18 GIDIYONI
Anali Wolimba Mtima Komanso Ankachita Zinthu Mosamala
MUNTHU wolimba mtima, amafunikanso kuchita zinthu mosamala. Akamachita zinthu mosamala, sakhala ndi mtima wodzidalira kwambiri kapena kuchita zinthu mwachisawawa. Gidiyoni anali ndi makhalidwe awiri onsewa. Iye anakhalapo pa nthawi imene Aisiraeli anayambiranso kulambira milungu yabodza. Choncho Mulungu anasiya kuwateteza ndipo Amidiyani analowa m’dzikolo n’kuyamba kuwazunza moti sankatha kukolola mbewu zawo. Komabe, Gidiyoni anali wolimba mtima moti ankapuntha tirigu kuti ena apeze chakudya. Koma ankachita zimenezi mosamala moti tiriguyo ankamupunthira muchoponderamo mphesa chomwe chiyenera kuti chinali chooneka ngati mtsuko chomwe ankachigoba kuchokera ku mwala.
Zinthu zinafika poipa, moti pamapeto pake Aisiraeli anapempha Yehova kuti awathandize. Choncho Yehova anatumiza mneneri kukawakumbutsa chifukwa chake anawasiya. Pambuyo pake, Yehova anatumiza mngelo kwa Gidiyoni kukamuuza zoti wasankhidwa kuti akapulumutse anthu ake. Gidiyoni anapempha kuti aone chizindikiro chakuti mngeloyo watumidwadi ndi Yehova. Choncho mngeloyo anachititsa kuti moto uyake pamwala womwe Gidiyoni amafuna kuperekerapo nsembe. Kenako mngelo uja anazimiririka. Usiku umenewo, Yehova anauza Gidiyoni kuti agwetse guwa lansembe la Baala ndi kudula mzati wopatulika kuti amangepo guwa lansembe la Yehova n’kuperekapo nsembe. Gidiyoni anamvera, koma chifukwa choopa bambo ake komanso amuna amumzinda, iye anachita zimenezi usiku kuti asamuone.
Zitachitika zimenezi, Amidiyani ndi Aamaleki pamodzi ndi anthu onse a Kum’mawa, anasonkhanitsa gulu lalikulu la asilikali ndipo anadzaza ngati dzombe m’chigwa cha Yezereeli. Zitatero, mzimu wa Yehova unayamba kuthandiza Gidiyoni ndipo anaitanitsa amuna a mafuko osiyanasiyana a Aisiraeli kuti abwere adzathandizane naye kumenya nkhondo. Apanso, mosamala Gidiyoni anapempha Yehova kuti amuonetse chizindikiro pofuna kumutsimikizira kuti ali naye. Yehova anamulezera mtima ndipo anamuonetsa zodabwitsa ziwiri. Usiku umenewo, Gidiyoni anaika ubweya wa nkhosa pansi ndipo Yehova anachititsa kuti ubweya wokhawo unyowe ndi mame koma nthaka yonse n’kukhala youma. Usiku wa mawa lake, anachititsa kuti ubweya wokha ukhale wouma koma nthaka yonse inyowe ndi mame.
Poyamba Gidiyoni ndi asilikali ake analipo ochepa poyerekeza ndi adani awo, koma Yehova anamuuza kuti achepetsebe asilikaliwo
Zodabwitsa ziwirizi zinalimbitsa mtima Gidiyoni ndipo anasonkhanitsa asilikali ake 32,000 kuti akamenyane ndi asilikali 135,000. Pa nthawi yomwe Gidiyoni ndi asilikali a Aisiraeli anali pa Kasupe wa Harodi, Yehova anamuuza kuti asilikali ake achuluka kwambiri ndipo abweze asilikali onse amantha. Asilikali 10,000 ndi omwe anatsala. Koma Yehova anaona kuti anali adakali ambiri moti anauza Gidiyoni kuti aonetsetse mmene amunawo akumwera madzi. Onse omwe anamwa madziwo atagwada n’kuweramitsa pansi nkhope zawo, anawabweza. Koma ena anali tcheru moti ananjuta n’kumamwa madziwo ndi manja akuyang’ana uku ndi uku. Pamapeto pake, Gidiyoni anatsala ndi asilikali 300 okha. Asilikali amenewa ndi omwe anapita nawo kunkhondo.
