Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w87 5/1 tsamba 3
  • Kodi Maulosi Onse Amachokera kwa Mulungu?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Maulosi Onse Amachokera kwa Mulungu?
  • Nsanja ya Olonda—1987
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Ulosi Nchiyani?
  • Kodi Nchiyani Chimene Chiri Chifuno Chaulosi?
    Nsanja ya Olonda—1987
  • Kodi Zili Nkanthu ndi Mmene Mumapembedzera?
    Nsanja ya Olonda—1994
  • Chifukwa Chimene Mungakhulupirire Ulosi wa Baibulo
    Nsanja ya Olonda—1999
  • Zipembedzo Zabodza Zimaphunzitsa Zinthu Zonama Zokhudza Mulungu
    Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale—Kuphunzira Baibulo Mokambirana
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1987
w87 5/1 tsamba 3

Kodi Maulosi Onse Amachokera kwa Mulungu?

“MULUNGU . . . ayenera kuganiziridwa kukhala wamkulu kwambiri ndi wa chilengedwe chonse kudzibindikiritsa Iyemwini ku chipembedzo chimodzi chokha, njira imodzi kapena pa icho, mtundu umodzi wokha.” Analemba motero wa nthanthi mu The Guardian nyuzipepala ya ku Nigeria. Iye anakhulupirira kuti zipembedzo za miyambo za chiAfrica zinavumbulutsidwa ndi Mulungu kaamba ka khalidwe la mu Africa ndipo kuti zipembedzo zina zazikulu zinapangidwa kugwirizana ndi mikhalidwe ya kumaloko.

Anthu okhulupirira miyambo amawona Chikristu monga chipembedzo cha azungu ndipo kuwona amatsenga a miyambo monga nthumwi zenizeni za ulosi. Kalata yolemberedwa ku Nigerian Daily Times inati: “Mulungu Wamphamvuyonse amadziwonetsera iye mwini panthawi zosiyanasiyana kwa anthu osiyanasiyana. . . Anthu anzeru amudziko amang’ung’udzang’ung’udza kuti Wamphamvuyonse tsopano akudziwonetsera mu Africa.” Ena akuyembekezera kaamba ka mneneri wa chiAfrica, wofanana ndi Yesu ndipo, ena amati, Muhammad.

Malingaliro awa amadzutsa mafunso monga awa: “Kodi maulosi onse amachokera kwa Mulungu? Kodi iye anavumbula zikhulupiriro zosiyanasiyana zachipembedzo zimene zimagawanitsa dziko? Kodi iye ali ndi zifuno zachipembedzo zosiyanasiyana kaamba ka mafuko osiyanasiyana? Kapena kodi pali aneneri owona ndi abodza, ndi zipembedzo zowona ndi zonyenga? Kodi nchiyani kwenikweni chimene chiri ulosi wowona, ndipo kodi nchiyani chimene chiri chifuno chake?

Kodi Ulosi Nchiyani?

Webster’s New Collegiate Dictionary ikulongosola ulosi monga “chilengezo chouziridwa cha chifuno cha umulungu 2: mawu ouziridwa mneneri 3: choneneratu cha chinthu chirinkudza.” Ichi chimapereka lingaliro lakuti pangakhale magwero osiyanasiyana a maulosi.

Mkuchinjiriza zipembedzo za miyambo, profesara wa ku yuniversite ya maphunziro a chipembedzo, E. Bolaji Idowu, akulankhula za “ganizo la Mulungu wa mbali zambiri la mu Africa.” Bukhu lake African Traditional Religion likulongosola kuti ichi “nthawi zambiri chimatenga chigogomezero chake ndi kuwonekera kuchokera ku khalidwe lachibadwa ndi kukula kwa anthu ndi nyengo.” Mwachitsanzo, iye akuti “pamene ku mbali zambiri za mu Africa, Mulungu amakhulupiriridwa kukhala wamwamuna kuli malo [makamaka ku malo amene ’amalemekeza akazi] kumene iye amalingariridwa kukhala wamkazi.” Kodi malingaliro a ku malo amodzi oterowo ndi owombana angakhale ouziridwa ndi Mulungu? Profesara Idowu akuvomereza kuti “palibe chiri chonse chingaletsa . . . fuko . . . liri lonse mu Africa kuchokera ku kupanga lingaliro laumwini la Mulungu.” Ichi chimasonyeza kuti maganizo a chipembedzo oterowo amachokera mu malingaliro a anthu ndi kawonedwe osati chivumbulutso cha umulungu.​—Yerekezani ndi Aroma 1:19-23.

Alauli a mwambo ndi oombeza maula samavumbula umunthu ndi zifuno za Mulungu wowona. Iwo amachita ndi zinthu zopatsidwa kwa mizimu ndi kuchita nsembe zofunidwa ndi “milungu” yawo yosiyanasiyana. Zoneneratu zawo ziri zozikidwa pa nzeru ya kuombeza ndi ulauli. Chotero, maulosi oterowo sali zilengezo zouziridwa za chifuno cha umulungu. Mulungu Wamphamvuyonse, amene anauzira ulosi wowona, sali magwero awo.​—2 Petro 1: 20, 21; Deuteronomo 13:1-5; 18:20-22.

Chotero, kodi nchiyani, chimene chiri magwero a zoneneratu zoterozo? Chonde werengani nkhani yotsatirapo kaamba ka mayankho ku mafunso awa ndi mafunso ena amene anadzutsidwa poyambirira m’kukambitsiranaku.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena