Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • wcg mutu 19 tsamba 90-tsamba 93
  • Anakwaniritsa Lumbiro Lovuta

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Anakwaniritsa Lumbiro Lovuta
  • Muziyenda Ndi Mulungu Molimba Mtima
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Zoti Mufufuze
  • Zomwe Tikuphunzirapo
  • Ganizirani Mfundo Yaikulu
  • Phunzirani Zambiri
  • Anasangalatsa Bambo Ake Komanso Yehova
    Phunzitsani Ana Anu
  • Yehova Amadalitsa Anthu Okhulupirika
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2016
  • Ankakondedwa Ndi Mulungu Komanso Anzake
    Nsanja ya Olonda—2011
  • Yefita Anasunga Chowinda Chake kwa Yehova
    Nsanja ya Olonda—2007
Onani Zambiri
Muziyenda Ndi Mulungu Molimba Mtima
wcg mutu 19 tsamba 90-tsamba 93

19 YEFITA NDI MWANA WAKE WAMKAZI

Anakwaniritsa Lumbiro Lovuta

Losindikizidwa
Losindikizidwa

ANTHU anali atasiya kulambira Yehova ku Isiraeli ndipo zinthu zinali zitafika poipa kwambiri. Zotsatira zake, Yehova analola kuti Aamoni apondereze Aisiraeli kwa zaka 18. (Ower. 10:8) Kenako Aisiraeli analapa n’kusiya kulambira milungu yonyenga ndipo anabwerera kwa Yehova. Koma pasanapite nthawi, Aamoni anasonkhana ku Giliyadi kuti awaukire.

Akulu a ku Giliyadi anapempha mwamuna wina dzina lake Yefita kuti adzatsogolere Aisiraeli pa nkhondo. Yefita anali atathawa m’chigawo cha Giliyadi chifukwa achibale ake ena ankamuchitira nkhanza. Kodi iye anakwiya kapena kuwasungira zifukwa? Ayi. Anabwerera ku Giliyadi kukawatsogolera pa nkhondoyo. Atafika, iye anayesetsa kukhazikitsa mtendere. Anatumiza anthu kuti akafotokozere mfumu ya Aamoni mwatsatanetsatane chifukwa chake siinkayenera kulanda malo a Aisiraeli. Zomwe Yefita ananena zinasonyeza kuti ankadziwa bwino mmene Yehova anapatsira malowo Aisiraeli komanso mmene anawathandizira kugonjetsa mizinda yozungulira. Komabe, mfumu ya Aamoni inachita makani ndipo inkafuna kuti amenyane basi.

Pamene Yefita ankakonzekera nkhondo, mzimu wa Yehova unayamba kumuthandiza. Choncho, sanachite zinthu mopupuluma pomwe analonjeza Yehova kuti: “Mukapereka Aamoni m’manja mwanga, aliyense amene adzatuluka m’nyumba yanga kudzandichingamira pamene ndikubwera mwamtendere kuchokera kwa Aamoni, ndidzam’pereka kwa inu Yehova kuti akhale nsembe yopsereza.”

Kodi pamenepa ankatanthauza kuti adzapereka nsembe munthu weniweni? Ayi. Yehova ankadana ndi zoti anthu aziperekedwa ngati nsembe. (Deut. 18:​10, 12) Apa iye ankatanthauza kuti munthu woyambirira amene adzatuluke m’nyumba kudzamuchingamira “adzakhala wa Yehova” m’njira yakuti munthuyo azikamutumikira kuchihema cha ku Silo. Yefita ankadziwa kuti zikhoza kukhala zovuta kuti akwaniritse lonjezoli chifukwa anali ndi mwana mmodzi yekha wamkazi ndipo iye ndi amene akanakhala woyamba kudzamuchingamira.

Yefita atalonjeza, anapita kunkhondo. Molimba mtima anatsogolera amuna omwe anali naye. Ndipo Yehova anachititsa kuti apambane nkhondoyo. Iwo anapha adani awo kenako anakaphanso “Aamoni ambirimbiri m’mizinda 20.”

Yefita anabwerera kwawo akusangalala kwambiri. N’kutheka kuti ankaganiza zoti wantchito wake ndi amene adzakhale woyambirira kutuluka m’nyumba kudzamuchingamira. Ngati zinali choncho ayenera kuti anakhumudwa chifukwa mwana wake ndi amene anali woyambirira kudzamuchingamira, akuimba maseche komanso kuvina. Atangomuona anang’amba zovala zake n’kunena kuti: “Mayine mwana wanga! Ndikumva chisoni kwambiri chifukwa ndikukuchotsa pakhomo.”

Yefita ndi mwana wake ankafunika kukwaniritsa lumbiro lawo. Komabe ankafunika kudzimana kwambiri

Mwana wa Yefita ankadziwa kuti moyo wake usinthiratu chifukwa cha zomwe bambo ake analonjeza. Iye ankafunika kudzipereka kwa Yehova kuti azichita utumiki wopatulika. Kutanthauza kuti sakanakwatiwa kapenanso kukhala ndi ana. Zimenezi zinali zovuta kwambiri kwa akazi a Chiisiraeli. Komabe molimba mtima, mtsikanayu anauza bambo ake kuti: “Ngati mwalonjeza kwa Yehova, ndichitireni mogwirizana ndi zimene mwanenazo.” Iye anapempha bambo ake kuti amulole achoke kwa kanthawi ndi atsikana anzake apite kumapiri kukalira chifukwa choti sadzakwatiwa komanso sadzakhala ndi ana.

Yefita wagwada ndipo akung’amba zovala zake pamene mwana wake akufika pamene ali n’kumugwira paphewa pomutsimikizira kuti zikhala bwino.

Mwana wa Yefita anali wodzichepetsa komanso wolimba mtima. Chifukwa cha zimenezi, chaka chilichonse atsikana a mu Isiraeli ankapita maulendo 4 kukamuyamikira komanso kukamulimbikitsa. Iye anali ndi mwayi waukulu wotumikira Yehova pachihema. N’kutheka kuti pa nthawiyi, Samueli anali wamng’ono ndipo ankakhala kuchihemako. Ndiye kodi mwana wa Yefita ankamuphunzitsa Samueli komanso kumulimbikitsa pomwe ankakula? Sitikudziwa. Koma ngati zinali choncho, popeza analibe mwana wakewake ayenera kuti ankasangalala kumuthandiza Samueli. Chomwe tikudziwa n’chakuti pa nthawiyo, anthu ankachita zachiwerewere pachihema. (1 Sam. 2:22) Ndiye kodi mwana wa Yefita ankachita nawo khalidwe loipali? Ayi. Mawu a Mulungu amati: “Mtsikanayo sanagonepo ndi mwamuna.”

Mtumwi Paulo anatchula mwana wamkazi wa Yefita pamndandanda wa amuna ndi akazi achikhulupiriro cholimba. (Aheb. 11:32) Yefita ndi mwana wake wamkazi anatisiyira chitsanzo chabwino cha kukhala olimba mtima. Yefita anamenyera nkhondo anthu a Mulungu ndipo mwana wake anamuthandiza. Onse anakwaniritsa zomwe analonjeza Yehova ngakhale kuti zinali zovuta.

Werengani nkhaniyi m’Baibulo:

  • Oweruza 10:​15, 16; 11: 1-40

Funso lokambirana:

Kodi Yefita ndi mwana wake wamkazi anasonyeza kulimba mtima m’njira ziti?

Zoti Mufufuze

  1. 1. N’chiyani chikusonyeza kuti Aamoni sankangofuna kumenyana ndi Aisiraeli, koma ankafunanso kuwasiyitsa kulambira koona? (it “Yefita” ¶6-wcgr) A

    Amuna a Chiisiraeli akugwetsa mzati wopatulika anthu akuona. Mkati mwa chithunzichi: Mzimayi akuphwanya kafano.

    Chithunzi A: “Iwo anachotsa milungu yonse yachilendo imene anali nayo ndipo anayamba kutumikira Yehova.”—Ower. 10:16

  2. 2. Kodi zimene Yefita anachita zikufanana bwanji ndi zimene Yakobo anachita atalumbira kwa Yehova? (it “Yefita” ¶11-wcgr)

  3. 3. N’chiyani chikusonyeza kuti Yefita ankafunika kudzimana kwambiri kuti akwaniritse lumbiro lake? (w17.04 4 ¶6)

  4. 4. Mneneri Samueli anabadwa cha m’ma 1180 B.C.E. N’chiyani chikusonyeza kuti mwina iye komanso mwana wa Yefita anatumikira kuchihema pa nthawi yofanana? (it “Yefita” ¶2-wcgr; onani tchati chakuti “Kuyambira Nthawi ya Makolo Akale Mpaka Nthawi ya Oweruza.”)

Zomwe Tikuphunzirapo

  • Makolo akamasonyeza kulimba mtima ngati Yefita, kodi zingakhudze bwanji ana awo?

  • Kodi Akhristu masiku ano, angatsanzire bwanji atsikana omwe ankapita kukayamikira komanso kuthandiza mwana wamkazi wa Yefita kuti akhalebe wolimba mtima? B

    Mlongo akutsegula mosangalala katoni ya mphatso ndipo akulankhula pa vidiyokomfelensi ndi anzake. Mukatoniyo muli zakudya, khadi ndi mphatso zina.

    Chithunzi B

  • Kodi mungatsanzire bwanji kulimba mtima kwa Yefita ndi mwana wake wamkazi?

Ganizirani Mfundo Yaikulu

  • Kodi nkhaniyi yandiphunzitsa chiyani za Yehova?

  • Kodi nkhaniyi ikugwirizana bwanji ndi cholinga cha Yehova?

  • Kodi ndingakonde kudzamufunsa chiyani Yefita komanso mwana wake akadzaukitsidwa?

Phunzirani Zambiri

Kodi chitsanzo cha Yefita ndi mwana wake chingathandize bwanji alongo osakwatiwa?

Muzigwiritsa Ntchito Bwino Nthawi Yomwe Simuli Pabanja (5:15)

Onani mmene Yefita ndi mwana wake wamkazi akutiphunzitsira mmene tingakhalirebe okhulupirika kwa Yehova.

“Yehova Amadalitsa Anthu Okhulupirika” (w16.04 5-9)

    Mabuku a Chichewa (1974-2026)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena