita zonse zomwe tingathe pousamalira. w23.02 20-21 ¶3-5

Lachisanu, November 29

Aliyense amene wanyoza mzimu woyera sadzakhululukidwa kwamuyaya.—Maliko 3:29.

Kodi mayina a khamu lalikulu adzapitiriza kukhala m’bukuli akadzapulumuka pa Aramagedo? Inde. (Chiv. 7:14) Yesu ananena kuti anthu amenewa, omwe ali ngati nkhosa, adzapita “ku moyo wosatha.” (Mat. 25:46) Koma anthu omwe adzapulumuke pa Aramagedowa, sadzalandira nthawi yomweyo moyo wosathawo. Mu Ulamuliro wa Zaka 1,000, Yesu “adzawaweta n’kuwatsogolera ku akasupe a madzi a moyo.” Anthu omwe adzalole kutsogoleredwa ndi Khristu, ndipo pamapeto pake n’kuweruzidwa kuti ndi okhulupirika kwa Yehova, mayina awo sadzafufutidwanso m’buku la moyo. (Chiv. 7:​16, 17) Komabe anthu omwe ali ngati mbuzi adzawonongedwa pa Aramagedo. Yesu ananena kuti iwo ‘adzapita ku chiwonongeko chosatha.’ (Mat. 25:46) Mouziridwa, mtumwi Paulo ananena kuti anthu amenewa “adzawaweruza kuti alandire chilango cha chiwonongeko chamuyaya.”—2 Ates. 1:9; 2 Pet. 2:9. w22.09 16 ¶7-8

Loweruka, November 30

Chilichonse chili ndi nthawi yake. —Mlal. 3:1.

Kuona zimene Yehova analenga kungathandize mabanja kupeza nthawi yopuma komanso yosangalala, zomwe zingachititse kuti onse m’banja azigwirizana kwambiri. Yehova anapanga malo ambiri okongola omwe tingakasangalaleko. Mabanja ambiri amakonda kupita kumalo osungirako zachilengedwe, madera a kumidzi, kumapiri kapenanso kunyanja. M’dziko latsopano la Mulungu, makolo ndi ana adzasangalala ndi chilengedwe cha Yehova kuposa kale lonse. Mosiyana ndi masiku ano, sitizidzaopa nyama ndipo nyamazo sizidzaopa anthu. (Yes. 11:​6-9) Tidzasangalala ndi zimene Yehova analenga mpaka kalekale. (Sal. 22:26) Koma makolo, musachite kudikira mpaka nthawi imeneyo kuti mudzathandize ana anu kuyamba kusangalala ndi chilengedwe. Mukamagwiritsa ntchito chilengedwe pophunzitsa ana anu zokhudza Yehova, mosakayikira iwo adzavomereza zimene Mfumu Davide inanena, kuti: “Inu Yehova, . . . palibe aliyense amene wachita zinthu zofanana ndi zimene inu mwachita.”—Sal. 86:8. w23.03 25 ¶16-17

    Mabuku a Chichewa (1974-2026)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena