Chidziŵitso pa Nyuzi
Chigumula Sichongoyerekeza
Mbiri ya Baibulo ya chigumula cha dziko lonse kwa nthaŵi yaitali yakhala ikusulizidwa kukhala yozikidwa pa nkhani yopeka osati pa zenizeni. New Catholic Encyclopedia ikutsutsa kuti: “Mwachisawawa chimavomerezedwa tsopano kuti nkhani ya Nowa ndi chingalawa siri chidutswa cha kusimba kwa mbiri yakale koma iri mbali yolingaliridwa ya chilengedwe chenicheni cha mtundu wina kotheratu.” Okaikira ena atsutsa kuti chinyezi chonse m’malo otizinga chingapangitse kokha mainches oŵerengeka a mvula ya pa dziko lonse.
Koma mogwirizana ndi mbiri ya Genesis, magwero a madzi a chigumula sanali kokha chinyezi cha m’malo otizinga. Pa Genesis 1:6 timauzidwa kuti Mlengi analamula kuti: “Pakhale thambo [malo otizinga] pakati pa madzi, lilekanitse madzi [a m’nyanja] ndi madzi [pamwamba pa thambo].” Madzi olenjekedwa pamwamba pa thambo mwachidziŵikire anakhala kumeneko kufikira Chigumula. Mogwirizana ndi mtumwi Petro, “kumwamba” kwa malo otizinga ndi madzi pansi pawo anali njira mwa imene “dziko lapansi la masiku aja [a Nowa] pomizidwa ndi madzi lidawonongeka.”—2 Petro 3:5, 6; Genesis 1:7.
Zotulukapo zosakaza za chigumula cha madzi chimenecho zinamvedwa posachedwapa mu South Africa pamene chigumula chinakantha dera la Natal ndi kutenga miyoyo yoposa 300. Akumachitira ndemanga pa tsokalo, katswiri wotetezera K.H. Cooper anawona kuti: “Kaŵirikaŵiri ndakhala ndikudabwa ndi chomwe chikachitika m’tsiku lino ndi mbadwo ngati kukanagwa mvula kwa masiku 40 ndi usiku 40 yosalekeza. . . . Kodi mvula yoteroyo ikanathetsa chifupifupi moyo wonse pa dziko lapansi? Kukhala nditawona posachedwapa zomwe zinachitika kokha pambuyo pa masiku anayi a kugwa mvula mu Natal,” Cooper a kupitiriza kuti, “tsopano ndiri wotsimikiziridwa za kuwona kwa nkhani ya m’Chipangano Chakale.”
Kudera Nkhaŵa Kaamba ka Osauka?
Ndimotani mmene mpata womwe umalekanitsa osauka kuchokera kwa olemera ungalunzanitsidwire? Iye inali nkhani yolingaliridwa ndi Papa John Paul II mu kalata yolemberedwa ku magulu onse yokhala ndi mutu wakuti Solicitudo rei socialis (Chodera Nkhaŵa cha Mayanjano). Papa ananena kuti tchalitchi chiyenera kudzimva kukhala cha thayo kuchotsako nsautso ya awo omwe akuvutika. Motani? “Titayang’anziana ndi nkhani za kusowa, mmodzi sanganyalanyaze izo m’chiyanjo cha zokometsera m’tchalitchi zochuluka koposa ndi zokongoletsera za mtengo wapatali kaamba ka kulambira kwa umulungu; mosiyanako likakhala thayo kugulitsa zinthuzi ndi cholinga chofuna kupereka chakudya, chakumwa, zovala ndi malo ogona kaamba ka awo amene akusowa zinthuzi.”
Ngakhale kuli tero, akumachitira ndemanga pa kalata yolembedwa kwa magulu onse ya papayo, katswiri wa Vatican Domenico Del Rio anawona mu La Repubblica: “Chiri chachiwonekere kuti anthu tsopano adzakhala akuyembekezera kuwona . . . papa iyemwiniyo, ndi awo omuzinga iye, akuika chitsanzo. Basilica ya Vatican ndi mabasilica a Roma ali odzazidwa ndi ‘zokongoletsera za mtengo wapatali,’ mwinamwakenso ndi ‘zokometsera m’tchalitchi zochuluka koposa.’” Komabe, mogwirizana ndi maganizi ya Fortune, “nduna za Vatican zakwiitsidwa pa lingaliro la kusiyana ndi zochuluka zoterozo monga ngati chotengera cha ku Grisi kuti apeze ndalama.”
Pamene Yesu analangiza wolamulira wolemera “kugulitsa chuma chake chonse ndi kugawira ndalamazo aumphwaŵi, munthu ameneyo sanali wofunitsitsa kutero. Iye “anachoka wachisoni, pakuti anali mwini chuma chimbiri.” Molondola, Yesu anachenjeza kuti: “Kumene kuli chuma chako, komwe udzakhala mtima wakonso.”—Marko 10:21, 22; Mateyu 6:21.