Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w90 12/15 tsamba 21
  • Chidziŵitso pa Nyuzi

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Chidziŵitso pa Nyuzi
  • Nsanja ya Olonda​—1990
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kuletsedwa Kukwatira
  • Kodi Nchifukwa Ninji Pali Chiwawa Chochuluka Motero?
  • Kodi “Mudzi wa Davide” Ulikuti?
  • Mikhole ya Ansembe Ochitira Ana Chisembwere Iulula Nkhani
    Galamukani!—1993
Nsanja ya Olonda​—1990
w90 12/15 tsamba 21

Chidziŵitso pa Nyuzi

Kuletsedwa Kukwatira

Wolongosoledwa kukhala “vuto lobisika kwa mibadwo yambiri” ndi bishopu wina wa Lutheran, mkhalidwe woipa wachisembwere pakati pa atsogoleri achipembedzo pomalizira pake ‘watulukira poyera.’ Komabe, Los Angeles Times ikusimba kuti limodzi nawo kwabwera “kuwululika kwapoyera kochititsa manyazi ndi milandu yodula imene yakakamiza matchalitchi angapo kukhala opandiratu ndalama.” Times yadziŵitsa kuti mabungwe a inshuwalansi akunena kuti m’makoti muli milandu yoposa 2,000 ya chisembwere chakugonana yoloŵetsamo atsogoleri achipembedzo.

Chodziŵikanso nchakuti, kukusimbidwa kuti ena a olakwa oipitsitsa ali atsogoleri achipembedzo a Roma Katolika. A. W. Richard Sipe, katswiri wa kuchiritsa matenda amaganizo ndiponso yemwe kale adali wodzipereka mwachipembedzo wa chipembedzo cha Benedict, wafunsa ansembe 1,000 ndi amuna ndi akazi ena 500, ambiri a iwo ananena kuti anakhalamo ndi phande m’machitachita akugonana ndi ziŵalo za atsogoleri achipembedzo. Magazini a Time akusimba kuti iye akuyerekezera kuti pafupifupi theka la ansembe a Roma Katolika okwanira 53,000 mu United States akuswa lumbiro lawo la kukhala mbeta. Mogwirizana ndi Sipe, pafupifupi 28 peresenti ya ansembe onse ali ndi maunansi opitirizabe ndi akazi, pamene 10 mpaka 13 peresenti amakhala ndi kugonana ndi amuna achikulire, ndipo 6 peresenti amafuna ana kaamba ka kugonana, makamaka anyamata. Milandu yoposa 100 ya kusadzisunga kwa atsogoleri achipembedzo m’zaka zisanu ndi chimodzi zapitazo yadyera akuluakulu a Katolika pakati pa madola mamiliyoni 100 ndi 300.

Anthu ambiri amaganiza kuti ambiri a mavutowa akanachotsedwa ngati ansembe analoledwa kukwatira. Ena angadabwe kudziŵa kuti palibe paliponse pamene Baibulo limaletsa aminisitala Achikristu a Mulungu kukwatira. Komabe, Tchalitchi cha Katolika, chakhala chikuletsa ansembe kukwatira chiyambire zaka za zana la 12. Mosangalatsa, pamene ankasonya ku mpatuko waukulu kuchoka ku kulambira kowona umene ukabuka pambuyo pa imfa ya atumwi, Paulo analemba kuti ‘ena adzataya chikhulupiriro, ndi kusamala mizimu yosocheretsa ndi maphunziro a ziŵanda, m’maonekedwe onyenga a iwo onena mabodza, . . . akuletsa ukwati.’​—1 Timoteo 4:1-3.

Kodi Nchifukwa Ninji Pali Chiwawa Chochuluka Motero?

Canada anadabwitsidwa ndikuchita mantha kudziŵa kuti Marc Lepine wazaka zakubadwa 25 anapha anthu ambiri pa University ya Montreal. Mwadala iye anapha akazi ophunzira maphunziro a uinjiniya 14, nasiya ophunzira 13 ena ali ovulala, kuphatikizapo amuna 4, asanadziphe yekha. Kunali kumodzi kwa kupha koipitsitsa m’mbiri ya dzikolo. Nduna yaikulu ya boma inalongosola kupha kosalingalirako kukhala “tsoka la anthu lalikulu koposa.”

Mogwirizana ndi The Toronto Star, mu United States, “pakhala kupha kwakukulu koposa 100 chiyambire Nkhondo Yadziko ya II ndipo kochuluka kwachitika m’zaka makumi aŵiri zapitazo.” Komabe, monga mmene bambo wa mmodzi wa minkhole ya Lepine anafunsira mothedwa nzeru kuti: “Kodi nchifukwa ninji pali chiwawa chochuluka motero m’dziko? Kodi nchifukwa ninji anthu amachitirana zinthu zoterezi?”

Kalongosoledwe ka Baibulo ka kuwonjezereka kwa chiwawa m’tsiku lathu nkomveka bwino lomwe. Mtumwi Yohane analemba kuti: “Dziko lonse lapansi ligona mwa woipayo.” (1 Yohane 5:19) Mofanana ndi mpweya umene timaupuma, mzimu woipa wochokera kwa Satana “woipayo,” ukulamulira kuganiza, zokhumba, ndi zochita zenizenizo za anthu ochuluka. Ndi mzimu wake wachipanduko, dyera, ndi kunyada, iye ‘akunyenga dziko lonse.’ (Chibvumbulutso 12:9) Komabe, alambiri owona a Mulungu amatonthozedwa ndi chidziŵitso chakuti ‘dziko lapansi lipita, ndi chilakolako chake; koma iye amene achita chifuniro cha Mulungu akhala ku nthaŵi yonse.’​—1 Yohane 2:17.

Kodi “Mudzi wa Davide” Ulikuti?

Ngati munati mukacheze ku Yerusalemu, ndiyeno nkupempha winawake kuti akuperekezeni ku Phiri la Ziyoni, mwachiwonekere kwambiri mukaperekezedwa ku mtumbira, kapena chitunda, chofutukukira kummwera kwa Mzinda Wakalewo. Chogaŵana malire akummawa ndi Chigwa cha Tyropoeon ndi akumadzulo ndi Chigwa cha Hinomu, chitunda chimenechi chimazindikiridwa ndi Tchalitchi cha Dormition, chokhala ndi tsindwi losongoka.

Komabe, mapu ndi zithunzithunzi zofalitsidwa ndi Watch Tower Society zimaika Phiri la Ziyoni pa chitunda chaching’onoko chokhala kummawa kwa limene tsopano likutchedwa Phiri la Ziyoni. Chitunda chimenechi ncholekanitsidwa ndi chinzake chokhala kumadzulo ndi Chigwa cha Tyropoeon ndikugaŵana malire akummawa ndi Chigwa cha Kedroni.

Kodi ndiati a malo aŵiri ameneŵa amene amazindikiritsa malo enieni a Phiri la Ziyoni loyambirira? Magazini a Biblical Archaeology Review (May/​June 1990) amavomereza kuti “mtumbira wakummawa, kapena chitunda, ndicho chinali Phiri la Ziyoni loyambirira, . . . limene Mfumu Davide analanda Ayebusi.” Pambuyo pakugwa kwake, mudzi wa Ayebusi umenewu unadzadziŵika kukhala “Mudzi wa Davide,” wotchedwanso “Ziyoni.” (2 Samueli 5:7) Biblical Archaeology Review ikunena kuti “ofukula m’mabwinja atsimikiza maganizo, mopanda chikaikiro kuti, chitunda chochepa chimenechi,” kaŵirikaŵiri chotchedwa phiri lakummawa, ndicho Phiri la Ziyoni la m’Baibulo kumene Davide anakhazikitsa malikulu ake olamulira ndi achipembedzo kaamba ka mtundu wa Israyeli.​—2 Samueli 6:11, 12, 17.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena