Dziko Latsopano—Paradaiso Wopezedwanso!
AŴIRI okwatirana chatsopano anali ndi nyumba yokongola kwambiri—munda wa maluwa waukulu wodzaza ndi maluwa, mitengo, mbalame, ndi zinyama. Anali Paradaiso, mphatso yoolowa manja kuchokera kwa Atate wawo wachikondi! Kodi iwo “anakhala achimwemwe kosatha pambuyo pake”? Ayi. Pasanapite nthaŵi yaitali, iwo anataya nyumba yawo. Koma nchifukwa ninji?
Mudzi wa Paradaiso umenewo unataidwa chifukwa chakuti aŵiriwo sanayamikire chimene Atate wawo anachita kaamba ka iwo. Moipirakobe, iwo anali osamvera. Kuti ayese umphumphu wawo, Atate wawo anawauza iwo kuti angadye chipatso cha mtengo uliwonse koma kuchotsako umodzi, koma iwo mowukira sanamvere ndipo anadya kuchokera ku iwo.—Genesis 2:15-17; 3:6, 7.
Nchifukwa ninji chilango choterocho kaamba ka chimene chingawoneke kukhala upandu waung’ono? Mwinamwake fanizo lidzathandiza kuyankha funso limenelo. Mwini sitolo alemba ntchito manejala wokhala ndi zolembera zoyenerera. Kuti atsimikizire kuti wolembedwa ntchito wake watsopanoyo angakhulupiriridwe, mwiniwakeyo amupatsa iye mfungulo koma anena kuti pansi pa mikhalidwe iriyonse iye safunikira kutsegula durowa ina yake. Ngati wolembedwa ntchitoyo achita tero, iye adzachotsedwa. atasiidwa yekha, chilakolako chigonjetsa manejalayo ndipo atsegula durowayo. Mwini wake amgwira iye m’kachitidweko ndi kumuchotsa iye.
Paradaiso Wotaika
Ndimotani mmene chimenechi chikugwirizanirana ndi aŵiri okwatirana achicheperewo? Chifukwa chakuti iwo anadya chipatso choletsedwacho, Atate wawo anawachotsa iwo m’mudzi wawo wokongola. Kunja kwa Paradaiso wa Edeni, minga ndi zipanda zinayang’anizana ndi aŵiri okwatiranawo, Adamu ndi Hava. M’malo mwa kukhala angwiro, iwo tsopano anali opanda ungwiro. Ndipo m’malo mwa kukhala ndi moyo kosatha, iwo anayamba kufa. Ana awo analowa m’malo kupanda ungwiro kwawo, kuchimwa, ndi imfa.—Aroma 5:12.
Potsirizira pake, “Yehova anawona kuti kuipa kwa munthu kunali kwakukulu.” Mofananamo, m’masiku a Nowa, Mulungu anagwiritsira ntchito Chigumula kuyeretsa dziko lapansi. Kodi panali anthu ena opulumuka? Kokha asanu ndi atatu—Nowa ndi ana ake amuna atatu limodzi ndi azikazi awo anayi. M’kukonzekera kaamba ka chimene chingatchedwe ulendo wawo wopita ku dziko lachilendo, iwo anayenera kugonjera ku malangizo a Mulungu ndipo anayenera kumanga chingalawa chachikulu chokhoza kunyamula iwo, mitundu yambiri ya zinyama, ndi chakudya chokwanira. (Genesis 6:5-7, 13-22) Munda umene poyambapo unasangalalidwa ndi Adamu ndi Hava unafafanizidwa ndi Chigumulacho. Chotero, Paradaiso anataika—koma osati kosatha!
Paradaiso Wopezedwanso
Zaka mazana angapo pambuyo pake, Mulungu anatumiza Mwana wake wobadwa yekha ku dziko lapansi kudzawombola mtundu wa anthu kuchokera ku uchimo ndi imfa. Ichi chinachipangitsa icho kukhala chothekera kaamba ka awo okhulupirira mwa Yesu Kristu kupeza moyo wosatha. (Yohane 3:16) Yesu ananeneratunso kuti Paradaiso akapezedwanso. Ndithudi, pamene Yesu anali kufa pa mtengo wozunzirapo, iye anauza waupandu wopachikidwa kumbali kwake kuti: “Udzakhala ndi ine m’Paradaiso.”—Luka 23:43.
