December
Lamlungu, December 1
Chikundiletsa kubatizidwa n’chiyani?—Mac. 8:36.
Kodi nduna ya ku Itiyopiya inali yokonzeka kubatizidwa? Taganizirani izi: Munthu wa ku Itiyopiyayu “anapita ku Yerusalemu kukalambira Mulungu.” (Mac. 8:27) Choncho iye ayenera kuti anali wotembenukira ku Chiyuda. Mosakayikira, iye anaphunzira zokhudza Yehova kuchokera m’Malemba opatulika a Chiheberi. Komabe anali wofunitsitsa kuphunzira zambiri. Pamene Filipo anakumana naye panjira, anamupeza akuwerenga mpukutu wa mneneri Yesaya. (Mac. 8:28) Ndunayi inkafuna kupitiriza kuphunzira. Inayenda mtunda wautali kuchoka ku Itiyopiya kuti ikalambire Yehova kukachisi ku Yerusalemu. Munthu wa ku Itiyopiyayu anaphunzira mfundo za choonadi zatsopano kuchokera kwa Filipo, kuphatikizapo zoti Yesu ndi Mesiya. (Mac. 8:34, 35) Iye anayamba kukonda kwambiri Yehova ndi Mwana wake. Chikondichi chinamuchititsa kusankha chinthu chofunika kwambiri pa moyo chomwe ndi kubatizidwa n’kukhala wotsatira wa Yesu Khristu. Filipo ataona kuti munthuyu anali wokonzeka, anamubatiza. w23.03 8-9 ¶3-6
Lolemba, December 2
Nthawi zonse mawu anu azisonyeza kuti ndinu okoma mtima.—Akol. 4:6.
Yehova sangasangalale nafe ngati sitilankhula zoona. (Miy. 6:16, 17) Ngakhale kuti anthu ambiri masiku ano amaona kuti palibe vuto kunama, ife timayesetsa kuti tiziona nkhaniyi mmene Yehova amaionera. (Sal. 15:1, 2) N’zoona kuti timapewa kulankhula mabodza ochita kuonekeratu, koma timapewanso kuchititsa anthu mwadala kuti aziona zinthu molakwika. Muzipewanso miseche. (Miy. 25:23; 2 Ates. 3:11) Mukaona kuti munthu wina wayamba kulankhula miseche, muziyesetsa kusintha nkhaniyo. Popeza kuti tikukhala m’dziko limene anthu ambiri amalankhula mawu oipa, tiyenera kuyesetsa kuti zolankhula zathu zizisangalatsa Yehova. Iye adzatidalitsa tikamayesetsa kugwiritsa ntchito bwino luso lolankhula mu utumiki, pamisonkhano komanso pocheza ndi ena. Yehova akadzawononga dziko loipali, zidzakhala zosavuta kumamulemekeza ndi zolankhula zathu.—Yuda 15. w22.04 9 ¶18-20
Lachiwiri, December 3
Timasonyeza chikondi, chifukwa Mulungu ndi amene anayamba kutikonda.—1 Yoh. 4:19.
Tikaganizira mmene Yehova ndi Yesu anatisonyezera chikondi, timafunitsitsa kuti ifenso tiziwakonda. (1 Yoh. 4:10) Timawakonda kwambiri tikazindikira kuti Yesu anatifera ifeyo aliyense payekha. Mtumwi Paulo ankadziwa mfundo imeneyi ndipo anasonyeza kuyamikira kwake pomwe analembera Akhristu a ku Galatiya kuti: “Mwana wa Mulungu . . . anandikonda n’kudzipereka yekha chifukwa cha ine.” (Agal. 2:20) Pogwiritsa ntchito dipo, Yehova anatikokera kwa iye kuti tikhale anzake. (Yoh. 6:44) Kodi simumasangalala kudziwa kuti Yehova anaona kanthu kenakake kabwino mwa inu ndiponso kuti anapereka mtengo wokwera n’cholinga choti mukhale mnzake? Kodi izi sizikuchititsani kuti muzikonda kwambiri Yehova ndi Yesu? Mungachite bwino kumadzifunsa kuti, ‘Kodi chikondi chimenechi chizindilimbikitsa kuchita chiyani?’ Kukonda Mulungu ndi Khristu kumatichititsa kuti tizikondanso ena.—2 Akor. 5:14, 15; 6:1, 2. w23.01 28 ¶6-7
Lachitatu, December 4
Ndidzasintha chilankhulo cha anthu kuti chikhale chilankhulo choyera. —Zef. 3:9.
Baibulo ndi lofunika kwambiri pokwaniritsa cholinga cha Yehova choti atumiki ake ‘azimutumikira mogwirizana.’ Malemba ambiri analembedwa m’njira yakuti anthu odzichepetsa okha ndi omwe amatha kuwamvetsa mosavuta. (Luka 10:21) Kulikonse anthu amawerenga Baibulo. Komatu ndi odzichepetsa okha omwe amamvetsa komanso kutsatira zimene limanena. (2 Akor. 3:15, 16) Baibulo limatithandiza kuona nzeru za Yehova. Iye amagwiritsa ntchito Malemba pophunzitsa anthu ake onse monga gulu. Koma amaphunzitsanso ndi kulimbikitsa aliyense payekha. Tikamawerenga Mawu ake timaona kuti Yehova amachita chidwi ndi aliyense payekha. (Yes. 30:21) N’kutheka kuti kangapo munawerengapo mavesi omwe ankangooneka ngati alembedwera inuyo. Komatu Baibulo limathandiza anthu ambiri. Kodi zinatheka bwanji kuti likhale ndi mfundo zomwe zikugwirizana ndi zomwe inuyo mukufunikira? Zili choncho chifukwa Baibulo linalembedwa ndi Mlengi wanzeru kwambiri m’chilengedwe chonse.—2 Tim. 3:16, 17. w23.02 4-5 ¶8-10
Lachinayi, December 5
Uziganizira mozama zinthu zimenezi ndipo uzizichita modzipereka kuti anthu onse aone kuti ukupita patsogolo.—1 Tim. 4:15.
