Tayerekezerani Dziko Lopanda Umbombo
KODI mungayerekezere dziko limene anthu ali ogwirizanika mmalo mwa kupikisana? Kumene anthu amachitira ena monga momwe iwo eni akakondera kuchitiridwa? Imeneyi ndiyo mikhalidwe ya dziko lopanda umbombo. Limenelo likakhala dziko labwino chotani nanga! Kodi iro lidzadzadi? Inde, iro lidzatero. Koma kodi ndimotani mmene umbombo—wokhathamira motero mwa anthu—ungathetsedwere?
Kuti tipeze yankho, choyamba tiyenera kuzindikira chiyambi cha umbombo. Baibulo limasonyeza kuti uwo nthaŵi zonse sunali mkhalidwe wa anthu. Mneneri Mose akutikumbutsa kuti palibe chirema chonga umbombo chimene chinapezedwa poyambapo m’munthu woyamba, cholengedwa changwiro cha Mlengiyo wopanda umbombo: “Thanthwe, ntchito yake ndiyangwiro; pakuti njira zake zonse ndichiweruzo.” Chotero, pamenepa, kodi ndikuti kumene umbombo unachokera? Anthu aŵiri oyambirira anaulola kuyambika mwa iwo—Hava mwaumbombo poyembekezera zimene akanapeza kuchokera m’kudya zipatso zimene Mulungu adaletsa, Adamu adaatero mwaumbombo posafuna kutaikiridwa ndi mkazi wake wokongolayo. Mose adawonjezera, mawu amene adalinso owona kwa Adamu ndi Hava kuti: “Anamchitira zovunda sindiwo ana ake, chirema nchawo.”—Deuteronomo 32:4, 5; 1 Timoteo 2:14.
Podzafika nthaŵi ya Chigumula cha dziko lonse cha tsiku la Nowa, umbombo ndi kusirira zinali zitayambika kuukulu wakuti “kuipa kwa anthu kunali kwakukulu padziko lapansi, ndiponso kuti ndingaliro zonse zamaganizo a mitima yawo zinali zoipabe zokhazokha.”—Genesis 6:5.
Mkhalidwe wosonkhezera umenewu wa umbombo mwa munthu wapitirizabe kufikira lerolino, ukumawonekera kufikira pachimake penipeni m’chitaganya chamakono chosayamikira ndi chaumbombo.
Kuthetsa Umbombo Kupyolera mwa Maphunziro
Monga momwedi umbombo pakati pa anthu wakulira, choteronso kuuthetsa kuli kothekera. Umbombo ungalakidwe. Komabe, kuti zimenezi zichitike, maphunziro oyenera ndi malangizo nzoyenerera, mwamalangizo ankhokera kapena mwa kutsatiridwa kwa zilangizo za malamulo amakhalidwe abwino. Zimenezi zingamvekere kukhala zosangalatsa, koma kodi ndani amene angapereke maphunziro amtundu umenewu ndi kutsimikizira kuti zimene zikuphunziridwa zikugwiritsidwa ntchito—ngakhale kukakamiza ngati kuli kofunikira?
Maphunziro oterowo ayenera kuchokera kumagwero amene iwo eni ali opanda umbombo. Sipayenera kukhala zolinga zobisika kapena kuyembekezera kubwezeredwa kanthu kena kaamba ka maphunziro amenewo. Kuwonjezera apa, kufunika ndi phindu za kupanda dyera ziyenera kuphunzitsidwa ndi kuchitiridwa chitsanzo. Wophunzirayo ayenera kukhutiritsidwa osati kokha kuti njira yoteroyo ya moyo njothekera koma kuti ndiyo njira yofunidwa, yokhala ndi mapindu kwa iyemwini ndi kwa omzungulira.
Ali Mulungu wakumwamba yekha amene angapereke maphunziro amtundu umenewu, pakuti kodi ndimunthu uti kapena gulu padziko lapansi limene lingakhale ndi ziyeneretso ndi ziyambi zotero? Anthu onse ali osayeneretsedwa pamaziko a chowonadi cha Baibulo ichi: “Onse anachimwa, napereŵera pa ulemerero wa Mulungu.”—Aroma 3:23.
Mokondweretsa, Yehova, Mulungu wakumwamba, amapereka maphunziro oterowo m’bukhu lake lophunziridwa, kapena malangizo, Baibulo Loyera. Mwana wake, Yesu Kristu, anachirikiza maphunziro amtundu umenewu pamene adali munthu padziko lapansi. Chapakati pa Ulaliki Wapaphiri wotchuka wa Yesu, iye analankhula za njira ya moyo imene inamvekera kukhala yachilendo kwa unyinji wa omvetserawo, popeza kuti inaphatikizapo kupanda dyera ngakhale kwa adani kapena otsutsa. Yesu anati: “Kondanani nawo adani anu, ndi kupempherera iwo akuzunza inu; kotero kuti mukakhale ana a atate wanu wakumwamba, chifukwa iye amakwezera dzuwa lake pa oipa ndi pa abwino, namavumbitsira mvura pa olungama ndi pa osalungama. Chifukwa kuti ngati muwakonda akukondana ndi inu ndimphotho yanji yomwe muli nayo? Kodi angakhale amisonkho sachita chomwecho?”—Mateyu 5:44-46.
Mbali ya ntchito ya Yesu padziko lapansi inali kuphunzitsa alangizi opanda dyera kotero kuti iwo pambuyo pake akaphunzitse ena m’njira yopanda dyera imeneyi ya moyo. Nthawi ina pambuyo pa imfa ya Yesu ndi chiukiriro, mtumwi Paulo anadzakhala mmodzi wa alangizi oterowo. M’makalata ake angapo ouziridwa, Paulo analimbikitsa kuthetsedwa kwa umbombo. Mwachitsanzo, iye adalembera Aefeso naati: “Koma dama ndi chidetso chonse, kapena chisiriro, zisatchulidwe ndi kutchulidwa komwe, monga kuyenera oyera mtima.”—Aefeso 5:3.
