Mapemphero Amene Amayankhidwa
CHIKHUMBO cha kulankhula ndi mphamvu ina yapamwamba chiri chakale monga munthu iyemwini. Mwachitsanzo, zosemasema zina zakale za Chiigupto ziri ndi mapemphero. Zina za izi zinapempha chitetezero chochokera kwa mulungu, pamene zinazo zinali ndemanga za chitamando kapena chidaliro mwa mulungu wolankhulidwapoyo. Pakati pa Agriki a m’zana lachisanu ndi chitatu B.C.E., nyimbo limodzinso ndi ndakatulo ndi mapemphero a chikumbukiro anali ofala. M’mapemphero a Chiroma, chisamaliro chinafunikira m’kufikira mulungu wakutiwakuti, popeza milungu yambiri inali kulambiridwa panthaŵiyo.
Kufikira ku tsiku lino, pemphero liri mbali yofala ya zipembedzo zazikulu zadziko. Odziŵika kwambiri kaamba ka kugwiritsira ntchito kwawo kobwerezabwereza kwa pemphero ali Abuddha, Ahindu, Ayuda, Asilamu, ndi awo odzinenera kukhala Akristu. Ngakhale kuti kugwiritsira ntchito pemphero kuli kofala m’zipembedzo za zana la 20, mitundu yosiyanasiyana ya njira ndi mkhalidwe wa pemphero zimapangitsa kuzizwitsa kwa ambiri ofuna kukhala ndi mapemphero awo atayankhidwa.
Kodi Pemphero Lirilonse Lingagwire Ntchito?
Popeza kupemphera kumatenga mitundu yosiyasiyana, kodi pemphero lirilonse lingakhale lokhutiritsa? Ena amadzimva kuti malinga ngati munthu yemwe akupemphera ali wowona mtima ndipo “amakhulupirira,” zilibe kanthu ndi mtundu uti wa pemphero umene wagwiritsiridwa ntchito. Nchiyani chimene mukulingalira? M’chiyang’aniro cha kusiyana kwa cholinga pa nkhaniyi, chiri chofunika kupyola malingaliro a anthu ndi kuyang’ana kaamba ka chidziŵitso chovumbulidwa kuchokera ku magwero apamwamba.
Mayankho a patsamba lotsatirawa anapezedwa kuchokera ku magwero amenewo, Baibulo Loyera. Limasonyeza kuti si pemphero lirilonse limene lingagwire ntchito ngati munthu akuyembekezera kuti pemphero lake limvedwe ndi kuyankhidwa.
Baibulo limalongosola:
Kwa amene mapemphero ayenera kuperekedwa
Chifukwa chimene mapemphero ena sayankhidwa
Chimene chingapemphedwe m’pemphero
Kodi ndi mbali yotani imene munthu wopereka pempheroyo amaichita?
Chofunika chachikulu ndi chikhulupiriro, osati chabe kukhulupirira kowona kwakuti Mulungu alipo ndipo kuti angamve mapemphero. (Ahebri 11:6) Chikhulupiriro choterocho chimasonyezedwa m’kukalamira kukhala m’chigwirizano ndi malamulo olungama a Mulungu okhazikitsidwa m’Baibulo. Mu Ulaliki wake wa pa Phiri, Yesu Kristu anagogomezera nsongayi: “Si yense wakunena kwa ine ‘Ambuye, Ambuye’ adzalowa mu Ufumu wa kumwamba, koma kokha awo akuchita chimene Atate wanga wa kumwamba afuna iwo kuchita.”—Mateyu 7:21, Today’s English Version.
Monga chitsanzo cha awo amene mapemphero awo sangamvedwe, mneneri wa Chihebri Yesaya analemba kuti: “Pochulukitsa mapemphero anu ine sindidzamva; manja anu adzala mwazi.” (Yesaya 1:15) Chotero alionse amene salemekeza kupatulika kwa moyo sangayembekezere mapemphero awo kumvedwa, mosasamala kanthu kuti ndi mobwerezabwereza chotani ndipo mowonetsetsa chotani mmene iwo amapempherera.
Nchifukwa ninji “okhulupirira” ena kaŵirikaŵiri sapeza mayankho ku mapemphero awo?