Kupezedwanso kwa Paradaiso kukatsatira chomwe kaŵirikaŵiri chimatchedwa mapeto a dziko, chonenedweratu ndi Yesu pamene ophunzira ake anafunsa kuti: “Chizindikiro cha kufika kwanu nchiyani ndi chamathedwe a pansi pano?” M’kuyankha, Yesu analoza ku nkhondo, kuperewera kwa chakudya, zivomezi, miliri, kuwonjezeka kwa kusayeruzika, ndi ndawala ya dziko lonse ya kulalikira Ufumu. Izi ndi mbali zina za chizindikiro zakhala zikuwoneka chiyambire 1914. (Mateyu 24:3-14) Izo ziri zoyambirira za mapeto a dongosolo iri la zinthu ndi kubwezeretsedwa kwa Paradaiso pa dziko lapansi iri.
Mu ulosi umodzimodziwo, Yesu ananenanso kuti: “Koma phunzirani ndi mkuyu fanizo lake: Pamene tsopano nthambi yake iri yanthete niphuka masamba ake, muzindikira kuti dzinja liyandikira. Chomwechonso inu, pamene mudzawona zimenezo, zindikirani kuti iye ali pafupi inde pakhomo. Indetu ndinena kwa inu mbadwo uwu sudzatha kuchoka kufikira zinthu zonsezi zidzachitidwa.” (Mateyu 24:32-35) Maulosi ena a Baibulo amasonyeza kuti kupezedwanso kapena kubwezeretsedwanso kwa Paradaiso kuli pafupi kwambiri, kuti dziko latsopano liri pa chizimezime. Koma kodi ilo lidzakhala ngati chiyani?
Dziko Latsopano—Losiyanadi Kotheratu!
Maboma alipowa adzalowedwa m’malo ndi Ufumu wa Mulungu. (Danieli 2:44) Padzakhala chilungamo ndi mtendere wosatha kaamba ka onse m’dziko latsopano pansi pa ulamuliro wa Ufumu wa Yesu Kristu, “Kalonga wa Mtendere.” (Yesaya 9:6, 7) Popeza kuti iye adzawononga oipa ndi mbali zosayeruzika zomwe tsopano zikulamulira mtundu wa anthu, kokha okonda mtendere “opanda mawanga” adzatsala. (Miyambo 2:21, 22; Chivumbulutso 19:11-21; 16:14-16) Inde, opulumukawo adzakhala ofatsa, anthu okonda mtendere. Ndi mpumulo wotani nanga umene iwo udzakhala!
Utundu ndi mitundu ina ya kunyada idzatheratu m’dziko latsopano. M’chenicheni, khamu lokulira la anthu labwera kale mu ulendo wautali kulaka zinthu zoterozo. Kodi iwo ndani? Mboni za Yehova. Ndipo nchifukwa ninji iwo ali osiyana chotero? Chifukwa amaphunzira Baibulo mwa khama, kuligwiritsira ntchito ilo m’moyo, ndipo ali ndi chikondi pakati pawo. (Yohane 13:34, 35; Machitidwe 10: 34, 35) Mbonizo tsopano zafika m’mamiliyoni pa dziko lonse, koma Baibulo likuneneratu kuti alambiri a Yehova a pa dziko lapansi potsirizira pake adzakhala “chiŵerengero chachikulu, chosakhoza kuchiŵerenga, cha anthu ochokera ku mtundu uliwonse fuko, anthu ndi manenedwe.” –Chivumbulutso 7:9, The Jerusalem Bible.
Nkhondo sidzatenganso miyoyo ya anthu. Mabiliyoni sadzawonongedwanso pa zida za nyukliya, zida zina za nkhondo, ndi magulu a nkhondo. Kusinthanso, kuwombana kwa magulu a anthu, ndi mitundu ina yonse ya upandu sizidzakhalako. (Yesaya 2:4) Kuphunzitsa kwa za nkhondo ndi kulembedwa nkhondo kudzatha, popeza izo zidzakhala zopanda phindu. Ndi tsiku lachimwemwe chotani nanga pamene Mulungu adzathetsa nkhondo!—Salmo 46:8, 9.
Mtendere weniweni udzakhalapo. “Katsala kanthaŵi,” anatero wamasalmo, “ndipo oipa adzatha psyiti . . . Koma ofatsa adzalandira dziko lapansi, nadzakondwera nawo mtendere wochuluka.”—Salmo 37:10, 11.
