Chitokoso Chakufesa Mbewu Zaufumu Kum’mwera kwa Chile
NKOSANGALATSA chotani nanga kuyenda m’mphepete mwa msewu wabata wa m’dera lakumidzi kum’mwera kwa Chile! Ng’ombe zimabudula mwamtendere m’minda yokhala ndi mitengo kutsogolo kwa mapiri aakulu a matanthwe otentha apansi panthaka okutidwa ndi chipale chofeŵa. Mukhoza kumva mbalame zikuimba ndi masamba akuweyuka m’mkokomo wa mphepo. Monga mmene malo otero angawonekere kukhala osangalatsa, mulinso zitokoso kwa awo ofesa mbewu za chowonadi Chaufumu.
Kodi mungakonde kukumana ndi ena a apainiya athu, kapena olengeza Ufumu anthaŵi zonse? Kodi bwanji osakhala nawo tsiku limodzi kapena aŵiri pamene akulengeza mbiri yabwino? Choyamba, tatiyeni timvetsere pamene Jaime ndi Oscar akusimba zisangalalo ndi zitokoso za tsiku loterolo kum’mwera kwa Chile.
Tsiku Lina m’Ntchito Yolalikira
“Tiyamba kuthunthumira ndi kuzindikira kuzizira komwe kwaloŵa m’nyumba yathu yaing’ono. Atavala nsokosi zaubweya ndi kachipewa kakapusi kakadali kumutu kwake, Oscar atsika pakama. Akoleza chitofu chankhuni, ayatsa mbaula ya gasi kuti afunditse chipinda, nabwerera pakama wake wofunda. Apo kunja kukadali mdima, ndipo tikhoza kumva mvula yomwe yakhala ikugwa usiku wonse. Tisunzumira kunja pazenera ndiyeno nkuyang’anana. Ha, kungakhale kokhweka chotani nanga kusagwira ntchito patsikuli! Kenaka tikumbukira makonzedwe athu a tsikulo ndi kufunika kwa kugwira ntchito m’gawo lakutali lomwe silinafikiridwe konse chaka chatha. Tikakamizika kupita.
“Panjira 8 koloko isanakwane, tiyenda mofulumira kwambiri ndi kuyembekezera kuti munthu wina adzatinyamule m’galimoto kapena kuti basi idzafika tiri kuyenda, kotero kuti tingafulumize ulendo wathu wopita ku misewu yakumbuyo yopita ku nyumba zakutali ndi midzi ya m’gawo lathu. Iyo talakita ikubwera ikukoka ngolo yotambalala yokhala ndi antchito. Woyendetsayo aiimitsa natilola kukwera. Ndife okondwera kuti, mvula yomwe inagwa usiku wapitawo, yatipulumutsa lero ku chokumana nacho choyenda paulendo wafumbi. Pamene tikudzanduka poyenda, tikugaŵana mbiri yabwino ndi antchito yaulimi. Pamene nthaŵi yotsika yafika, tiŵapatsa magazini angapo. Ha, ndife oyamikira chotani nanga kaamba ka ulendo womwe watipulumutsa ku kuyenda pansi makilomita 12!
“Ilo lidzakhala tsiku lalitali pamene tikudutsa dera lakumidzi kufunafuna anthu oyenerera. Pamene tinangoyamba ntchito yathuyi, sitinamvetsetse chifukwa chake anthu ankavomereza zimene tinali kunena koma ankasonyeza kuzengereza kulandira mabuku Abaibulo. Tinadzadziŵa kuti kaŵirikaŵiri chinali chifukwa chakuti iwo sakhoza kuŵerenga. Chotero timakupeza kukhala kopindulitsa kufotokoza kuti mabuku athu ndi mphatso zabwino za ana awo ndi achibale, amene pambuyo pake angagaŵane nawo zamkatimo. Ambiri a iwo omwe timalankhula nawo alibe katundu wambiri. Koma popeza kuti iwo ngachimwemwe kugaŵana ndi ena zomwe ali nazo, atalandira mabuku Abaibulo, iwo kaŵirikaŵiri amatipatsa mazira, mbatata, mabeet, anyezi, nyemba, mphodza, ndi garbanzos.”