Monga Akhristu oona, timakonda kwambiri Yehova. Timafunitsitsa kuti tizichita zonse zomwe tingathe pomutumikira. Kuti zimenezi zitheke timafunika kudziikira zolinga zauzimu monga kukhala ndi makhalidwe abwino, kuphunzira maluso othandiza komanso kupeza njira zimene tingathandizire ena. N’chifukwa chiyani tiyenera kuyesetsa kupita patsogolo mwauzimu? Chifukwa chachikulu n’chakuti timafuna kusangalatsa Atate wathu wakumwamba. Yehova amasangalala akationa tikugwiritsa ntchito luso lathu mmene tingathere pomutumikira. Kuwonjezera pamenepo timafuna kupita patsogolo mwauzimu kuti tizithandiza kwambiri abale ndi alongo athu. (1 Ates. 4:9, 10) Kaya takhala m’choonadi kwa nthawi yayitali bwanji, tonsefe tingathe kupita patsogolo mwauzimu. w22.04 22 ¶1-2
Lachisanu, December 6
Zidzadya minofu yake n’kulipsereza ndi moto.—Chiv. 17:16.
Posachedwapa maboma a m’dzikoli adzaukira Babulo Wamkulu, yemwe akuimira zipembedzo zonse zonyenga. Ichi chidzakhala chiyambi cha chisautso chachikulu. Kodi zimenezi zidzachititsa kuti anthu ambiri ayambe kulambira Yehova? Ayi. M’malomwake, Chivumbulutso chaputala 6 chimasonyeza kuti pa nthawi yovutayi, anthu omwe satumikira Yehova adzafunafuna chitetezo kwa andale komanso amalonda a m’dzikoli omwe amayerekezeredwa ndi mapiri. Chifukwa choti iwo sadzakhala kumbali ya Ufumu wa Mulungu, Yehova adzawaona kuti ndi otsutsa. (Luka 11:23; Chiv. 6:15-17) Kunena zoona, atumiki a Yehova adzachita zinthu mosiyana kwambiri ndi ena pa nthawi yovuta ya chisautso chachikulu. Iwo adzakhala gulu lokhalo lomwe lizidzatumikira Mulungu padzikoli ndipo azidzakana kukhala kumbali ya “chilombo.”—Chiv. 13:14-17. w22.05 16-17 ¶8-9
Loweruka, December 7
Iye anali ndi uthenga wabwino wosatha woti aulengeze kwa anthu amene akukhala padziko lapansi, kudziko lililonse, fuko lililonse, chilankhulo chilichonse ndi mtundu uliwonse.—Chiv. 14:6.
‘Uthenga wabwino wa Ufumu,’ si uthenga wokhawo womwe anthu a Mulungu ayenera kulengeza. (Mat. 24:14) Iwo amafunikanso kuthandiza pa ntchito ya angelo otchulidwa pa Chivumbulutso 8 mpaka 10. Angelowa amalengeza zinthu zoopsa zomwe zidzachitikire anthu amene amakana Ufumu wa Mulungu. N’chifukwa chake a Mboni za Yehova akhala akulengeza uthenga wachiweruzo womwe uli ngati “matalala ndi moto” wosonyeza ziweruzo zomwe Mulungu adzapereke ku mbali zosiyanasiyana za dziko la Satanali. (Chiv. 8:7, 13) Anthu akufunika kudziwa kuti mapeto ali pafupi n’cholinga choti asinthe moyo wawo n’kudzapulumuka pa tsiku la mkwiyo wa Yehova. (Zef. 2:2, 3) Koma anthu ambiri sasangalala ndi uthengawu moti pamafunika kulimba mtima kuti tiulengeze. Ndipotu pachisautso chachikulu, anthu adzakwiya kwambiri ndi uthenga womaliza wachiweruzo womwe tidzalengeze.—Chiv. 16:21. w22.05 7 ¶18-19
Lamlungu, December 8
Muzikonda Yehova Mulungu wanu ndi mtima wanu wonse, moyo wanu wonse ndi maganizo anu onse. —Mat. 22:37.
Taganizirani za Akhristu okwatirana omwe atsala pang’ono kukhala ndi mwana. N’kutheka kuti kwa zaka zambiri, iwo amakhala akumvetsera nkhani zokhala ndi malangizo okhudza kulera ana. Koma tsopano pa nthawiyi amafunikira kwambiri malangizo amenewa. Amakhala kuti akhala ndi mwana wawowawo woti amulere. Umenewutu ndi udindo waukulu. Kunena zoona, kusintha kwa zinthu pa moyo wathu kungachititse kuti tisinthe mmene timaonera mfundo za m’Baibulo zodziwika bwino. Chimenechi ndi chimodzi mwa zifukwa zimene atumiki a Yehova amawerengera komanso kuganizira mozama Malemba “masiku onse” a moyo wawo, monga mmene mafumu a Isiraeli anauzidwira. (Deut. 17:19) Makolo, muli ndi mwayi waukulu womwe Mkhristu angakhale nawo wophunzitsa ana anu zokhudza Yehova. Koma pali zambiri zimene muyenera kuchita kuposa pa kungowathandiza kudziwa zokhudza Mulungu wathu. Mumafunika kuwathandiza kuti azimukonda kwambiri. w22.05 26 ¶2-3
Lolemba, December 9
Muvale umunthu watsopano. —Akol. 3:10.
