Kodi Nchiyani Chimene Mulungu Wachita Kaamba ka Inu?
‘PALIBE CHIRICHONSE!’ ena angayankhe. ‘Ndimayenera kugwira ntchito molimbika ndi kudziyang’anira ine mwini.’ Ngati mmenemo ndi mmene mumamverera, tangowunikirani kwa kamphindi. Kodi inu munakhalako bwanji?
Miyezi ina isanu ndi inayi musanabadwe, zinthu ziwiri zazing’ono kwambiri zinakumana mkati mwa amayi wanu. Pamodzi izo zinapanga chinthu chatsopano, chinthu chapadera.
Chachikulu cha zinthu ziwiri zimenezo chinali dzira, lomwe linaperekedwa ndi amayi wanu. Chochepera cha zinthu zimenezi chinali ubwamuna wochokera kwa atate wanu—tating’ono kwambiri kotero kuti, malinga ndi kunena kwa bukhu la Sheila Kitzinger The Experience of Childbirth, ngati ubwamuna wonse umene unatulutsa anthu onse mu dziko lapansi ukanakhazikitsidwa kumbali ndi kumbali, iwo “ukanakwanira kuikidwa pa lochepera ndi inchi imodzi [2. 5 cm]” Koma pamene ubwamuna wa atate wanu unalowerera dzira la amayi wanu, lamulo la majini anu linakhazikitsidwa ndipo munakhalako!
Zochitika zocholowanacholowana za kukula zinayamba. Izo zinali “zocholowana kotero kuti, pambuyo pa loposa zana limodzi la kufufuzafufuza, asayansi saali okhoza kuzimvetsetsa izo,” analemba motero Andrea Dorfman mu Science Digest.
Monga chitsanzo cha njira ya kukula yomwe imazizwitsa asayansi, wolemba m’modzimodziyo akuchitira ndemanga: “Kuletsa kukula iri nkhani ina yocholowanacholowana mofananamo. Mkono wa kumanzere ndi wa kumanja, mwachitsanzo, imayamba kuchokera ku timphukira tosiyana tathupi tautali wa milimita imodzi, koma pomalizira pake imakhala ya utali wofanana. Kodi ndimotani mmene maselo amadziwira ndi liti pamene ayenera kuleka kuchulukitsidwa? . . . Chiwalo chirichonse chimawoneka kukhala chiri ndi kuthekera kwa mkatikati kwa kuletsa kukula.” Kodi sitiri achimwemwe kuti ichi chiri tero?
Kodi nchiyani chimene chimapangitsa ndi kuletsa kukula mu zinthu za moyo zonse? Kodi iri mphamvu yopanda malingaliro yotchedwa chibadwa? Kodi uli mchitidwe wa kulasa ndi kuphonya wotchedwa chisinthiko? Kodi icho sichiri chodziwikiratu kuti kucholowanacholowana kodabwitsa kosiyana mochititsa chidwi, ndipo kokongola kwambiri kwa mitundu ya moyo pa pulaneti ino yosangalatsa kungakhale kokha ntchito ya Mlengi wamphamvuyonse? Pamene icho chiri tero, kodi ife sitiyenera kudzimva mozama oyamikira kaamba ka zimene iye wachita kaamba ka ife?
Chitsimikiziro Chonka Muyayacha Zozizwitsa za Chilengedwe
Tsiku lirilonse—ngakhale ora lirilonse—timapindula kuchokera ku zozizwitsa za chilengedwe. Mwachitsanzo, kodi nchiyani chimene chimachitika pamene tigona? Ntchito za malingaliro ndi thupi mwa izo zokha zimacheperako. Ichi sichiri kaamba ka kuthekera kwathu, popeza kaŵirikaŵiri timagona popanda kuzindikira icho. Ndipo tulo tabwino tiri totsitsimula chotani nanga! Ena angathe kukhala kwa milungu popanda kudya koma awo amene amakhala masiku atatu popanda kugona amakhala ndi vuto mu kulingalira, kuwona, ndi kumva.
Pambuyo pakugalamuka m’mawa, mwinamwake winawake amakubweretserani inu khofi yotsekemera. Shuga, imene poyambirira inali yosowa ndi yodula, iripo tsopano yochuluka kwambiri kotero kuti kaŵirikaŵiri sitilingalira za icho. Koma kodi ndimotani mmene imapangidwira? Iyo imapangidwa mu mitengo kupyolera mwa fotosinfesisi—kugwirizana kwa kuwala kwa dzuwa ndi madzi ndi mpweya umene timatulutsa mu thupi lathu. Panthawi imodzimodziyo mpweya umene timapuma kulowetsa mu thupi lathu, wofunika kwambiri kaamba ka zolengedwa zonse za moyo pa dziko lapansi, umatulutsidwa. Fotosinfesisi ndi kachitidwe kocholowana kwambiri komwe sikanamvetsetsedwe kwenikweni ndi asayansi. “Ndimotani . . . mmene fotosinfesisi iyo yeni imafikidwira?” Linafunsa bukhu lakuti The Plants. (Life Nature Library) “Kumeneku kuli monga kufunsa ndimotani mmene moyo unayambira —ife sitidziwa chabe.”
Mwinamwake pamene mukumwa khofi wanu, mumakumbukira programu ya pa kanema ya wailesi ya usiku wapita. Mu diso lanu la maganizo mungawone zochitika zosangalatsa zimenezo kachiwirinso. Kodi ndimotani mmene zinafikitsidwira ku bongo wanu, kusungidwa kumeneko monga mpukutu wa mafilimu, kenaka ndi kuseweredwanso kotero kuti mungathe kulongosola izo kwa ena? Nzozizwitsa, kodi sitero? Kodi ndimotani mmene munthu anapezera nzeru ya kuchita zinthu zodabwitsa zimene iye amakwaniritsa? Mwachidziwikire osati kuchokera kwa zinyama. Kodi bongo wa munthu suuli wochititsa mantha kwenikweni?
Tsiku silinayambe kwenikweni. Koma kodi tiri ndi zochuluka zotani zomwe tingathe kuyamikirira Mlengi kaamba ka izo! Koma pali zina zowonjezereka.