Molimba mtima, Gidiyoni anakonzeka kukamenya nkhondo. Yehova anapatsa Gidiyoni chizindikiro chomutsimikizira kuti ali naye. Anamuuza kuti akalowe mozemba mumsasa wa adani awo usiku, ndipo iye anachitadi zomwezo. Atafika, anamva msilikali wina akuuza mnzake zomwe analota, zosonyeza kuti Aisiraeli adzapambana pankhondoyo. Yehova anathandiza Gidiyoni kuti akhale wolimba mtima ndipo iye anabwerera kwa asilikali ake n’kukawapatsa malangizo omenyera nkhondoyo. Usiku, Gidiyoni ndi asilikali ake anapita kumsasa wa adani. Gidiyoni atawapatsa chizindikiro, anagwiritsa ntchito mitsuko yaikulu, miyuni komanso malipenga a nyanga ya nkhosa n’kuchita phokoso lalikulu ndipo panaoneka kuwala. Iwo anafuula kuti, “Nkhondo ya Yehova komanso ya Gidiyoni!” Njira yomwe anagwiritsa ntchitoyi, inachititsa gulu la adaniwo kuona kuti aukiridwa. Yehova anasokoneza adaniwo moti anayamba kumenyana okhaokha. Asilikali pafupifupi 15,000 okha ndi omwe anapulumuka.
Gidiyoni anayamba kuwathamangitsa ndipo anawagonjetsa n’kuphanso mtsogoleri wawo. Iye anaperekanso chilango kwa anthu ena omwe anakana kuwathandiza ndi chakudya pomwe ankapita kukamenyana ndi adani a Mulungu. Kenako anthu anaganiza zomuika kuti akhale mfumu. Koma modzichepetsa, iye anakana ndi kuwauza kuti: “Yehova ndi amene azikulamulirani.” Yehova anadalitsa Gidiyoni chifukwa cha kulimba mtima komanso kuchita zinthu mosamala. Nthawi yonse yomwe Gidiyoni anali woweruza, ku Isiraeli sikunachitike nkhondo ndipo iye anakhala ndi moyo kwa zaka zambiri. Mtumwi Paulo anatchula Gidiyoni pa mndandanda wa amuna ndi akazi omwe anasonyeza chikhulupiriro cholimba.—Aheb. 11:32.
Werengani nkhaniyi m’Baibulo:
Funso lokambirana:
Kodi Gidiyoni anasonyeza kulimba mtima m’njira ziti?
Zoti Mufufuze
1. N’chifukwa chiyani tingati “mkate wa balere wozungulira” womwe msilikali wina analota, ndi chizindikiro chabwino choimira gulu lankhondo la Gidiyoni? (Ower. 7:13; it “Balere” ¶7-wcgr)
2. N’chifukwa chiyani Amidiyani anasokonezeka komanso kuchita mantha ndi kulira kwa nyanga za nkhosa 300? (it “Nyanga ya Nkhosa” ¶3-wcgr) A
Chithunzi A: Aisiraeli ankagwiritsa ntchito nyanga za nkhosa popereka chizindikiro
3. Kodi Gidiyoni ndi asilikali ake ankafunika kuchita chiyani kuti agonjetse Amidiyani? (w04 10/15 16 ¶9-10) B
Chithunzi B: Gidiyoni anathamangitsa Amidiyani mpaka ku Yogebeha, mtunda wa makilomita pafupifupi 80 (njira yeniyeni yomwe anadutsa sidziwika)
4. Kodi pali umboni wotani womwe umatsimikizira kuti nkhaniyi inachitikadi? (w05 4/15 32)
Zomwe Tikuphunzirapo
Ngakhale kuti Gidiyoni anathandiza anthu a Mulungu kuti apambane nkhondo, anakhalabe wodzichepetsa komanso ankalankhula ndi anthu ena mwamtendere. (Ower. 8:1-3) Kodi mitu ya mabanja komanso akulu angatsanzire bwanji Gidiyoni ngati munthu wina atakhumudwa ndi zochita zawo?
Ndi pa zochitika ziti pomwe tingafunike kuchita zinthu molimba mtima komanso mosamala? C
Chithunzi C
Mungatsanzire bwanji kulimba mtima kwa Gidiyoni?
Ganizirani Mfundo Yaikulu
Kodi nkhaniyi yandiphunzitsa chiyani za Yehova?
Kodi nkhaniyi ikugwirizana bwanji ndi cholinga cha Yehova?
Kodi ndingakonde kudzamufunsa chiyani Gidiyoni akadzaukitsidwa?
Phunzirani Zambiri
Kodi mungatsanzire bwanji Gidiyoni ngati mutapatsidwa mwayi wochita utumiki winawake?
“Nzeru Ili Ndi Odzichepetsa” (w00 8/1 16-18 ¶11-15-wcgr)
Gwiritsani ntchito zithunzi zofotokoza nkhani ya m’Baibulo pothandiza ana anu kuti azidalira Mulungu.