Kungodzimvera chisoni pa machimo athu sikokwanira, koma tiyeneranso kukhala okonzeka kuchitapo kathu. Chinthu chofunika kwambiri chomwe Yehova amachiganizira kuti akhululukire munthu, ndi kutembenuka. M’mawu ena, munthu ayenera kusiya zoipa zomwe amachita, n’kuyamba kuchita zimene Yehova amafuna. (Yes. 55:7) Munthuyo ayenera kusintha mmene amaganizira n’cholinga choti azitsogoleredwa ndi maganizo a Yehova. (Aroma 12:2; Aef. 4:23) Ayenera kukhala wotsimikiza mtima kuti asiye zinthu zoipa zomwe ankaziganizira komanso kuchita. (Akol. 3:7-9) Komanso tiyenera kukhulupirira nsembe ya Khristu kuti Yehova atikhululukire ndiponso kutiyeretsa ku machimo athu. Yehova angatikhululukire pogwiritsa ntchito nsembeyi ngati waona kuti tikuyesetsa kusintha moyo wathu.—1 Yoh. 1:7. w22.06 6 ¶16-17
Lachiwiri, December 10
Usachite mantha ndi mavuto amene ukumane nawo.—Chiv. 2:10.
Kuyambira kale anthu akhala akuchitira anzawo zoipa. (Mlal. 8:9) Mwachitsanzo, anthu amagwiritsa ntchito molakwika udindo wawo, ophwanya malamulo amachita zachiwawa, ana asukulu amanyoza kapena kuopseza anzawo ndipo anthu ena amachitira nkhanza ngakhale anthu a m’banja lawo. Mpake kuti anthu amaopa anthu anzawo. Ndiye kodi Satana amapezerapo mwayi wotani? Satana amagwiritsa ntchito kuopa anthu pofuna kutisiyitsa kuchita zomwe Yehova amafuna komanso kulalikira. (Luka 21:12) Mbali zosiyanasiyana za dziko la Satanali zimafalitsa mabodza oipa kwambiri okhudza Mboni za Yehova. Anthu amene amakhulupirira mabodzawa angamatinyoze ngakhalenso kutiukira. (Mat. 10:36) Koma kodi zimene Satana amachitazi ziyenera kutidabwitsa? Ayi. Iye ankachitanso zimenezi m’nthawi ya atumwi.—Mac. 5:27, 28, 40. w22.06 16 ¶10-11
Lachitatu, December 11
Amene akuthandiza anthu ambiri kuti akhale olungama adzawala ngati nyenyezi mpaka muyaya.—Dan. 12:3.
Kodi ndi enanso ati omwe ali m’gulu la “anthu ambiri” omwe adzathandizidwe kukhala olungama? Anthu amenewa akuphatikizapo omwe adzaukitsidwe, amene adzapulumuke pa Aramagedo komanso ana onse omwe angadzabadwe m’dziko latsopano. Pofika kumapeto kwa zaka 1,000, anthu onse adzakhala angwiro. Tiyenera kukumbukira kuti kukhala wangwiro sikutanthauza kuti basi munthu adzalandira moyo wosatha. Taganizirani zimene zinachitikira Adamu ndi Hava. Iwo anali angwiro, koma ankafunika kupitirizabe kumvera Yehova Mulungu kuti apatsidwe moyo wosatha. N’zomvetsa chisoni kuti analephera kumumvera. (Aroma 5:12) Popeza kuti onse adzakhala angwiro pofika kumapeto kwa zaka 1,000, kodi iwo adzakhala kumbali ya ulamuliro wa Yehova mpaka kalekale? Kapena kodi ena adzakhala ngati Adamu ndi Hava omwe sanamvere Mulungu ngakhale kuti anali angwiro? Padzafunika kupeza mayankho a mafunso amenewa. w22.09 22-23 ¶12-14
Lachinayi, December 12
Ufumu wa dziko wakhala Ufumu wa Ambuye wathu ndi wa Khristu wake.—Chiv. 11:15.
Mukaganizira mmene zinthu zilili m’dzikoli, kodi mumakayikira kuti zinthu zidzakhala bwino? Anthu m’mabanja ambiri sakukondananso, ndipo anthu achiwawa, odzikonda komanso ankhanza ali pena paliponse. Ambirinso zimawavuta kukhulupirira anthu audindo. Komatu zochitika zimenezi zingakulimbikitseni. N’chifukwa chiyani tikutero? Chifukwa anthu akuchita ndendende zimene zinatchulidwa mu ulosi wochititsa chidwi wokhudza “masiku otsiriza.” (2 Tim. 3:1-5) Kukwaniritsidwa kwa ulosiwu, womwe anthu oona mtima sangatsutse kuti ukukwaniritsidwa, kumapereka umboni woti Khristu Yesu anayamba kulamulira monga Mfumu ya Ufumu wa Mulungu. Komatu palinso maulosi ena ambiri onena za Ufumuwu. Maulosiwa ali ngati zidutswa za chithunzi zomwe zikaikidwa pamodzi chithunzicho chimaoneka bwinobwino ndipo amatithandizanso kuona pomwe tili munthawi ya Yehova ya zochitika zosiyanasiyana. w22.07 2 ¶1-2
Lachisanu, December 13
Nzeru imatsimikizirika kuti ndi yolungama chifukwa cha ntchito zake.—Mat. 11:19.
