Lipoti la Olengeza Ufumu
‘Kututa’ mu Venezuela
Panthaŵi ina Yesu anafananitsa ntchito yolalikira ndi kututa kwa chaka ndi chaka. (Mateyu 9:36-38) Mwini kututako ndi Yehova Mulungu, ndipo zotutazo nzochulukadi kuzungulira dziko lonse. Zimenezi zimaphatikizapo gawo logwiridwamo ntchito mwakamodzikamodzi mu Venezuela.
Ofesi yanthambi ya Watch Tower Society ya Venezuela ikusimba zimene zinachitika pamene kagulu ka akazi ka Mboni kanagwira ntchito m’gawo la Sabana Grande, Dera la Guárico. Mbonizo zikusimba motere: “Nyumba imene tinapatsidwa inali malo abwino kuchitira misonkhano, choncho panthaŵi yomweyo tinayamba kuitanira anthu kubwera kumisonkhano. Anthu sanazidziŵe Mboni za Yehova. Ngakhale kuti munali magulu anayi a evanjeliko mumzindawo, anthu anali olakalaka kuphunzira Baibulo.
“Tinagwira ntchito kwa maola atatu m’maŵa ndi maola atatu masana, kumka kunyumba ndi nyumba ndi kuitanira anthu kubwera kumsonkhano usiku wotsatira. Tinalibe mipando, choncho tinawapempha kubweretsa mipando yawo. Itayandikira nthaŵi yoyamba msonkhano, anthu anayamba kubwera, aliyense atanyamula mpando. Msonkhanowo utatha, tinawauza kuti tingakonde kulemba maina a ofuna kukhala ndi phunziro Labaibulo laulere. Opezekapo onse 29 anafuna kulembetsa maina awo pandandanda.
“Pamene tinali kutseka chitseko mlendo wotsirizira atachoka, tinawona amuna atatu ataimirira pafupi ndi bondo la nyumbayo. Pafupifupi 9 koloko, tinali kukhala pansi kuti tidye pamene iwo anagogoda pachitseko. Anafunsa mafunso onga: ‘Kodi nkulalikira kotani kumene mukukuchita m’mtauni munomu? Kodi nchifukwa chotani chimene mwachitira msonkhano muno nthaŵi ino yausiku?’
“Tinawafunsa ngati tidaswa lamulo lirilonse. Iwo anakana nanena kuti anali apasitala a matchalitchi atatu a evanjeliko m’tauniyo. Iwo anali okwiya chifukwa matchalitchi awo anali opanda anthu madzulowo. Tinawaloŵetsa m’nyumba ndi kuwafotokozera ntchito yathu. Tinawagaŵiranso mabuku ndi kuwapempha kubweranso pa Lachinayi lotsatira.
“Lachinayi lotsatira apasitalawo anabweranso pamodzi ndi anthu ena 22 amene anafuna kumva zimene tikanena. Apasitalawo analingalira kuti, pokhala ndife akazi, sitikalingana nawo m’kukambitsirana. Komabe, msonkhanowo unali wachipambano kulingana ndi mmene tinauwonera. Pomalizira pake tinalongosola kuti tinali kulemba ndandanda ya amene afuna kuphunzira zowonjezereka m’Baibulo. Ochuluka omwe anabwera ndi apasitalawo anafuna kuti maina awo aphatikizidwe pandandandayo, ndipo ena ananenadi kuti anafuna kupita nafe m’ntchito yolalikira!
“Tinafotokoza kuti akafunikira chidziŵitso cha Baibulo chowonjezereka ndi maphunziro asanagwirizane nafe m’ntchito yolalikira. Masiku onse anthu anali kubwera kunyumba, kutipempha kuwafotokozera Baibulo. Nthaŵi zina, titakambitsirana mpaka usiku kwambiri, tinatowapempha kupita kunyumba. Pamene tinali kuchoka m’gawolo pomalizira pake, anachita chisoni kwambiri natiuza kuti pamene tikabwerera, akapita nafe m’ntchito yolalikira. Analonjeza kuti pofika nthaŵiyo adzakhala atapanga kupita patsogolo kofunikirako.”
Pamene Mbonizo zinachoka m’gawolo, panali anthu 40 amene anafuna kuphunzira Baibulo. Maina a anthu okondwereraŵa anaperekedwa kumpingo wapafupi, umene uli pamtunda wamakilomita pafupifupi 50. M’kupita kwanthaŵi, Mboni zina zochokera kumzinda wina zasamukira kutauni imeneyi, ndipo kagulu ka olengeza mbiri yabwino achangu kapangidwa.