Kutsimikizira Kukhala “Achangu mu Ntchito Zokoma” mu Kenya
“ICHI ndi chimene ndakhala ndikufunafuna m’moyo wanga!” anafuula motero mwamuna wokhala ndi chiyambi cha Chihindu pambuyo pa kupezeka pa msonkhano waposachedwa wa Mboni za Yehova mu Kenya, Africa. “Ichi chiri china chake chapadera.”
Kodi nchiyani chimene chinamufulumiza iye kunena chimenecho? “Anthu amitundu yambiri, mayambidwe, ndi maiko—onse atakhala pamodzi mwaufulu ndi chikondi chowonekeratu kaamba ka wina ndi mnzake,” iye anatero. Koma kodi ndimotani mmene ichi chinakhalira chotheka m’dziko lodzaza ndi kusagwirizana ndi kunyada kwa utundu? Kodi nchiyani chimene chinatsogolera ku umodzi wotero ndi kugwirizana kwauzimu mu Kenya?
Apainiya Oyambirira Akonza Njira
Kubwerera mu 1931, Frank ndi Gray Smith anasambira kuchokera ku South Africa kupita ku Mombasa ndi makatoni 40 a mabuku. Kuchokera kumeneko iwo anapanga ulendo wotopetsa ndi wovuta kupita ku Nairobi, kumene anagawira mabuku awo onse chifupifupi mkati mwa mwezi. Onse anagwidwa ndi malungo, ndipo Frank anamwalira—wokhulupirika mpaka kumapeto. Pambuyo pake chaka chomwecho, Robert Nisbet ndi David Norman anatsatira paulendo wofananawo, kugawira makatoni 200 a zofalitsidwa mu East Africa. Chotero mbewu zoyambirira za chowonadi zinafesedwa mu Kenya. Kenaka mu 1935, Gray Smith ndi mkazi wake, limodzi ndi Robert Nisbet ndi mbale wake George, ananyamuka kutsatira chikondwerero chopezedwa. Nthawi imeneyi Robert anagwidwa ndi typhoid fever. Enawo anakanthidwa ndi malungo ndi blackwater fever. Chitsutso ndi kuthamangitsidwa kwa lamulo kochitidwa ndi boma la azungu zinawonjezera ku zovutazo. Mosasamala kanthu za zonse zimenezi, apainiya achangu oyambirira amenewa anagawira unyinji wochuluka wa mabuku, kuika maziko kaamba ka kukula. Mwachitsanzo, chifupifupi zaka 30 pambuyo pake, Mboni yogwira ntchito kudera la kumudzi mu Kenya inadabwitsidwa kupeza mwamuna yemwe anali ndi kope la bukhu la Reconciliation. Mbale wake anali atalipeza ilo mu 1935. Mwamuna ameneyu anapita patsogolo ndipo tsopano ali mmodzi wa Mboni za Yehova.
Kukula Kowonjezereka
Inali isanakwane 1949 pamene Mboni yoyambirira, Mary Whittington, anabwera kudzakhala mu Nairobi, likulu la Kenya. Iye anali atabatizidwa mu England kokha chaka chimodzi chapita. Iye anadziwa zochepa kwambiri za kukhala kutali, zitsenderezo, ndi chitsutso chomwe iye anayenera kuyang’anizana nacho. Komabe, iye anali ndi chimwemwe chakuwona ‘wamng’ono akusanduka chikwi.’ (Yesaya 60: 22) Lerolino, pa msinkhu wa zaka 73, iye akutumikirabe monga mpainiya wokhazikika.
Bill ndi Muriel Nisbet, omaliza maphunziro oyambirira a Sukulu ya Gileadi ya Baibulo ya Watchtower ogawiridwa ku Kenya, anafika mu 1956. Panthawiyo, kupatukana kwa mitundu kunali mkati, ndipo boma la azungu linali ndi malamulo omwe anaika malire ku ntchito yolalikira ndipo anaika malire ku ukulu wa misonkhano kukhala ndi opezekapo osaposera asanu ndi anayi. Chotero ntchito ya a Nisbet inamamatizidwa kokha ku munda wa azungu ndipo ndi kukambitsirana kwa mwamwawi ndi anthu a mu Africa. Mosasamala kanthu, kukula kunabwera.
Mu 1962 ntchito ya Mboni za Yehova inazindikiridwa mwalamulo. Mwamsanga pambuyo pake, mu 1963, ulamuliro wa azungu unatha, chotero kutsegula khomo kaamba ka kufutukuka kowonjezereka ku ntchito yathu ya Chikristu. Tsopano mabuku angasindikizidwe mu chinenero cha Chiswahili, ndipo akulu a Mboni za Yehova anavomerezedwa ndi boma kulembetsa maukwati awo. Kuyambira panthawi imeneyo, Mboni za Yehova zinakhala zida mkuthandiza chifupifupi mabanja 2, 000 kulembetsa maukwati awo mwalamulo.
Pofika mu 1972 ofesi ya nthambi yatsopano yabwino, moyenerera yokhala mu Nairobi, inaperekedwa. (Iyo kuyambira panthawi imeneyo inafutukulidwa. ) Kenya tsopano inali yokonzekeretsedwa bwino kuyang’anira ntchito ya Ufumu mu maiko khumi a ku East Africa pansi pa chisamaliro chake ndi kukwaniritsa chifuno kaamba ka zofalitsidwa mu zinenero zambiri za kumaloko.
Zitsanzo Zabwino za Changu
Olalikira a mbiri yabwino ya Ufumu mu Kenya anasonyeza ‘changu kaamba ka ntchito yabwino’ chofananacho chomwe chinazindikirika pakati pa Akristu a mu zana loyamba. (Tito 2:14) Iwo salola zitsenderezo kuwatsekereza iwo kukuthandiza ena kupeza chidziwitso cholongosoka cha Baibulo.
M’chochitika chimodzi, Mboni inalandira pempho kuchokera ku ofesi ya nthambi kukamufikira wokondwerera wa khungu, yemwe amakhala pa mtunda wa mamailosi 16 (26 km). Mboniyo mokhazikika inapanga ulendowo panjinga kukatsogoza phunziro la Baibulo ndi iye. Ngakhale kuti mwamuna ameneyo anapita pansi pa malingaliro otsutsa ndi kupsyinjika, tsopano ali Mboni iye mwini, mwachangu akuuza ena ponena za lonjezo la Mulungu la Paradaiso wobwezeretsedwa pamene ngakhale maso a akhungu adzatsegulidwa—Yesaya 35:5.
Mu madera ena kuyesetsa kwakukulu kunapangidwa kukapezeka pa misonkhano ya Chikristu. Mkazi wa zaka 70 zakubadwa mokhazikika amayenda chifupifupi ma mailosi asanu ndi imodzi (10 km) Kukapezekapo pa msonkhano wa mlungu ndi mlungu. Panjira, iye amapyola mu umodzi wa mitsinje yaikulu mu Kenya, ngakhale kuti ng’ona zimakhala zikubisala pafupi. Nthawi zina mafunde amakhala amphamvu kwambiri kotero kuti amakhala pafupi kumugwetsa iye. Komabe, iye amalingalira phwando lauzimu kukhala loyenerera kuyesetsako. Chiri chitsanzo chowonekera kwambiri chotani nanga cha changu!
Chitsanzo china chabwino cha changu ndi chiyamikiro chinaperekedwa ndi Mboni yomwe inayenda kwa maora asanu ndi anayi kukapezeka pa msonkhano wadera. Kodi ndi chifukwa ninji anachita choncho, ngakhale kuti iye anali ndi ndalama zokwanira kaamba ka kulipira basi? Wofulumizidwa ndi chikondi, iye anapereka ndalama zake kwa wophunzira Baibulo wake kotero kuti iye, nayenso, akasangalale ndi programu ya msonkhano! Inde, chikondi ndi ‘changu kaamba ka ntchito zokoma,’ chozikidwa pa chidziwitso cholongosoka cha Baibulo, zikuwonekera bwino mu Kenya.
Mzimu wa Upainiya
Changu chimenechi chakhala chikusonyezedwa mu utumiki waupainiya wanthawi zonse mu njira yowonekera. Ambiri apeza chimwemwe mu utumiki umenewu mosasamala kanthu za mikhalidwe yovuta. Mpainiya wokhazikika wachichepere amatumikira mu dera lotentha ndi la chinyezi pa mzinda wa pa doko wa Mombasa. Zaka zingapo zapita miyendo yake iwiri yonse inayenera kudulidwa ku chipatala chifukwa cha ngozi ya galimoto. Pamene iye anali m’chipatala, anafuna kudzipha yekha ndipo anapempha a namwino kumupatsa iye jekeseni yakupha, imene iye anakana kuchita tero. Pambuyo pa kutuluka, iye anapeza Mboni ndi kuyamba kuphunzira Baibulo ndi izo. Ichi chinatsogolera ku ubatizo wake ndi moyo watsopano mu utumiki wa nthawi zonse. Iye amasefukira ndi changu ndi chiyamikiro.
Unyinji waukulu wa amayi okhala ndi mathayo abanja akhalanso apainiya okhazikika. Pakati pa iwo pali mmodzi wokhala ndi ana atatu. Iye ali ndi kukwera kwa mwazi kokulira ndi vuto mkalankhulidwe. Iye amafunikira kugwira ntchito nthawi yonse, ndipo mwamuna wake si Mboni. Komabe, iye ali mpainiya wachimwemwe. Ngakhale kuli tero, si amayi okha amene amagawana mu utumiki wa upainiya wokhazikika; posachedwapa, tate yemwe ali ndi ana asanu ndi atatu oyenera kuwasamalira ndi ntchito yomwe imaphatikizamo kusinthana nthawi yogwira ntchito anatenganso mwawi wa utumiki umenewu.
Ambiri amene sali okhoza kukhala apainiya okhazikika amawala ndi mzimu waupainiya. Iwo amayang’ana kaamba ka mwawi wa kugawana mu utumiki wa nthawi zonse monga apainiya othandizira, mwakuwononga maora 60 mu ntchito yolalikira mwezi uliwonse.
Mu April 1984, ndiponso mu 1985, loposa gawo lachitatu la ofalitsa onse mu Kenya anatengamo mbali mu mtundu wina wake wa utumiki wa nthawi zonse. Mpingo umodzi unali ndi ofalitsa 73 omwe analembetsa monga apainiya othandizira mu mwezi umenewo, akumagwira ntchito limodzi ndi apainiya okhazikika asanu. Ziwalo zina 28 za mpingowo zinafika pa avereji ya maora 64. 6, ngakhale kuti ambiri a iwo anali osabatizidwa. Monga chotulukapo chake, chiwonkhetso cha maphunziro a Baibulo 233 anatsogozedwa!
Ukalamba nawonso sukutsimikizira kukhala choletsa. Gogo wa zaka 99 anatenga utumiki wa upainiya wothandizira. Mosasamala kanthu za zitsenderezo za kuthupi, iye amalola kuwala kwake kuunikira mopanda mantha kulinga kwa achichepere ndi achikulire. (Mateyu 5:16) Kupyolera mu zoyesayesa zake, unyinji wa ena athandizidwa kukhala olalikira a Ufumu ndipo mwachimwemwe amakumbukira kudzipereka ndi mzimu waupainiya wa gogo ameneyu. Inde, ‘changu chotero kaamba ka ntchito zokoma’ chatsogoza ambiri kukulitsa mzimu waupainiya.
Chitamando—Kuchokera Mkamwa mwa “Makanda”
Achichepere, nawonso, ngakhale sanabatizidwe, mwachimwemwe ndipo mofunitsitsa amatsagana ndi makolo awo m’kubweretsa mbiri yabwino kuchokera mu chowonadi cha Mulungu kwa anthu ena. (Mateyu 21:16) Mkati mwa ndawala yapadera, mtsikanawa zaka zinayi ndi theka anagwira ntchito limodzi ndi makolo ake mudera lakutali. Iye anawononga maora 160 muutumiki wa m’munda mwezi umenewo, kugawira mabuku 27, timabuku 66, ndi magazini 47 ndi anthu omwe anali okondweretsedwa mu Baibulo.