Pa nthawi ya mliriyi wa COVID-19 tinalandira malangizo a mmene tingachitire misonkhano komanso kugwira ntchito yolalikira. Mofulumira kwambiri tinayamba kuchita misonkhano yampingo, yadera komanso yachigawo kudzera pa vidiyokonferensi. Tinayambanso kulalikira pongogwiritsa ntchito foni komanso kulemba makalata. Yehova anadalitsa khama lathu. Malipoti a maofesi anthambi ambiri akusonyeza kuti chiwerengero cha ofalitsa chakwera. Ndipotu abale ndi alongo ambiri akumana ndi zosangalatsa pa nthawiyi. Anthu ena akhoza kumaona ngati gulu linkakhwimitsa zinthu kwambiri pa nthawi ya mliriwu. Koma nthawi zonse zinkachita kuonekeratu kuti malangizo omwe tinkapatsidwa anali anzeru. Ndipo tikamaganizira mmene Yesu wakhala akutsogolera anthu ake mwachikondi, timakhala otsimikiza kuti kaya tikumana ndi zotani m’tsogolomu, Yehova ndi Mwana wake wokondedwa sadzatisiya.—Aheb. 13:5, 6. w22.07 13 ¶15-16
Loweruka, December 14
Muzipemphera nthawi zonse. Muzithokoza pa chilichonse. Mulungu akufuna kuti muzichita zimenezi chifukwa ndinu otsatira a Khristu.—1 Ates. 5:17, 18.
Kuwonjezera pa kumutamanda m’mapemphero athu, tiyeneranso kumathokoza Yehova chifukwa cha zinthu zabwino zimene amatipatsa komanso chifukwa chokhala ndi anzathu ambiri abwino. Atate wathu wachikondi amatipatsa zimenezi ndi zinanso zambiri chifukwa amafuna tizisangalala. (Sal. 104:12-15, 24) Koposa zonse, timathokoza Yehova chifukwa chotipatsa chakudya chauzimu chochuluka komanso chiyembekezo chosangalatsa cha m’tsogolo. Zingakhale zosavuta kuiwala kuthokoza Yehova pa zonse zimene amatichitira. Ndiye n’chiyani chingatithandize? Tingalembe zinthu zosiyanasiyana zomwe tamupempha n’kumaona nthawi ndi nthawi mmene wayankhira mapemphero athuwo. Kenako tizipemphera n’kumuthokoza chifukwa chotithandiza.—Akol. 3:15. w22.07 22 ¶8-9
Lamlungu, December 15
Amakonda kwambiri chilamulo cha Yehova, ndipo amawerenga ndi kuganizira mozama chilamulocho masana ndi usiku.—Sal. 1:2.
Timadziwa kuti kungophunzira choonadi si kokwanira. Kuti tipindule mokwanira, tiyenera kumachita zinthu mogwirizana ndi choonadicho, kapena kuti kugwiritsa ntchito mfundo zake pa moyo wathu. Tikamachita zimenezo m’pamene timapeza chimwemwe chenicheni. (Yak. 1:25) Kodi tingadziwe bwanji kuti timachita zinthu mogwirizana ndi choonadi? M’bale wina anafotokoza kuti tingachite zimenezo podzifufuza n’kuona mbali zimene tikuchita bwino komanso zimene tiyenera kusintha. Mtumwi Paulo anafotokoza mfundoyi motere: “Mulimonse mmene tapitira patsogolo, tiyeni tipitirize kupita patsogolo pochita zomwe tikuchitazo.” (Afil. 3:16) Tangoganizirani madalitso omwe timapeza chifukwa choyesetsa kuti ‘tipitirize kuyendabe m’choonadi.’ Sikuti choonadi chimangotithandiza kukhala ndi moyo wabwino koma chimatithandizanso kuti tizisangalatsa Yehova ndi Akhristu anzathu. (Miy. 27:11; 3 Yoh. 4) Kunena zoona, zimenezi ndi zifukwa zabwino zotichititsa kuti tizikonda choonadi komanso kumachita zinthu mogwirizana ndi choonadicho. w22.08 18-19 ¶16-18
Lolemba, December 16
Wetani gulu la nkhosa za Mulungu.—1 Pet. 5:2.
Kodi akulu angasonyeze bwanji kuti amakonda Yehova ndi Yesu? Njira yofunika kwambiri yomwe angachitire zimenezi ndi kusamalira nkhosa za Yesu. (1 Pet. 5:1, 2) Yesu anasonyeza bwino mfundo imeneyi pamene ankalankhula ndi mtumwi Petulo. Pambuyo pokana Yesu maulendo atatu, Petulo ayenera kuti ankafunitsitsa kuti asonyeze Yesu kuti amamukonda. Ataukitsidwa, Yesu anafunsa Petulo kuti: “Simoni mwana wa Yohane, kodi ine umandikonda?” Sitikukayikira kuti Petulo akanachita chilichonse pofuna kusonyeza kuti amakonda Mbuye wake. Yesu anauza Petulo kuti: “Weta ana a nkhosa anga.” (Yoh. 21:15-17) Kwa moyo wake wonse Petulo ankasamalira mwachikondi nkhosa za Ambuye posonyeza kuti amakonda Yesu. Akulu, kodi mungasonyeze bwanji kuti mawu amene Yesu anauza Petulo ndi ofunikanso kwa inu? Mungasonyeze kuti mumakonda Yehova ndi Yesu poyesetsa kuti nthawi zonse muzipeza nthawi yolimbikitsa abale ndi alongo, komanso pochita khama kuthandiza amene anafooka kuti abwerere kwa Yehova.—Ezek. 34:11, 12. w23.01 29 ¶10-11
Lachiwiri, December 17
Mulungu ndi wokhulupirika ndipo sadzalola kuti muyesedwe kufika pamene simungapirire. —1 Akor. 10:13.
