Kuchitira Umboni M’malo Abizinezi—Njira Yachijapan
LAMULO la Yesu Kristu la kupereka ntchito yolalikira ku “malekezero ake a dziko” liyenera kuphatikiza malo abizinezi. (Machitidwe 1:8) Mu Japan, kupereka umboni Waufumu kwa anthu omagwira ntchito m’malo apoyera ndi m’maofesi a makampani aakulu kumapereka chitokoso. Ofalitsa Aufumu mu mpingo wina anatenga chilolezo kuchita umboni wamagazine m’nyumba ya maofesi a mzinda mkati mwa kupuma kwa chakudya chamasana. Ofalitsawo sanangopemphera kwa Yehova kuwapatsa kulimba mtima komanso anapereka chisamaliro chachikulu ku kavalidwe ndi makhalidwe awo ndipo anapanga makadi ovala osonyeza maina awo ndi kuwadziŵikitsa monga Mboni za Yehova.
Mboni inkafikira wantchito, mwakunena kuti: “Zikomo, ndinapatsidwa chilolezo kulankhula kwa anthu pano. Kodi mungalole kumvetsera kwa ine pamene mukudya?” Mboniyo inafunikira kusonyeza chiweruzo chabwino ndi kugwiritsira ntchito mawu “okometsedwa ndi mchere.” (Akolose 4:6, NW) Pa ulendo wawo woyamba, iwo anagaŵira magazine 39, koma kunawatengera maulendo anayi kuti akwaniritse nyumba yonseyo ya nyumba zosanjikana zisanu ndi zitatu mmene anthu 1,500 amagwiramo ntchito. Iwo anagaŵira chiwonkhetso cha magazine oposa pa zana limodzi ndipo anali okhoza kuyamba njira za magazine ndi kupanga maulendo obwereza.
Mmodzi wa ofalitsawo anapanga ulendo wobwereza kwa manijala. Pamene iye anamva lemba la mu New World Translation likuŵerengedwa, ananena kuti: “Baibulo ili nlosavuta kumvetsetsa. Lomwe ndinaŵerengapo linali m’Chijapanese chakale ndipo linali lovuta kwenikweni kuŵerenga.” Kope la New World Translation linaperekedwa kwa iye mlungu wotsatira.
Kodi mungachite zowonjezereka m’gawo la mpingo wanu kulalikira mbiri yabwino kwa “anthu onse,” kuphatikizapo aja a m’madera abizinezi?—Yerekezerani ndi 1 Timoteo 2:4.