Jaime waphunzira kupereka malingaliro pamene mwininyumba afuna kupereka katundu mosinthana ndi mabuku Abaibulo omwe wapatsidwa. Chifukwa ninji? Pachochitika china, apainiyawo anabwera ali ndi makilogramu 15 a ndiwo zamasamba, ndipo bwenzi lake lidafunikira kunyamula nkhuku yamoyo m’chola chake cha mabuku mbali yokulira yatsikulo! Kaŵirikaŵiri Jaime amalingalira kutenga merquén, chokoleretsa chokoma chokonzedwa kuchokera ku tsabola ndi zonunkhiritsa. Nkhaniyo ikupitiriza kuti:
“Podutsa minda, tifika pa marucas [nyumba] zina za eni malowo Amapuche [kutanthauza, “Anthu a dziko lino”]. Kulankhula ndi Amapuche okalamba nkovuta, popeza kuti ambiri amalankhula chinenero chakwawo chokha. Pamene achichepere ali pafupi, iwo kaŵirikaŵiri amatumikira monga omasulira. Pamene tiloŵa mkati kwambiri mwa dera lakumidzilo, tikumana ndi anthu amene sanawonepo Baibulo nkalelonse kapena kuchezera mzinda waukulu wonga Temuco, likulu la deralo. Ichi chimapereka chitokoso chakuŵathandiza kuzindikira mmene mikhalidwe yadziko ikunyonyotsokera. Tiyenera kutero mwapang’onopang’ono, kuŵasonyeza mmene mavuto akumaloko amasonyezera zimene zikuchitika kwinakwake.
“Pamene tsikuli likutha, tatopa kwambiri kwakuti tifunikira kupuma. Nyengo yasintha kuchokera ku dzuŵa lofanalo kunka ku mvula yachimphepo yopangitsa sumbulele kukhala yopanda ntchito. Minda yogaulidwa posachedwapa ichititsa nsapato zathu kukutidwa ndi matope. Pamene tikumva mawu akuti Pase no más (Loŵani), tiloŵa m’kitchini moyamikira ndi kusangalala ndi kufunda kwa chitofu cha nkhuni, kapu ya ‘khofi’ yopangidwa kuchokera ku dzinthu, cheese yofeŵa ndi yosalala, ndi mkate watsopano wopangidwa panyumba. Ha, fungo lamkatewo nlokoma chotani nanga!
“Pokhala ndi nyonga yowonjezereka, tipitirizabe kuyenda kusanade kwambiri, kudutsa minda yogaŵidwa mwakamodzikamodzi ndi mipanda, chinkana kuti mudzapeza minda ina ya tirigu yozunguliridwa ndi chitsamba chotchedwa pica-pica, chomera chobiriŵira nthaŵi zonse chokhala ndi maluŵa achikasu. Popeza kuti dzuŵa lidzaloŵa posachedwapa ndipo tiyenera kufika pamsewu wina waukulu kuti tikwere basi yomalizira kubwerera ku tauni, kuyenda kwathu kwa [makilomita 20] kudzatha posachedwapa.
“Tabwerera osungika ndi athanzi, otopa koma achimwemwe, popeza kuti takhala ndi makambitsirano ambiri osangalatsa ndi anthu onga nkhosa. Titadya, tibwereramo m’zomwe tachita tsikulo ndiyeno nkugona tiri otopa.”
Ulendo Wokacheza ku Chiloé
Gulu lazilumba la Chiloé nlopangidwa ndi tizilumba tating’ono toŵerengeka. Chilumba chachikulu nchamakilomita 180 mlitali ndipo chiri ndi mapiri okutidwa ndi zomera zobiriŵira olekanitsidwa ndi nyanja zazing’ono. Ndipo ndi mawonekedwe akugombe okongola ndi midzi ya asodzi imene mungaiwone kulikonse kumene mupita njochititsa kaso chotani nanga!
