Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w91 4/1 tsamba 16-19
  • Kufunafuna Mulungu kwa Anthu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kufunafuna Mulungu kwa Anthu
  • Nsanja ya Olonda—1991
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Chiŵiya Chogwira Ntchito
  • Maziko a Maphunziro Abaibulo
  • Mmene Mungayankhire Oyembekezera Kuimitsa Kukambitsirana
    Kukambitsirana za m’Malemba
  • Kodi Zipembedzo Zonse Zimalambira Mulungu Mmodzi?
    Nsanja ya Olonda—2009
  • Kodi Mukanena Chiyani kwa Mhindu?
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1999
  • Chifukwa Chake Anthu Ambiri Amakayikira Zoti Zipembedzo Zingagwirizanitse Anthu Onse
    Nsanja ya Olonda—2005
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1991
w91 4/1 tsamba 16-19

Kufunafuna Mulungu kwa Anthu

KODI nchifukwa ninji ifeyo, monga Mboni za Yehova, tapatsidwa “chinenero choyera”? Ndithudi, sikuti tichisunge kwa ife eni. Ndipo siziri tero kuti tisangalale ndi njira ya moyo yosangulutsa yofanana ndi njira yakachitidwe kazinthu yofeŵa, yogonjera ya Chikristu Chadziko. Mmalomwake, ziri choncho kotero kuti ‘onse aitanire padzina la Yehova, kuti amtumikire mogwirizana.’ (Zefaniya 3:9, NW) Inde, chinenero choyera chimaloŵetsamo kugwira ntchito mogwirizana ndi mamiliyoni a abale ndi alongo athu Achikristu​—ochokera m’mafuko onse, mitundu, ndi manenedwe​—amene akulalikira mbiri yabwino mokhulupirika mapeto asanadze.​—Marko 13:10; Aroma 13:11; Chibvumbulutso 14:6, 7.

Kulalikira kwathu lerolino nthaŵi zina kumapereka zitokoso zachilendo. Kodi nchifukwa ninji ziri choncho? Mkati mwa zaka za zana la 20 lino, kwakhala kuyendayenda kwakukulu kwa anthu kochititsidwa ndi nkhondo, chitsenderezo, mavuto achuma, ndi zifukwa zina. Monga chotulukapo, anthu a zinenero ndi zipembedzo zambiri asinthira ku miyambo ina yosakhala yawo. Chotero, zitaganya zazikulu za Ahindu, Abuda, ndi Asilamu zasamukira ku dziko la Kumadzulo. Pamene tigaŵira chinenero choyera kunyumba ndi nyumba, timakumana nawo anthuwa. Nthaŵi zina timadodometsedwa chifukwa chakuti timadziŵa zochepa zokha ponena za chiyambi chawo chachipembedzo. Kodi tingachitenji ponena za icho?​—Yerekezerani ndi Machitidwe 2:5-11.

Kodi tingagaŵire motani chowonadi kwa Msilamu kapena Myuda? Kodi iwo amasiyana motani? Kodi nchiyani chimene Mhindu kwenikweni amakhulupirira? Kodi nchifukwa ninji Asikh amavala nduŵira? Kodi bukhu lawo lopatulika ndiliti? Kodi Mbuda amasiyana motani ndi Mhindu? Kodi Ashinto a ku Japani amakhulupiriranji? Kodi Atao a ku China kapena Akonfyushani amakhulupirira Mulungu?a Kodi Myuda wa Orthodox amasiyana motani ndi Myuda wa Reform kapena Myuda wa Conservative? Kuti tifikire anthu osiyanasiyana kwakukulu ameneŵa, choyamba tiyenera kumvetsetsa lingaliro lawo ndiyeno nkudziŵa mmene tingawatsogozere kwa Mulungu wowona, Yehova m’njira yachifundo ndi yochenjera.​—Machitidwe 17:22, 23; 1 Akorinto 9:19-23; Akolose 4:6.

Kuti itithandize kukhala ndi kumvetsetsa kwabwinopo kwa zipembedzo zina, ziphunzitso zawo, ndi mbiri yawo yakumbuyo, Watch Tower Society inatulutsa kuzungulira dziko lonse bukhu latsopano lokhala ndi mutu wakuti Mankind’s Search for God pa Misonkhano ya “Chinenero Choyera” mkati mwa 1990. Okonzekeretsedwa ndi chiŵiya chimenechi, tidzakhala okhoza kulalikira bwinopo kwa anthu a dziko losakhala Lachikristu limodzinso ndi a m’Chikristu Chadziko.

Chiŵiya Chogwira Ntchito

Bukhu lamasamba 384 limeneli liri ndi mitu 16 yomwe imasimba mbiri yakale ya kufunafuna Mulungu kwa anthu kwa zaka zoposa zikwi zisanu ndi chimodzi zapitazo. Limayankha mafunso mazana ambiri onena za zipembedzo za dziko. Nazi zitsanzo za ena a iwo: Kodi ndi mfundo zotani zimene kaŵirikaŵiri zimatsimikizira chipembedzo cha munthu? Kodi nchifukwa ninji sikulakwa kusanthula zikhulupiriro zina? Kodi nkufanana kotani komwe kulipo pakati pa chikhulupiriro cha Roma Katolika ndi Chibuda? Kodi nthanthi zimachita mbali yotani m’zipembedzo zambiri? Kodi nchifukwa ninji anthu ambiri amakhulupirira matsenga, kukhulupirira mizimu, ndi kupenda nyenyezi? Kodi nchifukwa ninji Ahindu ali ndi milungu yachimuna ndi yachikazi yambiri? Kodi Asikh amasiyana motani ndi Ahindu? Kodi Buddha anali yani, ndipo kodi anaphunzitsanji? Kodi nchifukwa ninji Chishinto chiri kwakukulukulu chipembedzo cha ku Japani? Kodi nchifukwa ninji Ayuda ali ndi lamulo lapakamwa limodzinso ndi lolembedwa? Kodi timadziŵa motani kuti Kristu sali nthano? Kodi Korani imasiyana motani ndi Baibulo? Kodi nchifukwa ninji Akatolika amanena kuti Petro anali papa woyamba? Kodi nchifukwa ninji wansembe Wachikatolika Luther anapatuka kuchoka ku Tchalitchi cha Roma Katolika?

Mafunso angomkirabe, ndipo bukhuli nlodzala ndi mayankho kotero kuti tingalalikire mogwira mtima koposa kwa anthu okhala ndi ziyambi zosiyanasiyana zimenezi zachipembedzo. Bukhuli limazindikiritsa kuti anthu ambiri ali ndi chipembedzo chawochawo ndikuti chipembedzo ndi nkhani yaumwini kwenikweni. Komabe, pa tsamba 8, ilo limati: “Kwakukulukulu makolo athu ndi achibale amakhomereza malingaliro achipembedzo ndi amakhalidwe m’maganizo mwathu kuchokera kuukhanda. Monga chotulukapo, kaŵirikaŵiri timatsatira malingaliro achipembedzo a makolo ndi agogo athu.” Ichi chitanthauza kuti “m’zochitika zambiri anthu ena amatisankhira chipembedzo chathu. Zangodalira pa kumene ndi pamene tinabadwa.”​—Yerekezerani ndi Afilipi 3:4-6.

Ndiyeno bukhulo limadzutsa funso loyenera. “Kodi nkwanzeru kulingalira kuti chipembedzo chopatsidwa pa kubadwa kwa munthu ndicho chowonadi chenicheni?” Chotero, munthu aliyense akulimbikitsidwa kusanthula zipembedzo zina ndi maganizo opanda tsankho. Monga kwalongosoledwa pa tsamba 10 kuti: “Kumvetsetsana malingaliro kungatsogolere ku kulankhulana ndi kukambitsirana kothandiza pakati pa anthu azikhulupiriro zosiyana.” Ilo likupitiriza kuti: “Zowona, anthu angatsutsane mwamphamvu ponena za zikhulupiriro zawo zachipembedzo, koma palibe chifukwa chodera munthu kokha chifukwa chakuti iye ali ndi lingaliro losiyana.”​—Mateyu 5:43, 44.

Funso lalikulu lomwe likubuka m’bukhu lonselo nlakuti, Kodi munthu ali ndi moyo wosakhoza kufa umene umapulumuka pa imfa yake ndi kupitiriza ndi moyo pambuyo pa imfa? M’mipangidwe yosiyanasiyana, pafupifupi chipembedzo chirichonse chimaphunzitsa lingaliro limenelo. Monga momwe bukhu la Mankind’s Search for God (tsamba 52) likunenera kuti: “Pofunafuna Mulungu, munthu wagwira pachabe, napusitsidwa ndi chinyengo cha kusakhoza kufa kwa moyo. . . . Chikhulupiriro mu moyo wosakhoza kufa kapena zikhulupiriro zosiyanasiyana zotulukamo ndi choloŵa chomwe chapatsidwa kwa ife m’zaka zikwi zambiri.” Mafunso ena ngakuti: Kodi aliko malo otchedwa helo kumene miyoyo imazunzidwa? Kodi chiyembekezo chowona kaamba ka akufa nchotani? Kodi kuli Mulungu mmodzi, kapena kodi kuli milungu yambiri?​—Genesis 2:7; Ezekieli 18:4.

