Chinenero Choyera cha Mitundu Yonse
“Pakuti pamenepo ndidzapereka kwa mitundu kusinthira ku chinenero choyera, kuti iwo onse aitanire padzina la Yehova, kuti amtumikire mogwirizana.”—ZEFANIYA 3:9, “NW.”
1, 2. (a) Pokwaniritsa Zefaniya 3:9, kodi Yehova akuchitanji m’tsiku lathu? (b) Kuti timvetsetse mmene ulosi wa Zefaniya umatiyambukirira, kodi ndimafunso otani amene afunikira kuyankhidwa?
YEHOVA MULUNGU akukwaniritsa m’tsiku lathu ntchito imene iridi yozizwitsa. Iye akugwirizanitsa anthu amitundu yonse. Monga momwe iye adaneneratu kalekale m’Mawu ake Opatulika, iye akuchita zimenezo mwakuwaphunzitsa chinenero chatsopano.—Zefaniya 3:9, NW.
2 Kodi chinenero chimenecho nchiyani? Kodi nchifukwa ninji chiri chofunika? Kodi kuchiphunzira icho kumafunanji kwa ife mwaumwini?
Mphatso ya Kulankhula
3. (a) Kodi Adamu adapatsidwa mphatso yozizwitsa yotani? (b) Kodi Adamu ankalankhula chinenero chiti?
3 Luso la kulankhuzana kupyolera m’malankhulidwe liri mphatso yaumulungu imene imasiyanitsa anthu ndi nyama zolengedwa zonse. Munthu woyamba, Adamu, analengedwa ndi maganizo omwe anali okhoza kulingalira mwanzeru. Iye anapatsidwa mphamvu zotulutsa mawu, lirime, ndi milomo zomwe anagwiritsira ntchito kulankhula, limodzinso ndi mpambo wa mawu ndi luso la kupanga mawu atsopano. Adamu anakhoza kumva pamene Yehova analankhula naye, ndipo Adamu, nayenso akanakhoza kufotokoza malingaliro akewo mwa mawu. (Genesis 1:28-30; 2:16, 17, 19-23) Chinenero chomwe Adamu anapatsidwa mwachidziŵikire chinali chomwe pambuyo pake chinadzadziŵika kukhala Chihebri. Pafupifupi zaka 1,757 zoyambirira za kukhalapo kwa anthu, anthu onse anapitirizabe kulankhula chinenero chimodzi chimenecho.—Genesis 11:1.
4. Kodi zochitika za m’masiku a Nimrode zinayambukira motani chinenero cha anthu?
4 Kenaka, m’masiku a Nimrode, ndi cholinga chofuna kusokoneza zoyesayesa za anthu oipa, Yehova anasokoneza chinenero cha onse omwe anadzilola kugwirizanitsidwa m’kukhala ndi phande kumanga nsanja ya Babele. (Genesis 11:3-9) Kukuwonekera kuti choyamba Yehova anafafaniza chikumbukiro chonse cha chinenero chawo chimodzi ndiyeno anaika m’malingaliro mwawo zinenero zatsopano. Izi sizinaloŵetsemo mpambo wa mawu watsopano wokha komanso magalamala atsopano ndi njira zatsopano zoganizira. Kuchokera m’zinenero zomwe Yehova anaziyambitsa pa Babele, papangidwa zina mwapang’onopang’ono kufikira m’tsiku lino, mogwirizana ndi maphunziro azinenero, zinenero zikwi zitatu zikulankhulidwa padziko lonse lapansi.
5. Kodi tingadziŵe motani chimene “kusinthira ku chinenero choyera” kumaloŵetsamo?
5 Kwa anthu amene akulankhula zinenero zonsezi, kodi “kusinthira ku chinenero choyera” (NW) kukafunikira kuti asiye chinenero chawo ndi kuphunzira chinenero choyambirira chimene Mulungu anampatsa Adamu? Mikhalidwe yokhalapo poperekedwa ulosiwo imatithandiza kuyankha funso limeneli.
Kufunikira kwa Chinenero Choyera
6-8. (a) Kodi ndi mkhalidwe wachipembedzo wotani umene unachitika m’Yuda ulosi wa Zefaniya 3:9 usanaperekedwe? (b) Kodi ndi mkhalidwe wotani womwe unawanda m’mitundu yozungulira Yuda?
6 Ufumu wa Yuda unali utangolamulidwa choyamba ndi Manase ndipo kenaka ndi Amoni, amene anamangira Baala maguwa ansembe, nagwiritsira ntchito ula, ndi kupititsa patsogolo machitachita okhulupirira mizimu. (2 Mafumu 21:1-6; 2 Mbiri 33:21-23) Monga chotulukapo, mkati mwa kulamulira kwa mwana wa Amoni ndi mloŵa mmalo, Yosiya, Yehova anatumiza mneneri wake Zefaniya kukachenjeza kuti chiweruzo chaumulungu chikaperekedwa m’dzikolo.—Zefaniya 1:1, 2.
7 Ngakhale kuti Ayuda anadziŵa kuchokera m’mbiri yawo ndi m’Malemba owuziridwa kuti Yehova ndiye Mulungu wowona, iwo anamwerekera m’miyambo yoipa ya kulambira Baala. Iwo anagwadira dzuŵa ndi mwezi ndi nyenyezi zakumwamba, komwe kunali kuswa kwachindunji lamulo la Mulungu. (Deuteronomo 4:19; 2 Mafumu 23:5) Choposa pa zonsezi, iwo anali kutenga mbali m’kachitidwe ka kusakanizana zikhulupiriro, akumachita ngati kuti zipembedzo zonse zinali zofanana, mwakupanga malumbiro awo ponse paŵiri kwa Yehova ndi m’dzina la mulungu wonyenga Malcam. Maganizo awo anali akuti ‘Yehova sachita chokoma, kapena kuchita choipa.’ (Zefaniya 1:4-6, 12) Ponena za mitundu yozungulira Yuda, onsewo anali ndi mbiri yotsutsana ndi Yehova ndi anthu ake, chotero nawonso anali pamzere wolandira chiweruzo chaumulungu.—Zefaniya 2:4-15.
8 Ndimkhalidwe wa zochitika zoterozo umene unachititsa Yehova kuneneratu kuti ‘akapereka kwa mitundu kusinthira ku chinenero choyera, kuti iwo onse aitanire padzina la Yehova, kuti amtumikire mogwirizana.’ (Zefaniya 3:9, NW) Nangano, kodi chinenero choyeracho nchiyani?
9. (a) Kodi nchifukwa ninji chinenero choyera sichiri Chihebri kapena Mawu olembedwa a Mulungu okha? (b) Kodi chinenero choyeracho nchiyani, ndipo kodi chimayambukira motani miyoyo ya anthu amene amachilankhula?
9 Kodi nchinenero cha Chihebri? Ayi; anthu a Yuda anali nacho kale, koma zinthu zomwe anali kunena ndi kuchita mwachidziŵikire sizinali zoyera ndi zowongoka m’maso mwa Yehova. Ndiponso chinenero choyera sindicho Mawu olembedwa a Mulungu okha. Iwo anali nawonso. Koma chomwe anafunikira chinali kumvetsetsa koyenera kwa chowonadi chonena za Mulungu ndi zifuno zake, ndipo Yehova yekha ndiye akapereka chimenecho kupyolera mwa mzimu wake.Pamene iwo anaphunzira kulankhula chinenero choyera chimenecho, kulingalira kwawo, kalankhulidwe kawo, ndi mkhalidwe wawo, zonsezo zikazikidwa pa kuzindikira Yehova monga Mulungu yekha wowona. (Zefaniya 2:3) Iwo akaika chikhulupiriro chawo mwa iye, ndi kuchilikiza kotheratu ulamuliro wake. Ichi nchofunika mwapadera kwa ife lerolino. Chifukwa ninji?
Awo Amene Apatsidwa Chinenero Choyera
10. Kodi ulosi wa Zefaniya 3:9 unayenera kukwaniritsidwa mkati mwa nyengo ya nthaŵi iti?
10 Posonya ku kukwaniritsidwa kwa ulosi panyengo ya nthaŵi yakutiyakuti, Zefaniya 3:9, (NW) akuti: “Pakuti pamenepo ndidzapereka kwa mitundu kusinthira ku chinenero choyera.” Kodi zimenezo zidzachitika liti? Vesi 8 likuyankha kuti idzakhala nthaŵi imene Yehova ‘akusonkhanitsa amitundu,’ iye ‘asanawatsanulire mkwiyo wake wonse waukali,’ mpamene akupatsa ofatsa a dziko lapansi kusinthira ku chinenero choyera.
