Wokhalako Wamkulukulu Ali Wapadera
WOKHALAKO WAMKULUKULU. Kodi mumakhulupirira iye? Mosasamala kanthu za kufalikira kwa kuchoka mu matchalitchi mu maiko ambiri mamiliyoni amakhulupirirabe mwa Wokhalako wokoma mtima wamphamvu zonse kwa amene iwo angatembenukireko, makamaka pamene iwo ali mu nsautso.
Mwachitsanzo, mu Africa muli zipembedzo zambiri za kumaloko, za miyambo zomwe zimasiyana mokulira kuchokera ku china ndi chinzake ndi omwe amalambira milungu ya maina ambiri. Koma, anthu ambiriwo mwamphamvu amakhulupirira mwa Wokhalako Wamkulukulu yemwe ali “wapadera” ndi “wolamulira wotheratu wa chilengedwe chonse.”
Monga momwe chasimbidwira mu bukhu la Dr. Peter Becker Tribe to Township, mlaliki wosadziwa kwenikweni wa chikulire wa Chisotho wa mu South Africa ananena kuti: “Atate anga achikulire ndi atate awo . . . anadziwa ponena za Mulungu, Molimo, kale kwambiri asanabwere amishonale, Mulungu Wokhalako Wamkulukulu yemwe analenga zinthu zonse . . . Kodi chimaphula kanthu chimene ife [a Basuto] timatcha Mulungu, Molimo, a Zulu, Nkulunkulu, a Xhosa, Thixo . . . ?”
Komabe, kuchuluka kwa maina kuli kosokoneza. Mwachiwonekere mungavomereze kuti Mulungu wachilengedwe chonse ayenera kukhala mmodzi yemweyo kwa anthu onse ndipo ayenera kukhala ndi dzina la chilengedwe chonse. Zolembedwa zakale zouziridwa zosonkhanitsidwa, Baibulo, limalemekezedwa kuzungulira dziko. Ilo limalalikira: “Kuti adziwe kuti inu nokha, dzina lanu ndinu Yehova, Ndinu Wam’mwambamwamba padziko lonse lapansi.”(Masalmo 83:18) Chotero, malinga ndi Baibulo, Wokhalako Wamkulukulu ali ndi dzina lapadera.
Kodi Mulungu mmodzi Wokhalako, ameneyu ali wa mtunduwanji monga kwavumbulutsidwa ndi Baibulo? “Njira zake zonse ndi chiweruzo”; “Mulungu wachifundo ndi wachisomo, wolekereza, ndi wa ukoma mtima wochuluka, ndi wachowonadi”; “ali wodzala chikondi, ndi wachifundo”; “sali Mulungu wa chisokonezo koma wa mtendere”; “Mulungu ndiye chikondi.”—Deutronomo 32:4; Eksodo 34:6; Yakobo 5:11; 1 Akorinto 14:33; 1 Yohane 4:8.
Baibulo limavumbulutsanso kuti Yehova ali iye yekha amene ayenera kulambiridwa. Inde, pokhala wapadera, iye moyenerera amafuna kulambiridwa kotheratu. (Eksodo 20:5) Yesu Kristu anati: “[Yehova, NW] Mulungu wako udzamugwadira, ndipo iye yekha udzamulambira.”—Mateyu 4:10.
Mosasamala kanthu za chimenechi, anthu a Chiafrica ambiri, pamene amadzinenera kukhulupirira mwa Wokhalako Wamkulukulu, amalambira milungu yambiri. Kodi chimenecho sichidzawoneka kwa inu chopereka lingaliro losokoneza ponena za chizindikiro kapena mtundu waMulungu? Koma ngakhale mbali zambiri za dziko la Chipembedzo munthu womvekera bwino, wamphamvu wa Mulungu amaphimbidwa mwa kumulingalira iye kukhala Mulungu wa mbali zitatu. Mungakhale munamvapo za chimenechi kukhala Utatu Wopatulika, chiphunzitso chomwe chiri cha chinsinsi ndi chovuta kuchimvetsetsa. Mwachitsanzo, kabukhu kakuti The Blessed Trinity kamanena kuti: “Chiphunzitso cha Utatu Wodalitsidwa . . . chiri cha chinsinsi . . . Sichingatsimikiziridwe ndi chifukwa . . . Sichingatsimikiziridwe nkomwe kukhala chothekera.”a(Kanyenye ngwawo) kabukhuko kamawonjezera: “Chitsimikiziro, chotero, cha chinsinsi chimaphatikizapo kusonyeza kuti chinasungidwa muvumbulutso, mu Malemba Oyera.”
Koma kodi Malemba Oyera kwenikwenidi amaphunzitsa chiphunzitso chimenechi? Kodi Wokhalako Wamkulukuluyo ali anthu atatu mwa Mulungu mmodzi
[Mawu a M’munsi]
a Kofalitsidwa ndi Catholic Truth Society of London