Maziko a Maphunziro Abaibulo

Mwadongosolo lotsatira zaka pamene zipembedzo zazikulu za anthu zinakhalapo padziko, bukhuli limafotokoza chiyambi cha zipembedzozo​—Chihindu, Chibuda, Chitao, Chikonfyushani, Chishinto, Chiyuda, Chikristu, Chikristu Chadziko, ndi Chisilamu. M’mutu uliwonse mabuku opatulika a zipembedzo zimenezi agwidwa mawu kotero kuti wokhulupirira wowona mtima aliyense angafufuze payekha zogwidwa mawuzo. M’mutu wonena za Chisilamu, matembenuzidwe atatu a Chingelezi osiyanasiyana a Korani agwiritsiridwa ntchito. Matembenuzidwe aposachedwapa a Jewish Publication Society a Tanakh​—A New Translation of the Holy Scriptures agwidwa mawu m’mutu wonena za Chiyuda.​—Yerekezerani ndi Machitidwe 17:28; Tito 1:12.

Kodi nchiyani chomwe chirimo kaamba ka osakhulupirira kukhalako kwa Mulungu ndi osadziŵa? Mutu 14 umafotokoza kusakhulupirira Mulungu kwamakono ndi chifukwa chake Mboni za Yehova zimadziŵira kuti Mulungu aliko. M’mutu uliwonse, woŵerenga akutsogozedwa ku Baibulo. Chotero, mwakugwiritsira ntchito bukhu limeneli la Mankind’s Search for God, tiri okonzekeretsedwa bwinopo kuyambitsa maphunziro Abaibulo ndi anthu achikhulupiriro chirichonse kapena ndi awo omwe amanena kuti alibe chipembedzo chirichonse. Limachita ndi chipembedzo chirichonse mwaulemu ndi mochenjera, koma limadzutsa mafunso omwe angatsogolere munthu kwa Yehova ndi chowonadi. Kwa awo amene akufunafuna Mulungu mofunitsitsa, bukhuli lidzakhala dalitso lenileni.​—Salmo 83:18; Yohane 8:31, 32; 2 Timoteo 3:16, 17.

Mabokosi amalangizo ophunzitsira aphatikizidwa m’mutu uliwonse. Mwachitsanzo, pa masamba 226 ndi 227, pali bokosi lokhala ndi mutu wakuti “Judaism​—A Religion of Many Voices” limene limafotokoza magaŵano aakulu opezeka m’chipembedzo cha Chiyuda. Pansi pa mutu wakuti “Hinduism​—A Search for Liberation,” pali bokosi pa masamba 116 ndi 117, lakuti “Hinduism​—Some Gods and Goddesses.” Ilo limapereka ndandanda ya milungu yoŵerengeka yokha yoposa pa mamiliyoni 330 yolambiridwa ndi Ahindu. Kodi Abuda amakhulupirira Mulungu monga momwe dziko la Kumadzulo limamvetsetsera liwulo? Bokosi lakuti “Buddhism and God” pa tsamba 145 limayankha funsolo. Bukhuli lirinso ndi chosonyezera chothandiza chofunirapo mitu yaikulu mofulumira. Mbiri yonena za magwero aakulu ogwiritsiridwa ntchito m’kufufuza irinso maziko oŵerengera zowonjezereka ngati wina angafune umboni wowonjezereka.

Bukhuli liri ndi zithunzithunzi ndi mafanizo zoposa 200, koma izo sizirimo kaamba ka kukometsera. Fanizo lirilonse liri ndi mfundo yophunzitsa yomveketsa mowonjezereka chipembedzo chomwe chikufotokozedwa. Mwachitsanzo, patsamba 238 pali mpambo wa zithunzithunzi zomwe zikufotokoza mafanizo amene Yesu anaphunzitsa. Kwinanso, kuli mpambo wa zithunzithunzi zisanu zimenenso zikufotokoza mwafanizo mbali zosiyanasiyana za uminisitala wa Kristu​—zozizwitsa zake, kusandulika kwake, imfa yake yansembe, ndi kutumiza kwake ophunzira ake kukalalikira m’dziko lonse.

Patsamba 289 pali tsatanetsatane wa zithunzithunzi zomwe zidzakondweretsa Asilamu. Izo zimapereka wopenyererayo ku Mecca, kuloŵa m’msikiti waukulu momwe muli Kaaba kenaka ku mwala wakuda weniweniwo womwe Asilamu amalemekeza. Kulambira kosiyanasiyana kwa Chibuda kwafotokozedwa mwafanizo patsamba 157. Ahindu adzakondweretsedwa kuwona zithunzithunzi za milungu yawo yotchuka Ganesa ndi Krishna pamasamba 96 ndi 117.