‘Changu chimenechi kaamba ka ntchito zokoma’ chimawonekera mu sukulunso. Mu dera la kumudzi kunja kwa Nairobi, mnyamata wopita ku sukulu loyambirira, amene mayi wake anali kuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova, anali wokhoza kuthandiza mphunzitsi wake kuyamba panjira ya ku moyo wosatha. Mkilasi, pamene mphunzitsi anabweretsa mutu wa moyo pambuyo pa imfa, mnyamata wachichepere ameneyu mwaulemu ananena kuti mayi wake anamphunzitsa china chake chosiyana, chozikidwa pa Baibulo. Ichi chinadzutsa chidwi cha mphunzitsiyo. Iye analankhulana ndi mayi wa m’nyamatayo, yemwe anamutsogoza iye kwa Mboni ya chidziwitso chokulira. Tsopano mphunzitsi iye mwiniyo akufalitsa chowonadi cha Baibulo kwa ena, zikomo ku changu cha wachichepere ameneyo. Chiri chitsanzo chabwino chotani nanga cha changu chimene chiri pakati pa ana Achikristu lerolino!
Kukula Kowonjezereka Kukuyembekezeredwa
Loposa theka la anthu a mu Kenya ayenera kumva mbiri yabwino ya Ufumu. Chifukwa cha mtunda, madera ena akutali angakwaniritsidwe kokha kamodzi pa chaka. Pamene mufika m’madera oterowo, chiri chofala kwa Mboni kupatsidwa moni ndi mawu awa: “Kodi munali kuti? Takhala tikukusowani.” Kenaka, pambuyo pa kuchitira umboni kumeneko kwa masiku ochepa kapena milungu ndipo nthawi ifika kuti muchoke, munthu amakhudzidwa kumva mawu ngati awa: “Tsopano mukufuna kutisiyanso kachiwiri? Kodi ndimotani mmene tikapitira patsogolo?” Mwachimwemwe, makonzedwe apangidwa kubwererako pa ambiri a awa amene “ali anjala” yauzimu.
Lerolino, muli aminisitala a Ufumu 3, 686 mu Kenya. Pa Chikumbutso cha imfa ya Kristu mu 1986, 13, 067 anapezekapo. Chimenecho chinali chifupifupi kuwirikiza nthawi zinayi chiwerengero cha Mboni! Anthu oledzera, andewu, atsogoleri amagulu, olanda, ndi okhulupirira mizimu akale, ndi ena apanga kusintha kokulira mu miyoyo yawo ndipo tsopano akuyenda mnjira za chowonadi. Kodi nchiyani chimene ichi chimatiuza ponena za mtsogolo?
Mwachiwonekere kukula kowonjezereka kuyenera kuyembekezeredwa. Inde, anthu mu Kenya akuvomereza mwachiyanjo ku “mbiri yabwino ya ufumu”. (Mateyu 24:14). Ambiri alowa mu mathayo a Mboni za Yehova—anthu “achangu kaamba ka ntchito zokoma.” Chifukwa cha ntchito izi, amaima powonekera monga anthu apadera, omasuka ku zitsenderezo za utundu ndi ziletso zina ku umodzi weniweni. Zowonadi, “ichi chiri china chake chapadera.”
[Mapu patsamba 28]
(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)
KENYA
Nairobi
Mombasa
[Chithunzi patsamba 29]
Zikwi za nthumwi zolankhula Chiswahili zinapezeka pa Msonkhano wa “Asungiliri Aumphumphu” mu December 1985
[Chithunzi patsamba 30]
Zitsanzo za Baibulo zoperekedwa mu Chiswahili ndi Chingelezi zinamangilira amvetseri
[Chithunzi patsamba 31
Ubatizo wapoyera unapereka chitsimikiziro cha dalitso la Yehova