M’tauni ya Achao, kungochoka ku chilumba chachikulu, tipeza Rubén ndi Cecilia. Pamene iwo anafika m’March 1988, wansembe wakumaloko anachenjeza anthu ‘kusamvetsera kwa okwatirana aŵiri oyenda kuzungulira chilumbacho akulankhula za Baibulo.’ Ndemanga zake zosayenera zinatseka maganizo a anthu ena koma zinadzutsa chilakolako mwa ena. M’kupita kwanthaŵi Rubén ndi Cecilia anayamba kuchititsa maphunziro Abaibulo 28. Maphunziro angapo ndi aphunzitsi, anayi mwa iwo amagwiritsira ntchito mabuku a Watch Tower a “All Scripture Is Inspired of God and Beneficial” ndi Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo kuphunzitsira m’makalasi achipembezo pasukulu zawo.
Yehova amasamalira apainiya ogwira ntchito zolimba ameneŵa, amene amayenda mtunda wamakilomita 34 patsiku m’ntchito yolalikira Ufumu ndi kupanga ophunzira. (Mateyu 24:14; 28:19, 20) Tsiku lina, Rubén ndi Cecilia ankayenda m’kanjira kamphepete mwa gombe pamene anawona kuti kumbali yosadzala kwambiri kunali machoritos (mtundu wa nkhono) ochuluka okhoza kutengedwa. Rubén anayamba kukolola, koma kodi ndimotani mmene akazitengera kunyumba? Cecilia anathetsa vutolo. Nsokosi zake zinakhala matumba. Apainiyawo tsopano anali ndi chakudya chokoma cha m’nyanja!
Chakumpoto kwa Achao, alengezi aŵiri Aufumu anthaŵi zonse odziŵika monga apainiya apadera amayanjana ndi mpingo waung’ono ku Linao. Ntchito yolalikira inayambira kuno mu 1968, ndipo Mboni ya Yehova yoyamba m’Linao inabatizidwa mu 1970. Kwazaka zinayi mbaleyu anali yekha m’ntchito yolalikira ndipo anafunikira kupirira kujeda kochokera kwa ziŵalo zabanja ndi anansi. Pomalizira pake, mu 1974, mkazi wake anachitapo kanthu moyanja chowonadi cha Baibulo ndipo anabatizidwa. Izi zinatsatiridwa ndi maubatizo a achimwene ake anayi, achemwali anayi, amalume anayi, aphwake asanu ndi mmodzi, ndi mlamu wake wamwamuna ndi mkazi wake. Mpingo womwe unapangidwa kumeneko unali banja limodzi lalikulu. M’kupita kwanthaŵi, atatu mwa abale asanuwo anayamba kutumikira monga akulu ndipo mmodzi monga mtumiki wotumikira.
Luis ndi Juan ndi alaliki anthaŵi zonse amene amapereka chisamaliro pa kufesa mbewu Zaufumu ku Quemchi, tauni yaing’ono yokhala pamtunda wamakilomita 30 kuchokera ku Linao. Tsiku ndi tsiku, iwo amakwera mipanda, kudutsa minda yoŵirira ndi zomera, ndipo amakwera ndi kutsika mapiri, limodzi ndi mphepo ndi mvula monga zotsagana nawo zokhazikika. Kuti afike ku zilumba zapafupi, iwo amagwiritsira ntchito maboti aang’ono omwe amapita ku chilumba cha Chiloé kaŵiri kapena katatu pamlungu. Iwo amakhala pa chilumbacho kwa masiku angapo. Ulendo woyenda pakati pa zilumba ungapangitse munthu wokhala kumtunda kuchita mantha pang’ono, koma kuchereza alendo kwa okhala kuzilumba ndi kukoma mtima kumathetsa zimenezi. Wofalitsa wina wa Ufumu anagwirizana ndi Luis ndi Juan, ndipo pamodzi amayesayesa kufikira anthu 11,500 okhala m’gawo lawo. Chinkana kuti chiwonjezeko chinali chapang’onopang’ono, Luis ndi Juan anasangalala kukhala ndi anthu 36 opezekapo pa phwando la Chikumbutso la 1989.
Kubwerera ku Mtunda
Kupitirizabe kunka kumpoto, tidutsa ngalande ya Chacao ndi kufika ku mtunda. M’dera lino, apainiya Ramón ndi Irene, amagwira ntchito m’gawo lalikulu limene limaphatikizapo magulu akutali a Maullín, Carelmapu, ndi Pargua. Mboni zapachilumba cha Chiloé zimayenda kwa ola limodzi ndiyeno zimakwera transbordador (boti yoolotsa) kuti zidutse thamanda ndikukapezeka ku misonkhano Yachikristu ku Pargua. Ramón amayenda kwa ola limodzi ndi mphindi 20 ndi basi kuchokera ku Maullín kukachititsa misonkhano imene mwachisawawa pamapezeka anthu kuŵirikiza kaŵiri kuposa chiŵerengero cha ofalitsa. Kodi nchifukwa ninji kuyenda mtunda wamakilomita 38 kumatenga nthaŵi yaitali chotero? Chifukwa chakuti basi imaima paliponse m’njira kunyamula anthu olemedwa ndi matumba achiguduli a zipatso ndi ndiwo zamasamba, matumba a mbatata ndi anyezi, ndipo nthaŵi zina ngakhale nkhumba zamoyo ndi nkhuku. Zirizonse zimene sizingaikidwe pamwamba pa basi zimaloŵetsedwa mkati. Chotulukapo chomalizira ndi ulendo wautali wodzala ndi kununkha kwakukulu, kuwona zosakondweretsa, ndi phokoso.
Popeza kuti pali apainiya ochepa amene ali ndi magalimoto, kuiphonya basi yoyenda pakati pa matauni kumatulukapo m’kuyenda mtunda wautali, pokhapo ngati wina akunyamulani m’galimoto. Pamene Ramón ndi wophunzira Baibulo anali kuyenda m’galimoto la wina, woyendetsayo anafunsa kuti: “Kodi anthu akuchitapo kanthu motani pa ntchito yanu?” Pozindikira kudabwa kwawo, iye anati: “Ndine wansembe m’dera lino, ndipo inu ndinu Mboni za Yehova. Ndimaidziŵa bwino ntchito yanu ndipo ndimawakonda magazini anu.” Panalidi nkhani ya mafunso ndi mayankho asanaŵatsitse ku Pargua kukali nthaŵi kaamba ka msonkhano. Ndithudi wansembeyo anapeza mayankho ku mafunso ena pamene anapitirabe kuŵerenga magazini athu.
Sikosavuta nthaŵi zonse kwa Ramón ndi Irene kufikira nyumba 20 kumene amachititsa maphunziro Abaibulo. Ena amakhala kutsidya lina la Mtsinje wa Maullín kapena m’midzi ya asodzi yakutali ndipo ayenera kufikiridwa mwa boti yaing’ono. Chinkana kuti mvula yamvumbi ingakhale yolefulitsa, kunali kowonekera bwino kuti kupirira kosonyezedwa ndi iwo ndi olengeza Ufumu ena 18 omwazikana m’gawo lonseli lakumidzi kunali kubala zipatso pamene anthu 77 anasonkhana pamodzi kaamba ka Chikumbutso.
Ku Los Muermos, olengeza Ufumu anthaŵi zonse Juan ndi Gladys amachititsa maphunziro Abaibulo 23. Kuyenda mtunda wautali m’misewu yamatope kumafupidwa pamene mbewu Zaufumu zizika mizu m’mitima ya anthu ophunzitsika. M’dera lina lakutali ku mtandaza wa mapiri akugombe kwa nyanja pafupi ndi Estaquilla, Juan ndi Gladys anagwira ntchito m’dera limene silinafikiridwepo kumbuyoku. Iwo anapempha wophunzira Baibulo ngati angaŵabwereke kavalo wake kwa tsiku limodzi. Iye anayankha kuti: “Ndithudi. Kodi ndingapite nanu?” Posapita nthaŵi Juan anazindikira kuti uku kunayenera kukhala mwa chitsogozo cha Yehova. Kukanakhala kokhweka kusokera m’nkhalango yoŵirira, koma munthu wokondwererayo analidziŵa bwino deralo ndipo anaŵatsogolera ku nyumba zosakhoza kuwoneka kuchokera ku njira za m’mapiri. Atatopa kwambiri pambuyo poyenda kwa maola asanu ndi anayi ndi kukwera kavalo, mmodzi wa apainiya apaderawo anafunsa wophunzira Baibulo mmene anadzimvera. Mwamunayo anayankha nati: “Chinthu chokha chimene ndikupempha nchakuti mukanditenge paulendo wotsatira.” Munthu woyamikira amenewu anapitirizabe kupita patsogolo mwauzimu ndipo anabatizidwa mu January 1988. Mkazi wake anabatizidwa posachedwapo pamsonkhano wadera.
Mkati mwa kuchezetsa kwa woyang’anira dera, ofalitsa 11 ku Estaquilla anasangalala kukhala ndi opezekapo 110 pa nkhani yapoyera. M’tauni yaing’ono ya anthu 1,000 pafupi ndi Los Muermos, anthu 66 anakumana kaamba ka Chikumbutso. Chotero pali zambiri zochita m’munda uwu waukulu.—Mateyu 9:37, 38.
Chakumpoto kwambiri, tipeza apainiya Alan ndi Fernando. Tsiku lina pamene ankayenda pamsewu wafumbi, woyendetsa galimoto anaŵalola kukwera kumbuyo kwa galimoto yake yaikulu. Atatsika, anaseka kwambiri chifukwa chakuti anakutidwa ndi fumbi lochindikala kuchokera kumutu mpaka kumapazi. Nthabwala ndi chimwemwe chotsogoza maphunziro Abaibulo apanyumba 20 zimathandiza kugonjetsa zokumana nazo zosayenera zoterozo. Ndipo talingalirani chimwemwe chawo pamene anthu 65 anapezeka pa Chikumbutso ndipo anthu aŵiri oyambirira akumaloko anagwirizana nawo m’ntchito yolalikira mwezi wotsatira!
Kuoloka Bío-Bío
Kuti afikire anthu onga nkhosa pafupi ndi mapiri a Andes Mountains, nkofunika kuoloka pompho la madzi owinduka a Mtsinje wa Bío-Bío lamamita 50 kupita pansi. Zimenezi zimachitidwa pa chipangizo cha matabwa chosalimba cholenjekeka ku nsambo yodutsa phompholo. Ndi chikaikiro, mumakwerapo nkuchotsa mtukulo umene umamasula choimapo kuti chikunkhunizike pa nsambo. Mumamatira ku chinga la choimapocho pamene mukuyenda mofulumira kupita pakati pa phompholo, pamene muzendeŵera ndikuima. Mutapuma, mukankha ndi kukoka mtukulo wina, pang’onopang’ono mukuyenda kudutsa theka lotsalalo. Ndithudi zimenezi sizamunthu wamantha! Komabe, mlongo wina amachita chimenechi mlungu uliwonse kukafikira munthu wonga nkhosa ku mudzi wakutali wakumapiri!
Chitsanzo chabwino chokhazikitsidwa ndi apainiya ndi ofalitsa Ufumu ena chimalimbikitsa okondwerera omwe ali ndi mitima yachiyamikiro kupanga kuyesayesa kofananako kupezeka pamisonkhano Yachikristu. (Ahebri 10:24, 25) Banja lina limayenda mtunda wamakilomita 40 pakavalo kupita ku Mtsinje wa Bío-Bío ndiyeno kuyenda pansi mtunda wina wamakilomita 12 kupita ku Nyumba Yaufumu.
Kodi apainiyawo amakumbukiranji pamene ayang’ana kumbuyo zaka zapitazo? Kodi amakumbukira mapiri a matanthwe otentha apansi panthaka okutidwa ndi chipale chofeŵa, minda yokongola, ndi mitsinje yothamanga? Fumbi, mvula, matope, ndi kuyenda mitunda yaitali? Inde, koma iwo makamaka amakumbukira anthu aubwenzi amene amavomereza mwachiyanjo mbiri yabwino. Anthu onga nkhosa ameneŵa amapangadi kuyesayesa kofunikira. Ha, nkwachimwemwe chotani nanga kufesa mbewu Zaufumu kum’mwera kwa Chile!