Aminisitala Achikristu oyeneretsedwa kuzungulira dziko anafunsidwa kotero kuti malongosoledwe aukatswiri achipembedzo chirichonse chachikulu afikiridwe. Mwachitsanzo, chidziŵitso chothandiza chinachokera ku Israyeli kaamba ka mitu yonena za Chiyuda ndi chikhulupiriro cha Bahaʼi. Mboni m’maiko a Chisilamu zinafufuza mosamalitsa zamkati mwa mutu wonena za Asilamu. Chitsogozo chopindulitsa chonena za Ahindu, Asikh, ndi Ajain chinachokera ku India. Aminisitala a Kum’mawa anatsimikizira kuti mutu wonena za Chishinto unali wolongosoka, ndipo anaperekanso malangizo pa Chibuda, Chitao, ndi Chikonfyushani.

Chifukwa cha kufotokoza kosamalitsa kwa chipembedzo chirichonse m’bukhuli, awo okhala nalo m’chinenero chawo adzakhoza kuyambitsa maphunziro Abaibulo m’mutu woyenerana ndi chiyambi chachipembedzo cha munthu aliyense. Ndiyeno angafune kunka ku mutu wolongosola chiyambi cha Chikristu choyambirira ndi zifukwa zokhulupirira kuti Kristu ali Woimira wowona wa Mulungu, yemwe wagwiritsiridwa ntchito kuyandikitsa anthu kwa Mulungu. Mulinso mitu imene inalongosola mmene mpatuko unayambira, wotulukapo magaŵano ambiri ndi timagulu tampatuko ta Chikristu Chadziko. Mitu iŵiri yotsirizira imasonyeza mmene kulambira kowona kwabwezeretsedwera m’masiku ano otsiriza ndi chimene chidzachitika posachedwapa kwa Babulo Wamkulu, ulamuliro wadziko wachipembedzo chonyenga wa Satana. Pambuyo pachimenecho, dziko latsopano ndi chiyembekezo cha Baibulo chachiukiriro chikugogomezeredwa.​—Yohane 5:28, 29; 12:44-46; 14:6; Chibvumbulutso 21:1-4.

Iri ndibukhu lomwe liyeneradi kuthandiza ambiri padziko lonse kuyandikira kwa Mulungu, monga momwe Yakobo analongosolera m’mutu 4 wa kalata yake, vesi 8 kuti: ‘Yandikirani kwa Mulungu, ndipo adzayandikira kwa inu. Sambani m’manja, ochimwa inu; yeretsani mitima, a mitima iŵiri inu.’ Inde, monga momwe Yesaya akunenera kuti: “Funani Yehova popezeka Iye, itanani Iye pamene ali pafupi.”​—Yesaya 55:6; Yohane 6:44, 65.

Tatiyeni tonse tipitirizebe kutembenuzidwira ku njira yolondola, kwa Mfumu Ambuye wachilengedwe chonse, Yehova Mulungu. Ndipo ndithandizo la bukhuli, Mankind’s Search for God, tatiyenitu tithandize zikwi zowonjezereka kulambira Yehova ‘mu mzimu ndi m’chowonadi.’ (Yohane 4:23, 24) Tatiyeni tilimbikire kufunafuna ofuna chowonadi ndi kuwauza za Mulungu wachowonadi, popeza kuti, iye ndithudi, angapezedwe!

[Mawu a M’munsi]

a “Tao” limatchulidwa kuti dow; kumveka mofanana ndi now.

[Zithunzi patsamba 17]

Munthu wafunafuna Mulungu m’njira zambiri

[Chithunzi]

Akatolika owona mtima amatembenukira kwa Mariya

[Chithunzi]

Ahindu amalemekeza mtsinje wa Ganges

[Mawu a Chithunzi]

Harry Burdich, Transglobe Agency, Hamburg

[Chithunzi]

Ayuda ena opembedza amavala njirisi

[Mawu a Chithunzi]

GPO, Yerusalemu

[Chithunzi]

Amuna Achisilamu amapita paulendo wa- chipembedzo ku Mecca

[Mawu a Chithunzi]

Camerapix

[Chithunzi]

Ambiri amalambira Buddha

[Zithunzi patsamba 18]

Yesu anagwiritsira ntchito mafanizo kuthandiza anthu kupeza Mulungu wowona

[Mawu a Chithunzi]

Pictorial Archive (Near Eastern History) Est.

[Mawu a Chithunzi]

Pictorial Archive (Near Eastern History) Est.

[Mawu a Chithunzi]

Pictorial Archive (Near Eastern History) Est.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena