Banja Lachikristu Limaika Zinthu Zauzimu Poyamba
“Khalani nonse a mtima umodzi, ochitirana chifundo, okondana ndi abale, achisoni, odzichepetsa.”—1 PETRO 3:8.
1. Kodi nchosankha chotani chimene tonsefe tili nacho, ndipo kodi chosankha chathu chingayambukire motani mtsogolo mwathu?
HA NDIMOTANI nanga mmene lemba lapamwambali limagwirira ntchito m’bungwe lakale la mtundu wa anthu—banja! Ndipo nkofunika chotani nanga kuti makolo asonyeze utsogoleri m’mbali zimenezi! Mikhalidwe yawo yabwino ndi yoipa idzawonekera mwa ana. Komabe, mwaŵi wa kusankha umakhala kwa chiŵalo chilichonse cha banja. Monga Akristu, tingasankhe kukhala anthu auzimu kapena anthu akuthupi. Tingasankhe kukondweretsa Mulungu kapena kumkwiyitsa. Chosankha chimenecho chikakhala kaya dalitso, moyo wosatha ndi mtendere—kapena temberero, imfa yamuyaya.—Genesis 4:1, 2; Aroma 8:5-8; Agalatiya 5:19-23.
2. (a) Kodi ndimotani mmene Petro anasonyezera kukondwera kwake ndi banja? (b) Kodi mkhalidwe wauzimu nchiyani? (Onani mawu a m’tsinde.)
2 Mawu a mtumwi pa 1 Petro chaputala 3, vesi 8, analembedwa mwamsanga pambuyo pa uphungu wabwino umene anapereka kwa akazi ndi amuna okwatira. Petro analidi wokondweretsedwa ndi moyo wa mabanja Achikristu. Anadziŵa kuti mkhalidwe wauzimu wamphamvu ndiwo mfungulo kumabanja ogwirizana, achikondi ndi omverana chifundo. Motero, analongosola m’vesi 7 kuti ngati uphungu wake kwa amuna unanyalanyazidwa, chotulukapo chikakhala chopinga chauzimu pakati pa mwamuna ndi Yehova.a Mapemphero a mwamunayo angadodometsedwe ngati anyalanyaza zosoŵa za mkazi wake kapena kumkwiyitsa chifukwa chosoŵa chifundo.
Kristu—Chitsanzo Changwiro cha Mkhalidwe Wauzimu
3. Kodi Paulo anagogomezera motani chitsanzo cha Kristu kwa amuna?
3 Mkhalidwe wauzimu wa banja umadalira pachitsanzo chabwino. Pamene mwamuna ali Mkristu weniweni, amapereka chitsanzo m’kusonyeza mikhalidwe yauzimu. Ngati palibe mwamuna wokhulupirira, amayi kaŵirikaŵiri amayesa kuchita thayo limenelo. Mulimonse mmene zingakhalire, Yesu Kristu amapereka chitsanzo chabwino cha kuchitsatira. Khalidwe lake, mawu ake, ndi kaganizidwe kake nthaŵi zonse zinali zomangirira ndi zotsitsimula. Kaŵirikaŵiri, mtumwi Paulo amalunjikitsa woŵerenga kuchitsanzo chachikondi cha Kristu. Mwachitsanzo, iye amati: “Mwamuna ndiye mutu wa mkazi, monganso Kristu ndiye mutu wa [mpingo, NW], ali yekha mpulumutsi wa thupilo. Amuna inu, kondani akazi anu, monganso Kristu anakonda [mpingo, NW], nadzipereka yekha m’malo mwake.”—Aefeso 5:23, 25, 29; Mateyu 11:28-30; Akolose 3:19.
4. Kodi nchitsanzo chotani cha mkhalidwe wauzimu chimene Yesu anapereka?
4 Yesu anali chitsanzo chapadera cha mkhalidwe wauzimu ndi umutu wosonyezedwa mwachikondi, mokoma mtima, ndi mwachifundo. Anali wodzimana, osati wodzikonda. Nthaŵi zonse analemekeza Atate wake ndi kulemekeza umutu wake. Anatsatira chitsogozo cha Atate wake, kotero kuti anakhoza kunena kuti: “Sindikhoza kuchita kanthu kwa ine ndekha; monga momwe ndimva ndiweruza; ndipo maweruzidwe anga ali olungama; chifukwa kuti sinditsata chifuniro changa, koma chifuniro cha iye wondituma ine.” “Sindichita kanthu kwa ine ndekha, koma monga anandiphunzitsa Atate, ndilankhula izi.”—Yohane 5:30; 8:28; 1 Akorinto 11:3.
5. Kodi Yesu anapereka chitsanzo chotani kwa amuna pogaŵira zosoŵa kwa otsatira ake?
5 Kodi zimenezi zimatanthauzanji kwa amuna? Zimatanthauza kuti chitsanzo chimene afunikira kutsatira m’zinthu zonse ndicho Kristu, amene nthaŵi zonse anadzigonjetsera kwa Atate wake. Mwachitsanzo, monga momwe Yehova anagaŵirira chakudya kumitundu yonse ya zamoyo padziko lapansi, momwemonso Yesu anagaŵira chakudya kwa otsatira ake. Sananyalanyaze zosoŵa zawo zakuthupi zofunika. Zozizwitsa zake za kudyetsa amuna 5,000 ndi 4,000 zili umboni wachisamaliro chake ndi kuzindikira kwake thayo lake. (Marko 6:35-44; 8:1-9) Mofananamo lerolino, mitu ya banja yathayo imasamalira zosoŵa zakuthupi za mabanja awo. Koma kodi ntchito yawo imathera pamenepo?—1 Timoteo 5:8.
6. (a) Kodi nzosoŵa za banja ziti zimene ziyenera kusamaliridwa? (b) Kodi ndimotani mmene amuna ndi atate angasonyezere luntha?
6 Mabanja alinso ndi zosoŵa zina zofunika kwambiri, monga momwe Yesu anasonyezera. Ali ndi zosoŵa zauzimu ndi zamalingaliro. (Deuteronomo 8:3; Mateyu 4:4) Timadalirana, m’banja ndi mumpingo momwe. Timafunikira chitsogozo chabwino kutisonkhezera kukhala omangirira. M’zimenezi amuna ndi atate ali ndi mbali yaikulu yochita—makamaka ngati ali akulu kapena atumiki otumikira. Mabanja a kholo limodzi afunikiranso mikhalidwe yofananayo pamene akuthandiza ana awo. Makolo ayenera kumvetsetsa osati kokha zimene zikunenedwa ndi ziŵalo za banja komanso zimene sizinanenedwe. Zimenezo zimafunikira luntha, nthaŵi, ndi kuleza mtima. Ndicho chifukwa chake Petro ananena kuti amuna ayenera kukhala olingalira pokhala ndi akazi awo mwachidziŵitso.—1 Timoteo 3:4, 5, 12; 1 Petro 3:7.
Maupandu Ofunikira Kupeŵa
7, 8. (a) Kodi chofunika nchiyani kuti banja lipeŵe kusweka kwauzimu? (b) Kodi chofunika nchiyani kuwonjezera pakukhala ndi chiyambi chabwino m’njira Yachikristu? (Mateyu 24:13)
7 Kodi nchifukwa ninji chisamaliro cha mkhalidwe wauzimu wa banja chili chofunika motero? Mwachitsanzo, tingafunse kuti, Kodi nchifukwa ninji kuli kofunika kuti woyendetsa sitima ya pamadzi apereke chisamaliro chotheratu pamatchati ake pamene akuyendetsa sitima ya pamadzi kudzera pamalo angozi pamene pali posaya? Mu August 1992 sitima ya pamadzi ya paulendo wokasangalala Queen Elizabeth 2 (QE2) inadzeretsedwa pamalo a mchenga ndi miyala pamene kaŵirikaŵiri amalinyero amapanga zophophonya zambiri. Munthu wina wakomweko anasimba kuti: “Amalinyero ambiri achotsedwa ntchito chifukwa cha kulakwitsa zinthu kumene kwapangitsa ngozi mmalo amenewo.” Sitima ya QE2 inagunda chimwala cha m’madzi. Inawonongeka kwambiri. Mbali imodzi mwa zitatu ya sitimayo inawonongeka, ndipo sitimayo inachotsedwa pantchito kwa milungu ingapo kuti ikonzedwe.
8 Mofananamo, ngati “woyendetsa” banja sapenda mosamalitsa tchati, Mawu a Mulungu, banja lake lingawonongeke mosavuta mwauzimu. Kwa mkulu kapena mtumiki wotumikira, chotulukapo chingakhale cha kutayikiridwa mathayo mumpingo ndipo mwinamwake kuwonongeka kowopsa kwa ziŵalo zina za banja. Chifukwa chake, Mkristu aliyense ayenera kusamala kuti asagonjetsedwe ndi lingaliro lolakwika la kukhala mwauzimu, akumadalira kokha pazizolowezi zabwino za phunziro ndi changu zakale. M’njira yathu Yachikristu, kuyamba bwino kokha sikuli kokwanira; koma ulendowo uyenera kumalizidwa mwachipambano.—1 Akorinto 9:24-27; 1 Timoteo 1:19.
9. (a) Kodi phunziro laumwini nlofunika motani? (b) Kodi ndimafunso oyenerera ati amene tingadzifunse?
9 Kuti tipewe madzi osaya, miyala, ndi mchenga wauzimu, tifunikira kuyendera limodzi ndi “matchati” athu mwakukhala ndi phunziro lokhazikika la Mawu a Mulungu. Sitingangodalira paphunziro loyambirira limene linatibweretsa m’chowonadi. Mphamvu yathu yauzimu imadalira paprogramu yokhazikika ndi yachikatikati ya kuphunzira ndi utumiki. Mwachitsanzo, pamene tikhala pa Phunziro la Nsanja ya Olonda la mpingo ndi kukhala ndi kope lino, tingadzifunse kuti, ‘Kodi ine, kapena kodi ife monga banja, taphunziradi nkhaniyi, ndi kuŵerenga malemba ndi kusinkhasinkha kagwiridwe kawo ka ntchito? Kapena kodi tangolemba mizere pansi pa mayankho? Kodi mwinamwake, tanyalanyaza kuŵerenga nkhaniyo tisanafike pamsonkhano?’ Mayankho owona mtima amafunso ameneŵa angatisonkhezere kuganiza mwamphamvu ponena za zizoloŵezi zathu za phunziro ndi kusonkhezera chikhumbo cha kuwongolera—ngati zimenezo zili zofunika.—Ahebri 5:12-14.
10. Kodi nchifukwa ninji kudzipenda kwaumwini kuli kofunika?
10 Kodi nchifukwa ninji kudzipenda kwaumwini koteroko kuli kofunika? Chifukwa tikukhala ndi moyo m’dziko lolamulidwa ndi mzimu wa Satana, dziko limene, mwanjira zonyenga zambiri limayesayesa kupatutsa chikhulupiriro chathu mwa Mulungu ndi malonjezo ake. Lili dziko limene limafuna kutitanganitsa kotero kuti tikhale opanda nthaŵi yosamalira zosoŵa zauzimu. Chifukwa chake tingadzifunse kuti, ‘Kodi banja langa lili lolimba mwauzimu? Kodi ine monga kholo ndili wolimba monga momwe ndimafunikira kukhalira? Kodi ife monga banja tikukulitsa mphamvu yosonkhezera maganizo yauzimu imene imathandiza kupanga zosankha zozikidwa pachilungamo ndi kukhulupirika?’—Aefeso 4:23, 24.
11. Kodi nchifukwa ninji misonkhano Yachikristu ili yopindulitsa mwauzimu? Perekani chitsanzo.
11 Mkhalidwe wathu wauzimu uyenera kulimbitsidwa ndi msonkhano uliwonse umene timafikapo. Maola amtengo wapatali amenewo pa Nyumba Yaufumu kapena pa Phunziro Labuku Lampingo amatitsitsimula pambuyo pa maola ambiri amene timathera tikuyesayesa kupulumuka dziko laudani la Satana. Mwachitsanzo, kwakhala kotsitsimula chotani nanga kuphunzira buku la Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako! Zimenezi zatithandiza kupeza chidziŵitso chabwino kwambiri cha Yesu, moyo wake, ndi utumiki wake. Taŵerenga mosamalitsa malemba oikidwa, tafufuza, ndipo motero taphunzira zambiri m’zitsanzo zimene Yesu anatiikira.—Ahebri 12:1-3; 1 Petro 2:21.
12. Kodi ndimotani mmene utumiki wakumunda umayesera mkhalidwe wathu wauzimu?
12 Chiyeso chabwino pamkhalidwe wathu wauzimu ndicho utumiki Wachikristu. Kuti tichite khama m’kuchitira umboni mwa nthaŵi zonse ndi mwamwaŵi, kaŵirikaŵiri moyang’anizana ndi anthu amphwayi kapena otsutsa, tifunikira chisonkhezero choyenera, kukonda Mulungu ndi kukonda mnansi. Ndithudi, palibe amene amasangalala ndi kukanidwa, ndipo zimenezo zingachitike muutumiki wathu wakumunda. Koma tiyenera kukumbukira kuti ndiuthenga wabwino umene ukukanidwa, osati ife monga munthu payekha. Yesu anati: “Ngati dziko lapansi lida inu, mudziŵa kuti lidada ine lisanayambe kuda inu. Mukadakhala a dziko lapansi, dziko lapansi likadakonda zake za lokha; koma popeza simuli a dziko lapansi, koma ine ndinakusankhani inu mwa dziko lapansi, chifukwa cha ichi likudani inu. . . . Koma izi zonse adzakuchitirani chifukwa cha dzina langa, chifukwa sadziŵa wondituma ine.”—Yohane 15:18-21.
Ntchito Zimavumbula Zambiri Koposa Mawu
13. Kodi ndimotani mmene munthu mmodzi angaipitsire mkhalidwe wauzimu wa banja?
13 Kodi chimachitika nchiyani m’banja ngati onse akhala a udongo ndi adongosolo m’nyumba kusiyapo chiŵalo chimodzi chokha? Patsiku la mvula, onse amasamala kwambiri kusabweretsa matope m’nyumba kusiyapo woiwala uja. Mapazi a matope paliponse amapereka umboni wa kusasamala kwa munthu akumapereka ntchito yaikulu kwa ena. Zofananazo zimagwira ntchito pamkhalidwe wauzimu. Munthu mmodzi yekha wodzikonda kapena wonyalanyaza angawononge mbiri yabwino ya banja. Onse okhala m’banja, osati makolo okha, ayenera kuyesetsa kusonyeza mkhalidwe wamaganizo wa Kristu. Nkopereka mpumulo chotani nanga pamene onse agwirira ntchito pamodzi ndi cholinga cha moyo wosatha! Mkhalidwe wa magazino wa banjalo ndi wauzimu (koma osati wodzilungamitsa). M’banja limenelo kunyalanyaza zinthu zauzimu sikumapezekapezeka.—Mlaliki 7:16; 1 Petro 4:1, 2.
14. Kodi ndiziyeso zotani zakuthupi zimene Satana amatiikira m’njira yathu?
14 Tonsefe tili ndi zosoŵa zazikulu zakuthupi zofunika zimene ziyenera kupezedwa kuti zitichilikize m’moyo wathu wa tsiku ndi tsiku. (Mateyu 6:11, 30-32) Koma kaŵirikaŵiri zosoŵa zathu zimaphimbidwa ndi zokhumba zathu. Mwachitsanzo, dongosolo la Satana limatipatsa ziwiya zilizonse. Ngati tifuna nthaŵi zonse kukhala ndi zatsopano m’zinthu zonse, sitidzakhutiritsidwa, popeza kuti zatsopano mwamsanga zimakhala zakale, ndipo zinthu zina zamakono zimatulukira. Dongosolo lamalondali lakhazikitsa mchitidwe umene sumatha. Limatinyengerera kufunafuna mowonjezereka ndalama zochuluka zogulira zimene timakhumba zowonjezereka. Zimenezi zingatsogolere ku “zilakolako zambiri zopusa ndi zopweteka,” kapena “zikhumbo zauchitsiru ndi zaupandu.” Zingachititse moyo wosakhazikika ndi kukhala ndi nthaŵi yochepa ya zinthu zauzimu.—1 Timoteo 6:9, 10; The Jerusalem Bible.