Muzipewa msampha woganiza kuti palibe amene angamvetse vuto linalake lomwe mukulimbana nalo. Maganizo amenewa angakuchititseni kutaya mtima n’kumaona kuti simungathenso kulimbana ndi zilakolako zoipa. Koma Baibulo limapereka malangizo akuti: “Pamene mukukumana ndi mayeserowo iye adzapereka njira yopulumukira kuti muthe kuwapirira.” Choncho ngakhale kuti timalimbana ndi chilakolako chinachake choipa, tingathe kupirira. Mothandizidwa ndi Yehova, tingathe kupewa kutsatira chilakolakocho. Nthawi zonse muzikumbukira kuti: Popeza si inu angwiro, simungapeweretu kulakalaka zoipa. Koma mukayamba kulakalaka zinthu zoipa, muzichotsa mwamsanga maganizo amenewo ngati mmene Yosefe anachitira zinthu mofulumira pothawa mkazi wa Potifara. (Gen. 39:12) Simuyenera kuchita zoipa zomwe mukulakalakazo. w23.01 12-13 ¶16-17
Lachitatu, December 18
Mulungu alibe tsankho.—Aroma 2:11.
Chilungamo ndi khalidwe la Yehova. (Deut. 32:4) Chilungamo chimayendera limodzi ndi kupanda tsankho ndipo Yehova ndi wopanda tsankho. (Mac. 10:34, 35) Zimenezi zinaonekera bwino pomwe analola kuti Baibulo lilembedwe m’zilankhulo zosiyanasiyana. Yehova analonjeza kuti m’nthawi ya mapeto, anthu “adzadziwa zinthu zambiri zoona” zopezeka m’Baibulo ndipo ambiri adzazimvetsa. (Dan. 12:4) Chinthu chimodzi chimene chathandiza kuti anthu alimvetse ndi chakuti Baibulo komanso mabuku ofotokoza Baibulo zamasuliridwa, kufalitsidwa komanso kugawidwa kwa anthu ambiri. Pofika pano, anthu a Yehova amasulira Baibulo lathunthu kapena mbali yake m’zilankhulo zoposa 240, ndipo aliyense akhoza kulipeza kwaulere. Zimenezi zikuthandiza kuti anthu a mitundu yonse amve ‘uthenga wabwino wa Ufumu’ mapeto asanafike. (Mat. 24:14) Mulungu wathu wachilungamo amafuna kuti anthu ambiri akhale ndi mwayi womudziwa powerenga Mawu ake. Izi zili choncho chifukwa chakuti iye amatikonda kwambiri tonsefe. w23.02 5 ¶11-12
Lachinayi, December 19
Musamatengere nzeru za nthawi ino, koma khalani munthu watsopano posintha kwambiri maganizo anu. —Aroma 12:2.
Kodi mumakonda chilungamo? N’zosachita kufunsa. Komabe tonsefe si angwiro ndipo ngati sitingasamale, tingasokonezedwe ndi mmene dzikoli limaonera nkhani ya chilungamo. (Yes. 5:20) Anthu ambiri amaganiza kuti munthu wolungama ndi munthu amene ndi wonyada, wokonda kuweruza ena kapenanso amene amadziona kuti ndi wabwino kuposa ena. Komatu Mulungu sasangalala ndi makhalidwe amenewa ngakhale pang’ono. Yesu ali padzikoli anadzudzula mwamphamvu atsogoleri achipembedzo a mu nthawi yake, chifukwa chokhazikitsa mfundo zawozawo pa nkhani ya chilungamo. (Mlal. 7:16; Luka 16:15) Munthu wachilungamo samaganiza kuti ndi wabwino kuposa ena. Chilungamo ndi khalidwe labwino kwambiri. Mwachidule, chilungamo chimatanthauza kuchita zimene Yehova amaona kuti n’zoyenera. M’Baibulo, mawu akuti “chilungamo” amanena za kutsatira mfundo za Yehova, zomwe ndi zapamwamba kwambiri. w22.08 27 ¶3-5
Lachisanu, December 20
Ndakutchulani kuti anzanga.—Yoh 15:15.
Yesu ankakhulupirira ophunzira ake ngakhale kuti iwo ankalakwitsa zinthu zina. (Yoh. 15:16) Yakobo ndi Yohane atamupempha malo apadera mu Ufumu, Yesu sanakayikire zolinga zawo potumikira Yehova kapena kuwakana kuti asakhalenso atumwi ake. (Maliko 10:35-40) Patapita nthawi, ophunzira ake onse anamuthawa pa usiku umene anagwidwa. (Mat. 26:56) Komabe Yesu sanasiye kuwakhulupirira. Iye ankadziwa bwino zofooka zawo, komabe “anawakonda mpaka pamapeto a moyo wake.” (Yoh. 13:1) Ataukitsidwa, Yesu anapatsa atumwi ake 11 okhulupirika udindo wofunika kwambiri wotsogolera pa ntchito yophunzitsa anthu komanso kusamalira nkhosa zake za mtengo wapatali. (Mat. 28:19, 20; Yoh. 21:15-17) Iyetu sanalakwitse pokhulupirira anthu omwe sanali angwirowa. Iwo anapitirizabe kukhala okhulupirika mpaka pamapeto a moyo wawo wapadzikoli. Choncho Yesu ndi chitsanzo chabwino kwambiri pa nkhani yokhulupirira anthu omwe si angwiro. w22.09 6 ¶12
Loweruka, December 21
Yehova ali kumbali yanga, sindidzaopa.—Sal. 118:6.
