‘Kuthandizidwa kumvetsetsa Winawake Amene Sindinaganizire nkomwe kuti Ndingathe’
Mu kalata yotsatirayi ku Watch Tower Society, munthu akulongosola kumene iye analandira thandizo loterolo.
“Okondedwa Bambo:
“Ndingakonde kukudziwitsani kuti ndimochuluka chotani mmene mabuku anu akundithandizira ine kumvetsetsa wina wake amene sindinaganizire nkomwe kuti ndingathe. Baibulo liri tsopano bukhu losangalatsa kwambiri lomwe sindinawerengepo ndi kale lonse chifukwa chathandizo limene mwandipatsa ine kudzera mu mabuku anu.
“Kodi munganditumizire chonde ndandanda ya mabuku onse amene mumafalitsa, ngati kuli kotheka?
“Yoikidwa mkatimu iri K20. 00 kaamba ka makope awiri a Reasoning From the Scriptures . . . Ndiyenera kugawira ‘mthandizi wamng’ono.’”
Tingakondenso kuti nanu mukhale nalo bukhu la Baibulo lokwana kuika m’manja la masamba 448 Reasoning From the Scriptures. Liri kokha K 10. 00.
Chonde tumizani, mutalipiliratu positi, bukhu la Baibulo lokwana kuika m’manja la chikuto cholimba Reasoning From the Scriptures (Chingelezi). Ndaikamo K10. 00.