Kodi Ndani Amene Ali Alengezi Owona?
MOSASAMALA KANTHU za kumene mumakhala, m’njira ina kapena inzake ntchito yolengeza yoyambidwa ndi Yesu Kristu yakhudza moyo wanu. Koma si aliyense amene anadzinenera kukhala woimira Kristu anafalitsa uthenga wowona wa Mawu a Mulungu. Si alengezi onse—aposachedwapa kapena a kale—amene anali ndi chisonkhezero kaamba ka changu cha umishonale chofananacho chomwe chinazindikiritsa ophunzira a Kristu a m’zana loyamba.
Zowona, matchalitchi a Chikristu cha Dziko ali ndi chiyerekezo cha amishonale 220,000 omwe akugwira ntchito m’dziko lerolino, koma kodi amishonale amenewo amapambana chiyeso cha alengezi owona? Kulengeza Kwachikristu sikunatanthauzidwe kukhala mtundu wa ulamuliro wauzimu, kumene olalikira akagwira ntchito monga athenga ogwirizanitsa mphamvu za dziko. (Yerekezani ndi Yakobo 4:4.) Ndiponso, kulengeza kwa Akristu owona sikungapititse patsogolo chotchedwa nthanthi yaufulu ndi kusonkhezera kaamba ka masinthidwe oipa m’dongosolo la kachitidwe ka zinthu ka ndale ndi mayanjano; ndiponso Yesu analibe m’maganizo alaliki otchukitsa Baibulo mwa kugwiritsira ntchito ziwiya za magetsi omwe amafuula uthenga wawo wa “nthanthi ya kupita patsogolo” pa zowulutsira mawu za TV ndi wailesi. (Yohane 17:16; Mateyu 6:24) Chabwino, chotero, kodi mlengezi nchiyani?
Nchiyani Chimene Chiri Kulengeza Kowona?
Mu zinenero zoyambirira za Baibulo, Chihebri ndi Chigriki, mlengezi anali wolengeza wa uthenga wabwino, kapena mbiri yabwino.a Mbiri yabwino ya chiyani? Ya chipulumutso, ya ulamuliro wolungama ndi ya mtendere. Mwachitsanzo, Yesaya 52:7 amanena kuti: “Ha, akongolatu pamapiri mapazi a iye amene adza ndi uthenga wabwino, amene abukitsa mtendere, amene adza ndi uthenga wabwino wa zinthu zabwino, amene abukitsa chipulumutso; amene ati kwa Ziyoni: ‘Mulungu wako ndi mfumu!’”
Kuwonjezerapo, pa kubadwa kwa Mwana wa Mulungu, mngelo analengeza kwa abusa kuti: “Musawope, pakuti onani! Ndikuuzani inu uthenga wabwino wa chikondwero chachikulu, chimene chidzakhala kwa anthu onse. Pakuti wakubadwirani inu lero, m’mudzi wa Davide, Mpulumutsi, amene ali Kristu Ambuye.” (Luka 2:10, 11) Chotero, mbiri yabwino inazikidwa pa Yesu Kristu.
Zaka zina 30 pambuyo pake, Yesu analowa m’sunagoge m’mzinda wa Nazarete pa Sabata ndi kuimirira kuti aŵerenge. “Ndipo anapereka kwa iye bukhu la Yesaya mneneri. Ndipo mmene adafunyulula bukhulo, anapeza pomwe panalembedwa: ‘Mzimu wa Yehova, uli pa ine, chifukwa iye anandidzoza kuti [ndilengeze mbiri yabwino kwa osauka, NW.]’” Pambuyo pa kumaliza kuŵerenga, “iye anapinda bukhulo, nalipereka kwa mnyamata, nakhala pansi; ndipo maso awo a anthu onse m’sunagogemo anamyang’anitsa iye. Ndipo anayamba kunena kwa iwo, kuti: ‘Lero lemba iri lakwaniritsidwa m’makutu mwanu.’” Yesu anali movomerezeka mlaliki wa mbiri yabwino, ndipo mbiri yabwino imene iye analalikira inazikidwa pa “ufumu wa Mulungu.”—Luka 4:17-21; 8:1.
Yesu anayerekeza ntchito yake yolengeza ndi kututa ndipo ananena kuti “zotuta zichulukadi koma antchito ali oŵerengeka.” (Mateyu 9:36-38) Chotero, anaphunzitsa ndi kulamulira atsatiri ake kukhalanso alengezi. (Mateyu mutu 10; Luka mutu 10) Monga mmene chinaliri ndi Mphunzitsi wawo, maziko a kulalikira kwawo unali “ufumu wa kumwamba.” (Mateyu 10:7) Komabe, kulalikira Ufumu sikunali kokha ndi malire kwa atumwi a Yesu.