Mofananamo lerolino, Mboni za Yehova zikuphunzitsa amuna ndi akazi kugonjetsa zikhoterero zaumbombo. M’kupita kwanthaŵi awanso amakhala oyeneretsedwa kupita ndi kuphunzitsa ena njira zaumulungu zoterozo.
Chowonadi Chabaibulo Pantchito
Komatu inu mungafunse kuti: ‘Kodi anthu opanda ungwiro, okhathamira ndi umbombo, angakhoze kuuchotsa m’maumunthu awo?’ Inde, iwo angakhoze. Ndithudi, osati kotheratu, koma kuukulu umene uli wowonekera. Tiyeni tilingalire chitsanzo cha zimenezi.
Mbala yotsimikizirika inkakhala m’Spanya. Nyumba yake idaali yodzala ndi zinthu zakuba. Kenaka idayamba kuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova. Monga chotulukapo, chikumbu mtima chake chinayamba kumvuta, chotero anasankha kubwezera kwa eni ake a zinthu zimene anali ataba. Iye anafikira kwa amene poyamba anali bwana wake ndi kuulula kukhala ataba makina ochapira atsopano kwa iye. Bwana wakeyo, atachita chidwi kwambiri ndi kachitidwe kake kosintha, anasankha kusadziŵitsa apolisi koma anangolola mbala yapapitapoyo kulipilira mtengo wa makina ochapirawo.
Chotsatira, mbala yapapitapoyo inasankha kupita kwa aliyense amene anakumbukira kuti anambera akabwezere zinthu zobedwazo. Aliyense amene iye adamfikira anadabwa kuti chifukwa cha kugwiritsira ntchito kwake malamulo amakhalidwe abwino a Baibulo, iye anakhala ndi masinthidwe aakulu amenewa m’makhalidwe.
Tsopano anayang’anizana ndi vuto lenileni. Iye sanadziwe eni zinthu zochulukira zimene anali chikhalirebe nazo. Chotero, pambuyo popemphera kwa Yehova, anapita kumalikuru a apolisi ndi kukapereka mawailesi asanu ndi imodzi a steriyo amene iye anaba m’magalimoto. Apolisiwo anadabwa, popeza kuti iye adaali ndi mbiri yabwino ndi iwo. Iwo anagamula kuti mwamunayo alipire faindi chabe ndi kutumikira nthawi yochepa m’ndende.
Amene kale anali mbala ameneyu tsopano ali ndi chikumbumtima choyera, pokhala ataleka njira yake yaupandu ndi umbombo kuti akhale mbali ya mpingo wa padziko lonse wa Mboni za Yehova.
Zitsanzo zikwi zambiri zofanana zingaperekedwe mosavuta. Ngakhale kuti awo amene apanga masinthidwe otere m’miyoyo yawo ndiochepekera mwa nzika za padziko lapansi, chenicheni chakuti ochulukira atero chikusonyeza mphamvu ya ubwino umene umachokera m’kudziŵa ndi kugwiritsira ntchito malamulo amakhalidwe abwino a Baibulo.
Pamene chaka chirichonse chikutha, anthu owonjezerekawonjezereka amavomereza njira imeneyi ya moyo. Malangizo a Baibulo akuperekedwa m’mipingo ya Mboni za Yehova yoposa 60,000 padziko lonse lapansi. Mbonizo panthaŵi ino sizikuyembekezera kusintha dziko lathunthu, kuchotsa umbombo pakati pa anthu zikwi mamiliyoni ambiri amene tsopano akukhala ndi moyo. Komabe, ulosi wa Baibulo umasonyeza kuti mwamsanga tsopano, njira yopanda umbombo ya moyo idzafunga padziko lonse lapansi!
Dziko Latsopano Lopanda Umbombo
Simudzakhala malo a umbombo ndi kupanda dyera m’dziko latsopano likudzalo. Mtumwi Petro akutitsimikizira kuti chilungamo chidzakhala chizindikiro osati kokha cha “miyamba yatsopano” komanso cha “dziko lapansi latsopano.” (2 Petro 3:13) Umbombo udzakhala pakati pa “zoyambazo” zimene zidzakhala zitapita, limodzi ndi matenda, chisoni, ndipo ngakhale imfa.—Chivumbulutso 21:4.
Chotero, ngati mwasautsidwa ndi umbombo womakulakula ndi njira ya moyo yadyera yowonedwa motizungulira monse lerolino, musataye mtima! Yambani tsopano lino kukhalira moyo dziko latsopano likudzalo limene posachedwapa lidzakhala lenileni. Mwachithandizo cha Mulungu, yesayesani kuthetsa umbombo m’moyo wanu. Gwirizanani m’kuthandiza ena kuwona mapindu amene tsopano lino angasangalalidwe ndi moyo Wachikristu. Ikani chikhulupiriro chanu ndi chidaliro m’lonjezo la Yehova Mulungu lakuti mwamsanga pompa umbombo udzakhala pakati pa zinthu zochuluka zosasangalatsa zimene ‘sizidzakumbukika, kapena kuloŵa m’mitima yathu.’—Yesaya 65:17.
[Chithunzi patsamba 5]
Yesu analankhula za njira ya moyo imene imachirikiza kupanda dyera, osati umbombo
[Chithunzi patsamba 7]
Mwamsanga—padzakhala dziko lopanda umbombo