“Kufalikira kwa Mtendere”?
“KUFALIKIRA KWA MTENDERE.” “Oo, ndi Dziko Lamtendere Chotani Nanga.” “Mtendere Ukusefukira Kulikonse.” Iyi inali pakati pa mitu yankhani ya nyuzipepala imene inadabwitsa oŵerenga mkati mwa chaka chimodzi chapitacho kapena ziŵiri. Kuzungulira dziko lonse, masinthidwe m’nyuzi kuchokera ku tsoka ndi chisoni kumka ku chiyembekezo anali ozizwitsa. Kodi chinkachitika nchiyani?
Modabwitsa, sikale kwambiri pamene nkhondo zazikulu zingapo zinatha kapena kuchepetsedwa mwadzidzi mkati mwa miyezi yochepekera. Mu Afirika, mtendere ‘unaulika’ mu Angola. Cha Pakati pa Asia, Soviet Union inachotsa magulu ake ankhondo mu Afghanistan. Cha Pakati pa America, nkhondo inazilala pakati pa boma la Nicaragua ndi ankhondo Yachizembera opandukawo. Kumwera chakummawa kwa Asia, a ku Vietnam analola kutuluka mu Kampuchea. “Kusefukira kwa mtendere” kunafika ngakhale ku Middle East pamene nkhondo yokhetsa mwazi pakati pa Iran ndi Iraq potsirizira pake inaima.
Mwinamwake chapaderadi kwambiri chinali mkhalidwe watsopano pakati pa maulamuliro aakulu. Pambuyo pa zaka 40 za nkhondo ya mawu, kunali kovuta kukhulupirira zisonyezero za kuyanjana, mawu onena za zikondwerero zofanana, ndi zochitika zotsimikizirika kulinga ku mtendere pakati pa Soviet Union ndi United States. Ndiponso, mogwirizana ndi The Economist, Ulaya tsopano wakhala ndi nyengo yopitirizabe yaitali koposa popanda nkhondo m’mbiri yake yonse yodziŵika. Ndithudi, mtendere ukusimbidwa.
Kodi zitanthauzanji? Kodi andale zadziko ali pamphembenu pakudzetsa “mtendere m’nthawi yathu”? Zaka makumi asau ndi chimodzi zapitazo, mawu amenewa ananenedwa ndi nduna yaikulu ay Briteni a Neville Chamberlain. Anatsimikizira kukhala oseketsa momvetsa chisoni pamene, nthaŵi yaifupi pambuyo pake, nkhondo yachiŵiri yadziko inaulika. Kodi iwo tsopano potsirizira pake adzakhala owowna?