Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • wcg mutu 20 tsamba 94-tsamba 97
  • Analimba Mtima pa Nthawi Yomwe Anali Wofooka

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Analimba Mtima pa Nthawi Yomwe Anali Wofooka
  • Muziyenda Ndi Mulungu Molimba Mtima
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Zoti Mufufuze
  • Zomwe Tikuphunzirapo
  • Ganizirani Mfundo Yaikulu
  • Phunzirani Zambiri
  • Tizidalira Yehova Ngati Mmene Samisoni Ankachitira
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2023
  • Samsoni Anapambana Chifukwa cha Mphamvu za Yehova
    Nsanja ya Olonda—2005
  • Yehova Anapatsa Mphamvu Samisoni
    Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
  • Munthu Wamphamvu Kopambana
    Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo
Onani Zambiri
Muziyenda Ndi Mulungu Molimba Mtima
wcg mutu 20 tsamba 94-tsamba 97

20 SAMISONI

Analimba Mtima pa Nthawi Yomwe Anali Wofooka

Losindikizidwa
Losindikizidwa

SAMISONI anali pa mavuto aakulu. Iye anachita zinthu mopusa pomwe anaululira munthu wina za chinsinsi cha mphamvu zake. Zotsatirapo zake, Afilisiti anam’gwira ndipo anamuboola maso n’kumumanga. Anamuika m’ndende ndipo ankamugwiritsa ntchito ngati kapolo. Ngakhale kuti pa nthawiyi Samisoni sankaona, koma ankamva gulu la Afilisiti likumunyoza komanso kunyoza Yehova Mulungu wake. Samisoni ankadziwa kuti vuto linali iyeyo. Nthawi zonse ankachita zinthu molimba mtima. Kodi pa nthawiyi akanakwanitsanso kulimba mtima?

Kwa zaka 20, Samisoni anali woweruza mu Isiraeli koma anali wosiyana ndi oweruza ena. Kodi ankasiya bwanji? Oweruza monga Baraki, Gidiyoni ndi Yefita ankatsogolera asilikali pomenya nkhondo za Mulungu. Koma si mmene zinalili ndi Samisoni. Yehova ankagwiritsira ntchito Samisoni popanda asilikali omuthandizira kugonjetsa adani ake ndipo anapha Afilisiti ambirimbiri yekha. Kodi zimenezi zinatheka bwanji?

Pamene mngelo anauza makolo a Samisoni kuti adzakhala ndi mwana wamwamuna, anawauzanso kuti mwanayo adzakhala Mnaziri kwa moyo wake wonse. Mnaziri sankaloledwa kumeta tsitsi, choncho Samisoni nayenso sanametepo tsitsi lake. Akamachita zinthu mogwirizana ndi lumbiro lake, Yehova ankamudalitsa pomupatsa mphamvu zodabwitsa. Pa nthawi ina, Samisoni anakhadzula mkango pakati ndi manja ake. Iye anagwiritsa ntchito mphamvu zomwe Mulungu anamupatsa kugonjetsa Afilisiti omwe ankapondereza Aisiraeli. Aisiraeliwo anali atayambiranso kulambira milungu yonyenga.

Pa nthawi ina, chifukwa cha mantha Aisiraeli anagwira Samisoni n’kumumanga ndipo anamupereka kwa Afilisiti. Koma Samisoni anadula zingwezo ngati ulusi ndipo anapha Afilisiti 1,000 pogwiritsa ntchito fupa la nsagwada za bulu. Kenako Samisoni ali mumzinda wa Gaza, adani ake anamubisalira kuti amuphe kukamacha. Koma iye anadzuka pakati pa usiku n’kugwira zitseko za geti la mzindawo pamodzi ndi nsanamira zake n’kuzizula pamodzi ndi chokhomera cha getilo. Atatero, anazinyamula pamapewa ndipo anayenda ulendo wa makilomita 60 kupita pamwamba pa phiri lomwe linali pafupi ndi Heburoni.

Mobwerezabwereza, Samisoni ankagonjetsa Afilisiti. Iye anasonyeza kuti milungu yawo monga Dagoni inalibe mphamvu ndipo sikanatha kulimbana ndi mtumiki wa Yehova. Komabe, Afilisiti anapeza njira yogonjetsera Samisoni. Anagwiritsa ntchito Delila.

Samisoni ankakonda kwambiri Delila, koma Delilayo anali wosakhulupirika. Iye analandira ndalama kwa Afilisiti kuti adziwe chimene chinkapangitsa Samisoni kukhala wamphamvu. Choncho ankamuvutitsa Samisoni kuti amuululire chinsinsicho. Pamapeto pake Samisoni anatopa nazo ndipo anaulula. Ananena kuti ngati atamumeta tsitsi, sangakhalenso ndi mphamvu zodabwitsa. Choncho Delila anamudikira kuti agone ndipo anaitana munthu kuti adzamumete tsitsilo. Baibulo limati, ‘Yehova anamusiya.’ Choncho Samisoni analibenso mphamvu. Afilisiti anabwera kudzamugwira n’kumuboola maso.