Pamene chizunzo motsutsana ndi mpingo Wachikristu womakula chinabwera m’mzinda wa Yerusalemu, mbiri ya mbiri yakale pa Machitidwe 8:1 inasonyeza kuti “ndipo anabalalitsidwa onse m’maiko a Yudeya ndi Samariya, koma osati atumwi ayi.” Kodi ophunzira obalalitsidwawo anabisala ndi mantha? Ayi, popeza versi 4 likupitiriza kuti: “Pamenepo ndipo iwo akubalalitsidwa anapitapita nalalikira mawuwo.” Mwanjira imeneyi zotuta zambiri zinatutidwa ndi alengezi a m’zana loyamba amenewo.
Mosangalatsa, bukhu la A Theological Word Book of the Bible linanena kuti: “Mu CC [Chipangano Chatsopano] kulalikira kulibe chirichonse chochita ndi kupereka kwa mauthenga kwa anthu otembenuzidwa, kumene kuli chimene kaŵirikaŵiri chimatanthauza lerolino, koma nthaŵi zonse kumakhudza kulalikira kwa ‘uthenga wabwino wa Mulungu’ kwa dziko losakhala la Chikristu.” Chotero, alengezi onse Achikristu, ndi kulengeza kwawo sikuli ndi malire ku kulankhula kwa akhulupiriri anzawo.
Koma nchiyani chimene chiri mutu wa kulengeza kwamakono? Yesu ananeneratu kaamba ka tsiku lathu kuti “mbiri yabwino ya ufumu idzalalikidwa m’dziko lonse lapansi lokhalidwa ndi anthu kaamba ka umboni kwa mitundu yonse; ndipo pomwepo mapeto adzafika.” (Mateyu 24:14, NW) Ndipo Yesu analamulira osati kokha kwa awo amene anawona kukwera kwake kumwamba komanso atsatiri ake a mtsogolo kukhalanso “mboni za [iye] ponse paŵiri m’Yerusalemu ndi m’Yudeya monse ndi m’Samariya ndi ku malekezero ake a dziko lapansi.”—Machitidwe 1:8; onaninso Mateyu 28:19, 20.
Chotero, maziko a uthenga wa mlengezi ali mbiri yabwino ya Ufumu wa Yehova Mulungu m’manja mwa Wolamulira wake woikidwa, Yesu Kristu, Kalonga wa Mtendere. (Yesaya 9:6) Ndipo chimaphatikizapo chowonadi chonse chimene Yesu analankhula ndi chimene ophunzira ake analemba. Alengezi owona lerolino mokhulupirika amamamatira ku mutu umodzi umenewu.
Ndani Amachirikiza Kulengeza Kowona?
Alengezi owona amalambira Yehova monga Mulungu. Iye ali Mlengezi Wamkulu; iye ali Mchirikizi wa kulalikira mbiri yabwino. (Agalatiya 3:8; Chivumbulutso 10:7) Ndipo iye amakhumba kuti anthu onse kulikonse amve ndi kumvera uthenga wake. “Zowona ndizindikira kuti Mulungu alibe tsankhu,” analengeza motero mtumwi Petro ku khamu laling’ono pa doko laling’ono la Mediterranean ya ku Kaisareya. “Koma m’mitundu yonse, wakumuwopa Iye ndi wakuchita chilungamo alandiridwa naye. Mawu amene anatumiza kwa ana a Israyeli, akulalikira uthenga wabwino wa mtendere mwa Yesu Kristu: [Uyu] ndiye Ambuye wa onse.”—Machitidwe 10:34-36.
Baibulo linaneneratu kuti m’tsiku lathu alengezi adzatutanso zotuta zambiri. (Chivumbulutso 14:15, 16) Ŵerengani m’nkhani yotsatira zina za zokumana nazo zimene Mboni za Yehova zikukhala nazo pamene zikutengako mbali mu ntchito yotuta imeneyi. Santhulani mbiri yawo yolalikira pa masamba 12 mpaka 15 a magazini iyi. Kenaka lankhulani ndi Mboni za Yehova pamene ziitanira pa nyumba yanu ndi kuwona ngati simudzavomereza kuti izo ziri alengezi owona a lerolino.
[Mawu a M’munsi]
a Verebu la Chigriki kaamba ka “kubweretsa mbiri yabwino,” kapena “kulengeza,” (eu·ag·ge·liʹzo·mai) limabwera kuchokera kukaimidwe ka liwu la Chihebri lotchulidwa ‘kubweretsa mbiri yabwino’ (bis·sarʹ) mu Yesaya 52:7. Verebu lakuti bis·sarʹ pano limatanthauza “kubukitsa chipambano cha chilengedwe chonse cha Yahweh padziko lapansi ndi ulamuliro wake wa ufumu” ndi kubadwa kwa mbadwo watsopano, imanena tero The New International Dictionary of New Testament Theology.—Yerekezani ndi Nahumu 1:15, New World Translation of the Holy Scriptures—With References, mawu a m’munsi.