Kuperewera kwa zakudya kudzapereka njira ku zochuluka. M’malo ambiri, alimi osauka tsopano amalimbana ndi minga ndi zipanda, nthaka yoipa, zipululu zomayenderera, chirala, ndi kuwukira kosakaza kwa dzombe. Zonsezi zidzasinthidwa. (Yesaya 35:1, 6, 7) Chotulukapo chake? Kuwonjezeka kwakukulu m’zotulutsidwa! (Salmo 72:16) Kuchotsapo kuperewera kwa zakudya ndi zakumwa, Yehova adzapereka “phwando”!—Yesaya 25:6.
Ntchito yopindulitsa idzasangalalidwa ndi onse. Chidzakhala chokhutiritsa chotani nanga kumanga nyumba, kubzyala mitengo ya zipatso, ndi kupanga madimba! Ndipo chikakhala chosangalatsa chotani nanga kukhala mumthuzi wa mtengo wanu wa mkuyu ndi kudya zipatso zake zokoma!—Mika 4:4.
Nyumba zabwino koposa zidzaperekedwa kaamba ka aliyense. Lerolino, mamiliyoni amakhala m’nyumba zosamangidwa bwino kapena zosawoneka bwino za m’matauni. Ndi moyo wopanda chimwemwe chotani nanga! Mu Africa, mwachitsanzo, mamiliyoni a unyinji wa anthu akuda akuchoka m’midzi, koma iwo kaŵirikaŵiri amafunikira kukhala m’nyumba za matope kapena makande zokhala ndi denga la malata, mikhalidwe yopanda ukhondo, ndi yokhala ndi malo amseri ochepera. M’dziko latsopano, ngakhale kuli tero, anthu adzamanga nyumba zabwino ndi kukhalamo.—Yesaya 65:21, 22.
Umoyo wangwiro udzakhalapo m’malo mwa matenda ndi matenda onga AIDS yakupha. Mneneri wowuziridwa ananeneratu kuti palibe adzanena: “Ine ndidwala.” M’kuwonjezerapo, m’dziko latsopano lomwe liri pafupilo, “maso a akhungu adzatsegudwa, ndi makutu a ogontha adzatsegulidwa. Pamenepo wopunduka adzatumpha ngati nswala, ndi lilime la wosalankhula lidzayimba.”—Yesaya 33:24; 35:5, 6.
Imfa, misozi, ndi nyumba zokonzera maliro zidzachoka. (Chivumbulutso 21:4) Koma bwanji ponena za mabiliyoni omwe anafa kale? Monga munthu pa dziko lapansi, Yesu anaukitsa anthu angapo. Mwachitsanzo, iye kamodzi anakumana ndi gulu la opita kumanda akutsagana ndi bokosi la maliro la mwamuna wachichepere yemwe anangofa mu mzinda wa Nayini. Pambuyo pa liwu la chitonthozo kwa mayi wachisoniyo, mkazi wamasiye, Yesu ananena kuti: “Mnyamata iwe, ndinena ndi iwe, Tauka!” Ndipo iye anatero! (Luka 7:11-17) Pa chochitika china, Yesu anapereka chitsimikiziro ichi: “Ikudza nthaŵi pamene onse ali m’manda . . . adzatulukira.” (Yohane 5:28, 29) Popeza Mulungu analenga unyinji wofika m’makwintiliyoni wa nyenyezi ndi zolengedwa zina za kumwamba ndipo amaziitana izo “ngakhale ndi dzina,” ndithudi kuwukitsidwa kwa mabiliyoni a anthu akufa sikudzapangitsa vuto.—Yesaya 40:26.
Kodi Chiri kaamba ka Inu?
Yehova Mulungu poyambirira anakonza kuti mtundu wa anthu suyenera kufa nkomwe koma uyenera kusangalala kosatha ndi zinthu zabwino zimene amapereka mwachikondi. Chotero tangolingalirani madalitso a moyo m’dziko latsopano ndi mabanja achimwemwe! Lingalirani za ana okhoza kuseŵera mwachisungiko ndi nyama zomwe ziri zowopsya tsopano lino. (Yesaya 11:6-9) Lingalirani madalitso a mtendere, nyumba zabwino, ntchito yopatsa phindu, chakudya chochuluka. Inde, ndipo lingalirani za kukhala kosatha m’dziko lapansi la paradaiso.
Kodi mungakhale kumeneko? Inde, ngati mutenga ndi kugwirira ntchito pa chidziŵitso cholongosoka cha Mawu a Mulungu. Mboni za Yehova ziri zokonzekera kukuthandizani kumangirira chikhulupiriro m’malonjezo osalephera a Mulungu. Inu mungakhale ndi chidaliro kuti Paradaiso posachedwapa adzapezedwanso, popeza kuti dziko latsopano liri pafupi kwambiri!