Afilisiti anapatsa Samisoni ntchito yowawa yoti aziyendetsa mwala wa mphero. Iwo anasangalala poona kuti mdani wawo wamphamvu uja ndi kapolo wawo. Anakonza phwando pofuna kulemekeza Dagoni. Pa tsiku la phwandoli, anthu ambiri anasonkhana m’kachisi. Pafupifupi anthu 3,000 anali padenga. Afilisiti anaitanitsa Samisoni kuti adzawasangalatse, choncho anakamutenga n’kumuimika pakati pa zipalala zikuluzikulu ziwiri. Pa nthawiyi, Samisoni anali atalapa ndipo tsitsi lake linali litayambanso kukula.

Chifukwa cha zomwe analakwitsa, Samisoni anakhala mkaidi koma anagwiritsa ntchito moyenerera mwayi womaliza womwe anali nawo

Atagwira zipilalazo, anapempha Yehova kuti amupatsenso mphamvu. Anapemphera kuti: “Chonde ndikumbukireni ndi kundipatsa mphamvu kamodzi kokhaka. Inu Mulungu.” Anafuulanso kuti: “Ndife nawo limodzi Afilisitiwa!” Yerekezerani kuti mukumuona akukankha zipilalazo mwamphamvu mpaka zikugwa. Afilisiti asanapite kukamuletsa, zipilalazo zinali zitayamba kale kugwa ndipo kachisiyo anagwa. Aka kanali komaliza kuti Samisoni agwiritse ntchito mphamvu zake zodabwitsa. Pa nthawiyi anapha adani a Yehova ambiri kuposa amene anaphapo m’mbuyomo.

Samisoni waima pakati pa zipilala ziwiri ndipo akupemphera pamene gulu la anthu likumunyoza.

Patapita zaka zambiri pamene mtumwi Paulo ankatchula za anthu achikhulupiriro, anatchulanso za Samisoni. Paulo analemba kuti “anali ofooka koma anapatsidwa mphamvu” ndipo n’zosakayikitsa kuti ankaganizira za woweruza wolimba mtimayu.—Aheb. 11:​32-34.

Werengani nkhaniyi m’Baibulo:

  • Oweruza 13 mpaka 16

Funso lokambirana:

Kodi Samisoni anasonyeza kulimba mtima m’njira ziti?

Zoti Mufufuze

  1. 1. Zinatheka bwanji kuti Samisoni agwire mitembo koma n’kukhalabe Mnaziri? (w05 1/15 30 ¶1–31 ¶1)

  2. 2. N’chiyani chikusonyeza kuti Samisoni ankafunikira mzimu woyera wa Mulungu kuti anyamule zitseko ndi nsanamira zake kuchoka ku Gaza kukafika ku Heburoni? (w04 10/15 15 ¶7-8) A

    Samisoni akukwera phiri atanyamula zitseko za geti la mzinda pamodzi ndi nsanamira zake. Kumbuyo kwake kukuoneka mapu osonyeza mtunda wochoka ku Gaza n’kukwezeka kukafika ku Heburoni.

    Chithunzi A

  3. 3. N’chifukwa chiyani tinganene kuti mwina Delila anali Mwisiraeli? (w05 3/15 28 ¶3)

  4. 4. N’chifukwa chiyani Samisoni anapemphera kuti abwezere Afilisiti ‘chifukwa cha limodzi mwa maso ake’? (Ower. 16:28; it “Samisoni” ¶10-wcgr)

Zomwe Tikuphunzirapo

  • Chifukwa chopanikizika, Samisoni anaulula chinsinsi kwa Delila. Kodi akulu ndi akazi awo akuphunzirapo chiyani pa nkhaniyi? B

    Zithunzi: 1. Akulu atatu akulankhulana ndi mlongo wina. 2. Pambuyo pake, mmodzi mwa akuluwo akucheza ndi mkazi wake uku akumwa tiyi.

    Chithunzi B

  • Samisoni analakwitsa zinthu komabe pambuyo pake, Yehova anamugwiritsa ntchito modabwitsa. Ngati Mkhristu masiku ano walakwitsa zinazake, kodi chitsanzo cha Samisoni chingamuthandize bwanji kuti asafooke?

  • Mungatsanzire bwanji kulimba mtima kwa Samisoni?

Ganizirani Mfundo Yaikulu

  • Kodi nkhaniyi yandiphunzitsa chiyani za Yehova?

  • Kodi nkhaniyi ikugwirizana bwanji ndi cholinga cha Yehova?

  • Kodi ndingakonde kudzamufunsa chiyani Samisoni akadzaukitsidwa?

Phunzirani Zambiri

Phunzitsani ana anu zomwe zinapangitsa Samisoni kukhala wamphamvu kuposa amuna onse.

“Mzimu Woyera Unathandiza Samisoni Kukhala Ndi Mphamvu” (ijwis nkhani 14)

Kodi tingaphunzireponso chiyani pa nkhani ya Samisoni?

“Tizidalira Yehova Ngati Mmene Samisoni Ankachitira” (w23.09 2-7)

    Mabuku a Chichewa (1974-2026)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena