Mikhole ya Ansembe Ochitira Ana Chisembwere Iulula Nkhani
“MKATI mwa zaka khumi zapitazo, ansembe Achikatolika pafupifupi 400 ananeneredwa ku tchalitchi kapena kwa akuluakulu aboma akwawoko kuti anachitira ana chisembwere,” malinga ndi U.S.News & World Report. Posachedwapa, msonkhano wa dziko lonselo wa opyola m’nkhanza yoteroyo, unachitidwa pafupi ndi Chicago, Illinois. Ambiri anakamba poyera mmene anachitiridwa ndi ansembe ochitira chisembwere ana.
Koma NCR (National Catholic Reporter) ikunena kuti olankhulawo mobwerezabwereza anatchula mutu wina wankhani mkati mwa msonkhano wonsewo kuti: “Nkhanza yoyamba ndiyo ya chisembwere; yachiŵiri ndiponso yopweteka kwambiri, ndiyo ya m’maganizo.” Nkhanza yachiŵiri imeneyi imachitika pamene tchalitchi chikana kutchera khutu kwa ochitiridwa nkhanzawo, pamene chilephera kuwona zinenezo zawo mwamphamvu, mmalomwake chikumatetezera ansembe ochimwawo. “Moyenera kapena mosayenera,” ikusimba motero NCR, “iwo anapereka chithunzi cha atsogoleri achipembedzo Achikatolika kukhala gulu la makhalidwe oipa ndi losocheretsedwa lokonda chabe kutetezera malo awo ndi ulamuliro mmalo mwa kutumikira zosoŵa za olambira wamba.” Okamba nkhani ochuluka anayerekezera kwambiri ndi Reformation (Kulinganizanso), kumene kunagaŵa tchalitchi kotheratu m’zaka za zana la 16.
Malinga nkunena kwa Richard Sipe, wansembe wakale wina anasintha nakhala wochiritsa maganizo ndi katswiri wothandiza ochitiridwa chisembwere ndi atsogoleri achipembedzo Achikatolika, konseku nkukana mlandu kovumbula “kuloŵetsedwamo, kwakuya ndi kodzidziŵira yekha m’vutolo.” Iye anawonjezera kuti: “Tchalitchi chimadziŵa ndipo chakhala chikudziŵa zochuluka kwanthaŵi yaitali ponena za machitachita achisembwere a ansembe ake. Mwadala, chanyalanyaza, chalekerera, chaphimba ndipo chanama ponena za ukulu wa machitachita achisembwere a ansembe ake.”
Chotero, nzosadabwitsa kuti ambiri amene anapyola m’nkhanza imeneyi akupereka tchalitchi kukhoti. NCR ikugwira mawu loya wina amene amasamalira milandu yoteroyo kukhala akunena kuti pali milandu ya ansembe ochitira chisembwere ana pa lililonse la madera okwanira 188 oyanganiridwa ndi ansembe mu United States. Iye akuti ndalama zolipirira milandu yosapita ku khoti zakwera kufika pa $300,000 mlandu uliwonse. U.S.News & World Report ikunena kuti milandu yoteroyo yatayira kale tchalitchi ndalama zokwanira $400,000,000, chiŵerengero chimene chingawonjezereke mpaka $1,000,000,000 pofika m’chaka cha 2000. Ndipo Canadian Press posachedwa inasimba kuti amene anapyola m’nkhanza yochitira ana chisembwere pafupifupi 2,000 m’nyumba za tchalitchi zosungira ana amasiye ndi za odwala maganizo zokwanira 22 mu Quebec, akuimba mlandu magulu achipembedzo asanu ndi limodzi wowalipiritsa $1,400,000,000.
Komabe, nzosangalatsa kuwona kuti loya wa ku United States wotchulidwa poyambapo, amene akuimira mikhole 150 ya ansembe ochitira chisembwere ana m’maboma 23, akunena kuti sipanakhale wobweretsa mlandu kwa iye amene anafuna kupereka mlandu ku khoti. Aliyense choyamba anafuna kuti mlandu uweruzidwe “m’tchalitchi ndi ansembe.” NCR ikugamula kuti: “Zikuwoneka kuti, opyola m’nkhanzawo samayambirira kupita kukhoti, koma amatero ngati palibenso njira ina.”