Tikamakhulupirira kuti Yehova amatikonda ndipo ali kumbali yathu, sitingamaope Satana. Mwachitsanzo, amene analemba Salimo 118 anakumana ndi zinthu zina zodetsa nkhawa. Anali ndi adani ambiri ndipo ena anali a maudindo akuluakulu (vesi 9, 10). Nthawi zina ankapanikizidwa kwambiri (vesi 13). Komanso anapatsidwa uphungu wamphamvu ndi Yehova (vesi 18). Ngakhale zinali choncho, wolemba salimoyu anaimba kuti: “Sindidzaopa.” Kodi n’chiyani chinkamuchititsa kuona kuti ndi wotetezeka? Iye ankadziwa kuti ngakhale kuti Yehova anam’patsa uphungu wamphamvu, Atate wake akumwambawa ankamukonda. Wolemba salimoyu ankakhulupirira kuti kaya akumana ndi zotani, Mulungu wake wachikondiyu anali wokonzeka kumuthandiza. (Sal. 118:29) Tizikhulupirira kuti Yehova amatikonda ifeyo patokha. Zimenezi zidzatithandiza kuthetsa mantha pa zinthu zitatu zimene anthu ambiri amaziopa, zomwe ndi (1) kuopa kuti sakwanitsa kupezera banja lawo zinthu zofunika, (2) kuopa anthu komanso (3) kuopa imfa. w22.06 15 ¶3-4
Lamlungu, December 22
Wosangalala ndi munthu amene akupirira mayesero, chifukwa akadzavomerezedwa, adzalandira mphoto ya moyo.—Yak. 1:12.
Tizionetsetsa kuti kulambira Yehova kuzikhala pamalo oyamba pa moyo wathu. Monga Mlengi wathu, Yehova ndi woyenera kuti tizimulambira. (Chiv. 4:11; 14:6, 7) Choncho tizionetsetsa kuti chinthu chofunika kwambiri chizikhala kumulambira m’njira imene iye amaivomereza, yomwe ndi kumulambira “motsogoleredwa ndi mzimu komanso choonadi.” (Yoh. 4:23, 24) Timafuna kuti mzimu wake uzititsogolera pomulambira n’cholinga choti tizichita zinthu mogwirizana ndi mfundo za choonadi zopezeka m’Mawu ake. Kulambira kwathu kuyenera kukhala pamalo oyamba ngakhale zitakhala kuti tili m’dziko limene ntchito yathu ndi yoletsedwa. Panopa abale ndi alongo athu oposa 100 ali m’ndende, chabe chifukwa chokhala a Mboni za Yehova. Ngakhale zili choncho, iwo amasangalala kuchita zonse zomwe angathe kuti azipemphera, kuphunzira komanso kuuza ena zokhudza Mulungu ndi Ufumu wake. Tikamanyozedwa kapena kuzunzidwa, tingakhalebe osangalala podziwa kuti Yehova ali nafe ndipo adzatipatsa mphoto.—1 Pet. 4:14. w22.10 9 ¶13
Lolemba, December 23
Nzeru zimateteza.—Mlal. 7:12.
M’buku lonse la Miyambo, Yehova amatipatsa malangizo othandiza omwe tingawagwiritse ntchito nthawi ina iliyonse. Taonani zitsanzo ziwiri za malangizo anzeruwa. Choyamba, tizikhutira ndi zimene tili nazo. Lemba la Miyambo 23:4, 5 limapereka malangizo awa: “Usadzitopetse pofuna kupeza chuma. . . . Chifukwa ndithu chimamera mapiko ngati chiwombankhanga n’kuulukira m’mwamba.” Koma masiku ano anthu olemera ndi osauka omwe amadera nkhawa kwambiri za mmene angapezere ndalama. Nthawi zambiri zimenezi zimachititsa kuti azichita zinthu zimene zingawononge mbiri yawo, ubwenzi wawo ndi anthu ena ngakhalenso thanzi lawo. (Miy. 28:20; 1 Tim. 6:9, 10) Chachiwiri, tiziganiza kaye tisanalankhule. Ngati sitingasamale, zimene tingalankhule zingakhumudwitse kwambiri anthu ena. Lemba la Miyambo 12:18 limati: “Mawu a munthu amene amalankhula asanaganize amalasa ngati lupanga, koma lilime la anthu anzeru limachiritsa.” Timapitiriza kugwirizana ndi anthu ena tikamapewa kulankhula miseche pa zimene amalakwitsa.—Miy. 20:19. w22.10 21 ¶14; 22 ¶16-17
Lachiwiri, December 24
Idya mpukutu uwu ndipo upite kukalankhula ndi nyumba ya Isiraeli.—Ezek. 3:1.
