Pemphero pa Phiri la Hiei—Chokwaniritsa Chozizwitsa kaamba ka Mtendere wa Dziko Lonse?
KODI pemphero lingabweretse mtendere wa dziko lonse? “Mtendere sudzabwera kokha mwa kupemphera. Iwo suli wopepuka motero,” anatero Gijun Sugitani, mkonzi wa msonkhano wa pemphero wochitidwa mu August 1987 mu Japan. “Koma sindikuganiza kuti mtendere udzazindikiridwa popanda pemphero.” Kawonedwe kake kanali kofanana ndi kaja kosungidwa ndi anthu ena a ku Japan 500 ndi nthumwi 24 za kumaiko a kunja zopezeka pa Msonkhano wa Chipembedzo wa 1987 wochitidwa mu Kyoto, Japan.
Gulu la mpatuko la Buddhist Tendai linalengeza msonkhano wa pemphero umenewo monga chotsatira cha umene unachitika mu 1986 pa Assisi (Italy) ndipo anandandalitsa iwo kudzawombana ndi chikumbukiro cha 1,200 cha kutsegulidwa kwa Kachisi wa Enryakuji pa Phiri la Hiei. Munthu aliyense payekha wokhala ndi chiyambi cha chiBudda, Chikristu cha dzina, Confucian, chiHindu, Chisilamu, Chiyuda, Sikh, ndi chiShinto anatenga mbali m’kupereka mapemphero pa phirilo. Kodi msonkhanowo ndithudi unali chokwaniritsa chozizwitsa kaamba ka mtendere wa dziko lonse?
Msonkhano wa “Kukonza Maluŵa”
“Msonkhanowo uli kukonza maluŵa kwa chipembedzo,” anatero Etai Yamada, wansembe wamkulu wa gulu la mpatuko la Tendai ndi tcheyamani wolemekezedwa. “Palibe liri lonse la maluŵawo linataya mpangidwe wake ndi fungo.” Iye anatanthauza kuti malinga ngati zipembedzo ziri zogwirizana m’chikhumbo chawo kaamba ka mtendere wa dziko lonse, chirichonse chidzasunga zikhulupiriro zake zotsutsana, monga duŵa lirilonse palokha m’kukonzedwa kumodzi.
Pakati pa “maluŵa” otchuka pa msonkhanowo panali Tchalitchi cha Katolika, choimiridwa ndi Francis Cardinal Arinze wa ku Vatican Secretariat for Non-Christians. Arinze anaŵerenga uthenga wa papa, umene unanena kuti “mtendere sungafikiridwe popanda pemphero ndipo ngakhale kuti nkhondo zingayambidwe ndi chiŵerengero chochepera cha anthu, mtendere umafunikira kugwirizana ndi kulimba nji kwa aliyense.”—Mainichi Daily News, August 5, 1987, tsamba 12.
Ngati chiyembekezo kaamba ka mtendere wa dziko lonse “chimafunikira kugwirizana ndi kulimba nji kwa aliyense,” kodi Mulungu amene amaperekako mapemphero awo ali wa mphamvu chotani? Nthumwizo zinapemphera kaamba ka mtendere, koma zimakhulupirira kuti zoyesayesa za anthu zidzaubweretsa iwo. Mofanana ndi kakonzedwe ka maluŵa kokongoletsa, msonkhano wawo wa pemphero unali chisonyezero chokongola cha zoyesayesa zawo zawo.
Kakonzedwe ka maluŵa kali kosangalatsa kukayang’ana, koma pamene chochitika chapaderacho chatha, maluŵa opanda mizuwo amafota ndipo kukongola kwawo kumatha. Kukongola kwapadera kwa duŵa lirilonse ndi ukulu wa makonzedwewo mwamsanga umataika. Ndipo maluŵawo samatanthauzidwa kuti abale zipatso. Kodi msonkhanowo unathanso monga “kukonza maluŵa” kosabala chipatso?
Atsogoleri a zipembedzo otengamo mbali iwo eni sanali okhutiritsidwa ndi zotulukapo zake. “Iwo akanakonda kukhala achindunji kwambiri ponena za miyezo imene zipembedzo ziyenera kutenga mtsogolo koma ananena kuti panalibe nthaŵi yokwanira kaamba ka kukambitsirana koteroko,” ikusimba tero Asahi Evening News. Komabe, chotulukapo choterocho chinayembekezeredwa. “Cholinga chathu,” akutero Takaaki Kobayashi, mmodzi wa okonza msonkhanowo, “chinali kumva malingaliro a chipembedzo chirichonse ndi njira zabwino koposa za kupezera mtendere. Lamulo lalikulu liri lakuti wotengamo mbali aliyense ayenera kumvera ku kawonedwe ka ena popanda kuikapo ndemanga kapena kuvomereza kapena kutsutsana.” Zoyesayesa zawo pa msonkhano wa pempherowu zinali ndi malire ku kumvetsera kwa ena, osati kuchitapo kanthu. Monga chotulukapo chake, msonkhanowo “unalephera kukhazikitsa nkhani yokambitsirana yomvekera kaamba ka kufikira zolinga za msonkhanowo.”
