Yehova Amamva Kuchonderera Kwathu kwa Thandizo Lamwamsanga
THANDIZO linali lofunika mwamsanga. Izi zinawoneka m’chisoni chachikulu pankhope ya wopereka chikho wa mfumu. Atafunsidwa chomwe chidalakwika, wopereka chikhoyo anafotokoza chisoni chake pamzinda wa Yerusalemu wosakazidwa ndi malinga ake. Kenaka anafunsidwa kuti: “Ufunanji iwe?” “Pamenepo ndinapemphera Mulungu wakumwamba,” analemba motero pambuyo pake wopereka chikho Nehemiya. Kumeneko kunali kuchonderera kafulumira, kwakachetechete, kwamsanga kaamba ka thandizo la Yehova. Ndi chotulukapo chotani? Eya, Aritasasta mfumu ya ku Perisiya mosataya nthaŵi analamula Nehemiya kukamanganso malinga a Yerusalemu!—Nehemiya 2:1-6.
Inde, Mulungu amamva kuchonderera kwamwamsanga kwa awo omkonda. (Salmo 65:2) Chotero ngati chiyeso chikuwoneka kukhala chachikulu chosatha kuchipirira, mungapemphere monga momwe wamasalmo Davide anachitira m’Salmo 70, pamene anafunikira thandizo laumulungu mwamsanga. Mawu apamwamba pa salmo limeneli amasonyeza kuti chifuno chake ndicho ‘chikumbutso.’ Mongosiyanapo pang’ono, iwo amabwereza Salmo 40:13-17. Koma kodi ndimotani mmene Salmo la 70 limeneli lingatithandizire ifeyo monga anthu a Yehova?
Kuchonderera Chipulumutso Chamwamsanga
Davide akuyamba ndi kuchonderera nati: “Fulumirani kundipulumutsa, Mulungu; Fulumirani kundithandiza, Yehova.” (Psalm 70:1) Pamene tipsinjika, tingapemphere kuti Mulungu atithandize mofulumira. Yehova samatiyesa ndi zinthu zoipa, ndipo iye “adziwa kupulumutsa opembedza poyesedwa iwo.” (2 Petro 2:9; Yakobo 1:13) Koma bwanji ngati iye walola chiyeso kupitiriza, mwinamwake kuti atiphunzitse chinachake? Pamenepo tikhoza kumpempha nzeru yakuti tichilake. Ngati tipempha mwachikhulupiriro, iye atipatsa nzeru. (Yakobo 1:5-8) Mulungu amatipatsanso nyonga yofunika kuti tipirire ziyeso zathu. Mwachitsanzo, iye ‘amgwiriziza pa kama wodwalira.’—Salmo 41:1-3; Ahebri 10:36.
Uchimo wathu wobadwa nawo, limodzinso ndi kuyang’anizana ndi ziyeso kwanthaŵi zonse ndi zoyesayesa za Mdyerekezi zofuna kuwononga unansi wathu ndi Yehova, ziyenera kutisonkhezera kupempherera thandizo la Mulungu tsiku lirilonse. (Salmo 51:1-5; Aroma 5:12; 12:12) Naŵa mawu ofunika a pemphero lachitsanzo la Yesu: “Musatitengere kokatiyesa, koma mutipulumutse kwa woipayo.” (Mateyu 6:13) Inde, tikhoza kumpempha Mulungu kuti asatilole kugonja pamene tiyesedwa kusamvera ndikuti amletse Satana, “woipayo,” kusatifikira. Koma tiyeni tigwirizanitse kuchonderera kwathu kwa kupulumutsidwa ndi masitepe akupeŵa mikhalidwe imene ikatidzetsa m’chiyeso ndi m’misampha ya Satana.—2 Akorinto 2:11.
Amene Akuti, ‘Hede!’
Ife tingaikidwe pachiyeso mwakutonzedwa ndi adani kaamba ka chikhulupiriro chimene timachisonyeza. Ngati zimenezo zichitika kwa inuyo, lingalirani pa mawu a Davide aŵa: ‘Achite manyazi, nadodome amene afuna moyo wanga: Abwezedwe m’mbuyo, napepulidwe amene akonda kundichitira choipa. Abwerere, kukhale mphotho ya manyazi awo amene akuti, Hede, hede.’ (Salmo 70:2, 3) Adani a Davide anafuna kuti iye afe; ‘ankafuna moyo wake.’ Komabe, m’malo mwakuyesa kulipsira, iye anasonyeza chikhulupiriro chakuti Mulungu akawachititsa manyazi. Davide anapemphera kuti adani ake ‘achite manyazi, nadodome’—anyazitsidwe, akhwethemuke, alephere, alefuke m’kuyesayesa kwawo kuchita ziwembu zoipa. Inde, awo omfunira chivulazo ndi kukondwa m’tsoka lake asokonezeke nanyazitsidwe.
Ngati tikhala ndi chimene chingatchedwe chisangalalo chanjiru pamene tsoka ligwera mdani, tidzanena mlandu kwa Yehova kaamba ka tchimo lathu. (Miyambo 17:5; 24:17, 18) Komabe, pamene adani atonza Mulungu ndi anthu ake, tingapemphere kuti chifukwa cha dzina lake lopatulika, Yehova ‘awabweze ndi kuwachititsa manyazi’ pamaso pa anthu amene iwo afunako ulemerero. (Salmo 106:8) Kubwezera nkwa Mulungu, ndipo iye akhoza kudodometsa ndi kuchititsa manyazi adani ake ndi athu. (Deuteronomo 32:35) Mwachitsanzo, mtsogoleri wa Nazi, Adolf Hitler anafuna kufafaniza Mboni za Yehova m’Jeremani. Ha, iye analephera mochititsa manyazi chotani nanga, popeza kuti mazana ambiri a izo tsopano zikulengeza uthenga wa Ufumu kumeneko!
M’chiphwete chotonza, adani athu anganene kuti: ‘Hede, hede.’ Pokhala kuti akutonza Mulungu ndi anthu ake, alekeni adani ‘abwerere, kukhale mphotho ya manyazi awo,’ kuvutika ndi kunyazitsidwa. Pamene tikupempherera zimenezi, tiyeni tisunge umphumphu wathu ndi kukondweretsa mtima wa Yehova, kuti amyankhe Satana ndi aliyense wotonza Iye. (Miyambo 27:11) Ndipo tisawawope konse adani athu odzitukumula, popeza kuti “wokhulupirira Yehova adzachinjirizidwa.” (Miyambo 29:25, NW) Nebukadinezara, mfumu yonyada ya ku Babulo yemwe adatenga anthu a Mulungu muukapolo, anachititsidwa manyazi ndipo anakakamizika kuvomereza kuti ‘Mfumu ya Kumwamba akhoza kuchepetsa oyenda m’kudzikuza kwawo.’—Danieli 4:37.
“Abuke Mulungu”
Chinkana kuti adani angativutitse, lolani kuti nthaŵi zonse timkweze Yehova pamodzi ndi alambiri anzathu. Mmalo modzilola kumwerekera m’chipsinjo moti nkulephera kulememekeza Mulungu, Davite anati: ‘Asekerere nakondwerere mwa inu onse akufuna inu; nanene kosalekeza iwo akukonda chipulumutso chanu, Abuke Mulungu.” (Salmo 70:4) Anthu a Yehova akupitirizabe kukhala osangalala chifukwa chakuti ‘amasekerera nakondwera’ mwa iye. Monga Mboni zake zodzipereka, zobatizidwa, iwo ali nchisangalalo chachikulu chochokera muunansi wathithithi ndi iye. (Salmo 25:14) Komabe, izo zingawonedwe kukhala ofuna Mulungu odzichepetsa. Pokhala zokhulupirira zosunga malamulo a Mulungu, zimapitirizabe kufuna chidziŵitso chowonjezereka cha iye ndi Mawu ake.—Mlaliki 3:11; 12:13, 14; Yesaya 54:13.
Pamene Mboni za Yehova zikulengeza mbiri yabwino, kwenikweni izo zimati: “Abuke Mulungu.” Zimakweza Yehova, kumpatsa ulemu wopambana. Mwachisangalalo, zimathandiza ofuna chowonadi kuti aphunzire ponena za Mulungu ndi kumlemekeza. Mosiyana ndi okonda zokondweretsa akudziko, anthu a Yehova ‘amakonda chipulumutso.’ (2 Timoteo 3:1-5) Pokhala ozindikira za uchimo wawo wobadwa nawo, amayamikira mwakuya makonzedwe achikondi a Yehova Mulungu a chipulumutso cha ku moyo wamuyaya, wotheketsedwa mwa nsembe yadipo ya Mwana wake wokondedwa, Yesu Kristu. (Yohane 3:16; Aroma 5:8; 1 Yohane 2:1, 2) Kodi mumamlemekeza Mulungu ndi kusonyeza kuti ‘mumakonda chipulumutso’ mwakulambira kowona komtamanda?—Yohane 4:23, 24.