11. (a) Kodi ndikukwaniritsidwa kuŵiri kuti kumene Zefaniya 3:9 anakhala nako zisanafike nthaŵi zamakono? (b) Kodi kukwaniritsidwa kwake lerolino nkosiyana motani?
11 M’masiku a Mfumu Yosiya, Yehova asanalole makamu a Babulo kupereka chiweruzo, ambiri analeka kulambira konyenga ndipo, mmalomwake, anatumikira Yehova. (2 Mbiri 34:3-33) Kachiŵirinso, m’zaka za zana loyamba C.E., Yerusalemu asanawonongedwe ndi Aroma, anthu zikwi zambiri anaphunzira chowonadi chonena za Mulungu ndi chifuno chake ndi kukhala ogwirizana mu utumiki wake. Panthaŵiyo chinenero cha chowonadi chinkalemeretsedwa kwakukulu ndi zinthu zimene Yesu Kristu anachita m’kukwaniritsa chifuno cha Yehova. Koma ndi m’tsiku lathu pamene ulosi wa Zefaniya ukukwaniritsidwa pamlingo wa dziko lonse. Mitundu yonse tsopano ikusonkhanitsidwira ku nkhondo ya tsiku lalikulu la Mulungu Wamphamvuyonse pa Armagedo. (Chibvumbulutso 16:14, 16) Kusonkhanitsa kumeneko kwakhala kukuchitika chiyambire kubadwa kwa Ufumu mu 1914. Ndipo ndi m’nyengo imodzimodziyo mmene Yehova wakhala akupereka kwa anthu padziko lonse kusinthira ku chinenero choyera m’kukwaniritsa ulosiwu. Kuphunzira chinenerocho nkofunika koposa chifukwa chakuti opulumuka a chisautso chachikulu chikudzacho adzakhala anthu omwe mowonadi apanga chinenero choyeracho kukhala chinenero chawo.—Yoweli 2:32.
12. (a) Kodi masomphenya olembedwa pa Yesaya 6 ali ndi kugwirizana kotani ndi ulosi wonena za chinenero choyera? (b) Kodi nchifukwa ninji otsalira odzozedwa anafunikira thandizo ngati akanati apitirize kukhala ovomerezeka kaamba ka utumiki wa Yehova?
12 Mogwirizana ndi ichi, kunali kuchiyambiyambi kwa nyengo yotsatira Nkhondo Yadziko ya I pamene Yehova anayamba kutsegulira atumiki ake odzozedwa maso a kuzindikira masomphenya ozizwitsa olembedwa mu Yesaya mutu 6. (Mavesi 1-4) Masomphenyawa amagogomezera kufunika kwathu kwa milomo yoyera ndi cholinga chotumikira Yehova molandirika. Amasonyeza kuti, m’lingaliro lokwezeka, Yehova ngwoyera. Atumiki ake ayeneranso kusonyeza mkhalidwe umenewo. (1 Petro 1:15, 16) Koma otsalira odzozedwa anafunikira thandizo m’zimenezi. Mkati mwa Nkhondo Yadziko ya I, iwo anadzilola okha kumlingo wakutiwakuti kuikidwa mawanga mwakuloŵetsedwa m’zochitika zadziko. “Kuopa Yehova kuli mbe,” kapena kwaudongo, koma iwo analola kuopa munthu ndi magulu aumunthu kuyambukira milomo yawo, kuleketsa kulalikira kwawo Mawu a Mulungu pamlingo waukulu. (Salmo 19:9) Mwakugwirizana kwawo ndi Chikristu Chadziko, otsalirawo anali adakali odetsedwabe ndi miyambo yake ina ndi machitachita.
13, 14. (a) Kodi otsalira anasonyeza motani mkhalidwe wabwino, ndipo kodi Yehova anawachitiranji? (b) Kodi Yehova anawapatsa motani otsalira chinenero choyera?
13 Pozindikira mkhalidwe wawo, otsalirawo ananena monga mmene ananenera mneneri Yesaya kuti: ‘Tsoka kwa ine! Chifukwa ndathedwa; chifukwa ndiri munthu wa milomo yonyansa, ndikhala pakati pa anthu a milomo yonyansa; chifukwa kuti maso anga awona Mfumu, Yehova wa makamu.’ (Yesaya 6:5) Iwo anazindikira kuti mkhalidwe wawo unali wosalandirika. Iwo sanawumirire mofooka kulondola njira yolakwa kapena kukana kwamtu wagalu kulandira chidzudzulo cha Yehova. Iwo sanagwirizane ndi atsogoleri achipembedzo pamene anapereka utumiki wapakamwa ku Ufumu wa Mulungu ndipo kenaka ndikuvomereza Chigwirizano cha Amitundu ngati kuti chinalidi mbali ya Ufumu umenewo.
14 Chifukwa cha mkhalidwe wolapa wa otsalira odzichepetsa ameneŵa, Yehova m’chisomo chake anapitiriza kuyeretsa milomo yawo. Yesaya 6:6, 7 akutiuza kuti: ‘Pompo anaulukira kwa ine mmodzi wa aserafi, ali nalo khala lamoto m’dzanja mwake, limene analichotsa ndi mbaniro pa guwa la nsembe; nakhudza nalo kukamwa kwanga nati, Taona ichi chakhudza milomo yako; ndipo mphulupulu zako zachotsedwa, zochimwa zako zaomboledwa.’ Unali uthenga woyeretsa wochokera m’Mawu a Mulungu umene unawononga monga moto miyambo ndi ziphunzitso za anthu. Iwo unachotsa m’mitima yawo kuopa anthu ndi kuuloŵa mmalo ndi changu chotentha chogwiritsira ntchito milomo yawo kulemekeza Yehova. Chotero Yehova ankakwaniritsa lonjezo lake la ‘kupereka kwa mitundu kusinthira ku chinenero choyera [kwenikweni, mlomo waudongo], kuti iwo onse akaitanire padzina la Yehova.’—Zefaniya 3:9.
15. Kodi otsalira anavomereza motani mogwirizana ndi chifukwa chimene Yehova anawapatsira chinenero choyera?
15 Chotero pamene gulu la Yesaya m’nthaŵi zamakono linayamba kumva mawu a Yehova akufunsa, monga momwe alembedwera pa Yesaya 6:8 kuti: “Ndidzatumiza yani, ndipo ndani adzatimukira ife?” iwo mosangalala anayankha kuti: “Ndine pano; munditumize ine.” Sichinali chokhweka kwa onsewo kuyamba uminisitala wapoyera, koma anafuna kugwiritsidwa ntchito ndi Mulungu monga anthu a dzina lake. Mzimu wake unawalimbitsa iwo. Chiŵerengero chawo chinakula.
16. (a) Kodi ndizotulukapo zosayembekezereka zotani zimene kulalikira kwa otsalira kunatuta? (b) Kodi ndimotani mmene khamu lalikulu limaperekera umboni wakuti nalonso tsopano likulankhula chinenero choyera?
16 M’kupita kwa nthaŵi chinakhala chowonekeratu kuti kulalikira kwawo kunkabala zotulukapo zosayembekezereka. Kupyolera mwa iwo, Yehova ankathandiza gulu lina kuphunzira chinenero choyera. (Yesaya 55:5) Ameneŵa analibe chiyembekezo cha moyo wakumwamba, koma anazindikira kuti kukhala atsamwali a otsalira oloŵa Ufumu ndikutumikira mogwirizana nawo monga alengezi a Ufumu wa Mulungu kunali mwaŵi. Mopita patsogolo, ameneŵa atuluka ‘mwa mtundu uliwonse, ndi mafuko ndi anthu ndi manenedwe’ kufikira tsopano akupanga ‘khamu lalikulu’ lomafika m’mamiliyoni. Kalankhulidwe komwe kamatuluka mkamwa mwawo sindiko mtundu wina uliwonse womwe ungawazindikiritse iwo ndi mbali zirizonse zogaŵanikana zadziko. Iwo sakuzika ziyembekezo zawo pa munthu aliyense kapena gulu laumunthu lirilonse. Mmalomwake, ‘iwo akufuula ndi mawu aakulu, nanena, Chipulumutso kwa Mulungu wathu wakukhala pampando wachifumu, ndi kwa Mwanawankhosa.’—Chibvumbulutso 7:9, 10.
Chimene Kuphunzira Chinenerocho Kumafuna kwa Ife
17. Kodi nchifukwa ninji kuli kofunika kuti tiphunzire chinenero choyera bwino lomwe ndikuwongolera luso lathu lakuchigwiritsira ntchito?
17 Mosasamala kanthu za utali womwe takhala ogwirizana ndi gulu la Yehova, pali zambiri zomwe tingachite kuwongolera chidziŵitso chathu cha chinenero choyera ndi maluso athu a kuchigwiritsira ntchito bwino. Nkofunika koposa kupanga kuyesayesa kwa kuchita zimenezo. Chifukwa ninji? Chifukwa chakuti ichi nchisonyezero cha kukonda kwathu chowonadi.
18, 19. (a) Kuyambira pachiyambi penipeni, kodi nchifukwa ninji kuli kofunika kukulitsa chikondi cholimba kaamba ka chowonadi? (b) Kodi nchifukwa ninji kuli kofunika kupitirizabe kuchisungabe chikondicho?
18 Poyamba, chikondi choterocho chimathandiza kutsegula maganizo ndi mtima wa munthu kotero kuti iye akhale wokhoza kumvetsetsa chimene chiri m’malemba amene akusonyezedwa kwa iye; chimamsonkhezera iye kuyandikira kufupi ndi Yehova ndikuyamikira gulu Lake. Chotero, kukonda chowonadi ndiko mfungulo ya kumasuka ku zomangira za chipembedzo chonyenga. Anthu ena amati amakondwera ndi uthenga wa Baibulo koma samalola konse kuleka ziyambukiro za chipembedzo chonyenga ndi njira yake yamoyo yolekerera. Chifukwa ninji ayi? Monga momwe kwalongosoledwera pa 2 Atesalonika 2:10, iwo ‘sachilandira chikondi cha chowonadi kuti akapulumutsidwe.’ Nkofunika chotani nanga kuti tikhale ndi chikondi chimenecho!
19 Titakupatira chowonadi, kuchisungabe kwathu chikondi chimenecho kuli nsonga yofunika m’kukula kwathu kwauzimu. Kumbukirani kuti Yehova amalozera ku chowonadi kukhala “chinenero.” Pamene munthu aphunzira chinenero chatsopano, iye ayenera kupanga kuyesayesa kwakhama kuwunjika mpambo wake wa mawu, kutchula mawu molondola, kuphunzira tsatanetsatane wa galamala, ndi zina zotero. Kukonda chinenero chatsopanocho ndi anthu amene amachilankhula kudzamthandiza iye kupitirizabe kupanga kupita patsogolo. Iye angakhale wokhoza kulankhula chinenerocho ku mlingo wakutiwakuti m’miyezi yoŵerengeka, koma chimatenga zaka za kuyesayesa kwakhama munthuyo asanayambe kuchilankhula monga eni ake. Mtundu umenewu wa kuyesayesa umafunikira kuti tidziŵe mokwanira chinenero choyera.
20. (a) Kodi nchiyani chimene chimapangitsa chinenero choyera kukhala choyeradi? (b) Kodi nchifukwa ninji chisamaliro chachikulu nchofunikira kwa aliyense wa ife?
20 Nkofunikanso mwapadera kudziŵa kuti chinenero chimene Mulungu akupereka kwa atumiki ake chikunenedwa kukhala choyera. Izi nzowona, osati chifukwa cha kapangidwe kake ka galamala, koma chifukwa chakuti chimapereka umboni wa kuyera kwa makhalidwe ndi kwauzimu. M’chinenero chimenechi sikuloledwa kunama, kunyenga, kapena lirime lamachenjera. Anthu olankhula chinenero chimenechi ayenera kulankhula chowonadi nthaŵi zonse. (Zefaniya 3:13; Aefeso 4:25) Kalankhulidwe kawo mofananamo kayenera kuunikira miyezo yapamwamba ya Yehova yonena za mkhalidwe wa zakugonana. (Aefeso 5:3, 4) Malemba amatizindikiritsanso kuti chirichonse chogwirizana ndi Babulo Wamkulu, ulamuliro wadziko wa chipembedzo chonyenga, nchodetsedwa. (Chibvumbulutso 18:2-4) Zisonyezero za milungu yake zimatchedwa ‘mafano ochititsa manyazi.’ (Yeremiya 50:2) Pamenepo, moyenerera, anthu omwe amaphunzira chinenero choyera ayenera kuchotseratu zogwirizanitsa zakuthupi za kulambira konyenga, kukana ziphunzitso zake, kumasuka ku mapwando ake, ndiponso kuchotseratu m’kalankhulidwe kawo mawu alionse osonyeza kulingalira kwake kolakwa. Pambali pa ichi, pa Chibvumbulutso 16:13-16, tikudziŵitsidwa kuti mawu omemeza omwe akusonkhanitsa mitundu motsutsana ndi Ufumu wa Mulungu alinso odetsedwa, pokhala ouziridwa ndi ziŵanda. Chotero tifunikira kukhala amaso kusalola chirichonse cha zinthu zodetsedwazi kuipitsa kalankhulidwe kathu.
21. Kodi nchiyaninso chimene chiri m’chinenero choyera kuwonjezera pa mawu okambidwa?
21 Chomwe tikuphunzirachi chikutchedwa chinenero, ndipo moyenereradi, komatu izi sizikutanthauza kuti anthu ochilankhulawo amangophunzira mmene angagwiritsirire ntchito mawu omwe ali ofala kwa anthu a Yehova. Kamvekedwe ka mawu, kawonekedwe ka nkhope, ndi majesichala nzofunikanso. Izo zingapereke uthenga womwe mawu okha sangathe kuupereka. Kaŵirikaŵiri zimaunikira zimene ife tiri mkati. Zingasonyeze kaya ngati tataya nsanje, kutetana, ndi mkwiyo, zonse zomwe ziri ntchito zathupi lochimwa. Pamene mzimu wa Mulungu ugwira ntchito mwaufulu m’miyoyo yathu, zipatso zake zimawonekera m’njira imene timalankhuzana ndi ena.—Agalatiya 5:19-23; Aefeso 4:31, 32.
22. Pamene tiphunzira chinenero choyera bwino lomwe, kodi chimayambukira motani kupanga kwathu zosankha?
22 Aliyense amene waphunzira chinenero chatsopano amadziŵa kuti wafikira chilakiko chenicheni pamene adzipeza akulingaliradi m’chinenero chatsopanocho, m’malo mochitembenuza kuchokera m’lirime lake. Momwemonso, pamene tikuphunzira chowonadi, kupanga kuyesayesa kwakhama kuchigwiritsira ntchito m’miyoyo yathu, ndipo mokhazikika kuchigawana ndi ena, pang’onopang’ono timadzipeza ife eni tikulingalira m’mawu achowonadi. Sitimakhala tikulinganiza kosatha zakale ndizatsopano ndi kulimbikira kupanga chosankha. Ngakhale m’zinthu zazing’ono, malamulo a makhalidwe abwino a Baibulo amabwera m’maganizo ndi kupereka chitsogozo chomwe tikuchifunikira.—Miyambo 4:1-12.
23. Mosasamala kanthu za chimene chingakhale chinenero chakwawo, kodi nchiyani chimene chimasonyeza kuti Mboni za Yehova zonse padziko lonse lapansi zimalankhula chinenero choyera?
23 Nzowonadi kuti pali zinenero zikwi zambiri zimene zikugwiritsiridwa ntchito ndi anthu, koma chinenero choyera chingalankhulidwe m’zinenero zonsezi. Padziko lonse, Mboni za Yehova zikugwiritsira ntchito bwino mogwirizana chinenero choyera pamene zikutumikira mogwirizana kupereka umboni wapoyera umene umabweretsa ulemu kwa Yehova, Mulungu wathu wachikondi.
Mafunso Obwereramo
◻ Kodi nchiyani chimene chikuphatikizidwa m’mphatso ya kulankhula?
◻ Kodi chinenero choyera nchiyani?
◻ Kodi Zefaniya 3:9 akwaniritsidwa kwayani?
◻ Kodi tingapereke motani umboni wakuti timachikondadi chinenero choyera?
[Chithunzi patsamba 23]
Awo amene amachidziŵa chinenero choyera amachigaŵana ndi ena
[Chithunzi patsamba 25]
Chirichonse chimene chingakhale chinenero chakwawo, Mboni za Yehova zimalankhula chinenero choyera padziko lonse