16 BARAKI NDI DEBORA
“Tipitiradi Limodzi”
MOYO unafika povuta kwambiri kwa Aisiraeli chifukwa anapandukira Yehova. Iye anali atawachenjeza kuti adzalola adani awo kuti awaukire. Pa nthawiyi, Yabini ndi amene ankalamulira ku Kanani ndipo mkulu wa asilikali ake anali Sisera yemwe anali wankhanza kwambiri. Sisera ankatsogolera gulu lalikulu la asilikali lokhala ndi magaleta ankhondo 900 komanso zida zachitsulo.
Asilikali a Sisera anakhala akuopseza Aisiraeli kwa zaka 20. Zikuoneka kuti anali ndi chizolowezi choti akagonjetsa mzinda, ankagwira ukapolo atsikana komanso kuwagwiririra. Chifukwa cha mantha, anthu sankayenda m’misewu ikuluikulu komanso ankathawa m’nyumba zawo. Amuna ambiri a Aisiraeli analibe zida za nkhondo zoti angadzitetezere.
Pa nthawiyi, panali mayi wina wolimba mtima dzina lake Debora yemwe ankatumikira monga mneneri wa Yehova. Iye ankathanso kuweruza milandu yovuta ya anthu a Yehova. Pogwiritsa ntchito mneneri wamkaziyu, Yehova anasankha mwamuna wina dzina lake Baraki kuti akhale woweruza komanso kuti apulumutse anthu ake. Debora anaitanitsa Baraki kuti amupatse malangizo ochokera kwa Yehova. Baraki ayenera kuti anadabwa pomwe mneneriyu anamuuza kuti asonkhanitse amuna 10,000 n’kupita nawo kuphiri la Tabori ndipo Yehova adzapereka Sisera ndi asilikali ake m’manja mwake.
Kodi Baraki anakhumudwa chifukwa choti analandira malangizo kuchokera kwa mkazi? Ayi. M’malomwake anadzichepetsa ndipo ananena kuti apita pokhapokha ngati angapitire limodzi ndi mneneriyu. Komabe, zimenezi sizikusonyeza kuti Baraki analibe chikhulupiriro. Patapita nthawi, mtumwi Paulo ananena kuti Baraki anali m’gulu la amuna ndi akazi a chikhulupiriro. (Aheb. 11:1, 2, 32) Baraki anasonyeza chikhulupiriro pouza Debora kuti apitire limodzi ndi Barakiyo komanso gulu lake. Iye ankadziwa kuti Yehova akugwiritsa ntchito Debora ndipo Deborayo azimutsogolera pomupatsa malangizo ochokera kwa Yehova. Debora analimba mtima n’kunena kuti, “Tipitiradi limodzi.” Iye anauzanso Baraki kuti ngakhale kuti adzapambana nkhondoyo, palibe mwamuna aliyense amene adzaphe Sisera. Mulungu adzagwiritsa ntchito mkazi kuti aphe Sisera.
Nthawi yomweyo, Baraki anayamba kuchita zomwe Yehova anamuuza. Iye anasonkhanitsa amuna olimba mtima 10,000 n’kupita nawo pamwamba paphiri la Tabori ngakhale kuti anali ndi zida zochepa. Phiri la Tabori linali m’chigwa cha Yezereeli ndipo linali lalitali mamita 562. Phiri limeneli linkaoneka ngati mbale yolowa yovindikiridwa. Kuchokera pamwamba pa phiripo, Debora, Baraki ndi gulu lawo ankatha kuona Sisera ndi magaleta ake ankhondo akubwera chapatali.
Ndiye kodi Baraki akanatani? Monga mkulu wa asilikali, mwina akanaganiza zoti Sisera ndi magaleta ake ayandikire kaye phirilo, chifukwa Sisera akanavutika kukwera phiri ndi magaleta akewo moti Baraki akanawagonjetsa mosavuta. Koma ankadziwa kuti nkhondoyo si yake, ndi ya Yehova. Choncho anamvera malangizo a Debora. Kudzera mwa iye, Yehova anauza Baraki kuti anyamuke n’kuyamba kumenya nkhondo. Iwo anatsika kuchoka pamwamba pa phirilo mpaka pansi kuti akamenyane ndi asilikali oopsawo.
Woweruza komanso mneneri wamkazi, ankafunika kulimbana ndi mtsogoleri wankhondo wankhanza kwambiri limodzi ndi asilikali ake oyenda pa magaleta
Kwa anthu, zikanakhala zosatheka kuti Baraki ndi gulu lake awine nkhondoyi. Koma Yehova anaona kulimba mtima kwawo ndipo anawathandiza. Anachititsa kuti asilikali a Chikanani asokonezeke. Iye anagwetsa chimvula champhamvu ndipo chinachititsa kuti m’chigwa cha Yezereeli mukhale matope okhaokha moti magaleta ankhondowo ankavutika kwambiri kuyenda. Moti asilikali a Sisera ankayenera kumenyana ndi asilikali a Isiraeli popanda kugwiritsa ntchito magaleta. Ndipo palibe ngakhale msilikali mmodzi wa Sisera yemwe anapulumuka. Nanga kodi Sisera zinamuthera bwanji?
Sisera anakwanitsa kuthawa wapansi ndipo anakafika kumtunda movutikira chifukwa cha matope. Iye anasiya asilikali ake akuphedwa n’kumaganiza kuti wathawa. Koma Baraki anayamba kumutsatira. Yehova ankaona zomwe zinkachitikazo ndipo anali atadziwa kale zoti achitire Sisera.
Werengani nkhaniyi m’Baibulo:
Funso lokambirana:
Kodi Baraki ndi Debora anasonyeza kulimba mtima m’njira ziti?
Zoti Mufufuze
1. Kodi zinthu zinali bwanji kwa Aisiraeli pa nthawi imene Sisera ankawapondereza? (w15 8/1 13 ¶1)
2. N’chifukwa chiyani Debora sawerengedwa kuti ali m’gulu la oweruza 12 omwe anatumikira ku Isiraeli, Samueli asanakhale mneneri? (w86 6/1 31 ¶6-8-wcgr)
3. Kodi Debora anakhala bwanji ngati “mayi mu Isiraeli”? (Ower. 4:4, 5; 5:7; w15 8/1 13 ¶2) A
Chithunzi A
Chithunzi A
4. Kodi Debora ndi Baraki ankatanthauza chiyani pomwe anaimba kuti “nyenyezi zinamenya nkhondo” yolimbana ndi Sisera? (Ower. 5:20; w05 1/15 25 ¶5)
Zomwe Tikuphunzirapo
Ndi pa nthawi iti pomwe m’bale amafunika kudzichepetsa n’kulola kuti mkazi amuthandize ngati mmene anachitira Baraki? B
Chithunzi B
N’chifukwa chiyani Debora ankafunika kulimba mtima kuti apite kunkhondo limodzi ndi Baraki? Nanga ndi pa nthawi iti pomwe ifenso timafunika kulimba mtima kotereku?
Kodi tingatsanzire kulimba mtima kwa Baraki ndi Debora m’njira zinanso ziti?
Ganizirani Mfundo Yaikulu
Kodi nkhaniyi yandiphunzitsa chiyani za Yehova?
Kodi nkhaniyi ikugwirizana bwanji ndi cholinga cha Yehova?
Kodi ndingakonde kudzamufunsa chiyani Baraki ndi Debora akadzaukitsidwa?
Phunzirani Zambiri
Onani mmene nkhaniyi ingatithandizire kudziwa kuti Yehova amasangalala ndi zomwe timamuchitira.
“Kudzipereka Kwathu Kumachititsa Kuti Yehova Atamandidwe” (w17.04 28-32)
Kodi tingaphunzire chiyani kwa Baraki ndi Debora pa nkhani yokhala wodalirika, wodzichepetsa komanso womvera?
“Ndi Chikhulupiriro, Baraki Anagonjetsa Gulu Lankhondo Lamphamvu” (w03 11/15 28-31)