Khulupirirani Mpulumutsi
Pamene Davide analongosola malingaliro ake mu salmo limeneli, anadzimva kukhala wofunikira thandizo mofulumira kotero kuti adati: ‘Koma ine ndine wozunzika waumphaŵi; mundifulumirire, Mulungu: Inu ndinu mthandizi wanga ndi mpulumutsi wanga; Musachedwe, Yehova.’ (Salmo 70:5) Povutika ndi mayesero ozinga okhulupirira—masautso onga chizunzo, ziyeso, ndi ziukiro za Satana—tingawoneke kukhala ‘amphaŵi.’ Ngakhale kuti sitingakhale osoŵa chochita, timawoneka kukhala opanda chinjirizo kwa adani olunda. Komabe, tingakhale achidaliro kuti Yehova angathe ndipo adzatipulumutsa ife monga atumiki ake okhulupirika.—Salmo 9:17-20.
Yehova ndiye ‘Mpulumutsi’ pamene tifunikira chipulumutso. Zifooko zathu zenizenizo zingatiloŵetse mumkhalidwe wopereka chiyeso. Koma ngati ‘utsiru wathu ukhotetsa njira yathu,’ mtima wathu ‘usakwiire Yehova.’ (Miyambo 19:3) Iye sindiye ali ndi mlandu, ndipo ngwofuna kutithandiza ngati tipemphera kwa iye mwachikhulupiriro. (Salmo 37:5) Bwanji ngati tikulimbana kuti tipeŵe tchimo? Pamenepo tiyeni tikhale olunjika m’pemphero limenelo, tikumapempha thandizo laumulungu kuti tipitirizebe kulondola njira yolungama. (Mateyu 5:6; Aroma 7:21-25) Mulungu adzayankha pemphero lathu lochokera mumtima, ndipo tidzapita patsogolo mwauzimu ngati tigonjera ku chitsogozo cha mzimu wake woyera.—Salmo 51:17; Aefeso 4:30.
Pamene tiri m’zoŵaŵa za chiyeso cha chikhulupiriro, tingafike pakulingalira kuti sitingathe kupirirabe. Popeza kuti thupi lanthu lochimwa nlofooka, lingalakelake chipulumutso chofulumira. (Marko 14:38) Chotero tingachonderere kuti: ‘Musachedwe, Yehova.’ Makamaka ngati tikudera nkhaŵa ndi chitonzo pa dzina la Mulungu, tingasonkhezeredwe kupemphera monga momwe anachitira mneneri Danieli kuti: ‘Yehova, imvani; Yehova, khululukirani; Yehova, mverani nimuchite; musachedwa, chifukwa cha inu nokha, Mulungu wanga; pakuti . . . anthu anu anatchedwa dzina lanu.’ (Danieli 9:19) Tingakhale ndi chikhulupiriro chakuti Atate wathu wakumwamba sadzachedwa, popeza kuti mtumwi Paulo anapereka chitsimikizo ichi: ‘Tilimbike mtima poyandikira mpando wachifumu wachisomo, kuti tilandire chifundo ndi kupeza chisomo chakuthandiza nthaŵi yakusoŵa.’—Ahebri 4:16.
Tisaiŵale konse kuti Yehova ndiye Mpulumutsi. Monga atumiki ake, kudzatithandiza kukumbukira chimenechi ndi mawu a pemphero a Salmo 70. Nthaŵi zina tingafunikire kupemphera mobwerezabwereza ponena za nkhani yochititsa nkhaŵa yaikulu. (1 Atesalonika 5:17) Pangawoneke kukhala palibe thandizo ku vuto lakutilakuti, kukhala palibe potulukira m’chothetsa nzeru chathu. Koma Atate wathu wakumwamba wachikondi adzatilimbitsa ndipo sadzatilola kuyesedwa koposa kumene tingakupirire. Chifukwa chake, tisatope konse m’kupita pamaso pampando wachifumu wa Mfumu Yamuyaya m’pemphero lochokera mumtima. (1 Akorinto 10:13; Afilipi 4:6, 7, 13; Chibvumbulutso 15:3) Pempherani mwachikhulupiriro, ndipo dalirani mwa iye kotheratu, popeza kuti Yehova amamva kuchonderera kwathu kwa thandizo lamwamsanga.