15. Kodi chitsanzo cha mutu wabanja chili chofunika m’njira yotani?
15 Kachiŵirinso, chitsanzo choikidwa ndi mutu wabanja Lachikristu chili chofunika kwambiri. Mkhalidwe wake wamaganizo wachikatikati pantchito yakuthupi ndi mathayo auzimu ziyenera kusonkhezera ziŵalo zina za banja. Kukakhala kowonongadi ngati atate apereka malangizo abwino kwambiri komano nalephera kukhala ndi moyo mogwirizana ndi mawu ake. Ana mwamsanga angazindikire mkhalidwe wakuti udzichita zimene ndinena osati zimene ndichita. Mofananamo, mkulu kapena mtumiki wotumikira amene amalimbikitsa ena kuchita utumiki wa kunyumba ndi nyumba komano iye nachita mwa apa ndi apo ndi banja lake m’ntchito imeneyo mwamsanga amataya ulemu, m’banja ndi mumpingo momwe.—1 Akorinto 15:58; yerekezerani ndi Mateyu 23:3.
16. Kodi ndimafunso ati amene tingadzifunse?
16 Chifukwa chake, tingachite bwino kupenda miyoyo yathu. Kodi tili otanganitsidwa m’kupeza chipambano cha kudziko ndipo motero kunyalanyaza kupanga kupita patsogolo kwauzimu? Kodi tikupita patsogolo m’kulondola zinthu zakudziko komano tikumazirala mumpingo? Kumbukirani uphungu wa Paulo wakuti: “Mawuwa ali okhulupirika, ngati munthu akhumba udindo wa woyang’anira, aifuna ntchito yabwino.” (1 Timoteo 3:1) Kusamalira mathayo mumpingo kumasonyeza mkhalidwe wathu wauzimu koposa kukwezedwa pantchito. Tiyenera kukhala achikatikati kotero kuti otilemba ntchito asatilamulire monga ngati kuti tinadzipatulira kwa iwo ndipo osati kwa Yehova.—Mateyu 6:24.
Kulankhulana Kwabwino Kumachilikiza Mkhalidwe Wauzimu
17. Kodi chimawonjezera kukulitsa chikondi chenicheni cha m’banja nchiyani?
17 Nyumba mamiliyoni ambiri lerolino zangokhala malo ogonamo. Motani? Ziŵalo zabanja zimadza kunyumba kudzagona ndi kudya basi, ndiyeno mwamsanga zimachoka. Kaŵirikaŵiri samakhala pathebulo ndi kudyera chakudya limodzi. M’banjamo mulibe chikondi. Kodi chotulukapo chake nchiyani? Samalankhulana, kapena kukambitsirana mogwira mtima. Ndipo zimenezo zingachititse kusoŵeka kwa chikondwerero m’ziŵalo zina za banja, mwinamwake kusasamalirana kwenikweni. Pamene tikondana, timakhala ndi nthaŵi ya kukambitsirana ndi kumvetsera. Timalimbikitsana ndi kuthandizana. Mbali imeneyi ya mkhalidwe wauzimu imaphatikizapo kulankhulana kogwira mtima pakati pa okwatirana ndi pakati pa makolo ndi ana.b Pamafunikira nthaŵi ndi luso pamene tikusonkhezerana kulankhula zakukhosi kotero kuti tigaŵane chisangalalo chathu, zokumana nazo, ndi mavuto.—1 Akorinto 13:4-8; Yakobo 1:19.
18. (a) Kodi kaŵirikaŵiri chododometsa chachikulu cha kulankhulana nchiyani? (b) Kodi unansi wothandiza umazikidwa pachiyani?
18 Kulankhulana kwabwino kumafunikira nthaŵi ndi kuyesayesa. Kumatanthauza kupatula nthaŵi yolankhulana ndi kumvetserana wina ndi mnzake. Chododometsa chachikulu pazimenezi ndicho chiwiya chodya nthaŵi chimene chili cholemekezeka m’nyumba zambiri—TV. Chimenechi chimadzetsa mafunso akuti—kodi TV imakulamulirani, kapena kodi mumailamulira? Kulamulira TV kumafunikira chitsimikizo champhamvu—kuphatikizapo kukhala ndi mphamvu ya kuitseka. Koma kuchita zimenezo kudzatsegula njira ya kugwirizanitsa munthu aliyense monga ziŵalo za banja ndi monga abale ndi alongo auzimu. Unansi wopindulitsa umafunikira kulankhulana kwabwino, kumvetsetsana wina ndi mnzake, kumvetsetsa zosoŵa ndi zikondwerero zathu, kuuzana mmene timayamikirira zabwino zonse zimene atichitira. M’mawu ŵena, kukambitsirana kogwira mtima kumasonyeza kuti timayamikira ena ndi kuwalemekeza.—Miyambo 31:28, 29.
19, 20. Ngati timasamala onse m’banja, kodi tidzachitanji?
19 Chifukwa chake, ngati tisamalirana m’kakonzedwe ka banja—ndipo zimenezo zikuphatikizapo kusamalira ziŵalo za banja zosakhulupirira—tidzakhala tikuchita zambiri m’kumangirira ndi kusungitsa mkhalidwe wathu wauzimu. M’kakonzedwe ka banja, tidzakhala tikutsatira uphungu wa Petro wakuti: “Chotsalira, khalani nonse a mtima umodzi, ochitirana chifundo, okondana ndi abale, achisoni, odzichepetsa; osabwezera choipa ndi choipa, kapena chipongwe ndi chipongwe, koma penatu madalitso; pakuti kudzatsata ichi mwaitanidwa, kuti mukalandire dalitso.”—1 Petro 3:8, 9.
20 Tingakhale ndi dalitso la Yehova tsopano ngati tiyesayesa kusunga mkhalidwe wathu wauzimu, ndipo zimenezi zingachititse kupeza kwathu dalitso lake mtsogolomu posachedwa pamene tilandira mphatso ya moyo wosatha m’paradaiso padziko lapansi. Pali zinthu zina zimene ife monga banja tingachite kuthandizana mwauzimu. Nkhani yotsatira idzafotokoza mapindu a kuchitira zinthu pamodzi monga banja.—Luka 23:43; Chivumbulutso 21:1-4.
[Mawu a M’munsi]
a Mkhalidwe wauzimu wafotokozedwa kukhala “kuzindikira kapena kugwirizana ndi zofunika zachipembedzo: mkhalidwe kapena kakhalidwe ka kukhala wauzimu.” (Webster’s Ninth New Collegiate Dictionary) Munthu wauzimu ali wosiyana ndi munthu wakuthupi, wochita chifuniro chachibadwidwe.—1 Akorinto 2:13-16; Agalatiya 5:16, 25; Yakobo 3:14, 15; Yuda 19.
b Kuti mupeze malingaliro owonjezereka a kulankhulana m’banja, onani Nsanja ya Olonda ya September 1, 1991, tsamba 20-2.
Kodi Mukukumbukira?
◻ Kodi mkhalidwe wauzimu nchiyani?
◻ Kodi mutu wa banja ungatsanzire motani chitsanzo cha Kristu?
◻ Kodi tingapeŵe motani ziwopsezo za mkhalidwe wathu wauzimu?
◻ Kodi nchiyani chimene chingatayitse mkhalidwe wauzimu wa banja?
◻ Kodi nchifukwa ninji kulankhulana kogwira mtima kuli kofunika?
[Chithunzi patsamba 12]
Kufika pa Phunziro Labuku Lampingo kumalimbitsa mkhalidwe wauzimu wa banja