Kukhulupirira kokha sikuli kokwanira kusangalatsa Mulungu ndi kuti iye ayankhe mapemphero athu. Ngakhale munthu wokhulupirira zirizonse angadzinenere kuti iye amakhulupirira. Chikhulupiriro kuti chikhale ndi phindu, chiyenera kuzikidwa pa chidziŵitso cholongosoka, chomwe chingapezedwe kokha mwa kuphunzira Baibulo. M’kuwonjezerapo, kukhulupirira ndi chikhulupiriro ziyenera kutsimikiziridwa ndi ntchito zimene zimatulutsa. “Pakuti monga thupi lopanda mzimu liri lakufa, koteronso chikhulupiriro chopanda ntchito chiri chakufa.”—Yakobo 2:26.
M’khulupiriri wowona amafunikira kuŵerengera Mulungu m’zochita za tsiku ndi tsiku, osati kupita kupemphero kokha pamene ayang’anizana ndi ngozi. Iye adzafunanso kuchita ntchito zokhulupirika, ntchito zabwino zomwe zimaphatikizapo kulankhula ndi ena ponena za chikhulupiriro chake ndi kukhulupirira kwake mwa Mulungu.
Ndi mtundu wanji umene pemphero liyenera kutenga?
Pemphero siliyenera kukhala chabe mwambo, ndiponso silifunikira kuŵerengedwa kuchokera m’bukhu, ndiponso pemphero siliyenera kukhala ndi mawu obwerezabwereza ngati kuti kubwereza kumapangitsa ilo kukhala lokhutiritsa kwambiri. Ndipo pemphero siliyenera “kuchitidwa” kaamba ka kusonyeza kapena kusangalatsa ena. Yesu anapereka uphungu wabwinowu ponena za mtundu umene mapemphero athu ayenera kutenga ndi zimene tiyenera kupewa: “Pamene mupemphera, musakhale monga onyengawo; chifukwa iwo akonda kuimirira ndi kupemphera m’masunagoge, ndi pa mphambano za makwalala, kuti awonekere kwa anthu. . . . Ndipo popemphera musabwerezebwereze chabe iyayi, monga amachita anthu akunja, chifukwa ayesa kuti adzamvedwa ndi kulankhula lankhula kwawo.”—Mateyu 6:5-7.
Palibe mkhalidwe wapadera wa thupi umene walongosoledwa kaamba ka mapemphero kuti amvedwe. Komabe, mmodzi amene akupempherayo adzafunikira kukhala wodzichepetsa ndi waulemu ponse mumkhalidwe ndi m’mawu ogwiritsiridwa ntchito m’pemphero lake.
Ndi kwandani kumene mapemphero ayenera kuperekedwa?
Bukhu la Baibulo la Ahebri limalankhula za munthu amene “amafikira Mulungu.” (Ahebri 11:6) Ndi ndani amene ali Mulungu ameneyu? Pali kokha Mulungu mmodzi wamphamvuyonse, ngakhale kuti pali yambiri yopangidwa ndi anthu ndi milungu yonyenga. (1 Akorinto 8:5, 6) Mulungu wamphamvuyonse wa Baibulo amatchedwa Yehova. (Masalmo 83:18) Iye ali Mlengi wa zinthu zonse, ndipo kaamba ka chifukwa ichi pemphero liyenera kulunjikitsidwa kokha kwa iye. Yesu Kristu momvekera bwino anaphunzitsa otsatira ake kupemphera kuti: “Atate wathu wa kumwamba.” (Mateyu 6:9) Ayi, Yesu sanaphunzitse ophunzira ake kupemphera kwa iye, kwa amayi wake Mariya, kapena kwa munthu wina aliyense. Koma Mulungu tsopano amafuna kuti tizindikire malo a Mwana wake ndi kupereka mapemphero athu onse m’dzina la Yesu. Chimenecho ndicho chifukwa chake Kristu anauza otsatira ake: “Palibe munthu adza kwa Atate koma mwa ine.”—Yohane 14:6.
Mapemphero kuti akhale olandirika kwa Mulungu, chotero, iwo ayenera kulunjikitsidwa kwa Yehova Mulungu kupyolera mwa Mwana wake, Yesu Kristu. Uko ndiko kuti, iwo ayenera kunenedwa kwa Mulungu m’dzina la Yesu.
Nchiyani chimene chingapemphedwe m’mapemphero?
“Ngati tipempha kanthu monga mwachifuniro chake [Mulungu] atimvera.” Chitsimikiziro chowoneka chodabwitsa chimenechi chinalembedwa pa 1 Yohane 5:14. Koma kodi mwazindikira mawu akuti—“monga mwa chifuniro chake”? Inde, chifukwa choyamba chenicheni chimene mapemphero ambiri sayankhidwira chiri chakuti munthu wopempherayo sanayambe wayesera kupeza chimene chiri chifuniro cha Mulungu.—Miyambo 3:5-7.
Monga chitsogozo chothandiza kapena chitsanzo, Yesu anapatsa ophunzira ake pemphero lodziŵika mofala lerolino monga “Pemphero la Ambuye.” (Mateyu 6:9-13) Ngakhale kuti ilo siliyenera kunenedwa monga mwambo, ilo limakhazikitsa zoyambirira zoyenerera. Choyamba limabwera dzina la Mulungu ndi chifuno. Kenaka zosowa zakuthupi zandandalitsidwa, kukhululukira, ndi chipulumutso kuchokera ku mayeso a woipayo. Mawu akuti “Atate wathu” angathandize munthu wopempherayo kufutukula mapemphero ake ndi malingaliro ake kuphatikizapo osati kokha ziwalo za banja ndi achibale komanso ena omwe akufunafuna kusangalatsa Mpangi wawo.—Machitidwe 17:26, 27.
Kodi mapemphero ayenera kukhala autali wotani?
Baibulo silimakhazikitsa utali wachindunji kaamba ka mapemphero. Iwo angakhale achidule kwambiri kapena angaperekedwe mwachinsinsi. (Nehemiya 2:4; 1 Samueli 1:12, 13) Kumbali ina, mapemphero angakhale a atali. Panali chochitika pamene Yesu “anachezera m’pemphero kwa Mulungu.” Ichi mwachiwonekere chinali m’kupempha thandizo laumulungu m’kusankha atumwi ake 12. (Luka 6:12) Chotero utali wa mapemphero wolandirika umasiyana mogwirizana ndi zosowa.
Mapemphero Motsimikizirikadi Amayankhidwa
Baibulo liri ndi zolembera za mapemphero amene anayankhidwa ndi “Wakumva pemphero” wamkulu, Yehova Mulungu. (Masalmo 65:2) Chitsanzo chowonekera kwambiri chiri “pemphero loyesa” m’masiku a mneneri Eliya, cholembedwa mu 1 Mafumu mutu 18. M’zana loyamba, ophunzira a Yesu anakumanizana ndi yankho la mwamsanga limeneli ku pemphero: “Ndipo mmene adapemphera iwo, panagwedezeka pamalo pamene adasonkhanirapo; ndipo anadzazidwa onse ndi mzimu woyera, nalankhula mawu a Mulungu molimbika mtima.”—Machitidwe 4:23-31.
Pakati pa unyinji wa zokumana nazo zolandiridwa ndi ofalitsa a magazini ino pali zija za amuna ndi akazi a misinkhu yonse omwe anadzimva kuti anafika pa ngozi. Chifukwa cha chotulukapo chake, iwo anatsimikiziridwa kuti mapemphero awo anamvedwa ndi kuyankhidwa.
Kuti tichitire chitsanzo: Mwamuna wachichepere wokhala kuchigwa cha ku phiri lakutali la chiSwiss pafupi ndi malire a Italy ananena kuti: “Kupanda mphamvu kwanga m’kuyesera kupeza yankho [ku mavuto a moyo] kunali kowonekera kotero kuti ndinakhumba kokha kufa. . . . Ndinachita chinthu chokha chimene chinabwera m’malingaliro mwanga. Ndinapemphera: ‘Chonde Mulungu wosadziŵika, inu muyenera kukhalapo, ndipo muyenera kukhala Mulungu wachikondi. Ndithandizeni ine! Sindingapitirizenso—ndithandizeni kupeza chowonadi.’” Masiku ochepa pambuyo pake, okwatirana aŵiri achichepere omwe anali Mboni za Yehova anaitanira pa mwamuna ameneyu. Phunziro la Baibulo linakonzekeretsedwa, ndipo iye tsopano ali mboni yobatizidwa ya Yehova.