Ezekieli ankafunika kumvetsa uthenga wonse umene ankafunika kukalengeza. Uthengawo unkafunika umufike pamtima. Kenako panachitika chinthu china chochititsa chidwi. Ezekieli anazindikira kuti mpukutuwo “unali wotsekemera ngati uchi.” (Ezek. 3:3) Chifukwa chiyani? Chifukwa kulankhula moimira Yehova kunali kokoma kapena kuti kosangalatsa kwa iye. (Sal. 19:8-11) Iye ankayamikira kuti Yehova wamuvomereza kutumikira monga mneneri wake. Pambuyo pake Yehova anauza Ezekieli kuti: “Mvetsera mawu onse amene ndikukuuza ndipo uwaganizire mozama.” (Ezek. 3:10) Pomupatsa malangizowa, iye anamuuza kuti asunge mawu a mumpukutuwo mumtima mwake komanso kuwaganizira. Kuchita zimenezi kunathandiza Ezekieli kulimbitsa chikhulupiriro chake. Kunamuthandizanso kuti akalengeze kwa anthu uthenga wamphamvu womwe anatumidwa. (Ezek. 3:11) Kumvetsa komanso kukhulupirira uthengawo kunachititsa Ezekieli kukhala wokonzeka kuvomera utumiki womwe anapatsidwa. w22.11 6 ¶12-14
Lachitatu, December 25
Kumvera kumaposa nsembe. —1 Sam. 15:22.
Kodi tingatani ngati kusintha kwa zinthu m’gululi kukuyesa kukhulupirika kwathu? Tizichita zinthu mogwirizana ndi kusintha komwe kwachitika. Pa nthawi yomwe ankadutsa m’chipululu, Akohati ankanyamula likasa n’kumayenda patsogolo pa anthu onse. (Num. 3:29, 31; 10:33; Yos. 3:2-4) Umenewutu unali mwayi waukulu. Komabe zinthu zinasintha Aisiraeli atafika m’Dziko Lolonjezedwa. Likasa silinkafunikanso kumanyamulidwa pafupipafupi, choncho Akohati anapatsidwa ntchito zina. (1 Mbiri 6:31-33; 26:1, 24) Palibe paliponse pomwe pamasonyeza kuti Akohati anadandaula kapena kumafuna kupatsidwa udindo wapamwamba chifukwa choti m’mbuyomo ankachita utumiki wapadera. Kodi tikuphunzirapo chiyani? Muzigwirizana ndi mtima wonse ndi kusintha kulikonse komwe kumachitika m’gulu la Yehova, ngakhale komwe kwakhudza utumiki wanu. Muzisangalala ndi utumiki uliwonse womwe mwapatsidwa. Muzikumbukira kuti utumiki wanu si umene umasonyeza kuti ndinu ofunika kwambiri. Yehova amaona kuti ndinu ofunika chifukwa choti ndinu omvera osati chifukwa chakuti muli pa utumiki winawake. w22.11 23 ¶10-11
Lachinayi, December 26
Sanachite manyazi ndi maunyolo anga.—2 Tim. 1:16.
Onesiforo anamufunafuna mtumwi Petulo ndipo atamupeza, anayesetsa kumuthandiza. Pochita zimenezi, Onesiforo anaika moyo wake pangozi. Kodi ifeyo tikuphunzirapo chiyani? Tisamalole kuti kuopa anthu kutisokoneze kapena kutilepheretse kuthandiza abale athu omwe akuzunzidwa. M’malomwake, tizichita zonse zomwe tingathe kuti tiwathandize. (Miy. 17:17) Iwo amafunikira chikondi chathu ndi thandizo lathu. Taganizirani mmene abale ndi alongo athu ku Russia akuthandizira Akhristu anzawo omwe amangidwa. Ena akamaimbidwa milandu kukhoti, abale ndi alongo ambiri amapita komweko posonyeza kuti ali kumbali yawo. Kodi ifeyo tikuphunzirapo chiyani? Abale amene amatsogolera akamanyozedwa, kumangidwa kapena kuzunzidwa, musamachite mantha. Muziwapempherera, kusamalira anthu a m’banja lawo komanso kufunafuna njira zina zowathandizira.—Mac. 12:5; 2 Akor. 1:10, 11. w22.11 17 ¶11-12
Lachisanu, December 27
Amenewa . . . amandilimbikitsa kwambiri.—Akol. 4:11.
Imodzi mwa ntchito zimene akulu amagwira ndi kulimbikitsa abale ndi alongo awo ndi mfundo za m’Baibulo komanso kuwathandiza kuti asakhale ndi nkhawa. (1 Pet. 5:2) Pakachitika ngozi, choyamba akulu amaonetsetsa kuti aliyense ali ndi chakudya, zovala komanso pokhala. Komabe kwa miyezi yambiri pambuyo pa ngoziyo opulumukawo angafunike kupitirizabe kulimbikitsidwa ndi mfundo za m’Malemba. (Yoh. 21:15) Harold, yemwe amatumikira m’Komiti ya Nthambi, ndipo anakumanapo ndi abale ndi alongo ambiri omwe anakhudzidwa ndi ngozi ananena kuti: “Pamatenga nthawi kuti munthu ayambirenso kuchita zinthu ngati kale. Iwo angayambe kuiwala za zinthu zimene anataya komabe zingawavute kuiwala imfa ya okondedwa awo, zinthu zawo zamtengo wapatali komanso mmene zinalili zovuta kuti apulumuke. Akamakumbukira zinthu ngati zimenezi, angayambirenso kukhala ndi chisoni. Zimenezi sizitanthauza kuti munthu alibe chikhulupiriro. Koma ndi mmene munthu aliyense angamvere mwachibadwa.” Akulu amatsatira malangizo akuti “muzilira ndi anthu amene akulira.”—Aroma 12:15. w22.12 22 ¶1; 24-25 ¶10-11
Loweruka, December 28
Pitirizani kuyenda motsogoleredwa ndi mzimu, ndipo simudzachita zimene thupi lomwe si langwiro likulakalaka ngakhale pang’ono.—Agal. 5:16.
