“Ilo Silipita M’mbali”
Kukulira m’dziko lino lovutitsidwa sikuli kopepuka. Achichepere amayang’anizana ndi mikhalidwe yatsopano yambiri ndipo ayenera kupanga zosankha zamphamvu. Kodi ndiyenera kumwa? Kulandira mankhwala ogodomalitsa? Kodi ndi makhalidwe otani amene ali oyenera kwa wina wachiŵalo chosiyana? Achichepere afunikira mayankho ogwira ntchito, amene sapita m’mbali. Ataŵerenga bukhu latsopano lakuti Questions Young People Ask—Answers That Work, wachichepere wa ku Greensboro, North Carolina, analemba kuti:
“Bukhuli nlomveka bwino kwambiri ndipo liri ndi zitsanzo zabwino kaamba ka vuto lirilonse. Utayamba kuliŵerenga, sukhoza kuliika pansi, mitu yake njokondweretsadi. Ilo silipita m’mbali, kunena kwake titero, koma limapereka mayankho achindunji ku vutolo.
“Mwachidule, bukhuli mosapeŵeka nlozizwitsa, nlowonadi, nlabwinodi, . . . mawu okha sangalongosole ubwino wa bukhuli. Ndikayamikira mokulira bukhuli kwa onse, makamaka kwa achichepere.”
Landirani bukhu latsopanoli, lokhala ndi zithunzi zokongola mwakudzaza ndi kutumiza kapepalaka. K30 yokha.
Chonde tumizani, mutalipiriratu positi, bukhu lachikuto cholimba, lamasamba 320 Questions Young People Ask—Answers That Work. Ndatsekeramo K30 (Zambia).