Chidziŵitso pa Nyuzi
“Siali a Dziko Lapansi”
Pamene anthu oposa chikwi zana limodzi anasonkhana mu Olympic Stadium ya ku West Berlin kaamba ka chigawo chomalizira cha Msonkhano wa Evangelical Church ya ku Germany, prezidenti wa tchalitchi Helmut Simon anawafulumiza iwo kudziloŵetsa m’ndale zadziko.
Simon anandandalitsa nkhani zonga ngati kugwiritsira ntchito chuma molondola, kusamalira malo otizinga ndi zamoyo zake, kukhazikitsa dongosolo labwinopo la zachuma, kuthetsa mpikisano wa zida zankhondo, ndi kuthetsa kusalembedwa ntchito. Iye anadzimva kuti izi zinali pakati pa ziwopsyezo zosathetsedwa za mtundu wa anthu. Kuti awunikire omvetsera ake ku kufulumira kwa nkhanizi, nyuzipepala ya ku Germany Frankfurter Allgemeine Zeitung ikusimba kuti “iye ananena kuti palibe chirichonse chabwinopo chimene chikachitika m’chitaganya cha Kumadzulo ndi Kummawa kuposa kokha kulola nzika zawo kudziloŵetsa m’ndale zadziko.” Simon analimbikitsa opezekapo onse “kulingalira kudziloŵetsamo koteroko kukhala ntchito ndi kuwona msonkhano wa tchalitchiwo kukhala kachitidwe ka kuyenera kwa Chiprotesitanti.”
Komabe, kodi Akristu owona molondola angadziloŵetsa iwo eni m’machitachita a ndale zadziko oterowo? Kodi Yesu sananene kuti atsatiri ake “siali a dziko lapansi monga (iye sanali) wa dziko lapansi”? (Yohane 17:16) Yesu anaphunzitsa atsatiri ake kupempherera Ufumu wa Mulungu monga chiyembekezo chenicheni kaamba ka mtundu wa anthu. Nchifukwa ninji? Chifukwa chakuti, monga mmene mneneri Danieli ananeneratu kalelo, Ufumu wa Mulungu “udzaphwanya ndi kutha” maboma adziko olephera, “nudzakhala chikhalire.”—Danieli 2:44.
Kodi Kuba Sikuli Chimo?
Kodi kuba kuli chimo? Osati nthaŵi zonse, mogwirizana ndi wansembe Wachikatolika Ivo Storniolo. Nyuzipepala ya ku Brazil, O Estado de S. Paulo, ikugwira mawu Storniolo kukhala akunena kuti “Mulungu amadalitsa ndi kulekerera kuba kochitidwa ndi osauka.” Pambuyo pake, iye ananena kuti anali kulozera “kokha kwa osauka aja amene amaba ndi cholinga chofuna kukhalabe ndi moyo.” M’lingaliro la wansembeyu, achichepere opulupudza amene amaba sayenera kulangidwa, popeza kuti iwo “anaberedwa kumbuyoko ndi amphamvu.” “M’lingaliro lake,” ikudziŵitsa tero O Estado, “marginais [onyalanyazidwa mwamayanjano kapena opanda mwaŵi, osauka mwachisawawa, osalembedwa ntchito] alinso ‘pakati pa osankhidwa a Mulungu.’”
Kodi Baibulo limachilikiza lingaliro loterolo? Kutalitali. Pamene kuli kwakuti Yesu analimbikitsa atsatiri ake kusonyeza chifundo kwa osoŵa, iye sananenepo nkomwe kuti mavuto amayanjano, onga ngati kusauka, analungamitsidwa m’kuba. Mmalomwake, monga mmene mtumwi Paulo analembera: “Aliyense amene anali mbala ayenera kuleka kuba; mmalomwake ayenera kudziikizako iyemwini pa ntchito inayake yowona mtima ndi manja ake kotero kuti akakhale ndi chinachake chogaŵana ndi osauka.”—Aefeso 4:28, The New Jerusalem Bible.
Malonda Amafano
Kusonyezedwa kwa dziko kwa zinthu zachipembedzo ndi mipando, kochitidwira kumpoto kwa Italy, kunalola makampani 97 kupereka zopanga zawo. Pakati pa zinthu zosonyezedwa panali, chiwiya chothandizira kubisa mawu polapa chokhala ndi mpando wokometseredwa mwaudongo ndi wokutidwa ndi nsalu yabwino. Kuphatikizaponso ndi makandulo opanda fungo amwambo a “Pope John” oyaka kwa utali wa maola 40; nyimbo za mabelu a tchalitchi zolinganizidwiratu pa kompyuta; mabokosi a zaufulu otetezeredwa bwino “ofanana ndi mosungira ndalama”; mavideo amaphunziro kaamba ka ana (uko ndiko kuti, The Bible according to Johnny); ndi zola zosakhala za zikopa zenizeni zokhala ndi zofunikira kaamba ka Misa yapoyera.
Kukometsera kwa ansembe sikunapatulidwe pa chochitikacho. “Olinganiza [aŵiri] a zokometsera za chipembedzo” analongosola ku nyuzipepala ya ku Italy La Stampa kuti ‘kwakukulukulu, ansembe achichepere amafuna kuwoneka bwino, zovala zaubweya weniweni zokhala ndi kukometsera kwa ku Germany, kapetedwe, yunifomu, zopanda mitundu komabe zolemekezeka. Ndipo tiyamika Mulungu kuti malonda akuyendadi bwino.’
Kuchezera dziko kwa chipembedzo kukupanganso phindu m’zamalonda. “Chaka chirichonse pamakhala anthu 15 miliyoni amene amayenda kaamba ka zifukwa za chipembedzo, ndipo osamalira ochezerawo, kaya akhale achipembedzo kapena ayi, amapikisana kuti akhale nawo,” ikusimba tero nyuzipepala ya ku Italy La Repubblica. Posonyeza chimenechi, nyuzipepala ya ku Italy II Messaggero ikunena ponena za nyumba yopempherera ya “Woyera” Anthony mu Padua kuti “anthu amapereka mamiliyoni a ndalama osati kokha m’mahotela koma makamaka m’mabokosi a ndalama a nyumba yopempherera kaamba ka zithunzi zoyera ndi kukundikidwa.”
Nchosadabwitsa kuti pamene Dziko Lachikristu, limodzi ndi zipembedzo zonse zonyenga zidzawonongedwa, ‘ochita malonda a m’dziko adzalira nadzauchitira chifundo.’ Monga mmene Chibvumbulutso 18:11 chikupitirizira kuti: “Popeza palibe munthu agulanso malonda awo.”