Pofuna kutithandiza kuti tizichita zoyenera, Yehova mowolowa manja amatipatsa mzimu wake woyera. Tikamaphunzira Mawu a Mulungu, mzimu woyera umagwira bwino ntchito pa moyo wathu. Timalandiranso mzimu woyera tikapezeka pamisonkhano. Pamisonkhanoyi timacheza ndi abale ndi alongo omwe mofanana ndi ifeyo, akuyesetsa kuti azichita zoyenera ndipo zimenezi ndi zolimbikitsa. (Aheb. 10:24, 25; 13:7) Tikamapemphera kwa Yehova mochokera pansi pa mtima komanso kumuchonderera kuti atithandize kusiya khalidwe linalake, iye adzatipatsa mzimu wake woyera kuti tipitirize kulimbana ndi khalidwelo. Ngakhale kuti izi sizingachititse kuti tisiye kulakalaka zinthu zoipa, komabe zingatithandize kuti tisachite zoipazo. Tikayamba kuchita zinthu zokhudza kulambira nthawi zonse, tiziyesetsa kuti tisasiye kuzichita ndipo tizipitiriza kulakalaka zinthu zabwino. w23.01 11 ¶13-14
Lamlungu, December 29
Sindidzalola kuti chinthu china chizindilamulira.—1 Akor. 6:12.
Ngakhale kuti Baibulo si buku lofotokoza za thanzi kapena za zakudya, limatithandiza kudziwa mmene Yehova amaganizira pa nkhanizi. Mwachitsanzo, iye amatilimbikitsa kuti ‘tiziteteza thupi lathu’ ku zinthu zomwe zingaliwononge. (Mlal. 11:10) Baibulo limaletsa kudya kwambiri komanso kumwa kwambiri mowa chifukwa zimenezi zingawononge moyo. (Miy. 23:20) Yehova amayembekezera kuti tizidziletsa pa nkhani ya kuchuluka kwa chakudya komanso mowa. (1 Akor. 9:25) Tingasonyeze kuti timayamikira kwambiri mphatso ya moyo imene Mulungu anatipatsa pogwiritsa ntchito bwino luso loganiza. (Sal. 119:99, 100; Miy. 2:11) Mwachitsanzo, tingagwiritse ntchito luso loganiza pa nkhani ya zakudya zomwe timasankha. Ngati timakonda chakudya chinachake koma timadziwa kuti tikadya chimatidwalitsa, kuganiza bwino kumatithandiza kuti tizichipewa. Tingasonyezenso kuti ndife oganiza bwino tikamagona mokwanira, kuchita masewera olimbitsa thupi nthawi zonse, kukhala aukhondo komanso kusamalira pakhomo pathu. w23.02 21 ¶6-7
Lolemba, December 30
Umawerengamo zotani? —Luka 10:26.
Kodi mungatani kuti muzipeza mfundo zothandiza mukamawerenga Baibulo? Taganizirani zimene timawerenga pa 2 Timoteyo 3:16, 17. Lembali limati, “Malemba onse . . . ndi othandiza” (1) pophunzitsa (2) kudzudzula (3) kukonza zinthu ndiponso (4) kulangiza. Mungapeze mfundo 4 zothandizazi ngakhale m’mabuku a Baibulo amene simuwawerenga kawirikawiri. Mukamawerenga nkhani inayake muziona zimene ikukuphunzitsani zokhudza Yehova, cholinga chake kapena mfundo zake. Muziganizira mmene nkhaniyo ingakhalire yothandiza podzudzula. Muzichita zimenezi poona mmene mavesiwo akukuthandizirani kuzindikira komanso kupewa makhalidwe oipa ndiponso kupitirizabe kukhala okhulupirika kwa Yehova. Muziganizira mmene mungagwiritsire ntchito nkhaniyo powongola kapena kuti pokonza zolakwika mwina zimene munthu amene mukumulalikira wanena. Komanso muzifufuza malangizo omwe angakuthandizeni kuti muziona zinthu mmene Yehova amazionera. Nthawi zonse mukamaganizira zinthu 4 zimenezi, mudzapeza mfundo zothandiza zomwe zingachititse kuti muzipindula kwambiri mukamawerenga Baibulo. w23.02 11 ¶11
Lachiwiri, December 31
Ufumu wake sudzawonongedwa. —Dan. 7:14.
Ulosi wina m’buku la Danieli unaneneratu kuti Yesu adzalandira Ufumu wake kumapeto kwa nthawi 7. Kodi n’zotheka kudziwa nthawi yeniyeni yomwe zinthu zosangalatsazi zinachitika? (Dan. 4:10-17) “Nthawi zokwanira 7” zimaimira zaka 2,520. Zaka zimenezi zinayambira mu 607 B.C.E., pomwe Ababulo anachotsa mfumu yomaliza pampando wachifumu wa Yehova ku Yerusalemu. Nthawiyi inatha mu 1914 pomwe Yehova anaika Yesu, “amene ali woyenerera mwalamulo,” kukhala Mfumu ya Ufumu wa Mulungu. (Ezek. 21:25-27) Kodi ulosiwu umatithandiza bwanji? Kudziwa zokhudza “nthawi zokwanira 7” kumatitsimikizira kuti Yehova amakwaniritsa malonjezo ake pa nthawi yake. Mofanana ndi zimene anachita pokonzeratu nthawi yeniyeni yoti Ufumu wake udzakhazikitsidwe, adzaonetsetsanso kuti maulosi ena onse akwaniritsidwa pa nthawi yake yoyenera. Choncho ndife otsimikiza kuti tsiku la Yehova ‘silidzachedwa.’—Hab. 2:3. w22.07 3 ¶3-5