Namwino wolembetsedwa yemwe anali ndi moyo wopanda chimwemwe chifukwa cha mkhalidwe woipa wachisembwere wa mwamuna wake ndi kulekana kwawo potsirizira anali wachipembedzo mozama. Tsiku limodzi iye anapemphera mosowa chochita, kupembedzera kuti Mulungu amlole iye kudziŵa ngati anali ndi chifuno chaphindu. Masana amodzimodziwo, Mboni za Yehova zinabwera ku khomo kwake mu ntchito yawo yolalikira ya ku khomo ndi khomo. Iye anawaitana iwo kulowa m’nyumba mwake, kuwafunsa iwo mafunso ambiri, ndipo anasangalala kulandira mayankho a m’Malemba. M’kupita kwa nthaŵi, namwino iyemwiniyo anakhala wolalikira wa “mbiri yabwino” ndipo anali kutsogoza phunziro la Baibulo.—Mateyu 24:14.
Mmodzi wa Mboni za Yehova anali kuŵerenga Nsanja ya Olonda mu galimoto yake pamene mwadzidzidzi munthu wina anamgwira pakhosi. Iye anapemphera kwa Yehova Mulungu mowona mtima. Wowukirayo anathedwa mphamvu, ndipo kugwira kwake kunachepa mphamvu. Mboniyo inayamba kuyendetsa galimoto, kumutsanzika mwamunayo, ndi kumusiya iye atangoima ngati fano pakati pa msewu.
M’dziko la kuwonjezereka kwa kusuliza ndi kukaikira, okonda Mulungu ndi chowonadi angatsimikizire kuchokera ku chitsimikiziro chodalirika chakuti mapemphero operekedwa kwa Yehova Mulungu kupyolera m’ngalande yabwino, m’mkhalidwe wabwino, ndipo ndi mkhalidwe wabwino wa maganizo ndi mtima amamvedwa. Osati kokha kuti Mulungu wamphavuyonse adzamva mapemphero oterowo koma iyenso adzayankha iwo popanda kulephera, mogwirizana ndi chifuniro chake chaumulungu ndi panthaŵi yake yosankhidwa.
[Bokosi patsamba 4]
Mitundu ya Pemphero
Kusanthula kwachidule kwa mitundu yosiyanasiyana ya pemphero yogwiritsiridwa ntchito lerolino kudzatsimikizira kukhala kosangalatsa.
Logwiritsiridwa ntchito kaŵirikaŵiri mu chiHindu liri pemphero lalikulu lomwe limapereka ulemu kwa mulungu wosankhidwa kapena mulungu wachikazi, wa amene chikulingaliridwa kuti 330,000,000, imalambiridwa m’makachisi 10,000. Mobwerezabwereza, ngakhale kuli tero, Mapemphero a chiHindu ali olongosola ndipo angatenge mitundu iŵiri—kaya kusinkhasinkha (dhyana) kapena kutamanda (stotra). Kufunika kwambiri kumaikidwa pa kunena mapempherowo mofuula.
Mu Chinese Buddhist ndi malo opempherera a Taoist, mapemphero amanenedwa mokhazikika nthaŵi zitatu pa tsiku (mbandakucha, masana, ndi usiku). Mapemphero amenewa amatsogozedwa ndi kulira kwa belu laling’ono. Kuwathandiza iwo kupemphera, atsogoleri a chipembedzo a chiBuddha amanyamula chingwe cha mikanda 108. Anthu wamba ena amagwiritsiranso ntchito njira ya korona imeneyi kuŵerengera unyinji wa nthaŵi zimene mapempherowo anenedwa.
Kwa Asilamu odzipereka, mbali yofunika koposa ya kulambira kwawo iri pemphero la tsiku ndi tsiku (salat). Ilo liyenera kubwerezedwa nthaŵi zisanu pa tsiku pamene akuyang’ana ku Mecca mu Saudi Arabia.
Mapemphero Achiyuda amaphatikizapo awo otengedwa mwachindunji kuchokera m’Baibulo, monga ngati Masalmo. Mapemphero ena amaphatikizapo awo amene arabi osiyanasiyana awonjezerako.
Pakati pa awo odzinenera kukhala Akristu, pali mitundu yambiri ya mapemphero ndi njira za kupempherera. Awa amachokera ku mapemphero amene amabwerezedwa ndi korona m’manja ku mapemphero osindikizidwa, limodzinso ndi awo a mawu ochepa olankhulidwa popanda kuwabwereza.
[Chithunzi patsamba 7]
Mapemphero a Yesu anayankhidwa. Anu angayankhidwenso