Kodi Unali wa Akristu Owona?
Anthu okalamira kutsatira Yesu Kristu angadabwe: ‘Kodi Mkristu ayenera kugwirizana nawo m’misonkhano ya pemphero yotero?’ Chenicheni chakuti unachitidwira pa Phiri la Hiei, phiri lopatulika la gulu la mpatuko la chiBudda, chimapereka chakudya kaamba ka malingaliro. Kodi mungalingalire Yesu Kristu akukwera pa phiri lopatulika la chiBudda kukapereka pemphero kaamba ka mtendere?
Mtumwi Paulo anachenjeza otsatira a Yesu Kristu kuti: “Musakhale omangidwa m’goli ndi osakhulupirira osiyana. Pakuti chilungamo chigawana bwanji ndi chosalungama? Kapena kuwunika kuyanjana bwanji ndi mdima? Ndipo Kristu avomerezana bwanji ndi Beliyali? Kapena wokhulupirira ali nalo gawo lanji pamodzi ndi wosakhulupirira? Ndipo chiphatikizo chake nchanji ndi kachisi wa Mulungu ndi wa mafano? . . . ‘Chifukwa chake tulukani pakati pawo, ndipo patukani,’ ati Yehova, ‘ndipo musakhudza kanthu kosakonzeka’; ‘ndipo ine ndidzalandira inu.’”—2 Akorinto 6:14-17.
Kodi kupereka mapemphero pa msonkhano wosakanizana zikhulupiriro pa phiri lopatulika la chiBuddha sikukafikira ku ‘kuyanjana m’goli kwa Mkristu’? Chotero, kodi ichi chikutanthauza kuti, Akristu ayenera kukhala opanda mbali ponena za kupemphera kaamba ka mtendere? Kutalitali!
Pemphero kaamba ka Mtendere
Mu ulosi wake ponena za “masiku otsiriza,” mneneri Yesaya analankhula za ambiri amene adzanena kuti: “Idzani, anthu inu, ndipo tiyeni tikwere ku phiri la Yehova,” osati ku Phiri la chiBuddha la Hiei. “Phiri la Yehova” limaimira kulambira kowona kwa Mulungu wa Baibulo. ‘Kukwera’ ku phiri limenelo kumatulukapo mu chiyani? Nkulekelanji, popeza Yehova “adzatiphunzitsa ife m’njira zake, ndipo tidzayenda m’mabande ake,” anatero Yesaya! “Iye [Yehova] adzaweruza pakati pa amitundu,” anawonjezera mneneriyo. Monga chotulukapo chake, padzakhala mtendere wa dziko lonse, popeza Yesaya ananeneratu kuti olambira owona “adzasula malupanga awo akhale zolimira, ndi nthungo zawo zikhale anangwape; mtundu sudzanyamula lupanga kumenyana ndi mtundu wina, ndipo sadzaphunziranso nkhondo.”—Yesaya 2:2-4.
Mkhalidwe umenewu ulipo pakati pa Mboni za Yehova, ndipo mwamsanga udzakuta dziko lonse lapansi. Koma motani? Yehova Mulungu, osati anthu, adzabweretsa mtendere wosatha kupyolera mwa Ufumu wake. Iwo udzasesa dziko lapansi kuliyeretsa kuchotsa akuswa mtendere onse ndipo iye adzalowetsapo dziko lapansi la paradaiso. (Chivumbulutso 11:15, 18) Mosiyana ndi malongosoledwe opangidwa pa msonkhano wa zipembedzo womwe unali wofanana ndi “kukonza maluŵa” kosangalatsa koma kopanda chipatso, Mawu a Yehova samabwerera kwa iye popanda chotulukapo.—Yesaya 55:11.
Nchifukwa ninji, chotero, tiyenera kupemphera kaamba ka mtendere ngati Mulungu adzabweretsa iwo mosasamala kanthu za zoyesayesa za anthu? Mwa kupemphera kwa Mulungu kaamba ka Ufumu wake kuti udze, tikusonyeza chikhumbo chathu chenicheni kaamba ka mtendere ndipo tikuchitira chitsanzo chikhulupiriro chathu m’njira ya Mulungu ya kubweretsa iwo padziko lapansi. (Mateyu 6:9, 10) Kaya tidzawona mtendere wopangidwa ndi Mulungu kapena ayi chimadalira pa “kuyembekeza kwathu Yehova.” Chotero bwerani “ku phiri la Yehova” ndipo gawananimo m’pemphero kaamba ka mtendere wowona womwe iye walonjeza!—Masalmo 37:9, 11.
[Chithunzi patsamba 8]
Kukonzedwa kwa maluŵa kuli kosangalatsa kuwona, koma sikumatanthauzidwa kuti kubale zipatso
[Chithunzi patsamba 9]
Phiri la Hiei, phiri lopatulika la gulu la mpatuko la Buddhist Tendai, kumene msonkhano wa pemphero unachitidwa